Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 42

Yeremiya achenjeza anthu asapite ku Ejipito

1 Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi Yezaniya mwana wake wa Hosaya, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono, kufikira wamkulu, anayandikira,

2 nati kwa Yeremiyamneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m’malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;

3 kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi chomwe tichite.

4 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.

5 Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.

6 Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.

7 Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya.

8 Ndipo anaitana Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu,

9 nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pake,

10 Ngati mudzakhalabe m’dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu.

11 Musaope mfumu ya ku Babiloni, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndili ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m’dzanja lake.

12 Ndipo ndidzakuchitirani inu chifundo, kuti iye akuchitireni inu chifundo, nakubwezereni inu kudziko lanu.

13 Koma mukati, Sitidzakhala m’dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;

14 ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;

15 chifukwa chake mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe mu Ejipito, kukakhala m’menemo;

16 pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m’menemo m’dziko la Ejipito, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Ejipito; pamenepo mudzafa.

17 Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Ejipito kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku choipa chimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.

18 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala muYerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.

19 Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe mu Ejipito; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.

20 Pakuti mwanyenga m’miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.

21 Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamve mau a Yehova Mulungu wanu m’chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu.

22 Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, komwe mufuna kukakhalako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/42-c6969a88995b6bfbbdfc609f69f439a7.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 43

Amtenga Yeremiya napita naye ku Ejipito

1 Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,

2 pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe mu Ejipito kukhala m’menemo;

3 koma Baruki mwana wake wa Neriya atisonkhezera zoipa za inu, mutipereke m’dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am’nsinga ku Babiloni.

4 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m’dziko la Yuda.

5 Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m’dziko la Yuda;

6 ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;

7 ndipo anadza nalowa m’dziko la Ejipito; pakuti sanamvere mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.

Yeremiya aneneratu kuti Nebukadinezara adzagonjetsa Ejipito

8 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya mu Tapanesi, kuti,

9 Tenga miyala yaikulu m’dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba yaFaraomu Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;

10 ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake.

11 Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Ejipito; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.

12 Ndidzayatsa moto m’nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m’menemo ndi mtendere.

13 Ndipo adzathyola mizati ya zoimiritsa za Kachisi wa dzuwa, ali m’dziko la Ejipito; ndi nyumba za milungu ya Aejipito adzazitentha ndi moto.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/43-30549cf0aa0d720b379d0c2e21ee1ce8.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 44

Achenjeza mowaopsa Ayuda amene adathawira ku Ejipito

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m’dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m’dziko la Patirosi, akuti,

2 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa mizinda yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo;

3 chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.

4 Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.

5 Koma sanamvere, sanatchere khutu lao kuti atembenuke asiye choipa chao, osafukizira milungu ina.

6 Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m’mizinda ya Yuda ndi m’miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.

7 Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa chanji muchitira miyoyo yanu choipa ichi, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;

8 popeza muutsa mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu, pofukizira milungu ina m’dziko la Ejipito, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale chitemberero ndi chitonzo mwaamitunduonse a dziko lapansi?

9 Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazichita m’dziko la Yuda, ndi m’miseu ya Yerusalemu?

10 Sanadzichepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m’chilamulo changa, kapena m’malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.

11 Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang’anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda yense.

12 Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m’dziko la Ejipito akhale m’menemo, ndipo adzathedwa onse; m’dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.

13 Ndipo ndidzalanga iwo okhala m’dziko la Ejipito, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri;

14 kuti otsala a Yuda, amene ananka kudziko la Ejipito kukhala m’menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere kudziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m’menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo.

15 Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu ina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukulu, anthu onse okhala m’dziko la Ejipito, mu Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,

16 Koma mau amene wanena ndi ife m’dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe.

17 Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m’kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m’mizinda ya Yuda, ndi m’miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.

18 Koma chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi njala.

19 Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?

20 Ndipo Yeremiya anati kwa anthu onse, kwa amuna, ndi kwa akazi, kwa anthu onse amene anambwezera mau amenewa, ndi kuti,

21 Zofukizira zanu m’mizinda ya Yuda, ndi m’miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akulu anu, ndi anthu a m’dziko, kodi Yehova sanazikumbukire, kodi sizinalowe m’mtima mwake?

22 Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.

23 Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m’chilamulo chake, ndi m’malemba ake, ndi m’mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.

24 Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m’dziko la Ejipito.

25 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m’kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzachita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, chitani zowinda zanu.

26 Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m’dziko la Ejipito: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikulu, ati Yehova, kuti dzina langa silidzatchulidwanso m’kamwa mwa munthu aliyense wa Yuda m’dziko la Ejipito, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.

27 Taonani, ndiwayang’anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m’dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.

28 Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kutuluka kudziko la Ejipito kulowa m’dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m’dziko la Ejipito kuti akhale m’menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao.

29 Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha kwa inu, ati Yehova, chakuti Ine ndidzakulangani m’malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akuchitireni inu zoipa.

30 Yehova atero: Taonani, ndidzaperekaFaraoHofira mfumu ya Aejipito m’manja a adani ake, ndi m’manja a iwo akufuna moyo wake; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m’manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni mdani wake, amene anafuna moyo wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/44-53f99c37c8099d292a837badf50b8e7f.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 45

Mau a Mulungu kwa Baruki

1 Mau amene ananena Yeremiyamnenerikwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m’buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti,

2 Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki:

3 Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.

4 Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m’dziko lonseli.

5 Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m’malo monse m’mene mupitamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/45-0b689bc167264163b21b6bf2565be91d.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 46

Aneneratu kuti mfumu ya ku Babiloni idzagonjetsa Aejipito

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiyamneneriakunena zaamitundu.

2 Za Ejipito: kunena za nkhondo yaFaraoNeko mfumu ya Aejipito, imene inali pamtsinje wa Yufurate mu Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.

3 Konzani chikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.

4 Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.

5 Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m’mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.

6 Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pamtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa.

7 Ndani uyu amene auka ngati mtsinje, madzi ake ogavira monga mitsinje?

8 Ejipito auka ngati mtsinje, madzi ake agavira ngati mitsinje; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mizinda ndi okhalamo ake.

9 Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.

10 Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m’dziko la kumpoto pamtsinje wa Yufurate.

11 Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako.

12 Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.

13 Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.

14 Nenani mu Ejipito, lalikirani mu Migidoli, lalikirani mu Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.

15 Akulimba ako akokoledwa bwanji? Sanaime, chifukwa Yehova anawathamangitsa.

16 Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa.

17 Ndipo anafuula kumeneko, Farao mfumu ya Aejipito ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira.

18 Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.

19 Mwana wamkazi iwe wokhala mu Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo.

20 Ejipito ndi ng’ombe yaikazi yosalala; chionongeko chotuluka kumpoto chafika, chafika.

21 Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang’ombe a m’khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.

22 Mkokomo wake udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.

23 Adzatema nkhalango yake, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti achuluka koposa dzombe, ali osawerengeka.

24 Mwana wake wamkazi wa Ejipito adzachitidwa manyazi, adzaperekedwa m’manja a anthu a kumpoto.

25 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati, Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;

26 ndipo ndidzawapereka m’manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m’manja a atumiki ake; pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.

27 Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, iwe Israele: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kuchokera kutali, ndi mbeu yako kudziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m’mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye.

28 Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/46-d06c551d0b144f7a2231002a4b099d55.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 47

Aneneratu za chitsutso cha Afilisti

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiyamnenerionena za Afilisti,Faraoasanakanthe Gaza.

2 Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m’mwemo, pamzinda ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m’dziko adzakuwa.

3 Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao;

4 chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori.

5 Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m’chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?

6 Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala chete iwe? Dzilonge wekha m’chimake; puma, nukhale chete.

7 Udzakhala chete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? Za Asikeloni, ndi za m’mphepete mwa nyanja, pamenepo analiika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/47-efc82fcd73fad87d54951dff763e4861.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 48

Chitsutso cha Mowabu

1 Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.

2 Palibenso kutamanda Mowabu; mu Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.

3 Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu!

4 Mowabu waonongedwa; ang’ono ake amveketsa kulira.

5 Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko.

6 Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m’chipululu.

7 Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.

8 Ndipo wakufunkha adzafikira pa mizinda yonse, sudzapulumuka mzinda uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova.

9 Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; mizinda yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

10 Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi.

11 Mowabu wakhala m’mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.

12 Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao.

13 Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.

14 Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo?

15 Mowabu wapasuka, akwera kulowa m’mizinda yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu.

16 Tsoka la Mowabu layandikira kudza, nsautso yake ifulumiratu.

17 Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma!

18 Iwe mwana wamkazi wokhala mu Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.

19 Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?

20 Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.

21 Chiweruzo chafika padziko lachidikha; pa Holoni, ndi pa Yahazi, ndi pa Mefaati;

22 ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Betedibilataimu;

23 ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni;

24 ndi pa Keriyoti, ndi pa Bozira, ndi pa mizinda yonse ya dziko la Mowabu, yakutali kapena yakufupi.

25 Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova.

26 Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzamvimvinika m’kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso.

27 Kodi sunaseke Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.

28 Inu okhala mu Mowabu, siyani mizinda, khalani m’thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.

29 Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang’wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.

30 Ine ndidziwa mkwiyo wake, ati Yehova, kuti uli chabe; zonyenga zake sizinachite kanthu.

31 Chifukwa chake ndidzakuwira Mowabu; inde, ndidzafuulira Mowabu yense, adzalirira anthu a ku Kiriheresi.

32 Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mphakasa ndi mphesa zako.

33 Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.

34 Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.

35 Ndiponso ndidzaletsa mu Mowabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yake.

36 Chifukwa chake mtima wanga umlirira Mowabu monga zitoliro, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kiriheresi monga zitoliro, chifukwa chake zakuchuluka zake adadzionera zatayika.

37 Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zometedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.

38 Pamwamba pa matsindwi a Mowabu ndi m’miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m’mene mulibe chikondwero, ati Yehova.

39 Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.

40 Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati chiombankhanga, adzamtambasulira Mowabu mapiko ake.

41 Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

42 Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.

43 Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, zili pa iwe, wokhala mu Mowabu, ati Yehova.

44 Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m’dzenje; ndi iye amene atuluka m’dzenje adzagwidwa m’khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

45 Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m’kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.

46 Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako aamuna atengedwa ndende, ndi ana ako aakazi atengedwa ndende.

47 Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/48-a708b8159b4351a9714f0ec1fc95ba51.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 49

Chitsutso cha Aamoni

1 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M’mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m’mizinda mwake?

2 Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo midzi yake idzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.

3 Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana aakazi a Raba, muvale chiguduli; chitani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m’ndende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.

4 Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m’mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani?

5 Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera.

6 Koma pambuyo pake ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.

Za kulangidwa kwa Aedomu

7 Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?

8 Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala mu Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.

9 Akafika kwa inu akutchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? Akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?

10 Pakuti ndamvula Esau, ndamvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zake zaonongeka, ndi abale ake, ndi anansi ake, ndipo palibe iye.

11 Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine.

12 Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.

13 Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo mizinda yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire.

14 Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwaamitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.

15 Pakuti, taona, ndakuyesa iwe wamng’ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu.

16 Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m’mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.

17 Ndipo Edomu adzakhala chizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zovuta zake zonse.

18 Monga m’kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi mizinda inzake, ati Yehova, munthu aliyense sadzakhala m’menemo, mwana wa munthu aliyense sadzagona m’menemo.

19 Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang’anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

20 Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala mu Temani, ndithu adzawakoka, ana aang’ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

21 Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso la kugwa kwao; pali mfuu, phokoso lake limveka pa Nyanja Yofiira.

22 Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

Chitsutso cha Damasiko

23 Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.

24 Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zovuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.

25 Alekeranji kusiya mzinda wa chilemekezo, mzinda wa chikondwero changa?

26 Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m’miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.

27 Ndipo Ine ndidzayatsa moto m’khoma la Damasiko, udzathetsa zinyumba za Benihadadi.

Chitsutso cha Kedara ndi Hazori

28 Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a ku m’mawa.

29 Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zotchingira zao, ndi katundu wao yense, ndingamirazao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse.

30 Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala mu Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani.

31 Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mapiringidzo, okhala pa okha.

32 Ndipo ngamira zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng’ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira kumphepo zonse iwo amene ameta m’mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao kumbali zao zonse, ati Yehova.

33 Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lachikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.

Chitsutso cha Elamu

34 Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiyamneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,

35 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.

36 Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako.

37 Ndipo ndidzachititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera choipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;

38 ndipo ndidzaika mpando wachifumu wanga mu Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova.

39 Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/49-47c3d8ad9be05146370e0b170fc41d10.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 50

Chitsutso cha Babiloni

1 Mau amene ananena Yehova za Babiloni, za dziko la Ababiloni, mwa Yeremiyamneneri.

2 Lalikirani mwaamitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.

3 Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.

4 Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, ana a Israele adzadza, iwo ndi ana a Yuda; pamodzi adzayenda m’njira mwao alinkulira, nadzafuna Yehova Mulungu wao.

5 AdzafunsiraZiyoninkhope zao zilikuyang’ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m’chipanganocha muyaya chimene sichidzaiwalika.

6 Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; achoka kuphiri kunka kuchitunda; aiwala malo ao akupuma.

7 Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.

8 Thawani pakati pa Babiloni, tulukani m’dziko la Ababiloni, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.

9 Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe.

10 Ndipo Kasidi adzakhala chofunkha; onse amene amfunkhitsa iye adzakhuta, ati Yehova.

11 Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng’ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;

12 amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, chipululu, dziko louma, bwinja.

13 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babiloni adzadabwa, adzatsonyera pa zovuta zake zonse.

14 Gubani ndi kuzungulira Babiloni kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mivi; pakuti wachimwira Yehova.

15 Mumfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ake agwa; makoma ake agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; mumbwezere chilango; monga iye wachita mumchitire iye momwemo.

16 Muwathe ofesa ku Babiloni, ndi iwo amene agwira chisenga nyengo ya masika; chifukwa cha lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ake, nadzathawira yense ku dziko lake.

17 Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.

18 Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni ndi dziko lake, monga ndinalanga mfumu ya Asiriya.

19 Ndipo ndidzabwezeranso Israele kubusa lake, ndipo adzadya pa Karimele ndi pa Basani, moyo wake nudzakhuta pa mapiri a Efuremu ndi mu Giliyadi.

20 Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.

21 Kwera kukamenyana ndi dziko la Merataimu, ndi okhala mu Pekodi, ipha nuononge konse pambuyo pao, ati Yehova, chita monga mwa zonse ndinakuuza iwe.

22 Phokoso la nkhondo lili m’dziko lino, ndi lakuononga kwakukulu.

23 Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kuthyoka! Babiloni wasanduka bwinja pakati pa amitundu!

24 Ndakutchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babiloni, ndipo sunadziwe, wapezeka, ndiponso wagwidwa, chifukwa walimbana ndi Yehova.

25 Yehova watsegula pa nyumba ya zida zake, ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi ntchito m’dziko la Ababiloni.

26 Tadzani kudzamenyana ndi iye kuchokera ku malekezero ake, tsegulani pa nkhokwe zake; unjikani zake monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye.

27 Iphani ng’ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.

28 Mau a iwo akuthawa akupulumuka m’dziko la Babiloni, kuti alalikire mu Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.

29 Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele.

30 Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m’miseu yake, ndi anthu ankhondo ake onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.

31 Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.

32 Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m’mizinda yake, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.

33 Yehova wa makamu atero. Ana a Israele ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.

34 Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lake Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumutse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala mu Babiloni.

35 Lupanga lili pa Ababiloni, ati Yehova, pa okhala mu Babiloni, pa akulu ake, ndi pa anzeru ake.

36 Lupanga lili pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga lili pa anthu olimba ake, ndipo adzaopa.

37 Lupanga lili pa akavalo ao, ndi pa magaleta ao, ndi pa anthu onse osakanizidwa amene ali pakati pake, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga lili pa chuma chake, ndipo chidzalandidwa.

38 Chilala chili pamadzi ake, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaluka ndi kufuna zoopsa.

39 Chifukwa chake zilombo za kuchipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m’menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m’mibadwomibadwo.

40 Monga muja Mulungu anagwetsa Sodomu ndi Gomora ndi mizinda inzake, ati Yehova; anthu sadzakhalamo, mwana wa munthu sadzagonamo.

41 Taonani, anthu achokera kumpoto; ndiwo mtundu waukulu, ndipo maufumu ambiri adzaukitsidwa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

42 Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babiloni.

43 Mfumu ya ku Babiloni yamva mbiri yao, ndipo manja ake alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.

44 Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umchokere, ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang’anira wake; pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

45 Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babiloni; ndi zimene walingirira dziko la Ababiloni; ndithu adzawakoka, ana aang’ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

46 Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babiloni, ndipo mfuu wamveka mwa amitundu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/50-59c85454eb78617390ae264029fcc67e.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 51

1 Yehova atero: Taonani, ndidzaukitsira Babiloni, ndi iwo okhala mu Lebi-kamai, mphepo yoononga.

2 Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m’dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake.

3 Wauta asakoke uta wake, asadzikweze m’malaya ake achitsulo; musasiye anyamata ake; muononge ndithu khamu lake lonse.

4 Ndipo adzagwa ophedwa m’dziko la Ababiloni, opyozedwa m’miseu yake.

5 Pakuti Israele ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi uchimo kuchimwira Woyera wa Israele.

6 Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m’choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.

7 Babiloni wakhala chikho chagolide m’dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi;amitunduamwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.

8 Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire.

9 Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo.

10 Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire muZiyonintchito ya Yehova Mulungu wathu.

11 Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.

12 Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala mu Babiloni.

13 Iwe wokhala pamadzi ambiri, wochuluka chuma, chimaliziro chako chafika, chilekezero cha kusirira kwako.

14 Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mfuu.

15 Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yake, ndi luso anayala thambo;

16 pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m’mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, atulutsa mphepo ya m’nyumba za chuma zake.

17 Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golide achitidwa manyazi ndi fanizo lake losema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya m’menemo.

18 Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.

19 Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu.

20 Iwe ndiwe chibonga changa ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzathyolathyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;

21 ndi iwe ndidzathyolathyola kavalo ndi wokwera wake;

22 ndi iwe ndidzathyolathyola galeta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzathyolathyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzathyolathyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzathyolathyola mnyamata ndi namwali;

23 ndi iwe ndidzathyolathyola mbusa ndi zoweta zake; ndi iwe ndidzathyolathyola wakulima ndi goli la ng’ombe lake; ndi iwe ndidzathyolathyola akazembe ndi ziwanga.

24 Ndipo ndidzabwezera Babiloni ndi okhala mu Kasidi zoipa zao zonse anazichita mu Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.

25 Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.

26 Ndipo sadzachotsa pa iwe mwala wa pangodya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova.

27 Kwezani mbendera m’dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe.

28 Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ake, ndi ziwanga zake zonse, ndi dziko lonse la ufumu wake.

29 Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo.

30 Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m’malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka.

31 Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzake, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzake, kukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mzinda wake wagwidwa ponsepo;

32 pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa.

33 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwana wamkazi wa Babiloni akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang’ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye.

34 Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng’ona, wadzaza m’kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.

35 Wokhala mu Ziyoni adzati, Chiwawa anandichitira ine ndi thupi langa chikhale pa Babiloni; nadzatiYerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala mu Kasidi.

36 Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera chilango chifukwa cha iwe; ndidzaphwetsa nyanja yake, ndidzaphwetsa chitsime chake.

37 Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.

38 Adzabangula pamodzi ngati misona ya mikango; adzachita nthulu ngati ana a mikango.

39 Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova.

40 Ndidzawagwetsa kuti aphedwe monga anaankhosa amphongo, ndi atonde.

41 Sesaki wagwidwatu! Chimene dziko lonse lapansi linachitamanda chalandidwa dzidzidzi! Babiloni wakhalatu bwinja pakati pa amitundu!

42 Nyanja yakwera kufikira ku Babiloni; wamira ndi mafunde ake aunyinji.

43 Mizinda yake yakhala bwinja, dziko louma, chipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu aliyense.

44 Ndipo Ine ndiweruza Beli mu Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m’kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.

45 Anthu anga, tulukani pakati pake, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova.

46 Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m’dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m’dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.

47 Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake.

48 Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse zili m’menemo, zidzaimba mokondwerera Babiloni; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kuchokera kumpoto, ati Yehova.

49 Monga Babiloni wagwetsa ophedwa a Israele, momwemo pa Babiloni padzagwa ophedwa a dziko lonse.

50 Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu musaime chiimire; mukumbukire Yehova kutali, Yerusalemu alowe m’mtima mwanu.

51 Tili ndi manyazi, chifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m’malo opatulika a nyumba ya Yehova.

52 Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo padziko lake lonse olasidwa adzabuula.

53 Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.

54 Mau akufuula ochokera ku Babiloni, ndi a chionongeko chachikulu ku dziko la Ababiloni!

55 Pakuti Yehova afunkha Babiloni, aononga m’menemo mau aakulu; ndipo mafunde ake adzakokoma ngati madzi ambiri, mau ao apokosera;

56 pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babiloni, ndi anthu ake olimba agwidwa, mauta ao athyokathyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.

57 Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu.

58 Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babiloni adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zake zazitali zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira ntchito chabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.

59 Mau amene Yeremiyamnenerianauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babiloni chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo Seraya anali kapitao wa chigono chake.

60 Ndipo Yeremiya analemba m’buku choipa chonse chimene chidzafika pa Babiloni, mau onse awa olembedwa za Babiloni.

61 Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse,

62 nuti, Inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi.

63 Ndipo padzakhala, utatha kuwerenga buku ili, ulimange ndi mwala, nuliponye pakati pa Yufurate;

64 nuti, Chomwecho adzamira Babiloni, sadzaukanso chifukwa cha choipa chimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa. Mau a Yeremiya ndi omwewo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/51-11ede718d16c300df5b8bb1781d98078.mp3?version_id=1068—