Categories
RUTE

RUTE 1

Naomi ndi apongozi ake awiri

1 Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m’dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu ku Yuda anamuka nakagonera m’dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake aamuna awiri.

2 Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m’dziko la Mowabu, nakhala komweko.

3 Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri.

4 Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.

5 Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake aamuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo.

6 Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m’dziko la Mowabu; pakuti adamva m’dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.

7 Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; nanka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda.

8 Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.

9 Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m’nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.

10 Ndipo ananena naye, Iai, koma tidzapita nanu kwa anthu a kwanu.

11 Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m’mimba mwanga ana aamuna ena kuti akhale amuna anu?

12 Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindingathe kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana aamuna;

13 kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira.

14 Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Oripa anampsompsona mpongozi wake, koma Rute anamkangamira.

15 Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wake, bwerera umtsate mbale wako.

16 Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;

17 kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.

18 Ndipo pakuona kuti analimbika kumuka naye, analeka kulankhula naye.

19 Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?

20 Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.

21 Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa?

22 Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/1-6ea412b45d6cf5ccf1075e8415460ded.mp3?version_id=1068—

Categories
RUTE

RUTE 2

Rute akunkha m’munda wa Bowazi

1 Ndipo Naomi anali naye mbale wa mwamuna wake, ndiye munthu mwini chuma chambiri wa banja la Elimeleki; dzina lake ndiye Bowazi.

2 Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.

3 Namuka iye, nakatola khunkha m’munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.

4 Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.

5 Nati Bowazi kwa mnyamata woyang’anira ochekawo, Mkazi uyu ngwa yani?

6 Ndipo mnyamata woyang’anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu;

7 ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m’mawa mpaka tsopano; koma m’nyumba samakhalitsamo.

8 Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m’munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.

9 Maso ako akhale pamunda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauze anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,

10 Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?

11 Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.

12 Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.

13 Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.

14 Ndipo pa nthawi ya kudya Bowazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m’vinyo wosasayo. Nakhala iye m’mbali mwa ochekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.

15 Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Bowazi analamulira anyamata ake ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamchititse manyazi.

16 Ndiponso mumtayire za m’manja, ndi kuzisiya, natole khunkha, osamdzudzula.

17 Natola khunkha iye m’munda mpaka madzulo; naomba khunkhalo; napeza ngati efa wa barele,

18 nalisenza nalowa kumzinda; ndipo mpongozi wake anaona khunkhalo; Rute natulutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta.

19 Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi.

20 Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.

21 Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m’minda.

22 Nati Naomi kwa Rute mpongozi wake, Nchabwino, mwana wanga, kuti uzituluka nao adzakazi ake, ndi kuti asakukomane m’munda wina uliwonse.

23 Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/2-73a3f0dd9226b7c545ff303860ec9440.mp3?version_id=1068—

Categories
RUTE

RUTE 3

Bowazi anena za kumuombolera Rute cholowa

1 Pamenepo Naomi mpongozi wake ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?

2 Nanga Bowazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ake? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.

3 Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.

4 Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nuvundukule ku mapazi ake, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kuchita iwe.

5 Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzachita.

6 Pamenepo anatsikira popunthirapo, nachita zonse monga umo mpongozi wake adamuuza.

7 Ndipo atatha Bowazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wake, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kachetechete, navundukula ku mapazi ake, nagona.

8 Ndipo kunali, pakati pa usiku munthuyo anadzidzimuka, natembenuka; ndipo taona pa mapazi ake pagona mkazi.

9 Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mufunde mdzakazi wanu chofunda chanu, pakuti inu ndinu wondiombolera cholowa.

10 Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsate anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.

11 Ndipo tsopano, mwana wanga, usaope; ndidzakuchitira zonse unenazi; pakuti onse a pa mudzi wa anthu a mtundu wanga adziwa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.

12 Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera cholowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.

13 Gona usiku uno, ndipo kudzali m’mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m’mawa.

14 Nagona ku mapazi ake mpaka m’mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo.

15 Ndipo anati, Bwera nacho chofunda chako, nuchigwire; nachigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m’mzinda.

16 Ndipo pamene anadza kwa mpongozi wake, iye anati, Wapeza bwanji, mwana wanga? Pamenepo anamfotokozera zonse anamchitira munthuyo.

17 Natinso, Miyeso iyi isanu ndi umodzi ya barele anandipatsa, pakuti anati, Usafike kwa mpongozi wako wopanda kanthu.

18 Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga, mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/3-3b6f17c0d7b2c929f8b5357fd28c0a89.mp3?version_id=1068—

Categories
RUTE

RUTE 4

Bowazi akwatira Rute nabadwa Obedi

1 Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi.

2 Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mzinda, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo.

3 Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Mowabu ati agulitse kadziko kaja kadali ka mbale wathu Elimeleki;

4 ndipo ndati ndikuululira ichi, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola.

5 Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo padzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake.

6 Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

7 Koma kale mu Israele pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu avula nsapato yake, naipereka kwa mnansi wake; ndiwo matsimikizidwe mu Israele.

8 Ndipo woombolayo anati kwa Bowazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Navula nsapato yake.

9 Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, padzanja la Naomi.

10 Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.

11 Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m’nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;

12 ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.

13 Momwemo Bowazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wake; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna.

14 Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sanalole kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lake mu Israele.

15 Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana aamuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.

16 Ndipo Naomi anamtenga mwanayo, namuika pachifuwa pake, nakhala mlezi wake.

17 Ndi akazi anansi ake anamutcha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namutcha dzina lake Obedi; ndiye atate wa Yese atate wa Davide.

18 Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi;

19 ndi Hezironi anabala Ramu, ndi Ramu anabala Aminadabu;

20 ndi Aminadabu anabala Nasoni, ndi Nasoni anabala Salimoni;

21 ndi Salimoni anabala Bowazi, ndi Bowazi anabala Obedi;

22 ndi Obedi anabala Yese, ndi Yese anabala Davide.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/RUT/4-2464e9df2763cb283373dace0f0da481.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba za kusintha kwa zinthu m’dziko la Aisraele, kuchokera pa nthawi ya

Oweruza

kufikira pa nthawi yokhazikitsa ufumu. Nkhani yonse yagona pa anthu atatuwa: Samuele mweruzi omaliza, Saulo mfumu yoyamba, ndiponso Davide ndi zochita zake pa unyamata wake asanalowe ufumu.

Phunziro lopezeka m’bukuli monganso m’mabuku ena osimba mbiri ya Aisraele ndi lakuti, kukhala okhulupirika kwa Mulungu kumabweretsa mtendere ndi madalitso, koma kusamvera ndi kupandukira Mulungu kumadzetsa zoipa. Awa ndi mau amene Yehova adawauza wansembe Eli, “Popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.” (2.30).

Mau ena opezeka m’bukumu aonetsa kuti si Aisraele onse ankafuna kukhala ndi mfumu yowalamulira. Paja Yehova yekha anali ngati mfumu yao yeniyeni; koma chifukwa cha pempho laolo, Yehova adawasankhirabe mfumu. Chinthu chofunika chinali chakuti mfumuyo pamodzi ndi Aisraele onse amvere ulamuliro wa Mulungu ndi kutsata mau ake (2.7-10); akamatero, onse adzakhala pabwino, anthu olemera ndi osauka omwe.

Za mkatimu

Samuele pa ntchito yake yoweruza Aisraele

1.1—7.17

Saulo alowa ufumu

8.10—10.27

Zaka zoyamba za ufumu wa Saulo

11.1—15.35

Saulo ndi Davide

16.1—30.31

Imfa ya Saulo ndi ana ake

31.1-13

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 1

1 Ndipo panali munthu wina wa ku Ramatayimu Zofimu, wa dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Elikana, mwana wake wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, Mwefuremu.

2 Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma.

3 Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m’mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.

4 Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wake, ndi ana ake onse, aamuna ndi aakazi, gawo lao;

5 koma anapatsa Hana magawo awiri, chifukwa anakonda Hana, koma Yehova anatseka mimba yake.

6 Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukulu, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yake.

7 Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.

8 Ndipo mwamuna wake Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?

9 Chomwecho Hana anauka atadya mu Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.

10 Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;

11 nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.

12 Ndipo panali, m’mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake.

13 Koma Hana ananena mu mtima; milomo yake inatukula, koma mau ake sanamveke; chifukwa chake Eli anamuyesa woledzera.

14 Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako.

15 Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwe vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.

16 Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; chifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kuchuluka kwa kudandaula kwanga ndi kuvutika kwanga.

17 Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israele akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.

18 Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Chomwecho mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.

19 Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.

20 Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova,

21 Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lake onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya chaka ndi chaka, ndi ya chowinda chake.

22 Koma Hana sadakwere, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.

23 Ndipo Elikana mwamuna wake anati, Chita chimene chikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ake. Chomwecho mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wake, kufikira anamletsa kuyamwa.

24 Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng’ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng’ono.

25 Ndipo iwo anapha ng’ombe, nabwera naye mwanayo kwa Eli.

26 Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.

27 Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye;

28 chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/1-ef9f15a8491ab620c761f067435b8de5.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 2

Choyamikira cha Hana

1 Ndipo Hana anapemphera, nati,

Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova,

nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova;

pakamwa panga pakula kwa adani anga;

popeza ndikondwera m’chipulumutso chanu.

2 Palibe wina woyera ngati Yehova;

palibe wina koma Inu nokha;

palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

3 Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero;

m’kamwa mwanu musatuluke zolulutsa;

chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru,

ndipo Iye ayesa zochita anthu.

4 Mauta a amphamvu anathyoka,

koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m’chuuno.

5 Amene anakhuta anakasuma chakudya;

koma anjalawo anachira;

inde chumba chabala asanu ndi awiri;

ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.

6 Yehova amapha, napatsa moyo;

Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.

7 Yehova asaukitsa, nalemeretsa;

achepetsa, nakuzanso.

8 Amuutsa waumphawi m’fumbi,

nanyamula wosowa padzala,

kukamkhalitsa kwa akalonga;

ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero.

Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova,

ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.

9 Adzasunga mapazi a okondedwa ake,

koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima;

pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.

10 Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika;

kumwamba Iye adzagunda pa iwo;

Yehova adzaweruza malekezero a dziko.

Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake,

nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.

11 Ndipo Elikana ananka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo.

Kuchimwa kwa ana a Eli

12 Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova.

13 Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m’dzanja lake;

14 nachipisa m’chimphuli, kapena mumkhate, kapena m’nkhali, kapena mumphika; yonse imene chovuuliracho chinaitulutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yake. Ankatero ku Silo ndi Aisraele onse akufika kumeneko.

15 Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.

16 Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.

17 Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova.

18 Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m’chuuno ndiefodiwabafuta.

19 Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung’ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka.

20 Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m’malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.

21 Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana aamuna atatu, ndi ana aakazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.

22 Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo lachihema chokomanako.

23 Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa.

24 Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndilikuimva sili yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova.

25 Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.

26 Ndipo mwanayo Samuele anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima.

Mneneri aneneratu za kupasuka kwa banja la Eli

27 Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali mu Ejipito, m’nyumba yaFarao?

28 Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?

29 Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m’mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?

30 Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.

31 Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m’banja lako musakhalenso nkhalamba.

32 Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m’malo mwa zabwino zonse Iye akadachitira Israele. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba chikhalire.

33 Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha paguwa langa la nsembe, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m’banja lako adzamwalira akali biriwiri.

34 Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.

35 Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m’chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.

36 Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m’banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaone kakudya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/2-1a14a420767e8e6bd79f3928cafb4269.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 3

Masomphenya a Samuele

1 Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.

2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m’malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);

3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m’mene munali likasa la Mulungu.

4 Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano.

5 Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitane, kagone. Napita iye, nagona.

6 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitane, mwana wanga; kagone.

7 Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.

8 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.

9 Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m’malo mwake.

10 Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.

11 Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva.

12 Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.

13 Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.

14 Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.

Samuele awulula kwa Eli

15 Ndipo Samuele anagona kufikira m’mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.

16 Pamenepo Eli anaitana Samuele, nati, Mwana wanga, Samuele. Nati iye, Ndine.

17 Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe.

18 Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.

19 Ndipo Samuele anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ake amodzi apite pachabe.

20 Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhalemneneriwa Yehova.

21 Ndipo Yehova anaonekanso mu Silo, pakuti Yehova anadziwulula kwa Samuele ku Silo, mwa mau a Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/3-14d33f035d75dac34878bfdce1045d58.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 4

Afilisti akantha Aisraele

1 Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki.

2 Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.

Likasa lilandidwa, Hofeni ndi Finehasi aphedwa

3 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengerelikasa la chipanganola Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m’dzanja la adani athu.

4 Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati paakerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.

5 Pakufika likasalo la chipangano la Yehova kuzithando, Aisraele onse anafuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linachita chivomezi.

6 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n’lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.

7 Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza nkale lonse panalibe chinthu chotere.

8 Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m’manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m’chipululu ndi yomweyi.

9 Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao.

10 Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi.

11 Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.

12 Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong’ambika, ndi dothi pamutu pake.

Imfa ya Eli

13 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m’mbali mwa njira, alikuyang’anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m’mzindamo, nanena izi, a m’mzinda monse analira.

14 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.

15 Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong’o osapenya.

16 Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndachokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, Nkhondoyo idatani, mwana wanga?

17 Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa.

18 Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai.

19 Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera.

20 Ndipo pamene adati amwalire, anthu aakazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira.

21 Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.

22 Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/4-f29df2c77837670517c8d4370cb4933d.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 5

Likasa la Mulungu kunyumba ya Dagoni

1 Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.

2 Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni.

3 Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m’malo mwake.

4 Ndipo m’mawa mwake polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wake ndi zikhato zonse ziwiri za manja ake zinagona zoduka pachiundo; Dagoni anatsala thupi lokha.

5 Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m’nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino.

Masauko a Afilisti chifukwa cha likasa

6 Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, mu Asidodi ndi m’midzi yake.

7 Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.

8 Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko.

9 Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang’ono; ndi mafundo anawabuka.

10 Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu.

11 Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m’mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.

12 Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mzindawo kunakwera kumwamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/5-69ecef3fa6842f65ed3044ac708e7ad6.mp3?version_id=1068—