Categories
DANIELE

DANIELE 4

Loto la Nebukadinezara la mtengo waukulu

1 Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala padziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu.

2 Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam’mwambamwamba.

3 Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.

4 Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m’nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m’chinyumba changa.

5 Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m’mtima mwanga, zinandivuta ine.

6 Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babiloni, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa lotoli.

7 Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake.

8 Koma potsiriza pake analowa pamaso panga Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m’mtima mwake; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pake, ndi kuti,

9 Belitesazara iwe, mkulu wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe chinsinsi chikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwake.

10 Masomphenya a m’mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati padziko lapansi, msinkhu wake ndi waukulu.

11 Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi.

12 Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m’menemo munali zakudya zofikira onse, nyama zakuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m’mlengalenga zinafatsa m’thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako.

13 Ndinaona m’masomphenya a m’mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba.

14 Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama zakuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake.

15 Koma siyani chitsa ndi mizu yake m’nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo; nchokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zili m’machire a m’dziko.

16 Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, ndipo zimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri.

17 Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam’mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.

18 Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a mu ufumu wanga sangathe kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.

Daniele ammasulira lotolo

19 Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.

20 Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wake, nuonekera padziko lonse lapansi,

21 umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m’menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama zakuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m’mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake;

22 ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.

23 Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m’nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo, ndipo chikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zakuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;

24 kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam’mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu:

25 kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng’ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam’mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.

26 Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukadzatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.

27 Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.

Nebukadinezara achita misala

28 Chonsechi chinagwera mfumu Nebukadinezara.

29 Itatha miyezi khumi ndi iwiri, analikuyenda m’chinyumba chachifumu cha ku Babiloni.

30 Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?

31 Akali m’kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera.

32 Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng’ombe; ndipo zidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam’mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.

33 Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumchotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng’ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame.

34 Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam’mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;

35 ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m’khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?

36 Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi chifumu changa ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akulu anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika mu ufumu wanga, Iye nandionjezeranso ukulu wochuluka.

37 Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m’kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/4-801c9d31a940364f4371daa3b895fda9.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 5

Madyerero a Belisazara, dzanja lolemba pakhoma

1 Mfumu Belisazara anakonzera anthu ake aakulu chikwi chimodzi madyerero aakulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho.

2 Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndisilivaadazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali kuYerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang’ono, amweremo.

3 Nabwera nazo zotengera zagolide adazichotsa ku Kachisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang’ono, anamweramo.

4 Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala.

5 Nthawi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, ndipo zinalemba pandunji pa choikaponyali, pomata pa khoma la chinyumba cha mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yake ya dzanja lidalembalo.

6 Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m’chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.

7 Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m’khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.

8 Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoze kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwake.

9 Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru.

10 Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m’nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;

11 pali munthu mu ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli;

12 popeza mu Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.

Daniele amasulira lemba lolembedwa pakhoma

13 Pamenepo analowa naye Daniele kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, Ndiwe kodi Daniele uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?

14 Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana.

15 Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake; koma sanakhoze kufotokozera kumasulira kwa chinthuchi.

16 Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m’khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.

17 Pamenepo anayankha Daniele, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwake.

18 Mfumu inu, Mulungu Wam’mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;

19 ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.

20 Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake;

21 ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng’ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam’mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.

22 Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetse m’mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse;

23 koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang’ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m’dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.

24 Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kuchokera pamaso pake, nililembedwa lembali.

25 Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL ndi PARSIN.

26 Kumasulira kwake kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha.

27 TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera.

28 PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.

29 Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anaveka Daniele chibakuwa, ndi unyolo wagolide m’khosi mwake, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wachitatu mu ufumumo.

30 Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa.

31 Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/5-2890c293b689d8644c8698f24a6d6f67.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 6

Akalonga amtchulira Daniele chifukwa kwa Dariusi

1 Kudamkomera Dariusi kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m’madera onse a ufumu;

2 ndi akuyang’anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Daniele; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke.

3 Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang’anira ufumu wonse.

4 Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.

5 Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola chifukwa chilichonse Daniele amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.

6 Ndipo akulu awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariusi, mukhale ndi moyo chikhalire.

7 Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango.

8 Tsopano, mfumu, mukhazikitse choletsacho, ndi kutsimikiza cholembedwacho, kuti chisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.

9 Momwemo mfumu Dariusi anatsimikiza cholembedwa ndi choletsacho.

10 Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m’nyumba mwake, m’chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza kuYerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.

11 Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Daniele alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wake.

12 Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikize choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.

13 Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Daniele uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena choletsa munachitsimikizacho; koma apempha pemphero lake katatu tsiku limodzi.

14 Ndipo mfumu m’mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.

15 Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti choletsa chilichonse ndi lemba lililonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike.

Daniele aponyedwa m’dzanja la mikango

16 Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m’dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.

17 Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi chosindikizira chake, ndi chosindikizira cha akulu ake, kuti kasasinthike kanthu ka Daniele.

18 Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m’maso mwake munamuumira.

19 Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira kudzenje la mikango.

20 Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?

21 Pamenepo Daniele anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire.

22 Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.

23 Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m’dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m’dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneke bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake.

24 Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m’dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.

25 Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu.

26 Ndilamulira ine kuti m’maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.

27 Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m’mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.

28 Momwemo Daniele amene anakuzikabe pokhala Dariusi mfumu, ndi pokhala mfumu Kirusi wa ku Persiya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/6-981d7959016bac1e1deaa649561e5716.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 7

Masomphenya a Daniele a zamoyo zinai ndi Nkhalamba ya kale lomwe

1 Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m’mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule.

2 Daniele ananena, nati, Ndinaona m’masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu.

3 Ndipo zinatuluka m’nyanja zilombo zazikulu zinai zosiyanasiyana.

4 Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, ndipo chinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, ndipo chinapatsidwa mtima wa munthu.

5 Ndipo taonani, chilombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi m’kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri.

6 Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, napatsidwa ulamuliro.

7 Pambuyo pake ndinaona m’masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.

8 Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing’ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m’nyanga m’menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu.

9 Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.

10 Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.

11 Pamenepo ndinapenyera chifukwa cha phokoso la mau aakulu idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adachipha chilombochi, ndi kuononga mtembo wake, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto.

12 Ndipo zilombo zotsalazo anazichotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi.

13 Ndinaona m’masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngatimwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake.

14 Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.

Kumasulira kwa masomphenyawo

15 Koma ine Daniele, mzimu wanga unalaswa m’kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m’mtima mwanga anandivuta.

16 Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi:

17 Zilombo zazikulu izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka padziko lapansi.

18 Koma opatulika a Wam’mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, kunthawi zonka muyaya.

19 Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake;

20 ndi za nyanga khumi zinali pamutu pake, ndi nyanga ina idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pake; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikulu, imene maonekedwe ake anaposa zinzake.

21 Ndinapenya, ndipo nyanga yomweyi inachita nkhondo ndi opatulikawo, niwagonjetsa, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe;

22 ndi mlandu unakomera opatulika a Wam’mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo.

23 Anatero, chilombo chachinai ndicho ufumu wachinai padziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya.

24 Kunena za nyanga khumi, mu ufumu uwu adzauka mafumu khumi, ndi pambuyo pao idzauka ina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzachepetsa mafumu atatu.

25 Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam’mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam’mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m’dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.

26 Koma woweruza mlandu adzakhalako, ndipo adzachotsa ulamuliro wake, kuutha ndi kuuononga kufikira chimaliziro.

27 Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam’mwambamwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera.

28 Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m’mtima mwanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/7-51d7947851b9764152935d3f83aef9cb.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 8

Masomphenya a nkhosa yamphongo ndi tonde

1 Chaka chachitatu cha Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Daniele, atatha kundionekera oyamba aja.

2 Ndipo ndinaona m’masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali mu Susa, m’nyumba ya mfumu, ndiwo m’dziko la Elamu; ndinaona m’masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.

3 Ndipo ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziwiri, ndi nyanga ziwirizo zinali za msinkhu wautali, koma imodzi inaposa inzake; yoposayo inaphuka m’mbuyo.

4 Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m’dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa.

5 Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pamaso ake.

6 Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziwiri, imene ndidaiona ilikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yake yaukali.

7 Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, nawawidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, nathyola nyanga zake ziwiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pake, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m’dzanja lake.

8 Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m’malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga.

9 Ndipo mu imodzi ya izi munaphuka nyanga yaing’ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwera, ndi kum’mawa, ndi kudziko lokometsetsa.

10 Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, ndi kuzipondereza.

11 Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa.

12 Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nkugwetsa pansi choonadi, ndi kuchita chifuniro chake, ndipo inakula.

13 Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?

14 Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama.

15 Ndipo kunali, nditaona masomphenyawo, ine Daniele ndinafuna kuwazindikira; ndipo taonani, panaima popenyana ndi ine ngati maonekedwe a munthu.

16 Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabriele, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo.

17 Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinachita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya chimaliziro.

18 Ndipo m’mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo.

19 Ndipo anati, Taona, ndidzakudziwitsa chimene chidzachitika pa chitsiriziro cha mkwiyowo; pakuti pa nthawi yoikika mpakutha pake.

20 Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziwiri ndizo mafumu a Mediya ndi Persiya.

21 Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pamaso ake ndiyo mfumu yoyamba.

22 Ndi kuti zinaphuka zinai m’malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.

23 Ndipo potsiriza pake pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi.

24 Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo.

25 Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m’dzanja mwake, nadzadzikuza m’mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja.

26 Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri.

27 Ndipo ine Daniele ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kuchita ntchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/8-e065fbdd4ddd883f70d9afb5946e9a66.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 9

Pemphero la Daniele

1 Chaka choyamba cha Dariusi mwana wa Ahasuwero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Ababiloni;

2 chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiyamneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko aYerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.

3 Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m’pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.

4 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,

5 tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu;

6 sitinamvere atumiki anu aneneri, amene ananena m’dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m’dziko.

7 Ambuye, chilungamo ncha Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala mu Yerusalemu, ndi kwa Aisraele onse okhala pafupi ndi okhala kutali, kumaiko onse kumene mudawaingira, chifukwa cha kulakwa kwao anakulakwirani nako.

8 Yehova, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani.

9 Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;

10 sitinamvere mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m’malamulo ake anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ake aneneri.

11 Inde Israele yense walakwira chilamulo chanu, ndi kupatuka, kuti asamvere mau anu; chifukwa chake temberero lathiridwa pa ife, ndi lumbiro lolembedwa m’chilamulo cha Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamchimwira.

12 Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitike monga umo panachitikira Yerusalemu.

13 Monga mulembedwa m’chilamulo cha Mose choipa ichi chonse chatidzera; koma sitinapepese Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kuchita mwanzeru m’choonadi chanu.

14 Chifukwa chake Yehova wakhala maso pa choipacho, ndi kutifikitsira icho; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu ntchito zake zonse azichita; ndipo sitinamvere mau ake.

15 Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m’dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa.

16 Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.

17 Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ake, nimuwalitse nkhope yanu pamalo anu opatulika amene ali opasuka, chifukwa cha Ambuye.

18 Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mzinda udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka.

19 Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mzinda wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.

Masabata makumi asanu ndi awiriwo, ndi Wodzozedwayo

20 Ndipo pakunena ine, ndi kupemphera, ndi kuvomereza tchimo langa, ndi tchimo la anthu a mtundu wanga Israele, ndi kutula chipembedzero changa pamaso pa Yehova Mulungu wanga, chifukwa cha phiri lopatulika la Mulungu wanga;

21 inde pakunena ine m’kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m’masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.

22 Ndipo anandilangiza ine, ndi kulankhula nane, nati, Daniele iwe, ndatuluka tsopano ine kukuzindikiritsa mwaluntha.

23 Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linatuluka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.

24 Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.

25 Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.

26 Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.

27 Ndipo iye adzapanganachipanganocholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/9-236a26c0a0740568f02ebe570c60a565.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 10

Daniele aona masomphenya oopsa, mngelo amlimbikitsa

1 Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.

2 Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu.

3 Chakudya chofunika osachidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu.

4 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m’mphepete mwa mtsinje waukulu, ndiwo Tigrisi,

5 ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m’chuuno ndi golide woona wa ku Ufazi;

6 thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji.

7 Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala.

8 Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya aakuluwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi chimphamvu ine.

9 Ndipo ndinamva kunena kwa mau ake, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ake ndinagwidwa ndi tulo tatikulu pankhope panga, nkhope yanga pansi.

10 Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.

11 Nati kwa ine, Daniele, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndilikunena ndi iwe, nukhale chilili; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera.

12 Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako.

13 Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya.

14 Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m’tsogolo.

15 Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala duu.

16 Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, chifukwa cha masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndilibenso mphamvu.

17 Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? Pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.

Nkhondo ya pakati pa Persiya ndi Grisi

18 Pamenepo anandikhudzanso wina, maonekedwe ake ngati munthu, nandilimbikitsa ine.

19 Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa.

20 Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki.

21 Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaele kalonga wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/10-34ad840c4677fa3e7f4ab846b2212453.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 11

1 Ndipo ine, chaka choyamba cha Dariusi Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa.

2 Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu mu Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.

3 Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzachita ufumu ndi ulamuliro waukulu, nidzachita monga mwa chifuniro chake.

4 Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m’mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.

Nkhondo ya pakati pa mfumu ya kumpoto ndi ya kumwera

5 Ndipo mfumu ya kumwera, ndiye wina wa akalonga ake, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wake ndi ulamuliro waukulu.

6 Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.

7 Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m’malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m’linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawagonjetsa;

8 ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika zasilivandi golide adzazitenga kunka nazo ndende ku Ejipito; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto.

9 Ndipo adzalowa mu ufumu wa mfumu ya kumwera, koma adzabwera m’dziko lakelake.

10 Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo aakulu ochuluka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake.

11 Ndi mfumu ya kumwera idzawawidwa mtima, nidzatuluka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukulu; koma unyinjiwo udzaperekedwa m’dzanja lake.

12 Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzapambana.

13 Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pachimaliziro cha nthawi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri.

14 Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwera, ndi achiwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.

15 Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda mizinda yamalinga; ndi ankhondo a kumwera sadzalimbika, ngakhale anthu ake osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika.

16 Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzachita chifuniro chake cha iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pake; ndipo adzaima m’dziko lokometsetsalo, ndi m’dzanja mwake mudzakhala chionongeko.

17 Ndipo adzalimbitsa nkhope yake, kudza ndi mphamvu ya ufumu wake wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzachita chifuniro chake, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kuvomerezana naye.

18 Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake.

19 Pamenepo adzatembenuzira nkhope yake kumalinga a dziko lakelake; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso.

20 Ndipo m’malo mwake adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku owerengeka adzathyoledwa iye, si mwamkwiyo, kapena kunkhondo ai.

21 Ndi m’malo mwake adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatse ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.

22 Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano.

23 Ndipo atapangana naye adzachita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka.

24 Adzafika kachetechete kuminda yokometsetsa ya derali, nadzachita chosachita atate ake, kapena makolo ake; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi chuma, nadzalingiririra malinga ziwembu zake; adzatero nthawi.

25 Nadzautsa mphamvu yake ndi mtima wake ayambane ndi mfumu ya kumwera ndi khamu lalikulu la nkhondo; ndi mfumu ya kumwera idzachita nkhondo ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.

26 Inde iwo akudyako chakudya chake adzamuononga; ndi ankhondo ake adzasefukira, nadzagwa ambiri ophedwa.

27 Ndipo mafumu awa onse awiri mitima yao idzakumbuka kuchita zoipa, nadzanena bodza ali pa gome limodzi; koma osapindula nalo; pakuti kutha kwake kudzakhala pa nthawi yoikika.

28 Ndipo adzabwerera kudziko lake ndi chuma chambiri; ndi mtima wake udzatsutsana ndichipanganochopatulika, nadzachita chifuniro chake, ndi kubwerera kudziko lake.

29 Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwera; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.

30 Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; chifukwa chake adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake; adzabweranso, nadzasamalira otaya chipangano chopatulika.

31 Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho.

32 Ndipo akuchitira choipa chipanganocho iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu.

33 Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.

34 Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling’ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.

35 Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya chitsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika.

36 Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m’mtimacho chidzachitika.

37 Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena chokhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.

38 Koma kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziwe, adzaulemekeza ndi golide, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.

39 Ndipo adzachita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wachilendo; aliyense womvomereza adzamchulukitsira ulemu, nadzawachititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wake.

40 Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m’maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.

41 Adzalowanso m’dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

42 Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Ejipito lomwe silidzapulumuka.

43 Ndipo adzachita mwamphamvu ndi chuma cha golide, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Ejipito; Libiya ndi Akusi adzatsata mapazi ake.

44 Koma mbiri yochokera kum’mawa ndi kumpoto idzamvuta; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuononga konse ambiri.

45 Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira chimaliziro chake wopanda wina wakumthandiza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/11-e88b18815ad3fadf9a5d29e135b6b547.mp3?version_id=1068—

Categories
DANIELE

DANIELE 12

Nthawi ya chimaliziro, mau otsekedwa

1 Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m’buku.

2 Ndipo ambiri a iwo ogona m’fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.

3 Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.

4 Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.

5 Pamenepo ine Daniele ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m’mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m’mphepete mwa mtsinje tsidya lija.

6 Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?

7 Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.

8 Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?

9 Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro.

10 Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.

11 Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, ndipo chidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

12 Wodala iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.

13 Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/12-843acd5848983070b6ca8d2f6993b101.mp3?version_id=1068—

Categories
HOSEYA

HOSEYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneri Hoseya adalalikira pambuyo pa mneneri Amosi, ku Israele, ufumu wakumpoto, mzinda wa Samariya usanapasuke. Iye amamva chisoni poona kuti Aisraelewo ngosakhulupirika ndi opembedza milungu ina. Tsono anayerekeza kusakhulupirika kwaoko ndi zimene mwiniwakeyo adazipeza m’banja lake, mkazi wake atamchokera nkutsata amuna ena. Chonchonso anthu a Mulunguwo anafulatira Yehova Mbuye wao natsata milungu ina. Mulungu sadzalephera kuwalanga chifukwa cha kusakhulupirika kwaoko; komabe potsiriza, chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, adzawakokeranso kwa Iye ndipo adzayanjana nawonso. Atsimikiza chikondi chakecho ndi mauwa, “Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele…Mtima wanga watembenuka m’kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi” (11.8).

Za mkatimu

Ukwati wa Hoseya ndi banja lake

1.1—3.5

Mau a Yehova odzudzula Israele

4.1—13.16

Uthenga wa kulapa ndinso lonjezo la kukonzedwanso kwa zinthu

14.1-9