Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 22

1 Yehova atero: Tsikira kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,

2 ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.

3 Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m’dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.

4 Pakuti ngati mudzachitadi ichi pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera m’magaleta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ake, ndi anthu ake.

5 Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.

6 Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.

7 Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zake; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m’moto.

8 Ndipoamitunduambiri adzapita pa mzinda uwu, nadzati yense kwa mnzake, Yehova anatero nao mzinda waukulu uwu chifukwa ninji?

9 Ndipo adzayankha, Chifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu ina, ndi kuitumikira.

10 Musamlirire wakufa, musachite maliro ake; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.

11 Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m’malo mwake mwa Yosiya atate wake, amene anatuluka m’malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iliyonse;

12 koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili.

13 Tsoka iye amene amanga nyumba yake ndi chisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi chosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzake ntchito osamlipira, osampatsa mphotho yake;

14 amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira tsindwi lam’kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.

15 Kodi udzakhala mfumu, chifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadye ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? Kumeneko kunamkomera.

16 Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Yehova.

17 Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.

18 Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! Kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! Kapena, Kalanga ine ulemerero wake!

19 Adzamuika monga kuika bulu, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata zaYerusalemu.

20 Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako mu Basani; nufuule mu Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha.

21 Ndinanena ndi iwe m’phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvere mau anga.

22 Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m’ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa chifukwa cha choipa chako chonse.

23 Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m’mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!

24 Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;

25 ndipo ndidzakupereka iwe m’dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m’dzanja la iwo amene uwaopa, m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, m’dzanja la Ababiloni.

26 Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m’dziko lina, limene sunabadwiremo; m’menemo udzafa.

27 Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako.

28 Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m’dziko limene salidziwa?

29 Iwe dziko, dziko, dziko lapansi, tamvera mau a Yehova.

30 Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso mu Yuda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/22-be03f905051d5fcc470d12846f260479.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 23

Mau akutsutsa abusa osakhulupirika

1 Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! Ati Yehova.

2 Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa Israele, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipirikitsa, ndipo simunazizonde; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa ntchito zanu, ati Yehova.

3 Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m’maiko onse m’mene ndinazipirikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso kumakola ao; ndipo zidzabalana ndi kuchuluka.

4 Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova.

Mphukira wa Davide

5 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m’dziko lino.

6 Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.

7 Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m’dziko la Ejipito;

8 koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israele kuwatulutsa m’dziko la kumpoto, ndi kumaiko onse kumene ndinawapirikitsirako, ndipo adzakhala m’dziko lao.

Mau akutsutsa aneneri onama

9 Za aneneri. Mtima wanga usweka m’kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.

10 Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.

11 Pakutimnenerindi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m’nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.

12 Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m’mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

13 Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera zaBaala, nasocheretsa anthu anga Israele.

14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.

15 Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse.

16 Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m’kamwa mwa Yehova.

17 Anena chinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m’kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu.

18 Pakuti ndani waima mu upo wa Yehova, kuti aone namve mau ake? Ndani wazindikira mau anga, nawamva?

19 Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa.

20 Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atachita, mpaka atatha maganizo a mtima wake; masiku otsiriza mudzachidziwa bwino.

21 Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanene ndi iwo, koma ananenera.

22 Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.

23 Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patali?

24 Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.

25 Ndamva chonena aneneri, amene anenera zonama m’dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.

26 Ichi chidzakhala masiku angati m’mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a chinyengo cha mtima wao?

27 Amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wake, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimtcha nalo Baala.

28 Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lake; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi chiyani polinganiza ndi tirigu? Ati Yehova.

29 Kodi mau anga safanafana ndi moto? Ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?

30 Chifukwa chake, taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene amaba mau anga, yense kumbera mnansi wake.

31 Taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene achita ndi malilime ao, ndi kuti, Ati Iye.

32 Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao achabe; koma Ine sindinatume iwo, sindinauze iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.

33 Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi chiyani? Pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakuchotsani inu, ati Yehova.

34 Koma za mneneri, ndi wansembe, ndi anthu, amene adzati, Katundu wa Yehova, ndidzamlanga munthuyo ndi nyumba yake.

35 Mudzatero yense kwa mnansi wake, ndi yense kwa mbale wake, Yehova wayankha chiyani? Ndipo Yehova wanena chiyani?

36 Ndipo katundu wa Yehova simudzatchulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wake; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu.

37 Uzitero kwa mneneri, Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanenanji?

38 Koma ngati muti, Katundu wa Yehova, chifukwa chake Yehova atero: Chifukwa muti mau awa, Katundu wa Yehova, ndipo ndatuma kwa inu, kuti, Musati, Katundu wa Yehova;

39 chifukwa chake, taonani, ndidzakuiwalani inu konse, ndipo ndidzakuchotsani, ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzauchotsa pamaso panga;

40 ndipo ndidzakutengerani inu chitonzo chamuyaya, ndi manyazi amuyaya, amene sadzawailika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/23-00573ef131fb76fc8dd805a98d9e6125.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 24

Za madengu awiri a nkhuyu; za mtundu wao m’tsogolo

1 Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am’nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa kuYerusalemu, nawatengera ku Babiloni.

2 Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.

3 Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona chiyani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.

4 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

5 Chifukwa Yehova, Mulungu wa Israele, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am’nsinga a Yuda, amene ndawachotsera m’malo muno kunka kudziko la Ababiloni, kuwachitira bwino.

6 Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.

7 Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziwa, kuti ndine Yehova, nadzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao.

8 Ndipo monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Chomwecho ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ake, ndi otsala a mu Yerusalemu, amene atsala m’dziko ili, ndi amene akhala m’dziko la Ejipito.

9 Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m’mene ndidzawapirikitsiramo.

10 Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi mliri mwa iwo, mpaka athedwa m’dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/24-ab180ed073e85176f7a0ba1b9de6849e.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 25

Atalangidwa Aisraele adzalangidwa amitundu ena omwe

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;

2 amenemneneriYeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala muYerusalemu, kuti,

3 Kuyambira chaka chakhumi ndi chitatu cha Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunena; koma simunamvere.

4 Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ake onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvere, simunatchere khutu lanu kuti mumve;

5 ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu, ndi kukhala m’dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;

6 musatsate milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, musautse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu; ndingachitire inu choipa.

7 Koma simunandimvere Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu ndi kuonapo choipa inu.

8 Chifukwa chake Yehova wa makamu atero: Popeza simunamvere mau anga,

9 taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.

10 Ndiponso ndidzawachotsera mau akusekera ndi mau akukondwera, ndi mau a mkwati, ndi mau a mkwatibwi, mau a mphero, ndi kuwala kwa nyali.

11 Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni zaka makumi asanu ndi awiri.

12 Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, chifukwa cha mphulupulu zao, ndi dziko la Ababiloni; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.

13 Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m’buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.

14 Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu aakulu adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa machitidwe ao, monga mwa ntchito ya manja ao.

15 Pakuti Yehova, Mulungu wa Israele, atero kwa ine, Tenga chikho cha vinyo wa ukaliwu padzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.

16 Ndipo adzamwa, nadzayenda dzandidzandi, nadzachita misala, chifukwa cha lupanga limene Ine ndidzatumiza mwa iwo.

17 Ndipo ndinatenga chikho padzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;

18 Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino;

19 Faraomfumu ya ku Ejipito, ndi atumiki ake, ndi akulu ake, ndi anthu ake onse;

20 ndi anthu onse osakanizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi,

21 Edomu, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni,

22 ndi mafumu onse a Tiro, ndi mafumu onse a Sidoni, ndi mafumu a chisumbu chimene chili patsidya pa nyanja;

23 Dedani, ndi Tema, ndi Buzi, ndi onse amene ameta m’mbali mwa tsitsi;

24 ndi amfumu onse a Arabiya, ndi mafumu onse a anthu osakanizidwa okhala m’chipululu;

25 ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a ku Mediya,

26 ndi mafumu onse a kumpoto, a kutali ndi a kufupi, wina ndi mnzake; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao.

27 Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, chifukwa cha lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.

28 Ndipo padzakhala, ngati akana kutenga chikho padzanja lako kuti amwe, uziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Kumwa muzimwa,

29 Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pa mzinda umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m’dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.

30 Chifukwa chake muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzatchula mau ake mokhalamo mwake moyera; adzabangulitsira khola lake; adzafuula, monga iwo akuponda mphesa, adzafuulira onse okhala m’dziko lapansi.

31 Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.

32 Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzatuluka kumtundu kunka m’mitundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

33 Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.

34 Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika.

35 Ndipo abusa adzasowa pothawira, mkulu wa zoweta adzasowa populumukira.

36 Mau akufuula abusa, ndi kukuwa mkulu wa zoweta! Pakuti Yehova asakaza busa lao.

37 Ndipo makola amtendere adzaonongeka chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.

38 Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/25-e9af955247c709db254f198f3addd49c.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 26

Yeremiya aneneratu za kupasuka kwa Kachisi ndi Yerusalemu. Atsutsidwapo afe

1 Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ochokera kwa Yehova, kuti,

2 Yehova atero: Ima m’bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa mizinda yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m’nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.

3 Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yake yoipa; kuti ndileke choipa, chimene ndinati ndiwachitire chifukwa cha kuipa kwa ntchito zao.

4 Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m’chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu,

5 kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvere;

6 pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.

7 Ndipo ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya alinkunena mau awa m’nyumba ya Yehova.

8 Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.

9 Bwanji mwanenera m’dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m’nyumba ya Yehova.

10 Ndipo pamene akulu a Yuda anamva zimenezi, anakwera kutuluka kunyumba ya mfumu kunka kunyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova.

11 Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mzinda uwu monga mwamva ndi makutu anu.

12 Pamenepo Yeremiya ananena kwa akulu onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mzinda uwu mau onse amene mwamva.

13 Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.

14 Koma ine, taonani, ndili m’manja anu; mundichitire ine monga mokomera ndi moyenera m’maso anu.

15 Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mzinda uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m’makutu anu.

16 Pamenepo akulu ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa: pakuti watinenera ife m’dzina la Yehova Mulungu wathu.

17 Ndipo anauka akulu ena a m’dziko, nati kwa msonkhano wa anthu, kuti,

18 Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero:Ziyoniadzalimidwa ngati munda,Yerusalemuadzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.

19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu.

20 Ndipo panalinso munthu amene ananenera m’dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mzinda uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya;

21 ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;

22 ndipo Yehoyakimu mfumu anatuma anthu ku Ejipito, Elinatani mwana wake wa Akibori, ndi anthu ena pamodzi ndi iye, anke ku Ejipito;

23 ndipo anamtulutsa Uriya mu Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m’manda a anthu achabe.

24 Koma dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asampereke m’manja a anthu kuti amuphe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/26-efa5ae6606a5317f75ecd515da624889.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 27

Yeremiya awachenjeza agonje kwa mfumu ya ku Babiloni

1 Poyamba kukhala mfumu Zedekiyamwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2 Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;

3 nuzitumize kwa mfumu ya Edomu, ndi kwa mfumu ya Mowabu, ndi kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kwa mfumu ya Tiro, ndi kwa mfumu ya Sidoni, ndi dzanja la amithenga amene afika kuYerusalemukwa Zedekiya mfumu ya Yuda;

4 nuwauze iwo anene kwa ambuyao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Muzitero kwa ambuyanu:

5 Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m’dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.

6 Tsopano ndapereka maiko onse awa m’manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga; ndiponso nyama zakuthengo ndampatsa iye kuti zimtumikire.

7 Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.

8 Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.

9 Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu, Musadzatumikira mfumu ya ku Babiloni;

10 pakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akuchotseni inu m’dziko lanu, kunka kutali kuti ndikupirikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.

11 Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m’dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.

12 Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m’goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.

13 Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi mliri, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babiloni?

14 Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babiloni; pakuti akunenerani zonama.

15 Pakuti sindinawatume iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m’dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.

16 Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babiloni posachedwa; pakuti akunenerani inu zonama.

17 Musamvere amenewa; mtumikireni mfumu ya ku Babiloni, ndipo mudzakhala ndi moyo; chifukwa chanji mzinda uwu udzakhala bwinja?

18 Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m’nyumba ya Yehova, ndi m’nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babiloni.

19 Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m’mzinda uwu,

20 zimene sanazitenge Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Babiloni; ndi akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu;

21 inde, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za zipangizo zotsala m’nyumba ya Yehova, ndi m’nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu;

22 adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang’anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/27-248ad33dcce3cb6f96bd97037358eedf.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 28

Yeremiya atsutsana ndi mneneri wonyenga, Hananiya

1 Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azurimneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m’nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,

2 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Ndathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.

3 Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m’nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anazichotsa muno, kunka nazo ku Babiloni;

4 ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am’nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.

5 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa Hananiya mneneri pamaso pa ansembe, ndi pamaso pa anthu onse amene anaima m’nyumba ya Yehova,

6 Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am’nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.

7 Koma mumvetu mau awa amene ndinena m’makutu anu, ndi m’makutu a anthu onse:

8 Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu aakulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za mliri.

9 Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

10 Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli pa khosi la Yeremiya, nalithyola.

11 Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Chomwecho ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babiloni zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulichotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anachoka.

12 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atathyola Hananiya mneneri goli kulichotsa pa khosi la Yeremiya, kuti,

13 Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Wathyola magoli amtengo; koma udzapanga m’malo mwao magoli achitsulo.

14 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Ndaika goli lachitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama zakuthengo.

15 Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutume iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.

16 Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.

17 Ndipo anafa Hananiya mneneri chaka chomwecho mwezi wachisanu ndi chiwiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/28-96111d6c19129eab8dfd1f8441622ff4.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 29

Kalata ya Yeremiya wolembera kwa Ayuda otengedwa kunka ku Babiloni

1 Amenewa ndi mau a kalata ija anatumiza Yeremiya mneneri kuchokera kuYerusalemukunka kwa akulu otsala a m’nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadinezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babiloni;

2 anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,

3 anatumiza kalatayo m’dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti,

4 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, kwa am’nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni:

5 Mangani nyumba, khalani m’menemo; limani minda, idyani zipatso zake;

6 tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu aamuna, patsani ananu aakazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.

7 Nimufune mtendere wa mzinda umene ndinakutengerani am’nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.

8 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.

9 Pakuti anenera kwa inu zonama m’dzina langa; sindinatume iwo, ati Yehova.

10 Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang’anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.

11 Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.

12 Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.

13 Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

14 Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupirikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.

15 Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri mu Babiloni.

16 Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m’mzinda uno, abale anu amene sanatulukire pamodzi ndi inu kundende;

17 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.

18 Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m’maufumu onse a dziko lapansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;

19 chifukwa sanamvere mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.

20 Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m’ndende, amene ndachotsa mu Yerusalemu kunka ku Babiloni.

21 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za Ahabu mwana wake wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wake wa Maaseiya, amene anenera zonama m’dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo iye adzawapha pamaso panu;

22 ndipo am’nsinga onse a Yuda amene ali mu Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaotcha m’moto;

23 chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m’dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.

24 Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti,

25 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Chifukwa watumiza makalata m’dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti,

26 Yehova anakuyesa iwe wansembe m’malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m’nyumba ya Yehova, oyang’anira munthu yense wamisala, wodziyesamneneri, kuti umuike iye m’zigologolo ndi m’goli.

27 Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu,

28 popeza watitumizira mau ku Babiloni, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m’menemo; limani minda, idyani zipatso zao?

29 Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m’makutu a Yeremiya mneneri.

30 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, akuti,

31 Uwatumizire mau am’nsinga onse, akuti, Atero Yehova za Semaya Mnehelamu: Chifukwa Semaya wanenera kwa inu, koma Ine sindinamtume, ndipo anakukhulupiritsani zonama;

32 chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/29-cea3dcb5f5a7a4399bde9f4c85037465.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 30

Yehova alonjeza kubweza undende wa anthu a Israele

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2 Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kuti, Lemba m’buku mau onse amene ndanena kwa iwe.

3 Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.

4 Awa ndi mau ananena Yehova za Israele ndi Yuda.

5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.

6 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?

7 Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m’menemo.

8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzathyola goli lake pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;

9 koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene Ndidzawaukitsira.

10 Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa.

11 Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.

12 Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuli kosapoleka ndi bala lako lili lowawa.

13 Palibe amene adzanenera mlandu wako, ulibe mankhwala akumanga nao bala lako.

14 Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka.

15 Chifukwa chanji ulirira bala lako? Kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka, ndakuchitira iwe izi.

16 Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusiridwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.

17 Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; chifukwa anatcha iwe wopirikitsidwa, nati, NdiyeZiyoni, amene kulibe munthu amfuna.

18 Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzachitira chifundo zokhalamo zake, ndipo mzinda udzamangidwa pamuunda pake, ndi chinyumba chidzakhala momwe.

19 Ndipo padzatuluka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzachulukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawachitiranso ulemu, sadzachepa.

20 Ana aonso adzakhala monga kale, ndipo msonkhano wao udzakhazikika pamaso panga, ndipo ndidzalanga onse amene akupsinja iwo.

21 Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova.

22 Ndipo inu mudzakhala anthu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu.

23 Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, chatuluka, chimphepo chakukokolola: chidzagwa pamutu pa oipa.

24 Mkwiyo waukali wa Yehova sudzabwerera, mpaka wachita, mpaka watha zomwe afuna kuchita m’mtima mwake: masiku akumaliza mudzachizindikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/30-8f3f361dedb646e2cccf0d7c429732f2.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 31

Mwa chikondi cha Mulungu adzabweza Israele

1 Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.

2 Atero Yehova, Anthu opulumuka m’lupanga anapeza chisomo m’chipululu; Israele, muja anakapuma.

3 Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.

4 Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.

5 Ndiponso udzalima minda ya mpesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa.

6 Pakuti lidzafika tsiku, limene alonda a pa mapiri a Efuremu adzafuula, Ukani inu, tikwere kuZiyonikwa Yehova Mulungu wathu.

7 Pakuti Yehova atero, Imbirani Yakobo ndi kukondwa, fuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israele.

8 Taonani, ndidzatenga iwo kudziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikulu lidzabwera kuno.

9 Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m’njira yoongoka m’mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba.

10 Tamvani mau a Yehova,amitunduinu, lalikirani m’zisumbu zakutali; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israele adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa achita ndi zoweta zake.

11 Pakuti Yehova wapulumutsa Yakobo, namuombola iye m’dzanja la iye amene anamposa mphamvu.

12 Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje waZiyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing’ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni.

13 Ndipo namwali adzasangalala m’masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.

14 Ndipo ndikhutitsa moyo wa ansembe ndi mafuta, ndipo anthu anga adzakhuta ndi zokoma zanga, ati Yehova.

Rakele adzatonthozedwa

15 Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.

16 Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti ntchito yako idzalandira mphotho, ati Yehova; ndipo adzabweranso kuchokera kudziko la mdani.

17 Ndipo chilipo chiyembekezero cha chitsirizo chako, ati Yehova; ndipo ana ako adzafikanso ku malire ao.

18 Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang’ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.

19 Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ntchafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, chifukwa ndinasenza chitonzo cha ubwana wanga.

20 Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.

Aisraele adzakhalanso bwino m’dziko mwao

21 Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang’anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israele, tatembenukiranso kumizinda yako iyi.

22 Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m’mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m’dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.

23 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m’dziko la Yuda ndi m’mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.

24 Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.

25 Pakuti ndakhutidwa mtima wolema, ndadzazanso mtima uliwonse wachisoni.

26 Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine.

27 Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.

28 Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang’anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang’anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.

29 Masiku omwewo sadzanenanso, Atate adya mphesa zowawa, ndi mano a ana ayayamira.

30 Koma yense adzafa chifukwa cha mphulupulu yake; yense amene adya mphesa zowawa, mano ake adzayayamira.

Pangano latsopano pakati pa Mulungu ndi anthu ake

31 Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda;

32 si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m’dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.

33 Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m’kati mwao, ndipo m’mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;

34 ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.

35 Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:

36 Ngati malembawa achoka pamaso panga, ati Yehova, pamenepo mbeunso ya Israele idzaleka kukhala mtundu pamaso panga kunthawi zonse.

37 Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzachotsa mbeu zonse za Israele chifukwa cha zonse anazichita, ati Yehova.

38 Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mzindawu udzamangidwira Yehova kuyambira pa Nsanja ya Hananele kufikira ku Chipata cha Kungodya.

39 Ndipo chingwe choyesera chidzatulukanso kulunjika ku chitunda cha Garebu, ndipo chidzazungulira kunka ku Gowa.

40 Ndipo chigwa chonse cha mitembo, ndi cha phulusa, ndi minda yonse kufikira kumtsinje wa Kidroni, kufikira kungodya kwa Chipata cha Akavalo kuloza kum’mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse kunthawi zamuyaya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/31-707978ad201dbf68b2c2abfea31f091a.mp3?version_id=1068—