Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 13

1 Ndipo mau a Yehova anandidzera ine, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israele onenerawo, nuziti nao onenera za m’mtima mwaomwao, Tamverani mau a Yehova.

3 Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu waowao, chinkana sanaone kanthu.

4 Aneneri ako, Israele, akhala ngati nkhandwe m’mapululu.

5 Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israele, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.

6 Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.

7 Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanene?

8 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.

9 Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m’buku lolembedwamo nyumba ya Israele; kapena kulowa m’dziko la Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

10 Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;

11 uziti nao olimata ndi dothi losapondeka, kuti lidzagwa, lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu; ndi inu, matalala aakulu, mudzagwa; ndi mkuntho udzalithithimula.

12 Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Lili kuti dothi munalimata nalo?

13 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho mu ukali wanga; ndipo lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu mu mkwiyo wanga, ndi matalala aakulu adzalitha mu ukali wanga.

14 M’mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ake agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pake; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

15 M’mwemo ndidzakwaniritsa ukali wanga pa lingalo, ndi pa iwo analimata ndi dothi losapondeka, ndipo ndidzati kwa inu, Lingalo palibe, ndi olimata palibe,

16 ndiwo aneneri a Israele akunenera zaYerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova.

Mau akutsutsa aneneri aakazi onama

17 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, uziika nkhope yako itsutsane nao ana aakazi a anthu ako, akunenera za m’mtima mwao, nunenere chowatsutsa,

18 nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iliyonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?

19 Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza.

20 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kuiuluza; ndipo ndidzazikwatula m’manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kuiuluza.

21 Zokuta mitu zanu zomwe ndidzazing’amba, ndi kulanditsa anthu anga m’manja mwanu; ndipo sadzakhalanso m’mphamvu mwanu kusakidwa; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

22 Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetse chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;

23 chifukwa chake simudzaonanso zopanda pake, kapena kupenda; koma ndidzalanditsa anthu anga m’manja mwanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/13-6321c0ed8fb48e646b0e9cb037dd8592.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 14

Chilango cha pa opembedza mafano

1 Pamenepo anafika kwa ine akulu ena a Israele nakhala pansi pamaso panga.

2 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

3 Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi?

4 Chifukwa chake ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Aliyense wa nyumba ya Israele wakuutsa mafano ake mumtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadza kwamneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ake aunyinji;

5 kuti ndigwire nyumba ya Israele mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.

6 Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Bwerani, lekani mafano anu, tembenuzani nkhope zanu kuzisiya zonyansa zanu zonse.

7 Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera mu Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m’mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;

8 ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa chodabwitsa, ndi chizindikiro, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

9 Ndipo akacheteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamcheta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israele.

10 Ndipo adzasenza mphulupulu yao, mphulupulu ya mneneri idzanga mphulupulu ya uja wamfunsira;

11 kuti nyumba ya Israele isasocherenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.

Malango a Mulungu ali olungama

12 Ndipo anandidzera mau a Yehova akuti,

13 Likandichimwira dziko ndi kuchita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulithyolera mchirikizo wake, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,

14 chinkana akadakhala m’mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.

15 Ndikapititsa zilombo zoipa pakati padziko, ndi kupulula ana, kuti likhale lachipululu losapitako munthu chifukwa cha zilombo,

16 chinkana anthu omwewo atatu akadakhala m’mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lachipululu.

17 Kapena ndikadza padziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati padziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;

18 chinkana anthu atatuwo akadakhala m’mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; koma iwo akadapulumuka okha.

19 Kapena ndikatumizira dzikolo mliri, ndi kulitsanulira ukali wanga ndi mwazi, kulidulira munthu ndi nyama;

20 chinkana Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadakhala m’mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi chilungamo chao.

21 Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumiziraYerusalemumaweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?

22 Koma onani mudzatsala opulumuka m’mwemo amene adzatulutsidwa, ndiwo ana aamuna ndi aakazi; taonani, adzatuluka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zochita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo.

23 Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichite kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/14-ee8961a8876891ea583c9964907bdafd.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 15

Mtengo wopanda pake

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uliwonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango?

3 Kodi atengako mtengo kupanga nao ntchito? Atengako chichiri kodi kupachikapo chipangizo chilichonse?

4 Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zake zonse ziwiri, nupserera pakati pake, kodi ukomera ntchito iliyonse?

5 Taonani, pokhala wamphumphu sunayenere ntchito iliyonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso ntchito iliyonse?

6 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala muYerusalemu.

7 Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzatuluka kumoto, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.

8 Ndipo ndidzasandutsa dziko chipululu; popeza anachita cholakwa, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/15-b6e0b7a88321e34c615468447e6b148d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 16

Kusakhulupirika kwa Yerusalemu

1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, DziwitsaYerusalemuzonyansa zake, nuziti,

3 Atero Ambuye Yehova kwa Yerusalemu, Chiyambi chako ndi kubadwa kwako ndiko kudziko la Akanani; atate wako anali Mwamori, ndi mai wako Muhiti.

4 Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadule nchofu yako, sanakuyeretse ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthire mchere konse, kapena kukukulunga m’nsalu ai.

5 Panalibe diso linakuchitira chifundo, kukuchitira chimodzi chonse cha izi, kuchitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwako.

6 Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikuvimvinizika m’mwazi mwako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m’mwazi wako. Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m’mwazi mwako, Khala ndi moyo.

7 Ndinakuchulukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, mawere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamaliseche ndi wausiwa.

8 Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.

9 Ndipo ndinakusambitsa ndi madzi, inde ndinakutsuka kukuchotsera mwazi wako, ndi kukudzoza mafuta.

10 Ndinakuvekanso ndi nsalu zopikapika, ndi kukuveka nsapato za chikopa cha katumbu; ndinakuzenenga nsalu yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsalu yasilika.

11 Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m’manja mwako, ndi unyolo m’khosi mwako.

12 Momwemo ndinaika chipini m’mphuno mwako, ndi maperere m’makutu mwako, ndi korona wokongola pamutu pako.

13 Ndipo unadzikometsera ndi golide, ndisiliva, ndi chovala chako ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika; unadya ufa wosalala, ndi uchi, ndi mafuta; ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindulapindula kufikira unasanduka ufumu.

14 Ndi mbiri yako inabuka mwaamitunduchifukwa cha kukongola kwako; pakuti ndiko kwangwiro, mwa ulemerero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova.

15 Koma unatama kukongola kwako, ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo; unali wake.

16 Ndipo unatengako zovala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawangamawanga, ndi kuchitapo chigololo; zotere sizinayenere kufika kapena kuchitika.

17 Unatenganso zokometsera zako zokoma za golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kuchita nao chigololo.

18 Unatenganso zovala zako za nsalu yopikapika, ndi kuwaveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi chofukiza changa pamaso pao.

19 Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uchi, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zichite fungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.

20 Unatenganso ana ako aamuna ndi aakazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidachepa kodi,

21 kuti unawapha ana anga ndi kuwapereka, pakuwapititsa pamoto?

22 Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukire masiku a ubwana wako, muja unakhala wamaliseche ndi wausiwa, womvimvinizika m’mwazi wako.

23 Ndipo kudachitika utatha zoipa zako zonse, (tsoka iwe, tsoka, ati Ambuye Yehova)

24 unadzimangira nyumba yachimphuli, unadzimangiranso chiunda m’makwalala ali onse.

25 Unamanga chiunda chako pa mphambano zilizonse, ndipo unanyansitsa kukongola kwako, ndi kutukula mapazi ako kwa yense wopitako, ndi kuchulukitsa chigololo chako.

26 Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, aakulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga.

27 Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana aakazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.

28 Unachitanso chigololo ndi Aasiriya, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unachita chigololo nao, koma sunakoledwe.

29 Unachulukitsanso chigololo chako m’dziko la Kanani, mpaka dziko la Ababiloni, koma sunakoledwe nachonso.

30 Ha? Mtima wako ngwofooka, ati Ambuye Yehova, pakuchita iwe izi zonse, ndizo ntchito za mkazi wachigololo wouma m’maso.

31 Pakumanga nyumba yako yachimphuli pa mphambano zilizonse, ndi pomanga chiunda chako m’makwalala ali onse, sunakhale ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.

32 Ndiwe mkazi wokwatibwa wochita chigololo, wolandira alendo m’malo mwa mwamuna wake.

33 Anthu amaninkha akazi onse achigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kuchokera kumbali zonse, kuti achite nawe chigololo.

34 M’mwemo usiyana konse ndi akazi ena m’chigololo chako; pakuti palibe wokutsata kuchita nawe chigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.

35 Chifukwa chake, wachigololo iwe, tamvera mau a Yehova:

36 Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nuvundukuka umaliseche wako mwa chigololo chako ndi mabwenzi ako, ndi chifukwa cha mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawapatsa;

37 chifukwa chake taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwavundukulira umaliseche wako, kuti aone umaliseche wako wonse.

38 Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi achigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.

39 Ndidzakuperekanso m’dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yachimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakuvula zovala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa.

40 Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao.

41 Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kuchita chigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yachigololo.

42 M’mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakuchokera, ndipo ndidzakhala chete wosakwiyanso.

43 Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako, koma wandivuta nazo zonsezi, chifukwa chake taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzachita choipa ichi choonjezerapo pa zonyansa zako zonse.

44 Taona, aliyense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga make momwemo mwana wake.

45 Iwe ndiwe mwana wa mai ako wonyansidwa naye mwamuna wake ndi ana ake, ndipo iwe ndiwe mng’ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Muhiti, ndi atate wako ndiye Mwamori.

46 Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala kudzanja lako lamanzere, iye ndi ana ake aakazi; ndi mng’ono wako wokhala kudzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ake aakazi.

47 Koma sunayende m’njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang’ono pokha; unawaposa iwo m’kuvunda kwako, m’njira zako zonse.

48 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, Sodomu mng’ono wako sanachite, iye kapena ana ake aakazi, monga umo unachitira iwe ndi ana ako aakazi.

49 Taona, mphulupulu ya mng’ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.

50 Ndipo anadzikuza, nachita chonyansa pamaso panga; chifukwa chake ndinawachotsa pakuchiona.

51 Ngakhale Samariya sanachite theka la zochimwa zako, koma unachulukitsa zonyansa zako, kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazichita.

52 Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zochimwa zako unazichita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m’chilungamo chao, nawenso uchite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama.

53 Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ake, ndi undende wa Samariya ndi ana ake, ndi undende wa andende ako pakati pao;

54 kuti usenze manyazi ako, ndi kuti uchite manyazi chifukwa cha zonse unazichita pakuwatonthoza.

55 Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ake adzabwerera umo unakhalira kale, ndipo Samariya ndi ana ake adzabwerera umo anakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale.

56 Ndipo sunakambe za mbale wako Sodomu pakamwa pako tsiku la kudzikuza kwako;

57 chisanavundukuke choipa chako monga nthawi ya chitonzo cha ana aakazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana aakazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.

58 Wasenza choipa chako ndi zonyansa zako, ati Yehova.

59 Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzachita ndi iwe monga umo unachitira; popeza wapepula lumbiro ndi kuthyola pangano.

60 Koma ndidzakumbukira Ine pangano langa ndi iwe m’masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.

61 Pamenepo udzakumbukira njira zako ndi kuchita manyazi, pakulandira abale ako aakulu ndi aang’ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako aakazi, angakhale sali a pangano lako.

62 Pakuti ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova;

63 kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/16-5266d6ae848f35c0213b9d16ba11a56b.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 17

Fanizo la ziombankhanga ziwiri ndi mpesa

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israele,

3 nuziti, Atero Ambuye Yehova, Chiombankhanga chachikulu ndi mapiko aakulu, ndi maphiphi aatali, odzala nthenga cha mathothomathotho, chinafika ku Lebanoni, nkutenga nsonga ya mkungudza,

4 chinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kumuka nayo kudziko la malonda, chinaiika m’mzinda wa amalonda.

5 Chinatengakonso mbeu ya m’dziko, ndi kuibzala m’nthaka yokoma, chinaiika panali madzi ambiri, chinaioka ngati mtengo wamsondodzi.

6 Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala waufupi msinkhu, nthambi zake zinapindikira momwe, ndi mizu yake pansi pake, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.

7 Panalinso chiombankhanga china chachikulu, ndi mapiko aakulu, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unachipindira mizu yake, nuchilunjikitsira zake, kuchokera pookedwa pake, kuti chiuthirire madzi.

8 Unaokedwa mu nthaka yabwino kuli madzi ambiri, kuti uphuke nthambi, nubale zipatso, nukhale mpesa wabwino.

9 Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? Sadzausula ndi kudula zipatso zake, kuti uume, kuti masamba ake onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikulu, kapena anthu ambiri akuuzula?

10 Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? Sudzauma chiumire kodi pakuuomba mphepo ya kum’mawa? Udzauma pookedwa apo udaphuka.

11 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti.

12 Uziti, tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nchiyani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babiloni inadza kuYerusalemu, nkutenga mfumu yake ndi akalonga ake, nkubwera nao kuli iye ku Babiloni;

13 ndipo inatenga wa mbumba yachifumu, nkuchita naye pangano, nkumlumbiritsa, nkuchotsa amphamvu a m’dziko;

14 kuti ufumuwo ukhale wopepuka, kuti usadzikweze, koma kuti pakusunga pangano lake ukhale.

15 Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?

16 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamchititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lake, imene anathyola pangano lake, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babiloni.

17 NdipoFaraondi nkhondo yake yaikulu, ndi khamu lake launyinji, sadzachita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.

18 Pakuti anapepula lumbiro, ndi kuthyola pangano, angakhale anapereka dzanja lake; popeza anachita izi zonse sadzapulumuka.

19 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analithyola, ndidzawabweza pamutu pake.

20 Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babiloni, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwake anandilakwira nako.

21 Ndipo othawa ake onse m’magulu ake onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa kumphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.

22 Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kuiika; ndidzabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kuioka paphiri lalitali lothuvuka;

23 paphiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m’munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko aliwonse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.

24 Ndipo mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung’ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kuchichita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/17-8990e2855f87d8f3c387aac6418261f3.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 18

Udindo ndi wakewake wa munthu

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Mutani inu ndi kunena mwambi uwu za dziko la Israele, wakuti, Atate adadya mphesa zosacha, ndi mano a ana ayayamira.

3 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, simudzaonanso chifukwa cha kunena mwambiwu mu Israele.

4 Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.

5 Koma munthu akakhala wolungama, nakachita chiweruzo ndi chilungamo,

6 wosadya pamapiripo, wosakweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,

7 wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,

8 wosapereka molira phindu, wosatenga choonjezerapo wobweza dzanja lake lisachite chosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzake,

9 amayenda m’malemba anga, nasunga maweruzo anga kuchita chokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova.

10 Akabala mwana ndiye mkhungu, wokhetsa mwazi, wochita chimodzi cha izi,

11 wosachita zabwino zonse zija, koma anadyanso pamapiri, naipsa mkazi wa mnansi wake,

12 nasautsa osauka ndi osowa, natenga zofunkha, wosabwezera chigwiriro, nakweza maso ake kumafano, nachita chonyansa,

13 napereka molira phindu, nalandira choonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? Sadzakhala ndi moyo, anachita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, mwazi wake umkhalira.

14 Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zochimwa zonse adazichita atate wake, naopa wosachita zoterezo,

15 wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake,

16 kapena kusautsa wina aliyense, wosatenga chigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,

17 naletsa dzanja lake pa wozunzika, wosalandira phindu kapena choonjezerapo, wochita maweruzo anga, nayenda m’malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wake, adzakhala ndi moyo ndithu.

18 Atate wake, popeza anazunza chizunzire, nafunkha za mbale wake, nachita chimene sichili chabwino pakati pa anthu ake, taona, adzafa mu mphulupulu yake.

19 Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wake? Mwanayo akachita chiweruzo ndi chilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwachita, adzakhala ndi moyo ndithu.

20 Moyo wochimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; chilungamo cha wolungama chidzamkhalira, ndi choipa cha woipa chidzamkhalira,

21 Koma woipayo akabwerera kusiya machimo ake onse adawachita nakasunga malemba anga onse, ndi kuchita chiweruzo ndi chilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

22 Nnena chimodzi chonse cha zolakwa zake zonse adazichita chidzakumbukika chimtsutse; m’chilungamo chake adachichita adakhala ndi moyo.

23 Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?

24 Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m’kulakwa kwake analakwa nako, ndi m’kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa.

25 Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israele, Kodi njira yanga njosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?

26 Wolungamayo akatembenukira kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, adzafa momwemo; m’mphulupulu yake adaichita adzafa.

27 Ndipo woipayo akatembenukira kuleka choipa chake adachichita, nakachita chiweruzo ndi chilungamo, adzapulumutsa moyo wake.

28 Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zake zonse adazichita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

29 Koma nyumba ya Israele imanena, Njira ya Ambuye njosayenera. Inu, nyumba ya Israele, kodi njira zanga nzosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?

30 Chifukwa chake ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israele, yense monga mwa njira zake, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.

31 Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?

32 Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; chifukwa chake bwererani, nimukhale ndi moyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/18-0ada652a499ae2f94e22320e83a43101.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 19

Fanizo la mkango waukazi, ndi la mpesa

1 Ndipo iwe, takwezera akalonga a Israele nyimbo ya maliro,

2 uziti, Mai wako ndi chiyani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ake pakati pa misona.

3 Ndipo unalera mmodzi wa ana ake, iye nasanduka msona, unaphunzira kugwira nyama, unalusira anthu.

4 Mitundu ya anthu idamva mbiri yake, unagwidwa m’mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera kudziko la Ejipito.

5 Pakuona tsono waukaziwo, kuti unalindirira, ndi kuti chiyembekezo chake chidatha, unatenga wina wa ana ake, numsandutsa msona.

6 Ndipo unayendayenda pakati pa mikango, nukhala msona, nuphunzira kugwira nyama, nulusira anthu.

7 Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula mizinda yao, ndipo dziko ndi kudzala kwake linasanduka labwinja, chifukwa cha phokoso la kubangula kwake.

8 Pamenepo mitundu ya anthu inadzipereka kuukola kuchokera kumaiko a kumbali zonse, niuphimba ndi ukonde wao, nugwidwa uwu m’mbuna mwao.

9 Nauika m’chitatanga ndi zokowera, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni; anaulonga m’malinga, kuti mau ake asamvekenso pa mapiri a Israele.

10 Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri.

11 Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zachifumu, za ochita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, ndipo zinaoneka m’kusomphoka kwao pakati pa nthambi zake zambiri.

12 Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum’mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha.

13 Ndipo tsopano waokedwa m’chipululu m’dziko louma ndi la ludzu.

14 Unatulukanso moto kundodo za kunthambi zake, unatha zipatso zake; m’mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yachifumu ya kuchita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/19-13f826a7a8eed27f6f6df022ee53cead.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 20

Machimo a Aisraele chitulukire iwo m’dziko la Ejipito

1 Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chiwiri, mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israele kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.

2 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

3 Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.

4 Udzawaweruza kodi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzawaweruza? Uwadziwitse zonyansa za makolo ao,

5 nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israele, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m’dziko la Ejipito, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu;

6 tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m’dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;

7 ndipo ndinanena nao, Aliyense ataye zonyansa za pamaso pake, nimusadzidetsa ndi mafano a Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

8 Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m’dziko la Ejipito.

9 Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso paamitunduamene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m’dziko la Ejipito.

10 Momwemo ndinatuluka nao m’dziko la Ejipito, ndi kulowa nao kuchipululu.

11 Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.

12 Ndipo ndinawapatsansomasabataanga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.

13 Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m’chipululu, sanayende m’malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m’chipululu kuwatha.

14 Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.

15 Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m’chipululu, kusawalowetsa m’dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;

16 popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m’malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.

17 Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawathe onse m’chipululu.

18 Ndipo ndinati kwa ana ao m’chipululu, Musamayenda m’malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;

19 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m’malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita;

20 muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

21 Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m’malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m’chipululu.

22 Koma ndinabweza dzanja langa ndi kuchichita, chifukwa cha dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawatulutsa pamaso pao.

23 Ndinawakwezeranso dzanja langa m’chipululu, kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m’maiko;

24 popeza sanachite maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.

25 Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo;

26 ndinawadetsanso m’zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.

27 Chifukwa chake wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa ichinso atate anu anandichitira mwano pakundilakwira Ine.

28 Nditafika nao m’dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.

29 Pamenepo ndinanena nao, Msanje wotani uwu mumapitako? Momwemo dzina lake litchedwa Msanje, mpaka lero lino.

30 Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anachitira makolo anu? Muchita chigololo kodi kutsata zonyansa zao?

31 Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;

32 ndi ichi chimauka mumtima mwanu sichidzachitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m’maiko, kutumikira mtengo ndi mwala.

Mulungu adzabweza Israele kuchokera kubalalikidwa iwo

33 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu.

34 Ndipo ndidzakutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani m’maiko munabalalikamo ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa.

35 Ndipo ndidzalowa nanu m’chipululu cha mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso.

36 Monga ndinaweruza makolo anu m’chipululu cha dziko la Ejipito, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.

37 Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m’chimango chachipangano;

38 ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m’dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m’dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

39 Ndipo inu, nyumba ya Israele, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ake, ndi m’tsogolo momwe, popeza simundimvere Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.

40 Pakuti paphiri langa lopatulika, paphiri lothuvuka la Israele, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israele, onsewo adzanditumikira Ine m’dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse.

41 Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m’maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.

42 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m’dziko la Israele, m’dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu.

43 Ndi pomwepo mudzakumbukira njira zanu, ndi zonse mudazichita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, chifukwa cha zoipa zanu zonse mudazichita.

44 M’mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditachita nanu chifukwa cha dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa machitidwe anu ovunda, nyumba ya Israele inu, ati Ambuye Yehova.

45 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

46 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango yakuthengo la kumwera kwa Yuda;

47 nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uliwonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uliwonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.

48 Ndi anthu onse adzaona kuti Ine Yehova ndinauyatsa, sudzazimika.

49 Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/20-0c8be4710d7500d5d2c1113cd1f4b867.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 21

Lupanga la Yehova

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kuYerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israele kulitsutsa;

3 nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m’chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.

4 Popeza ndidzakulikhira olungama ndi oipa, chifukwa chake lupanga langa lidzasololokera anthu onse, kuyambira kumwera kufikira kumpoto;

5 ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupanga langa m’chimake, silidzabwereranso.

6 Koma wobadwa ndi munthu iwe, usa moyo, ndi kuduka msana, ndi kuwawa mtima, uuse moyo pamaso pao.

7 Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo chifukwa ninji? Uzikati, Chifukwa cha mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uliwonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uliwonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona ilinkudza, inde idzachitika, ati Ambuye Yehova.

8 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

9 Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Ambuye, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso;

10 lanoledwa kuti liphetu, lituulidwa kuti linge mphezi; tisekererepo kodi? Ndilo ndodo yachifumu ya mwana wanga, yopeputsa mtengo uliwonse.

11 Ndipo analipereka alituule, kuti achite nalo lupangali analinola, inde analituula kulipereka m’dzanja la wakupha.

12 Fuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israele, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; chifukwa chake panda pantchafu pako.

13 Pakuti pali kuyesedwa; ndipo nanga ndodo yachifumu yopeputsa ikapanda kukhalanso? Ati Ambuye Yehova.

14 Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitilize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuluyo, limene liwazinga.

15 Ndalozetsa nsonga ya lupanga kuzipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kuchuluke; ha! Analituula linyezimire, analisongoza liphe.

16 Udzisonkhanitsire pamodzi, muka kudzanja lamanja; undandalitsa nkhondo kumuka kulamanzere; kulikonse ilozako nkhope yako.

17 Inenso ndidzaomba manja anga, ndipo ndidzakukwaniritsa ukali wanga; Ine Yehova ndanena.

18 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

19 Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babiloni; zonse ziwiri zichokere dziko lomwelo; nulembe chizindikiro cholozera, uchilembe pa mphambano ya njira ya kumzinda.

20 Uiike njira yodzera lupanga kunka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.

21 Pakuti mfumu ya ku Babiloni aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mivi, afunsira kwaaterafi, apenda ndi chiwindi.

22 M’dzanja lake lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kufuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga.

23 Ndipo kudzakhala ngati kuombeza konyenga pamaso pa iwo amene anawalumbirira malumbiro; koma akumbutsa mphulupulu kuti akodwe.

24 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwakumbutsa mphulupulu yanu povumbuluka zolakwa zanu, kotero kuti machimo anu aoneka m’zonse muzichita, popeza mukumbukika, mudzagwidwa ndi dzanja.

25 Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israele, amene lafika tsiku lako, nthawi ya mphulupulu yotsiriza;

26 atero Ambuye Yehova, Chotsa chilemba, vula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza chopepuka, chepsa chokwezeka.

27 Ndidzagubuduzagubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.

28 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za chitonzo chao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.

29 Akuonera zopanda pake, akuombezera mabodza, lupanga likugoneka pa makosi a oipa olasidwa, amene lafika tsiku lao nthawi ya mphulupulu yotsiriza.

30 Ulibwezere m’chimake. Pamalo unalengedwapo m’dziko la kubadwa kwako ndidzakuweruza.

31 Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m’manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga.

32 Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati padziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndachinena.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/21-1ec8b6245e509ec6be31328feaec9044.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 22

Machimo oopsa a Yerusalemu

1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzaweruza, udzauweruza mzindawo wa mwazi kodi? Uudziwitse tsono zonyansa zake zonse.

3 Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mzinda wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao.

4 Wapalamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zakozako; chifukwa chake ndakuika ukhale chitonzo chaamitundundi choseketsa cha maiko onse.

5 Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera.

6 Taona akalonga a Israele, yense monga mwa mphamvu yake, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi.

7 Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.

8 Wanyoza zopatulika zanga, waipsamasabataanga.

9 Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.

10 Anavula umaliseche wa atate ao mwa iwe, mwa iwe anachepsa wodetsedwa ndi kooloka kwake.

11 Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.

12 Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.

13 Taona, ndaomba manja pa phindu lako lonyenga waliona, ndi pa mwazi wokhala pakati pako.

14 Mtima wako udzaimika kodi, manja ako adzalimbikira masikuwo ndidzachita nawe? Ine Yehova ndanena, ndidzachichita.

15 Ndipo ndidzakumwaza mwa amitundu, ndi kukubalalitsa m’maiko, ndi kukuthera zodetsa zako zikuchokere.

16 Ndipo udzaipsidwa mwa iwe wekha pamaso pa amitundu; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

17 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

18 Wobadwa ndi munthu iwe, nyumba ya Israele yandikhalira mphala; onsewo ndiwo mkuwa, ndi seta, ndi chitsulo, ndi ntovu, m’kati mwa ng’anjo; ndiwo mphala zasiliva.

19 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwasanduka mphala nonsenu, chifukwa chake taonani, ndidzakusonkhanitsani m’kati mwaYerusalemu.

20 Monga asonkhanitsa mtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi ntovu, ndi seta, m’kati mwa ng’anjo, kuzivukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani.

21 Inde ndidzakusonkhanitsani, ndi kukuvukutirani ndi moto wa kuzaza kwanga, ndipo mudzasungunuka pakati pake.

22 Monga siliva asungunuka m’kati mwa ng’anjo, momwemo inu mudzasungunuka m’kati mwake; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga.

23 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

24 Wobadwa ndi munthu iwe, nena ndi Yuda, Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, losavumbwa mvula tsiku la ukalilo.

25 Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake.

26 Ansembe ake achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.

27 Akalonga ake m’kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.

28 Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pake, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova, posanena Yehova.

29 Anthu a m’dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa.

30 Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.

31 Chifukwa chake ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yaoyao ndinaibweza pamutu pao, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/22-d8a722121f0f014f8f1aec44f2bcb03d.mp3?version_id=1068—