Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 16

Samuele adzoza Davide akhale mfumu

1 Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.

2 Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng’ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.

3 Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake.

4 Ndipo Samuele anachita chimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akulu a mzindawo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?

5 Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Yese ndi ana ake, nawaitanira kunsembeko.

6 Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang’ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake.

7 Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang’ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.

8 Pamenepo Yese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samuele. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankhe.

9 Pamenepo Yese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankhe.

10 Ndipo Yese anapititsapo ana ake aamuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa.

11 Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng’ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.

12 Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.

13 Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.

Davide atumikira Saulo

14 Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye.

15 Ndipo anyamata a Saulo ananena naye, Onani tsopano, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ulikuvuta inu.

16 Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wochokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzaimba ndi dzanja lake, ndipo mudzakhala wolama.

17 Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuimba bwino, nimubwere naye kwa ine.

18 Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.

19 Chifukwa chake Saulo anatumiza mithenga kwa Yese, nati, Unditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa.

20 Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake.

21 Ndipo Davide anafika kwa Saulo, naima pamaso pake; ndipo iye anamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zake.

22 Ndipo Saulo anatumiza kwa Yese, nati, Ulole kuti Davide aime pamaso panga; pakuti ndamkomera mtima.

23 Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/16-4baa67cf749f6a2df9e92c63b6123143.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 17

Davide apha Goliyati

1 Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.

2 Ndipo Saulo ndi anthu a Israele anasonkhana, namanga zithando pa chigwa cha Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.

3 Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa.

4 Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.

5 Ndipo anali ndi chisoti chamkuwa pamutu pake, navala malaya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa,

6 nakuta msongolo wake ndi chovala chamkuwa, ndiponso pachikota pake panali nthungo yamkuwa.

7 Ndipo mtengo wa mkondo wake unali ngati mtanda woombera nsalu; ndi mutu wa mkondowo unalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a chitsulo; ndipo womnyamulira chikopa anamtsogolera.

8 Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israele, nanena nao, Munatulukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Saulo? Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.

9 Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikamgonjetsa ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife.

10 Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.

11 Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.

12 Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m’masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.

13 Ndipo ana atatu aakulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama.

14 Ndipo Davide anali wotsiriza; ndi akulu atatuwo anamtsata Saulo.

15 Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu.

16 Ndipo Mfilistiyo anayandikira m’mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.

17 Ndipo Yese anati kwa Davide mwana wake, Uwatengere abale ako efa wa tirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;

18 nunyamule nchinchi izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa chikwi chao, nukaone m’mene akhalira abale ako, nulandire chikole chao.

19 Tsono Saulo, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israele, anali m’chigwa cha Ela, ku nkhondo ya Afilisti.

20 Ndipo Davide anauka m’mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula.

21 Ndipo Israele ndi Afilisti anandandalitsa nkhondo zao, khamu lina kuyang’anana ndi khamu lina.

22 Ndipo Davide anasiya akatundu ake m’dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake.

23 Ndipo m’mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.

24 Ndipo Aisraele onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri.

25 Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele.

26 Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?

27 Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamchitira munthu wakumupha iye mwakutimwakuti.

28 Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m’chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.

29 Ndipo Davide anati, Ndachitanji tsopano? Palibe chifukwa kodi?

30 Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo.

31 Ndipo pamene mau adanena Davide anamveka, anawapitiriza kwa Saulo; ndipo iye anamuitana.

32 Ndipo Davide anati kwa Saulo, Asade nkhawa munthu aliyense chifukwa cha iyeyo; ine kapolo wanu ndidzapita kuponyana ndi Mfilisti uyu.

33 Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake.

34 Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina chimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo,

35 ndinachithamangira, ndi kuchikantha, ndi kuitulutsa m’kamwa mwake; ndipo pamene chinandiukira, ndinagwira tchowa lake ndi kuchikantha ndi kuchipha.

36 Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.

37 Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m’dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.

38 Ndipo Saulo anaveka Davide zovala zake za iye yekha, namveka chisoti chamkuwa pamutu pake, namvekanso malaya aunyolo.

39 Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesere kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindingathe kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowere. Nazivula Davide.

40 Natenga ndodo yake m’dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m’thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m’dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.

41 Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula chikopa chake anamtsogolera.

42 Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.

43 Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake.

44 Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo.

45 Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.

46 Lero lino Yehova adzakupereka iwe m’dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.

47 Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo Iye adzakuperekani inu m’manja athu.

48 Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.

49 Ndipo Davide anapisa dzanja lake m’thumba mwake, natulutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m’mphumi, ndipo iye anagwa pansi chafufumimba.

50 Chomwecho Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m’dzanja la Davide munalibe lupanga.

51 Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m’chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa.

52 Ndipo anthu a Israele ndi Ayuda ananyamuka, nafuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka kufika kuchigwako, ndi ku zipata za Ekeroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa panjira ya ku Saaraimu, kufikira ku Gati ndi ku Ekeroni.

53 Ndipo ana a Israele atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m’zithando zao.

54 Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao kuYerusalemu; koma zida zake anazisunga m’hema wake.

55 Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.

56 Ndipo mfumu inati, Ufunsire kuti mnyamatayo ndi mwana wa yani.

57 Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m’dzanja lake.

58 Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/17-39ae287577a1349503594e76cbf705a1.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 18

Ubwenzi wa Davide ndi Yonatani

1 Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.

2 Ndipo Saulo anamtenga tsiku lomwelo, osamlolanso apite kwao kwa atate wake.

3 Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.

4 Ndipo Yonatani anavula malaya ake anali nao, napatsa Davide, ndi zovala zake, ngakhale lupanga lake, ndi uta wake, ndi lamba lake.

5 Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang’anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.

6 Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu aakazi anatuluka m’mizinda yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira.

7 Ndipo akazi anathirirana mang’ombe m’kuimba kwao, nati,

Saulo anapha zikwi zake,

koma Davide zikwi zake zankhani.

Saulo aipidwa ndi Davide

8 Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha?

9 Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m’tsogolo mwake, Saulo anakhala maso pa Davide.

10 Ndipo kunali m’mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m’nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m’dzanja la Saulo munali mkondo.

11 Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake.

12 Ndipo Saulo anaopa Davide chifukwa Yehova anali naye, koma adamchokera Saulo.

13 Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao.

14 Ndipo Davide anakhala wochenjera m’mayendedwe ake onse; ndipo Yehova anali naye.

15 Ndipo pamene Saulo anaona kuti analikukhala wochenjera ndithu anamuopa.

16 Koma Aisraele onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kutuluka ndi kulowa nao.

Davide mkamwini wa Saulo

17 Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.

18 Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani mu Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?

19 Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Saulo kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adriyele Mmehola kukhala mkazi wake.

20 Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anakonda Davide; ndipo pakumva Saulo, anakondwera nako.

21 Nati Saulo, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kachiwiri.

22 Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m’tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu.

23 Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m’makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.

24 Ndipo anyamata a Saulo anamuuza, kuti, Anatero Davide.

25 Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.

26 Ndipo pamene anyamata ake anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu.

27 Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.

28 Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide.

29 Saulo nayamba kumuopa Davide kopambana; ndi Saulo anali mdani wa Davide masiku onse.

30 Pomwepo mafumu a Afilisti anatuluka; ndipo nthawi zonse anatuluka iwo, Davide anali wochenjera koposa anyamata onse a Saulo, chomwecho dzina lake linatamidwa kwambiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/18-4d8023ff7be6fa1d31eb3f56cac89548.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 19

Yonatani anenera Davide kwa Saulo

1 Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.

2 Koma Yonatani mwana wa Saulo anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Yonatani anauza Davide, nati, Saulo atate wanga alikufuna kukupha; chifukwa chake tsono uchenjere m’mawa, mukhale m’malo mosadziwika, nubisale;

3 ndipo ine ndidzakutuluka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.

4 Ndipo Yonatani analankhula ndi Saulo atate wake movomereza Davide, nanena naye, Mfumu asachimwire mnyamata wake Davide; chifukwa iyeyo sanachimwire inu, ndipo ntchito zake anakuchitirani zinali zabwino ndithu;

5 popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?

6 Ndipo Saulo anamvera mau a Yonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye.

7 Pamenepo Yonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Yonatani anafika naye Davide kwa Saulo, iye nakhalanso pamaso pake monga kale.

Saulo afuna kupha Davide, Mikala ampulumutsa

8 Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anatuluka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe aakulu, ndipo iwo anamthawa iye.

9 Ndipo mzimu woipa wochokera kwa Yehova unali pa Saulo, pakukhala iye m’nyumba mwake, ndi mkondo wake m’dzanja lake; ndipo Davide anaimba ndi dzanja lake.

10 Ndipo Saulo anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kuchoka pamaso pa Saulo; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.

11 Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m’mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m’mawa.

12 Chomwecho Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.

13 Ndipo Mikala anatenga terafi namuika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda.

14 Ndipo pamene Saulo anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, Iye alikudwala.

15 Ndipo Saulo anatumiza mithengayo kuti ikaone Davide, nati, Mumtengere iye pa kama wake, kuti ndidzamuphe.

16 Ndipo pakulowa mithengayo, onani, pakama pali chifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake.

17 Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.

Saulo ndi amithenga ake anenera

18 Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti.

19 Ndipo wina anauza Saulo, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti mu Rama.

20 Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso.

21 Ndipo pamene anauza Saulo, iye anatumiza mithenga ina; koma iyonso inanenera. Ndipo Saulo anatumiza mithenga kachitatu, nayonso inanenera.

22 Pamenepo iyenso anamuka ku Rama, nafika ku chitsime chachikulu chili ku Seku, nafunsa nati, Samuele ndi Davide ali kuti? Ndipo wina anati, Taonani, ali ku Nayoti mu Rama.

23 Ndipo anapita komweko ku Nayoti mu Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti mu Rama.

24 Ndiponso anavula zovala zake, naneneranso pamaso pa Samuele, nagona wamaliseche usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Chifukwa chake amati, Kodi Saulonso ali pakati pa aneneri?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/19-8510294aa70509c7c38982666285fe13.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 20

Pangano pakati pa Davide ndi Yonatani

1 Ndipo Davide anathawa ku Nayoti mu Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga?

2 Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang’ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai.

3 Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.

4 Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Chilichonse mtima wako, unena ndidzakuchitira.

5 Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake.

6 Atate wako akandifuna pang’ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pachaka ya banja lao lonse.

7 Tsono akati, Chabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundichitira choipa.

8 Chifukwa chake uchitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamchititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli choipa chilichonse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?

9 Ndipo Yonatani anati, Iai ndi pang’ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukuchitira choipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?

10 Tsono Davide anati kwa Yonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa?

11 Nati Yonatani kwa Davide, Tiyeni timuke kuthengo. Namuka onse awiri kuthengoko.

12 Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi?

13 Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.

14 Ndipo undionetsere chifundo cha Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe;

15 komanso usaleke kuchitira chifundo a m’nyumba yanga nthawi zonse: mungakhale m’tsogolomo Yehova atathera adani onse a Davide padziko lapansi.

16 Chomwecho Yonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.

17 Ndipo Yonatani anamlumbiritsa Davide kachiwiri, chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.

18 Tsono Yonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.

19 Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mlandu uja, nukhale pamwala wa Ezeri.

20 Ndipo ine ndidzaponya mivi itatu pambali pake, monga ngati ndilikuponya pachandamali.

21 Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.

22 Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mivi ili kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke.

23 Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.

24 Chomwecho Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya.

25 Mfumu nikhala pa mpando wake, monga ankachita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Yonatani anaimirira, ndi Abinere anakhala pa mbali ya Saulo; koma Davide anasoweka pamalo pake.

26 Koma Saulo sananene kanthu tsiku lomwelo; chifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.

27 Ndipo kunali tsiku lachiwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pake; ndipo Saulo anati kwa Yonatani mwana wake, Mwana wa Yese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?

28 Ndipo Yonatani anayankha Saulo, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu;

29 nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m’mzindamo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu.

Saulo aipidwa ndi Yonatani

30 Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?

31 Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.

32 Ndipo Yonatani anayankha Saulo atate wake, nanena, Aphedwe chifukwa ninji? Anachitanji?

33 Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide.

34 Pamenepo Yonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku lachiwiri la mwezi, pakuti mtima wake unali ndi chisoni chifukwa cha Davide, popeza atate wake anamchititsa manyazi.

Davide ndi Yonatani alekana

35 Ndipo m’mawa, Yonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnyamata.

36 Ndipo anauza mnyamata wakeyo, Thamanga uzikatola mivi imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya muvi kuutumphitsa iye.

37 Ndipo mnyamatayo atafika pamalo a muvi umene Yonatani anauponya, Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Muviwo suli m’tsogolo mwako kodi?

38 Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake.

39 Koma mnyamatayo sanadziwe kanthu; Davide ndi Yonatani okha anadziwa za mlanduwo.

40 Ndipo Yonatani anapatsa mnyamata wake zida zake, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumzinda.

41 Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.

42 Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m’dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/20-80ca1657173ef1072f1124bdffcd6f26.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 21

Davide athawira kwa wansembe Ahimeleki ku Nobu

1 Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?

2 Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.

3 Chifukwa chake tsono muli ndi chiyani? Mundipatse m’dzanja langa mikate isanu, kapena chilichonse muli nacho.

4 Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndilibe mkate wachabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.

5 Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; chichokere ine, zotengera za anyamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wachabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?

6 Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo.

7 Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.

8 Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m’dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? Chifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mlandu wa mfumu ukuti ndifulumire.

9 Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m’chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m’nsalu, kumbuyo kwaefodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.

Davide athawira kwa Akisi

10 Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo chifukwa cha kuopa Saulo, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati.

11 Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang’ombe za iye kodi m’magule ao, ndi kuti,

Saulo anapha zikwi zake,

koma Davide zikwi zake zankhani?

12 Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.

13 Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m’manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.

14 Tsono Akisi ananena ndi anyamata ake, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji?

15 Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m’nyumba mwanga?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/21-63e01a6fa1d08cafb69490e7eba77ca7.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 22

Davide apulumukira ku phanga la Adulamu

1 Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.

2 Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.

3 Ndipo Davide anachoka kumeneko kunka Mizipa wa ku Mowabu; nati kwa mfumu ya Mowabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga atuluke nakhale nanu, kufikira ndidziwa chimene Mulungu adzandichitira.

4 Ndipo anawatenga kunka nao pamaso pa mfumu ya Mowabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo.

5 NdipomneneriGadi anati kwa Davide, Musamakhala m’lingamo; chokani, mulowe m’dziko la Yuda. Potero Davide anachokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.

Saulo aphetsa ansembe ndi onse ena a ku Nobu

6 Pakumva Saulo kuti anadziwika Davide, ndi anthu ake akukhala naye, Saulo analikukhala mu Gibea, patsinde pa mtengo wa bwemba, m’dzanja lake munali mkondo wake, ndi anyamata ake onse anaimirira pali iye.

7 Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yampesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;

8 kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?

9 Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Saulo, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Yeseyo alikufika ku Nobu, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi.

10 Ndipo iye anamfunsira kwa Yehova, nampatsa chakudya, nampatsanso lupanga la Goliyati Mfilistiyo.

11 Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubi, ndi banja lonse la atate wake, ansembe a ku Nobu; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.

12 Ndipo Saulo anati, Imva tsopano iwe mwana wa Ahitubi. Nayankha iye, Ndine, mbuye wanga.

13 Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?

14 Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m’nyumba mwanu?

15 Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang’ono ponse.

16 Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako.

17 Mfumu niuza asilikali akuima chomzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; chifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululire. Koma anyamata a mfumu sanafune kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.

18 Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvalaefodiwabafuta.

19 Ndipo anakantha Nobu ndiwo mzinda wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng’ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.

Apulumuka Abiyatara

20 Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake ndiye Abiyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide.

21 Ndipo Abiyatara anadziwitsa Davide kuti Saulo anapha ansembe a Yehova.

22 Ndipo Davide anati kwa Abiyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Saulo; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako.

23 Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/22-5568db2f055c8ef03acf0441a85c4979.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 23

Davide alanditsa a ku Keila

1 Tsono anauza Davide, kuti, Onani Afilisti alikuponyana ndi Keila, nafunkha za m’madwale.

2 Chifukwa chake Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila.

3 Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Taonani, ife tikhalira m’mantha ku Yuda kuno; koposa kotani nanga tikafika ku Keila kuponyana ndi makamu a nkhondo a Afilisti.

4 Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m’dzanja lako.

5 Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng’ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala mu Keila.

6 Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndiefodim’dzanja lake.

7 Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m’dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m’mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.

8 Ndipo Saulo anamemeza anthu onse kunkhondo, kuti atsikire ku Keila, kumangira misasa Davide ndi anthu ake.

9 Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.

10 Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, mnyamata wanu wamva zoona kuti Saulo afuna kudza ku Keila, kuononga mzindawo chifukwa cha ine.

11 Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m’dzanja lake? Kodi Saulo adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israele, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika.

12 Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m’dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.

13 Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.

Davide ndi Yonatani abwereza kupangana

14 Ndipo Davide anakhala m’chipululu m’ngaka, nakhala m’dziko la mapiri m’chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereke m’dzanja lake.

15 Ndipo Davide anaona kuti Saulo adatuluka kudzafuna moyo wake; Davide nakhala m’chipululu cha Zifi m’nkhalango ku Horesi.

16 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu.

17 Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa.

18 Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake.

19 Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m’ngaka za m’nkhalango ku Horesi, m’phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?

20 Chifukwa chake mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m’mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m’dzanja la mfumu.

21 Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo.

22 Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m’mene akhalitsa, ndi amene adamuona m’menemo; chifukwa anandiuza kuti iye achita mochenjera ndithu.

23 Chifukwa chake yang’anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m’dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.

24 Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Saulo; koma Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, m’chigwa cha kumwera kwa chipululu.

25 Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m’chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m’chipululu cha Maoni.

26 Ndipo Saulo anamuka mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake kuseri kwake; ndipo Davide anafulumira kuthawa, chifukwa cha kuopa Saulo; popeza Saulo ndi anthu ake anazinga Davide ndi anthu ake kwete kuti awagwire.

27 Koma mthenga unafika kwa Saulo ndi kuti, Mufulumire kubwerera; popeza nkhondo yovumbulukira ya Afilisti yalowa m’dziko.

28 Chomwecho Saulo anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; chifukwa chake anatchula dzina lake la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.

29 Ndipo Davide anakwera kuchokera kumeneko, nakhala m’ngaka za Engedi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/23-4447fd46cc1dd3daf68d93bc099963b6.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 24

Davide aleka Saulo osamupha

1 Ndipo kunali, pakubwerera Saulo potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku chipululu cha Engedi.

2 Tsono Saulo anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisraele onse, namuka, kukafuna Davide ndi anthu ake m’matanthwe a zinkhoma.

3 Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m’kati mwa phangamo.

4 Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m’dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.

5 Ndipo kunali m’tsogolo mwake kuti mtima wa Davide unamtsutsa chifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo.

6 Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.

7 Chomwecho Davide analetsa anyamata ake ndi mau awa, osawaloleza kuukira Saulo. Ndipo Saulo ananyamuka, natuluka m’phangamo, namuka njira yake.

8 Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m’phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.

9 Davide nanena ndi Saulo, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukuchitirani choipa.

10 Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m’dzanja langa m’phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.

11 Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m’dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m’dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.

12 Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera chilango kwa inu.

13 Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Uchimo utulukira mwa ochimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.

14 Nanga mfumu ya Israele inatulukira yani; inu mulikupirikitsa yani? Galu wakufa, kapena nsabwe.

15 Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang’anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m’dzanja lanu.

16 Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi.

17 Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.

18 Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m’dzanja lako.

19 Pakuti munthu akapeza mdani wake, adzamleka kodi kuti achoke bwino? Chifukwa chake Yehova akubwezere zabwino pa ichi unandichitira ine lero lomwe.

20 Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m’dzanja lako.

21 Chifukwa chake tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m’nyumba ya atate wanga.

22 Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/24-792cf5bc848ebeda165c0744188e9f4e.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 25

Amwalira Samuele

1 Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m’nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.

Za Davide, Nabala ndi Abigaile

2 Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele.

3 Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.

4 Ndipo Davide anamva kuchipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zake.

5 Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo, Mukwere ku Karimele, mumuke kwa Nabala ndi kundiperekera moni;

6 ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.

7 Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititse manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele.

8 Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; chifukwa chake muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tilikufika tsiku labwino; mupatse chilichonse muli nacho m’dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.

9 Ndipo pakufika anyamata a Davide, analankhula ndi Nabala monga mau aja onse m’dzina la Davide, naleka.

10 Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Masiku ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.

11 Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira?

12 Chomwecho anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa.

13 Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.

14 Koma mnyamata wina anauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akuchokera kuchipululu kulonjera mbuye wathu; koma iye anawakalipira.

15 Koma anthu aja anatichitira zabwino ndithu, sanatichititse manyazi, ndi panalibe kanthu kadatisowa, nthawi zonse tinali kuyenderana nao kubusa kuja;

16 iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo.

17 Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.

18 Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zowotchaotcha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu.

19 Nati kwa anyamata ake, Nditsogolereni; onani ndidza m’mbuyo mwanu. Koma sanauze mwamuna wake Nabala.

20 Ndipo kudatero pakuberekeka iye pabulu wake, natsikira pamalo obisika a m’phirilo, onani, Davide ndi anthu ake analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao.

21 Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m’chipululu, sikadasowe kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m’malo mwa zabwino.

22 Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m’mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo.

23 Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pabulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira,

24 Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m’makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.

25 Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaone anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza.

26 Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.

27 Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.

28 Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse.

29 Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m’phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m’choponyera mwala.

30 Ndipo kudzali, pamene Yehova anachitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israele;

31 mudzakhala opanda chakudodoma nacho, kapena chakusauka nacho mtima wa mbuye wanga, chakuti munakhetsa mwazi wopanda chifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera chilango ndipo Yehova akadzachitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukire mdzakazi wanu.

32 Ndipo Davide anati kwa Abigaile, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine;

33 ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera chilango ndi dzanja la ine ndekha.

34 Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi.

35 Chomwecho Davide analandira m’dzanja lake zimene iye anamtengera; nanena naye, Ukwere kwanu mumtendere; ona, ndamvera mau ako, ndavomereza nkhope yako.

36 Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m’nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m’kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m’mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.

37 Tsono m’mawa vinyo atamchokera Nabala, mkazi wake anamuuza zimenezi; ndipo mtima wake unamyuka m’kati mwake, iye nasanduka ngati mwala.

38 Ndipo kunali, atapita masiku khumi, Yehova anamkantha Nabala, nafa.

39 Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.

40 Ndipo anyamata a Davide pakufika kwa Abigaile ku Karimele, analankhula naye, nati, Davide anatitumiza kwa inu, kukutengani, mukhale mkazi wake.

41 Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yake pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.

42 Ndipo Abigaile anafulumira nanyamuka, nakwera pabulu, pamodzi ndi anamwali ake asanu akumtsata; natsatira mithenga ya Davide, nakhala mkazi wake.

43 Davide anatenganso Ahinowamu wa ku Yezireele, ndipo onse awiri anakhala akazi ake.

44 Pakuti Saulo anapatsa Mikala, mwana wake, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi, wa ku Galimu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/25-d381c6f0904c481d264163e4bd4aa933.mp3?version_id=1068—