Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 32

Yeremiya atsekeredwa m’kaidi nagula munda wa Hanamele

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara.

2 Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangiraYerusalemumisasa; ndipo Yeremiyamnenerianatsekeredwa m’bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.

3 Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m’dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,

4 ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m’dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m’dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;

5 ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komweko kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?

6 Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

7 Taonani, Hanamele mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.

8 Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m’bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m’dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.

9 Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri asiliva.

10 Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m’miyeso.

11 Ndipo ndinatenga kalata yogulira, yina yosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi yina yovundukuka;

12 ndipo ndinapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata yogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m’bwalo la kaidi.

13 Ndipo ndinauza Baruki pamaso pao, kuti,

14 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero; Tenga makalata awa, kalata yogulira, yosindikizidwa, ndi kalata yovundukuka, nuwaike m’mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.

15 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yampesa idzagulidwanso m’dziko muno.

Pemphero la Yeremiya

16 Ndipo nditapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti,

17 Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;

18 amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m’chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu;

19 wamkulu mu upo, wamphamvu m’ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;

20 amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m’dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, mu Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;

21 ndipo munatulutsa anthu anu Israele m’dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;

22 ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uchi;

23 ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m’chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;

24 taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m’dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.

25 Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mzinda waperekedwa m’manja a Ababiloni.

Mulungu anenetsa kuti Aisraele adzalangidwa, nalonjeza kuwalanditsanso

26 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,

27 Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse; kodi kuli kanthu kondikanika Ine?

28 Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzapereka mzindawu m’dzanja la Ababiloni, m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzaulanda,

29 ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukiziraBaala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.

30 Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.

31 Pakuti mzinda uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;

32 chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu.

33 Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m’mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.

34 Koma anaika zonyansa zao m’nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.

35 Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m’chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa chaMoleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m’mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.

36 Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mzinda umene, munena inu, waperekedwa m’dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri:

37 Taonani, ndidzawasokolotsa m’maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m’kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,

38 ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;

39 ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;

40 ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m’mitima yao, kuti asandichokere.

41 Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m’dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

42 Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa choipa chonsechi, chomwecho ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonjeza.

43 Ndipo minda idzagulidwa m’dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m’dzanja la Ababiloni.

44 Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m’dziko la Benjamini, ndi m’malo ozungulira Yerusalemu, ndi m’mizinda ya Yuda, ndi m’mizinda ya kumtunda, ndi m’mizinda ya kuchidikha, ndi m’mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/32-da42984124ea1c020c25599dfc686e82.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 33

Yehova abwereza kunena kuti anthu ake adzakhazikikanso m’dziko mwao, padzakhalanso mphukira

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yachiwiri, pamene iye anali chitsekedwere m’bwalo la kaidi, kuti,

2 Atero Yehova wochita zake, Yehova wolenga zake kuti azikhazikitse; dzina lake ndi Yehova:

3 Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zopambana, zimene suzidziwa.

4 Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israele, za nyumba za mzinda uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda’zi, zinagwetsedwa ziwatchinjirizire mitumbira, ndi lupanga:

5 Adza kumenyana ndi Ababiloni, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m’mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mzinda uno nkhope yanga chifukwa cha zoipa zao zonse.

6 Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.

7 Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israele, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja.

8 Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.

9 Ndipo ndidzayesa mzinda uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso paamitunduonse a padziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.

10 Atero Yehova: M’malo muno, m’mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m’mizinda ya Yuda, m’makwalala aYerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,

11 mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m’nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.

12 Yehova wa makamu atero: M’malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m’mizinda yake yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao.

13 M’mizinda ya kumtunda, m’mizinda ya kuchidikha, m’mizinda ya kumwera, m’dziko la Benjamini, m’malo ozungulira Yerusalemu, m’mizinda ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.

14 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israele ndi za nyumba ya Yuda.

15 Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukutsira Davide mphukira ya chilungamo; ndipo adzachita chiweruzo ndi chilungamo m’dzikomu.

16 Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu.

17 Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wachifumu wa nyumba ya Israele;

18 ndiponso ansembe a fuko la Levi sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakuchita nsembe masiku onse.

19 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

20 Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m’nyengo yao;

21 pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.

22 Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.

23 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

24 Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.

25 Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;

26 pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/33-a575237a23ca2d5aaafb9b5b2cae67be.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 34

Zedekiya adzatengedwa, Yerusalemu adzalandidwa

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndiYerusalemu, ndi mizinda yake yonse, akuti,

2 Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mzindawu m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;

3 ndipo iwe sudzapulumuka m’dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m’dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni.

4 Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;

5 udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! Pakuti ndanena mau, ati Yehova.

6 Ndipo Yeremiyamneneriananena mau onsewa kwa Zedekiya mfumu ya Yuda mu Yerusalemu,

7 pamene nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni inamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yonse ya Yuda imene inatsala, ndi Lakisi ndi Azeka; pakuti mizinda ya Yuda yamalinga yotsala ndi imeneyi.

Oyesa abale ao akapolo aopsedwa

8 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, mfumu Zedekiya atapangana pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu;

9 kuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Muhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzake kapolo wake;

10 ndipo akulu onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula;

11 koma pambuyo pake anabwerera, nabweza akapolo ake aamuna ndi aakazi, amene anawamasula, nawagonjetsanso akhale akapolo aamuna ndi aakazi;

12 chifukwa chake mau a Yehova anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

13 Yehova Mulungu wa Israele atero: Ndinapangana mapangano ndi makolo anu tsiku lija ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito, kutuluka m’nyumba ya ukapolo, kuti,

14 Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wake amene ali Muhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi chimodzi, mudzammasule akuchokereni; koma makolo anu sanandimvere Ine, sananditchere Ine khutu.

15 Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kuchita chimene chili cholungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzake; ndipo munapangana pangano pamaso panga m’nyumba imene itchedwa dzina langa;

16 koma mwabwerera ndi kuipitsa dzina langa, ndi kubwezera mu ukapolo yense kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, amene munammasula akachite zao, ndipo munawagonjetsa, akhale akapolo anu aamuna ndi aakazi.

17 Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m’maufumu onse a dziko lapansi.

18 Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanachite mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwanawang’ombe ndi kupita pakati pa mbali zake;

19 akulu a Yuda, ndi akulu a Yerusalemu, adindo, ndi ansembe, ndi anthu onse a m’dziko, amene anapita pakati pa mbali za mwanawang’ombe;

20 ndidzapereka iwo m’dzanja la adani ao, ndi m’dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za mlengalenga, ndi cha zilombo za padziko lapansi.

21 Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m’dzanja la adani ao, ndi m’dzanja la akufuna moyo wao, ndi m’dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokerani.

22 Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumzinda uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/34-63113c59ba909ab6a8ae7ebe210f5290.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 35

Kukhulupirika kwa Arekabu kukhale chitsanzo cha kwa Yuda

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,

2 Pita kunyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m’nyumba ya Yehova, m’chipinda china, nuwapatse iwo vinyo amwe.

3 Ndipo ndinatenga Yazaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habaziniya, ndi abale ake, ndi ana aamuna ake, ndi nyumba yonse ya Arekabu;

4 ndipo ndinawalowetsa m’nyumba ya Yehova, m’chipinda cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, chokhala pambali pa chipinda cha akulu, ndicho chosanjika pa chipinda cha Maaseiya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;

5 ndipo ndinaika pamaso pa ana aamuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.

6 Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kwamuyaya;

7 ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m’mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m’dziko limene mukhalamo alendo.

8 Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m’zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu aamuna ndi aakazi;

9 ngakhale kudzimangira nyumba zokhalamo; ndipo sitili nao munda wampesa, kapena munda, kapena mbeu;

10 koma takhala m’mahema, nitimvera, nitichita monga mwa zonse anatiuza Yonadabu kholo lathu.

11 Koma panali, pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anadza m’dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke kuYerusalemuchifukwa tiopa nkhondo ya Ababiloni, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala mu Yerusalemu.

12 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,

13 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala mu Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga? Ati Yehova.

14 Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ake, asamwe vinyo, alikuchitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvere Ine.

15 Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m’dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchere khutu lanu, simunandimvere Ine.

16 Pakuti monga ana a Yonadabu mwana wa Rekabu achita lamulo la kholo lao limene anawauza, koma anthu awa sanandimvere Ine.

17 Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu choipa chonsecho ndawanenera iwo; chifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandivomere.

18 Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kuchita monga mwa zonse anakuuzani inu;

19 chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wakuima pamaso panga kumuyaya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/35-3888b283f4a24703e3cc430378eea07b.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 36

Mau a Yeremiya alembedwa pampukutu nawerengedwa mu Kachisi, natenthedwa ndi mfumu

1 Ndipo panali chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2 Tenga buku lampukutu, nulembe m’menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akuneneraamitunduonse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.

3 Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.

4 Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m’buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.

5 Ndipo Yeremiya anauza Baruki, kuti, Ndaletsedwa sindithai kulowa m’nyumba ya Yehova;

6 koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m’makutu a anthu m’nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m’makutu a Ayuda onse amene atuluka m’mizinda yao.

7 Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yake yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukulu.

8 Ndipo Baruki mwana wa Neriya anachita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiyamneneri, nawerenga m’buku mau a Yehova m’nyumba ya Yehova.

9 Ndipo panali chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wachisanu ndi chinai, anthu onse a muYerusalemu, ndi anthu onse ochokera m’mizinda ya Yuda kudza ku Yerusalemu, analalikirakusala kudyapamaso pa Yehova.

10 Ndipo Baruki anawerenga m’buku mau a Yeremiya m’nyumba ya Yehova, m’chipinda cha Gemariya mwana wa Safani mlembi, m’bwalo la kumtunda, pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova, m’makutu a anthu onse.

11 Pamene Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, anamva m’buku mau onse a Yehova,

12 anatsikira kunyumba ya mfumu, nalowa m’chipinda cha mlembi; ndipo, taonani, akulu onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akulu onse.

13 Ndipo Mikaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m’makutu a anthu.

14 Chifukwa chake akulu onse anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki, kukanena, Tenga m’dzanja lako mpukutu wauwerenga m’makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m’dzanja lake, nadza kwa iwo.

15 Ndipo anati kwa iye, Khala pansi tsopano, nuwerenga m’makutu athu. Ndipo Baruki anauwerenga m’makutu ao.

16 Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang’anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.

17 Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye?

18 Ndipo Baruki anayankha iwo, Pakamwa pake ananditchulira ine mau awa onse, ndipo ndinawalemba ndi inki m’bukumo.

19 Ndipo akulu anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.

20 Ndipo analowa kwa mfumu kubwalo; ndipo anasunga buku m’chipinda cha Elisama mlembi; nafotokozera mau onse m’makutu a mfumu.

21 Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kutuluka nao m’chipinda cha Elisama mlembi. Ndipo Yehudi anauwerenga m’makutu a mfumu, ndi m’makutu a akulu onse amene anaima pambali pa mfumu.

22 Ndipo mfumu anakhala m’nyumba ya nyengo yachisanu mwezi wachisanu ndi chinai; ndipo munali moto m’mbaula pamaso pake.

23 Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m’moto wa m’mbaulamo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m’mbaulamo.

24 Ndipo sanaope, sanang’ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.

25 Tsononso Elinatani ndi Delaya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.

26 Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.

27 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, mfumu itatentha mpukutuwo, ndi mau amene analemba Baruki ponena Yeremiya, kuti,

28 Tenganso mpukutu wina, nulembe m’menemo mau oyamba aja anali mu mpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wautentha.

29 Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m’menemo, kuti, Mfumu ya ku Babiloni idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m’menemo anthu ndi nyama?

30 Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.

31 Ndipo ndidzamlanga iye ndi mbeu zake ndi atumiki ake chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzawatengera iwo, ndi okhala mu Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, zoipa zonse ndawanenera iwo, koma sanamvere.

32 Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m’menemo ponena Yeremiya mau onse a m’buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m’moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/36-3fca11dc016c7b095ae97734cdf1cc5e.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 37

Yeremiya m’kaidi

1 Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m’malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m’dziko la Yuda.

2 Koma ngakhale iye, ngakhale atumiki ake, ngakhale anthu a padziko, sanamvere mau a Yehova, amene ananena mwa Yeremiya mneneri.

3 Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.

4 Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; chifukwa sanamuike iye m’nyumba yandende.

5 Ndipo nkhondo yaFaraoinatuluka mu Ejipito; ndipo pamene Ababiloni omangira misasaYerusalemuanamva mbiri yao, anachoka ku Yerusalemu.

6 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti,

7 Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao.

8 Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mzinda uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.

9 Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Ababiloni adzatichokera ndithu; pakuti sadzachoka.

10 Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m’hema wake ndi kutentha mzinda uwu ndi moto.

11 Ndipo panali pamene nkhondo ya Ababiloni inachoka ku Yerusalemu chifukwa cha nkhondo ya Farao,

12 pamenepo Yeremiya anatuluka mu Yerusalemu kumuka kudziko la Benjamini, kukalandira gawo lake kumeneko.

13 Pokhala iye mu Chipata cha Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Ababiloni.

14 Ndipo anati Yeremiya, Kunama kumeneko; ine sindipandukira kwa Ababiloni; koma sanamvere iye; ndipo Iriya anamgwira Yeremiya, nanka naye kwa akulu.

15 Ndipo akulu anakwiyira Yeremiya, nampanda iye, namuika m’nyumba yandende m’nyumba ya Yonatani mlembi; pakuti anaiyesa ndende.

16 Atafika Yeremiya kunyumba yadzenje, ku tizipinda take nakhalako Yeremiya masiku ambiri;

17 pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m’tseri m’nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni.

18 Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndachimwira inu chiyani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m’nyumba yandende?

19 Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babiloni sidzakudzerani inu, kapena dziko lino?

20 Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere kunyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko.

21 Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m’bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m’mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m’bwalo la kaidi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/37-731da6219102e7766b994b7aceb04e4f.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 38

Yeremiya aponyedwa m’dzenje muli thope

1 Ndipo Sefatiya mwana wa Matani ndi Gedaliya mwana wa Pusuri, ndi Yukala mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malikiya, anamva mau amene Yeremiya ananena ndi anthu onse, kuti,

2 Yehova atero, Iye wakukhala m’mzindawu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo.

3 Yehova atero, Mzindawu udzapatsidwatu m’dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.

4 Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m’mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.

5 Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m’manja mwanu; pakuti mfumu singathe kuchita kanthu kotsutsana nanu.

6 Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m’dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m’bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m’dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m’thopemo.

7 Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m’dzenje; mfumu ilikukhala pa Chipata cha Benjamini;

8 Ebedemeleki anatuluka m’nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,

9 Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m’zonse anachitira Yeremiyamneneri, amene anamponya m’dzenje; ndipo afuna kufa m’menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m’mzindamu.

10 Ndipo mfumu inamuuza Ebedemeleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numtulutse Yeremiya mneneri m’dzenjemo, asanafe.

11 Ndipo Ebedemeleki anatenga anthuwo, nalowa nao m’nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya chuma, natenga m’menemo nsalu zakale zotaya ndi zansanza zovunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m’dzenjemo.

12 Ndipo Ebedemeleki Mkusi anati kwa Yeremiya, Kulungatu zingwe ndi nsaluzi zotaya zakale ndi zansanza ndi kuzikwapatira. Ndipo Yeremiya anachita chomwecho.

13 Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m’dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m’bwalo la kaidi.

14 Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m’khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.

15 Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Ndikakufotokozerani, kodi simudzandipha ine? Ndipo ndikakupangirani, simudzandimvera ine.

16 Ndipo mfumu Zedekiya analumbira m’tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m’manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako.

17 Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzindawu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;

18 koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m’dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m’manja mwao.

19 Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Ababiloni, angandipereke ine m’manja mwao, angandiseke.

20 Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.

21 Koma ngati mukana kutuluka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa:

22 Taonani, akazi onse otsala m’nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m’thope, abwerera m’mbuyo.

23 Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m’manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.

24 Ndipo Zedekiya anati kwa Yeremiya, Anthu asadziwe mau amene, ndipo sudzafa.

25 Koma akamva akulu kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife chomwe wanena kwa mfumu; osatibisira ichi, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe;

26 pamenepo uziti kwa iwo, Ndinagwa ndi pembedzero langa pamaso pa mfumu, kuti asandibwezerenso kunyumba ya Yonatani ndifere komweko.

27 Ndipo akulu onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveke mlandu.

28 Ndipo Yeremiya anakhala m’bwalo la kaidi mpaka tsiku lakugwidwaYerusalemu. Ndipo anali komweko pogwidwa Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/38-e9b3304ac04a26143a3e692c9bafda54.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 39

Nebukadinezara alanda Yerusalemu, nalanditsa Yeremiya

1 Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse kuYerusalemu, ndi kuumangira misasa.

2 Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mzinda unabooledwa.

3 Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m’chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Neregali-Sarezare mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.

4 Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m’mzinda usiku, panjira pamunda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira panjira ya kuchidikha.

5 Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m’zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m’dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.

6 Pamenepo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya ku Ribula pamaso pake; mfumu ya ku Babiloni niphanso aufulu onse a Yuda.

7 Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m’zigologolo, kunka naye ku Babiloni.

8 Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.

9 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m’mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am’nsinga ku Babiloni.

10 Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m’dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.

11 Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti,

12 Umtenge, numyang’anire bwino, usamsautse, koma umchitire monga iye adzanena nawe.

13 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkulu wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Neregali-Sarezere mkulu wa alauli, ndi akulu onse a mfumu ya ku Babiloni;

14 iwonso anatumiza, namchotsa Yeremiya m’bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.

15 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, potsekeredwa iye m’bwalo la kaidi, kuti,

16 Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mzinda uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.

17 Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m’manja a anthu amene uwaopa.

18 Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/39-fc60515d9c44e2b7a4f22b8156954c00.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 40

Yeremiya apita kwa Gedaliya ku Mizipa

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m’maunyolo pamodzi ndi am’nsinga onse aYerusalemundi Yuda, amene anatengedwa am’nsinga kunka nao ku Babiloni.

2 Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera choipa ichi malo ano;

3 ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani.

4 Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.

5 Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babiloni inamyesa wolamulira mizinda ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kulikonse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke.

6 Ndipo Yeremiya ananka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa, nakhala kumeneko kwa anthu otsala m’dziko.

Gedaliya wolamulira mu Yerusalemu aphedwa ndi Ismaele

7 Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m’minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m’dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni;

8 pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efayi wa ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao.

9 Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m’dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani.

10 Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m’mbiya zanu, nimukhale m’mizinda imene mwailanda.

11 Chomwecho pamene Ayuda onse okhala mu Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi mu Edomu, ndi amene anali m’maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;

12 pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri.

13 Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m’minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa,

14 nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo.

15 Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya ku Mizipa m’tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; chifukwa chanji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?

16 Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anati kwa Yohanani mwana wa Kareya, Usachite ichi; pakuti unamizira Ismaele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/40-310a59eaaf6183bc4b662472b4423a5a.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 41

Gedaliya ndi ena aphedwa ndi Ismaele

1 Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi mu Mizipa.

2 Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.

3 Ismaele naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Ababiloni amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo.

4 Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,

5 anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang’amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndilubanim’manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.

6 Ndipo Ismaele mwana wa Netaniya anatuluka mu Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wake wa Ahikamu.

7 Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mzinda, Ismaele mwana wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

8 Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m’mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

9 Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.

10 Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.

11 Koma pamene Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo akhala naye, anamva zoipa zonse anazichita Ismaele mwana wa Netaniya,

12 anatenga anthu onse, nanka kukamenyena ndi Ismaele mwana wa Netaniya, nampeza pamadzi ambiri a mu Gibiyoni.

13 Ndipo panali pamene anthu onse amene anali ndi Ismaele anaona Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, anasekera.

14 Ndipo anthu onse amene Ismaele anatenga ndende kuwachotsa mu Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wake wa Kareya.

15 Koma Ismaele mwana wake wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.

16 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismaele mwana wake wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibiyoni;

17 ndipo anachoka, natsotsa mu Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa mu Ejipito,

18 chifukwa cha Ababiloni; pakuti anawaopa, chifukwa Ismaele mwana wake wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni anamuika wolamulira m’dzikomo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/41-b9aaab098fe54b2eec566100a7bba58e.mp3?version_id=1068—