Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 23

Ohola ndi Oholiba achigololowo

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, panali akazi awiri, mai wao ndi mmodzi;

3 ndipo anachita chigololo iwo mu Ejipito, anachita chigololo mu ubwana wao; pomwepo anthu anasindikiza mawere ao, pomweponso anakhudza nsonga za mawere za unamwali wao.

4 Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkulu, ndi Oholiba mng’ono wake; nakhala anga, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndiYerusalemundiye Oholiba.

5 Koma Ohola anachita chigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ake Aasiriya oyandikizana naye;

6 ovala chibakuwa, ziwanga, ndi akazembe, onsewo anyamata ofunika, anthu oyenda pa akavalo.

7 Ndipo anachita nao zigololo zake, ndiwo anthu osankhika a ku Asiriya onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.

8 Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye mu unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao.

9 Chifukwa chake ndampereka m’dzanja la mabwenzi ake, m’dzanja la Aasiriya amene anawaumirira.

10 Iwowa anavula umaliseche wake, anatenga ana ake aamuna ndi aakazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lake linamveka mwa akazi atamchitira maweruzo.

11 Pamene mng’ono wake Oholiba anachiona, anavunda ndi kuumirira kwake koposa iyeyo; ndi zigololo zake zidaposa zigololo za mkulu wake.

12 Anaumirira Aasiriya, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, ovala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika.

13 Ndipo ndinamuona kuti anadetsedwa, onse awiri adatenga njira yomweyi.

14 Ndipo anaonjeza zigololo zake, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Ababiloni olembedwa ndi kundwe;

15 omangira malamba m’chuuno mwao, ndi nduwira zazikulu zonyika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babiloni, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.

16 Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga kudziko la Ababiloni.

17 Namdzera a ku Babiloni ku kama wa chikondi, namdetsa ndi chigololo chao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wake unafukidwa nao.

18 M’mwemo iye anawulula chigololo chake, navula umaliseche wake; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkulu wake.

19 Koma anachulukitsa zigololo zake, nakumbukira masiku a ubwana wake, muja anachita chigololo m’dziko la Ejipito.

20 Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya abulu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo.

21 Momwemo wautsanso choipa cha ubwana wako, pakukhudza Aejipito nsonga za mawere ako, chifukwa cha mawere a ubwana wako.

22 Chifukwa chake, Oholiba, atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakuutsira mabwenzi ako amene moyo wako wakufidwa nao, ndi kukufikitsira iwowa pozungulira ponse atsutsane nawe,

23 a ku Babiloni, ndi Ababiloni, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasiriya onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo.

24 Ndipo adzakudzera ndi zida, magaleta a nkhondo, ndi magaleta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zotchinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.

25 Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakuchitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakuchotsera ana ako aamuna ndi aakazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto.

26 Adzakuvulanso zovala zako, ndi kukuchotsera zokometsera zako zokongola.

27 Motero ndidzakuleketsera choipa chako, ndi chigololo chako chochokera m’dziko la Ejipito; ndipo sudzazikwezeranso maso ako, kapena kukumbukiranso Ejipito.

28 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakupereka m’dzanja la iwo amene uwada, m’dzanja la iwo amene moyo wako ufukidwa nao;

29 ndipo adzachita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira ntchito, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa; ndi umaliseche wa zigololo zako udzavulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe.

30 Izi adzakuchitira chifukwa watsataamitundu, ndi kuchita nao chigololo, popezanso wadetsedwa ndi mafano ao.

31 Wayenda m’njira ya mkulu wako, chifukwa chake ndidzapereka chikho chake m’dzanja lako.

32 Atero Ambuye Yehova, M’chikho cha mkulu wako udzamweramo ndicho chachikulu ngati thumba; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m’menemo.

33 Udzadzala ndi kuledzera ndi chisoni, ndi chikho chodabwitsa ndi cha chipasuko, ndi chikho cha mkulu wako Samariya.

34 Udzamwa ichi ndi kugugudiza, ndi kuchechetachecheta zibade zake, ndi kung’amba mawere ako; pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova.

35 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso choipa chako ndi zigololo zako.

36 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Uwafotokozere tsono zonyansa zao.

37 Pakuti anachita chigololo, ndi m’manja mwao muli mwazi, ndipo anachita chigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao aamuna amene anandibalira, kuti athedwe.

38 Anandichitiranso ichi, anadetsa malo anga opatulika tsiku lomwelo, naipsamasabataanga;

39 pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m’malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m’kati mwa nyumba yanga.

40 Ndiponso munatuma kuitana anthu ochokera kutali, ndiwo munawatumira mthenga; ndipo taona, anadza amenewo unasamba, chifukwa cha iwo unapaka maso ako mankhwala, ndi kuvala zokometsera;

41 ndipo unakhala pa kama waulemu, pali gome lokonzekeratu patsogolo pake; pamenepo unaika chofukiza chonga ndi mafuta anga.

42 Ndipo phokoso lalikulu lidaleka pomwepo, ndipo pamodzi ndi anthu wamba anabwera nao olodzera ochokera kuchipululu, naika makoza m’manja mwa awiriwo, ndi akorona okongola pamitu pao.

43 Pamenepo ndinati za uyu anakalamba nazo zigololo, Tsopano iwo adzachita zigololo naye, ndi iyenso nao.

44 Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wachigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo.

45 Ndipo anthu olungama adzawaweruza monga mwa maweruzo a achigololo, ndi maweruzo a akazi okhetsa mwazi; pakuti ndiwo achigololo, ndi m’manja mwao muli mwazi.

46 Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda chuma chao.

47 Ndi msonkhanowo udzawaponya miyala, ndi kuwatha ndi malupanga ao, adzawapha ana ao aamuna ndi aakazi, ndi kutentha nyumba zao ndi moto.

48 Momwemo ndidzaleketsa dama m’dzikomo, kuti alangizidwe akazi onse kusachita monga mwa dama lanu.

49 Ndipo adzakubwezerani dama lanu, nimudzasenza machimo a mafano anu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/23-9d19d7d9b8e01685d157c05288302b20.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 24

Fanizo la mphika wobwadamuka

1 Anandidzeranso mau a Yehova chaka chachisanu ndi chinai, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, ndi kuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Udzilembere dzina la tsiku lomwe lino, mfumu ya ku Babiloni wayandikiraYerusalemutsiku lomwe lino.

3 Ndipo uphere nyumba yopandukayo fanizo, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tereka mphika; uutereke, nuthire madzi m’menemo.

4 Longamo pamodzi ziwalo zake, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.

5 Tengako choweta chosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ake omwe uwaphike m’mwemo.

6 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mzinda wokhetsa mwazi, mphika m’mene muli dzimbiri, losauchokera dzimbiri lake; uchotsemo chiwalochiwalo; sanaugwere maere.

7 Pakuti mwazi wake uli m’kati mwake anauika pathanthwe poyera, sanautsanulire panthaka kuukwirira ndi fumbi.

8 Pofuna kuutsa ukali, ndi kubwezera chilango, ndaika mwazi wake pathanthwe poyera, kuti usakwiririke.

9 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mzinda wokhetsa mwazi, ndidzakulitsa mulu wa nkhuni.

10 Zichuluke nkhuni, koleza moto, nyama ipse, uwiritse msuzi wake, ubwadamuke, ndi mafupa ake atibuke.

11 Pamenepo uukhazike pa makala ake opanda kanthu m’menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wake; ndi kuti chodetsa chake chisungunuke m’mwemo, kuti dzimbiri lake lithe.

12 Ntchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lake lalikulu siliuchokera, dzimbiri lake liyenera kumoto.

13 M’chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.

14 Ine Yehova ndachinena, chidzachitika; ndipo ndidzachichita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unachitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova.

Kumwalira kwa mkazi wa Ezekiele kuli chizindikiro cha kwa Yuda

15 Mau a Yehova anandidzeranso, akuti,

16 Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikuchotsera chokonda maso ako ndi chikomo, koma usamve chisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.

17 Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire chilemba, nuvale nsapato kumapazi ako, usaphimbe milomo yako. Kapena kudya mkate wa anthu.

18 Ndipo nditalankhula ndi anthu m’mawa, madzulo ake mkazi wanga anamwalira; ndi m’mawa mwake ndinachita monga anandilamulira.

19 Nanena nane anthu, Simudzatiuza kodi zitani nafe izi muzichita?

20 Ndipo ndinanena nao, Anandidzera mau a Yehova, akuti,

21 Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m’maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.

22 Ndipo mudzachita monga umo ndachitira ine, osaphimba milomo yanu, kapena kudya mkate wa anthu.

23 Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu kumapazi anu, simudzachita chisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzake.

24 Momwemo Ezekiele adzakhala kwa inu chizindikiro; umo monse anachitira iye mudzachita ndinu; chikadza ichi mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25 Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwachotsera mphamvu yao, chimwemwe chao chopambana, chowakonda m’maso mwao, ndi chokhumbitsa mtima wao, ana ao aamuna ndi aakazi,

26 kuti tsiku lomwelo wopulumukayo adzakudzera, kukumvetsa m’makutu mwako?

27 Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso chete, momwemo udzawakhalira chizindikiro; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/24-2b20ed4fd402c04b53702f660891531d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 25

Aneneratu za kulangidwa kwa Aamoni

1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kwa ana a Amoni, nuwanenere;

3 nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Ha! Kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israele; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;

4 chifukwa chake taona, ndidzakupereka kwa ana a kum’mawa ukhale waowao, kuti amange misasa yao mwa iwe, namange pokhala pao mwa iwe, iwo adzadya zipatso zako ndi kumwa mkaka wako.

5 Ndipo ndidzayesa Raba khola langamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing’ono; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

6 Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kuvina, ndi kukondwera ndi chipeputso chonse cha moyo wako, kupeputsa dziko la Israele,

7 chifukwa chake taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale chofunkha chaamitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m’maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Za kulangidwa kwa Mowabu

8 Atero Ambuye Yehova, Popeza Mowabu ndi Seiri akuti, Taona nyumba ya Yuda ikunga amitundu onse;

9 chifukwa chake taona ndidzatsegula pambali pake pa Mowabu kuyambira kumizinda, kumizinda yake yokhala mphepete, yokometsetsa ya m’dziko, Beteyesimoti, Baala-Meoni, ndi Kiriyataimu,

10 kuwapereka kwa ana a kum’mawa pamodzi ndi ana a Amoni; ndipo ndidzawapereka akhale aoao, kuti ana a Amoni asakumbukikenso mwa amitundu;

11 ndipo ndidzakwaniritsa maweruzo mu Mowabu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Za kulangidwa kwa Edomu

12 Atero Ambuye Yehova, Popeza Edomu anachita mobwezera chilango pa nyumba ya Yuda, napalamula kwakukulu pakuibwezera chilango,

13 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.

14 Ndipo ndidzalibwezera Edomu chilango mwa dzanja la anthu anga Israele; ndipo adzachita mu Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera chilango kwanga, ati Ambuye Yehova.

Za kulangidwa kwa Afilisti

15 Atero Ambuye Yehova, Popeza Afilisti anachita mobwezera chilango nabwezera chilango ndi mtima wopeputsa kuononga, ndi udani wosatha,

16 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatambasulira Afilisti dzanja langa, ndi kulikha Akereti, ndi kuononga otsalira mphepete mwa nyanja.

17 Ndipo ndidzawabwezera chilango chachikulu, ndi malango ankharwe; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwabwezera chilango Ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/25-b9f49c294d5ef8c51de794106802614c.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 26

Za kulangidwa kwa Tiro

1 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodolaYerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;

3 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Tiro, ndidzakukweretseraamitundu, monga nyanja iutsa mafunde ake.

4 Ndipo adzagumula malinga a Tiro, ndi kugwetsa nsanja zake; inde ndidzausesa fumbi lake, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.

5 Udzakhala poyanika khoka pakati pa nyanja, pakuti Ine ndachinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala chofunkha cha amitundu.

6 Ndi ana ake aakazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Tiro Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, yochokera kumpoto ndi akavalo, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.

8 Ana ako aakazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira chikopa.

9 Nadzaikira malinga ako zogumulira, nadzagwetsa nsanja zako ndi zida zake.

10 Popeza achuluka akavalo ake, fumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magaleta, polowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m’mzinda popasukira linga lake.

11 Ndi ziboda za akavalo ake iye adzapondaponda m’makwalala ako onse; adzapha anthu ako ndi lupanga; ndi zoimiritsa za mphamvu yako zidzagwa pansi.

12 Ndipo adzalanda chuma chako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi fumbi lako, m’madzi.

13 Ndipo ndidzaleketsa phokoso la nyimbo zako, ndi kulira kwa mazeze ako sikudzamvekanso.

14 Ndipo ndidzakuyesa pathanthwe poyera; udzakhala poyanika khoka, sadzakumanganso; pakuti Ine Yehova ndachinena, ati Ambuye Yehova.

15 Atero Ambuye Yehova kwa Tiro, Zisumbu sizidzagwedezeka nanga pomveka kugwa kwako, pobuula olasidwa, pakuchitika kuphako pakati pako?

16 Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe.

17 Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pokhala pa anthu a panyanja, mzinda womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!

18 Pamenepo zisumbu zidzanjenjemera tsiku la kugwa kwako, inde zisumbu za kunyanja zidzatenga nkhawa pa kuchokera kwako.

19 Pakuti atero Ambuye Yehova, Pamene ndikusandutsa mzinda wopasuka, ngati mizinda yosakhalamo anthu, ndi kukukweretsera nyanja, nadzakumiza madzi aakulu;

20 pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m’dziko la amoyo,

21 ndidzakuika woopsa; ndipo sudzaonekanso, chinkana akufunafuna sudzapezekanso konse, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/26-04c1a8181cb6af7962f31e979ed5dd0d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 27

Nyimbo ya maliro ya pa Tiro

1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro;

3 nuti kwa Tiro, Iwe wakukhala polowera m’nyanja, wakuchita malonda ndi mitundu ya anthu m’zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Tiro, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.

4 M’mphepete mwako muli m’kati mwa nyanja, iwo anakumanga iwe anakonza kukongola kwako kukhale kwangwiro.

5 Anacheka matabwa ako onse amlombwa wa ku Seniri, anatenga mikungudza ya ku Lebanoni kukupangira milongoti.

6 Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu.

7 Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Ejipito, likhale ngati mbendera yako; chophimba chako ndicho nsalu yamadzi ndi yofiirira zochokera ku zisumbu za Elisa.

8 Okhala mu Sidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Tiro, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako.

9 Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.

10 Apersiya, Aludi, Aputi, anali m’khamu lako; anthu ako a nkhondo anapachika chikopa ndi chisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.

11 Anthu a Arivadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapachika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.

12 Tarisisi anagulana nawe malonda m’kuchuluka kwa chuma chilichonse; anagula malonda ako ndisilivandi chitsulo, seta ndi ntovu.

13 Yavani, Tubala, Meseki, anagulana nawe malonda; ndi anthu amoyo ndi zotengera zamkuwa anagulana nawe malonda.

14 Iwo a nyumba ya Togarima anagula malonda ako ndi akavalo, ndi akavalo a nkhondo, ndi nyuru.

15 Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda.

16 Aramu anachita nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsalu yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.

17 Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.

18 Damasiko anagulana nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chilichonse, ndi vinyo wa ku Heliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera.

19 Vedani ndi Yavani anagula malonda ako ndi thonje, unagulana nao chitsulo chosalala, ngaho, ndi nzimbe.

20 Dedani anagulana nawe malonda ndi nsalu za mtengo wake zoyenda nazo pa kavalo.

21 Arabiya ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; anaankhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe.

22 Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide.

23 Harani ndi Kane ndi Edeni, amalonda a ku Sheba Asiriya ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.

24 Awa anagulana nawe malonda ndi zovala zosankhika, ndi matumba a nsalu zofiirira ndi zopikapika, ndi chuma cha thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.

25 Zombo za ku Tarisisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzadzidwa ndi chuma ndi ulemu waukulu pakati pa nyanja.

26 Opalasa ako anakufikitsa kumadzi aakulu; mphepo ya kum’mawa inakuthyola m’kati mwa nyanja.

27 Chuma chako, zako zogulana nazo malonda ako, amalinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m’kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.

28 Pakumveka mfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.

29 Ndi onse ogwira nkhafi, amalinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika kuzombo zao, nadzaima pamtunda,

30 nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira fumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m’maphulusa,

31 nadzameta mpala chifukwa cha iwe, nadzadzimangira ziguduli m’chuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.

32 Ndipo pakulira adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kukulirira, ndi kuti, Wakunga Tiro ndani, wakunga uyu waonongeka pakati pa nyanja?

33 Pakutuluka malonda ako m’nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a padziko lapansi ndi chuma chako chochuluka ndi malonda ako.

34 Muja unathyoka ndi nyanja m’madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.

35 Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri, zikhululuka nkhope zao.

36 Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala choopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/27-37e6dc37e4164cbd3801ad208769d31a.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 28

Aneneratu za kulangidwa kwa mfumu ya ku Tiro

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,

3 taona, ndiwe wanzeru woposa Daniele, palibe chinsinsi angakubisire;

4 mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera chuma, wadzionereranso golide ndisilivamwa chuma chako;

5 mwa nzeru zako zazikulu ndi kugulana malonda kwako wachulukitsa chuma chako, ndi mtima wako wadzikuza chifukwa cha chuma chako;

6 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu;

7 chifukwa chake taona ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.

8 Adzakutsitsira kumanda, nudzafa mafedwe a ophedwa m’kati mwa nyanja.

9 Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m’dzanja la iye wakupha iwe.

10 Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova.

Nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Tiro

11 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

12 Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Tiro, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi chizindikiro, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.

13 Unali mu Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.

14 Unalikerubiwodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali paphiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.

15 Unali wangwiro m’njira zako chilengedwere iwe, mpaka chinapezeka mwa iwe chosalungama.

16 Mwa kuchuluka kwa malonda ako anakudzaza m’kati mwako ndi chiwawa, ndipo unachimwa; chifukwa chake ndinakukankha kukuchotsa paphiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukuchotsa pakati pa miyala yamoto.

17 Unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako, waipsa nzeru zako; chifukwa cha kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.

18 Mwa mphulupulu zako zochuluka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; chifukwa chake ndatulutsa moto m’kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.

19 Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka choopsa, ndipo sudzakhalanso konse.

Za kulangidwa kwa Sidoni

20 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

21 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Sidoni, nuunenere;

22 uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuchita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu.

23 Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m’makwalala ake, ndi olasidwa adzagwa m’kati mwake ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

24 Ndipo nyumba ya Israele siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya aliyense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25 Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israele mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwaiwowa, pamaso paamitundu; ndipo adzakhala m’dziko mwaomwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.

26 Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m’mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/28-5896267dc01ceab54fb27e030b438f4b.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 29

Aneneratu za kulangidwa kwa Ejipito

1 Chaka chakhumi, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi ndi chiwiri la mweziwo, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako itsutsane nayeFaraomfumu ya Aejipito, nunenere motsutsana ndi iye, ndi Ejipito yense;

3 nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aejipito, ng’ona yaikulu yakugona m’kati mwa mitsinje yake, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.

4 Koma ndidzaika mbedza m’kamwa mwako, ndi kumamatiritsa nsomba za m’mitsinje mwako kumamba ako; ndipo ndidzakukweza kukutulutsa m’kati mwa mitsinje yako, pamodzi ndi nsomba zonse za m’mitsinje mwako zomamatira pa mamba ako.

5 Ndipo ndidzakutaya kuchipululu, iwe ndi nsomba zonse za m’mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale chakudya cha zilombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga.

6 Ndi onse okhala mu Ejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anakhalira nyumba ya Israele mchirikizo wabango.

7 Muja anakugwira ndi dzanja unathyoka, ndi kulasa mapewa ao onse; ndi muja anakutsamira unathyoka, ndi kuwagwedeza ziuno zao zonse.

8 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama.

9 Ndi dziko la Ejipito lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine.

10 Chifukwa chake taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene kufikira malire a Kusi.

11 Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai.

12 Ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi mizinda yake pakati pa mizinda yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aejipito mwaamitundu, ndi kuwabalalitsa m’maiko.

13 Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aejipito kumitundu ya anthu kumene anamwazikirako;

14 ndipo ndidzabweza undende wa Ejipito, ndi kuwabwezera kudziko la Patirosi, kudziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka.

15 Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawachepsa, kuti asachitenso ufumu pa amitundu.

16 Ndipo sudzakhalanso chotama cha nyumba ya Israele, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

17 Ndipo kunali chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

18 Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anachititsa ankhondo ake ntchito yaikulu yoponyana ndi Tiro; mitu yonse inachita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Tiro, iye kapena ankhondo ake, pa ntchito anagwirayo;

19 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Ejipito kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzachoka nao aunyinji ake, nadzafunkha ndi kulanda zake, ndizo mphotho ya khamu lake.

20 Ndamninkha dziko la Ejipito chombwezera ntchito yake, popeza anandigwirira ntchito, ati Ambuye Yehova.

21 Tsiku ilo ndidzameretsera nyumba ya Israele nyanga; ndipo ndidzakutsegulira pakamwa pakati pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/29-713979686ed4072d33222d2c7eec252d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 30

Ejipito adzagonjetsedwa ndi mfumu ya ku Babiloni

1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, nenera, uziti, Atero Ambuye Yehova, Liritsani, Ha, tsikulo!

3 Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo yaamitundu.

4 Ndi lupanga lidzadzera Ejipito, ndi mu Kusi mudzakhala kuwawa kwakukulu, pakugwa ophedwa mu Ejipito; ndipo adzachotsa aunyinji ake, ndi maziko ake adzagadamuka.

5 Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Libiya, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.

6 Atero Yehova, Iwonso ochirikiza Ejipito adzagwa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatsika, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene adzagwa m’kati mwake ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

7 Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi mizinda yake idzakhala pakati pa mizinda yopasuka.

8 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto mu Ejipito, naonongeka onse akumthandiza.

9 Tsiku ilo mithenga idzatuluka pamaso panga m’zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukulu pakati pao, monga tsiku la Ejipito, pakuti taona, likudza.

10 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaleketsa kusokosera kwa Ejipito ndi dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni.

11 Iye ndi anthu ake pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Ejipito malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa.

12 Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m’dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse zili m’mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndachinena.

13 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito.

14 Ndipo ndidzasandutsa Patirosi labwinja, ndi kuika moto mu Zowani, ndi kukwaniritsa maweruzo mu No.

15 Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika penipeni pa Ejipito, ndi kulikha aunyinji a No.

16 Ndipo ndidzaika moto mu Ejipito; Sini adzamva kuwawa kwakukulu, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana.

17 Anyamata a Oni ndi Pibeseti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende.

18 Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m’menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake aakazi adzalowa undende.

19 Motero ndidzakwaniritsa maweruzo mu Ejipito, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

20 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi woyamba, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

21 Wobadwa ndi munthu iwe, ndathyola dzanja laFaraomfumu ya Aejipito, ndipo taona, silinamangidwe kuti lipole, kulikulunga ndi nsalu, kulilimbitsa ligwire lupanga.

22 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Farao mfumu ya Aejipito, ndidzathyola manja ake, lolimba ndi lothyokalo, ndi kutayitsa lupanga m’dzanja lake.

23 Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m’maiko.

24 Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m’dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.

25 Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni, nalitambasula iye padziko la Ejipito.

26 Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa mwa amitundu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/30-42693f5ca2cabb372e2a4682a75d345d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 31

Mau ena oneneratu za Farao

1 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi wachitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwaFaraomfumu ya Aejipito ndi aunyinji ake, Ufanana ndi yani mu ukulu wako?

3 Taona, Asiriya anali mkungudza wa ku Lebanoni ndi nthambi zokoma zovalira, wautali msinkhu, kunsonga kwake ndi kumitambo.

4 Madzi anaumeretsa, chigumula chinaukulitsa, mitsinje yake inayenda, nizungulira munda wake, nipititsa michera yake kumitengo yonse yakuthengoko.

5 Chifukwa chake msinkhu wake unaposa mitengo yonse yakuthengo, ndi nthambi zake zinachuluka, ndi nthawi zake zinatalika, chifukwa cha madzi ambiri pophuka uwu.

6 Mbalame zonse za m’mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zake, ndi pansi pa nthawi zake zinaswana nyama zonse zakuthengo, ndi pa mthunzi wake inakhala mitundu yonse yaikulu ya anthu.

7 M’mwemo unakoma mu ukulu wake, m’kutalika kwa nthawi zake, popeza muzu wake unakhala kumadzi ambiri.

8 Mikungudza ya m’munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwa siinanga nthambi zake, mifula siinanga nthawi zake; m’munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwake.

9 Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zake zochuluka; ndi mitengo yonse ya mu Edeni inali m’munda wa Mulungu inachita nao nsanje.

10 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wake, nufikitsa nsonga yake kumitambo, nukwezeka mtima wake m’kukula kwake,

11 ndidzaupereka m’dzanja la wamphamvu waamitundu; iye adzachita naotu, Ine ndautaya mwa choipa chake.

12 Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zake zidagwa pamapiri ndi m’zigwa zonse, ndi nthambi zake zinathyokera ku timitsinje tonse ta m’dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi inatsika kumthunzi wake, niusiya.

13 Pogwera pake padzakhala mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi nyama zonse zakuthengo zidzakhala pa nthambi zake;

14 kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m’kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.

15 Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinachititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinachepsa mitsinje yake, ndi madzi aakulu analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebanoni, ndi mitengo yonse yakuthengo inafota chifukwa cha uwo.

16 Ndinagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwake, muja ndinagwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edeni yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebanoni, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwake mwa dziko lapansi.

17 Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lake okhala mumthunzi mwake pakati pa amitundu.

18 Momwemo ufanana ndi yani mu ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni m’munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/31-0b2a1b3711d044216d55eadb23bb0f83.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 32

Nyimbo ya maliro ya pa Farao

1 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri, mwezi wakhumi ndi chiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, takwezeraFaraomfumu ya Aejipito nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango waamitundu, unanga ng’ona ya m’nyanja, unabuka m’mitsinje mwako, nuvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.

3 Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakuvuulira m’khoka mwanga.

4 Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi kukhutitsa zilombo za dziko lonse lapansi ndi iwe.

5 Ndipo ndidzaika nyama yako pamapiri, ndi kudzaza zigwa ndi msinkhu wako.

6 Ndipo ndidzamwetsa dziko losambiramo iwe ndi mwazi wako, kufikira kumapiri; ndi mitsinje idzadzala nawe.

7 Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nyenyezi zake; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.

8 Ndidzakudetsera miyuni yonse yakuunikira kuthambo, ndi kuchititsa mdima padziko lako, ati Ambuye Yehova.

9 Ndidzavutanso mitima ya mitundu yambiri ya anthu, pakufikitsa Ine chionongeko chako mwa amitundu, m’maiko amene sunawadziwe.

10 Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzachita malunga chifukwa cha iwe, pakung’animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense chifukwa cha moyo wake tsiku lakugwa iwe.

11 Pakuti atero Ambuye Yehova, Lupanga la mfumu ya ku Babiloni lidzakudzera.

12 Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Ejipito, ndi aunyinji ake onse adzaonongeka.

13 Ndidzaononganso nyama zake zonse za kumadzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzavundulira, ndi ziboda za nyama zosawavundulira.

14 Pamenepo ndidzadikhitsa madzi ake, ndi kuyendetsa madzi a m’mitsinje mwao ngati mafuta, ati Ambuye Yehova.

15 Pakusanduliza Ine dziko la Ejipito likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zake, pakukantha Ine onse okhala m’mwemo, pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

16 Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana aakazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.

Mau a kulirira aunyinji a Ejipito

17 Kunalinso chaka chakhumi ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, anandidzera mau a Yehova, ndi kuti,

18 Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Ejipito, nuwagwetsere iye ndi ana aakazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

19 Uposa yani m’kukoma kwako? Tsika, nuikidwe ndi osadulidwa.

20 Adzagwa pakati pa iwo ophedwa ndi lupanga, operekedwa kwa lupanga, mkokereko ndi aunyinji ake onse.

21 Amphamvu oposa ali m’kati mwa manda adzanena naye, pamodzi ndi othandiza ake, Anatsikira, agonako osadulidwawo, ophedwa ndi lupanga.

22 Asiriya ali komwe ndi msonkhano wake wonse, manda ake amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga;

23 manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lake lizinga manda ake; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anopsetsa m’dziko la amoyo.

24 Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m’dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

25 Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ake onse, manda ake amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa m’dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa.

26 Meseki, Tubala, ndi aunyinji ake onse ali komweko, manda ake amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m’dziko la amoyo.

27 Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao zili pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m’dziko la amoyo.

28 Ndipo udzathyoledwa pakati pa osadulidwa, nudzagona pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga.

29 Edomu ali komwe, mafumu ake ndi akalonga ake onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.

30 Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Asidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nachita manyazi chifukwa cha kuopsetsa anachititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.

31 Farao adzawaona, nadzasangalala nao aunyinji ake onse, Farao ndi ankhondo ake onse ophedwa ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

32 Pakuti ndinaika kuopsa kwake m’dziko la amoyo; ndipo adzaikidwa pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, ndiye Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/32-914048b71749fbe4fadf26ceea5d8c77.mp3?version_id=1068—