Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 12

Ukulu wa Israele m’tsogolo

1 Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele.

Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m’kati mwake;

2 Taonani, ndidzaikaYerusalemuakhale chipanda chodzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo chidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.

3 Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndiamitunduonse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.

4 Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo aliyense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo aliyense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.

5 Ndipo akalonga a Yuda adzanena m’mtima mwao, Okhala mu Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga mu Yehova wa makamu Mulungu wao.

6 Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m’malo mwake, mu Yerusalemu.

7 Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala mu Yerusalemu usakulire Yuda.

8 Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala mu Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.

9 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu.

10 Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.

11 Tsiku lomwelo kudzakhala maliro aakulu mu Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m’chigwa cha Megido.

12 Ndipo dziko lidzalira, banja lililonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha;

13 banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha;

14 mabanja onse otsala, banja lililonse pa lokha, ndi akazi ao pa okha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/12-2118067be46e224f9ad6caa6e917a36b.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 13

Kuyeretsedwa kwa Yerusalemu

1 Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala muYerusalemukasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.

2 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m’dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m’dziko aneneri ndi mzimu wachidetso.

3 Ndipo kudzachitika, akaneneranso wina, atate wake ndi mai wake ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m’dzina la Yehova; ndipo atate wake ndi mai wake ombala adzamgwaza ponenera iye.

4 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzachita manyazi yense ndi masomphenya ake, ponenera iye; ndipo sadzavala chofunda chaubweya kunyenga nacho;

5 koma adzati, Sindilimneneri, ndili wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga.

6 Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m’manja mwako nza chiyani? Adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m’nyumba ya ondikonda.

7 Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing’onozo.

8 Ndipo kudzachitika m’dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m’menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lachitatu lidzasiyidwa m’mwemo.

9 Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayengasiliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/13-a48dca69451c712359d3cb13edf5c628.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 14

Yehova adzathandiza a ku Yerusalemu polimbana ndi amitundu

1 Taonani likudza tsiku la Yehova, limene zofunkha zako zidzagawanika pakati pako.

2 Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndiYerusalemu; ndipo mzindawo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mzinda lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m’mzindamo.

3 Pamenepo Yehova adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja, monga anachitira nkhondo tsiku lakudumana.

4 Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum’mawa, ndi phiri la Azitona lidzang’ambika pakati kuloza kum’mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.

5 Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.

6 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, sikudzakhala kuunika, zowalazo zidzada;

7 koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbee.

8 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum’mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.

Yehova mfumu ya dziko lonse lapansi

9 Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha.

10 Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m’malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.

11 Ndipo anthu adzakhala m’menemo, ndipo sipadzakhalanso kuonongetsa; koma Yerusalemu adzakhala mosatekeseka.

12 Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali chilili pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuwala m’funkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m’kamwa mwao.

13 Ndipo kudzali tsiku lomwelo, kuti chisokonezo chachikulu chochokera kwa Yehova chidzakhala pakati pao; ndipo adzagwira yense dzanja la mnzake; ndi dzanja lake lidzaukira dzanja la mnzake.

14 Ndi Yuda yemwe adzachita nkhondo ku Yerusalemu; ndi zolemera za amitundu onse ozungulirapo zidzasonkhanitsidwa, golide, ndisiliva, ndi zovala zambirimbiri.

15 Momwemonso mliri wa pa akavalo, nyuru,ngamira, ndi abulu, ndi nyama zonse zokhala m’misasa iyo, udzakhala ngati mliri uwo.

16 Ndipo kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusungachikondwerero cha Misasa.

17 Ndipo kudzachitika kuti aliyense wa mabanja a dziko wosakwera kunka ku Yerusalemu kulambira mfumu Yehova wa makamu, pa iwowa sipadzakhala mvula.

18 Ndipo banja la ku Ejipito likapanda kukwera, losafika, sudzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga chikondwerero cha Misasa?

19 Ili ndi tchimo la Ejipito, ndi tchimo la amitundu onse osakwerako kusunga chikondwerero cha Misasa.

20 Tsiku lomwelo padzaoneka pa miliu ya akavalo Opatulikira Yehova; ndi mbiya za m’nyumba ya Yehova zidzanga mbale za kuguwa la nsembe.

21 Inde mbiya zonse za mu Yerusalemu ndi mu Yuda zidzakhala zopatulikira Yehova wa makamu; ndi onse akuphera nsembe adzafika nadzatengako, ndi kuphikamo; ndipo tsiku lomwelo simudzakhalanso Mkanani m’nyumba ya Yehova wa makamu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/14-53a0f47735b45fc9f2b90c20be8958b5.mp3?version_id=1068—

Categories
MALAKI

MALAKI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneri Malaki adalalikira nthawi imene Ayuda anali atamanganso Kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Iye analangiza ansembe ndi anthu ao, kuti adziperekenso kwa Yehova ndi kumamutumikira mokhulupirika, ndi kuti apewe ziphuphu, zachiphamaso ndi kunyenga kulikonse, ndipo asamale za chipembedzo.

Ansembe ndi anthu ena amachita chinyengo pa zopereka zao kwa Mulungu, ndipo samatsana chiphunzitso cha Mulungu.

Mneneriyo anawauzanso kuti lidzafika tsiku limene Yehova adzabwera kudzazenga mlandu ndi kuyeretsa anthu ake, ndipo adachita izi potumiza wamthenga wake kuti akakonze njira ndi kunenera za chipangano chake.

Za mkatimu

Kuchimwa kwa Aisraele pa zinthu zina ndi zina

1.1—2.16

Yehova akubwera kudzaweruza ndi kuyeretsa anthu ake

2.17—4.6

Categories
MALAKI

MALAKI 1

Kusayamika kwa Israele pa chikondi cha Mulungu

1 Katundu wa mau a Yehova wa kwa Israele mwa Malaki.

2 Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;

3 koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m’chipululu.

4 Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.

5 Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.

6 Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?

7 Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M’menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.

8 Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.

9 Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.

10 Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m’dzanja lanu.

11 Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwaamitundu; ndipo m’malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

12 Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Ambuye laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.

13 Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.

14 Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m’gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/1-5411abd1b38cae2bed800f0e3693a448.mp3?version_id=1068—

Categories
MALAKI

MALAKI 2

Mau akutsutsa ansembe

1 Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu.

2 Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.

3 Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho.

4 Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kutichipanganochanga chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.

5 Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa.

6 Chilamulo cha zoona chinali m’kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeke m’milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.

7 Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.

8 Koma inu mwapatuka m’njira; mwakhumudwitsa ambiri m’chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu.

9 Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.

Za kukwatira akazi achilendo. Za kuleka mkazi kosayenera

10 Kodi sitili naye Atate mmodzi ife tonse? Sanatilenge kodi Mulungu mmodzi? Tichita monyengezana yense ndi mnzake chifukwa ninji, ndi kuipsa chipangano cha makolo athu?

11 Yuda wachita monyenga, ndi mu Israele ndi muYerusalemumwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.

12 Yehova adzalikha munthu wakuchita ichi, wogalamutsa ndi wovomereza m’mahema a Yakobo, ndi iye wopereka chopereka kwa Yehova wa makamu.

13 Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m’dzanja lanu.

14 Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.

15 Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.

16 Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.

17 Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/2-f56e10ee099421a823118c4582ffae26.mp3?version_id=1068—

Categories
MALAKI

MALAKI 3

Za mthenga wokonzeratu njira ya Ambuye

1 Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wachipanganoamene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.

2 Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;

3 ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsasiliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.

4 Pamenepo chopereka cha Yuda ndiYerusalemuchidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija.

5 Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

6 Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.

Za kusalanda za Mulungu ndi madalitso atsatapo

7 Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?

8 Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka.

9 Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.

10 Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

11 Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m’munda, ati Yehova wa makamu.

12 Ndipoamitunduonse adzatcha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.

13 Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi chiyani?

14 Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?

15 Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.

16 Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.

17 Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.

18 Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/3-789b8f3961efcb83707bd67ef5b71b72.mp3?version_id=1068—

Categories
MALAKI

MALAKI 4

Oipa adzalangidwa, okoma adzadalitsidwa. Asamale chilamulo; adzafika Eliya

1 Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.

2 Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m’mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang’ombe onenepa otuluka m’khola.

3 Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.

4 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.

5 Taonani, ndidzakutumizirani Eliyamnenerilisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.

6 Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/4-2b57f622ee755e75b295c6e1107275a1.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Mateyu

limafotokoza za uthenga wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, amene kudzera mwa iye Mulungu anakwaniritsa malonjezano ake amene adanena kwa anthu ake mu Chipangano Chakale. Uthenga Wabwinowu si wa mtundu wa Ayuda okha ai, umene Yesu anabadwira ndi kukhala pakati pao, koma ndi wa dziko lonse.

Buku la

Mateyu

ndi lolembedwa mwadongosolo. Likuyamba ndi kubadwa kwa Yesu, kenaka ndi kulongosola za ubatizo ndi mayesero ake, komanso ndikudzanena za utumiki wake wolalikira, kuphunzitsa ndi kuchiritsa m’dera la Galileya. Zitatha izi, Uthengawu ukunena za ulendo wa Yesu kuchoka ku Galileya kupita ku Yerusalemu ndiponso zochitika mu sabata yomaliza ya utumiki wa Yesu, ndi kudzatsendera ndi kupachikidwa kwake pamtanda komanso kuukitsidwa kwake.

Bukuli likumuonetsa Yesu ngati Mphunzitsi wamkulu, amene ali ndi mphamvu zomasulira Malamulo a Mulungu ngati mwini wake, komanso amene amaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. Zambiri mwa ziphunzitso zake zimagawidwa m’magulu asanu: Choyamba ndi chiphunzitso cha paphiri, chimene chikunena za khalidwe labwino, maudindo, cholowa ndi matsiriziro ake a mzika za Ufumu wa Kumwamba (mutu 5 mpaka 7); Chachiwiri ndi malangizo kwa ophunzira ake 12 pa za utumiki wao (mutu 10); Chachitatu ndi mafanizo a Ufumu wa Kumwamba (mutu 13); Chachinai ndi chiphunzitso kuti kutsata Yesu kumatanthauza chiyani (mutu 18) ndipo chachisanu ndi chiphunzitso cha chimaliziro cha nthawi ino komanso kubweranso kwa Ufumu wa Kumwamba (mutu 24 mpaka 25).

Za mkatimu

Kubadwa kwa Yesu Khristu ndi mbiri ya makolo ake

1.1—2.23

Utumiki wa Yohane Mbatizi

3.1-12

Yesu abatizidwa nayesedwa

3.13—4.11

Utumiki wa Yesu ku Galileya

4.12—18.35

Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu

19.1—20.34

Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira

1.1—27.66

Ambuye auka kwa akufa naonekera kwa anthu

28.1-20

Categories
MATEYU

MATEYU 1

Makolo a Yesu Khristu monga mwa thupi

1 Buku la kubadwa kwa YesuKhristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.

2 Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;

3 ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;

4 ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni; ndi Nasoni anabala Salimoni;

5 ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese;

6 ndi Yese anabala Davide mfumuyo.

Ndipo Davide anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya;

7 ndi Solomoni anabala Rehobowamu; ndi Rehobowamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa;

8 ndi Asa anabala Yehosafati; ndi Yehosafati anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya;

9 ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;

10 ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;

11 ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babiloni.

12 Ndipo pambuyo pake pa kutengedwako ku Babiloni, Yekoniya anabala Sealatiele; ndi Sealatiele anabala Zerubabele;

13 ndi Zerubabele anabala Abihudi; ndi Abihudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;

14 ndi Azoro anabala Zadoki; ndi Zadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliudi;

15 ndi Eliudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;

16 ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wake wa Maria, amene Yesu, wotchedwa Khristu, anabadwa mwa iye.

17 Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.

Kubadwa kwa Yesu Khristu

18 Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.

19 Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m’mtima kumleka iye m’tseri.

20 Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani,mngelowa Ambuye anaonekera kwa iye m’kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.

21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.

22 Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwamneneri, ndi kuti,

23 Onani namwali adzaima,

nadzabala mwana wamwamuna,

ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele.

Ndilo losandulika, Mulungu nafe.

24 Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake;

25 ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/1-e89841c80421bb3611a8c1a8a2be86f8.mp3?version_id=1068—