Categories
HABAKUKU

HABAKUKU 3

Pemphero la Habakuku

1 Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoti.

2 Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha;

Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka,

pakati pa zaka mudziwitse;

pa mkwiyo mukumbukire chifundo.

3 Mulungu anafuma ku Temani,

ndi Woyerayo kuphiri la Parani.

Ulemerero wake unaphimba miyamba,

ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.

4 Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika;

anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m’dzanja lake,

ndi komweko kunabisika mphamvu yake.

5 Patsogolo pake panapita mliri,

ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.

6 Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi;

anapenya, nanjenjemeretsaamitundu;

ndi mapiri achikhalire anamwazika,

zitunda za kale lomwe zinawerama;

mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.

7 Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka;

nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.

8 Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje?

Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi,

kapena ukali wanu panyanja,

kuti munayenda pa akavalo anu,

pa magaleta anu a chipulumutso?

9 Munapombosola uta wanu;

malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona.

Munang’amba dziko lapansi ndi mitsinje.

10 Mapiri anakuonani, namva zowawa;

chigumula cha madzi chinapita;

madzi akuya anamveketsa mau ake,

nakweza manja ake m’mwamba.

11 Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;

pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo.

Pa kung’anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.

12 Munaponda dziko ndi kulunda,

munapuntha amitundu ndi mkwiyo.

13 Munatulukira chipulumutso cha anthu anu,

chipulumutso cha odzozedwa anu;

munakantha mutu wa nyumba ya woipa,

ndi kufukula maziko kufikira m’khosi.

14 Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake;

anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza;

kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.

15 Munaponda panyanja ndi akavalo anu,

madzi amphamvu anaunjikana mulu.

16 Ndinamva, ndi m’mimba mwanga munabwadamuka,

milomo yanga inanthunthumira pamau,

m’mafupa mwanga mudalowa chivundi,

ndipo ndinanjenjemera m’malo mwanga;

kuti ndipumule tsiku lamsauko,

pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.

17 Chinkana mkuyu suphuka,

kungakhale kulibe zipatso kumpesa;

yalephera ntchito yaazitona,

ndi m’minda m’mosapatsa chakudya;

ndi zoweta zachotsedwa kukhola,

palibenso ng’ombe m’makola mwao;

18 koma ndidzakondwera mwa Yehova,

ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.

19 Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga,

asanduliza mapazi anga ngati a mbawala,

nadzandipondetsa pa misanje yanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HAB/3-d60f571ace2388a1506eb2489361e3af.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Iyeyu adalalika mau ake pa nthawi imene mfumu Yosiya anali pafupi kukhazikitsa malamulo oongolera zinthu mu ufumu wake (621 BC.) Bukuli lili ndi mitu yosiyanasiyana ya mauthenga a uneneri monga: tsiku la chiweruzo ndi chiwonogeko, pamene Yuda adzalangidwe chifukwa chopembedza milungu ina. Yehova adzalanganso mitundu ina. Ngakhale Yerusalemu adzawonongeke, patsogolopo mzindawo udzakonzedwanso, ndipo anthu odzichepetsa ndi olungama adzakhala m’menemo.

Za mkatimu

Za tsiku la Yehova pamene Mulungu adzaimba mlandu

1.1—2.3

Tsoka lodzagwera mitundu ina ya anthu yozungulira Israele

2.4-15

Tsoka lodzagwera Yerusalemu; adzalapa ndipo Yehova adzamuwombola

3.1-20

Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA 1

Mau oopsa akuchenjeza Yerusalemu ndi Yuda

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.

2 Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka, ati Yehova.

3 Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.

4 Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala muYerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala aBaalakuwachotsa m’malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;

5 ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;

6 ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.

7 Khala chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake.

8 Ndipo kudzachitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akuvala chovala chachilendo.

9 Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.

10 Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera ku Chipata cha Nsomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.

11 Chemani okhala m’chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenzasilivaaonongeka.

12 Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m’mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.

13 Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.

14 Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.

15 Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;

16 tsiku la lipenga ndi lakufuulira mizinda yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungodya.

17 Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.

18 Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m’dziko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEP/1-a55a56d6e3bf63af96fb2f17018a8680.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA 2

Mau akuchenjeza amitundu ena

1 Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu;

2 lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.

3 Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.

4 Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa.

5 Tsoka, okhala m’dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m’dziko.

6 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala busa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta.

7 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m’nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.

8 Ndinamva kutonza kwa Mowabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao.

9 Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.

10 Ichi adzakhala nacho m’malo mwa kudzikuza kwao, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.

11 Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m’zisumbu zonse zaamitundu.

12 Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.

13 Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.

14 Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m’mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m’mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza.

15 Uwu ndi mzinda wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m’mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama zakuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEP/2-334bf4cb7c19772e6b8e1886a0f2cce5.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA 3

Mau akudzudzula Yerusalemu. Malonjezo a kwa okhulupirika otsala

1 Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mzinda wozunza!

2 Sanamvera mau, sanalole kulangizidwa; sanakhulupirire Yehova, sanayandikire kwa Mulungu wake.

3 Akalonga ake m’kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.

4 Aneneri ake ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza chilamulo.

5 Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m’mawa ndi m’mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.

6 Ndaonongaamitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; mizinda yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.

7 Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pake pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, navunditsa machitidwe ao onse.

8 Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.

9 Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.

10 Kuchokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera nacho chopereka changa.

11 Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m’phiri langa lopatulika.

12 Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.

13 Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m’kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.

14 Imba, mwana wamkazi waZiyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi waYerusalemu.

15 Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa.

16 Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.

17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m’chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.

18 Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene katundu wake anawakhalira mtonzo.

19 Taonani, nthawi yomweyo ndidzachita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale chilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m’dziko lonse.

20 Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEP/3-838b68b290a5f5d1b0ef62c8710cedad.mp3?version_id=1068—

Categories
HAGAI

HAGAI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneriyu adalalika mau ake chaka cha 520 BC., Ayuda ena atabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo. Anthuwo anali atabwerera ku ukapolo namakhala ku Yerusalemu kwa zaka zingapo, koma Kachisi anali bwinja lenileni. Atsogoleri anapereka uthenga kwa anthu kuti amangenso Kachisi, ndipo Ambuye akulonjeza kuti m’tsogolo anthu ake adzakhala pabwino ndi pa mtendere.

Za mkatimu

Yehova awalamula kuti amangenso Nyumba yake

1.1-15

Mau ena owalimbitsa mtima Ayudawo

2.1-23

Categories
HAGAI

HAGAI 1

Mau akudzudzula ndi kudandaulira Ayuda amangenso Kachisi

1 Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagaimnenerikwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,

2 Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.

3 Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,

4 Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m’nyumba zanu zochingidwa m’katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?

5 Chifukwa chake tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.

6 Mwabzala zambiri, koma mututa pang’ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m’thumba lobooka.

7 Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.

8 Kwerani kudziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.

9 Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang’ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Chifukwa ninji? Ati Yehova wa makamu. Chifukwa cha nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwake.

10 M’mwemo chifukwa cha inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zake.

11 Ndipo ndinaitana chilala chidzere dziko, ndi mapiri, ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zimene ibala nthaka, ndi anthu, ndi zoweta, ndi ntchito zonse za manja.

12 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova.

13 Ndipo Hagai mthenga wa Yehova, mu uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova.

14 Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira ntchito m’nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,

15 tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HAG/1-16890db4935bf58079d8e7fb62233cae.mp3?version_id=1068—

Categories
HAGAI

HAGAI 2

Ulemerero wa Kachisi wachiwiri

1 Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku la makumi awiri ndi chimodzi la mweziwo, mau a Yehova anadza mwa Hagaimneneri, ndi kuti,

2 Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti,

3 Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi mu ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m’maso mwanu ngati chabe?

4 Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m’dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;

5 monga momwe ndinapangana nanu muja munatuluka mu Ejipito, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu.

6 Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe;

7 ndipo ndidzagwedezaamitunduonse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.

8 Silivandi wanga, golide ndi wanga, ati Yehova wa makamu.

9 Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m’malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.

Madzudzulo ndi malonjezo

10 Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wachisanu ndi chinai, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,

11 Atero Yehova wa makamu: Funsatu ansembe za chilamulo, ndi kuti,

12 Munthu akanyamulira nyama yopatulika m’ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.

13 Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.

14 Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo ntchito iliyonse ya manja ao; ndi ichi achipereka, chili chodetsedwa.

15 Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m’tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pamwala mu Kachisi wa Yehova,

16 pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku choponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha.

17 Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m’ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.

18 Musamalire, kuyambira lero ndi m’tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wachisanu ndi chinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kachisi wa Yehova, samalirani.

19 Kodi mbeu ikali m’nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndiazitonasizinabale; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani.

Adani adzaonongeka, Zerubabele adzakwezeka

20 Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yachiwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti,

21 Nena ndi Zerubabele chiwanga cha Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi;

22 ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake.

23 Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealatiele, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HAG/2-1d736c146f8a3d48f54df6f3d1e19fdb.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli lili ndi zigawo ziwiri: Gawo loyamba ndi mau amene mneneri adalalikira kuyambira chaka cha 520 BC. Zekariya akulongosola zimene adaziwona m’masomphenya ndipo akuwachenjeza anthuwo nawalimbitsa mtima kuti akonzenso Kachisi komanso mzinda wa Yerusalemu. Iwo ayenera adziyeretsa popeza Yehova adzawadalitsa (1—8). Gawo lachiwiri ndi kaundula wa mauneneri osiyanasiyana onena za kubwera kwa Mesiya ndipo tsiku la chiweruzo (9—14).

Za mkatimu

Mau oyamba

1.1—8.23

Mau a Yehova aimba mlandu mitundu ina ya anthu

9.1-8

Mau ena olonjeza zabwino

9.9—14.21

Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 1

Mneneri adandaulira anthu Ayuda aleke zoipa zao

1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Idomneneri, ndi kuti,

2 Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu.

3 Chifukwa chake uziti nao, Atero Yehova wa makamu: Bwererani kudza kwa Ine, ati Yehova wa makamu, ndipo Ine ndidzabwerera kudza kwa inu, ati Yehova wa makamu.

4 Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova.

5 Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi?

6 Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.

Masomphenya oyamba: akavalo

7 Tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wakhumi ndi chimodzi, ndiwo mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,

8 Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.

9 Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani.

10 Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m’dziko.

11 Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m’dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula.

12 Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundoYerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?

13 Ndipo Yehova anamyankha mthenga wakulankhula ndi ine mau okoma, mau akutonthoza mtima.

14 Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, fuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndichitira nsanje Yerusalemu ndiZiyonindi nsanje yaikulu.

15 Ndipo ndikwiya naoamitunduokhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang’ono, ndipo anathandizira choipa.

16 Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.

17 Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Mizinda yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.

Masomphenya achiwiri: nyanga zinai ndi osula anai

18 Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.

19 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.

20 Ndipo Yehova anandionetsa osula anai.

21 Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/1-f5510f91626ffadd7875a2ee85142e76.mp3?version_id=1068—