Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 6

Afilisti abweza likasa ku dziko la Aisraele

1 Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.

2 Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake.

3 Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israele, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yopalamula, mukatero mudzachiritsidwa, ndi kudziwa chifukwa chake dzanja lake lili pa inu losachoka.

4 Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.

5 Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.

6 Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndiFaraoanaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?

7 Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng’ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng’ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;

8 ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m’bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke.

9 Ndipo muyang’anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.

10 Ndipo anthuwo anatero; natenga ng’ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagaleta, natsekera anao kwao;

11 naika likasa la Yehova pagaletapo, ndi bokosi m’mene munali mbewa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao.

12 Ndipo ng’ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, zinali kuyenda mumseu, zilikulira; sizinapatukire ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi.

13 Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m’chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona.

14 Ndipo galetalo linafika m’munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pamwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng’ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.

15 Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m’mene munali zokometsera zagolide, naziika pamwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.

16 Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekeroni tsiku lomwelo.

17 Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolide amene Afilisti anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yopalamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekeroni limodzi;

18 ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, mizinda ya malinga, ndi midzi yopanda malinga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m’munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.

19 Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m’likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.

Likasa lisungidwa ku Kiriyati-Yearimu

20 Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife?

21 Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/6-9ca9e6ba1aaac566a6452163c956e7f0.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 7

1 Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m’nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.

Afilisti akanthidwa ku Mizipa

2 Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu mu Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.

3 Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndiAsitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m’manja a Afilisti.

4 Pomwepo ana a Israele anachotsa Abaalandi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.

5 Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.

6 Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele mu Mizipa.

7 Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisraele anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele pakumva ichi, anachita mantha ndi Afilistiwo.

8 Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m’manja a Afilistiwo.

9 Ndipo Samuele anatengamwanawankhosawoyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza.

10 Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.

11 Ndipo Aisraele anatuluka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betekara.

12 Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.

13 Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele.

14 Ndipo mizinda ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa midzi yao m’manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere;

15 ndipo Samuele anaweruza Israele masiku onse a moyo wake.

16 Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m’malo onse amenewa.

17 Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/7-a0cd6d3c24ae536611a2a58c4d542716.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 8

Aisraele akhumba mfumu

1 Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake aamuna akhale oweruza a Israele.

2 Dzina la mwana wake woyamba ndiye Yowele, ndi dzina la wachiwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba.

3 Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.

4 Pamenepo akulu onse a Israele anasonkhana, nadza kwa Samuele ku Rama;

5 nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo muchitidwa m’mitundu yonse ya anthu.

6 Koma chimenechi sichinakondweretse Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.

7 Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.

8 Monga ntchito zao zonse anazichita kuyambira tsiku lija ndinawatulutsa ku Ejipito, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu ina, momwemo alikutero ndi iwenso.

9 Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.

10 Ndipo Samuele anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova.

11 Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu aamuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;

12 idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.

13 Ndipo idzatenga ana anu aakazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate.

14 Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mpesa yanu, ndi minda yaazitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake.

15 Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yampesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake.

16 Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake.

17 Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapolo ake.

18 Ndipo tsiku lija mudzafuula chifukwa cha mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo.

19 Koma anthu anakana kumvera mau a Samuele; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu;

20 kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kutuluka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu.

21 Ndipo Samuele anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m’makutu a Yehova.

22 Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumzinda wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/8-ba15a571f84f2990e673f761ffe7ad5f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 9

Saulo afuna abulu olowerera a atate wake

1 Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.

2 Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m’chifuwa.

3 Ndipo abulu a Kisi, atate wa Saulo, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Saulo mwana wake, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna abuluwo.

4 Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.

5 Pamene anafika ku dziko la Zufu, Saulo anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira abuluwo, ndi kutenga nkhawa chifukwa cha ife.

6 Koma ananena naye, Onatu, m’mzinda muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.

7 Ndipo Saulo ananena ndi mnyamata wake, Koma taona, tikapitako timtengere chiyani munthuyo? Popeza mkate udatha m’zotengera zathu, ndiponso tilibe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tili nacho chiyani?

8 Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Saulo nati, Onani m’dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wasiliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.

9 Kale mu Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwamnenerimakono ano, anatchedwa mlauli kale.

10 Pamenepo Saulo anati kwa mnyamata wake, Wanena bwino; tiye tipite. Chomwecho iwowa anapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulunguyo.

11 Pakukwera kumzindako anapeza anthu aakazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?

12 Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m’tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumzinda kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;

13 mutafika m’mzinda, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi ino mudzampeza.

14 Ndipo iwowa anakwera kumzinda; ndipo m’mene analowa m’mzindamo, onani, Samuele anatulukira pali iwo, kuti akakwere kumsanje.

Saulo akomana ndi Samuele

15 Ndipo Yehova anaululiratu m’khutu la Samuele dzulo lake la tsiku limene Saulo anabwera, kuti,

16 Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m’manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

17 Ndipo pamene Samuele anaona Saulo, Yehova anati kwa iye, Ona munthu amene ndinakuuza za iye! Ameneyu adzaweruza anthu anga.

18 Pomwepo Saulo anayandikira kwa Samuele pakati pa chipata, nati, Mundidziwitse nyumba ya mlauliyo ili kuti.

19 Ndipo Samuele anayankha Saulo nati, Ine ndine mlauliyo. Kwera, batsogola kumsanje, pakuti mudzadya ndi ine lero; ndipo m’mawa ndidzakulola upite, ndi kukudziwitsa zonse zili mumtima mwako.

20 Za abulu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo chifuniro chonse cha Israele chili kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako?

21 Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling’ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?

22 Ndipo Samuele anatenga Saulo ndi mnyamata wake, napita nao ku chipinda cha alendo, nawakhalitsa pamalo a ulemu pakati pa oitanidwa onse; ndiwo anthu monga makumi atatu.

23 Ndipo Samuele ananena ndi wophika, Tenga nyama ndinakupatsa, ndi kuti, Ibakhala ndi iwe.

24 Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija.

25 Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumzinda, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.

26 Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja.

27 Ndipo pamene analikutsika polekeza mzinda, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/9-156a4f04714f79d136328efe3c001e4e.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 10

Samuele adzoza Saulo akhale mfumu ya Israele

1 Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?

2 M’mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezeka; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga?

3 Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.

4 Iwowa adzakupatsani moni, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m’manja mwao.

5 Ndipo m’tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumzindako mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;

6 ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.

7 Ndipo zitakufikirani zizindikiro izi mudzachita monga mudzaona pochita, pakuti Mulungu ali nanu.

8 Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.

9 Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samuele, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikiro zija zonse zinachitika tsiku lija.

Saulo pakati pa aneneri

10 Ndipo pamene anafika ku Gibea, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao.

11 Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri?

12 Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Chifukwa chake mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulonso ali mwa aneneri?

13 Ndipo pamene adatha kunenera anafika kumsanjeko.

14 Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeze, tinadza kwa Samuele.

15 Ndipo mbale wa atate wa Saulo anati, Undiuze chimene Samuele analankhula nawe.

16 Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo.

Anthu avomereza Saulo akhale mfumu yao

17 Ndipo Samuele anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;

18 nanena ndi ana a Israele, Atero Yehova, Mulungu wa Israele kuti, Ine ndinatulutsa Israele mu Ejipito, ndipo ndinakupulumutsani m’manja a Aejipito, ndi m’manja a maufumu onse anakusautsani;

19 koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m’matsoka anu onse, ndi m’masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.

20 Chomwecho Samuele anayandikizitsa mafuko onse a Israele, ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa.

21 Nayandikizitsa fuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; ndipo anayandikizitsa banja la Amatiri, mmodzimmodzi; nasankhidwa Saulo mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.

22 Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.

23 Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa ndipo anthu onse anamlekeza m’chifuwa.

24 Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.

25 Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m’buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake.

26 Ndi Saulo yemwe anamuka kunyumba yake ku Gibea; ndipo am’khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao.

27 Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/10-95a6ee37567a676ffa0759069c658c2d.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 11

Saulo alanditsa Yabesi-Giliyadi m’manja mwa Aamoni

1 Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupanganechipanganondi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.

2 Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse.

3 Ndipo akulu a ku Yabesi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m’malire onse a Israele; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzatulukira kwa inu.

4 Tsono mithengayo inafika ku Gibea kwa Saulo, nalankhula mau amenewa m’makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.

5 Ndipo, onani, Saulo anachokera kumunda alikutsata ng’ombe; nati Saulo, Choliritsa anthu misozi nchiyani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabesi.

6 Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Saulo mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wake unayaka kwambiri.

7 Natenga ng’ombe ziwiri nazidula nthulinthuli, nazitumiza m’malire monse mwa Israele, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Saulo ndi pa Samuele, adzatero nazo ng’ombe zake. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, natuluka ngati munthu mmodzi.

8 Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israele anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu.

9 Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa.

10 Chifukwa chake anthu a ku Yabesi anati, Mawa tidzatulukira kwa inu, ndipo mudzatichitira chokomera inu.

11 Ndipo m’mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.

12 Ndipo anthu anati kwa Samuele, Ndani iye amene anati, Kodi Saulo adzatiweruza ife? Tengani anthuwo kuti tiwaphe.

13 Koma Saulo anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso mu Israele.

14 Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko.

15 Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova mu Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/11-016196b2669147218b10b5547fd4b6c5.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 12

Samuele adzinenera kwa anthu

1 Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.

2 Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga aamuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.

3 Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng’ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m’manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.

4 Ndipo iwo anati, Simunatinyenge, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m’manja mwa wina aliyense.

5 Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wake ali mboni lero kuti simunapeze kanthu m’dzanja langa. Nati iwo, Iye ali mboni.

6 Ndipo Samuele ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, natulutsanso makolo anu m’dziko la Ejipito.

7 Chifukwa chake tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova, za ntchito zonse zolungama za Yehova anakuchitirani inu ndi makolo anu.

8 Pamene Yakobo anafika ku Ejipito, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anatulutsa makolo anu mu Ejipito, nawakhalitsa pamalo pano.

9 Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, Iye nawapereka m’dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m’dzanja la Afilisti, ndi m’dzanja la mfumu ya Mowabu, iwo naponyana nao.

10 Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira AbaalandiAsitaroti, koma mutipulumutse tsopano m’manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.

11 Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m’manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.

12 Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu.

13 Chifukwa chake siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.

14 Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ake, ndi kusakana lamulo lake la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, chabwino.

15 Koma mukapanda kumvera mau a Yehova, ndi kupikisana ndi lamulo la Yehova, dzanja la Yehova lidzatsutsana nanu, monga linatsutsana ndi makolo anu.

16 Chifukwa chake tsono, imani pano, muone chinthu ichi chachikulu Yehova adzachichita pamaso panu.

17 Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.

18 Momwemo Samuele anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samuele.

19 Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu.

20 Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Musaope; munachitadi choipa ichi chonse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;

21 musapatukire inu kutsata zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza zili zopanda pake.

22 Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.

23 Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.

24 Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuluzo Iye anakuchitirani.

25 Koma mukaumirirabe kuchita choipa, mudzaonongeka, inu ndi mfumu yanu yomwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/12-b3e8f6e0e4b7239e9e4ff4a98fa1e8db.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 13

Nkhondo pakati pa Israele ndi Afilisti

1 Saulo anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wake; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.

2 Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.

3 Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m’dziko monse, nati, Amve Ahebri.

4 Ndipo Aisraele onse anamva kunena kuti Saulo anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisraele. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Saulo ku Giligala.

5 Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum’mawa kwa Betaveni.

6 Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m’kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m’mapanga, ndi m’nkhalango, ndi m’matanthwe, ndi m’malinga, ndi m’maenje.

7 Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordani nafika ku dziko la Gadi ndi Giliyadi; koma Saulo akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.

Samuele adzudzula Saulo pa kupereka iye nsembe

8 Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samuele; koma Samuele sanafike ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Saulo.

9 Pamenepo Saulo anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.

10 Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samuele anafika. Ndipo Saulo anamchingamira kukamlonjera iye.

11 Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafike masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;

12 chifukwa chake ndinati, Afilisti adzatitsikira pano pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.

13 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Munachita kopusa; simunasunge lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene Iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi ino ufumu wanu, ukhale pa Israele nthawi yosatha.

14 Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunge chimene Yehova anakulamulirani.

15 Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi.

16 Ndipo Saulo, ndi Yonatani mwana wake, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.

17 Ndipo owawanya anatuluka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofura, ku dera la Suwala;

18 gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang’ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko.

19 Ndipo m’dziko lonse la Israele simunapezeke wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisraele angadzisulire malupanga kapena mikondo;

20 koma Aisraele onse ankatsikira kwa Afilisti, kuti awasanjire munthu yense chikhasu chake, cholimira chake, nkhwangwa yake, ndi chisenga chake;

21 ndipo mtengo wakukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mano unali masekeli awiri mwa atatu ndi mtengo wa nkhwangwazo; ndi kusongola zotwikira unali sekeli imodzi mwa atatu.

22 Chomwecho kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeke mkondo kapena lupanga m’manja a anthu onse anali ndi Saulo ndi Yonatani; koma Saulo yekha ndi Yonatani mwana wake anali nazo.

23 Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anatuluka kunja ku mpata wa ku Mikimasi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/13-10899f1ff6fc5ded85d5d61b9af849a9.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 14

Yonatani agonjetsa Afilisti

1 Ndipo kunali tsiku lina kuti Yonatani mwana wa Saulo ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauze atate wake.

2 Ndipo Saulo analikukhala m’matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;

3 ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovalaefodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.

4 Ndipo pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali ina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzake; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzake ndilo Sene.

5 Phiri lija linaimirira kuyang’ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzake kumwera pandunji pa Geba.

6 Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.

7 Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.

8 Ndipo Yonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziwulula kwa iwo.

9 Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m’malo mwathu, osakwera kwa iwo.

10 Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m’manja mwathu; ndipo ichi chidzatikhalira chizindikiro.

11 Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m’mauna m’mene anabisala.

12 Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m’mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m’dzanja la Israele.

13 Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake.

14 Kuwapha koyambako, Yonatani ndi wonyamula zida zake, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng’ombe ziwiri tsiku limodzi.

15 Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.

16 Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang’ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.

Saulo alumbirira anthu

17 Pamenepo Saulo ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anatichokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Yonatani ndi wonyamula zida zake panalibe.

18 Ndipo Saulo ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israele.

19 Ndipo kunali m’mene Saulo anali chilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m’chigono cha Afilisti linachitikabe, nilikula; ndipo Saulo ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako.

20 Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu.

21 Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anatuluka m’dziko lozungulira kukalowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisraele amene anali ndi Saulo ndi Yonatani.

22 Anateronso Aisraele onse akubisala m’phiri la Efuremu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapirikitsa kolimba kunkhondoko.

23 Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.

24 Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.

25 Ndipo anthu onsewo analowa munkhalango, panali uchi pansi.

26 Ndipo pakufika anthuwo m’nkhalangomo, onani, madzi a uchi anachuluka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lake pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.

27 Koma Yonatani sanamve m’mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m’dzanja lake, naitosa m’chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m’maso mwake munayera.

28 Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema.

29 Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m’maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang’ono uchiwu.

30 Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? Popeza tsopano palibe kuwapha kwakukulu kwa Afilisti.

31 Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri.

32 Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng’ombe, ndi anaang’ombe, naziphera pansi; anthu nazidya zili ndi mwazi wao.

33 Pamenepo anauza Saulo, kuti, Onani anthu alikuchimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munachita konyenga; kunkhunizani mwala waukulu kwa ine lero.

34 Ndipo Saulo anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng’ombe yake, ndi munthu yense ndi nkhosa yake, aziphe pano, ndi kuzidya, osachimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng’ombe yake, usiku uja naziphera pomwepo.

35 Ndipo Saulo anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.

Yonatani atsutsidwa afe

36 Ndipo Saulo anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Chitani chilichonse chikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Mulungu kuno.

37 Ndipo Saulo anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m’dzanja la Israele kodi? Koma Iye sanamyankhe tsiku lomweli.

38 Ndipo Saulo anati, Musendere kuno, inu nonse akulu a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m’mene muli choipa ichi lero.

39 Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m’mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.

40 Ndipo iye ananena ndi Aisraele onse, Inu mukhale mbali ina, ndipo ine ndi Yonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, Chitani chimene chikukomerani.

41 Chifukwa chake Saulo ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israele, muonetse choonadi. Ndipo maere anagwera Saulo ndi Yonatani; koma anthuwo anapulumuka.

42 Ndipo Saulo anati, Muchite maere pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga. Ndipo anagwera Yonatani.

43 Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang’ono ndi nsonga ya ndodo inali m’dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.

44 Pamenepo Saulo anati, Mulungu andilange, naonjezereko, pakuti udzafa ndithu, Yonatani.

Anthu alanditsa Yonatani

45 Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi mu Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pamutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe.

46 Ndipo Saulo analeka kuwapirikitsa Afilistiwo; ndi Afilistiwo anamuka ku malo a iwo okha.

47 Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga.

48 Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m’manja a akuwawawanya.

49 Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng’ono wake ndiye Mikala;

50 ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.

51 Ndipo atate wa Saulo ndiye Kisi; ndipo Nere atate wa Abinere ndiye mwana wa Abiyele.

52 Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/14-413e02b2fb659cf6dbe15cf29c081abc.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 15

Saulo alamulidwa aononge Amaleke

1 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ake Aisraele; chifukwa chake tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova.

2 Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m’mene iye anakwera kutuluka mu Ejipito.

3 Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng’ombe ndi nkhosa,ngamirandi bulu.

4 Ndipo Saulo anamemeza anthu, nawawerenga ku Telaimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.

5 Ndipo Saulo anafika kumzinda wa Amaleke, nalalira kuchigwa.

6 Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.

7 Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito.

8 Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.

9 Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng’ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafune kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse.

Samuele adzudzula Saulo pa kusamvera kwake

10 Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samuele, nati,

11 Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.

12 Ndipo Samuele analawirira m’mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.

13 Ndipo Samuele anadza kwa Saulo; ndipo Saulo anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova.

14 Ndipo Samuele anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndilikumva m’makutu anga, ndi kulirako kwa ng’ombe ndilikumva, nchiyani?

15 Ndipo Saulo anati, Anazitenga kwa Aamaleke; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng’ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konsekonse.

16 Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

17 Nati Samuele, M’mene munali wamng’ono m’maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.

18 Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konsekonse Aamaleke akuchita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.

19 Chifukwa ninji tsono simunamvere mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova?

20 Ndipo Saulo ananena ndi Samuele, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleke, ndi Aamaleke ndinawaononga konsekonse.

21 Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng’ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.

22 Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.

23 Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

24 Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.

25 Chifukwa chake tsono, mukhululukire tchimo langa, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova.

26 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israele.

27 Ndipo pakupotoloka Samuele kuti achoke, iye anagwira chilezi cha mwinjiro wake, ndipo chinang’ambika.

28 Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang’amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.

29 Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.

30 Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.

31 Chomwecho Samuele anabwerera natsata Saulo; ndi Saulo analambira Yehova.

32 Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.

33 Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.

34 Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo.

35 Ndipo Samuele sanadzenso kudzaona Saulo kufikira tsiku la imfa yake; koma Samuele analira chifukwa cha Saulo; ndipo Yehova anali ndi chisoni kuti anamlonga Saulo mfumu ya Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/15-11f48f1ca6cd8d83a51e6798fd489228.mp3?version_id=1068—