Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 12

1 Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?

2 Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m’kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.

3 Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.

4 Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.

5 Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m’dziko lamtendere, udzachita chiyani m’kudzikuza kwa Yordani?

6 Pakuti ngakhale abale ako, ndi nyumba ya atate wako, ngakhale iwo anakunyenga iwe; ngakhale anakufuulira iwe; usamvere iwo, ngakhale anena nawe mau abwino.

Dziko lipasuka. Aneneratu za olipasula

7 Ndachoka kunyumba yanga, ndasiya cholowa changa; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m’dzanja la adani.

8 Cholowa changa chandisandukira mkango wa m’nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda.

9 Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m’thengo, mudze nazo zidye.

10 Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.

11 Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira.

12 Akufunkha afika pa mapiri oti see m’chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.

13 Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.

14 Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza cholowa chimene ndalowetsamo anthu anga Israele; taonani, ndidzazula iwo m’dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao.

15 Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawachitira chisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku cholowa chake, ndi yense kudziko lake.

16 Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira paliBaala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.

17 Koma ngati sakumva, ndidzazula mtundu umene wa anthu, kuuzula ndi kuuononga, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/12-a5de94c9e171e6ad6eab1ad83382b277.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 13

Fanizo la mpango wabafuta lifanizira kulangidwa kwao

1 Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m’chuuno mwako, usauike m’madzi.

2 Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kuvala m’chuuno mwanga.

3 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti,

4 Tenga mpango umene unaugula, umene uli m’chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m’menemo m’phanga la m’mwala.

5 Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Yufurate, monga Yehova anandiuza ine.

6 Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.

7 Ndipo ndinanka ku Yufurate, ndikukumba, nditenga mpango m’malo m’mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu.

8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

9 Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukulu kwaYerusalemu.

10 Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m’kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.

11 Pakuti monga mpango uthina m’chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.

12 Chifukwa chake uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?

13 Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m’dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu.

14 Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge.

15 Tamvani inu, Tcherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena.

16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanaphunthwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.

17 Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m’tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m’nsinga.

18 Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.

19 Mizinda ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda yense wachotsedwa m’ndende yenseyo, wachotsedwa m’nsinga.

20 Tukulani maso anu, taonani iwo amene achokera kumpoto; zili kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma?

21 Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako kukhala akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?

22 Ndipo ngati udzati m’mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zitendene zako zaphwetekwa.

23 Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.

24 Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.

25 Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.

26 Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.

27 Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m’munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/13-8ee6bba6039d2b9c06aa75be9d77a9f5.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 14

Yeremiya apempherera anthu

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za chilala.

2 Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu waYerusalemuwakwera.

3 Akulu ao atuma ang’ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao.

4 Chifukwa cha nthaka yochita ming’alu, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, afunda mitu yao.

5 Inde, mbawalanso ya m’thengo ibala nisiya ana ake, chifukwa mulibe udzu.

6 Mbidzi zinaima pamapiri oti see, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, chifukwa palibe udzu.

7 Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu.

8 Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m’dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?

9 Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.

Yehova osamvera pempherolo

10 Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao.

11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.

12 Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.

13 Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi chilala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.

14 Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m’dzina langa; sindinatume iwo, sindinauze iwo, sindinanene nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao.

15 Chifukwa chake atero Yehova za aneneri onenera m’dzina langa, ndipo sindinawatume, koma ati, Lupanga ndi chilala sizidzakhala m’dziko muno; ndi lupanga ndi chilala aneneriwo adzathedwa.

16 Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m’miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.

17 Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.

18 Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m’mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakutimnenerindi wansembe ayendayenda m’dziko osadziwa kanthu.

19 Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndiZiyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!

20 Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu.

21 Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.

22 Mwa zachabe za mitundu ya anthu zilipo kodi, zimene zingathe kuvumbitsa mvula? Kapena miyamba kubweretsa mivumbi? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? Ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/14-501b372628aa936d39973ae106cd13d7.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 15

Yehova akanadi kumvera

1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.

2 Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.

3 Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung’amba, mbalame za m’mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.

4 Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m’maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita muYerusalemu.

5 Pakuti ndani adzakuchitira iwe chisoni, Yerusalemu? Ndani adzakulirira iwe? Ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako?

6 Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m’mbuyo; chifukwa chake ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.

7 Ndawapeta ndi chopetera m’zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.

8 Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.

9 Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lake lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.

Kulira kwa Yeremiya, kuyankha kwa Yehova

10 Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.

11 Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi ya nsautso.

12 Kodi angathe munthu kuthyola chitsulo, chitsulo cha kumpoto, ndi mkuwa?

13 Chuma chako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wake, ichicho chidzakugwera chifukwa cha zochimwa zako zonse, m’malire ako onse.

14 Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako kudziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m’mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.

15 Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang’anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m’chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa.

16 Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.

17 Sindinakhala m’msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.

18 Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?

19 Chifukwa chake atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa cha mtengo wake ndi chonyansa, udzakhala ngati m’kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.

20 Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.

21 Ndipo ndidzakulanditsa iwe m’dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m’dzanja la oopsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/15-6b54fddbec1ce86e4278e81c0e2e9ba6.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 16

Aneneratu za kutengedwa ukapolo kwa Israele ndi kubweranso kwao

1 Ndiponso mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

2 Usatenge mkazi, usakhale ndi ana aamuna ndi aakazi m’malo muno.

3 Pakuti Yehova atero za ana aamuna ndi za ana aakazi akubadwa m’malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m’dziko muno:

4 Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.

5 Pakuti Yehova atero, Usalowe m’nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.

6 Akulu ndi ang’onong’ono adzafa m’dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;

7 anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao chifukwa cha akufa, anthu sadzapatsa iwo chikho cha kutonthoza kuti achimwe chifukwa cha atate ao kapena mai wao.

8 Usalowe m’nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa.

9 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwitibwi.

10 Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Chifukwa chake nchiyani kuti Yehova watinenera ife choipa chachikulu ichi? Mphulupulu yathu ndi yanji? Tchimo lathu lanji limene tachimwira Yehova Mulungu wathu?

11 Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa;

12 ndipo mwachita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wake woipa, kuti musandimvere Ine;

13 chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m’dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.

14 Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m’dziko la Ejipito.

15 Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuchokera kudziko la kumpoto, ndi kumaiko ena kumene anawapirikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso kudziko lao limene ndinapatsa makolo ao.

16 Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m’mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m’mapanga a m’matanthwe.

17 Pakuti maso anga ali panjira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.

18 Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao.

19 Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko,amitunduadzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.

20 Kodi munthu adzadzipangira yekha milungu, imene siili milungu?

21 Chifukwa chake, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/16-1b407fb52396f77521cd5150d05a6ee3.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 17

Tchimo la Yuda ndi losafafanizika

1 Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m’mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe ao.

2 Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao kumitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitali.

3 Iwe phiri langa la m’munda, ndidzapereka chuma chako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, chifukwa cha tchimo, m’malire ako onse.

4 Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m’dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m’mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.

Anthu azikhulupirira Yehova yekha

5 Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake.

6 Ndipo adzakhala ngati tsanya la m’chipululu, ndipo saona pamene chifika chabwino; koma adzakhala m’malo oumitsa m’chipululu, dziko lachikungu lopanda anthu.

7 Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova.

8 Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.

9 Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?

10 Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.

11 Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.

12 Malo opatulika athu ndiwo mpando wachifumu wa ulemerero, wokhazikika pamsanje chiyambire.

13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m’dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.

14 Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.

15 Taonani, ati kwa ine, Mau a Yehova ali kuti? Adze tsopano.

16 Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumire kuchokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumbe tsiku la tsoka; Inu mudziwa, chimene chinatuluka pa milomo yanga chinali pamaso panu.

17 Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la choipa.

18 Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza.

Za kusunga tsiku la Sabata

19 Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime mu Chipata cha Ana a Anthu, m’mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m’mene atulukamo, ndi m’zipata zonse zaYerusalemu;

20 ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala mu Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi;

21 atero Yehova: Tadzayang’anirani nokha, musanyamule katundu tsiku laSabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;

22 musatulutse katundu m’nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire ntchito ili onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;

23 koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve asalandire langizo.

24 Ndipo padzakhala, ngati mundimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mzinda uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira ntchito m’menemo;

25 pamenepo padzalowa pa zipata za mzinda uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; ndipo mzinda uwu udzakhala kunthawi zamuyaya.

26 Ndipo adzachokera kumizinda ya Yuda, ndi kumalo akuzungulira Yerusalemu, ndi kudziko la Benjamini, ndi kuchidikha, ndi kumapiri, ndi kumwera, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndilubani, ndi kudza nazo zamayamikiro, kunyumba ya Yehova.

27 Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m’zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/17-8e2b311aa4083ebce739626f64fe5aa1.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 18

Mbiya ya woumba. Anthu osalapa

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2 Tauka, tatsikira kunyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga.

3 Ndipo ndinatsikira kunyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba ntchito yake ndi njinga.

4 Ndipo pamene mbiya alikuiumba ndi dothi inaonongeka m’dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya ina, monga kunamkomera woumba kuiumba.

5 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

6 Nyumba ya Israele inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? Ati Yehova. Taonani, monga dothi m’dzanja la woumba, momwemo inu m’dzanja langa, nyumba ya Israele.

7 Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga;

8 ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka choipa chao, ndidzaleka choipacho ndidati ndiwachitire.

9 Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wake ndi kuuoka;

10 koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire.

11 Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m’Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu.

12 Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa.

13 Chifukwa chake atero Yehova; Funsanitu m’mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israele wachita chinthu choopsetsa kwambiri.

14 Kodi matalala a Lebanoni adzalephera pamwala wa m’munda? Kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutali?

15 Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m’njira zao, m’njira zakale, kuti ayende m’njira za m’mbali, m’njira yosatundumuka;

16 kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake.

17 Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum’mawa pamaso pa adani; ndidzayang’anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la Tsoka lao.

18 Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena maumneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.

19 Mundimvere ine, Yehova, mumve mau a iwo akulimbana ndi ine.

20 Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.

21 Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.

22 Mfuu umvekedwe m’nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.

23 Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m’nthawi ya mkwiyo wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/18-d1575486fef31cc1ed71d41dbd7d22ef.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 19

Nsupa ya woumba isweka, Yerusalemu apasuka

1 Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe;

2 nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;

3 nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala muYerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.

4 Chifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano achilendo, nafukizira m’menemo milungu ina, imene sanaidziwe, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda; nadzaza malo ano ndi mwazi wa osachimwa;

5 namanga misanje yaBaala, kuti apsereze ana ao m’menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauze, sindinachinene, sichinalowe m’mtima mwanga;

6 chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wake wa Hinomu, koma Chigwa Chophera anthu.

7 Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m’malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi padzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m’mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi.

8 Ndipo ndidzayesa mzindawu chodabwitsa, ndi chotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya chifukwa cha zopanda pake zonse.

9 Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m’nkhondo yozinga ndi m’kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.

10 Pamenepo uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe,

11 nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mzinda uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro mu Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.

12 Ndidzatero ndi malo ano, ati Yehova, ndi okhalamo, kusanduliza mzinda uwu ngati Tofeti;

13 ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.

14 Pamenepo Yeremiya anadza kuchokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m’bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse:

15 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mzinda uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/19-24cd5d3a1e39d9e68a6b982626dcc07b.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 20

Pasuri wansembe apanda Yeremiya, nammanga m’kaidi

1 Ndipo Pasuri mwana wake wa Imeri wansembe, amene anali kapitao wamkulu m’nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya alikunenera zimenezi.

2 Ndipo Pasuri anampanda Yeremiyamneneriyo, namuika matangadza amene anali mu Chipata cha Benjamini cha kumtunda, chimene chinali kunyumba ya Yehova.

3 Ndipo panali m’mawa mwake, kuti Pasuri anatulutsa Yeremiya m’matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanatche dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.

4 Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am’nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.

5 Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mzinda uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m’manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni.

6 Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m’nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babiloni, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza.

7 Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwapambana; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.

8 Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, Chiwawa ndi chofunkha; pakuti mau a Yehova ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse.

9 Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m’dzina lake, pamenepo m’mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.

10 Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang’anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.

11 Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.

12 Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona impso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera chilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga.

13 Muimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m’dzanja la ochita zoipa.

14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa; lisadalitsike tsiku limene amai wanga anandibala ine.

15 Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye.

16 Munthuyo akhale ngati mizinda imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;

17 chifukwa sanandiphe ine m’mimba; kuti mai wanga akhale manda anga, ndi mimba yake yaikulu nthawi zonse.

18 Chifukwa chanji ndinatuluka m’mimba kuti ndione kutopa ndi kulira, kuti masiku anga athe ndi manyazi?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/20-1062b3a578554cf0c3a97e8523edb082.mp3?version_id=1068—

Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 21

Kufunsira kwa Zedekiya, kuyankha kwa Yeremiya

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,

2 Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere.

3 Ndipo Yeremiya anati kwa iwo, Muzitero kwa Zedekiya:

4 Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m’manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.

5 Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m’mkwiyo, ndi m’kupsa mtima, ndi mu ukali waukulu.

6 Ndipo ndidzakantha okhalamo m’mzinda uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi mliri waukulu.

7 Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m’mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m’dzanja la adani ao, ndi m’dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.

8 Ndipo uziti kwa anthu awa, Yehova atero, Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa.

9 Iye amene akhala m’mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.

10 Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.

Aneneratu motsutsa mbumba yachifumu ya Yuda

11 Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:

12 Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m’mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m’dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.

13 Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m’chigwa, ndi pa thanthwe la m’chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m’zokhalamo zathu?

14 Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m’nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/21-05eda18790608ead0517e8b517a6043d.mp3?version_id=1068—