Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 14

Abisalomu abwera ku Yerusalemu

1 Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.

2 Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu.

3 Nulowe kwa mfumu, nulankhule nayo monga momwemo. Chomwecho Yowabu anampangira mau.

4 Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.

5 Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? Iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira.

6 Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana aamuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha.

7 Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.

8 Ndipo mfumu inanena ndi mkaziyo, Pita kunyumba yako, ndipo ndidzalamulira za iwe.

9 Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wachifumu wao zikhale zopanda chifukwa.

10 Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine aliyense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.

11 Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.

12 Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.

13 Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake.

14 Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.

15 Chifukwa chake tsono chakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndicho kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzachita chopempha mdzakazi wake.

16 Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wake m’dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kutichotsa ku cholowa cha Mulungu.

17 Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.

18 Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.

19 Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m’kamwa mwa mdzakazi wanu.

20 Mnyamata wanu Yowabu anachita chinthu ichi kuti asandulize mamvekedwe a mlanduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse zili m’dziko lapansi.

21 Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.

22 Ndipo Yowabu anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yowabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yachita chopempha mnyamata wake.

23 Chomwecho Yowabu ananyamuka nanka ku Gesuri, nabwera naye Abisalomu kuYerusalemu.

24 Ndipo mfumu inati, Apatukire kunyumba ya iye yekha, koma asaone nkhope yanga. Chomwecho Abisalomu anapatukira kunyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.

25 Ndipo mu Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pamutu wake mwa iye munalibe chilema.

26 Ndipo pometa tsitsi lake amameta potsiriza chaka, chifukwa tsitsi linamlemerera, chifukwa chake atalimeta anayesa tsitsi la pamutu wake, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.

27 Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana aamuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope.

28 Ndipo Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, osaona nkhope ya mfumu.

29 Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera.

30 Chifukwa chake iye anati kwa anyamata ake, Onani munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m’mundawo.

31 Pamenepo Yowabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu kunyumba yake, nanena naye, Chifukwa ninji anyamata anu anatentha za m’munda mwanga;

32 Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.

33 Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/14-95907f2b1ec9e20e16d47603ad4d93ce.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 15

Kupanduka kwa Abisalomu, ndi kuthawa kwa Davide

1 Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera.

2 Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima panjira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumzinda uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele.

3 Abisalomu nanena naye, Ona zokamba zako ndizo zabwino ndi zolungama; koma mfumu sinauze wina kuti adzamve za iwe.

4 Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m’dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mlandu wake kapena chifukwa chake, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamchitira zachilungamo!

5 Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu aliyense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lake, namgwira, nampsompsona.

6 Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele.

7 Ndipo kunali pakutha zaka zinai Abisalomu ananena kwa mfumu, Mundilole ndimuke ku Hebroni ndikachite chowinda changa ndinachiwindira Yehova.

8 Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri mu Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu kuYerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova.

9 Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Chomwecho ananyamuka, nanka ku Hebroni.

10 Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.

11 Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m’kupulukira kwao, osadziwa kanthu.

12 Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.

13 Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israele itsata Abisalomu.

14 Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa.

15 Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.

16 Mfumu nituluka, ndi banja lake lonse linamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi aang’ono, kusunga nyumbayo.

17 Ndipo mfumu inatuluka, ndi anthu onse anamtsata; naima kunyumba ya pa yokha.

18 Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.

19 Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopirikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.

20 Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe.

21 Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.

22 Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana aang’ono onse amene anali naye.

23 Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu.

Zadoki ndi Abiyatara abwerera ndi likasa ku Yerusalemu

24 Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamulalikasa la chipanganola Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m’mzindamo.

25 Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwerera nalo likasa la Mulungu kumzindako; akandikomera mtima Yehova, Iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso ili, ndi pokhala pake pomwe.

26 Koma Iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andichitire chimene chimkomera.

27 Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumzinda mumtendere pamodzi ndi ana ako aamuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.

28 Ona ndidzaima pa madooko a m’chipululu kufikira afika mau ako akunditsimikizira ine.

29 Chifukwa chake Zadoki ndi Abiyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko.

30 Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.

31 Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.

32 Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai Mwariki anadzakomana naye ali ndi malaya ake ong’ambika, ndi dothi pamutu pake.

33 Ndipo Davide ananena naye, Ukapita pamodzi ndi ine udzandilemetsa;

34 koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.

35 Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abiyatara ansembewo kodi? Motero chilichonse udzachimva cha m’nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abiyatara ansembewo.

36 Onani, ali nao komweko ana aamuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze chilichonse mudzachimva.

37 Chomwecho Husai bwenzi la Davide anadza m’mzindamo; ndipo Abisalomu anafika ku Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/15-63c875280022ce6038f7c5e2df28be7b.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 16

Davide akomana ndi Ziba

1 Ndipo pamene Davide anapitirira pang’ono pamutu paphiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao abulu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi nchinchi zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m’dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo.

2 Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m’dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m’chipululu akamweko.

3 Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala kuYerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.

4 Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.

Simei atukwana Davide

5 Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.

6 Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali ku dzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwake.

7 Ndipo anatero Simei pakutukwana, Choka, choka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe;

8 Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m’malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m’dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m’kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi.

9 Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake.

10 Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?

11 Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m’matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.

12 Kapena Yehova adzayang’anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m’malo mwa kunditukwana kwa lero.

13 Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m’njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi.

14 Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko.

Za uphungu woipa wa Ahitofele

15 Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse aamuna a Israele, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofele pamodzi naye.

16 Ndipo kunali pakudza kwa Abisalomu Husai Mwariki, bwenzi la Davide, Husai ananena ndi Abisalomu, Mfumu ikhale ndi moyo. Mfumu ikhale ndi moyo.

17 Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?

18 Husai nanena ndi Abisalomu, Iai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israele, ine ndili wake, ndipo ndidzakhala naye iyeyu.

19 Ndiponso ndidzatumikira yani? Si pamaso pa mwana wake nanga? Monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu.

20 Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite.

21 Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi aang’ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisraele onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.

22 Chomwecho iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi aang’ono a atate wake pamaso pa Aisraele onse.

23 Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/16-e1c1af682979aefcf23877cea3690d89.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 17

1 Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide;

2 ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;

3 ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere.

4 Ndipo mauwa anamuyenerera Abisalomu, ndi akulu onse a Israele.

Uphungu wa Husai

5 Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai Mwariki yemwe, timvenso chimene anene iye.

6 Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe.

7 Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino.

8 Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.

9 Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, aliyense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.

10 Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wake ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisraele onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.

11 Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.

12 Chomwecho tidzamvumbulukira pamalo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye.

13 Ndiponso ngati walowa kumzinda wina, Aisraele onse adzabwera ndi zingwe kumzindako, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang’ono kumeneko.

14 Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.

15 Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti.

16 Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.

17 Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m’mzinda.

18 Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anachoka msanga onse awiri, nafika kunyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali nacho chitsime pabwalo pake; ndipo anatsikira m’menemo.

19 Ndipo mkazi anatenga chivundikiro nachiika pakamwa pa chitsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sichinadziwike.

20 Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka kuYerusalemu.

Davide ndi anthu ake aoloka Yordani

21 Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m’chitsime, nanka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu.

22 Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m’mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.

23 Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m’manda a atate wake.

Abisalomu ndi anthu ake aolokanso Yordani

24 Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye.

25 Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m’malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.

26 Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m’dziko la Giliyadi.

27 Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,

28 iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina,

29 ndi uchi ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng’ombe, kuti adye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m’chipululumo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/17-f2adeb6b8e61aada20305195d2310c17.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 18

Abisalomu agonja pankhondo, naphedwa

1 Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.

2 Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang’anire Yowabu, lina aliyang’anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang’anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.

3 Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m’mzinda.

4 Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu inaima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.

5 Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.

6 Chomwecho anthuwo anatulukira kuthengo kukamenyana ndi Israele; nalimbana ku nkhalango ya ku Efuremu.

7 Ndipo anthu a Israele anakanthidwa pamenepo pamaso pa anyamata a Davide, ndipo kunali kuwapha kwakukulu kumeneko tsiku lomwelo, anthu zikwi makumi awiri.

8 Pakuti nkhondo inatanda padziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga.

9 Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yake, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkulu. Ndipo mutu wake unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye inapitirira.

10 Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yowabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.

11 Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.

12 Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m’dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m’kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.

13 Ndikadachita chonyenga pa moyo wake, palibe mlandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsutsa.

14 Pomwepo Yowabu anati, Sindiyenera kuchedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.

15 Ndipo anyamata khumi onyamula zida zake za Yowabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha.

16 Ndipo Yowabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupirikitsa Aisraele; pakuti Yowabu analetsa anthuwo.

17 Ndipo anatenga Abisalomu namponya m’chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.

18 Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m’chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.

Davide alira Abisalomu

19 Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera chilango adani ake.

20 Ndipo Yowabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, chifukwa mwana wa mfumu wafa.

21 Pamenepo Yowabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yowabu, nathamanga.

22 Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kachiwiri kwa Yowabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yowabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo?

23 Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi.

24 Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.

25 Pamenepo mlondayo anafuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira.

26 Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakuchipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, Iyenso abwera ndi mau.

27 Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki. Ndipo mfumu inati, Iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.

28 Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.

29 Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwe ngati kutani.

30 Ndipo mfumu inati, Patuka nuime apa. Napatuka, naimapo.

31 Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.

32 Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukuchitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.

33 Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/18-f350444df31a95afcb7a1577118c8f26.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 19

Yowabu adzudzula Davide

1 Ndipo anauza Yowabu, Onani mfumu ilikulira misozi, nilira Abisalomu.

2 Ndipo chipulumutso cha tsiku lija chinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu ili ndi chisoni chifukwa cha mwana wake.

3 Ndipo tsiku lija anthu analowa m’mzinda kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo.

4 Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana.

5 Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang’ono;

6 m’mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu.

7 Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.

8 Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pachipata. Ndipo anauza anthu kuti, Onani mfumu ilikukhala pachipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisraele adathawa, munthu yense ku hema wake.

9 Ndipo anthu onse a m’mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m’dzanja la adani athu, natipulumutsa m’dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m’dziko kuthawa Abisalomu.

10 Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Chifukwa chake tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?

Davide abwerera kunka ku Yerusalemu

11 Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am’mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.

12 Inu ndinu abale anga, muli fupa langa ndi mnofu wanga; chifukwa ninji tsono muli am’mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?

13 Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m’malo mwa Yowabu.

14 Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.

15 Chomwecho mfumu inabwera nifika ku Yordani. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordani.

16 Ndipo Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini, wa ku Bahurimu, anafulumira natsika pamodzi ndi anthu a Yuda kuti akakomane ndi mfumu Davide.

17 Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.

18 Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.

19 Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka kuYerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu.

20 Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinachimwa; chifukwa chake, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.

21 Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simei chifukwa cha kutemberera wodzozedwa wa Yehova?

22 Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa mu Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero?

23 Ndipo mfumu inanena ndi Simei, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye.

Mefiboseti akomana ndi Davide

24 Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasambe mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.

25 Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Chifukwa ninji sunapite nane Mefiboseti?

26 Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira bulu kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndili wopunduka.

27 Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu; chifukwa chake chitani chimene chikukomerani.

28 Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?

29 Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.

30 Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.

Barizilai akomana ndi Davide

31 Ndipo Barizilai, Mgiliyadi anatsika kuchokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordani ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordani.

32 Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka chakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.

33 Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.

34 Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu?

35 Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oimba? Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.

36 Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordani pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphotho yotere?

37 Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m’mzinda wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.

38 Ndipo mfumu inayankha, Kimuhamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamchitira chimene chikukomereni; ndipo chilichonse mukadzapempha kwa ine ndidzakuchitirani inu.

39 Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake.

Nsanje pakati pa Yuda ndi Israele

40 Chomwecho mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Kimuhamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israele.

41 Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?

42 Ndipo anthu onse a Yuda anayankha anthu a Israele. Chifukwa mfumu ili ya chibale chathu; tsono mulikukwiyiranji pa mlandu umenewu? Tinadya konse za mfumu kodi? Kapena kodi anatipatsa mtulo uliwonse?

43 Ndipo anthu a Israele anayankha anthu a Yuda, nati, Ife tili ndi magawo khumi mwa mfumu, ndi mwa Davide koposa inu; chifukwa ninji tsono munatipeputsa ife, osayamba kupangana nafe za kubwezanso mfumu yathu? Koma mau a anthu a Yuda anali aukali koposa mau a anthu a Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/19-662918239c96845129277106b3fd8f48.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 20

Mpanduko ndi imfa ya Sheba

1 Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.

2 Chomwecho anthu onse a Israele analeka kutsata Davide, natsata Sheba mwana wa Bikiri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordani kufikira kuYerusalemu.

3 Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi aang’onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m’nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.

4 Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso.

5 Chomwecho Amasa anamuka kukaitana anthu a Yuda asonkhane; koma anachedwa, napitiriza nthawi imene idamuikira.

6 Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze mizinda ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.

7 Ndipo anatuluka namtsata anthu a Yowabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onse amphamvu; natuluka mu Yerusalemu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.

8 Pamene anafika iwo pamwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m’chimake m’chuuno mwake; ndipo m’kuyenda kwake lidasololoka.

9 Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.

10 Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m’dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m’mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.

11 Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu.

12 Ndipo Amasa analikukunkhulira m’mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye.

13 Atamchotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumtsata Yowabu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.

14 Ndipo anapyola mafuko onse a Israele kufikira ku Abele ndi ku Betimaaka, ndi kwa Abikiri onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso.

15 Ndipo anadza nammangira misasa mu Abele wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mzindawo, ndipo unagunda linga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yowabu anakumba lingalo kuti aligwetse.

16 Pamenepo mkazi wanzeru wa m’mzindamo anafuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yowabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndilankhule nanu.

17 Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva.

18 Ndipo iye analankhula, nati, Kale adanena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abele; ndipo potero mlandu udatha.

19 Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?

20 Ndipo Yowabu anayankha nati, Iai ndi pang’ono ponse, chikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga.

21 Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka mumzinda muno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga.

22 Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka mumzindamo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu.

23 Ndipo Yowabu anali woyang’anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang’anira Akereti ndi Apeleti;

24 ndi Adoramu anayang’anira msonkho; ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri;

25 ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe;

26 ndiponso Ira Myairi anali ansembe a Davide.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/20-30d14305c7cf97d8ef2dc1d79a6039de.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 21

Njala m’dziko, chifukwa chake, matsirizidwe ake

1 Ndipo m’masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.

2 Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).

3 Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova?

4 Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifunasilivakapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa mu Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.

5 Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife chotionongera kuti tisakhalenso m’malire ali onse a Israele.

6 Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.

7 Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.

8 Koma mfumu inatenga ana aamuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Saulo, ndiwo Arimoni ndi Mefiboseti; ndiponso ana aamuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Saulo, amene iye anambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola;

9 niwapereka m’manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m’phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m’masiku a kukolola, m’masiku oyamba, poyamba kucheka barele.

10 Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalole mbalame za m’mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo zakuthengo usiku.

11 Ndipo anauza Davide chimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng’ono wa Saulo anachita.

12 Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m’khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;

13 nachotsa kumeneko mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapachikidwa.

14 Naika mafupa a Saulo ndi Yonatani mwana wake ku dziko la Benjamini mu Zela, m’manda a Kisi atate wake; nachita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pake Mulungu anapembedzeka za dzikolo.

Nkhondo zakupha ziphona za Afilisti

15 Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.

16 Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.

17 Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.

18 Ndipo kunali chitapita ichi, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa.

19 Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unanga mtanda wa woombera nsalu.

20 Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.

21 Ndipo pakutonza Israele iyeyu, Yonatani mwana a Simea mbale wa Davide anamupha.

22 Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/21-dbab99efb488033e27a03ad83fe84c80.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 22

Nyimbo yoyamikira Yehova ya Davide

1 Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la Saulo.

2 Ndipo anati,

Yehova ndiye thanthwe langa,

ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.

3 Mulungu wa thanthwe langa,

Iye ndidzamkhulupirira;

chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa,

nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;

Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.

4 Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande;

chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.

5 Pakuti mafunde a imfa anandizinga,

mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine.

6 Zingwe za kumanda zinandizingira;

misampha ya imfa inandifikira ine.

7 M’kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,

inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;

ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake,

ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.

8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.

Maziko a dziko la kumwamba anasunthika.

Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.

9 M’mphuno mwake munatuluka utsi,

ndi moto wotuluka m’kamwa mwake unaononga;

makala anayaka nao.

10 Anaweramitsa miyambanso, natsika;

ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.

11 Ndipo Iye anaberekeka pakerubinauluka;

inde anaoneka pa mapiko a mphepo.

12 Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye,

kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga.

13 Cheza cha pamaso pake

makala a moto anayaka.

14 Yehova anagunda kumwamba;

ndipo Wam’mwambamwamba ananena mau ake.

15 Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza;

mphezi, nawaopsa.

16 Pamenepo m’munsi mwa nyanja munaoneka,

maziko a dziko anaonekera poyera,

ndi mtonzo wa Yehova,

ndi mpumo wa mpweya wa m’mphuno mwake.

17 Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga;

Iye ananditulutsa m’madzi aakulu.

18 Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,

kwa iwo akudana ndi ine;

pakuti anandiposa mphamvu.

19 Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;

koma Yehova anali mchirikizo wanga.

20 Iye ananditulutsanso ku malo aakulu;

Iye anandipulumutsa,

chifukwa akondwera ndi ine.

21 Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;

monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho.

22 Pakuti ndinasunga njira za Yehova,

osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.

23 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga;

ndipo za malemba ake, sindinawapatukire.

24 Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye,

ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga.

25 Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;

monga mwa kuyera kwanga pamaso pake.

26 Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo,

ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro.

27 Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;

ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.

28 Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;

koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.

29 Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;

ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.

30 Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;

ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.

31 Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro;

mau a Yehova anayesedwa;

Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.

32 Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?

Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?

33 Mulungu ndiye linga langa lamphamvu;

ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake.

34 Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala;

nandiika pa misanje yanga.

35 Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;

kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.

36 Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;

ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.

37 Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,

ndi mapazi anga sanaterereke.

38 Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga;

ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha.

39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sangathe kuuka,

inde anagwa pansi pa mapazi anga.

40 Pakuti Inu munandimanga m’chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo;

munandigonjetsera akundiukira.

41 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,

kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.

42 Anayang’ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;

ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe.

43 Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko,

ndinawapondereza ngati dothi la m’makwalala.

44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;

munandisunga ndikhale mutu waamitundu;

Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine.

45 Alendo adzandigonjera ine,

pakumva za ine, adzandimvera pomwepo.

46 Alendo adzafota,

nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.

47 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;

ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa;

48 inde Mulungu wakundibwezera chilango ine,

ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.

49 Amene anditulutsa kwa adani anga;

inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;

mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.

50 Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,

ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.

51 Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu;

naonetsera chifundo wodzozedwa wake,

kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/22-06f0c38dcd56c1f96249c9363cdb4311.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 23

Nyimbo yotsiriza ya Davide

1 Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:

Atero Davide mwana wa Yese,

atero munthu wokwezedwa,

ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo,

ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.

2 Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine,

ndi mau ake anali pa lilime langa.

3 Mulungu wa Israele anati,

Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine;

kudzakhala woweruza anthu molungama;

woweruza m’kuopa Mulungu.

4 Iye adzakhala ngati kuunika kwa m’mawa,

potuluka dzuwa, M’mawa mopanda mitambo;

pamene msipu uphuka kutuluka pansi,

chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.

5 Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu;

koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha,

lolongosoka mwa zonse ndi losungika;

pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse,

ndi kufuma kwanga konse,

kodi sadzachimeretsa?

6 Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya,

pakuti siigwiridwa ndi dzanja;

7 koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo;

ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m’malo mwao.

Angwazi a Davide

8 Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.

9 Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;

10 iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m’mbuyo mwake kukafunkha kokha.

11 Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Muharari. Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pa Lehi pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo.

12 Koma iyeyo anaima pakati pamundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu.

13 Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m’phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m’chigwa cha Refaimu.

14 Pamenepo Davide anali m’linga, ndi boma la Afilisti linali mu Betelehemu.

15 Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! Wina akadandipatsa madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu chili pachipatapo!

16 Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, ndipo zinatunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.

17 Nati, Ndisachite ichi ndi pang’ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi.

18 Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

19 Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikane ndi atatu oyamba.

20 Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m’mbuna nyengo ya chipale chofewa;

21 ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m’dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m’dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

22 Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

23 Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikane ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang’anira olindirira ake.

24 Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;

25 Sama Mharodi, Elika Mharodi;

26 Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekowa.

27 Abiyezere Mwanatoti, Mebunai Muhusa;

28 Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa;

29 Helebi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea wa ana a Benjamini;

30 Benaya Mpiratoni, Hidai wa ku timitsinje ta Gaasi;

31 Abiyaliboni Mwarabati, Azimaveti Mbahurimi;

32 Eliyaba Msaaliboni wa ana a Yaseni, Yonatani;

33 Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari;

34 Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele Mgiloni;

35 Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba;

36 Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi;

37 Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya;

38 Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri;

39 Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/23-8ccdfe58f58a58338ec50c7f9a340fd8.mp3?version_id=1068—