Categories
YONA

YONA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Yona

likusiyana ndi mabuku ena a aneneri a mu Baibulo chifukwa likufotokoza mwatsatanetsatane zimene adachita mneneriyo amene sadafune kumvera lamulo la Mulungu. Mulungu anamuuza kuti apite kumzinda wa Ninive, umene unali likulu ka ufumu wamphamvu wa Asiriya, amene anali mdani woipitsitsa wa Aisraele. Koma Yona sanafune kukalalikira uthenga wa Mulungu kumeneko, chifukwa amakhulupirira kuti Mulunguyo sakaononga mzindawo. Patachitika zinthu zingapo zodabwitsa, iyeyo anavomera ndipo pa mapeto ake anakwiya ataona kuti uthenga wake wa chilango sunapherezere.

Bukuli likuonetsa kuti Mulungu ali ndi ulamuliro wonse pa chilengedwe. Komanso likuonetsa kuti Mulungu ndi wachikondi ndi wachifundo, amene amafunitsitsa kukhululukira ndi kupulumutsa adani a anthu ake ngati alapa, osati ndi kuwalanga kapena kuwaononga.

Za mkatimu

Kuitanidwa kwa Yona ndi kusamvera kwake

1.1-17

Yona alapa napulumutsidwa

2.1-10

Uthenga wa Yona wotsutsana ndi Ninive

3.1-10

Chifundo cha Mulungu pa Ninive

4.1-11

Categories
YONA

YONA 1

Kuitanidwa kwa Yona, kuthawa kwake, ndi kulangidwa kwake

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti,

2 Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.

3 Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m’menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.

4 Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.

5 Pamenepo amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m’nyanja akatundu anali m’chombo kuchipepuza. Koma Yona adatsikira m’munsi mwa chombo, nagona tulo tofa nato.

6 Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam’tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike.

7 Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M’mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.

8 Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani? Ntchito yako njotani? Ufuma kuti? Dziko lako nliti? Nanga mtundu wako?

9 Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.

10 Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ichi nchiyani wachichita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza.

11 Tsono anati kwa iye, Tichitenji nawe, kuti nyanja itichitire bata? Popeza namondwe anakulakulabe panyanja.

12 Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m’nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkulu amene wakugwerani chifukwa cha ine.

13 Koma amunawo anapalasa kubwerera kumtunda, koma sanathe; pakuti namondwe wa panyanja anakulakula mokomana nao.

14 Pamenepo anafuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike chifukwa cha moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosachimwa; pakuti, Inu Yehova, mwachita monga mudakomera Inu.

15 Momwemo ananyamula Yona, namponya m’nyanja; ndipo nyanja inaleka kukokoma kwake.

16 Ndipo amunawo anaopa Yehova ndi mantha aakulu, namphera Yehova nsembe, nawinda.

17 Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m’mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JON/1-eec6119ff97f72a5cc6a099ea60f44b9.mp3?version_id=1068—

Categories
YONA

YONA 2

Pemphero la Yona ali m’mimba mwa chinsomba

1 Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m’mimba mwa nsombayo.

2 Ndipo anati,

Ndinaitana Yehova m’nsautso wanga,

ndipo anandiyankha ine;

ndinafuula ndili m’mimba ya manda,

ndipo munamva mau anga.

3 Pakuti munandiponya mwakuya m’kati mwa nyanja,

ndipo madzi anandizinga;

mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.

4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu;

koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.

5 Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,

madzi akuya anandizungulira,

kayandeyande wa m’nyanja anandikulunga mutu.

6 Ndinatsikira kumatsinde a mapiri,

mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;

koma munandikwezera moyo wanga

kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.

7 Pokomoka moyo wanga m’kati mwanga ndinakumbukira Yehova;

ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.

8 Iwo osamalira mabodza opanda pake

ataya chifundo chaochao.

9 Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika,

ndidzakwaniritsa chowinda changa.

Chipulumutso ncha Yehova.

10 Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JON/2-58e99d0de00220c8f33c33195a6f9d77.mp3?version_id=1068—

Categories
YONA

YONA 3

Yona ku Ninive. Kulapa kwa a ku Ninive

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yachiwiri, ndi kuti,

2 Nyamuka, pita ku Ninive mzinda waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.

3 Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Ninive, monga mwa mau a Yehova. Koma Ninive ndiwo mzinda waukulu pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.

4 Ndipo Yona anayamba kulowa mzindawo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Ninive adzapasuka.

5 Ndipo anthu a Ninive anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng’ono wa iwowa.

6 Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m’maphulusa.

7 Ndipo analalikira, nanena mu Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng’ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;

8 koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, ndipo zifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m’manja mwake.

9 Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.

10 Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JON/3-92e8214f7f0593aea9f5e7ae42a01d63.mp3?version_id=1068—

Categories
YONA

YONA 4

Kudandaula kwa Yona, kumdzudzula kwa Mulungu

1 Koma sikudakomere Yona konse, ndipo anapsa mtima.

2 Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m’dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.

3 Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.

4 Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?

5 Pamenepo Yona anatuluka m’mzinda, nakhala pansi kum’mawa kwa mzinda, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mzinda.

6 Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m’nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.

7 Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m’mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota.

8 Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum’mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.

9 Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

10 Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirepo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

11 ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m’mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JON/4-564daa16dc68aaf72129c732994fd76f.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneriyu adalalika mau ake ku Yuda panthawi ya mneneri Yesaya. Iye ankadziwiratu kuti ufumu wa Yuda nawonso udzawonongedwa. Monga muja Yehova adalangira ufumu wakumpoto chifukwa Aisraelewo ntchito zao zinali zopanda chilungamo, momwemonso adzalanga ndi Ayuda omwe chifukwa cha zochita zao zosalungama. Komabe pa mau ake Mika akuonetsa chikhulupiriro chakuti Mulungu adzakonzanso zinthu kutsogoloko kuti zidzakhale bwino.

Kutsogoloko Mulungu adzakhazikitsanso ufumu wake kudzera mwa mmodzi mwa zidzukulu za Davide, ndipo adzadzetsa mtendere ponseponse (5.2-4).

Mau ena ofunikira kwambiri amene akunena mwachidule zimene aneneri anali kulalikira ndi awa akuti, “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (6.8)

Za mkatimu

Mau a Yehova otsutsa Aisraele ndi Ayuda

1.1—3.12

Mau ena a Yehova olonjeza zabwino

4.1—5.15

Mau ena a Yehova ochenjeza anthu, mau ena otsutsa chikhulupiriro

6.1—7.20

Categories
MIKA

MIKA 1

Mau akuchenjeza Israele ndi Yuda chifukwa cha machimo ao

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndiYerusalemu.

2 Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m’mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.

3 Pakuti, taonani, Yehova alikutuluka m’malo mwake, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi.

4 Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang’ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetsereka.

5 Chichitika ichi chonse chifukwa cha kulakwa kwa Yakobo, ndi machimo a nyumba ya Israele. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? Ndi misanje ya Yuda ndi iti? Si ndiyo Yerusalemu?

6 Chifukwa chake ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m’munda, ngati zooka m’munda wampesa; ndipo ndidzataya miyala yake m’chigwa, ndi kufukula maziko ake.

7 Ndi mafano ake osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zake zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ake onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi wachiwerewere, ndipo zidzabwerera kumphotho ya mkazi wachiwerewere.

8 Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.

9 Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu.

10 Musachifotokoza mu Gati, musalira misozi konse; m’nyumba ya Afira ndinagubuduka m’fumbi.

11 Pitiratu, wokhala mu Safiri iwe, wamaliseche ndi wamanyazi; wokhala mu Zanani sanatuluke; maliro a Betezele adzakulandani pokhala pake.

12 Pakuti wokhala mu Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu.

13 Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala mu Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi waZiyonindi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe.

14 Chifukwa chake pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti-Gati; nyumba za Akizibu zidzakhala chinthu chabodza kwa mafumu a Israele.

15 Ndidzakutengeranso wokhala mu Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu.

16 Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/1-dd0804d9b0b670726b7ec842db775a3e.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 2

Mau akutsutsa akulanda za eni

1 Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m’mawa achichita, popeza chikhozeka m’manja mwao.

2 Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.

3 Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa.

4 Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.

5 Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m’msonkhano wa Yehova.

6 Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka.

7 Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? Izi ndi ntchito zake kodi? Mau anga samchitira zokoma kodi, iye amene ayenda choongoka?

8 Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.

9 Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; muchotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha.

10 Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.

11 Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiyemneneriwa anthu ake.

12 Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.

13 Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/2-bae0082b6ea1ed09cf70abcdcf3f139c.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 3

Chilangizo cha Mulungu chifukwa cha atsogolera ndi aneneri onyenga

1 Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo?

2 Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;

3 inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.

4 Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.

5 Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m’kamwa mwao, amkonzera nkhondo;

6 chifukwa chake kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii.

7 Ndipo alauli adzachita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe.

8 Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.

9 Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.

10 AmangaZiyonindi mwazi, ndiYerusalemundi chisalungamo.

11 Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.

12 Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m’nkhalango.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/3-bfd32fbc93b47b106e48b12587cc5ecf.mp3?version_id=1068—

Categories
MIKA

MIKA 4

Kuitanidwa kwa amitundu

1 Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.

2 Ndipoamitunduambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake; pakuti kuZiyonikudzatuluka chilamulo, ndi kuYerusalemumau a Yehova.

3 Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.

4 Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.

5 Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya.

6 Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzamemeza wakutsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo, ndi iye amene ndinamsautsa;

7 ndipo wotsimphinayo ndidzamuyesa wotsala, ndi iye wotayidwa kutali mtundu wamphamvu; ndipo Yehova adzakhala mfumu yao m’phiri la Ziyoni kuyambira pamenepo kufikira kosatha.

8 Ndipo iwe, nsanja ya nkhosa, chitunda cha mwana wamkazi wa Ziyoni, udzafikira iwe, inde udzafika ulamuliro wakale, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.

9 Tsono ufuulitsa chifukwa ninji? Palibe mfumu mwa iwe kodi? Watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?

10 Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m’mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m’manja a adani ako.

11 Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.

12 Koma sadziwa zolingirira za Yehova, kapena kuzindikira uphungu wake; pakuti anawasonkhanitsa ngati mitolo kudwale.

13 Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/4-badb7f0515bb48122b4a78b506a35223.mp3?version_id=1068—