Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 6

Elisa ayandamitsa chitsulo pamadzi

1 Ndipo ana a aneneri anati kwa Elisa, Taonani tsono, pamalo tikhalapo ife pamaso panu patichepera

2 Mutilole tipite ku Yordani, tikatengeko aliyense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo. Nati, Mukani.

3 Ndipo wina anati, Mulole mupite nafe anyamata anu. Nati, Ndidzamuka.

4 Namuka nao, nafika ku Yordani, iwo natema mitengo.

5 Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m’madzi; ndipo anafuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! Popeza njobwereka.

6 Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo.

7 Nati, Katole. Natambasula dzanja lake, naitenga.

Aaramu alangidwa ndi khungu ku Dotana

8 Ndipo mfumu ya Aramu inalinkuchita nkhondo ndi Israele, nipangana ndi anyamata ake, kuti, Misasa yanga idzakhala pakutipakuti.

9 Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.

10 Pamenepo mfumu ya Israele inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumchenjeza; nadzisunga osapitako, kawirikawiri.

11 Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?

12 Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa,mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m’kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.

13 Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotani.

14 Pamenepo anatumizako akavalo ndi magaleta ndi khamu lalikulu, nafikako usiku, nauzinga mzindawo.

15 Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, natuluka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mzinda ndi akavalo ndi magaleta. Ndi mnyamata wake ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji?

16 Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.

17 Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.

18 Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu uchite khungu. Ndipo Iye anawakantha, nawachititsa khungu, monga mwa mau a Elisa.

19 Ndipo Elisa ananena nao, Ngati njira ndi iyi? Ngati mzinda ndi uwu? Munditsate ine, ndidzakufikitsani kwa munthu mumfunayo; nawatsogolera ku Samariya.

20 Ndipo kunali, pakufika ku Samariya, Elisa anati, Yehova, muwakanganulire awa maso kuti aone. Nawakanganulira Yehova maso ao, naona iwo, ndipo tapenyani, ali pakati pa Samariya.

21 Niti mfumu ya Israele kwa Elisa pakuwaona, Atate wanga, ndiwakanthe kodi, ndiwakanthe?

22 Nati, Musawakanthe; kodi mumakantha omwe mwawagwira ndi lupanga ndi uta wanu? Apatseni mkate ndi madzi adye namwe, namuke kwa mbuye wao.

23 Ndipo anawakonzera chakudya chambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzenso ku dziko la Israele.

Aaramu amangira Samariya misasa

24 Ndipo zitatha izi, Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse, nakwera, namangira misasa Samariya.

25 Koma mu Samariya munali njala yaikulu; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa bulu unagulidwa masekeli asilivamakumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa kabu wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi masekeli asiliva asanu.

26 Ndipo popita mfumu ya Israele alikuyenda palinga, mkazi anamfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu.

27 Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa?

28 Nanena naye mfumu, Ufunanji? Nati iye, Mnzanga uyu ananena ndi ine, Tenga mwana wako timudye lero, ndi mwana wanga timudye mawa.

29 Ndipo tinaphika mwana wanga ndi kumudya, ndi mawa wake ndinanena naye, Tenga mwana wako, timudye; koma wambisa mwana wake.

30 Ndipo pakumva mfumu mau a mkaziyo, anang’amba zovala zake alinkupita nayenda palinga, anthu napenya; ndipo taonani, pali chiguduli m’kati pa thupi lake.

31 Nati iye, Andilange Mulungu naonjezeko, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati uti ukhale pa iye lero lino.

Elisa aneneratu za chakudya chochuluka

32 Koma Elisa anakhala pansi m’nyumba mwake, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m’mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kuchotsa mutu wanga? Taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi chitseko. Kodi mapazi a mbuye wake samveka dididi pambuyo pake?

33 Akali chilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, choipa ichi chichokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/6-eb8594cf0b2113b356e525206ac3a264.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 7

1 Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya.

2 Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m’mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.

Akhate anai awulula za kuthawa Aaramu

3 Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?

4 Tikati, Tilowe m’mzinda, m’mzinda muli njala, tidzafa m’mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.

5 Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pake pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.

6 Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.

7 Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi abulu ao, misasa ili chimangire; nathawa apulumutse moyo wao.

8 Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m’hema mmodzi, nadya namwa, natengakosilivandi golide ndi zovala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m’hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.

9 Pamenepo ananenana wina ndi mnzake, Sitilikuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tilikukhala chete; tikachedwa kufikira kwacha, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m’nyumba ya mfumu.

10 Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.

11 Ndipo iye anaitana alonda ena, ndi iwo anafotokozera a m’nyumba ya mfumu.

12 Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m’mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m’misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m’mzinda tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m’mzindamo.

13 Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m’mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione.

14 Motero anatenga magaleta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.

15 Ndipo anawalondola mpaka ku Yordani; ndipo taonani, m’njira monse munadzala ndi zovala ndi akatundu adazitaya Aaramu m’kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.

16 Natuluka anthu, nafunkha m’misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso ya ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.

17 Koma mfumu idayang’anitsa pachipata kazembe amene uja idafotsamira padzanja lake; ndipo anthu anampondereza pachipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu.

18 Ndipo kunachitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa chipata cha Samariya;

19 ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angachite mazenera m’mwamba, chikachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ichi ndi maso ako, koma osadyako ai;

20 kudamchitikira momwemo; popeza anthu anampondereza pachipata nafa iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/7-8517cc8607b698666ebc4801cda98146.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 8

Wa ku Sunemu abwera kwao itatha njalayo

1 Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.

2 Nanyamuka mkaziyo, nachita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lake, nagonera m’dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.

3 Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m’dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu.

4 Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikulu zonse Elisa wazichita.

5 Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m’mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitsira mwana wake ananena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wake Elisa anamuukitsayo?

6 Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m’munda, chichokere iye m’dziko mpaka lero lino.

Hazaele mfumu ya Aramu

7 Ndipo Elisa anafika ku Damasiko, podwala Benihadadi mfumu ya Aramu; ndipo anamuuza, kuti, Munthu wa Mulungu wadza kuno.

8 Niti mfumu kwa Hazaele, Tenga chaufulu m’dzanja lako, nukakumane naye munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzachira kodi nthenda iyi?

9 Namuka Hazaele kukakomana naye, napita nacho chaufulu, ndicho cha zokoma zonse za mu Damasiko, zosenzangamiramakumi anai, nafika naima pamaso pake, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzachira nthenda iyi?

10 Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzachira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.

11 Ndipo anamyang’ana chidwi, mpaka anachita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu.

12 Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang’amba akazi ao okhala ndi pakati.

13 Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.

14 Ndipo anachoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wake; ameneyo ananena naye, Anakuuza chiyani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzachira ndithu.

15 Ndipo kunali m’mawa mwake, anatenga chimbwi, nachiviika m’madzi, nachiphimba pankhope pa mfumu, nifa; ndipo Hazaele analowa ufumu m’malo mwake.

Yehoramu mfumu ya Yuda

16 Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.

17 Ndiye wa zaka makumi atatu ndi chiwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu zaka zisanu ndi zitatu kuYerusalemu.

18 Nayenda m’njira ya mafumu a Israele, m’mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.

19 Koma Yehova sanafune kuononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ake kosalekeza.

20 Masiku ake Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha.

21 Pamenepo Yoramu anaoloka kunka ku Zairi, ndi magaleta ake onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magaleta, nathawira anthu kwa mahema ao.

22 Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi.

23 Ndi machitidwe ena a Yoramu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda.

24 Nagona Yoramu ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Ahaziya mfumu ya Yuda

25 Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

26 Ahaziya ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu chaka chimodzi. Ndi dzina la make ndiye Ataliya mdzukulu wa Omuri mfumu ya Israele.

27 Ndipo anayenda m’njira ya nyumba ya Ahabu, nachita choipa pamaso pa Yehova, m’mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa chibale cha banja la Ahabu.

28 Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndi Aaramu analasa Yoramu.

29 Ndipo mfumu Yoramu anabwera kuti ampoletse mu Yezireele mabalawo adamkantha Aaramu ku Rama, polimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Natsikirako Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda kukamuona Yoramu mwana wa Ahabu mu Yezireele, pakuti anadwala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/8-6d5a9374d21f5302a629b0cc8d1b9f73.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 9

Yehu adzozedwa mfumu ya Israele

1 Ndipo Elisamneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m’chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m’dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi.

2 Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ake, nupite naye ku chipinda cham’katimo.

3 Nutenge nsupa ya mafutayo, nuwatsanulire pamutu pake, nunene, Atero Yehova, Ndakudzoza iwe ukhale mfumu pa Israele. Utatero, tsegula pakhomo, nuthawe osachedwa,

4 Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Giliyadi.

5 Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe.

6 Nanyamuka, nalowa m’nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele.

7 Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele.

8 Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana aamuna onse womangika ndi womasuka mu Israele.

9 Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya.

10 Ndipo agalu adzamudya Yezebele pa dera la Yezireele, wopanda wina wakumuika. Pamenepo anatsegula pakhomo, nathawa.

11 Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake.

12 Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine chakutichakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israele.

13 Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.

Yehu awapha Yoramu ndi Ahaziya

14 Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Giliyadi, iye ndi Aisraele onse, chifukwa cha Hazaele mfumu ya Aramu;

15 koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezireele ampoletse mabala ake anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kutuluka m’mzinda kukafotokozera mu Yezireele.

16 Nayenda Yehu m’galeta, namuka ku Yezireele, popeza Yoramu anagonako; ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatsikira kukamuona Yoramu.

17 Ndipo mlonda ali chilili pachilindiro mu Yezireele, naona gulu la Yehu lilinkudza, nati, Ndiona gulu. Nati Yoramu, Tenga wapakavalo, numtumize akomane nao, nanene, Mtendere kodi?

18 Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m’mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera.

19 Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m’mbuyo mwanga.

20 Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimisi, pakuti ayendetsa moyaluka.

21 Nati Yoramu, Manga. Namanga galeta wake. Ndipo Yoramu mfumu ya Israele ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatuluka yense m’galeta wake, natuluka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pamunda wa Naboti mu Yezireele.

22 Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anati, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mai wako Yezebele?

23 Natembenuza Yoramu manja ake, nathawa, nati kwa Ahaziya, Chiwembu, Ahaziya.

24 Yehu anakoka uta wake ndi mphamvu zonse, nalasa Yoramu pachikota, nupyoza muvi pa mtima wake, naonyezeka iye m’galeta wake.

25 Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wake, Mnyamule, numponye m’munda wa Naboti wa ku Yezireele; pakuti kumbukira m’mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wake, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.

26 Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ake, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova. Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.

27 Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.

28 Ndipo anyamata ake anamnyamulira pagaleta kunka naye kuYerusalemu, namuika ku manda ake pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Davide.

29 Ndipo pa chaka chakhumi ndi chimodzi cha Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya analowa ufumu pa Yuda.

Imfa ya Yezebele

30 Ndipo pofika Yehu ku Yezireele, Yezebele anamva, nadzikometsera m’maso, naluka tsitsi lake, nasuzumira pazenera.

31 Ndipo polowa Yehu pachipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimiri, iwe wakupha mbuyako?

32 Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.

33 Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wake pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi.

34 Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.

35 Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezeko kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.

36 Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele;

37 ndi thupi la Yezebele lidzakhala ngati ndowe pamunda m’dera la Yezireele, kuti sadzati, Ndi Yezebele uyu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/9-025679fdefc5ea4c7d899176448b91a2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 10

Yehu aononga mbumba ya Ahabu

1 Ndipo Ahabu anali nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri mu Samariya. Nalemba makalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,

2 Tsono ikakufikani inu kalata iyi, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mizinda yalinga, ndi zida,

3 musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.

4 Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaime pamaso pake, nanga ife tidzaima bwanji?

5 Ndipo iye wakuyang’anira nyumba, ndi iye wakuyang’anira mzinda, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani.

6 Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m’mzinda, amene anawalera.

7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m’madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele.

8 Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu ya ana a mfumu. Nati iye, Muiunjike miulu iwiri polowera pa chipata kufikira m’mawa.

9 Ndipo kunali m’mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?

10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya.

11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu mu Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.

12 Pamenepo ananyamuka, nachoka, namuka ku Samariya. Ndipo pokhala kunyumba yosengera ya abusa panjira,

13 Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tilikutsika kulonjera ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikulu.

14 Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiye ndi mmodzi yense.

Aphedwa aneneri a Baala

15 Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta.

16 Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M’mwemo anamuyendetsa m’galeta wake.

17 Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu mu Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya.

18 Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikiraBaalapang’ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri.

19 Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.

20 Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.

21 Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m’nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa.

22 Nati kwa iye wosunga nyumba ya zovala, Tulutsira otumikira Baala onse zovala. Nawatulutsira zovala.

23 Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m’nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.

24 Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndilikuwaika m’manja mwanu apulumuke, moyo wake kulipa moyo wake.

25 Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumzinda wa nyumba ya Baala.

26 Natulutsa zoimiritsa zija zinali m’nyumba ya Baala, nazitentha.

27 Nagamula fano la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.

28 Momwemo Yehu anaononga Baala mu Israele.

Yehu apembedza mafano

29 Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang’ombe agolide okhala mu Betele ndi mu Dani.

30 Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m’mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele.

31 Koma Yehu sanasamalire kuyenda m’chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.

32 Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israele; ndipo Hazaele anawakantha m’malire onse a Israele,

33 kuyambira ku Yordani kum’mawa, dziko lonse la Giliyadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroere, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Giliyadi ndi Basani.

34 Ndipo machitidwe ena a Yehu, ndi zonse anazichita, ndi mphambu yake yonse, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

35 Nagona Yehu ndi makolo ake, namuika mu Samariya. Ndi Yehowahazi mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

36 Ndipo masiku ake akukhala Yehu mfumu ya Israele mu Samariya ndiwo zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/10-d1e186fb1aa681d106f89ab885c7e630.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 11

Ataliya apha achifumu onse, Yowasi apulumuka

1 Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.

2 Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m’chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.

3 Nakhala naye wobisika m’nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.

4 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m’nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.

5 Nawalamulira, kuti, Chochita inu ndi ichi: limodzi la magawo atatu la inu olowa paSabatalizilindira nyumba ya mfumu,

6 ndi lina lizikhala ku chipata cha Suri, ndi lina ku chipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuitchinjiriza.

7 Ndipo magawo awiri a inu, ndiwo onse otulukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu.

8 Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zake m’manja mwake, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu potuluka ndi polowa iye.

9 Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

10 Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m’nyumba ya Yehova.

11 Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m’manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

12 Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m’manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.

13 Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m’nyumba ya Yehova;

14 napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m’dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang’amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu.

15 Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang’anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m’nyumba ya Yehova.

16 Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo kunyumba ya mfumu, namupha pomwepo.

Pangano la Yehoyada wansembe

17 Ndipo Yehoyada anachitachipanganopakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.

18 Namuka anthu onse a m’dzikomo kunyumba yaBaala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang’anira nyumba ya Yehova.

19 Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m’dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu kunyumba ya Yehova, nadzera njira ya chipata cha otumikira, kunka kunyumba ya mfumu. Nakhala iye pa chimpando cha mafumu.

20 Nakondwerera anthu onse a m’dziko, ndi m’mzinda munali phee; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga kunyumba ya mfumu.

21 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/11-4ba17fef3ffb7bf5dbcc293ffc28e9b5.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 12

Yowasi akonza Kachisi

1 Chaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi analowa ufumu wake; nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi anai; ndi dzina la mai wake ndiye Zibiya wa ku Beereseba.

2 Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m’mene anamlangizira wansembe Yehoyada.

3 Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.

4 Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m’mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.

5 Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, paliponse akapeza pogamuka.

6 Koma kunali, chaka cha makumi awiri mphambu zitatu cha mfumu Yowasi, ansembe sanathe kukonza mogamuka nyumba.

7 Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.

8 Navomera ansembe kusalandiranso ndalama za anthu, kapena kukonza mogamuka nyumba.

9 Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi paguwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova.

10 Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m’bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m’matumba, naziyesa ndalama zopereka m’nyumba ya Yehova.

11 Napereka ndalama zoyesedwa m’manja mwa iwo akuchita ntchitoyi, akuyang’anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira ntchito ya pa nyumba ya Yehova,

12 ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.

13 Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova;

14 pakuti anazipereka kwa iwo akugwira ntchitoyi, nakonza nazo nyumba ya Yehova.

15 Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m’manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.

16 Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi.

Yowasi agonja kwa Hazaele mfumu ya Aramu

17 Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.

18 Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.

19 Machitidwe ena tsono a Yowasi ndi zonse adazichita sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

20 Ndipo anyamata ake ananyamuka, napangana, nakantha Yowasi kunyumba ya Milo potsikira ku Sila.

21 Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi mwana wa Somere, anyamata ake, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ake m’mzinda wa Davide; ndi Amaziya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/12-13d6fb3e643593576c6027b830fdf6f2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 13

Yehowahazi mfumu ya Israele

1 Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke.

3 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israele, nawapereka m’dzanja la Hazaele mfumu ya Aramu, ndi m’dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele, masiku onsewo.

4 Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m’mene mfumu ya Aramu inawapsinja.

5 Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi padzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m’mahema mwao monga kale.

6 Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m’mwemo; ndipo chifanizocho chinatsalanso mu Samariya.

7 Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.

8 Machitidwe ena tsono a Yehowahazi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

9 Ndipo Yehowahazi anagona ndi makolo ake, namuika mu Samariya; nakhala mfumu m’malo mwake Yowasi mwana wake.

Yehowasi mfumu ya Israele

10 Chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi.

11 Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.

12 Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

13 Ndipo Yowasi anagona ndi makolo ake, ndi Yerobowamu anakhala pa mpando wachifumu wake; namuika Yowasi mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele.

Kumwalira kwa Elisa

14 Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yehowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!

15 Nanena naye Elisa, Tenga uta ndi mivi; nadzitengera uta ndi mivi.

16 Nati kwa mfumu ya Israele, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ake pa manja a mfumu.

17 Nati, Tsegulani zenera la kum’mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu mu Afeki mpaka mudzawatha.

18 Nati iye, Tengani mivi; naitenga. Nati kwa mfumu ya Israele, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

19 Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.

20 Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amowabu analowa m’dziko poyambira chaka.

21 Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m’manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.

22 Ndipo Hazaele mfumu ya Aramu anapsinja Israele masiku onse a Yehowahazi.

23 Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa chachipanganochake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.

24 Nafa Hazaele mfumu ya Aramu, nakhala mfumu m’malo mwake Benihadadi mwana wake.

25 Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m’dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele mizinda ija adailanda m’dzanja la Yehowahazi atate wake ndi nkhondo. Yehowasi anamkantha katatu, naibweza mizinda ya Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/13-7fec170b86d17c24e561a8f820d8ac0d.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 14

Amaziya mfumu ya Yuda ndi Yehowasi mfumu ya Israele

1 Chaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai muYerusalemu; dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.

3 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.

4 Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

5 Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m’dzanja lake, anakantha anyamata ake amene adakantha mfumu atate wake;

6 koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m’buku la chilamulo cha Mose, m’mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.

7 Anapha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.

8 Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso.

9 Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama yakuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.

10 Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;

11 Koma Amaziya sanamvere. Motero anakwera Yehowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda.

12 Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawira yense kuhema kwake.

13 Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.

14 Natenga golide ndisilivayense, ndi zotengera zonse anazipeza m’nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m’nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya.

15 Machitidwe ena tsono a Yehowasi adazichita, ndi mphamvu yake, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

16 Nagona Yehowasi ndi makolo ake, namuika mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele; nakhala mfumu m’malo mwake Yerobowamu mwana wake.

17 Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu.

18 Machitidwe ena tsono a Amaziya, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

19 Ndipo anamchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.

20 Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Davide.

21 Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m’malo mwa atate wake Amaziya.

22 Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.

Yerobowamu wachiwiri mfumu ya Israele

23 Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.

24 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

25 Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitaimneneriyo, ndiye wa Gatihefere.

26 Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele.

27 Ndipo Yehova sadanene kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehowasi.

28 Machitidwe ena tsono a Yerobowamu, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, umo anachita nkhondo, nabweza kwa Israele Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

29 Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m’malo mwake Zekariya mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/14-9f68ca5a021fc518427088ea3b7a8904.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 15

Azariya mfumu ya Yuda

1 Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri muYerusalemu; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.

3 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.

4 Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

5 Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhatempaka tsiku la imfa yake, nakhala m’nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang’anira banja la mfumu, naweruza anthu a m’dziko.

6 Machitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

7 Nagona Azariya ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m’mzinda wa Davide; nakhala mfumu m’malo mwake Yotamu mwana wake.

Zekariya mfumu ya Israele

8 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele mu Samariya miyezi isanu ndi umodzi.

9 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

10 Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamchitira chiwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m’malo mwake.

11 Machitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

12 Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.

Salumu mfumu ya Israele

13 Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wake chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi mu Samariya.

14 Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi mu Samariya, namupha; nakhala mfumu m’malo mwake.

15 Machitidwe ena tsono a Salumu ndi chiwembu chake anachichita, taonani, zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

Menahemu mfumu ya Israele

16 Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m’mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m’mwemo.

17 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi mu Samariya.

18 Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

19 Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente asilivachikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m’dzanja lake.

20 Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israele ndalamazi, nasonkhetsa achuma, yense masekeli makumi asanu a siliva, kuti azipereke kwa mfumu ya Asiriya. Nabwerera mfumu ya Asiriya osakhala m’dzikomo.

21 Machitidwe ena tsono a Menahemu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

22 Nagona Menahemu ndi makolo ake; nakhala mfumu m’malo mwake Pekahiya mwana wake.

Pekahiya mfumu ya Israele

23 Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.

24 Nachita choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

25 Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye mu Samariya, m’nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m’malo mwake.

26 Machitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazichita, taonani zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

Peka mfumu ya Israele

27 Chaka cha makumi asanu mphambu ziwiri cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.

28 Nachita choipa pamaso pa Yehova, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

29 Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.

30 Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m’malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.

31 Machitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazichita, taonani, zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

Yotamu mfumu ya Yuda

32 Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

33 Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndipo dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

34 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anachita monga mwa zonse anazichita atate wake Uziya.

35 Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.

36 Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

37 Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye.

38 Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ake, namuika pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Davide kholo lake; nakhala mfumu m’malo mwake Ahazi mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/15-05ab450120faa7f323cd084ad9302a92.mp3?version_id=1068—