Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 52

Yerusalemu amangidwa misasa, nalandidwa, napasulidwa

1 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza chimodzi pamene analowa ufumu wake; ndipo analamulira muYerusalemuzaka khumi kudza chimodzi; dzina la amake ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.

2 Ndipo iye anachita zoipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse anazichita Yehoyakimu.

3 Pakuti zonse zinachitika mu Yerusalemu ndi mu Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mpaka anawachotsa pamaso pake; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babiloni.

4 Ndipo panaoneka chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anafika, iye ndi nkhondo yake, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zithando; ndipo anammangira malinga pozungulira pake.

5 Ndipo mzinda unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha mfumu Zedekiya.

6 Mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, njala inavuta m’mzinda, ndipo anthu a m’dziko analibe zakudya.

7 Pamenepo anaboola mzinda, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m’mzinda usiku panjira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pamunda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mzinda pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha.

8 Koma nkhondo ya Ababiloni inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m’zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yake yonse inambalalikira iye.

9 Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m’dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza.

10 Ndipo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya pamaso pake; niphanso akulu onse a Yuda mu Ribula.

11 Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, ndipo mfumu ya ku Babiloni inammanga m’zigologolo, nimtengera ku Babiloni, nimuika m’ndende mpaka tsiku la kufa kwake.

12 Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa mu Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:

13 ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.

14 Ndipo nkhondo yonse ya Ababiloni, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pake.

15 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m’mzinda, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babiloni, ndi otsala a unyinjiwo.

16 Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m’minda.

17 Ndi mizati yamkuwa imene inali m’nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m’nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, nanka nao mkuwa wake wonse ku Babiloni.

18 Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa.

19 Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikaponyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golide, wa zija zagolide, ndisiliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazichotsa.

20 Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng’ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomoni anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanathe kuyesa kulemera kwake.

21 Koma nsanamirazo, utali wake wa nsanamira ina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi chingwe cha mikono khumi ndi iwiri chinaizinga; kuchindikira kwake kunali zala zinai; inali yagweregwere.

22 Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pake; utali wake wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi sefa ndi makangaza pakorona pozungulira pake, onse amkuwa: nsanamira inzake yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.

23 Ndipo pambali pake panali makangaza makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi limodzi; ndipo makangaza onse anali zana limodzi pamade pozungulira pake.

24 Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi akudikira pakhomo atatu;

25 ndipo m’mzinda anatenga kazembe amene anali woyang’anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m’mzinda; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m’dziko; ndi amuna makamu asanu ndi limodzi a anthu a m’dziko, amene anapezedwa pakati pa mzinda.

26 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula.

27 Ndipo mfumu ya ku Babiloni anawakantha, nawapha pa Ribula m’dziko la Hamati. Chomwecho Yuda anatengedwa ndende kutuluka m’dziko lake.

28 Amenewa ndi anthu amene Nebukadinezara anatenga ndende: chaka chachisanu ndi chiwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu;

29 chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara iye anatenga ndende kuchokera mu Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;

30 chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Nebukadinezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

31 Ndipo panali chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namtulutsa iye m’ndende;

32 nanena naye bwino, naika mpando wake upose mipando ya mafumu amene anali naye mu Babiloni.

33 Ndipo anapindula zovala zake za m’ndende, ndipo sanaleke kudya pamaso pake masiku onse a moyo wake.

34 Koma phoso lake mfumu ya ku Babiloni sanaleke kumpatsa, phoso tsiku ndi tsiku gawo lake, mpaka tsiku la kufa kwake, masiku onse a moyo wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/52-e8eb32e595d971e54a46f0c28857ea45.mp3?version_id=1068—

Categories
MALIRO

MALIRO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mau a m’bukuli ali ngati ndakatulo zolira chifukwa cha kupasuka kwa Yerusalemu ndi mavuto aakulu a ukapolo, zimene zidachitika m’chaka cha 586 BC. Mau ake ndi achisoni ndi odandaula, komabe mauwo aonetsanso mtima wokhulupirira Mulungu poyembekeza kuti adzakhalanso pabwino nthawi yake itakwana. Ayuda akhala akugwiritsabe ntchito ndakatulo zimenezi pa chipembedzo mpaka lero, pa masiku okumbukira kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu m’chaka cha 586 BC.

Za mkatimu

Zomumvetsa chisoni Yerusalemu

1.1-22

Chilango chogwera mzindawo

2.1-22

Yerusalemu azunzika, alapa ndipo ayembekeza chikhululukiro

3.1-66

Yerusalemu wasanduka bwinja

4.1-22

Pemphero lopempha chikhululukiro

5.1-22

Categories
MALIRO

MALIRO 1

Tsoka la Yerusalemu

1 Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha!

Ukunga mkazi wamasiye!

Waukuluwo mwaamitundu, kalonga wamkazi m’madera a dziko

wasanduka wolamba!

2 Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake;

mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza:

Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu,

asanduka adani ake.

3 Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu;

akhala mwa amitundu, sapeza popuma;

onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.

4 M’njira zaZiyonimulira posoweka akudzera msonkhano;

pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo;

anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.

5 Amaliwongo ake asanduka akulu ake, adani ake napindula;

pakuti Yehova wamsautsa pochuluka zolakwa zake;

ana ake aang’ono alowa m’ndende pamaso pa adani ake.

6 Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni;

akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa,

anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa.

7 M’masiku a msauko wake ndi kusochera kwake

Yerusalemuukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire;

pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,

mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake.

8 Yerusalemu wachimwa kwambiri;

chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa;

onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche;

inde, uusa moyo, nubwerera m’mbuyo.

9 Udyo wake unali m’nsalu zake;

sunakumbukire chitsiriziro chake;

chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;

taonani, Yehova, msauko wanga,

pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.

10 Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse;

pakuti waona amitundu atalowa m’malo ake opatulika,

amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.

11 Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate;

ndi zokondweretsa zao agula zakudya

kuti atsitsimutse moyo wao;

taonani, Yehova, nimupenye;

pakuti ndasanduka wonyansa.

12 Kodi muyesa chimenechi chabe,

nonsenu opita panjira?

Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china

ngati changachi amandimvetsa ine,

chimene Yehova wandisautsa nacho

tsiku la mkwiyo wake waukali?

13 Anatumiza moto wochokera kumwamba

kulowa m’mafupa anga, unawagonjetsa;

watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m’mbuyo;

wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.

14 Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake;

zalukidwa, zakwera pakhosi panga;

iye wakhumudwitsa mphamvu yanga;

Ambuye wandipereka m’manja mwao, sindithai kuwagonjetsa.

15 Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga;

waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga,

Ambuye wapondereza namwaliyo,

mwana wamkazi wa Yuda,

monga mopondera mphesa.

16 Chifukwa cha zimenezi ndilira;

diso langa, diso langatu likudza madzi:

Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira;

ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.

17 Ziyoni atambasula manja ake, palibe wakumtonthoza;

Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ake;

Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao.

18 Yehova ali wolungama;

pakuti ndapikisana ndi m’kamwa mwake;

mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu,

nimuone chisoni changa;

anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m’ndende.

19 Ndinaitana akundikondawo koma anandinyenga;

ansembe ndi akulu anga anamwalira m’mzindamu,

alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao.

20 Onani, Yehova; pakuti ndavutika,

m’kati mwanga mugwedezeka;

mtima wanga wasanduka mwa ine;

pakuti ndapikisana nanu ndithu;

kunjako lupanga limangopha ana; m’nyumba muli imfa.

21 Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza;

adani anga onse atha kumva msauko wanga,

nakondwera kuti mwatero ndinu;

mudzafikitsa tsiku lija mwalitchula,

ndipo iwowo adzanga ine.

22 Zoipa zao zonse zidze pamaso panu,

muwachitire monga mwandichitira ine

chifukwa cha zolakwa zanga zonse,

pakuti ndiusa moyo kwambiri,

ndi kulefuka mtima wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LAM/1-bbd4750281abfa0129d1115cc39d1523.mp3?version_id=1068—

Categories
MALIRO

MALIRO 2

Yerusalemu amangidwa misasa, njala isautsa, mudzi upasuka

1 Ambuye waphimbatu ndi mtambo

mwana wamkazi waZiyoni, pomkwiyira!

Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba

kukoma kwake kwa Israele;

osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.

2 Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni;

wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake;

wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.

3 Pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Israele;

wabweza m’mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo,

natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.

4 Wathifula uta wake ngati mdani,

waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo;

wapha onse okondweretsa maso;

watsanulira ukali wake ngati moto

pahema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.

5 Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele;

wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake;

nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.

6 Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m’munda;

waononga mosonkhanira mwake;

Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndiSabatamu Ziyoni;

wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.

7 Ambuye wataya guwa lake la nsembe,

malo ake opatulika amnyansira;

wapereka m’manja a adani ake makoma a zinyumba zake;

iwo anapokosera m’nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.

8 Yehova watsimikiza mtima kupasula linga

la mwana wamkazi wa Ziyoni;

watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo;

waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.

9 Zipata zake zalowa pansi;

waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake;

mfumu yake ndi akalonga ake

ali pakati paamitunduakusowa chilamulo;

inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.

10 Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;

aponya fumbi pa mitu yao,

anamangirira chiguduli m’chuuno mwao:

Anamwali a kuYerusalemuaweramitsa pansi mitu yao.

11 Maso anga alefuka ndi misozi, m’kati mwanga mugwedezeka;

chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka

kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga;

chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m’makwalala a mzindawu.

12 Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?

Pokomoka iwo ngati olasidwa m’makwalala a mzindawu,

potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.

13 Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani,

mwana wamkazi wa Yerusalemu?

Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe,

mwana wamkazi wa Ziyoni?

Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?

14 Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa;

osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,

koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.

15 Onse opita panjira akuombera manja:

Atsonya, napukusira mitu yao

pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,

kodi uwu ndi mzinda wotchedwa wokongola, wangwiro,

wokondweretsa dziko lonse?

16 Adani ako onse ayasamira pa iwe,

atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza;

ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.

17 Yehova wachita chomwe analingalira;

watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale;

wagwetsa osachitira chisoni;

wakondweretsa adani pa iwe,

wakweza nyanga ya amaliwongo ako.

18 Mtima wao unafuula kwa Ambuye,

linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni,

igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku;

usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.

19 Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda;

tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye;

takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako,

timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.

20 Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi?

Kodi akazi adzadya zipatso zao,

kunena ana amene anawalera wokha?

Kodi wansembe ndimneneriadzaphedwa

m’malo opatulika a Ambuye?

21 Wamng’ono ndi nkhalamba agona pansi m’makwalala;

anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga;

munawapha tsiku la mkwiyo wanu,

munawagwaza osachitira chisoni.

22 Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano;

panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova;

omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LAM/2-b9a4074b3874b6c6d24f0350d38f13b9.mp3?version_id=1068—

Categories
MALIRO

MALIRO 3

Yeremiya achita nkhawa, adziponya kwa Yehova

1 Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake.

2 Wanditsogolera, nandiyendetsa mumdima, si m’kuunika ai.

3 Zoonadi amandibwezerabwezera dzanja lake

monditsutsa tsiku lonse.

4 Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa,

nathyola mafupa anga.

5 Wandimangira zithando za nkhondo,

wandizinga ndi ulembe ndi mavuto.

6 Wandikhalitsa mumdima ngati akufa kale.

7 Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke;

walemeretsa unyolo wanga.

8 Inde, pofuula ine ndi kuitana andithandize

amakaniza pemphero langa.

9 Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema,

nakhotetsa mayendedwe anga.

10 Andikhalira chilombo cholalira kapena mkango mobisalira.

11 Wapambutsa njira zanga, nanding’amba; nandipululutsa.

12 Wathifula uta wake, nandiyesa polozetsa muvi.

13 Walasa impso zanga ndi mivi ya m’phodo mwake.

14 Ndasanduka wondiseka mtundu wanga wonse,

ndi nyimbo yao tsiku lonse.

15 Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa chivumulo.

16 Wathyolanso mano anga ndi tinsangalabwi,

wandikuta ndi phulusa.

17 Watalikitsanso moyo wanga ndi mtendere;

ndinaiwala zabwino.

18 Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha,

osayembekezanso kanthu kwa Yehova.

19 Kumbukirani msauko wanga ndi kusochera kwanga,

ndizo chivumulo ndi ndulu.

20 Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine.

21 Ndili nacho chiyembekezo

popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu.

22 Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova,

pakuti chisoni chake sichileka,

23 chioneka chatsopano m’mawa ndi m’mawa;

mukhulupirika ndithu.

24 Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova;

chifukwa chake ndidzakhulupirira.

25 Yehova akhalira wabwino omlindirira,

ndi moyo womfunafuna.

26 Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha

chipulumutso cha Yehova.

27 Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono.

28 Akhale pa yekha, natonthole,

pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.

29 Aike kamwa lake m’fumbi; kapena chilipo chiyembekezo.

30 Atembenuzire wompanda tsaya lake, adzazidwe ndi chitonzo.

31 Pakuti Ambuye sadzataya kufikira nthawi zonse.

32 Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni

monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake.

33 Pakuti samasautsa dala,

ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni.

34 Kupondereza andende onse a m’dziko,

35 kupambutsa chiweruzo cha munthu

pamaso pa Wam’mwambamwamba;

36 kukhotetsa mlandu wa munthu, zonsezi Ambuye sazikonda.

37 Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi,

ngati Ambuye salamulira?

38 Kodi m’kamwa mwa Wam’mwambamwamba

simutuluka zovuta ndi zabwino?

39 Kodi munthu wamoyo adandauliranji

pokhala m’zochimwa zake?

40 Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova.

41 Titukulire mitima yathu ndi manja athu omwe

kwa Mulungu ali kumwamba.

42 Ife tilakwa ndi kupikisana nanu,

ndipo Inu simunatikhululukire.

43 Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola,

mwatipha osachitira chisoni.

44 Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.

45 Mwatiika pakati paamitundu

ngati zinyalala ndi za kudzala.

46 Adani athu onse anatiyasamira.

47 Mantha ndi dzenje zitifikira, ndi phokoso ndi chionongeko.

48 M’diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi

chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa.

49 Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula,

50 kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona.

51 Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa

chifukwa cha ana aakazi onse a m’mzinda mwanga.

52 Ondida opanda chifukwa anandiinga ngati mbalame;

53 anaononga moyo wanga m’dzenje,

naponya mwala pamwamba pa ine;

54 madzi anayenda pamwamba pamutu panga,

ndinati, Ndalikhidwa.

55 Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m’dzenje lapansi;

56 munamva mau anga;

musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.

57 Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.

58 Ambuye munanenera moyo wanga milandu yake; munaombola moyo wanga.

59 Yehova, mwaona choipa anandichitiracho, mundiweruzire.

60 Mwaona kubwezera kwao konse

ndi zopangira zao zonse za pa ine.

61 Mwamva chitonzo chao, Yehova,

ndi zopangira zao zonse za pa ine,

62 milomo ya akutsutsana nane

ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.

63 Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao.

64 Mudzawabwezera chilango, Yehova,

monga mwa machitidwe a manja ao.

65 Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera;

66 mudzawalondola mokwiya

ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LAM/3-c9e87ecdbb892072838aaaf6509216cc.mp3?version_id=1068—

Categories
MALIRO

MALIRO 4

Tsoka la anthu Ayuda

1 Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika;

miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa

pa malekezero a makwalala onse.

2 Ana aZiyonia mtengo wapatali,

olingana ndi golide woyengetsa,

angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.

3 Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;

koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga

wasanduka wankhanza,

ngati nthiwatiwa za m’chipululu.

4 Lilime la mwana woyamwa limamatira

kumalakalaka kwake ndi ludzu;

ana aang’ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.

5 Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m’makwalala;

omwe analeredwa navekedwa mlangali afungatira madzala.

6 Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga,

ikula koposa tchimo la Sodomu,

umene unapasuka m’kamphindi, anthu osauchitira kanthu.

7 Omveka ake anakonzeka

koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka,

matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu;

maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.

8 Maonekedwe ao ada koposa makala,

sazindikirika m’makwalala;

khungu lao limamatira pa mafupa ao,

lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.

9 Ophedwa ndi lupanga amva bwino

kupambana ophedwa ndi njala;

pakuti amenewa angokwalika napyozedwa,

posowa zipatso za m’munda.

10 Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao;

anali chakudya chao poonongeka

mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

11 Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake;

anayatsa moto mu Ziyoni, unanyambita maziko ake.

12 Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire,

ngakhale onse okhala kunja kuno,

kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m’zipata zaYerusalemu.

13 Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri

ndi mphulupulu za ansembe ake,

amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.

14 Asochera m’makwalala ngati akhungu,

aipsidwa ndi mwazi;

anthu sangakhudze zovala zao.

15 Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu,

chokani, chokani, musakhudze kanthu.

Pothawa iwo ndi kusochera,

anthu anati kwaamitundu,

Sadzagoneranso kuno.

16 Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;

iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.

17 Maso athu athedwa, tikali ndi moyo,

poyembekeza thandizo chabe;

kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.

18 Amalondola mapazi athu, sitingayende m’makwalala athu;

chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa;

pakuti chitsiriziro chathu chafikadi.

19 Otilondola anaposa ziombankhanga

za m’mlengalenga m’liwiro lao,

anatithamangitsa pamapiri natilalira m’chipululu.

20 Wodzozedwa wa Yehova,

ndiye mpweya wa m’mphuno mwathu,

anagwidwa m’maenje ao;

amene tinanena kuti,

Tidzakhala m’mthunzi mwake pakati pa amitundu,

21 kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu,

wokhala m’dziko la Uzi;

chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso;

udzaledzera ndi kuvula zako.

22 Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni,

Yehova sadzakutenganso ndende;

koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu,

nadzavumbulutsa zochimwa zako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LAM/4-9251eb354beca9579bd87a69a3e2e0d9.mp3?version_id=1068—

Categories
MALIRO

MALIRO 5

Adandaulira Yehova pa tsoka la ukapolo wao

1 Yehova, kumbukirani chotigwerachi,

penyani nimuone chitonzo chathu.

2 Cholowa chathu chasanduka cha alendo,

ndi nyumba zathu za achilendo.

3 Ndife amasiye opanda atate,

amai athu akunga akazi amasiye.

4 Tinamwa madzi athu ndi ndalama,

tiona nkhuni zathu pozigula.

5 Otilondola atigwira pakhosi pathu,

tatopa osaona popumira.

6 Tinagwira mwendo Ejipito

ndi Asiriya kuti tikhute zakudya.

7 Atate athu anachimwa, kulibe iwo;

ndipo tanyamula mphulupulu zao.

8 Akapolo atilamulira;

palibe wotipulumutsa m’dzanja lao.

9 Timalowa m’zoopsa potenga zakudya zathu,

chifukwa cha lupanga la m’chipululu.

10 Khungu lathu lapserera ngati pamoto

chifukwa cha kuwawa kwa njala.

11 Anaipitsa akazi muZiyoni,

ndi anamwali m’midzi ya Yuda.

12 Anawapachika akalonga manja ao;

sanalemekeze nkhope za akulu.

13 Anyamata ananyamula mphero,

ana nakhumudwa posenza nkhuni.

14 Akulu adatha kuzipata,

anyamata naleka nyimbo zao.

15 Chimwemwe cha mtima wathu chalekeka,

masewera athu asanduka maliro.

16 Korona wagwa pamutu pathu;

kalanga ife! Pakuti tinachimwa.

17 Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka,

chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi;

18 paphiri la Ziyoni lopasukalo

ankhandwe ayendapo.

19 Inu, Yehova, mukhala chikhalire,

ndi mpando wanu wachifumu ku mibadwomibadwo.

20 Bwanji mutiiwala chiiwalire,

ndi kutisiya masiku ambirimbiri.

21 Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova,

ndipo tidzatembenuzidwadi,

mukonzenso masiku athu ngati kale lija.

22 Koma mwatikaniza konse,

mwatikwiyira kopambana.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LAM/5-405eaa8ba3e76f80259bbc5075409028.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mneneri Ezekiele anakhala ku ukapolo ku Babiloni kuyambira nthawi imene mzinda wa Yerusalemu unali usanalandidwe mpaka nthawi imene mzinda wa Yerusalemu unagwa m’manja mwa adani mu chaka cha 586 BC. Uthenga wake umapita kwa anthu amene anali ku ukapolo ku Babiloni komanso kwa anthu a mu Yerusalemu. Buku la

Ezekiele

lili ndi mfundo zisanu ndi imodzi zazikulu: (1) Mulungu aitana Ezekiele kuti akhale mneneri. (2) Machenjezo kwa anthu kuti Mulungu adzawaweruza komanso za kugwa ndi kupasuka kwa Yerusalemu. (3) Mauthenga ochokera kwa Yehova onena za chiweruzo chake pa maiko osiyanasiyana amene amazunza ndi kupotoza anthu ake; (4) Mau a chitonthozo kwa Israele kuti ngakhale mzinda wa Yerusalemu wapasuka, Yehova adzadalitsanso anthu ake; (5) Uneneri wolosera motsutsana ndi Gogi; (6) Kachisi wa Yehova adzamangidwanso ndi kukhala wa ulemerero kuposa kale, ndipo dziko lidzadalitsidwa.

Ezekiele anali munthu wa chikhulupiriro champhamvu komanso wa nzeru zakuthwa polongosola zimene adzaziwona m’masomphenya. Amapereka uthenga wake pogwiritsa ntchito zifanizo zochititsa chidwi ndi zachilendo. Phunziro lalikulu ndilo lakuti anthu atembenuke mtima ndi kusintha maganizo ao, popeza aliyense adzaweruzidwa chifukwa cha zolakwa zake. Choncho anthu asaleke kukhulupirira Yehova amene adzadzutsanso fuko lake la Israele. Ezekiele anali wansembe komanso mneneri, ndipo amakonda kunena za Kachisi wa Yehova ndi kufunika kwakuti anthu akhale oyera mtima pa ntchito yotumikira Mulungu.

Za mkatimu

Kuitanidwa kwa Ezekiele

1.1—3.27

Mauthenga achiweruzo onena za Yerusalemu

4.1—24.27

Chiweruzo cha Mulungu pa maiko

25.1—32.32

Lonjezo la Mulungu kwa anthu ake

33.1—37.2

8

Mau a Yehova otsutsa dziko la Gogi

38.1—39.29

Masomphenya a Kachisi komanso dziko lakutsogolo

40.1—48.35

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 1

Masomphenya a Ezekiele

1 Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.

2 Tsiku lachisanu la mwezi, ndicho chaka chachisanu cha kutengedwa ndende mfumu Yehoyakini,

3 anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m’dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.

4 Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m’mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, ndi m’kati mwake mudaoneka ngati chitsulo chakupsa m’kati mwa moto.

5 Ndi m’kati mwake mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,

6 ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.

7 Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang’ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.

8 Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.

9 Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuke poyenda; chilichonse chinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.

10 Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya kudzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng’ombe pa mbali ya kudzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga.

11 Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; chilichonse chinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.

12 Ndipo zinayenda, chilichonse chinalunjika kutsogolo kwake uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuke poyenda.

13 Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makala amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unachita cheza, ndi m’motomo mudatuluka mphezi.

14 Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong’anima.

15 Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodziimodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.

16 Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.

17 Poyenda zinayenda kumbali zao zinai, zosatembenuka poyenda.

18 Ndi mikombero yake inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.

19 Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka.

20 Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’njingazo.

21 Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izo; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.

22 Ndi pa mitu ya zamoyozi panali chifaniziro cha thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao.

23 Ndi pansi pathambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika kulinzake; chilichonse chinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, chakuno ndi chauko.

24 Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.

25 Ndipo panamveka mau pamwamba pathambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao.

26 Ndi pamwamba pathambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake.

27 Ndipo ndinapenya ngati chitsulo chakupsa, ngati maonekedwe ake a moto m’kati mwake pozungulira pake, kuyambira maonekedwe a m’chuuno mwake ndi kumwamba kwake; ndipo kuyambira maonekedwe a m’chuuno mwake ndi kunsi kwake ndinaona ngati maonekedwe ake a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.

28 Ngati maonekedwe a utawaleza uli m’mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/1-a870287340db53835ae59b76eaa34614.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 2

Kuitanidwa kwa Ezekiele

1 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, khala chilili, ndipo ndidzanena nawe.

2 Ndipo unandilowa mzimu pamene ananena nane, ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo ndinamumva Iye wakunena nane.

3 Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israele, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe.

4 Ndipo anawa, ndiwo achipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nao, Atero Yehova Mulungu.

5 Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panalimneneripakati pao.

6 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka.

7 Ndipo ukanene nao mau anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka.

8 Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ichi ndilikunena nawe; usakhale iwe wopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye chomwe ndikupatsa.

9 Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londitulutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m’mwemo;

10 naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m’kati ndi kubwalo; munalembedwa m’mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/2-e720a08140f6e31b4fee057fa8ad2290.mp3?version_id=1068—