Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 23

1 Pamene ukhala ulinkudya ndi mkulu,

zikumbukira ameneyo ali pamaso pako;

2 nuike mpeni pakhosi pako,

ngati uli wadyera.

3 Usakhumbe zolongosoka zake;

pokhala zakudya zonyenga.

4 Usadzitopetse kuti ulemere;

leka nzeru yakoyako.

5 Kodi upenyeranji chimene kulibe?

Pakuti chuma chimera mapiko,

ngati mphungu youluka mumlengalenga.

6 Usadye zakudya zake za wa maso ankhwenzule,

ngakhale kukhumba zolongosoka zake.

7 Pakuti monga asinkha m’kati mwake, ali wotere;

ati kwa iwe, Idya numwe;

koma mtima wake suli pa iwe.

8 Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza,

ndi kutaya mau ako okondweretsa.

9 Usalankhule m’makutu a wopusa;

pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako.

10 Usasunthe chidziwitso chakale cha m’malire;

ngakhale kulowa m’minda ya amasiye;

11 pakuti Mombolo wao walimba;

adzawanenera mlandu wao pa iwe.

12 Lozetsa mtima wako kumwambo,

ndi makutu ako ku mau anzeru.

13 Usamane mwana chilango;

pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai.

14 Udzammenya ndi nthyole,

nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda.

15 Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru,

mtima wanga wa inedi udzakondwa.

16 Imso zanga zidzasangalala,

polankhula milomo yako zoongoka.

17 Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo;

koma opabe Yehova tsiku lonse.

18 Pakutitu padzakhala mphotho;

ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.

19 Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru,

ulunjikitse mtima wako m’njiramo.

20 Usakhale mwa akumwaimwa vinyo,

ndi ankhuli osusuka.

21 Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka;

ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

22 Tamvera atate wako anakubala,

usapeputse amai ako atakalamba.

23 Gula ntheradi, osaigulitsa;

nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.

24 Atate wa wolungama adzasekeradi;

wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.

25 Atate wako ndi amai ako akondwere,

amai ako akukubala asekere.

26 Mwananga, undipatse mtima wako,

maso ako akondwere ndi njira zanga.

27 Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya;

ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza.

28 Pakuti abisalira ngati wachifwamba,

nachulukitsa anthu a chiwembu.

29 Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka?

Ndani ali ndi makangano? Ndani ang’ung’udza?

Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso?

30 Ngamene achedwa pali vinyo,

napita kukafunafuna vinyo wosakanizidwa.

31 Usayang’ane pavinyo alikufiira,

alikung’azimira m’chikho,

namweka mosalala.

32 Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka,

najompha ngati mamba.

33 Maso ako adzaona zachilendo,

mtima wako udzalankhula zokhota.

34 Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja,

pena wogona pansonga ya mlongoti wa ngalawa.

35 Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine;

anandikwapula, osamva ine;

ndidzauka nthawi yanji?

Ndidzafunafunanso vinyoyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/23-31ad928ab24bdf4ab95ef06141cbdc8d.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 24

1 Usachitire nsanje anthu oipa,

ngakhale kufuna kukhala nao;

2 pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko;

milomo yao ilankhula za mphulupulu.

3 Nzeru imangitsa nyumba;

luntha liikhazikitsa.

4 Kudziwa kudzaza zipinda zake

ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.

5 Mwamuna wanzeru ngwamphamvu;

munthu wodziwa ankabe nalimba.

6 Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo,

ndi kupulumuka pochuluka aphungu.

7 Nzeru italikira chitsiru;

satsegula pakamwa kubwalo.

8 Wolingalira zakuchita zoipa

anthu adzamtcha wachiwembu.

9 Maganizo opusa ndiwo tchimo;

wonyoza anyansa anthu.

10 Ukalefuka tsiku la tsoka

mphamvu yako ichepa.

11 Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse;

omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa.

12 Ukanena, Taonani, sitinadziwe chimenechi;

kodi woyesa mitima sachizindikira ichi?

Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa?

Ndipo kodi sabwezera munthu yense

monga mwa machitidwe ake?

13 Mwananga, idya uchi pakuti ngwabwino,

ndi chisa chake chitsekemera m’kamwa mwako.

14 Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m’moyo wako;

ngati waipeza padzakhala mphotho,

ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.

15 Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama;

usapasule popuma iyepo.

16 Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso;

koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.

17 Usakondwere pakugwa mdani wako;

mtima wako usasekere pokhumudwa iye;

18 kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa,

ndi kuleka kumkwiyira.

19 Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa;

ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu.

20 Pakuti woipayo sadzalandira mphotho;

nyali ya amphulupulu idzazima.

21 Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe,

osadudukira anthu osinthasintha.

22 Pakuti tsoka lao lidzaoneka modzidzimuka;

ndipo ndani adziwa chionongeko cha zaka zao?

23 Izinso zili za anzeru,

poweruza chetera silili labwino.

24 Wonena kwa woipa, Wolungama iwe;

magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira.

25 Omwe amdzudzula adzasekera,

nadzadalitsika ndithu.

26 Wobwezera mau oongoka

apsompsona milomo.

27 Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda;

pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.

28 Usachitire mnzako umboni womtsutsa opanda chifukwa;

kodi udzanyenga ndi milomo yako?

29 Usanene, Ndidzamchitira zomwezo anandichitira ine

ndidzabwereza munthuyo monga mwa machitidwe ake.

30 Ndinapita pamunda wa waulesi,

polima mphesa munthu wosowa nzeru.

31 Taonani, ponsepo panamera minga,

ndi kuwirirapo khwisa;

tchinga lake lamiyala ndi kupasuka.

32 Pamenepo ndinayang’ana ndi kuganizira,

ndinaona ndi kulandira mwambo.

33 Tulo tapang’ono, kungoodzera pang’ono,

kungomanga manja pang’ono m’kugona,

34 ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala;

ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/24-d041c432688e739b0966df167545db65.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 25

Miyambo ya Solomoni yosonkhanitsa nthawi ya Hezekiya

1 Iyinso ndiyo miyambo ya Solomoni

imene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.

2 Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu;

koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.

3 Pamlengalenga patalika, ndi padziko pakuya,

koma mitima ya mafumu singasanthulike.

4 Chotserasilivamphala yake,

mmisiri wa ng’anjo atulutsamo mbale.

5 Chotsera woipa pamaso pa mfumu,

mpando wake udzakhazikika m’chilungamo.

6 Usadzitame pamaso pa mfumu,

ngakhale kuima m’malo mwa akulu.

7 Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno,

kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga,

amene maso ako anamuona.

8 Usatuluke mwansontho kukalimbana,

ungalephere pa kutha kwake,

atakuchititsa mnzako manyazi.

9 Nena mlandu wako ndi mnzako,

osawulula zinsinsi za mwini;

10 kuti wakumva angakutonze,

mbiri yako yoipa ndi kusachoka.

11 Mau oyenera a pa nthawi yake

akunga zipatso zagolide m’nsengwa zasiliva.

12 Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka,

momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.

13 Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika,

momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma;

atsitsimutsa moyo wa ambuyake.

14 Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula,

momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.

15 Chipiriro chipembedza mkulu;

lilime lofatsa lithyola fupa.

16 Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira,

kuti ungakukole, nusanze.

17 Phazi lako lilowe m’nyumba ya mnzako kamodzikamodzi;

kuti angatope nawe ndi kukuda.

18 Wochitira mnzake umboni wonama

ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.

19 Kukhulupirira munthu wa chiwembu tsiku latsoka

kunga dzino lothyoka ndi phazi loguluka.

20 Monga wovula malaya tsiku lamphepo,

ngakhale kuthira vinyo wosasa m’soda,

momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni.

21 Mdani wako akamva njala umdyetse,

akamva ludzu ummwetse madzi.

22 Pakuti udzaunjika makala amoto pamutu pake;

ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.

23 Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula;

chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.

24 Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika

kuposa kukhala m’nyumba ndi mkazi wolongolola.

25 Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa,

momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali.

26 Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka,

momwemo wolungama ngati agonjera woipa.

27 Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino;

chomwecho kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu.

28 Wosalamulira mtima wake

akunga mzinda wopasuka wopanda linga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/25-40ef2cfb514d1d550f773dc0220cfe21.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 26

1 Monga chipale chofewa m’malimwe, ndi mvula m’masika,

momwemo ulemu suyenera chitsiru.

2 Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka,

momwemo temberero la pachabe silifikira.

3 Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham’kamwa chiyenera bulu,

ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru.

4 Usayankhe chitsiru monga mwa utsiru wake,

kuti ungafanane nacho iwe wekha.

5 Yankha chitsiru monga mwa utsiru wake,

kuti asadziyese wanzeru.

6 Wotumiza mau ndi dzanja la chitsiru

adula mapazi ake, namwa zompweteka.

7 Miyendo ya wopunduka ili yolobodoka,

momwemo mwambi m’kamwa mwa zitsiru.

8 Monga thumba la ngale m’mulu wa miyala,

momwemo wochitira chitsiru ulemu.

9 Monga munga wolasa dzanja la woledzera,

momwemo mwambi m’kamwa mwa zitsiru.

10 Monga woponya mivi ndi kulasa onse,

momwemo wolembera chitsiru,

ndi wolembera omwe alikupita panjira.

11 Monga galu abweranso kumasanzi ake,

momwemo chitsiru chichitanso zopusa zake.

12 Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru?

Ngakhale chitsiru chidzachenjera koma ameneyo ai.

13 Waulesi ati, Mkango uli panjira,

wobangulawo uli m’makwalala.

14 Monga chitseko chikankhikira pa zitsulo za pamphuthu,

momwemo waulesi agubuduka pakama pake.

15 Waulesi alonga dzanja lake m’mbale;

kumtopetsa kulibweza kukamwa kwake.

16 Waulesi adziyesa wanzeru

koposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira.

17 Wakungopita ndi kuvutika ndi ndeu yosakhala yake

akunga wogwira makutu a galu.

18 Monga woyaluka woponya nsakali,

mivi, ndi imfa,

19 momwemo wonyenga mnzake ndi kuti,

ndi kusewera kumeneku.

20 Posowa nkhuni moto ungozima;

ndi popanda kazitape makangano angoleka.

21 Monga makala ozizira pa makala akunyeka,

ndi nkhuni pamoto;

momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.

22 Mau a kazitape ndi zakudya zolongosoka

zitsikira m’kati mwa mimba.

23 Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa

ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva.

24 Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake;

koma akundika chinyengo m’kati mwake.

25 Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire;

pakuti m’mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.

26 Angakhale abisa udani wake pochenjera,

koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.

27 Wokumba dzenje adzagwamo,

wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.

28 Lilime lonama lida omwewo linawasautsa;

ndipo m’kamwa mosyasyalika mungoononga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/26-5c6ccb3e673edac2f1b7f6d743fb9f2d.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 27

1 Usanyadire zamawa,

popeza sudziwa tsiku lina lidzabala chiyani?

2 Wina akutume, si m’kamwa mwako ai;

mlendo, si milomo ya iwe wekha.

3 Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu;

koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.

4 Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka;

koma ndani angalakike ndi nsanje?

5 Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika.

6 Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika;

koma mdani apsompsona kawirikawiri.

7 Mtima wokhuta upondereza chisa cha uchi;

koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.

8 Monga mbalame yosochera kuchisa chake,

momwemo munthu wosochera kumalo ake.

9 Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima,

ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.

10 Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye;

usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako;

mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.

11 Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga;

kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.

12 Wochenjera aona zoipa, nabisala;

koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.

13 Tenga malaya a woperekera mlendo chikole;

woperekera mkazi wachiwerewere chikole umgwire mwini.

14 Yemwe adalitsa mnzake ndi mau aakulu pouka mamawa,

anthu adzachiyesa chimenecho temberero.

15 Kudonthadontha tsiku lamvula,

ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.

16 Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo;

dzanja lake lamanja lingogwira mafuta.

17 Chitsulo chinola chitsulo;

chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.

18 Wosunga mkuyu adzadya zipatso zake;

wosamalira ambuyake adzalemekezedwa.

19 Monga m’madzi nkhope zionana,

momwemo mitima ya anthu idziwana.

20 Kunsi kwa manda ndi kuchionongeko sikukhuta;

ngakhale maso a munthu sakhutai.

21 Silivaasungunuka m’mbiya,

ndi golide m’ng’anjo,

motero chomwe munthu achitama adziwika nacho.

22 Ungakhale ukonola chitsiru m’mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale,

koma utsiru wake sudzamchoka.

23 Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji,

samalira magulu ako;

24 pakuti chuma sichili chosatha;

kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.

25 Amatuta udzu, msipu uoneka,

atchera masamba a kumapiri.

26 Anaankhosa akuveka,

atonde aombolera munda;

27 mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya;

ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/27-622317ae4643f2833d73206325c895f5.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 28

Mau olinganiza zosiyana

1 Woipa athawa palibe momthamangitsa;

koma olungama alimba mtima ngati mkango.

2 Pochimwa dziko akalonga ake achuluka;

koma anthu ozindikira ndi odziwa

alikhazikikitsa nthawi yaikulu.

3 Munthu waumphawi wotsendereza osauka

akunga mvula yamadzi yokokolola dzinthu.

4 Omwe asiya chilamulo atama oipa;

koma omwe asunga chilamulo akangana nao.

5 Oipa samvetsetsa chiweruzo;

koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse.

6 Waumphawi woyenda mwangwiro

apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.

7 Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira;

koma mnzao wa adyera achititsa atate wake manyazi.

8 Wochulukitsa chuma chake, pokongoletsa ndi phindu,

angokundikira yemwe achitira osauka chisoni.

9 Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo,

ngakhale pemphero lake linyansa.

10 Wosocheretsa oongoka mtima alowe m’njira yoipa,

adzagwa mwini m’dzenje lake;

koma angwiro adzalandira cholowa chabwino.

11 Wolemera adziyesa wanzeru;

koma wosauka wozindikira aululitsa zake.

12 Posekera olungama pali ulemerero wambiri;

koma pouka oipa anthu amabisala.

13 Wobisa machimo ake sadzaona mwai;

koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.

14 Wodala munthu wakuopa kosalekeza;

koma woumitsa mtima wake adzagwa m’zoipa.

15 Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda,

momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.

16 Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa;

koma yemwe ada chisiriro adzatanimphitsa moyo wake.

17 Wopalamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje;

asamuletse.

18 Woyenda mwangwiro adzapulumuka;

koma wokhota m’mayendedwe ake adzagwa posachedwa.

19 Wolima munda wake zakudya zidzamkwanira;

koma wotsata anthu opanda pake umphawi udzamkwanira.

20 Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri;

koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.

21 Chetera silili labwino,

ngakhale kulakwa kuti ukadye kanthu.

22 Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera,

osadziwa kuti umphawi udzamfikira.

23 Adzamkomera mtima wodzudzula m’tsogolo mwake,

koposa wosyasyalika ndi lilime lake.

24 Wobera atate wake, pena amake, nati, Palibe kulakwa;

ndiye mnzake wa munthu wopasula.

25 Wodukidwa mtima aputa makangano;

koma wokhulupirira Yehova adzakula.

26 Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa;

koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.

27 Wogawira aumphawi sadzasowa;

koma wophimba maso ake adzatembereredwa kwambiri.

28 Pouka oipa anthu amabisala;

koma pakufa amenewo olungama achuluka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/28-9657f1c463c151f413bb32405a142b8a.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 29

1 Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri,

adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.

2 Pochuluka olungama anthu akondwa;

koma polamulira woipa anthu ausa moyo.

3 Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake;

koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma.

4 Mfumu akhazikitsa dziko ndi chiweruzo;

koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa.

5 Wosyasyalika mnzake

atcherera mapazi ake ukonde.

6 M’kulakwa kwa woipa muli msampha;

koma wolungama aimba, nakondwera.

7 Wolungama asamalira mlandu wa osauka;

koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.

8 Anthu onyoza atentha mzinda;

koma anzeru alezetsa mkwiyo.

9 Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa,

ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.

10 Anthu ankhanza ada wangwiro;

koma oongoka mtima asamalira moyo wake.

11 Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse;

koma wanzeru auletsa nautontholetsa.

12 Mkulu akamvera chinyengo,

atumiki ake onse ali oipa.

13 Waumphawi ndi wotsendereza akumana;

Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo.

14 Mfumu yolamulira osauka mwantheradi,

mpando wake udzakhazikika kufikira nthawi zonse.

15 Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru;

koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.

16 Pochuluka oipa zolakwa zichuluka;

koma olungama adzaona kugwa kwao.

17 Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa;

nadzasangalatsa moyo wako.

18 Popanda chivumbulutso anthu amasauka;

koma wosunga chilamulo adalitsika.

19 Kapolo sangalangizidwe ndi mau,

pakuti azindikira koma osavomera.

20 Kodi uona munthu wansontho m’mau ake?

Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai.

21 Yemwe alera kapolo wake mwa ufulu kuyambira ubwana wake,

pambuyo pake adzadziyesa mwana wobala.

22 Mwamuna wamkwiyo aputa makangano;

waukali achuluka zolakwa.

23 Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa;

koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.

24 Woyenda ndi mbala ada moyo wakewake;

amva kulumbira, koma osawulula kanthu.

25 Kuopa anthu kutchera msampha;

koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.

26 Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu;

koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova.

27 Munthu woipa anyansa olungama;

ndipo woongoka m’njira anyansa wochimwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/29-e0e661a79b323b61f7b9284f54a3320d.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 30

Chivomerezo, pemphero ndi malangizo a Aguri

1 Mau a Aguri mwana wa Yake; uthenga.

Munthuyo anati, Ndadzitopetsa, Mulungu;

ndadzitopetsa, Mulungu, ndathedwa;

2 pakuti ndipambana anthu onse kupulukira,

ndilibe luntha la munthu.

3 Sindinaphunzire nzeru

ngakhale kudziwa Woyerayo.

4 Ndani anakwera kumwamba natsikanso?

Ndani wakundika nafumbata mphepo?

Ndani wamanga madzi m’malaya ake?

Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko?

Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.

5 Mau onse a Mulungu ali oyengeka;

ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.

6 Usaonjezere kanthu pa mau ake,

angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama.

7 Zinthu ziwiri ndakupemphani,

musandimane izo ndisanamwalire:

8 Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza;

musandipatse umphawi, ngakhale chuma,

mundidyetse zakudya zondiyenera;

9 ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani?

Kapena ndingasauke ndi kuba,

ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

10 Usanamizire kapolo kwa mbuyake,

kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.

11 Pali mbadwo wotemberera atate ao,

osadalitsa amai ao.

12 Pali mbadwo wodziyesa oyera,

koma osasamba litsiro lao.

13 Pali mbadwo wokwezatu maso ao,

zikope zao ndi kutukula.

14 Pali mbadwo mano ao akunga malupanga,

zibwano zao zikunga mipeni;

kuti adye osauka kuwachotsa kudziko,

ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.

15 Msundu uli ndi ana aakazi awiri ati, Patsa, patsa.

Pali zinthu zitatu sizikhuta konse,

ngakhale zinai sizinena, Kwatha:

16 Manda, ndi chumba,

dziko losakhuta madzi,

ndi moto wosanena, Kwatha.

17 Diso lochitira atate wake chiphwete,

ndi kunyoza kumvera amake,

makwangwala a kumtsinje adzalikolowola,

ana a mphungu adzalidya.

18 Zinthu zitatu zindithetsa nzeru,

ngakhale zinai, sindizidziwa:

19 Njira ya mphungu m’mlengalenga,

njira ya njoka pamwala,

njira ya ngalawa pakati pa nyanja,

njira ya mwamuna ndi namwali.

20 Chomwecho njira ya mkazi wachigololo;

adya, napukuta pakamwa, nati,

Sindinachite zoipa.

21 Chifukwa cha zinthu zitatu dziko linthunthumira;

ngakhale chifukwa cha zinai silingathe kupirira nazo;

22 chifukwa cha kapolo pamene ali mfumu;

ndi chitsiru chitakhuta zakudya;

23 chifukwa cha mkazi wodedwa wokwatidwa;

ndi mdzakazi amene adzalandira cholowa cha mbuyake.

24 Zilipo zinai zili zazing’ono padziko;

koma zipambana kukhala zanzeru:

25 Nyerere ndi mtundu wosalimba,

koma zitengeratu zakudya zao m’malimwe.

26 Mbira ndi mtundu wopanda mphamvu,

koma ziika nyumba zao m’matanthwe.

27 Dzombe lilibe mfumu,

koma lituluka lonse mabwalomabwalo.

28 Buluzi ungamgwire m’manja,

koma ali m’nyumba za mafumu.

29 Pali zinthu zitatu ziyenda chinyachinya;

ngakhale zinai ziyenda mwaufulu:

30 Mkango umene uposa zilombo kulimba,

supatukira chinthu chilichonse;

31 tambala wolimba m’chuuno, ndi tonde,

ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake.

32 Ngati wapusa podzikweza,

ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa.

33 Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo;

ndi popsinja mfuno, mwazi utulukamo,

ndi polimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/30-db9df611125b9f92b067f0360681c25b.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 31

Malangizo a mai wa Lemuwele

1 Mau a Lemuwele mfumu, uthenga umene amake anamphunzitsa.

2 Chiyani mwananga, Chiyani mwana wa mimba yanga?

Chiyani mwana wa zowinda zanga?

3 Musapereke mphamvu yako kwa akazi,

ngakhale kuyenda m’njira yoononga mafumu.

4 Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo;

akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti?

5 Kuti angamwe, naiwale malamulo,

naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.

6 Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali,

ndi vinyo kwa owawa mtima;

7 amwe, naiwale umphawi wake,

osakumbukiranso vuto lake.

8 Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula,

ndi mlandu wa amasiye onse.

9 Tsegula pakamwa pako

nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.

10 Mkazi wangwiro ndani angampeze?

Pakuti mtengo wake uposa ngale.

11 Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira,

sadzasowa phindu.

12 Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa,

masiku onse a moyo wake.

13 Afuna ubweya ndi thonje,

nachita mofunitsa ndi manja ake.

14 Akunga zombo za malonda;

nakatenga zakudya zake kutali.

15 Aukanso kusanake,

napatsa banja lake zakudya, nagawira adzakazi ake ntchito.

16 Asinkhasinkha za munda, naugula;

naoka mipesa ndi zipatso za manja ake.

17 Amanga m’chuuno mwake ndi mphamvu,

nalimbitsa mikono yake.

18 Azindikira kuti malonda ake ampindulira;

nyali yake sizima usiku.

19 Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake,

nafumbata mtengo wake.

20 Aolowera chikhato chake osauka;

natambasulira aumphawi manja ake.

21 Saopera banja lake chipale chofewa;

pakuti banja lake lonse livala mlangali.

22 Adzipangira zimbwi zamawangamawanga;

navala bafuta ndi guta wofiirira.

23 Mwamuna wake adziwika kubwalo,

pokhala pakati pa akulu a dziko.

24 Asoka malaya abafuta, nawagulitsa;

napereka mipango kwa ogulitsa malonda.

25 Avala mphamvu ndi ulemu;

nangoseka nthawi ya m’tsogolo.

26 Atsegula pakamwa pake ndi nzeru,

ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.

27 Ayang’anira mayendedwe a banja lake,

sadya zakudya za ulesi.

28 Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala;

mwamuna wake namtama, nati,

29 Ana aakazi ambiri anachita mwangwiro,

koma iwe uposa onsewo.

30 Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe;

koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

31 Mumpatse zipatso za manja ake;

ndi ntchito zake zimtame kubwalo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/31-3d11d4411361f4cf307575b7480eae73.mp3?version_id=1068—

Categories
MLALIKI

MLALIKI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli lipereka maganizo a Mphunzitsi wina amene adayesetsa kumvetsa za moyo wa munthu; poona kuti moyowo sukhalira kutha ndiponso ndi wodzaza ndi mavuto, poonanso kuti zinthu siziyenda motsata chilungamo monga momwe mwini wake ankayembekezera. Mlalikiyo atafufuza zonsezi anagoti, “Zachabechabe…zachabechabe zonse ndi chabe.” Sankamvetsa njira zake za Mulungu, amene amaongolera moyo wa anthu ndi zinthu zina zonse mwa njira yodziwa Iye yekha, potsata zomwe Iye amaganizira pa chiyambi. Komabe Mlalikiyo akuwauza anthu kuti agwire ntchito molimbika ndiponso azikondwerera mphatso za Mulungu mpaka kukhutira pa nthawi yonse ya moyo wao.

Mwina anthu sangavomerezane ndi maganizo ambiri a Mlaliki, poona kuti maganizowo ngokayikitsa ndi otayitsa mtima. Komabe popeza kuti bukuli lipezeka mu Baibulo, ndiye kuti ngakhale maganizo amenewa angathe kuthandiza anthu ambiri kumvetsa za m’mene moyo wao uliri, akamasinkhasinkha mau ena ambiri a mu Baibulo momwemo onena za madalitso aakulu amene Mulungu wasungira anthu okhulupirira Iyeyo.

Za mkatimu

Kodi moyo uli ndi cholinga?

1.1—2.26

Zonena zokhudza moyo

3.1—11.8

Malangizo otsiriza

11.9—12.8

Mau omaliza

12.9-14