Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 33

Udindo wa mneneri

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Nena ndi ana a anthu a mtundu wako, uziti nao, Ndikafikitsira dziko lililonse lupanga, nakatenga eni dziko munthu wa pakati pao, nakamuika awadikirire,

3 nakaona iye lupanga lilikudzera dziko, nakaomba lipenga ndi kuchenjeza anthu;

4 ndipo wina, kumva adamva mau a lipenga, koma osalabadira, likadza lupanga, nilimchotsa, wadziphetsa ndi mtima wake.

5 Anamva mau a lipenga, osawalabadira, wadziphetsa ndi mtima wake; akadalabadira, akadalanditsa moyo wake.

6 Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osachenjeza anthu, nilidza lupanga, nilichotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m’mphulupulu zake, koma mwazi wake ndidzaufunsa padzanja la mlonda.

7 Iwe tsono, wobadwa ndi munthu, ndakuika mlonda wa nyumba ya Israele, m’mwemo imva mau a pakamwa panga, nundichenjezere iwo.

8 Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumchenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m’mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa padzanja lako.

9 Koma ukachenjeza woipa za njira yake, aileke; koma iye osaileka njira yake, adzafa m’mphulupulu mwake iye, koma iwe walanditsa moyo wako.

10 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israele, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zochimwa zathu zitikhalira, ndipo tichita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji?

11 Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?

12 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu a mtundu wako, Cholungama cha wolungama sichidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwake, ndi kunena za choipa cha woipa, sadzagwa nacho tsiku lakubwerera iye kuleka choipa chake; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi chilungamo chake tsiku lakuchimwa iye.

13 Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama chilungamo chake, akachita chosalungama, sizikumbukika zolungama zake zilizonse; koma m’chosalungama chake anachichita momwemo adzafa.

14 Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka tchimo lake, nakachita choyenera ndi cholungama;

15 woipayo akabweza chikole, nakabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m’malemba a moyo wosachita chosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

16 Zoipa zake zilizonse anazichita sizidzakumbukika zimtsutse, anachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo ndithu.

17 Koma ana a anthu a mtundu wako akuti, Njira ya Ambuye siiyenera; koma iwowa njira yao siiyenera.

18 Akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, nakachita chosalungama, adzafa m’mwemo.

19 Ndipo woipa akabwerera kuleka choipa chake, nakachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo nazo.

20 Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israele inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zake.

Kulangidwa kwa Aisraele chifukwa cha zoipa zao

21 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri cha undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lachisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka kuYerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mzinda.

22 Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m’mawa, m’mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.

23 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

24 Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala kumabwinja a dziko la Israele anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko cholowa chake; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife cholowa chathu.

25 Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?

26 Mumatama lupanga lanu, mumachita chonyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wake; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?

27 Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m’malinga ndi m’mapanga adzafa ndi mliri.

28 Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu.

29 Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, posanduliza Ine dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, chifukwa cha zonyansa zao zonse anazichita.

30 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe kumakoma ndi kumakomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wake, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova.

31 Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.

32 Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawachita.

33 Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziwa kuti panalimneneripakati pao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/33-9f70beffcbecb4375d2833c5b355eea6.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 34

Aneneratu motsutsa abusa osakhulupirika a anthu a Mulungu

1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?

3 Mukudya mafuta, muvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa.

4 Zofooka simunazilimbitse; yodwala simunaichiritse, yothyoka simunailukire chika, yopirikitsidwa simunaibweze, yotayika simunaifune; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.

5 M’mwemo zinamwazika posowa mbusa, ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zilizonse zakuthengo, popeza zinamwazika.

6 Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.

7 Chifukwa chake abusa inu, imvani mau a Yehova:

8 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunefune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;

9 chifukwa chake, abusa inu, imvani mau a Yehova:

10 Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga padzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.

11 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.

12 Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m’malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.

13 Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m’maiko, ndi kulowa nazo m’dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m’dziko.

14 Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri aatali a Israele padzakhala kholo lao, apo adzagona m’khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsera pa mapiri a Israele.

15 Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova.

16 Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.

17 Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.

18 Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?

19 Ndi nkhosa zanga zidye kodi zoponderezeka ndi mapazi anu, ndi kumwa zovunduliridwa ndi mapazi anu?

20 Chifukwa chake atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda.

21 Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,

22 chifukwa chake ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.

23 Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.

24 Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.

25 Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m’dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m’chipululu, ndi kugona kunkhalango.

26 Pakuti ndidzaika izi ndi midzi yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m’nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.

27 Ndi mitengo yakuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m’manja mwa iwo akuwatumikiritsa.

28 Ndipo sadzakhalanso chakudya chaamitundu, ndi chilombo chakuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.

29 Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m’dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.

30 Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.

31 Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/34-94f4aa5fb41523cccc67caa521ae4650.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 35

Aneneratu za kulangidwa kwa a kuphiri la Seiri

1 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kuphiri la Seiri, nulinenere molitsutsa;

3 nuti nalo, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndiipidwa nawe phiri la Seiri, ndipo ndidzakutambasulira dzanja langa, ndi kukusanduliza lachipululu ndi lodabwitsa.

4 Ndidzapasula mizinda yako, nudzakhala lachipululu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

5 Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israele kumphamvu ya lupanga m’nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza;

6 chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndikukonzeratu uphedwe, ndi mwazi udzakulondola; popeza sunadane nao mwazi, mwazi udzakulondola.

7 Ndipo ndidzaika phiri la Seiri lodabwitsa ndi lachipululu, ndi kuononga pomwepo wopitapo ndi wobwerapo.

8 Ndipo ndidzadzaza mapiri ake ndi ophedwa ake pa zitunda zako, ndi m’zigwa zako, ndi m’mitsinje mwako monse; adzagwa ophedwa ndi lupanga.

9 Ndidzakusandutsa mabwinja osatha; ndi m’mizinda mwako simudzakhalanso anthu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

10 Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko;

11 chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndidzachita monga mwa mkwiyo wako, ndi monga mwa nsanje yako unachita nayo pa kukwiya nao iwe; ndipo ndidzadziwika nao pamene ndikuweruza.

12 Ndipo udzadziwa kuti Ine Yehova ndidamva zamwano zako zonse udazinena pa mapiri a Israele, ndi kuti, Apasuka, apatsidwa kwa ife tiwadye.

13 Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundichulukitsira mau anu ndawamva Ine.

14 Atero Ambuye Yehova, Pokondwerera dziko lonse ndidzakusanduliza lachipululu.

15 Monga momwe unakondwerera cholowa cha nyumba ya Israele, popeza chidapasuka, momwemo ndidzakuchitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/35-c078e1a6e3fed80ae2fdeec17b6b3a0a.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 36

Aneneratu za mapiri a Israele

1 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israele, uziti, Mapiri a Israele inu, imvani mau a Yehova.

2 Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Ha! Ingakhale misanje yakale ili yathu, cholowa chathu;

3 chifukwa chake unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Chifukwa, inde chifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale cholowa chaamitunduotsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;

4 chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi mizinda yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira;

5 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu yense, amene anadzipatsira dziko langa likhale cholowa chao ndi chimwemwe cha mtima wonse, ndi mtima wopeputsa, kuti alande zake zonse zikhale zofunkha.

6 Chifukwa chake unenere za dziko la Israele, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;

7 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao.

8 Koma inu, mapiri a Israele, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israele zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika.

9 Pakuti taonani, Ine ndikhalira nanu kumodzi, ndipo ndidzakutembenukirani; ndipo mudzabzalidwa ndi kupaliridwa,

10 ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu nyumba yonse ya Israele, yonseyi, ndi m’mizindamo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa mizinda.

11 Ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzachuluka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzachitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

12 Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israele; adzakhala nawe dziko laolao, ndipo udzakhala cholowa chao osafetsanso ana ao.

13 Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;

14 chifukwa chake sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso a mtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.

15 Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzasenzanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.

Za kukonzekanso kwa Israele

16 Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,

17 Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israele anakhala m’dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi machitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga chidetso cha mkazi amene akusamba.

18 M’mwemo ndinawatsanulira ukali wanga, chifukwa cha mwazi anautsanulira padziko, ndi chifukwa cha mafano analidetsa nalo dziko;

19 ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m’maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa machitidwe ao ndinawaweruza.

20 Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, natuluka m’dziko mwake.

21 Koma ndinawaleka chifukwa cha dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israele adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adankako.

22 Chifukwa chake nena kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Sindichichita ichi chifukwa cha inu, nyumba ya Israele, koma chifukwa cha dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.

23 Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikulu kuti lili loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.

24 Pakuti ndidzakutengani kukutulutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m’maiko onse, ndi kubwera nanu m’dziko lanu.

25 Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.

26 Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m’kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m’thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.

27 Ndipo ndidzaika mzimu wanga m’kati mwanu, ndi kukuyendetsani m’malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.

28 Ndipo mudzakhala m’dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

29 Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala.

30 Ndipo ndidzachulukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m’munda, kuti musalandirenso chitonzo cha njala mwa amitundu.

31 Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.

32 Dziwani kuti sindichita ichi chifukwa cha inu, ati Ambuye Yehova; chitani manyazi, dodomani, chifukwa cha njira zanu, nyumba ya Israele inu.

33 Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukuchotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m’mizindamo; ndi pamabwinja padzamangidwa.

34 Ndi dziko lachipululu lidzalimidwa, chinkana linali lachipululu pamaso pa onse opitako.

35 Ndipo adzati, Dziko ili lachipululu lasanduka ngati munda wa Edeni ndi mizinda yamabwinja, ndi yachipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m’mwemo.

36 Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali chipululu; Ine Yehova ndanena ndidzachita.

37 Atero Ambuye Yehova, Ichi chomwe adzandipempha a nyumba ya Israele ndiwachitire ichi, ndidzawachulukitsira anthu ngati nkhosa.

38 Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za kuYerusalemupa zikondwerero zake zoikika, momwemo mizinda yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/36-7985bfadcc97b0fed2f108aba39fd9b5.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 37

Masomphenya a mafupa

1 Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anatuluka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m’kati mwa chigwa, ndicho chodzala ndi mafupa;

2 ndipo anandipititsa pamenepo pozungulira ponse, ndipo taonani, anali aunyinji pachigwa pansi, ndipo anaumitsitsa.

3 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu.

4 Pamenepo anati kwa ine, Nenera kwa mafupa awa, nuti nao, Mafupa ouma inu, imvani mau a Yehova.

5 Atero Ambuye Yehova kwa mafupa awa, Taonani, ndidzalonga mpweya mwa inu, ndipo mudzakhala ndi moyo.

6 Ndipo ndidzakuikirani mtsempha, ndi kufikitsira inu mnofu, ndi kukuta inu ndi khungu, ndi kulonga mpweya mwa inu; ndipo mudzakhala ndi moyo; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7 M’mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobedegobede, ndi mafupa anasendererana, fupa kutsata fupa linzake.

8 Ndipo ndinapenya, taonani, panali mitsempha pa iwo, panadzaponso mnofu, ndi khungu linawakuta pamwamba pake; koma munalibe mpweya mwa iwo.

9 Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.

10 M’mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira chilili, gulu la nkhondo lalikulukulu ndithu.

11 Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa.

12 Chifukwa chake, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu mutuluke m’manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m’dziko la Israele.

13 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova potsegula Ine kumanda kwanu, ndi kukweza inu kukutulutsani m’manda mwanu, anthu anga inu.

14 Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m’dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kuchichita, ati Yehova.

15 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

16 Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israele anzake; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efuremu, ndi wa nyumba yonse ya Israele anzake;

17 nuiphatikize wina ndi unzake ikhale mtengo umodzi m’dzanja lako.

18 Ndipo ana a anthu a mtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi?

19 Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m’dzanja la Efuremu, ndi wa mafuko a Israele anzake, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m’dzanja langa.

20 Ndipo mitengo imene ulembapo idzakhala m’dzanja mwako pamaso pao.

21 Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati paamitundukumene adankako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m’dziko mwao;

22 ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m’dzikomo, pa mapiri a Israele; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.

23 Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao zilizonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m’mene anachimwamo, ndi kuwayeretsa; m’mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.

24 Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m’maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwachita.

25 Ndipo adzakhala m’dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m’mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.

26 Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.

27 Kachisi wanganso adzakhala nao, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

28 Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/37-fd5f501cb844bf13fed39107e5bdec0d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 38

Aneneratu za kulangidwa kwa Gogi

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwaGogi, wa kudziko la Magogi, ndiye mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala; nunenere motsutsana naye,

3 uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala;

4 ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m’chibwano mwako ndi zokowera, ndi kukutulutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo ovala mokwanira onsewo, msonkhano waukulu ndi zikopa zotchinjiriza, onsewo ogwira bwino malupanga;

5 Persiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi chikopa ndi chisoti chachitsulo;

6 Gomeri ndi magulu ake onse, nyumba ya Togarima, ku malekezero a kumpoto, ndi magulu ake onse, mitundu yambiri pamodzi ndi iwe.

7 Ukonzekeretu, inde udzikonzeretu, iwe ndi msonkhano wako wonse unakusonkhanira, nukhale iwe mtsogoleri wao.

8 Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m’dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituluke m’mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israele, amene adakhala achipululu chikhalire; koma litulutsidwa m’mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.

9 Ndipo udzakwera udzadza ngati mkuntho, udzanga mtambo kuphimba dziko, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.

10 Atero Ambuye Yehova, Kudzachitika tsiku ilo kuti m’mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira chiwembu choipa,

11 nudzati, Ndidzakwera kunka kudziko la midzi yopanda malinga, ndidzanka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mapiringidzo, kapena zitseko;

12 kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwaamitundu, odzionera zoweta ndi chuma, okhala pakati padziko.

13 Sheba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisisi, ndi misona yake yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? Wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kuchoka nazosilivandi golide, kuchoka nazo zoweta ndi chuma, kulanda zankhondo zambiri?

14 Chifukwa chake nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israele, sudzachidziwa kodi?

15 Ndipo udzatuluka m’malo mwako m’malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukulu ndi nkhondo yaikulu;

16 ndipo udzakwerera anthu anga Israele ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzachitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.

17 Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israele, akunenera masiku aja za zaka za m’tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?

18 Ndipo kudzachitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israele, ati Ambuye Yehova, ukali wanga udzakwera m’mphuno mwanga.

19 Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m’moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m’dziko la Israele;

20 motero kuti nsomba za m’nyanja, ndi mbalame za m’mlengalenga, ndi nyama zakuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi.

21 Ndipo ndidzamuitanira lupanga kumapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu aliyense lupanga lake lidzaombana nalo la mbale wake.

22 Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mvumbi waukulu, ndi matalala aakulu, moto ndi sulufure.

23 Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/38-0a97333a7e67014a8a5ca3354643c0b4.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 39

1 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana nayeGogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala;

2 ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe uchoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe kumapiri a Israele;

3 ndipo ndidzakantha uta wako kuuchotsa m’dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mivi yako kudzanja lako lamanja.

4 Udzagwa pa mapiri a Israele, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zilombo zakuthengo, akuyese chakudya.

5 Udzagwa kuthengo, koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.

6 Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m’zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7 Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israele, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipoamitunduadzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israele.

8 Taonani, chikudza, chidzachitika, ati Ambuye Yehova, ndilo tsiku ndanenalo.

9 Ndipo iwo okhala m’mizinda ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;

10 osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.

11 Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda mu Israele, chigwa cha opitawo kum’mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wake wonse, nadzachitcha, Chigwa cha unyinji wa Gogi.

12 Ndi a nyumba ya Israele adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.

13 Inde anthu onse a m’dziko adzawaika, nadzamveka nako tsiku lakulemekezedwa Ine, ati Ambuye Yehova.

14 Ndipo adzasankha anthu akupitapitabe m’dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.

15 Ndipo opitapitawo adzapitapita m’dziko, ndipo wina akaona fupa la munthu aikepo chizindikiro, mpaka oikawo aliika m’chigwa cha unyinji wa Gogi.

16 Ndipo dzina la mzinda lidzakhala Hamona. Momwemo adzayeretsa dziko.

17 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse zakuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani kumbali zonse, kudza kunsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikulu pa mapiri a Israele, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.

18 Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa anaankhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng’ombe, zonsezi zonenepa za ku Basani.

19 Ndipo mudzadya zonona mpaka mudzakhuta, ndi kumwa mwazi mpaka mudzaledzera za nsembe yanga ndakupherani.

20 Ndipo podyera panga mudzakhuta akavalo, ndi magaleta, ndi anthu amphamvu, ndi anthu onse a nkhondo, ati Ambuye Yehova.

21 Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona chiweruzo changa ndachichita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira.

22 Ndipo nyumba ya Israele idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m’tsogolomo.

23 Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israele idalowa undende chifukwa cha mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m’mwemo ndinawapereka m’dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.

24 Ndinachita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.

25 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kuchitira chifundo nyumba yonse ya Israele, ndipo ndidzachitira dzina langa loyera nsanje.

26 Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m’dziko lao, opanda wina wakuwaopsa;

27 nditabwera nao kuchoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m’maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri.

28 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kunka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m’dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.

29 Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israele, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/39-bb7b478a0cd292a008dd3d6a44ba88e7.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 40

Masomphenya a Ezekiele, kukonzekanso kwa Kachisi ndi mabwalo ake

1 Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mzindawo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.

2 M’masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m’dziko la Israele, nandikhalitsa paphiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mzinda kumwera.

3 Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m’dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye.

4 Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m’makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israele zonse uziona.

5 Ndipo taonani, panali linga kunja kwake kwa nyumba ya Kachisi poizinga, ndi m’dzanja lake la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uliwonse mkono kudza chikhato; ndipo anayesa chimangidwecho kuchindikira kwake bango limodzi, ndi msinkhu wake bango limodzi.

6 Pamenepo anafika kuchipata choloza kum’mawa, nakwera pa makwerero ake; ndipo anayesa chiundo cha chipata, bango limodzi kuchindikira kwake; ndicho chiundo choyamba, bango limodzi.

7 Ndi chipinda cha alonda, chonse ncha bango limodzi m’litali mwake, ndi bango limodzi kupingasa kwake, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi chiundo cha chipata kumbali ya kukhonde la kuchipata m’katimo, bango limodzi.

8 Anayesanso khonde la kuchipata kumbali ya ku Kachisi, bango limodzi. Pamenepo anayesa khonde la kuchipata mikono isanu ndi itatu,

9 ndi mphuthu zake mikono iwiri; ndi khonde la kuchipata linaloza ku Kachisi.

10 Ndi zipinda za alonda za kuchipata cha kum’mawa ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, chakuno ndi chauko.

11 Ndipo anayesa kupingasa kwa chipata pakhoma pake mikono khumi, ndi utali wake wa chipata mikono khumi ndi itatu;

12 ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi chakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi chauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko.

13 Ndipo anayesa chipata kuyambira kutsindwi la chipinda cha alonda chimodzi, kufikira kutsindwi la chinzake, kupingasa kwake ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.

14 Anamanganso nsanamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa chipata lidafikira kunsanamira.

15 Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la chipata kufikira khomo la khonde la chipata m’katimo ndiko mikono makumi asanu.

16 Ndipo panali mazenera amkati okhazikika pazipinda ndi m’makoma a pakati pao, m’kati mwa chipata pozungulira ponse; momwemonso pamphuthu; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m’katimo, ndi pa nsanamirazo panali akanjedza.

17 Pamenepo analowa nane kubwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.

18 Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wake wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi.

19 Pamenepo anayesa kupingasa kwake kuyambira pakhomo pake pachipata chakunsi, kufikira kumaso kwake kwa bwalo la m’kati kunja kwake, mikono zana kum’mawa, ndi kumpoto.

20 Ndi chipata cha bwalo lakunja choloza kumpoto anachiyesa m’litali mwake, ndi kupingasa kwake zonse mikono zana.

21 Ndi zipinda zake ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, ndi makoma a pakati pake; ndi mphuthu zake zinali monga mwa muyeso wa chipata choyambacho, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

22 Ndi mazenera ake, ndi mphuthu zake, ndi akanjedza ake, anali monga mwa muyeso wa chipata choloza kum’mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi mphuthu zake zinali pakhomo.

23 Ndipo panali chipata cha bwalo lam’kati, chopenyana ndi chipata chinzake chakunja kumpoto, ndi cha kum’mawa; ndipo anayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata mikono zana.

24 Ndipo ananditsogolera kunka kumwera, ndipo taonani, panali chipata kumwera, nayesa makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake, monga mwa miyeso yomweyi.

25 Ndimo munali mazenera m’menemo, ndi m’mphuthu zake pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

26 Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi mphuthu zake kumaso kwake; ndi pa nsanamira zake chakuno ndi chauko panali akanjedza.

27 Ndipo panali chipata cha bwalo lam’kati chakuloza kumwera, nayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata kumwera mikono zana.

28 Pamenepo analowa nane pa chipata cha kumwera m’bwalo lam’kati, nayesa chipata cha kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;

29 ndi zipinda zake, ndi makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m’menemo, ndi m’mphuthu zake pozungulirapo; m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

30 Ndipo panali mphuthu pozungulirapo, m’litali mwake mikono makumi awiri mphambu isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu.

31 Ndi mphuthu zake zinaloza kubwalo lakunja, ndi pa nsanamira zake panali akanjedza, ndi pokwererapo panali makwerero asanu ndi atatu.

32 Ndipo analowa ndine m’bwalo lam’kati kuloza kum’mawa, nayesa chipata cha kum’mawa monga mwa miyeso yomweyi;

33 ndi zipinda zake, ndi makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m’menemo, ndi m’mphuthu zake pozungulirapo, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

34 Ndi mphuthu zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu.

35 Pamenepo anabwera nane kuchipata cha kumpoto, nachiyesa monga mwa miyeso yomweyi;

36 zipinda zake, makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake; ndimo munali mazenera m’menemo pozungulirapo, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

37 Ndi nsanamira zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu.

38 Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi chitseko chake; pamenepo anatsuka nsembe yopsereza.

39 Ndipo m’khonde la pachipata munali magome awiri chakuno, ndi magome awiri chauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula.

40 Ndi kumbali ina ya khonde kunja, pakukwerera polowera pa chipata cha kumpoto, kunali magome awiri, ndi kumbali inzake ya kuchipata kunali magome awiri.

41 Magome anai chakuno, ndi magome anai chauko, kumbali ya chipata; magome asanu ndi atatu, amene anapherapo nsembe.

42 Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m’litali mwake mkono ndi nusu, kupingasa kwake mkono ndi nusu, msinkhu wake mkono umodzi; pamenepo ankaika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera.

43 Ndi zichiri zangowe, chikhato m’litali mwake, zinamangika m’katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe.

44 Ndi kunja kwa chipata cha m’kati kunali tinyumba ta oimba m’bwalo lam’kati, kumbali ya chipata cha kumpoto; ndipo tinaloza kumwera, kena kumbali ya chipata cha kum’mawa kanaloza kumpoto.

45 Ndipo anati kwa ine, Kanyumba aka koloza kumwera nka ansembe odikira Kachisi.

46 Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye.

47 Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m’litali mwake, ndi mikono zana kupingasa kwake, laphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.

48 Pamenepo anadza nane kukhonde la Kachisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; ndi kupingasa kwa chipata, mikono itatu chakuno, ndi mikono itatu chauko.

49 M’litali mwake mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi chakuno, ndi imodzi chauko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/40-8aec0ea6c80347fc88f71918f3079199.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 41

Kukonzekanso kwa Kachisi: malo opatulika kwambiri

1 Ndipo anadza nane ku Kachisi, nayesa nsanamira zake, kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko, ndiko kupingasa kwa chihema chija.

2 Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; nayesa malo opatulika, m’litali mwake mikono makumi anai, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.

3 Nalowa m’katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri.

4 Anayesanso m’kati mwa Kachisi m’tsogolomo, m’litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m’mopatulika kwambiri.

5 Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kuchindikira kwake mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwake kwa zipinda za m’mphepete mikono inai, pozungulira pake ponse pa Kachisi.

6 Ndipo zipinda za m’mphepete zinasanjikizana china pa chinzake; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, ndipo zinalowa kukhoma lochirikiza zipinda za m’mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwe ndi khoma la nyumba.

7 Ndipo zipinda za m’mphepete zinakula m’kupingasa kwao, pozinga nyumba m’kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pake pa nyumba; motero kupingasa kwake kwa nyumba kunakula kumwamba kwake, momwemonso anakwera kuyambira chipinda chakunsi, kupita chapakati, kufikira cham’mwamba.

8 Ndinaonanso kuti kunyumba kunali chiunda pozungulira pake; maziko a zipinda za m’mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikulu.

9 Kuchindikira kwa khoma la kuzipinda za m’mphepete kunja kwake kunali mikono isanu; ndipo mpata wake unali malo olowera m’zipinda za m’mphepete za Kachisi.

10 Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pake ponse pa nyumba.

11 Ndi makomo a zipinda za m’mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwera; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwake pozungulira pake.

12 Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwake; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pake linali la mikono isanu kuchindikira kwake; ndi m’litali mwake mikono makumi asanu ndi anai.

13 Momwemo anayesa Kachisi m’litali mwake mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ake, mikono zana limodzi;

14 kupingasa kwake komwe kwa kukhomo kwa nyumba, ndi kumpatawo kum’mawa, mikono zana limodzi.

15 Momwemo anayesa m’litali mwake nyumbayo inali kutsogolo kwake kwa mpata wokhala chakuno chake, ndi makonde ake am’mwamba, chakuno ndi chauko, mikono zana limodzi, ndi Kachisi wa m’katimo, ndi makonde a kubwalo;

16 ziundo, ndi mazenera amkati okhazikika, ndi makonde am’mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa chiundo, otchinga ndi matabwa pozungulira pake, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;

17 kufikira kumwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m’katimo, ndi kunja kwake, ndi khoma lonse kwete m’kati ndi kunja, monga mwa miyeso.

18 Ndipo panalembedwapo ndiakerubindi akanjedza, kanjedza pakati pa akerubi; ndi kerubi aliyense anali ndi nkhope zake ziwiri;

19 nkhope ya munthu kuloza kukanjedza chakuno, ndi nkhope ya mwanawamkango kuloza kukanjedza chauko, momwemo m’nyumba monse pozungulira pake.

20 Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kachisi.

21 Mphuthu za Kachisi zinali zaphwamphwa, ndi maonekedwe a pakhomo pa malo opatulika ananga maonekedwe a Kachisi.

22 Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m’litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.

23 Ndipo Kachisi ndi malo opatulika kwambiri anali nazo zitseko ziwiri.

24 Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, china chopatukana pa khomo lina china pa linzake.

25 Ndipo panalembedwa pamenepo pa zitseko za Kachisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakoma; ndipo panali matabwa ochindikira pakhomo pakhonde panja.

26 Ndipo panali mazenera amkati okhazikika, ndi akanjedza chakuno ndi chauko, kumbali zake za khonde; momwemonso pa zipinda za m’mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ochindikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/41-4de6676b8abb8d904adf0a2941a37301.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 42

Kukonzekanso kwa Kachisi: zipinda zopatulika

1 Pamenepo anatuluka nane kunka kubwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane kunyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.

2 Chakuno cha m’litali mwake mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwake mikono makumi asanu.

3 Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam’kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam’mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri.

4 Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwake mikono khumi m’kati mwake, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto.

5 Ndipo zipinda zapamwamba zinachepa, pakuti makonde am’mwamba analanda pamenepo, chifukwa chake zinachepa koposa zapansi ndi zapakati m’nyumba yazipinda.

6 Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; chifukwa chake zam’mwambazo zinachepa koposa zakunsi ndi pakati kuyambira pansi.

7 Ndipo linga linali kunjalo, lolingana ndi nyumba yazipinda, kuloza kubwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m’litali mwake munali mikono makumi asanu.

8 Pakuti kupingasa kwake kwa nyumba yazipinda inali m’bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza kukhomo la Kachisi inali mikono zana limodzi.

9 Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum’mawa, poloweramo kuchoka kubwalo lakunja.

10 M’kuchindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, chakuno cha mpatawo, chakuno cha nyumba, panali nyumba yazipinda.

11 Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe njira ya kunyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m’litali mwake, momwemonso kupingasa kwake; ndi m’matulukiro mwake monse munali monga mwa machitidwe a inzake, ndi monga mwa makomo a inzake.

12 Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwera panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum’mawa polowamo.

13 Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.

14 Atalowa ansembe asatulukenso m’malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.

15 Atatha tsono kuyesa nyumba ya m’katimo, anatuluka nane njira ya chipata choloza kum’mawa nayesa bwalo pozungulira pake.

16 Anayesa mbali ya kum’mawa, ndi bango loyesera, mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.

17 Anayesa mbali ya kumpoto mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.

18 Anayesa mbali ya kumwera mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.

19 Anatembenukira kumbali ya kumadzulo, nayesa mikono mazana asanu ndi bango loyesera.

20 Analiyesa mbali zake zinai, linali nalo linga pozungulira pake, utali wake mikono mazana asanu, chitando chake mikono mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/42-233009028c0d1a808737e99e171f8ed2.mp3?version_id=1068—