Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 3

1 Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya chimene wachipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israele.

2 Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndipo anandidyetsa mpukutuwo.

3 Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m’mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M’mwemo ndinaudya, ndi m’kamwa mwanga munazuna ngati uchi.

4 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Muka, nufike kwa nyumba ya Israele, nunene nao mau anga.

5 Pakuti sutumizidwa kwa anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, koma kwa nyumba ya Israele;

6 si kwa mitundu yambiri ya anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, amene sungathe kudziwitsa chinenedwe chao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe.

7 Koma nyumba ya Israele siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israele ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.

8 Taona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zao; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yao.

9 Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

10 Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m’mtima mwako, utawamva m’makutu mwako.

11 Numuke, nufike kwa andende kwa ana a anthu a mtundu wako, nunene nao ndi kuwauza, Atero Yehova Mulungu, ngakhale akamva kapena akaleka kumva.

12 Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukulu, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m’malo mwake.

13 Ndipo ndinamva mkokomo wa mapiko a zamoyozo pakukhudzana, ndi mlikiti wa njingazo m’mbali mwa izo, ndilo phokoso la mkokomo waukulu.

14 M’mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.

15 Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako wodabwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.

Mlonda wa Israele

16 Ndipo kunali atatha masiku asanu ndi awiri, mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,

17 Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israele, m’mwemo mvera mau otuluka m’kamwa mwanga, nundichenjezere iwo.

18 Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, wosanena kumchenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna padzanja lako.

19 Koma ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako.

20 Momwemonso akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, ndi kuchita chosalungama, ndipo ndikamuikira chomkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamchenjeze, adzafa m’tchimo lake, ndi zolungama zake adazichita sizidzakumbukika; koma mwazi wake ndidzaufuna padzanja lako.

21 Koma ukamchenjeza wolungamayo, kuti asachimwe wolungamayo, ndipo sachimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anachenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.

22 Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, tuluka kunka kuchidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.

23 Ndipo ndinauka ndi kutuluka kunka kuchidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona kumtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.

24 Pamenepo unandilowa mzimu ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo analankhula ndi ine, nanena nane, Muka, katsekedwe m’nyumba mwako.

25 Koma iwe wobadwa ndi munthu, taona, adzakuikira iwe zingwe zolimba, nadzakumanga nazo, ndipo sudzatuluka pakati pao;

26 ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

27 Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wosafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/3-a22541549787c5f2cb85151df2f9bdd4.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 4

Aneneratu mophiphiritsa za kumangidwa misasa Yerusalemu

1 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, dzitengere njerwa, nuiike pamaso pako, nulembepo mzinda, ndiwoYerusalemu;

2 nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pake.

3 Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele.

4 Ndipo iwe ugonere pansi mbali yako ya kumanzere, nuikepo mphulupulu ya nyumba ya Israele; monga mwa kuwerenga kwa masiku amene udzagonapo udzasenza mphulupulu yao.

5 Ndipo Ine ndakuikira zaka za mphulupulu yao ngati masiku, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai, kuti usenze mphulupulu ya nyumba ya Israele.

6 Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi.

7 Ndipo ulozetse nkhope yako kuzingidwa kwake kwa Yerusalemu, ndi dzanja lako losafundika, nuunenere.

8 Ndipo taona ndidzakumanga ndi zingwe zolimba kuti usakunkhulire, mpaka watsiriza masiku a kuzingidwa kwako.

9 Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m’mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai,

10 Ndipo chakudya chako uzichidya chiyesedwe masekeli makumi awiri tsiku limodzi; uzidyako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake.

11 Uzimwanso madzi monga mwa muyeso, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la hini; uzimwako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake.

12 Ndipo uzichidya ngati timikate ta barele, ndi kutiocha pamaso pao ndi zonyansa za munthu.

13 Ndipo Yehova anati, Motero ana a Israele adzadya chakudya chao chodetsedwa, mwaamitundukumene ndidzawaingitsirako.

14 Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m’kamwa mwanga nyama yonyansa.

15 Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng’ombe m’malo mwa zonyansa za munthu, uotche mkate wako pamenepo.

16 Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzathyola mchirikizo, ndiwo chakudya, mu Yerusalemu; ndipo adzadya chakudyacho monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;

17 kuti asowe chakudya ndi madzi, nasumwesumwe, naondetse mu mphulupulu zao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/4-80727d0cad26107c1d853d419941572b.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 5

1 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndevu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo.

2 Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.

3 Utengekonso owerengeka ndi kuwamanga m’mkawo wa malaya ako.

4 Nutengekonso pa amenewa ndi kuwaponya pakati pa moto, ndi kuwatentha m’moto; kuchokera kumeneko udzatuluka moto pa nyumba yonse ya Israele.

Aneneratu za kupasuka kwa Yerusalemu

5 Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati paamitundu, ndi pozungulira pake pali maiko.

6 Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.

7 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayende m’malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawachite;

8 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kuchita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.

9 Ndipo ndidzachita mwa iwe chimene sindinachichite ndi kale lonse, ndi kusadzachitanso momwemo, chifukwa cha zonyansa zako zonse.

10 Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse.

11 M’mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, popeza wadetsa malo anga opatulika ndi zonyansa zako zonse ndi zoipsa zako zonse, ndidzakuchepsa; diso langa silidzalekerera, ndi Inenso sindidzachita chifundo.

12 Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.

13 Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m’changu changa, pokwaniridwa nao ukali wanga.

14 Ndidzakuikanso ukhale bwinja ndi chotonza pakati pa amitundu akukuzinga, pamaso pa onse akupitirirapo.

15 Momwemo chidzakhala chotonza ndi mnyozo, chilangizo ndi chodabwitsa kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikuchitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehova ndanena.

16 Pakuwatumizira Ine mivi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukuthyolerani mchirikizo, ndiwo chakudya.

17 Inde ndidzakutumizirani njala ndi zilombo, ndipo zidzakusowetsa ana ako; ndi mliri ndi mwazi zidzakugwera; ndidzakufikitsiranso lupanga; Ine Yehova ndachinena.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/5-5d4cb66c79e4f5f42467e2d46b52df7d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 6

Aneneratu motsutsa mapiri a Israele

1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kumapiri a Israele, uwanenere,

3 nunene, Mapiri a Israele inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu.

4 Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.

5 Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israele pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.

6 Pokhala inu ponse mizinda idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi ntchito zanu zifafanizidwe.

7 Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

8 Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwaamitundupobalalitsidwa inu m’maiko maiko.

9 Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m’zonyansa zao zonse.

10 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanene chabe kuti ndidzawachitira choipa ichi.

11 Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, chifukwa cha zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israele; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.

12 Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wokhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga.

13 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.

14 Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa chipululu cha ku Ribula mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/6-82040e3b617ac479a72203a6dcf6a05b.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 7

Kutha kwake kwa dziko la Israele

1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

2 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israele, Kwatha; kwafika kutha kwake pangodya zinai za dziko.

3 Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.

4 Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzachita chifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

5 Atero Yehova Mulungu, Choipa, choipa cha pa chokha, taona chilinkudza.

6 Kutha kwafika, kwafika kutha. Kwakugalamukira, taona kwafika.

7 Tsoka lako lakufikira, nzika iwe, yafika nthawi, tsiku lili pafupi, ndilo laphokoso, si lakufuula mokondwera kumapiri.

8 Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.

9 Ndipo diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.

10 Taona, tsikuli, taona, lafika; tsoka lako latuluka, ndodo yaphuka mphundu za maluwa, kudzitama kwaphuka.

11 Chiwawa chauka chikhale ndodo ya choipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa chuma chao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.

12 Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve chisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wonse.

13 Pakuti wogulitsa sadzabwera ku chogulitsacho, chinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wake wonse sadzapita pachabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wake m’mphulupulu yake.

14 Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wake wonse.

15 Kunja kuli lupanga, ndi m’katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m’mzindawo njala ndi mliri zidzamutha.

16 Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m’mphulupulu zake.

17 Manja onse adzalenda, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi.

18 Ndipo adzadzimangira m’chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi.

19 Adzatayasilivawao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao.

20 Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa.

21 Ndipo ndidzachipereka m’dzanja la alendo chikhale cholandika, ndi kwa oipa a m’dziko chikhale chofunkha; ndipo adzachiipsa.

22 Ndipo nkhope yanga idzawayang’anira kumbali, ndipo iwo adzadetsa pobisika panga, nadzalowamo achifwamba, nadzamudetsa.

23 Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi milandu yamwazi, ndi mzinda wadzala ndi chiwawa.

24 Chifukwa chake ndidzabwera naoamitunduoipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.

25 Chionongeko chilinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe.

26 Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya amneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.

27 Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzavala chipasuko, ndi manja a anthu a m’dziko adzanjenjemera. Ndidzawachitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/7-dbc33ede877ae5018e0d32f964cb5abe.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 8

Masomphenya a zoipitsitsa za mu Kachisi

1 Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chimodzi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, tsiku lachisanu la mweziwo, pokhala ine m’nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko.

2 Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, chifaniziro cha maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m’chuuno mwake ndi kunsi kwake, moto; ndi kuyambira m’chuuno mwake ndi kumwamba kwake, monga maonekedwe a cheza, ngati chitsulo chakupsa.

3 Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati padziko ndi thambo, numuka nane m’masomphenya a Mulungu kuYerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m’katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje.

4 Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa Israele, monga mwa maonekedwe ndinawaona kuchidikha chija.

5 Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako kunjira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga kunjira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa chipata cha guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pake.

6 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.

7 Ndipo anadza nane kuchipata cha kubwalo, ndipo popenya ine, taonani, pobooka palinga.

8 Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, booletsa kulinga; ndipo nditabooletsa palinga, ndinaona khomo.

9 Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzichita komweko.

10 M’mwemo ndinalowa ndi kupenya, ndipo taonani, maonekedwe ali onse a zokwawa, ndi zilombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israele, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse.

11 Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m’dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.

12 Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m’chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.

13 Anatinso kwa ine, Udzaonanso zonyansa zazikulu zina azichita.

14 Pamenepo anadza nane kuchitseko cha chipata cha nyumba ya Yehova choloza kumpoto; ndipo taonani, apo panakhala akazi akulirira Tamuzi.

15 Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzaonanso zonyansa zazikulu zoposa izi.

16 Ndipo anadza nane ku bwalo lam’kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang’ana kum’mawa, napembedza dzuwa kum’mawa.

17 Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.

18 Chifukwa chake Inenso ndidzachita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawachitira chifundo Ine; ndipo chinkana afuula m’makutu mwanga ndi mau aakulu, koma sindidzawamvera Ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/8-e4ba243ff4895848bd14b8adcb5e6125.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 9

Malango a pa ochimwa

1 Pamenepo Iye anafuula m’makutu mwanga ndi mau aakulu, ndi kuti, Asendere oyang’anira mzinda, aliyense ndi chida chake choonongera m’dzanja lake.

2 Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya chipata cha kumtunda choloza kumpoto, aliyense ndi chida chake chophera m’dzanja lake; ndi munthu mmodzi pakati pao wovala bafuta, ndi zolembera nazo m’chuuno mwake. Ndipo analowa, naima m’mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.

3 Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israele unakwera kuchoka pakerubi, pamene unakhalira kunka kuchiundo cha nyumba, naitana munthu wovala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m’chuuno mwake.

4 Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mzinda, pakati paYerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.

5 Nati kwa enawo, ndilikumva ine, Pitani pakati pa mzinda kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musachite chifundo;

6 iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.

7 Nati kwa iwo, Muipse nyumbayi ndi kudzaza mabwalo ndi ophedwa, mukani. Ndipo anatuluka, nakantha m’mzindamo.

8 Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula, ndi kuti, Kalanga ine, Ambuye Mulungu! Kodi mudzaononga otsala onse a Israele pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?

9 Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mzindawo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.

10 Ndipo Inenso diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, koma ndidzawabwezera njira yao pamutu pao.

11 Ndipo taonani, munthu wovala bafutayo, wokhala ndi zolembera nazo m’chuuno mwake, anabweza mau, ndi kuti, Ndachita monga munandilamulira ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/9-21cb3082e288211a99b5da53b633bfca.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 10

Masomphenya a akerubi

1 Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kuthambo lokhala pamwamba pa mitu yaakerubikudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a chifaniziro cha mpando wachifumu pamwamba pao.

2 Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wovala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makala a moto ochokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mzinda. Nalowa, ndili chipenyere ine.

3 Tsono akerubi anaima kudzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzaza bwalo la m’kati.

4 Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchokera kukerubi kunka kuchiundo cha nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi cheza cha ulemerero wa Yehova.

5 Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.

6 Ndipo kunali pomlamulira munthu wovala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m’mbali mwa njinga.

7 Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lake pakati pa akerubi kumoto uli pakati pa akerubi, napalako, nauika m’manja mwa iye wovala bafuta, ndiye naulandira, natuluka.

8 Ndipo panaoneka pa akerubi chonga dzanja la munthu pansi pa mapiko ao.

9 Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m’mbali mwa akerubi, njinga imodzi m’mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga ina m’mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo.

10 Ndipo maonekedwe ake, zonse zinai zinafanana, ngati njinga ziwiri zopingasitsana.

11 Pakuyenda akerubi anayenda kumbali zao zinai, sanatembenuke poyenda; koma komwe udalozako mutu anatsatako, sanatembenuke poyenda.

12 Ndipo thupi lao lonse, ndi misana yao, ndi manja ao, ndi mapiko ao, ndi njinga zomwe, zinadzala ndi maso pozungulira pao, zingakhale njingazi anai aja anali nazo.

13 Kunena za njingazi, wina anazifuulira, ndili chimvere ine, Kunkhulirani.

14 Ndipo aliyense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yachiwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yachitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yachinai ndiyo nkhope ya chiombankhanga.

15 Pamenepo akerubi anakwera, ndizo zamoyo zija ndinaziona kumtsinje Kebara.

16 Ndipo pakuyenda akerubi, njinga zinayenda pambali pao, ndi pakutambasula mapiko ao akerubiwo kuuluka padziko, njingazi sizinatembenuke pambali pao.

17 Pakuima iwo zinaima izi, ndi pakukwera iwo izi zinakwera pamodzi nao; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mwa izo.

18 Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiundo cha nyumba, nuima pamwamba pa akerubi.

19 Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndili chipenyere, pakuchoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa chitseko cha chipata cha kum’mawa cha nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.

20 Awa ndi zamoyozo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israele kumtsinje Kebara, ndipo ndinadziwa kuti ndiwo akerubi.

21 Yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense mapiko anai, ndi chifaniziro cha manja a munthu pansi pa mapiko ao.

22 Ndi chifaniziro cha nkhope zao ndicho nkhope zomwezo ndinaziona kumtsinje Kebara, maonekedwe ao ndi iwo eni; aliyense anayenda, nalunjika m’tsogolo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/10-d459c63013bae8a7fe7fc5cf88dcf3da.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 11

Chiweruzo cha Mulungu pa mafumu a Ayuda

1 Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane kuchipata cha kum’mawa cha nyumba ya Yehova choloza kum’mawa; ndipo taonani, pa chitseko cha chipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.

2 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m’mzinda muno;

3 ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mzinda uwu ndi mphika, ife ndife nyama.

4 Chifukwa chake uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.

5 Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo anati kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israele, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m’mtima mwanu.

6 Mwachulukitsa ophedwa anu m’mzinda muno, mwadzazanso makwalala ake ndi ophedwawo.

7 Chifukwa chake atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m’kati mwake, iwo ndiwo nyama imene, ndi mzinda uwu ndiwo mphika; koma inu mudzatulutsidwa m’kati mwake.

8 Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.

9 Ndipo ndidzakutulutsani m’kati mwake, ndi kukuperekani m’manja a alendo, ndi kuchita maweruzo pakati panu.

10 Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

11 Mzinda uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m’kati mwake, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele;

12 ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayende m’malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, koma mwachita monga mwa maweruzo aamitunduokhala pozungulira panu.

13 Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula ndi mau aakulu, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu? Mudzatsiriza kodi otsala a Israele?

14 Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti,

15 Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako aamuna a chibale chako, ndi nyumba yonse ya Israele, yonseyi ndiwo amene okhala muYerusalemuananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale cholowa chathu;

16 chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawachotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m’maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi kumaiko adafikako.

17 Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m’maiko m’mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele.

18 Ndipo adzafikako, nadzachotsako zonyansa zake zonse, ndi zake zonse zakuipitsamo.

19 Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m’kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m’thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;

20 kuti ayende m’malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.

21 Koma iwo amene mtima wao unatsata mtima wa zonyansa zao, ndi zoipitsitsa zao, ndidzawabwezera njira yao pamutu pao, ati Yehova Mulungu.

22 Pamenepoakerubianatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.

23 Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchoka pakati pa mzinda, nuima paphiri la kum’mawa kwa mzinda.

24 Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m’masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M’mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.

25 Pamenepo ndinanena ndi andendewo zonse zija adandionetsa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/11-cbb910feacce70f66beedaa88604a47b.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 12

Khoma labooledwa lofanizira ukapolo ndi ubalaliko wao

1 Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.

3 Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nuchoke usana pamaso pao, uchoke pokhala iwepo kunka malo ena pamaso pao; kapena adzachizindikira, angakhale ndiwo nyumba yopanduka.

4 Uzitulutsa akatundu ako usana pamaso pao, ngati a pa ulendo wa kundende; ndipo madzulo uzituluka wekha pamaso pao, monga amatuluka olowa kundende.

5 Udziboolere khoma pamaso pao, nuwatulutsire akatundu pamenepo.

6 Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwatulutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika chizindikiro cha nyumba ya Israele.

7 Ndipo ndinachita monga momwe anandilamulira, ndinatulutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawatulutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso pao.

8 Ndipo m’mawa mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,

9 Wobadwa ndi munthu iwe, kodi nyumba ya Israele, nyumba yampanduko, siinati kwa iwe, Uchitanji?

10 Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Katundu uyu anena za kalonga wa muYerusalemu, ndi nyumba yonse ya Israele yokhala pakati pao.

11 Uziti, Ine ndine chizindikiro chanu, monga ndachita ine momwemo kudzachitidwa nao; adzachotsedwa kunka kundende.

12 Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pake mumdima, nadzatuluka; adzaboola palinga, nadzatulutsapo; adzaphimba nkhope yake kuti asapenye dziko ndi maso ake.

13 Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.

14 Ndipo onse omzinga kumthandiza, ndi magulu ake onse, ndidzawamwaza kumphepo zonse, ndidzawasololeranso lupanga lakuwatsata.

15 Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwaamitundu, ndi kuwabalalitsa m’maiko.

16 Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

17 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

18 Wobadwa ndi munthu iwe, udye mkate wako ndi kunthunthumira, ndi kumwa madzi ako ndi kunjenjemera, ndi kutenga nkhawa;

19 nunene kwa anthu a m’dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala mu Yerusalemu, ndi za dziko la Israele, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lachipululu, kuleka kudzala kwake chifukwa cha chiwawa cha onse okhalamo.

20 Ndi mizinda yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Aneneratu kutsutsa aneneri onama

21 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

22 Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m’dziko la Israele, wakuti, Masiku achuluka, ndi masomphenya ali onse apita pachabe?

23 Chifukwa chake unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzautchulanso mwambi mu Israele; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzachitika masomphenya ali onse.

24 Pakuti sikudzakhalanso masomphenya achabe, kapena ula wosyasyalika m’nyumba ya Israele.

25 Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m’masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu.

26 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

27 Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israele akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri; ndipo anenera za nthawi zili kutali.

28 Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/12-f748c86ff27bd295330b9a89b3c5537e.mp3?version_id=1068—