Categories
HOSEYA

HOSEYA 11

Kusayamika kwa Israele; machenjezo ndi malonjezo

1 Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.

2 Monga anawaitana, momwemo anawachokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.

3 Koma Ine ndinaphunzitsa Efuremu kuyenda, ndinawafungata m’manja mwanga; koma sanadziwe kuti ndinawachiritsa.

4 Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira chakudya.

5 Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera.

6 Ndi lupanga lidzagwera mizinda yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao.

7 Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m’mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m’mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.

8 Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m’kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.

9 Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m’mzinda.

10 Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo.

11 Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m’dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m’nyumba zao, ati Yehova

12 Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/11-ceba3fb5fd7ce2456bce62a4af4cb393.mp3?version_id=1068—

Categories
HOSEYA

HOSEYA 12

Mlandu wa Yehova pa Israele ndi Yuda

1 Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum’mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.

2 Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake.

3 M’mimba anagwira kuchitendeni cha mkulu wake, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu;

4 inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;

5 ndiye Yehova Mulungu wa makamu, chikumbukiro chake ndi Yehova.

6 M’mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.

7 Ndiye Mkanani, m’dzanja lake muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa.

8 Ndipo Efuremu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera chuma m’ntchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala tchimo.

9 Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m’mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika.

10 Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndachulukitsa masomphenya; ndi padzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo.

11 Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng’ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m’michera ya munda.

12 Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.

13 Ndipo mwamneneriYehova anakweretsa Israele kuchokera mu Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.

14 Efuremu wautsa mkwiyo wowawa, m’mwemo Iye adzamsiyira mwazi wake, ndi Ambuye wake adzambwezera chomtonza chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/12-a5247bf8c8d8ea87b7d0596d40ac0965.mp3?version_id=1068—

Categories
HOSEYA

HOSEYA 13

Tchimo la Israele ndi kulangidwa kwake

1 Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwaBaala, anafa.

2 Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga asilivawao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang’ombe.

3 Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m’mawa, ndi ngati mame akamuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.

4 Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m’dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.

5 Ndinakudziwa m’chipululu, m’dziko lotentha kwambiri.

6 Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; chifukwa chake anandiiwala Ine.

7 Chifukwa chake ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira.

8 Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung’amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.

9 Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako.

10 Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m’mizinda yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?

11 Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamchotsanso mu ukali wanga.

12 Mphulupulu ya Efuremu yamangika, tchimo lake lisungika.

13 Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana.

14 Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.

15 Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum’mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.

16 Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/13-aebf9218e58c9049adaf7d9c0c43f99f.mp3?version_id=1068—

Categories
HOSEYA

HOSEYA 14

Mulungu adandaulira Israele alape, nalonjeza kuwakhululukira

1 Israele, bwerera kunka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.

2 Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng’ombe.

3 Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.

4 Ndidzachiritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamchokera.

5 Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni.

6 Nthambi zake zidzatambalala, ndi kukoma kwake kudzanga kwa mtengo waazitona, ndi fungo lake ngati Lebanoni.

7 Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebanoni.

8 Efuremu adzati, Ndili ndi chiyaninso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndili ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zochokera kwa Ine.

9 Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/14-0bb80116005c4a009b21e41104698cc2.mp3?version_id=1068—

Categories
YOWELE

YOWELE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Yowele adalalikira makamaka pa nthawi ya ufumu wa Persiya, koma za moyo wake sitidziwa bwino. Iye akamba za mliri wa dzombe ndi chilala; zimene zaonongeratu mbeu zonse ndi mitengo yomwe. Mneneriyu aona ngati ichi ndi chizindikiro chosonyeza kuti tsiku la Yehova lidzabwera pamene Mulungu adzalanga anthu onse okana malamulo ake. Tsono Yowele akuwapempha anthuwo kuti atembenuke mtima ndi kubwerera kwa Chauta, poyembekeza kuti mwina Mulungu adzawakhulukira ndi kuwadalitsa monga adawalonjezera. Mau ena odziwika ndi akuti lidzafika tsiku pamene Yehova adzatuma mzimu wake pa anthu onse, aamuna ndi aakazi, achikulire ndi achinyamata omwe.

Za mkatimu

Mliri wa dzombe

1.1—2.17

Lonjezo la kukonzedwanso kwa zinthu

2.18-27

Tsiku la Ambuye

2.28—3.21

Categories
YOWELE

YOWELE 1

Tsoka lochokera ku dzombe ndi chilala

1 Mau a Yehova a kwa Yowele mwana wa Petuwele.

2 Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m’dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?

3 Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.

4 Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.

5 Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.

6 Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ake akunga mano a mkango, nukhala nao mano a chibwano a mkango waukulu.

7 Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka.

8 Lirani ngati namwali wodzimangira m’chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake.

9 Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro.

10 M’munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang’onong’ono.

11 Gomani, akulima m’minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m’minda zatayika.

12 Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse yakuthengo yafota; pakuti chimwemwe chathera ana a anthu.

13 Mudzimangire chiguduli m’chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m’chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.

14 Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m’dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.

15 Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

16 Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?

17 Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata.

18 Ha! Nyama ziusa moyo, magulu a ng’ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.

19 Ndifuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m’chipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse yakuthengo.

20 Inde nyama zakuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m’chipululu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOL/1-fd86bdda9874eba3be4da86cc13e9789.mp3?version_id=1068—

Categories
YOWELE

YOWELE 2

Chilango choopsa cha Mulungu

1 Muombe lipenga muZiyoni, nimufuulitse m’phiri langa lopatulika; onse okhala m’dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;

2 tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m’mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.

3 Moto unyambita pamaso pao, ndi m’mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m’mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.

4 Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo.

5 Atumphako ngati mkokomo wa magaleta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.

6 Pamaso pao mitundu ya anthu ikumva zowawa, nkhope yonse zitumbuluka.

7 Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m’mabande ao.

8 Sakankhana, ayenda lililonse m’mopita mwake; akagwa m’zida, siithyoka nkhondo yao.

9 Alumphira mzinda, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu.

10 Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;

11 ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m’chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?

12 Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro;

13 ndipo ng’ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.

14 Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.

15 Ombani lipenga mu Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa,

16 sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m’chipinda mwake, ndi mkwatibwi m’mogona mwake.

17 Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kutiamitunduawalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?

Lonjezo lakuti chidzachuluka chakudya

18 Pamenepo Yehova anachitira dziko lake nsanje, nachitira anthu ake chifundo.

19 Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu;

20 koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum’mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.

21 Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wachita zazikulu.

22 Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m’chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.

23 Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere mu Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba.

24 Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m’zosungiramo zao.

25 Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.

26 Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anachita nanu modabwitsa; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.

27 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndili pakati pa Israele, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.

28 Ndipo kudzachitika m’tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;

29 ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.

30 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo.

31 Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.

32 Ndipo kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m’phiri la Ziyoni ndi muYerusalemumudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOL/2-8172963882fc05844fd17ada36452125.mp3?version_id=1068—

Categories
YOWELE

YOWELE 3

Aneneratu za chilango cha Mulungu pa adani ake; Israele adzakonzekanso

1 Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi aYerusalemu,

2 ndidzasonkhanitsaamitunduonse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa.

3 Ndipo anachitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.

4 Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.

5 Popeza inu munatengasilivawanga ndi golide wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma mu akachisi anu;

6 munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwachotsa kutali kwa malire ao;

7 taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera chilango chanu pamutu panu;

8 ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m’dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena.

9 Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.

10 Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi zikwakwa zanu zikhale nthungo; wofooka anene, Ndine wamphamvu.

11 Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.

12 Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira.

13 Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu.

14 Aunyinji, aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira mlandu.

15 Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao.

16 Ndipo Yehova adzadzuma ali kuZiyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.

17 Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,

18 Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m’mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m’nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.

19 Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m’dziko lao.

20 Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo.

21 Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala mu Ziyoni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOL/3-13f23c99e02b5a637d29036cec975688.mp3?version_id=1068—

Categories
AMOSI

AMOSI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Amosi anali mneneri woyamba amene uthenga wake unalembedwa pafupifupi wonse. Ngakhale amachokera ku Yuda, iye analalikira kwa anthu a mu ufumu wa kumpoto kwa Israele m’zaka za pafupifupi 750 BC. Iyi inali nthawi imeneyo dziko linali pa mtendere, ndipo zinthu zimayenda bwino kumbali ya chuma komanso anthu amakonda kupembedza. Komabe Amosi adaona kuti odyerera chuma anali olemera okha basi, ndipo iwo amagwiritsa ntchito mphamvu zawo pofuna kupondereza osauka. Kupembedza kwao kunali kwachinyengo ndipo chitetezo sichinali monga zinthu zimaonekera. Analalikira ndi mtima wake wonse komanso mwamphamvu kuti Mulungu adzaononga dzikolo. Iye anawadandaulira kuti chilungamo chiyende “ngati mtsinje wosefuka” (5.24), ndi kuti pakutero, “kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.” (5.15)

Za mkatimu

Chiweruzo pa maiko oyandikana ndi Israele

1.1—2.5

Chiweruzo pa Israele

2.6—6.14

Masomphenya asanu

7.1—9.15

Categories
AMOSI

AMOSI 1

Chilango cha Mulungu pa amitundu ozinga Israele

1 Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng’ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.

2 Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali muZiyoni, nadzamveketsa mau ake ali muYerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.

3 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo;

4 koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi.

5 Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m’chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.

6 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu;

7 koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu;

8 ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.

9 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;

10 koma ndidzatumiza moto pa linga la Tiro, ndipo udzanyeketsa nyumba zake zachifumu.

11 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang’amba ching’ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;

12 koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira.

13 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m’pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;

14 koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu;

15 ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ake pamodzi, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/AMO/1-e3e1be81b1dade46fd35afdd8b965bd2.mp3?version_id=1068—