Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 26

Davide alekanso Saulo osamupha

1 Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m’phiri la Hakila, kupenya kuchipululu!

2 Ndipo Saulo ananyamuka, natsikira chipululu cha Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israele osankhika, kukafuna Davide m’chipululu cha Zifi.

3 Saulo namanga zithando m’phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.

4 Chifukwa chake Davide anatumiza ozonda, nazindikira kuti Saulo anabwera ndithu.

5 Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake.

6 Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.

7 Chomwecho Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Saulo anagona tulo m’kati mwa linga la magaleta, ndi mkondo wake wozika kumutu kwake; ndi Abinere ndi anthuwo anagona pomzinga iye.

8 Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m’dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.

9 Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?

10 Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.

11 Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwake, ndi chikho cha madzi, ndipo tiyeni, timuke.

12 Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m’tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse.

13 Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba paphiri; pakati pao panali danga lalikulu;

14 ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?

15 Davide nati kwa Abinere, Sindiwe mwamuna weniweni kodi? Ndani mwa Aisraele anafanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? Pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.

16 Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikire mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti?

17 Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.

18 Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m’dzanja langa muli choipa chotani?

19 Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.

20 Chifukwa chake tsono, mwazi wanga usagwe pansi kutali ndi Yehova; pakuti mfumu ya Israele yatuluka kudzafuna nsabwe, monga munthu wosaka nkhwali pamapiri.

21 Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.

22 Davide nayankha, nati, Tapenyani mkondo wa mfumu! Abwere mnyamata wina kuutenga.

23 Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m’dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.

24 Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.

25 Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/26-b98ae642e4e59491a07ac35012ffd8a8.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 27

1 Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m’malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m’dzanja lake.

2 Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.

3 Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala.

4 Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso.

5 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kuminda, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji mu mzinda wachifumu pamodzi ndi inu?

6 Ndipo Akisi anampatsa Zikilagi tsiku lomweli; chifukwa chake Zikilagi ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.

7 Ndipo kuwerenga kwake kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko chaka chimodzi ndi miyezi inai.

8 Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m’dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.

9 Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunge ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng’ombe, ndi abulu, ndingamira, ndi zovala; nabwera nafika kwa Akisi.

10 Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.

11 Ndipo Davide sadasunge wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.

12 Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/27-af70c510ae202128647983831e70ed96.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 28

Saulo afunsira mkazi wobwebweta ku Endori

1 Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisraele. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzatuluka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako.

2 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.

3 M’menemo Samuele ndipo atafa, ndipo Aisraele onse atalira maliro ake, namuika mu Rama, m’mzinda mwao. Ndipo Saulo anachotsa m’dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse.

4 Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.

5 Ndipo pamene Saulo anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wake unanjenjemera kwakukulu.

6 Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.

7 Tsono Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ake anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta.

8 Ndipo Saulo anadzizimbaitsa navala zovala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire aliyense ndidzakutchulira dzina lake.

9 Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa chimene anachita Saulo, kuti analikha m’dzikomo obwebweta onse, ndi aula; chifukwa ninji tsono mulikutchera moyo wanga msampha, kundifetsa.

10 Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.

11 Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samuele.

12 Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau aakulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo.

13 Ndipo mfumuyo inanena naye, Usaope, kodi ulikona chiyani? Mkaziyo nanena ndi Saulo, Ndilikuona milungu ilikukwera kutuluka m’kati mwa dziko.

14 Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira.

15 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.

16 Ndipo Samuele ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako?

17 Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang’amba ufumuwo, kuuchotsa m’dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.

18 Chifukwa sunamvere mau a Yehova, ndi kukwaniritsa mkwiyo wake woopsa pa Amaleke, chifukwa chake Yehova wakuchitira chinthu ichi lero.

19 Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m’dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m’dzanja la Afilisti.

20 Pomwepo Saulo anagwa pansi tantha, naopa kwakukulu, chifukwa cha mau a Samuele; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wake wonse anakhala osadya kanthu.

21 Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine.

22 Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.

23 Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ake, pamodzi ndi mkaziyo anamkakamiza; iye anamvera mau ao. Chomwecho anauka pansi, nakhala pakama.

24 Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang’ombe wonenepa m’nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa;

25 nabwera nazo kwa Saulo ndi kwa anyamata ake; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nachoka usiku womwewo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/28-a800276c4ba57dc452e3e422f84edeb6.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 29

Afilisti abweza Davide ku nkhondo

1 Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.

2 Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ake ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi.

3 Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa achitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Saulo, mfumu ya Israele, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.

4 Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa?

5 Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang’ombe m’magulu ao, kuti,

Saulo anapha zikwi zake,

koma Davide zikwi zake zankhani?

6 Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kutuluka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m’gulumo kundikomera; pakuti sindinaona choipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.

7 Chifukwa chake, bwerera, numuke mumtendere, kuti angaipidwe mtima nawe akalonga a Afilisti.

8 Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinachitanji? Ndipo munapeza chiyani mwa mnyamata wanu nthawi yonse ndili pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?

9 Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, Iye asamuke nafe kunkhondoko.

10 Chifukwa chake ulawirire m’mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m’mawa, mumuke kutacha.

11 Chomwecho Davide analawirira, iye ndi anthu ake, kuti amuke m’mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera Yezireele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/29-b91cf043566a8902ea8eb171a59a955d.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 30

Davide alanditsa a ku Zikilagi m’manja mwa Aamaleke

1 Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;

2 nagwira akazi ndi onse anali m’mwemo, aakulu ndi aang’ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka.

3 Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumzindako, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo.

4 Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.

5 Ndipo akazi awiri a Davide anatengedwa ukapolo, Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele.

6 Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.

7 Ndipo Davide ananena ndi Abiyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kunoefodi. Abiyatara nabwera ndi efodi kwa Davide.

8 Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.

9 Chomwecho Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena.

10 Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m’mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.

11 Ndipo ena anapeza Mwejipito kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa chakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;

12 nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi.

13 Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? Ufumira kuti? Nati iye, Ndili mnyamata wa ku Ejipito, kapolo wa Mwamaleke; mbuye wanga anandisiya, chifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.

14 Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto.

15 Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m’dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.

16 Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, chifukwa cha chofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.

17 Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wake; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pangamira, nathawa.

18 Ndipo Davide analanditsa zonse anazitenga Aamaleke, napulumutsa akazi ake awiri.

19 Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang’ono kapena kakakulu, ana aamuna kapena ana aakazi, kapena chuma kapena china chilichonse cha zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse.

20 Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng’ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide.

21 Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.

22 Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuke nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke.

23 Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m’dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe.

24 Ndipo ndani adzavomerezana nanu mlandu uwu? Pakuti monga gawo lake la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lake la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana chimodzimodzi.

25 Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ichi, chikhale lemba ndi chiweruzo pa Aisraele.

26 Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.

27 Anatumiza kwa iwo a ku Betele, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwera, ndi kwa iwo a ku Yatiri;

28 ndi kwa iwo a ku Aroere, ndi kwa iwo a ku Sifimoti, ndi kwa iwo a ku Esitemowa;

29 ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a ku m’mizinda ya Ayerameele, ndi kwa iwo a m’mizinda ya Akeni;

30 ndi kwa iwo a ku Horoma, ndi kwa iwo a ku Borasani, ndi kwa iwo a ku Ataki;

31 ndi kwa iwo a ku Hebroni, ndi kumalo konse kumene Davide ndi anthu ake ankayendayenda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/30-b3459f2dc69d5a103407831dd375e1d2.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 31

Saulo ndi ana ake atatu aphedwa ndi Afilisti pa Gilibowa

1 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m’phiri la Gilibowa.

2 Ndipo Afilisti anapirikitsa, osawaleka Saulo ndi ana ake; ndipo Afilisti anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.

3 Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo.

4 Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.

5 Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye.

6 Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija.

7 Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m’menemo.

8 Ndipo kunali m’mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m’phiri la Gilibowa.

9 Ndipo anadula mutu wake, natenga zida zake, natumiza m’dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira kunyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu.

10 Ndipo anaika zida zake m’nyumba yaAsitaroti; napachika mtembo wake ku linga la ku Beteseani.

11 Koma pamene a ku Yabesi-Giliyadi anamva zimene Afilisti anamchitira Saulo,

12 ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko.

13 Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/31-610789dde4cb7b5a6b397c61a813dec3.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba za ufumu wa Davide ndiponso za nkhondo zimene iye anamenya ndi adani ake m’dziko mwake ndiponso ndi maiko oyandikana ndi dziko la Israele, pofuna kulimbitsa ndi kukulitsa ufumu wakewo.

Davide anali munthu wa chikhulupiriro cholimba ndi wokonda Mulungu kwambiri, ndipo amadziwa kukopa mitima ya anthu ake. Komabe nthawi zina anagwa m’machimo oopsa chifukwa chotsata zilakolako ndi zikhumbitso zoipa. Mneneri Natani atamdzudzula chifukwa cha zoipazo, iye anadzichepetsa navomera kuti walakwadi nkuvomera chilango chimene Mulungu apereka.

Aisraele adatengeka mtima ndi mfumu Davide, ndipo patapita zaka zambiri, pamene dziko lao lidapasuka, Aisraelewo ankakumbukira khalidwe lake labwino ndi ntchito zake zazikulu, kotero kuti ankalakalaka kukhalanso ndi mfumu ina yokhala ndi mtima ngati wa Davide, pakati pa zidzukulu zake.

Za mkatimu

Ufumu wa Davide mu dziko la Yuda

1.1—4.12

Ufumu wa Davide m’dziko lonse la Israele

5.1—24.25

a. Zaka zoyamba

5.1—10.19

b. Davide ndi Bateseba

11.1—12.25

c. Ana ake amuukira ndiponso zovuta zina

12.26—20.26

d. Zaka zotsiriza za ufumu wake

21.1—24.25

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 1

Amuuza Davide za imfa ya Saulo

1 Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri;

2 pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong’ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.

3 Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele.

4 Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.

5 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa?

6 Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.

7 Ndipo iye pakucheukira m’mbuyo mwake anandiona, nandiitana. Ndipo ndinayankha, Ndine.

8 Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine Mwamaleke.

9 Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, chifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe.

10 M’mwemo ndinakhala pambali pake ndi kumtsiriza chifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wake, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pake, ndi chigwinjiri cha pa mkono wake, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.

11 Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing’amba; nateronso anthu onse okhala naye.

12 Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.

13 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke.

14 Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaope kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova?

15 Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye.

16 Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.

Davide alirira Saulo ndi Yonatani

17 Ndipo Davide analirira Saulo ndi Yonatani mwana wake ndi nyimbo iyi ya maliro;

18 nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m’buku la Yasara,

19 Ulemerero wako, Israele, unaphedwa pa misanje yako.

Ha! Adagwa amphamvu!

20 Usachinene ku Gati,

usachibukitse m’makwalala a Asikeloni,

kuti ana aakazi a Afilisti angasekere,

kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.

21 Mapiri inu a Gilibowa,

pa inu pasakhale mame kapena mvula,

kapena minda yakutengako zopereka.

Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa,

chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.

22 Uta wa Yonatani sunabwerere,

ndipo lupanga la Saulo silinabwerere chabe,

pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.

23 Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m’miyoyo yao,

ndipo mu imfa yao sanasiyane;

anali nalo liwiro loposa chiombankhanga,

anali amphamvu koposa mikango.

24 Ana aakazi inu a Israele, mulirire Saulo,

amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa,

amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu.

25 Ha! Amphamvuwo anagwa pakati pa nkhondo!

Yonatani anaphedwa pamisanje pako.

26 Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe,

mbale wanga Yonatani;

wandikomera kwambiri;

chikondi chako, ndinadabwa nacho,

chinaposa chikondi cha anthu aakazi.

27 Ha! Amphamvuwo anagwa,

ndi zida za nkhondo zinaonongeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/1-1c93e06fecc8f07e74cfd9f28faf5269.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 2

Davide alowa ufumu wa Yuda

1 Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m’mizinda wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.

2 Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele.

3 Ndipo Davide anakwera nao anyamata ake okhala naye, munthu yense ndi banja lake; iwowa nakhala m’midzi ya Hebroni.

4 Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.

5 Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika.

6 Ndipo tsopano Yehova achitire inu chokoma ndi choonadi; inenso ndidzakubwezerani chokoma ichi, popeza munachita chinthuchi.

7 Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.

Isiboseti alowa ufumu wa Israele

8 Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;

9 namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.

10 Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.

11 Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi.

Ayuda ndi Aisraele alimbana ku Gibiyoni

12 Ndipo Abinere mwana wa Nere ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Saulo anatuluka ku Mahanaimu kunka ku Gibiyoni.

13 Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo.

14 Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire.

15 Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Saulo, ndi khumi ndi awiri anyamata a Davide.

16 Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m’nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni.

17 Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abinere ndi anthu a Israele anathawa pamaso pa anyamata a Davide.

18 Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.

19 Ndipo Asahele anapirikitsa Abinere. Ndipo m’kuthamanga kwake sanapatukire kulamanja, kapena kulamanzere, pakutsata Abinere.

20 Pomwepo Abinere anacheuka nati, Kodi ndi iwe Asahele? Iye nayankha, Ndine.

21 Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye.

22 Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?

23 Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi mutu wa mkondo m’mimba mwake, ndi mutuwo unatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.

24 Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, panjira ya ku chipululu cha Gibiyoni.

25 Ndipo ana a Benjamini anaunjikana pamodzi kutsata Abinere, nakhala gulu limodzi, naima pamwamba pa chitunda.

26 Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?

27 Yowabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapanda kunena, anthu akadabalalika m’mawa osatsata yense mbale wake.

28 Chomwecho Yowabu anaomba lipenga, anthu onse naima, naleka kupirikitsa Aisraele, osaponyana naonso.

29 Ndipo Abinere ndi anthu ake anachezera usiku wonse kupyola chidikha, naoloka Yordani, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu.

30 Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele.

31 Koma anyamata a Davide anakantha anthu a Benjamini ndi a Abinere, namwalira mazana atatu mphambu makumi asanu ndi limodzi.

32 Ndipo ananyamula Asahele namuika m’manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/2-0ee27ac230e960d2b6a310649eda3dd9.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 3

1 Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere.

Ana obadwira Davide ku Hebroni

2 Ndipo ana a Davide anabadwira ku Hebroni. Mwana woyamba ndiye Aminoni, wa Ahinowamu wa ku Yezireele;

3 wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;

4 ndi wachinai Adoniya mwana wa Hagiti; ndi wachisanu Sefatiya mwana wa Abitala;

5 ndi wachisanu ndi chimodzi Itireamu wa Egila mkazi wa Davide. Awa anambadwira Davide ku Hebroni.

Abinere apangana ndi Davide

6 Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide, Abinere analimbikira nyumba ya Saulo.

7 Ndipo Saulo adali ndi mkazi wamng’ono, dzina lake ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abinere, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng’ono wa atate wanga?

8 Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m’dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu.

9 Mulungu alange Abinere, naonjezepo, ndikapanda kumchitira Davide monga Yehova anamlumbirira;

10 kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.

11 Ndipo iye sanakhoze kuyankha Abinere mau amodzi chifukwa cha kumuopa iye.

12 Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu.

13 Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.

14 Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.

15 Pomwepo Isiboseti anatumiza namchotsera kwa mwamuna wake, kwa Palatiele mwana wa Laisi.

16 Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.

17 Ndipo Abinere analankhula nao akulu a Israele nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu;

18 chitani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.

19 Ndipo Abinere analankhulanso m’kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m’makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini.

20 Abinere nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abinere ndi anthu okhala naye madyerero.

21 Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.

Yowabu apha Abinere

22 Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.

23 Tsono pofika Yowabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yowabu nati, Abinere mwana wa Nere anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendere.

24 Pomwepo Yowabu anadza kwa mfumu, nati, Mwachitanji? Taonani, Abinere anadza kwa inu, chifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti achokedi.

25 Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu.

26 Ndipo Yowabu anatuluka kwa Davide, natumizira Abinere mithenga, amene anambweza ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanachidziwe.

27 Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m’mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.

28 Ndipo pambuyo pake, pakuchimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osachimwira mwazi wa Abinere mwana wa Nere, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;

29 chilango chigwere pamutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya.

30 Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo.

Davide alira Abinere

31 Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng’ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m’chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha.

32 Ndipo anaika Abinere ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ake nilira ku manda a Abinere, nalira anthu onse.

33 Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti,

Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru?

34 Manja anu sanamangidwe,

mapazi anu sanalongedwe m’zigologolo;

monga munthu wakugwa ndi anthu oipa

momwemo mudagwa inu.

Ndipo anthu onse anamliranso.

35 Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.

36 Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.

37 Momwemo anthu onse ndi Aisraele onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumire kwa mfumu kupha Abinere mwana wa Nere.

38 Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwe kodi kuti kalonga ndi munthu womveka wagwa lero mu Israele?

39 Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/3-9e537c503b5b1bc046cd33d7368d7fd2.mp3?version_id=1068—