Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 19

Eliya athawa Yezebele

1 Ndipo Ahabu anauza Yezebele zonse anazichita Eliya, ndi m’mene anawaphera ndi lupanga aneneri onsewo.

2 Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.

3 Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.

4 Koma iye mwini analowa m’chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.

5 Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.

6 Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi.

7 Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakukanika.

8 Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.

Eliya kuphiri la Horebu

9 Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya?

10 Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiyachipanganochanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.

11 Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang’amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m’mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m’chivomezicho.

12 Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m’motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.

13 Ndipo atamva Eliya, anafunda nkhope yake ndi chofunda chake, natuluka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya?

14 Nati iye, Ndachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele ataya chipangano chanu, nagumula maguwa la nsembe anu, napha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.

15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Bwerera ulendo wako, udzere kuchipululu kunka ku Damasiko, ndipo utafikako udzoze Hazaele akhale mfumu ya Aramu;

16 ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhalemnenerim’malo mwako.

17 Ndipo kudzachitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaele; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu.

18 Ndiponso ndidasiya mu Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadiraBaalamaondo ao, osampsompsona ndi milomo yao.

19 Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng’ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.

20 Ndipo iye anasiya ng’ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndiyambe ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji?

21 Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng’ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng’ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/19-48172288e3b76673a661e5e4daa0369f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 20

Nkhondo pakati pa Ahabu ndi Benihadadi

1 Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo.

2 Natumiza mithenga kumzinda kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati kwa iye,

3 Atero Benihadadi,Silivawako ndi golide wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga.

4 Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndili nazo.

5 Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golide wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;

6 koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m’nyumba mwako, ndi m’nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti chifuniro chonse cha maso ako adzachigwira ndi manja ao, nadzachichotsa.

7 Pamenepo mfumu ya Israele anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti munthu uyu akhumba choipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golide wanga; ndipo sindinamkaniza.

8 Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musavomereze.

9 Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba mundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzachita, koma ichi sindingachichite. Nichoka mithengayo, nimbwezera mau.

10 Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.

11 Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo.

12 Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m’misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamzindapo.

13 Ndipo taonani,mnenerianadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m’dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.

14 Nati Ahabu, Mwa yani? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe.

15 Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israele onse zikwi zisanu ndi ziwiri.

16 Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m’misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.

17 Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kutuluka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, Mu Samariya mwatuluka anthu.

18 Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m’nkhondo, agwireni, amoyo.

19 Tsono anatuluka m’mzinda anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata.

20 Ndipo aliyense anapha munthu wake; ndipo Aaramu anathawa, Aisraele nawapirikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.

21 Tsono mfumu ya Israele inatuluka, nikantha apakavalo ndi apamagaleta, nawapha Aaramuwo maphedwe aakulu.

22 Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israele, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe muchenjere ndi chimene muchichita; popeza chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.

23 Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m’mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu.

24 Tsono chitani ichi, chotsani mafumu aja yense ku malo ake, muike m’malo mwao akazembe.

25 Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magaleta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pachidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.

26 Tsono kunachitika, pakufikanso chaka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Afeki kukaponyana ndi Aisraele.

27 Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.

28 Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m’dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

29 Ndipo awa anakhala m’misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israele anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.

30 Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m’mzinda, m’chipinda cha m’katimo.

31 Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m’chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo.

32 Motero anavala chiguduli m’chuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israele, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.

33 Tsono anthuwo anamyang’anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni. Pamenepo Benihadadi anatuluka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m’galeta mwake.

34 Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza mizinda ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda mu Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera mu Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.

35 Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha.

36 Ndipo ananena naye, Popeza sunamvere mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha. Ndipo m’mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.

37 Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha.

38 Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pake.

39 Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m’malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva,

40 Tsono pochita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.

41 Ndipo iye anafulumira kuchotsa mpango kumaso kwake, ndi mfumu ya Israele inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.

42 Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m’dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m’malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m’malo mwa anthu ake.

43 Pamenepo mfumu ya Israele inanka kwao wamsunamo ndi wokwiya, nafika ku Samariya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/20-37c338fe2b6fe8a8db8bc73014964727.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 21

Yezebele aphetsa Naboti

1 Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezireele anali ndi munda wampesa, unali mu Yezireelemo, m’mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samariya.

2 Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wampesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m’malo mwake ndidzakupatsa munda wampesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake.

3 Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang’ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.

4 Ndipo Ahabu analowa m’nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M’mwemo anagona pa kama wake, nayang’ana kumbali, nakana kudya mkate.

5 Koma Yezebele mkazi wake anadza kwa iye, nati kwa iye, Muchitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate?

6 Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezireele, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m’malo mwake; koma anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wampesa.

7 Ndipo Yezebele mkazi wake anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisraele tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezireele ndidzakupatsani ndine.

8 M’mwemo analemba makalata m’dzina la Ahabu nakhomerapo chizindikiro chake, natumiza makalatawo kwa akulu ndi omveka anali m’mzinda mwake, nakhala naye, Naboti.

9 Ndipo analemba m’makalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu;

10 ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.

11 Ndipo anthu aja a mzinda wake, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m’mzinda mwake, anachita monga Yezebele anawatumizira, monga munalembedwa m’makalata amene iye anawatumizira.

12 Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu.

13 Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m’mzinda, namponya miyala, namupha.

14 Pomwepo anatuma mau kwa Yezebele, nati, Naboti waponyedwa miyala, nafa.

15 Ndipo kunali, atamva Yezebele kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebele anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wampesa wa Naboti Myezireele uja anakana kukugulitsani ndi ndalama, popeza Naboti sali ndi moyo, koma wafa.

16 Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti Myezireele wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wampesa wa Naboti, kuulandira.

Eliya auza Ahabu za kuonongeka kwa mbumba yake

17 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,

18 Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israele, akhala mu Samariya; taona, ali ku munda wampesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira.

19 Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.

20 Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.

21 Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka mu Israele;

22 ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.

23 Ndipo za Yezebele yemwe Yehova ananena, nati, Agalu adzadya Yezebele ku linga la Yezireele.

24 Mwana aliyense wa Ahabu amene adzafera m’mzinda, agalu adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m’mlengalenga zidzamudya.

25 Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.

26 Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele.

27 Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang’amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang’anyang’a.

28 Pamenepo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,

29 Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m’masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/21-c02d66f8ac8156ac43718c71950356dc.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 22

Ahabu apangana ndi Yehosafati

1 Ndipo Aaramu ndi Aisraele anakhala chete zaka zitatu, osathirana nkhondo.

2 Koma kunachitika chaka chachitatu, kuti Yehosafati mfumu ya Yuda anatsikira kwa mfumu ya Israele.

3 Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m’dzanja la mfumu ya Aramu.

4 Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M’mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako.

5 Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israele, Funsira ku mau a Yehova lero.

6 Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m’dzanja la mfumu.

7 Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibemneneriwina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?

8 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.

9 Tsono mfumu ya Israele anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Imila.

10 Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.

11 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.

12 Ndipo aneneri onse ananena momwemo, nati, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, ndipo mudzachita mwai; popeza Yehova adzaupereka m’dzanja la mfumu.

Mikaya anenera motsutsa Ahabu

13 Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m’kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.

14 Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.

15 Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Giliyadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzachita mwai, popeza Yehova adzaupereka m’dzanja la mfumu.

16 Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokhazokha m’dzina la Yehova?

17 Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake.

18 Pamenepo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Kodi sindinakuuze kuti uyu sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa?

19 Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m’mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.

20 Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Giliyadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.

21 Pamenepo mzimu wina unatuluka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Nati Yehova kwa iye, Motani?

22 Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m’kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene.

23 Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m’kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena choipa cha inu.

24 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe?

25 Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m’chipinda cha pakati kubisala.

26 Pamenepo inati mfumu ya Israele, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu;

27 ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m’kaidi, mumdyetse chakudya cha nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.

28 Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.

Ahabu aphedwa mu nkhondo ya pa Aramu

29 Tsono mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Giliyadi.

30 Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.

31 Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magaleta ake, niti, Musaponyana ndi anthu aang’ono kapena aakulu, koma ndi mfumu ya Israele yokha.

32 Ndipo kunali, akapitao a magaleta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israele imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anafuula.

33 Ndipo pamene akapitao a magaleta anaona kuti sindiye mfumu ya Israele, anabwerera osampirikitsa.

34 Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.

35 Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m’galeta mwake kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unatuluka m’bala pa phaka la galeta.

36 Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumzinda kwao, ndi yense ku dziko la kwao.

37 Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samariya, naika mfumu mu Samariya.

38 Ndipo potsuka galetayo pa thawale la ku Samariya agalu ananyambita mwazi wake, paja pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.

39 Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi mizinda yonse adaimanga, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

40 Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ake; ndi Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Yehosafati mfumu ya Yuda

41 Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda chaka chachinai cha Ahabu mfumu ya Israele.

42 Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu muYerusalemu. Ndi dzina la amake linali Azuba mwana wa Sili.

43 Ndipo anayenda m’njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.

44 Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele.

45 Tsono machitidwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

46 Ndipo anachotsa m’dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wake Asa.

47 Ndipo mu Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu.

48 Yehosafati anamanga zombo za ku Tarisisi kukatenga golide ku Ofiri; koma sizinamuke, popeza zinaphwanyika pa Eziyoni-Gebere.

49 Pamenepo Ahaziya mwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m’zombo. Koma Yehosafati anakana.

50 Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ake, naikidwa ndi makolo ake m’mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Ahaziya mfumu Israele

51 Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m’chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.

52 Nachita choipa pamaso pa Yehova, nayenda m’njira ya atate wake, ndi ya amake, ndi ya Yerobowamu mwana wa Nebati, amene adachimwitsa Israele.

53 NatumikiraBaala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele, monga umo anachitira atate wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/22-9f1097c9a2d8df5e1ab4d1ed3bbfede1.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likupitiriza kunena za mbiri ya mafumu a ku Israele ndi a ku Yuda. Bukuli lili ndi zigawo ziwiri: Gawo loyamba ndilo la maufumu awiri kuyambira pa chaka ngati cha 850 BC mpaka chaka cha 721 BC ndipo lachiwiri ndi la ufumu wa Yuda wokha, kufikira pa nthawi ya kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu chaka cha 586 BC.

Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atazinga mzinda wa Yerusalemu nkuwuononga, anasankha Gedaliya kuti akhale bwanamkubwa woyang’anira dziko la Yuda m’dzina lake.

Israele ndi Yuda, onse awiri adaonongeka chifukwa cha kusakhulupirika kwa mafumu ake ndi kwa anthu ao. Makamaka Ayuda ndiwo adakhumudwa kwambiri, poona kuti mzinda wa Yerusalemu wapasuka ndipo anthu ake ambiri atengedwa kupita ku ukapolo. Mneneri wotchuka pa masiku oyamba aja anali Elisa, amene adalowa m’malo mwa Eliya uja.

Za mkatimu

Za maufumu awiri aja

1.1—17.41

a. Mneneri Elisa

1.1—8.5

b. Mafumu a ku Yuda ndi mafumu a ku Israele

8.6—17.4

c. Kupasuka kwa mzinda wa Samariya

17.5-41

Za ufumu wa Yuda

18.1—24.20

a. Kuyambira Hezekiya mpaka Yosiya

18.1—21.26

b. Ufumu wa Yosiya

22.1—23.30

c. Mafumu otsiriza a Yuda

23.31—24.20

d. Kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu

25.1-30

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 1

Eliya ndi nthenda ya Ahaziya

1 Ndipo atamwalira Ahabu, Mowabu anapandukana ndi Israele.

2 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.

3 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni?

4 Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya.

5 Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera chifukwa ninji?

6 Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

7 Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ake a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani?

8 Ninena naye, Ndiye munthu wovala zaubweya, namangira m’chuuno mwake ndi lamba lachikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe.

9 Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba paphiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.

10 Nayankha Eliya, nanena ndi mtsogoleriyo, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo unatsika moto kumwamba, nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake.

11 Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ake. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga.

12 Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo moto wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake.

13 Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.

14 Taonani, watsika moto wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wake pamaso panu.

15 Pamenepo mthenga wa Yehova anati kwa Eliya, Tsika naye, usamuopa. Nanyamuka iye, natsikira naye kwa mfumu.

16 Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

17 Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m’malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.

18 Machitidwe ake ena tsono adawachita Ahaziya, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/1-5866a6817fc93d2a14a902eeedc21d07.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 2

Eliya atengedwa kunka kumwamba

1 Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.

2 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndinke ku Betele. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Betele.

3 Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete.

4 Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.

5 Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete.

6 Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.

7 Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordani.

8 Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.

9 Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha chimene ndikuchitire ndisanachotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine.

10 Nati iye, Wapempha chinthu chapatali, koma ukandipenya pamene ndichotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero ai.

11 Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.

12 Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing’amba pakati.

Elisa mneneri, zozizwitsa zake

13 Pamenepo anatola chofunda chake cha Eliya chidamtayikiracho, nabwerera, naima m’mphepete mwa Yordani.

14 Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.

15 Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pake, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake.

16 Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya paphiri lina, kapena m’chigwa china. Koma anati, Musatumiza.

17 Koma anamuumiriza kufikira anachita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.

18 Nabwerera kwa iye ali chikhalire ku Yeriko, ndipo anati kwa iwo, Kodi sindinanene nanu, Musamuka?

19 Ndipo amuna amumzinda anati kwa Elisa, Taonani, mumzinda muno m’mwabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa.

20 Pamenepo anati, Nditengereni chotengera chatsopano, muikemo mchere. Ndipo anabwera nacho kwa iye.

21 Ndipo anatuluka kunka ku magwero a madzi, nathiramo mchere, nati, Atero Yehova, Ndachiritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.

22 Chotero madzi anachiritsidwa mpaka lero lino, monga mwa mau a Elisa ananenawo.

23 Ndipo anachokako kukwera ku Betele, ndipo iye ali chikwerere m’njiramo, munatuluka anyamata aang’ono m’mzindamo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi!

24 Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m’dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri.

25 Ndipo anachokako kunka kuphiri la Karimele; nabwera kumeneko nafika ku Samariya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/2-aa9e1d9ad2eebd2db3ff694927b82c20.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 3

Chipulumutso chodabwitsa cha nkhondo za Yuda, Israele, ndi Edomu

1 Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m’chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa chaBaalaadachipanga atate wake.

3 Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo.

4 Ndipo Mesa mfumu ya Mowabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israele ubweya wa anaankhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.

5 Koma kunachitika, atafa Ahabu mfumu ya Mowabu anapandukana ndi mfumu ya Israele.

6 Ndipo mfumu Yehoramu anatuluka mu Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisraele onse.

7 Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.

8 Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku chipululu cha Edomu.

9 Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.

10 Ndipo mfumu ya Israele inati, Kalanga ife! Pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m’dzanja la Mowabu.

11 Koma Yehosafati anati, Palibe panomneneriwa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israele anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m’manja a Eliya.

12 Nati Yehosafati, Mau a Yehova ali ndi iyeyo. Pamenepo mfumu ya Israele, ndi Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anatsikira kuli iye.

13 Ndipo Elisa anati kwa mfumu ya Israele, Ndili ndi chiyani ndi inu? Mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israele inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m’dzanja la Mowabu.

14 Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pake, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang’anitsani, kapena kukuonani.

15 Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, wanthetemyayo ali chiimbire, dzanja la Yehova linamgwera.

16 Ndipo anati, Atero Yehova, Kumbani m’chigwa muno mukhale maenje okhaokha.

17 Pakuti atero Yehova, Simudzaona mphepo, kapena kuona mvula, koma chigwacho chidzadzala ndi madzi; ndipo mudzamwa inu, ndi ng’ombe zanu, ndi zoweta zanu.

18 Ndipo ichi chidzapepuka pamaso pa Yehova; adzaperekanso Amowabu m’dzanja lanu.

19 Ndipo mudzakantha mizinda yonse ya malinga, ndi mizinda yonse yosankhika, ndi kulikha mitengo yonse yabwino, ndi kufotsera zitsime zonse zamadzi, ndi kuipitsa pa nthaka ponse pabwino ndi miyala.

20 Ndipo kunachitika m’mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.

21 Atamva tsono Amowabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m’chuuno ndi okulapo, naima iwo m’malire.

22 Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amowabu madzi ali pandunji pao ali psu ngati mwazi;

23 nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzake; ndipo tsopano, tiyeni Amowabu inu, tikafunkhe.

24 Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israele, Aisraele ananyamuka, nakantha Amowabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m’dziko ndi kukantha Amowabu.

25 Napasula mizinda, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake mu Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.

26 Ndipo ataona mfumu ya Mowabu kuti nkhondo idamuvuta, anapita nao anthu mazana asanu ndi awiri akusolola lupanga, kupyola kufikira kwa mfumu ya Edomu, koma sanakhoze.

27 Pamenepo anagwira mwana wake wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m’malo mwake, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israele kwambiri; potero anamchokera, nabwerera ku dziko lao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/3-122ee4c7781c1bb9cddfbe4fdf28cbdb.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 4

Elisa achulukitsa mafuta a mkazi wamasiye

1 Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.

2 Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m’nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m’nyumba, koma mtsuko wa mafuta.

3 Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang’ono.

4 Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako aamuna ndi kutsanulira m’zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.

5 Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake aamuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.

6 Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka.

7 Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.

Mkazi wa ku Sunemu ndi mwana wake

8 Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate.

9 Ndipo mkaziyo anati kwa mwamuna wake, Taona, tsopano ndidziwa kuti munthu uyu wakupitira pathu pano chipitire ndiye munthu woyera wa Mulungu.

10 Timmangire kachipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi choikaponyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m’mwemo.

11 Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m’chipinda chosanja, nagona komweko.

12 Nati kwa Gehazi mnyamata wake, Itana Msunamu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pake.

13 Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.

14 Pamenepo anati, Nanga timchitire iye chiyani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wake wakalamba.

15 Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo.

16 Ndipo anati, Nyengo ino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, Iai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.

17 Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo chaka chimene chija Elisa adanena naye.

18 Ndipo atakula mwanayo, linadza tsiku lakuti anatuluka kunka kwa atate wake, ali kwa omweta tirigu.

19 Nati kwa atate wake, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amake.

20 Namnyamula, napita naye kwa amake. Ndipo anakhala pa maondo ake kufikira usana, namwalira.

21 Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, natuluka, namtsekera.

22 Naitana mwamuna wake, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.

23 Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpaSabata? Koma anati, Kuli bwino.

24 Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.

25 Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;

26 uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? Mwamuna wanu ali bwino? Mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.

27 Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.

28 Ndipo mkaziyo anati, Ngati ndinapempha mwana kwa mbuyanga? Kodi sindinati, Musandinyenga?

29 Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m’chuuno, nutenge ndodo yanga m’dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.

30 Koma make wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata.

31 Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.

32 Ndipo pamene Elisa analowa m’nyumba, taonani, mwanayo ngwakufa, adamgoneka pakama pake.

33 Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova.

34 Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pake ndi pakamwa pake, maso ake ndi maso ake, zikhato zake ndi zikhato zake, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.

35 Pamenepo anabwera nayenda m’nyumba, chakuno kamodzi, chauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ake.

36 Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunamu uja. Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako.

37 Iye nalowa, nagwa pa mapazi ake, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wake, natuluka.

Muli imfa m’nkhalimo

38 Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m’dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri.

39 Natuluka wina kukatchera ndiwo kuthengo, napeza chonga ngati mpesa, natcherapo zipuzi kudzaza m’funga mwake, nadza, nazichekerachekera m’nkhali ya chakudya, popeza sanazidziwe.

40 Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali, pakudya chakudyacho, anafuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m’nkhalimo. Ndipo sanathe kudyako.

41 Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m’nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m’nkhalimo munalibe chowawa.

Mikate makumi awiri ikwanira anthu ambiri

42 Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m’thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.

43 Koma mnyamata wake anati, Chiyani? Ndigawire amuna zana ichi kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasiyako.

44 Potero anawagawira, nadya, nasiyapo, monga mwa mau a Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/4-95c655919329f382124d2077541740fb.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 5

Naamani wakhateyo achiritsidwa

1 Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.

2 Ndipo Aaramu adatuluka magulumagulu, nabwera nalo m’ndende buthu lochokera ku dziko la Israele, natumikira mkazi wa Naamani iyeyu.

3 Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwamneneriali mu Samariya, akadamchiritsa khate lake.

4 Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.

5 Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatengasilivamatalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.

6 Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, yakuti, Pakulandira kalata iyi, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake.

7 Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang’amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.

8 Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang’amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang’amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israele.

9 M’mwemo Naamani anadza ndi akavalo ake ndi magaleta ake, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa.

10 Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe mu Yordani kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.

11 Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m’mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.

12 Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a mu Israele? Ndilekerenji kukasamba m’mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nachoka molunda.

13 Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?

14 Potero anatsika, namira mu Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng’ono, nakonzeka.

15 Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu.

16 Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pake, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkakamiza achilandire, koma anakana.

17 Ndipo Naamani anati, Mukakana, andipatse akatundu a dothi osenza nyuru ziwiri; pakuti mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova.

18 Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi; akalowa mbuye wanga m’nyumba ya Rimoni kulambiramo, nakatsamira padzanja langa, nanenso ndikagwadira m’nyumba ya Rimoni, pakugwadira ine m’nyumba ya Rimoni, Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi.

19 Ndipo ananena naye, Pita mumtendere. Ndipo anachoka, nayenda kanthawi.

Gehazi alangidwa ndi khate

20 Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m’manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.

21 Motero Gehazi anatsata Naamani. Ndipo pamene Naamani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagaleta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi?

22 Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri.

23 Nati Naamani, Ulole ulandire matalente awiri. Namkakamiza namanga matalente awiri a siliva m’matumba awiri, ndi zovala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ake awiri; iwo anatsogola atazisenza.

24 Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m’manja mwao, naziika m’nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nachoka.

25 Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?

26 Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeze kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo ino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda yaazitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng’ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi?

27 Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/5-e91135f44109863d00953d86d9614426.mp3?version_id=1068—