Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 16

Ahazi mfumu ya Yuda

1 Chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Peka mwana wa Remaliya Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi muYerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake;

3 popeza anayenda m’njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa zaamitunduamene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.

4 Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.

5 Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu kukachita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoze kumgonjetsa.

6 Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napirikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komwemo kufikira lero lino.

7 Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m’dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m’dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo.

8 Natenga Ahazisilivandi golide wopezeka m’nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya.

9 Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.

Guwa la nsembe la ku Damasiko

10 Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse.

11 Ndipo Uriya wansembe anamanga guwa la nsembelo, monga mwa zonse anazitumiza mfumu Ahazi zochokera ku Damasiko; momwemo Uriya wansembe analimanga asanabwere mfumu ku Damasiko.

12 Atafika mfumu kuchokera ku Damasiko, anapenya mfumu guwa la nsembelo, nayandikiza mfumu ku guwa la nsembelo, napereka nsembe pomwepo.

13 Nafukiza nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yaufa, natsanulira nsembe yake yothira, nawaza mwazi wa nsembe zake zamtendere paguwa la nsembelo.

14 Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati paguwa lake la nsembe ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa lake la nsembe.

15 Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Paguwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam’mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m’dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.

16 Nachita Uriya wansembe monga mwa zonse adalamulira mfumu Ahazi.

17 Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nachotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng’ombe zamkuwa zili pansi pake, naziika pa chiunda chamiyala.

18 Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a paSabataadawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya.

19 Machitidwe ena tsono adawachita Ahazi, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

20 Nagona Ahazi ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m’mzinda wa Davide; nakhala mfumu m’malo mwake Hezekiya mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/16-728cf72d15365473b82eb1ea97f1cf0c.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 17

Hoseya mfumu yotsiriza ya Israele

1 Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.

2 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israele asanakhale iye.

3 Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.

4 Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m’kaidi.

Asiriya apasula Samariya, Aisraele natengedwa ukapolo

5 Pamenepo mfumu ya Asiriya anakwera m’dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu.

6 Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m’mizinda ya Amedi.

7 Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m’dziko la Ejipito pansi padzanja laFaraomfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina,

8 nayenda m’miyambo yaamitunduamene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m’miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.

9 Ndipo ana a Israele anachita m’tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m’mizinda mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumzinda walinga komwe.

10 Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira;

11 nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;

12 natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musachita ichi.

13 Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja lamnenerialiyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.

14 Koma sanamvere, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirire Yehova Mulungu wao.

15 Ndipo anakaniza malemba ake, ndichipanganoanachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa.

16 Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang’ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikiraBaala.

17 Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.

18 Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha.

19 Yudanso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m’malemba a Israele amene adawaika.

20 Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m’dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake.

21 Pakuti anang’amba Israele, kumchotsa kunyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati; Yerobowamu naingitsa Israele asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukulu.

22 Nayenda ana a Israele m’zolakwa zonse za Yerobowamu, zimene anazichita osazileka;

23 mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m’dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.

Mfumu ya Asiriya amangitsa alendo m’midzi ya Samariya

24 Ndipo mfumu ya Asiriya anabwera nao anthu ochokera ku Babiloni, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Sefaravaimu, nawakhalitsa m’mizinda ya Samariya, m’malo mwa ana a Israele; nakhala iwo eni ake a Samariya, nakhala m’mizinda mwake.

25 Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaope Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa.

26 Motero ananena ndi mfumu ya Asiriya, kuti, Amitundu aja mudawachotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m’mizinda ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; chifukwa chake anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, ilikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.

27 Pamenepo mfumu ya Asiriya analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawachotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.

28 Nadza wina wa ansembewo adawachotsa ku Samariya, nakhala ku Betele, nawalangiza m’mene azimuopera Yehova.

29 Koma a mtundu uliwonse anapanga milungu yaoyao, naiika m’nyumba za misanje adazimangaAsamariya, a mtundu uliwonse m’mizinda mwao mokhala iwo.

30 Ndipo anthu a Babiloni anapanga Sukoti-Benoti, ndi anthu a Kuta anapanga Neregali, ndi anthu a Hamati anapanga Ashima,

31 ndi Aavi anapanga Nibihazi ndi Taritaki; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m’moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.

32 Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m’nyumba za misanje.

33 Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawachotsako.

34 Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele,

35 ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu ina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe;

36 koma Yehova amene anakukwezani kukutulutsani m’dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;

37 ndi malemba, ndi maweruzo, ndi chilamulo, ndi choikika anakulemberani muzisamalira kuzichita masiku onse, nimusamaopa milungu ina;

38 ndi chipangano ndinachichita nanu musamachiiwala, kapena kuopa milungu ina iai;

39 koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m’dzanja la adani anu onse.

40 Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba.

41 Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/17-3e839b1cecdb13f3819915c88e9976da.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 18

Hezekiya wabwino akhazikanso chipembedzo cha Yehova

1 Ndipo kunali chaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai muYerusalemu; ndi dzina la make ndiye Abi mwana wa Zekariya.

3 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita Davide kholo lake.

4 Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.

5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.

6 Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

7 Ndipo Yehova anali naye, nachita iye mwanzeru kulikonse anamukako, napandukira mfumu ya Asiriya osamtumikira.

8 Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mzinda walinga.

9 Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa.

10 Pakutha pake pa zaka zitatu anaulanda, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Israele analanda Samariya.

11 Ndipo mfumu ya Asiriya anachotsa Aisraele kunka nao ku Asiriya, nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m’mizinda ya Amedi;

12 chifukwa sanamvere mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwirachipanganochake, ndicho zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvere kapena kuzichita.

Senakeribu amangira Yerusalemu misasa

13 Chaka chakhumi ndi zinai cha Hezekiya Senakeribu mfumu ya Asiriya anakwerera mizinda yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.

14 Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asiriya ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundichokere; chimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asiriya anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu asilivandi matalente makumi atatu a golide.

15 Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m’nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu.

16 Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golide wa pa zitseko za Kachisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asiriya.

17 Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.

18 Ndipo m’mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang’anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.

19 Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Chikhulupiriro ichi nchotani uchikhulupirira?

20 Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira?

21 Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Ejipito; ndilo munthu akatsamirapo lidzampyoza dzanja lake; ateroFaraomfumu ya Aejipito kwa onse omkhulupirira iye.

22 Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira paguwa la nsembe pano mu Yerusalemu?

23 Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.

24 Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata aang’ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Ejipito akupatse magaleta ndi apakavalo?

25 Ngati ndakwerera malo ano wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.

26 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu mu Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe mu Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga.

27 Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? Si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?

28 Naima kazembeyo, nafuula ndi mau aakulu mu Chiyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikulu mfumu ya Asiriya.

29 Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m’dzanja lake;

30 kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova, ndi kuti Yehova adzatilanditsa ndithu, ndi mzinda uwu sudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya Asiriya.

31 Musamvere Hezekiya; pakuti itero mfumu ya Asiriya, Mupangane nane zamtendere, nimutulukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wake, ndi yense ku mkuyu wake, ndi kumwa yense madzi a m’chitsime chake;

32 mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko laazitonandi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.

33 Kodi mulungu uliwonse waamitunduwalanditsa dziko lake m’dzanja la mfumu ya Asiriya ndi kale lonse?

34 Ili kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m’dzanja langa?

35 Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m’dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m’dzanja langa?

36 Koma anthuwo anakhala chete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.

37 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang’anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong’ambika, namuuza mau a kazembeyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/18-7287d1aa3800a05d802ca33cdb0cfbe8.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 19

Nkhawa ya Hezekiya ndi pemphero lake

1 Ndipo kunali, atamva mfumu Hezekiya, anang’amba zovala zake, nafundira chiguduli, nalowa m’nyumba ya Yehova.

2 Natuma Eliyakimu woyang’anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesayamnenerimwana wa Amozi.

3 Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero lino ndilo tsiku la chisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.

4 Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.

5 Ndipo anyamata a mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.

6 Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asiriya anandichitira nao mwano.

7 Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m’dziko lake.

8 Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asiriya alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adachoka ku Lakisi.

9 Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, watuluka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,

10 Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti,Yerusalemusudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya Asiriya.

11 Taona, udamva icho mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?

12 Kodi milungu yaamitunduinawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala mu Telasara?

13 Ili kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?

14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15 Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati paakerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16 Tcherani khutu lanu, Yehova nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Senakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.

17 Zoona, Yehova, mafumu a Asiriya anapasula amitundu ndi maiko ao,

18 naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; chifukwa chake anaiononga.

19 Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m’dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.

Yesaya amtonthoza mtima Hezekiya

20 Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Chondipempha iwe pa Senakeribu mfumu ya Asiriya ndachimva.

21 Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi waZiyoniakunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.

22 Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m’mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele.

23 Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magaleta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zake za Lebanoni, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yake yaitali, ndi mitengo yake yosankhika yamlombwa, ndidzalowanso m’ngaka mwake mwenimweni, ku nkhalango zake za madimba.

24 Ndakapa, ndamwa madzi achilendo, ndi ku mapazi anga ndidzaphwetsa mitsinje yonse ya Ejipito.

25 Sunamva kodi kuti Ine ndinachichita kale lomwe, ndi kuchipanga masiku akalekale? Tsopano ndachifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula mizinda yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.

26 Chifukwa chake okhalamo ao anali ofooka manja, anaopsedwa, nachita manyazi, ananga udzu wakuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.

27 Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako.

28 Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m’makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m’mphuno mwako, ndi cham’kamwa changa m’milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.

29 Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.

30 Ndipo opulumuka a nyumba ya Yuda otsalawo adzaphukanso mizu, ndi kupatsa zipatso pamwamba.

31 Pakuti ku Yerusalemu kudzatuluka otsala, ndi akupulumukawo kuphiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi.

32 Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzalowa m’mzinda muno, kapena kuponyamo muvi, kapena kufikako ndi chikopa, kapena kuundira mtumbira.

33 Adzabwerera njira yomweyo anadzera, ndipo sadzalowa m’mzinda muno, ati Yehova.

34 Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.

Mthenga wa Yehova awapha Aasiriya

35 Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m’misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.

36 Nachoka Senakeribu mfumu ya Asiriya, namuka, nabwerera, nakhala ku Ninive.

37 Ndipo kunali popembedza iye m’nyumba ya Nisiroki mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/19-aea863c5c1572d087d92c2107d71efd2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 20

Hezekiya adwala nachira

1 Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesayamnenerimwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.

2 Pamenepo anatembenuzira nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, ndi kuti,

3 Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m’choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m’kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.

4 Ndipo kunali, asanatulukire Yesaya m’kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti,

5 Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.

6 Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mzinda uno m’dzanja la mfumu ya Asiriya; ndidzatchinjiriza mzinda uno, chifukwa cha Ine ndekha, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.

7 Nati Yesaya, Tenga nchinchi yankhuyu. Naitenga, naiika pafundo, nachira iye.

8 Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu?

9 Nati Yesaya, Chizindikiro ndichi akupatsa Yehova, kuti Yehova adzachichita chonena Iye; kodi mthunzi umuke m’tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m’mbuyo makwerero khumi?

10 Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.

11 Nafuulira kwa Yehova Yesaya mneneriyo, nabweza Iye mthunzi m’mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.

Hezekiya achimwa mwa kuonetsa chuma chake

12 Nthawi ija Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babiloni anatumiza makalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya.

13 Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake,siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m’nyumba mwake, kapena mu ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.

14 Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? Anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutali ku Babiloni.

15 Nati iye, Anaona chiyani m’nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m’nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pachuma changa kosawaonetsa.

16 Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.

17 Taonani, akudza masiku kuti zonse za m’nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kunka ku Babiloni, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.

18 Nadzatenga ena a ana ako otuluka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m’chinyumba cha mfumu ya Babiloni.

19 Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi choonadi zikakhala masiku anga?

20 Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mzinda madzi, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

21 Nagona Hezekiya ndi makolo ake; nakhala mfumu m’malo mwake Manase mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/20-848d3a1a4323acfc71e8d1d03e61bbc6.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 21

Manase woipitsitsa

1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu muYerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.

2 Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa zaamitunduamene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.

3 Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsiraBaalamaguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.

4 Namanga iye maguwa a nsembe m’nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, Mu Yerusalemu ndidzaika dzina langa.

5 Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.

6 Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.

7 Ndipo anaika chifanizo chosema chimene adachipanga m’nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomoni mwana wake kuti, M’nyumba muno ndi mu Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israele ndidzaikamo dzina langa kosatha.

8 Ndipo sindidzachotsanso mapazi a Israele m’dziko ndidalipereka kwa makolo ao; chokhachi asamalire kuchita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa chilamulo chonse anawalamulira Mose mtumiki wanga.

9 Koma sanamvere, nawalakwitsa Manase, nawachititsa choipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israele.

10 Pamenepo Yehova ananena mwa atumiki ake aneneri, ndi kuti,

11 Popeza Manase mfumu ya Yuda anachita zonyansa izi, pakuti zoipa zake zinaposa zonse adazichita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ake;

12 chifukwa chake atero Yehova Mulungu wa Israele, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda choipa, chakuti yense achimvera chidzamliritsa mwini khutu.

13 Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.

14 Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m’dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;

15 popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao mu Ejipito, mpaka lero lino.

16 Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.

17 Machitidwe ena tsono a Manase, ndi zochimwa zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

18 Nagona Manase ndi makolo ake, naikidwa m’munda wa nyumba yake, m’munda wa Uza, nakhala mfumu m’malo mwake Amoni mwana wake.

Amoni mfumu ya Yuda

19 Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka ziwiri mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.

20 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo amachitira Manase atate wake.

21 Nayenda iye m’njira monse anayendamo atate wake, natumikira mafano anawatumikira atate wake, nawagwadira;

22 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ake, sanayende m’njira ya Yehova.

23 Ndipo anyamata ake a Amoni anamchitira chiwembu, napha mfumuyo m’nyumba yakeyake.

24 Koma anthu a m’dzikomo anapha onse akumchitira chiwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m’dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wake m’malo mwake.

25 Machitidwe ena tsono a Amoni adawachita, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

26 Naikidwa iye m’manda mwake m’munda wa Uza; nakhala mfumu m’malo mwake Yosiya mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/21-c236c48a7cb1dc7ca11b38ad0fd6a2f4.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 22

Yosiya wabwino akonzanso Kachisi

1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu chimodzi muYerusalemu; ndi dzina la make ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.

2 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m’njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.

3 Ndipo kunali chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, kunyumba ya Yehova, ndi kuti,

4 Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo kunyumba ya Yehova,

5 ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m’dzanja la antchito akuyang’anira nyumba ya Yehova; iwo azipereke kwa ogwira ntchito ya m’nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,

6 kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.

7 Koma sanawawerengere ndalamazo zoperekedwa m’dzanja lao, pakuti anachita mokhulupirika.

Hilikiya apeza buku la chilamulo

8 Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m’nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.

9 Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m’nyumba, nazipereka m’dzanja la antchito akuyang’anira nyumba ya Yehova.

10 Ndipo Safani mlembiyo anafotokozera mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe wandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

11 Ndipo kunali, atamva mfumu mau a m’buku la chilamulo, inang’amba zovala zake.

12 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Akibori mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,

13 Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo.

Hulida mneneri wamkazi

14 Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulidamneneriwamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala za mfumu; analikukhala iye mu Yerusalemu m’dera lachiwiri, nalankhula naye.

15 Ndipo Hulida ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,

16 Atero Yehova, Taonani, nditengera malo ano choipa, ndi iwo okhalamo, chokwaniritsa mau onse a m’buku adaliwerenga mfumu ya Yuda;

17 popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake mkwiyo wanga udzayakira malo ano wosazimikanso.

18 Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva,

19 popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ano ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang’amba zovala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.

20 Chifukwa chake, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m’manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m’maso mwako choipa chonse ndidzachifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/22-120fa1f6395fe1286d98d295727db481.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 23

Yosiya awerenga bukulo kwa anthu nachita pangano ndi Yehova

1 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a muYerusalemu.

2 Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse aang’ono ndi aakulu; nawerenga iye m’makutu mwao mau onse a m’buku lachipanganoadalipeza m’nyumba ya Yehova.

3 Niima mfumu pachiunda, ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m’buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.

4 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangiraBaala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.

5 Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m’mizinda ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.

6 Natulutsa chifanizocho m’nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nachitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nachipera chikhale fumbi, naliwaza fumbi lake pa manda a ana a anthu.

7 Nagamula nyumba za anyamata adama okhala kunyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsalu zolenjeka za chifanizocho.

8 Natulutsa ansembe onse m’mizinda ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa chipata cha Yoswa kazembe wa mzinda, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa chipata cha mzinda.

9 Koma ansembe a misanje sanakwere kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda chotupitsa pakati pa abale ao.

10 Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m’chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwaMoleki.

11 Nachotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku chipinda cha Natani-Meleki mdindoyo, chokhala kukhonde; natentha magaleta a dzuwa ndi moto.

12 Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa chipinda chosanja cha Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwachotsa komweko, nitaya fumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.

13 Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum’mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la chionongeko, imene Solomoni mfumu ya Israele adaimangira Asitaroti chonyansa cha Asidoni, ndi Kemosi chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu chonyansa cha ana a Amoni.

14 Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu.

15 Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo.

16 Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu natulutsa mafupa kumanda, nawatentha paguwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi.

17 Anatinso, Chizindikiro ichi ndichiona nchiyani? Namuuza anthu a m’mzindawo, Ndicho manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazichitira guwa la nsembe la ku Betele.

18 Nati iye, Mlekeni, munthu asakhudze mafupa ake. Naleka iwo mafupa ake akhale pamodzi ndi mafupa amneneriuja anatuluka mu Samariya.

19 Ndi nyumba zonse zomwe za ku misanje yokhala m’mizinda ya Samariya, adazimanga mafumu a Israele kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazichotsa, nazichitira monga mwa ntchito zonse adazichita ku Betele.

20 Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu.

Achita Paska

21 Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanuPaska, monga mulembedwa m’buku ili la chipangano.

22 Zedi silinachitike Paska lotere chiyambire masiku a oweruza anaweruza Israele, ngakhale m’masiku a mafumu a Israele, kapena mafumu a Yuda;

23 koma Paska ili analichitira Yehova mu Yerusalemu, Yosiya atakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu.

24 Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndiaterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m’dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu, Yosiya anazichotsa; kuti alimbitse mau a chilamulo olembedwa m’buku adalipeza Hilikiya wansembe m’nyumba ya Yehova.

25 Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukenso wina wolingana naye.

26 Koma Yehova sanakhululuke mkwiyo wake waukulu waukali umene adapsa mtima nao pa Yuda, chifukwa cha zoputa zonse Manase adaputa nazo mkwiyo wake.

27 Nati Yehova, Ndidzachotsa Yudanso pamaso panga, monga umo ndinachotsera Israele; ndipo ndidzataya mzinda uwu ndidausankha, ndiwo Yerusalemu, ndi nyumba ndidainena, Dzina langa lidzakhala komweko.

28 Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

29 Masiku akeFaraoNeko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.

30 Ndipo anyamata ake anamtengera wakufa m’galeta, nabwera naye ku Yerusalemu kuchokera ku Megido, namuika m’manda akeake. Ndipo anthu a m’dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m’malo mwa atate wake.

Yehowahazi, Yehoyakimu ndi Yehoyakini mafumu oipa a Yuda

31 Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu miyezi itatu mu Yerusalemu ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

32 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita makolo ake.

33 Ndipo Farao Neko anammanga mu Ribula, m’dziko la Hamati; kuti asachite ufumu mu Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi lasiliva, ndi talente limodzi la golide.

34 Ndipo Farao Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m’malo mwa Yosiya atate wake, nasanduliza dzina lake likhale Yehoyakimu; koma anapita naye Yehowahazi, nafika iye mu Ejipito, nafa komweko.

35 Ndipo Yehoyakimu anapereka siliva ndi golide kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m’dziko siliva ndi golide, yense monga mwa kuyesedwa kwake, kuzipereka kwa Farao Neko.

36 Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.

37 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita makolo ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/23-f58ca7d0d791a39b2213239cb10f5f3a.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 24

1 Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.

2 Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.

3 Zedi ichi chinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwachotsa pamaso pake, chifukwa cha zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazichita;

4 ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzazaYerusalemundi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira.

5 Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

6 Nagona Yehoyakimu ndi makolo ake, ndipo Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

7 Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezenso kutuluka m’dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito.

Ayamba kutengedwa ukapolo kunka ku Babiloni

8 Yehoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la make ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.

9 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita atate wake.

10 Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babiloni anakwerera Yerusalemu, naumangira mzindawo misasa.

11 Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babiloni kumzinda, ataumangira misasa anyamata ake,

12 Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.

13 Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele mu Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena.

14 Nachoka nao a mu Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m’dziko.

15 Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m’dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.

16 Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula chikwi chimodzi, onsewo achamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babiloni anadza nao andende ku Babiloni.

17 Ndipo mfumu ya Babiloni analonga Mataniya mbale wa atate wake akhale mfumu m’malo mwake, nasanduliza dzina lake likhale Zedekiya.

Zedekiya mfumu yotsiriza ya Yuda

18 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

19 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adachita Yehoyakimu.

20 Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidachitika mu Yerusalemu ndi mu Yuda, mpaka adawataya pamaso pake; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babiloni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/24-bcd12fd621ef038c342d14527c9fc502.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 25

Yerusalemu apasulidwa, anthu natengedwa kunka ku Babiloni

1 Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzeraYerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.

2 Ndipo mzindawo unazingidwa ndi timalinga mpaka chaka chakhumi ndi chimodzi cha mfumu Zedekiya.

3 Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m’mzindamo, panalibe chakudya kwa anthu a m’dzikomo.

4 Pamenepo linga la mzindawo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamzinda pouzinga; nimuka mfumu panjira ya kuchidikha.

5 Koma nkhondo ya Ababiloni inalondola mfumu, nayipeza m’zidikha za Yeriko; koma nkhondo yake yonse inambalalikira.

6 Ndipo anaigwira mfumu, nakwera nayo kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula, naweruza mlandu wake.

7 Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.

8 Ndipo mwezi wachisanu, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo, ndicho chaka chakhumi mphambu chisanu ndi chinai cha mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, Nebuzaradani mkulu wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babiloni, anadza ku Yerusalemu,

9 natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto.

10 Ndi khamu lonse la Ababiloni linali ndi mkulu wa olindirira linagumula linga la Yerusalemu louzinga.

11 Ndi anthu otsalira m’mzinda, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babiloni, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkulu wa olindirira anamuka nao andende.

12 Koma mkulu wa olindirira anasiya osaukadi a m’dziko akhale osunga minda yampesa, ndi alimi.

13 Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m’nyumba ya Yehova, ndi maphaka ake, ndi thawale lamkuwa, zinali m’nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, natenga mkuwa wake kunka nao ku Babiloni.

14 Nachotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo.

15 Ndi zopalira moto, ndi mbale zowazira za golide yekhayekha, ndi zasilivayekhayekha, mkulu wa asilikali anazichotsa.

16 Nsanamira ziwiri, thawale limodzi, ndi maphakawo adazipangira nyumba ya Yehova Solomoni, mkuwa wa zipangizo izi zonse sanakhoze kuyesa kulemera kwake.

17 Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.

18 Ndipo mkulu wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi olindira pakhomo atatu;

19 natenga m’mzindamo mdindo woikidwa woyang’anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m’mzindamo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m’dziko; ndi anthu a m’dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m’mzindamo.

20 Ndipo Nebuzaradani mkulu wa olindirira anawatenga, napita nao kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula.

21 Niwakantha mfumu ya Babiloni, niwaphera ku Ribula m’dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwachotsa m’dziko lao.

Gedaliya wolamulira mu Yerusalemu aphedwa ndi Ismaele

22 Koma kunena za anthu otsalira m’dziko la Yuda, amene adawasiya Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iyeyu anamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani akhale wowalamulira.

23 Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babiloni adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmaakati, iwo ndi anthu ao omwe.

24 Nawalumbirira Gedaliya iwo ndi anthu ao, nanena nao, Musamaopa anyamata a Ababiloni; khalani m’dziko; tumikirani mfumu ya Babiloni, ndipo kudzakukomerani.

25 Koma kunali mwezi wachisanu ndi chiwiri anadza Ismaele mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yachifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Ababiloni okhala naye ku Mizipa.

26 Pamenepo ananyamuka anthu onse aang’ono ndi aakulu, ndi akazembe a makamu, nadza ku Ejipito; pakuti anaopa Ababiloni.

27 Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m’kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;

28 nakamba naye zokoma, namkweza mpando wake waulemu upose mipando ya mafumu anali pamodzi naye mu Babiloni.

29 Nasintha zovala zake za m’kaidi, namadya iye mkate pamaso pake masiku onse a moyo wake.

30 Ndi kunena za chakudya chake, panali chakudya chosalekeza chopatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku lililonse gawo lake, masiku onse a moyo wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/25-f076b948b51a7a609962fda8c98bcb09.mp3?version_id=1068—