Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 2

Masomphenya achitatu: Yerusalemu ayesedwa ndi chingwe

1 Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi chingwe choyesera m’dzanja lake.

2 Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, KukayesaYerusalemu, kuona ngati chitando chake nchotani, ndi m’litali mwake motani.

3 Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anatuluka, ndi mthenga wina anatuluka kukomana naye,

4 nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m’midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.

5 Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m’kati mwake.

6 Haya, haya, thawani kudziko la kumpoto ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.

7 HayaZiyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babiloni.

8 Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwaamitunduamene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso lake.

9 Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.

10 Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.

11 Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.

12 Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m’dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu.

13 Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/2-abdfe21c52da40c6a4c722e081e0afc0.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 3

Masomphenya achinai: Satana atsutsana ndi Yoswa, Mulungu amuyesa wolungama

1 Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndiSatanaalikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye.

2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankhaYerusalemuakudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?

3 Koma Yoswa analikuvala nsalu zonyansa naima pamaso pa mthenga.

4 Ndipo Iye anayankha nanena ndi iwo akuima pamaso pake, ndi kuti, Mumvule nsalu zonyansazi. Nati kwa iye, Taona, ndakuchotsera mphulupulu zako, ndipo ndidzakuveka zovala za mtengo wake.

5 Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo.

6 Ndipo mthenga wa Yehova anamchitira Yoswa umboni, ndi kuti,

7 Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m’njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.

8 Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.

9 Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pamwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.

10 Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/3-6e416660f40a36224188901a3941cce1.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 4

Masomphenya achisanu: choikaponyali chagolide ndi nyali zake

1 Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m’tulo take.

2 Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;

3 ndi mitengo iwiri yaazitonapomwepo, wina kudzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina kudzanja lake lamanzere.

4 Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziyani mbuyanga?

5 Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.

6 Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.

7 Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao.

8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,

9 Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ake omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa inu.

10 Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating’ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m’dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.

11 Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa choikaponyali nchiyani?

12 Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide?

13 Ndipo anandiyankha, nati, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.

14 Pamenepo anati, Awa ndi ana aamuna awiri a mafuta oimirira pamaso pa Mbuye wa dziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/4-8c44396282dee4e72e15e44a9e3759e4.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 5

Masomphenya achisanu ndi chimodzi: mpukutu wouluka

1 Pamenepo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, taonani, mpukutu wouluka.

2 Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wake mikono makumi awiri, ndi chitando chake mikono khumi.

3 Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lilikutulukira padziko lonse; pakuti aliyense wakuba adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi aliyense wakulumbira zonama adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili.

4 Ndidzalitulutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m’nyumba ya wakuba, ndi m’nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yake, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yake ndi miyala yake.

Masomphenya achisanu ndi chiwiri: mkazi ndi efa

5 Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anatuluka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nchiyani ichi chilikutulukachi.

6 Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m’dziko lonse;

7 ndipo taonani, chozunguniza chantovu chotukulidwa: ndipo ichi ndi mkazi wokhala pakati pa efa.

8 Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m’kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake.

9 Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m’mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati padziko ndi thambo.

10 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo?

11 Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m’dziko la Sinara; kuti amuike efayo, namkhazikeko pamalo kwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/5-45094e51310b7976780daac915e3895f.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 6

Masomphenya achisanu ndi chitatu: magaleta anai

1 Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.

2 Ku galeta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi kugaleta wachiwiri akavalo akuda;

3 ndi kugaleta wachitatu a kavalo oyera; ndi kugaleta wachinai akavalo olimba amawanga.

4 Ndipo ndinayankha ndinati kwa mthenga wolankhula ndi ine, Izi nziyani, mbuyanga?

5 Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakutuluka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

6 Galeta wa akavalo akuda atulukira kudziko la kumpoto; ndi oyerawo atulukira kuwatsata; ndi amawanga atulukira kudziko la kumwera.

7 Ndi amphamvuwo anatuluka nayesa kunka kuyendayenda m’dziko; pakuti adati, Mukani, yendayendani m’dziko. Momwemo anayendayenda m’dziko.

8 Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akutuluka kunka kudziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m’dziko la kumpoto.

Akorona a Yoswa

9 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,

10 Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni,

11 ndipo utengesilivandi golide, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe;

12 nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m’malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova:

13 inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri.

14 Ndipo akorona adzakhala wa Helidai, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Heni mwana wa Zefaniya, akhale chikumbutso mu Kachisi wa Yehova.

15 Ndipo iwo akukhala kutali adzafika, nadzamanga ku Kachisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ichi chidzachitika ngati mudzamvera mwachangu mau a Yehova Mulungu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/6-6943f1ec7080e79cd0132cf692a2d81c.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 7

Kusala kosalamulidwa ndi Yehova

1 Ndipo kunachitika chaka chachinai cha mfumu Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya tsiku lachinai la mwezi wachisanu ndi chinai, ndiwo Kisilevi.

2 Ndipo a ku Betele anatuma Sarezere ndi Regemumeleke ndi anthu ao, apepeze Yehova,

3 nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri?

4 Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

5 Nena kwa anthu onse a m’dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?

6 Ndipo pamene mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi?

7 Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, mujaYerusalemuanali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m’mizinda mwake pozungulira pake, ndi m’dziko la kumwera, ndi m’chidikha munali anthu okhalamo?

8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Zekariya, ndi kuti,

9 Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani chiweruzo choona, nimuchitire yense mnzake chifundo ndi ukoma mtima;

10 musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m’mtima mwake kumchitira choipa munthu mnzake.

11 Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.

12 Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m’menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.

13 Ndipo kunachitika, monga Iye anafuula, koma iwo sanamvere; momwemo iwo adzafuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu;

14 koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwaamitunduonse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m’mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/7-6fa61a3e094bb34955944e7cfd5d72b2.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 8

Madalitso olonjezedwa ndi Mulungu

1 Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

2 Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanjeZiyonindi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu.

3 Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati paYerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.

4 Atero Yehova wa makamu: M’miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yake m’dzanja lake chifukwa cha ukalamba wake.

5 Ndi m’miseu ya mzinda mudzakhala ana aamuna ndi aakazi akusewera m’miseu yake.

6 Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa pamaso panga? Ati Yehova wa makamu.

7 Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m’dziko la kum’mawa, ndi m’dziko la kumadzulo;

8 ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m’kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m’choonadi ndi m’chilungamo.

9 Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kachisi, kuti amangidwe.

10 Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.

11 Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu.

12 Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.

13 Ndipo kudzachitika kuti, monga munali chotembereretsa mwaamitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israele, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala chodalitsa nacho; musaope, alimbike manja anu.

14 Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke;

15 momwemonso ndinalingirira masiku ano kuchitira chokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musaopa.

16 Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m’zipata zanu;

17 ndipo musalingirira choipa m’mtima mwanu yense pa mnzake; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.

18 Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

19 Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.

20 Atero Yehova wa makamu: Kudzachitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m’mizinda yambiri adzafika,

21 ndi okhala m’mzinda umodzi adzamuka kumzinda wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.

22 Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova.

23 Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/8-7943b914bf6b33accc8f7a991ede24b2.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 9

Kulangidwa kwa amitundu ena

1 Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele;

2 ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Tiro ndi Sidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri.

3 Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundikasilivangati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo.

4 Taonani, Ambuye adzamlanda zake, nadzakantha mphamvu yake igwe m’manja; ndipo adzatha ndi moto.

5 Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.

6 Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala mu Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.

7 Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m’kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko mu Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi.

8 Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.

9 Kondwera kwambiri, mwana wamkazi waZiyoni; fuula mwana wamkazi waYerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.

10 Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwaamitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.

11 Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m’dzenje m’mene mulibe madzi.

12 Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.

13 Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.

14 Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera.

15 Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe.

16 Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m’korona yakunyezimira padziko lake.

17 Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/9-d3b0e5262d121c9a64a8d58cfbe0db23.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 10

Malonjezo a kwa Israele

1 Pemphani kwa Yehova mvula, m’nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mivumbi ya mvula, kwa yense zophukira kuthengo.

2 Pakutiaterafianena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.

3 Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zake, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wake waulemerero kunkhondo.

4 Kwa iye kudzafuma mwala wa kungodya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi.

5 Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m’thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi.

6 Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.

7 Ndipo iwo a ku Efuremu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzachiona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova.

8 Ndidzawaimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzachuluka monga anachulukira kale.

9 Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukira m’maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera.

10 Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa mu Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m’dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira.

11 Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m’nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka.

12 Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m’dzina lake; ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/10-503331c6c85d45c22e6c740027a12733.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 11

Kulangidwa kwa osalapa

1 Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako.

2 Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi.

3 Mau a kuchema kwa abusa! Pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! Pakuti kudzikuza kwa Yordani kwaipsidwa.

4 Atero Yehova Mulungu wanga: Dyetsani zoweta zakukaphedwa;

5 zimene eni ake azipha, nadziyesera osapalamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazichitira chifundo.

6 Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m’dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m’dzanja la mnansi wake, ndi m’dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m’dzanja mwao sindidzawalanditsa.

7 M’mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.

8 Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.

9 Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; chilikufa chife; chosoweka chisoweke; ndi zotsala zidyane, chonse nyama ya chinzake.

10 Ndipo ndinatenga ndodo yanga Chisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalichita ndi mitundu yonse ya anthu.

11 Ndipo linathyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova.

12 Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli asilivamakumi atatu.

13 Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga masekeli makumi atatu a siliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m’nyumba ya Yehova.

14 Pamenepo ndinadula ndodo yanga ina, ndiyo Chomanganitsa, kuti ndithetse chibale cha pakati pa Yuda ndi Israele.

15 Ndipo Yehova anati kwa ine, Dzitengerenso zipangizo za mbusa wopusa.

16 Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m’dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yothyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang’amba ziboda zao.

17 Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/11-c561b50ce92666c22592fbac7470bb2b.mp3?version_id=1068—