Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 13

1 Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate;

koma wonyoza samvera chidzudzulo.

2 Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m’kamwa mwake;

koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.

3 Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake;

koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.

4 Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu;

koma moyo wa akhama udzalemera.

5 Wolungama ada mau onama;

koma woipa anyansa, nadzichititsa manyazi.

6 Chilungamo chitchinjiriza woongoka m’njira;

koma udyo ugwetsa wochimwa.

7 Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;

alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.

8 Chiombolo cha moyo wa munthu ndicho chuma chake;

koma wosauka samva chidzudzulo.

9 Kuunika kwa olungama kukondwa;

koma nyali ya oipa idzazima.

10 Kudzikuza kupikisanitsa;

koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.

11 Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa;

koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.

12 Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima;

koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.

13 Wonyoza mau adziononga yekha;

koma woopa malangizo adzalandira mphotho.

14 Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,

apatutsa kumisampha ya imfa.

15 Nzeru yabwino ipatsa chisomo;

koma njira ya achiwembu ili makolokoto.

16 Yense wochenjera amachita mwanzeru;

koma wopusa aonetsa utsiru.

17 Mthenga wolakwa umagwa m’zoipa;

koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.

18 Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;

koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.

19 Chifuniro chikondweretsa moyo chitachitidwa;

koma kusiya zoipa kunyansa opusa.

20 Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:

koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.

21 Zoipa zilondola ochimwa;

koma olungama adzalandira mphotho yabwino.

22 Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino;

koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.

23 M’kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;

koma zinazo zimaonongeka posowa chiweruzo.

24 Wolekerera mwanake osammenya amuda;

koma womkonda amyambize kumlanga.

25 Wolungama adya nakhutitsa moyo wake;

koma mimba ya oipa idzasowa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/13-7e0058e913f39c50a46da6638a98fbd4.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 14

1 Mkazi yense wanzeru amanga banja lake;

koma wopusa alipasula ndi manja ake.

2 Woyenda moongoka mtima aopa Yehova;

koma wokhota m’njira yake amnyoza.

3 M’kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza;

koma milomo ya anzeru idzawasunga.

4 Popanda zoweta modyera muti see;

koma mphamvu ya ng’ombe ichulukitsa phindu.

5 Mboni yokhulupirika siidzanama;

koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

6 Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;

koma wozindikira saona vuto m’kuphunzira.

7 Pita pamaso pa munthu wopusa,

sudzazindikira milomo yakudziwa.

8 Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake;

koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.

9 Zitsiru zinyoza kupalamula;

koma mwa oongoka mtima muli chiyanjano.

10 Mtima udziwa kuwawa kwakekwake;

mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.

11 Nyumba ya oipa idzapasuka;

koma hema wa oongoka mtima adzakula.

12 Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;

koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.

13 Ngakhale m’kuseka mtima uwawa;

ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.

14 Wobwerera m’mbuyo m’mtima adzakhuta njira yake;

koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.

15 Wachibwana akhulupirira mau onse;

koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.

16 Wanzeru amaopa nasiya zoipa;

koma wopusa amanyada osatekeseka.

17 Wokangaza kukwiya adzachita utsiru;

ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.

18 Achibwana amalandira cholowa cha utsiru;

koma ochenjera amavala nzeru ngati korona.

19 Oipa amagwadira abwino,

ndi ochimwa pa makomo a olungama.

20 Waumphawi adedwa ndi anzake omwe;

koma akukonda wolemera achuluka.

21 Wonyoza anzake achimwa;

koma wochitira osauka chifundo adala.

22 Kodi oganizira zoipa sasochera?

Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.

23 M’ntchito zonse muli phindu;

koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.

24 Korona wa anzeru ndi chuma chao;

utsiru wa opusa ndiwo utsiru.

25 Mboni yoona imalanditsa miyoyo;

koma wolankhula zonama angonyenga.

26 Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;

ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

27 Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,

kupatutsa kumisampha ya imfa.

28 Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;

koma popanda anthu kalonga aonongeka.

29 Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;

koma wansontho akuza utsiru.

30 Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;

koma nsanje ivunditsa mafupa.

31 Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake;

koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.

32 Wochimwa adzakankhidwa m’kuipa kwake;

koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.

33 Nzeru ikhalabe m’mtima wa wozindikira,

nidziwika pakati pa opusa.

34 Chilungamo chikuza mtundu wa anthu;

koma tchimo lichititsa fuko manyazi.

35 Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru;

koma idzakwiyira wochititsa manyazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/14-9edb0598af40259cf8f0a0a5776b6b60.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 15

1 Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo;

koma mau owawitsa aputa msunamo.

2 Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa;

koma m’kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.

3 Maso a Yehova ali ponseponse,

nayang’anira oipa ndi abwino.

4 Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo;

koma likakhota liswa moyo.

5 Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake;

koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.

6 M’nyumba ya wolungama muli katundu wambiri;

koma m’phindu la woipa muli vuto.

7 Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru,

koma mtima wa opusa suli wolungama.

8 Nsembe ya oipa inyansa Yehova;

koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.

9 Njira ya oipa inyansa Yehova;

koma akonda wolondola chilungamo.

10 Wosiya njira adzalangidwa mowawa;

wakuda chidzudzulo adzafa.

11 Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova;

koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?

12 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa,

samapita kwa anzeru.

13 Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;

koma moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima.

14 Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;

koma m’kamwa mwa opusa mudya utsiru.

15 Masiku onse a wosauka ali oipa;

koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.

16 Zapang’ono, ulikuopa Yehova,

zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.

17 Kudya masamba, pali chikondano,

kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.

18 Munthu wozaza aputa makani;

koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

19 Mayendedwe a waulesi akunga linga laminga,

koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu.

20 Mwana wanzeru akondweretsa atate wake;

koma munthu wopusa apeputsa amake.

21 Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru;

koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake.

22 Zolingalira zizimidwa popanda upo;

koma pochuluka aphungu zikhazikika.

23 Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m’kamwa mwake;

ndi mau a pa nthawi yake kodi sali abwino?

24 Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera,

kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda.

25 Yehova adzapasula nyumba ya wonyada;

koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake.

26 Ziwembu zoipa zinyansa Yehova;

koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.

27 Wopindula monyenga avuta nyumba yake;

koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.

28 Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;

koma m’kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.

29 Yehova atalikira oipa;

koma pemphero la olungama alimvera.

30 Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;

ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.

31 Khutu lomvera chidzudzulo cha moyo

lidzakhalabe mwa anzeru.

32 Wokana mwambo apeputsa moyo wake;

koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru.

33 Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru;

ndipo chifatso chitsogolera ulemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/15-bf725c31508083cb97a33647d1ef2100.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 16

1 Malongosoledwe a mtima nga munthu;

koma mayankhidwe a lilime achokera kwa Yehova.

2 Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake;

koma Yehova ayesa mizimu.

3 Pereka zochita zako kwa Yehova,

ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

4 Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao;

ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.

5 Yense wonyada mtima anyansa Yehova;

zoonadi sadzapulumuka chilango.

6 Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi;

apatuka pa zoipa poopa Yehova.

7 Njira za munthu zikakonda Yehova

ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.

8 Zapang’ono, pokhala chilungamo,

ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.

9 Mtima wa munthu ulingalira njira yake;

koma Yehova ayendetsa mapazi ake.

10 Mau a mlauli ali m’milomo ya mfumu;

m’kamwa mwake simudzachita chetera poweruza.

11 Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova;

ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m’thumba.

12 Kuchita mphulupulu kunyansa mafumu;

pakuti mpando wao wakhazikika ndi chilungamo.

13 Milomo yolungama ikondweretsa mafumu;

wonena zoongoka amkonda.

14 Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa;

wanzeru adzaukhulula.

15 M’kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo;

kukoma mtima kwake kunga mtambo wa mvula ya masika.

16 Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide,

kulandira luntha ndi kusankhika koposasiliva?

17 Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;

wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake.

18 Kunyada kutsogolera kuonongeka;

mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.

19 Kufatsa mtima ndi osauka

kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.

20 Wolabadira mau adzapeza bwino;

ndipo wokhulupirira Yehova adala.

21 Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera;

ndipo kukoma kwa milomo kuonjezera kuphunzira.

22 Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake;

koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.

23 Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake,

nuphunzitsanso milomo yake.

24 Mau okoma ndiwo chisa cha uchi,

otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.

25 Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka,

koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.

26 Wantchito adzigwirira yekha ntchito;

pakuti m’kamwa mwake mumfulumiza.

27 Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa;

ndipo m’milomo mwake muli moto wopsereza.

28 Munthu wokhota amautsa makani;

kazitape afetsa ubwenzi.

29 Munthu wa chiwawa akopa mnzake,

namuyendetsa m’njira yosakhala bwino.

30 Wotsinzina ndiye aganizira zokhota;

wosunama afikitsa zoipa.

31 Imvi ndiyo korona wa ulemu,

idzapezedwa m’njira ya chilungamo.

32 Wosakwiya msanga aposa wamphamvu;

wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.

33 Maere aponyedwa pamfunga;

koma ndiye Yehova alongosola zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/16-0ed9dacf531d43cebd0ca0689d79c719.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 17

1 Nyenyeswa youma, pokhala mtendere,

iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano.

2 Kapolo wochita mwanzeru

adzalamulira mwana wochititsa manyazi,

nadzagawana nao abale cholowa.

3 Silivaali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng’anjo;

koma Yehova ayesa mitima.

4 Wochimwa amasamalira milomo yolakwa;

wonama amvera lilime losakaza.

5 Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi;

wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.

6 Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;

ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

7 Mlomo wangwiro suyenera chitsiru;

ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang’ono ponse.

8 Wolandira chokometsera mlandu achiyesa ngale;

paliponse popita iye achenjera.

9 Wobisa cholakwa afunitsa chikondano;

koma wobwerezabwereza mau afetsa ubwenzi.

10 Chidzudzulo chilowa m’kati mwa wozindikira,

kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.

11 Woipa amafuna kupanduka kokha;

koma adzamtumizira mthenga wankhanza.

12 Kukomana ndi chitsiru m’kupusa kwake

kuopsa koposa chilombo chochichotsera anake.

13 Wobwezera zabwino zoipa,

zoipa sizidzamchokera kwao.

14 Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi;

tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.

15 Wokometsa mlandu wa wamphulupulu,

ndi wotsutsa wolungama,

onse awiriwa amnyansa Yehova.

16 Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m’dzanja la chitsiru,

popeza wopusa alibe mtima?

17 Bwenzi limakonda nthawi zonse;

ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.

18 Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,

napereka chikole pamaso pa mnzake.

19 Wokonda ndeu akonda kulakwa;

ndipo wotalikitsa khomo lake afunafuna kuonongeka.

20 Wokhota mtima sadzapeza bwino;

ndipo mwini lilime lokhota adzagwa m’zoipa.

21 Wobala chitsiru adzichititsa chisoni;

ndipo atate wa wopusa sakondwa.

22 Mtima wosekerera uchiritsa bwino;

koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.

23 Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m’mfunga,

kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo.

24 Nzeru ili pamaso pa wozindikira;

koma maso a wopusa ali m’malekezero a dziko.

25 Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni,

namvetsa zowawa amake wombala.

26 Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino,

ngakhale kukwapula akulu chifukwa aongoka mtima.

27 Wopanda chikamwakamwa apambana kudziwa;

ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.

28 Ngakhale chitsiru chikatonthola achiyesa chanzeru;

posunama ali wochenjera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/17-cea309feb0c02552c48bba5eca7424da.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 18

1 Wopanduka afunafuna chifuniro chake,

nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.

2 Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;

koma kungovumbulutsa za m’mtima mwake.

3 Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;

manyazi natsagana ndi chitonzo.

4 Mau a m’kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;

kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.

5 Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino,

ngakhale kuchitira chetera wolungama.

6 Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;

ndipo m’kamwa mwake muputa kukwapulidwa.

7 M’kamwa mwa wopusa mumuononga,

milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.

8 Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka,

zotsikira m’kati mwa mimba.

9 Wogwira ntchito mwaulesi

ndiye mbale wake wa wosakaza.

10 Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba;

wolungama athamangiramo napulumuka.

11 Chuma cha wolemera ndicho mzinda wake wolimba;

alingalira kuti ndicho khoma lalitali.

12 Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;

koma chifatso chitsogolera ulemu.

13 Wobwezera mau asanamvetse apusa,

nadzichititsa manyazi.

14 Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;

koma ndani angatukule mtima wosweka?

15 Mtima wa wozindikira umaphunzira;

khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.

16 Mtulo wa munthu umtsegulira njira,

numfikitsa pamaso pa akulu.

17 Woyamba kudzinenera ayang’anika wolungama;

koma mnzake afika namuululitsa zake zonse.

18 Maere aletsa makangano,

nulekanitsa amphamvu.

19 Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta,

kulanda mzinda wolimba nkosavuta;

makangano akunga mipiringidzo ya linga.

20 Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m’kamwa mwake;

iye nadzakhuta phindu la milomo yake.

21 Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;

wolikonda adzadya zipatso zake.

22 Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino;

Yehova amkomera mtima.

23 Wosauka amadandaulira;

koma wolemera ayankha mwaukali.

24 Woyanjana ndi ambiri angodziononga;

koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/18-2ffd527be5c96b42d81c856660161173.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 19

1 Wosauka woyenda mwangwiro

aposa wokhetsa milomo ndi wopusa.

2 Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino;

ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.

3 Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake;

mtima wake udandaula pa Yehova.

4 Chuma chionjezetsa mabwenzi ambiri;

koma mnzake wa waumphawi amleka.

5 Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;

wolankhula mabodza sadzapulumuka.

6 Ambiri adzapembedza waufulu;

ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.

7 Abale onse a wosauka amuda;

nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye?

Awatsata ndi mau, koma kuli zii.

8 Wolandira nzeru akonda moyo wake;

wosunga luntha adzapeza zabwino.

9 Mboni yonama sidzapulumuka chilango;

wolankhula mabodza adzaonongeka.

10 Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;

nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?

11 Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo;

ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.

12 Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;

koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.

13 Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake;

ndipo makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe.

14 Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate;

koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.

15 Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;

ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.

16 Wosunga lamulo asunga moyo wake;

wonyalanyaza mayendedwe ake adzafa.

17 Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova;

adzambwezera chokoma chakecho.

18 Menya mwanako, chiyembekezero chilipo,

osafunitsa kumuononga.

19 Munthu waukali alipire mwini;

pakuti ukampulumutsa udzateronso.

20 Tamvera uphungu, nulandire mwambo,

kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.

21 Muli zolingalira zambiri m’mtima mwa munthu;

koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.

22 Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake;

ndipo wosauka apambana munthu wonama.

23 Kuopa Yehova kupatsa moyo;

wokhala nako adzakhala wokhuta;

zoipa sizidzamgwera.

24 Waulesi alonga dzanja lake m’mbale,

osalibwezanso kukamwa kwake.

25 Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera;

nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.

26 Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai,

ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

27 Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa,

leka kumva mwambo.

28 Mboni yopanda pake inyoza chiweruzo;

m’kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa.

29 Akonzera onyoza chiweruzo,

ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/19-c425ba6bdcf12be7ad411a40b3222ef1.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 20

1 Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa;

wosochera nazo alibe nzeru.

2 Kuopsa kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango;

womputa achimwira moyo wakewake.

3 Kuli ulemu kwa mwamuna kupewa ndeu;

koma zitsiru zonse zimangokangana.

4 Waulesi salima chifukwa cha chisanu;

adzapemphapempha m’masika osalandira kanthu.

5 Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya;

koma munthu wozindikira adzatungapo.

6 Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake;

koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?

7 Wolungama woyenda mwangwiro,

anake adala pambuyo pake.

8 Mfumu yokhala pa mpando woweruzira

ipirikitsa zoipa zonse ndi maso ake.

9 Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga,

ndayera opanda tchimo?

10 Miyeso yosiyana, ndi malichero osiyana,

zonse ziwirizi zinyansa Yehova.

11 Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake;

ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.

12 Khutu lakumva, ndi diso lopenya,

Yehova anapanga onse awiriwo.

13 Usakonde tulo ungasauke;

phenyula maso, udzakhuta zakudya.

14 Wogula ati, Chachabe chimenecho,

koma atachoka adzitama.

15 Alipo golide ndi ngale zambiri;

koma milomo yodziwa ndiyo chokometsera cha mtengo wapatali.

16 Tenga malaya a woperekera mlendo chikole;

woperekera mkazi wachilendo chikole umgwire mwini.

17 Zakudya za chinyengo zikondweretsa munthu;

koma pambuyo pake m’kamwa mwake mudzadzala tinsangalabwi.

18 Uphungu utsimikiza zolingalira,

ponya nkhondo utapanga upo.

19 Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi;

usadudukire woyasama milomo yake.

20 Wotemberera atate wake ndi amake,

nyali yake idzazima mu mdima woti bii.

21 Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake;

koma chitsiriziro chake sichidzadala.

22 Usanene, Ndidzabwezera zoipa;

yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.

23 Miyeso yosiyana inyansa Yehova,

ndi mulingo wonyenga suli wabwino.

24 Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna;

munthu tsono angazindikire bwanji njira yake?

25 Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika,

kuli msampha kwa munthu,

ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda.

26 Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu,

niyendetsapo njinga ya galeta.

27 Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova;

usanthula m’kati monse mwa mimba.

28 Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu;

chifundo chichirikiza mpando wake.

29 Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao;

kukongola kwa nkhalamba ndi imvi.

30 Mikwingwirima yopweteka ichotsa zoipa;

ndi mikwapulo ilowa m’kati mwa mimba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/20-2b43d7887d7b72d12907ad946cec2411.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 21

1 Mtima wa mfumu uli m’dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi;

aulozetsa komwe afuna.

2 Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake;

koma Yehova ayesa mitima.

3 Kuchita chilungamo ndi chiweruzo

kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

4 Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,

ndi nyali ya oipa, zili tchimo.

5 Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu;

koma yense wansontho angopeza umphawi.

6 Kupata chuma ndi lilime lonama

ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

7 Chiwawa cha amphulupulu chidzawakokolola;

chifukwa akana kuchita chiweruzo.

8 Wosenza tchimo njira yake ikhotakhota;

koma ntchito ya woyera mtima ilungama.

9 Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika

kuposa kukhala m’nyumba ndi mkazi wolongolola.

10 Wamphulupulu mtima wake umkhumba zoipa;

sakomera mtima mnzake.

11 Polangidwa wonyoza, wachibwana alandira nzeru,

naphunzira pakuyang’ana pa wanzeru.

12 Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu,

kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.

13 Wotseka makutu ake polira waumphawi,

nayenso adzalira koma osamvedwa.

14 Mphatso ya m’tseri ipembedza mkwiyo,

ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.

15 Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama;

koma kuwaononga akuchita mphulupulu.

16 Munthu wosochera panjira ya nzeru

adzakhala m’msonkhano wa akufa.

17 Wokonda zoseketsa adzasauka;

wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

18 Wochimwa ndiye chiombolo cha wolungama;

ndipo wachiwembu adzalowa m’malo mwa oongoka mtima.

19 Kukhala m’chipululu kufunika

kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong’ung’udza.

20 Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;

koma wopusa angozimeza.

21 Wolondola chilungamo ndi chifundo

apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.

22 Wanzeru akwera pa mzinda wa olimba,

nagwetsa mphamvu yake imene anaikhulupirira.

23 Wosunga m’kamwa mwake ndi lilime lake

asunga moyo wake kumavuto.

24 Wonyada wodzikuza dzina lake ndiye wonyoza;

achita mwaukali modzitama.

25 Chifuniro cha waulesi chimupha;

chifukwa manja ake akana kugwira ntchito.

26 Ena asirira modukidwa tsiku lonse;

koma wolungama amapatsa osamana.

27 Nsembe ya oipa inyansa;

makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.

28 Mboni yonama idzafa;

koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika.

29 Munthu woipa aumitsa nkhope yake;

koma woongoka mtima akonza njira zake.

30 Kulibe nzeru ngakhale luntha

ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.

31 Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo;

koma wopulumutsa ndiye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/21-bf18b07f5d70f5c7c7a8eabca72c35d8.mp3?version_id=1068—

Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 22

1 Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri;

kukukomera mtima anzako kuposasilivandi golide.

2 Wolemera ndi wosauka akumana,

wolenga onsewo ndiye Yehova.

3 Wochenjera aona zoipa, nabisala;

koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.

4 Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova

ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.

5 Minga ndi misampha ili m’njira ya wokhota;

koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo.

6 Phunzitsa mwana poyamba njira yake;

ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.

7 Wolemera alamulira osauka;

ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.

8 Wofesa zosalungama adzakolola tsoka;

ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera.

9 Mwini diso lamataya adzadala;

pakuti apatsa osauka zakudya zake.

10 Ukainga wonyoza, makangano adzatuluka;

makani ndi manyazi adzalekeka.

11 Wokonda kuyera mtima,

mfumu idzakhala bwenzi lake

chifukwa cha chisomo cha milomo yake.

12 Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa;

koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.

13 Waulesi ati, Pali mkango panjapo,

ndidzaphedwa pamakwalalapo.

14 M’kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya;

yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.

15 Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana;

koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.

16 Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake,

ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.

Malangizo a pa makhalidwe oyenera munthu

17 Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru,

nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.

18 Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m’kati mwako,

ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.

19 Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi,

kuti ukhulupirire Yehova.

20 Kodi sindinakulembere zoposa

za uphungu ndi nzeru;

21 kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona,

nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?

22 Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi,

ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo.

23 Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao;

omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.

24 Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga;

ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;

25 kuti ungaphunzire mayendedwe ake,

ndi kutengera moyo wako msampha.

26 Usakhale wodulirana mpherere,

ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake.

27 Ngati ulibe chobwezera

kodi achotserenji kama lako pansi pako?

28 Usasunthe chidziwitso chakale cha m’malire,

chimene makolo ako anachiimika.

29 Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake?

Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/22-5349935a35273ed6009f979506c51d4f.mp3?version_id=1068—