Categories
OWERUZA

OWERUZA 13

Aisraele agonjera Afilisti; abadwa Samisoni

1 Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m’dzanja la Afilisti zaka makumi anai.

2 Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.

3 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.

4 Chifukwa chake udzisamalire, usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chinthu chilichonse chodetsa;

5 pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa MulunguMnazirichibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m’dzanja la Afilisti.

6 Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunse uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;

7 koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chilichonse chodetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire mpaka tsiku la kufa kwake.

8 Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa.

9 Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m’munda, mwamuna wake Manowa palibe.

10 Ndipo mkaziyo anafulumira nathamanga, nauza mwamuna wake, nanena naye, Taona, wandionekera munthu anandidzerayo tsiku lija.

11 Nanyamuka Manowa natsata mkazi wake, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna uja munalankhula ndi mkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene.

12 Nati Manowa, Achitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ake a mwanayo ndi machitidwe ake adzatani?

13 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Zonse ndinazinena ndi mkazi azisamalire.

14 Chilichonse chichokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena choledzeretsa, kapena kudya chilichonse chodetsa; zonse ndinamlamulira azisunge.

15 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikuchedwetseni kuti tikukonzereni mwanawambuzi.

16 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undichedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwe kuti ndiye mthenga wa Yehova.

17 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atachitika mau anu, tikuchitireni ulemu.

18 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza lili lodabwitsa?

19 Pamenepo Manowa anatenga mwanawambuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anachita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere.

20 Pakuti kunali, pakukwera lawi la moto paguwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m’lawi la paguwalo; ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.

21 Ndipo mthenga wa Yehova sanaonekerenso kwa Manowa kapena kwa mkazi wake. Pamenepo anadziwa Manowa kuti ndiye mthenga wa Yehova.

22 Nati Manowa kwa mkazi wake, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu.

23 Koma mkazi wake ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa padzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi ino.

24 Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.

25 Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/13-03726c0d6c23c8497e643c593cbc7fdb.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 14

Ukwati wa Samisoni

1 Ndipo Samisoni anatsikira ku Timna, naona mkazi wa ku Timna wa ana aakazi a Afilisti.

2 Nakwera iye, nauza atate wake ndi amai wake, nati, Ndapenya mkazi mu Timna wa ana aakazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga.

3 Koma atate wake ndi amai wake ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana aakazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samisoni kwa atate wake, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.

4 Koma atate wake ndi amai wake sanadziwe kuti chidachokera kwa Yehova ichi; popeza analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israele.

Samisoni apha mkango

5 Pamenepo anatsikira Samisoni, ndi atate wake ndi mai wake ku Timna, nadza ku minda yampesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira.

6 Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung’amba monga akadang’amba mwanawambuzi, wopanda kanthu m’dzanja lake; koma sanauze atate wake kapena amai wake chimene adachichita.

7 Ndipo anatsika nakamba ndi mkazi, namkonda Samisoni pamaso pake.

8 Atapita masiku ndipo anabweranso kudzamtenga, napatuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m’chitanda cha mkango munali njuchi zoundana, ndi uchi.

9 Ndipo anaufula ndi dzanja lake, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wake ndi amai wake, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauze kuti adaufula uchiwo m’chitanda cha mkango.

Awaphera anthu mwambi

10 Ndipo atate wake anatsikira kwa mkazi; ndi Samisoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata.

11 Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzake makumi atatu akhale naye.

12 Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m’masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu;

13 koma ngati simutha kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve.

14 Ndipo ananena nao,

Chakudya chinatuluka m’mwini kudya,

ndi chozuna chinatuluka m’mwini mphamvu.

Ndipo masiku atatu sanakhoze kutanthauzira mwambiwo.

15 Koma kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anati kwa mkazi wa Samisoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?

16 Ndipo mkazi wa Samisoni analira pamaso pake, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzire atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe?

17 Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo.

18 Ndipo amuna a pamzinda anati kwa Samisoni tsiku lachisanu ndi chiwiri, lisanalowe dzuwa,

Chozuna choposa uchi nchiyani;

ndi champhamvu choposa mkango nchiyani?

Pamenepo ananena nao,

Mukadapanda kulima ndi ng’ombe yanga,

simukadatha kumasulira mwambi wanga.

19 Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake.

20 Ndipo mkazi wake wa Samisoni anakhala wa mnzake, amene adakhala bwenzi lake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/14-f7204f85e9f43d3d5265e3ea9e984b11.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 15

Samisoni atentha za m’minda ya Afilisti

1 Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kucheka tirigu Samisoni anakacheza ndi mkazi wake ndi kumtengera mwanawambuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kuchipinda. Koma atate wake sanamlole kulowamo.

2 Nati atate wake, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi lako; mng’ono wake sakoma koposa iye nanga? Ukhale naye, m’malo mwa winayu.

3 Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi ino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine.

4 Namuka Samisoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza michira, naika muuni pakati pa michira iwiri iliyonse.

5 Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosacheka wa Afilisti, natentha miulu, ndi tirigu wosacheka yemwe, ndi minda yaazitonayomwe.

6 Pamenepo Afilisti anati, Wachita ichi ndani? Nati, Samisoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wake, nampereka kwa mnzake. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wake ndi moto.

7 Ndipo Samisoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani chilango ndi pamenepo ndidzaleka.

8 Ndipo anawakantha nyung’unyu ndi ntchafu, makanthidwe aakulu; natsika nakhala m’phanga mwa thanthwe la ku Etamu.

Ayesa kumanga Samisoni, napha iye anthu ambiri

9 Pamenepo Afilisti anakwera, namanga misasa mu Yuda, natandika mu Lehi.

10 Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera chifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samisoni, kumchitira iye monga anatichitira ife.

11 Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo.

12 Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m’dzanja la Afilisti, Nanena nao Samisoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha.

13 Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m’dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kuchokera kuthanthwe.

14 Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake.

15 Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha bulu, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi.

16 Nati Samisoni,

Ndi chibwano cha bulu, miulumiulu,

amuna chikwi ndawakantha ndi chibwano cha bulu.

17 Ndipo kunali, atatha kunena, anataya chibwano m’dzanja lake; nawatcha malowo Ramatilehi ndiko kunena chitunda cha chibwano.

18 Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m’dzanja la osadulidwa awa?

19 Pamenepo Mulungu anang’amba pokumbika paja pa Lehi, natulukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wake, natsitsimuka iye; chifukwa chake anawatcha dzina lake, Kasupe wa wofuula, ndiwo mu Lehi mpaka lero lino.

20 Ndipo Samisoni anaweruza Israele m’masiku a Afilisti zaka makumi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/15-960a0e8fc743a979e2905ff9e7b34771.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 16

Samisoni ku Gaza

1 Ndipo Samisoni anamuka ku Gaza, naonako mkazi wadama, nalowana naye.

2 Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mzinda, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.

3 Koma Samisoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mzinda, ndi mphuthu ziwirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba paphiri lili pandunji pa Hebroni.

Delila apereka Samisoni

4 Ndipo pambuyo pake kunali kuti anakonda mkazi m’chigwa cha Soreki, dzina lake ndiye Delila.

5 Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi.

6 Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Ndikupempha, undiuze umo muchokera mphamvu yako yaikulu, ndi chimene angakumange nacho, kuti akuzunze.

7 Nanena naye Samisoni, Akandimanga nazo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma, ndidzakhala wofooka, wakunga munthu wina.

8 Pamenepo akalonga a Afilisti anakwera nazo kwa mkaziyo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma; ndipo iye anammanga nazo.

9 Koma anali nao omlalira m’chipinda cha m’kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m’khosi yathonje pokhudza moto. M’mwemo mphamvu yake siinadziwike.

10 Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Taona, wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze tsopano, ndikupempha, chimene angakumange nacho.

11 Nanena naye, Akandimangitsa nazo zingwe zatsopano, zosagwira nazo ntchito pamenepo ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina.

12 Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Ndi omlalira analikulinda m’chipinda cha m’kati. Koma anazidula pa manja ake ngati thonje.

13 Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze chimene angakumange nacho. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko.

14 Ndipo anachimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samisoni; nagalamuka iye patulo take, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe.

15 Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? Wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo muchokera mphamvu yako yaikulu.

16 Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ake, namkakamiza, moyo wake unavutika nkufuna kufa.

17 Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndineMnaziriwa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense.

18 Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wake wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi ino, pakuti wandifotokozera za mtima wake wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m’dzanja lao.

19 Pamenepo anamgonetsa pa mabondo ake, naitana munthu, nameta njombi zake zisanu ndi ziwiri; nayamba kumzunza, nimchokera mphamvu yake.

20 Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m’tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.

21 Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m’kaidi.

22 Koma atammeta tsitsi la pamutu pake linayamba kumeranso.

Samisoni agwetsa nyumba ya Dagoni, namwalira

23 Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikulu, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samisoni mdani wathu m’dzanja lathu.

24 Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m’dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri.

25 Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samisoni, atisewerere. Naitana Samisoni m’kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuka iye pakati pa mizati.

26 Ndipo Samisoni anati kwa mnyamata womgwira dzanja, Ndileke, ndikhudze mizati imene nyumba ikhazikikapo, kuti nditsamirepo.

27 Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang’ana pakusewera Samisoni.

28 Pamenepo Samisoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi ino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri.

29 Ndipo Samisoni anagwira mizati iwiri ya pakati imene nyumba inakhazikikapo, natsamirapo wina ndi dzanja lamanja, ndi unzake ndi dzanja lamanzere.

30 Nati Samisoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m’mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo.

31 Pamenepo anatsika abale ake ndi banja lonse la atate wake, namnyamula, nakwera naye, namuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m’manda a Manowa atate wake. Ndipo adaweruza Israele zaka makumi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/16-4723bcd192e2e9ec1099fbb48dad071e.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 17

Mika ndi fano lake

1 Ndipo ku mapiri a Efuremu kunali munthu dzina lake ndiye Mika.

2 Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m’makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.

3 Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m’mwemo ndikubwezera izi.

4 Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m’nyumba ya Mika.

5 Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga chovala cha wansembe, ndiaterafi, namninkha zansembe mwana wake wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wake.

6 Masikuwa panalibe mfumu mu Israele, yense anachita chomuyenera m’maso mwake.

7 Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu ku Yuda, wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko.

8 Adachokera munthuyo m’mudzi mu Betelehemu ku Yuda, kugonera paliponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wake anafika ku mapiri a Efuremu, kunyumba ya Mika.

9 Ndipo Mika ananena naye, Ufumira kuti? Nati kwa iye, Ndine Mlevi wa ku Betelehemu ku Yuda, ndilikumuka kugonera kumene ndikapeza pokhala.

10 Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndalama khumi pachaka, ndi chovala chofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.

11 Ndi Mleviyo anavomera kukhalitsa ndi munthuyo; ndi mnyamatayo anamkhalira ngati mmodzi wa ana ake.

12 Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wake, nakhala m’nyumba ya Mika.

13 Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandichitira chokoma, popeza ndili naye Mlevi akhale wansembe wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/17-59a84d5e6368e3c98c0f66ba33ef7c46.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 18

Ana a Dani alanda mafano a Mika

1 Masiku ajawo panalibe mfumu mu Israele; masiku ajanso fuko la Adani anadzifunira cholowa chakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sichinawagwere cholowa chao pakati pa mafuko a Israele.

2 Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m’dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efuremu kunyumba ya Mika, nagona komweko.

3 Pokhala iwo m’nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napatukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? Uchitanji muno? Ukhala nacho chiyani kuno?

4 Ndipo ananena nao, Mika anandichitira chakutichakuti, napangana nane za ntchito, ndipo ndikhala wansembe wake.

5 Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma.

6 Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova.

7 Pamenepo amuna asanuwa anachoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m’mwemo, kuti anakhala okhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m’dzikomo munalibe mwini bwalo wakuchititsa manyazi m’chinthu chilichonse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu aliyense.

8 Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu?

9 Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli chete kodi? Musamachita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo.

10 Pomuka inu mudzafikira anthu okhazikika mtima ndi dziko lachitando; pakuti Mulungu walipereka m’dzanja lanu; pamenepo mposasowa kanthu kalikonse kali padziko lapansi.

11 Pamenepo amuna mazana asanu ndi limodzi, omangira zida za nkhondo m’chuuno, anaphumulako a banja la a Dani, anachokera ku Zora, ndi ku Esitaoli.

12 Nakwera namanga misasa mu Kiriyati-Yearimu, mu Yuda; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo chigono cha Dani, mpaka lero; taona, ali m’tseri mwa Kiriyati-Yearimu.

13 Ndipo anapitirira komweko kunka ku mapiri a Efuremu, nadza kunyumba ya Mika.

14 Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m’nyumba izi muli chovala cha wansembe, ndiaterafindi fano losema, ndi fano loyenga? Ndipo tsopano dziwani choyenera inu kuchita.

15 Napatuka iwo kunkako, nafika kunyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji.

16 Ndipo amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida zao za nkhondo m’chuuno, ndiwo a ana a Dani, analikuima polowera pa chipata;

17 koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera analowako, natenga fano losema, ndi chovala cha wansembe ndi aterafi, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa chipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m’chuuno.

18 Atalowa iwo m’nyumba ya Mika, natengako fano losema, chovala cha wansembe, ndi aterafi, ndi fano loyenga, wansembeyo ananena nao, Muchitanji?

19 Ndipo ananena naye, Khala chete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; chikukomera nchiti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa fuko ndi banja mu Israele?

20 Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye chovala cha wansembe, ndi aterafi ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu.

21 Atatero anabwerera, nachoka, natsogoza ana aang’ono ndi zoweta ndi akatundu.

22 Atafika kutali ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m’nyumba zoyandikizana ndi yake, natsata ndi kuwapeza ana a Dani.

23 Ndipo anafuula kwa ana a Dani. Nacheuka iwo nati kwa Mika, Chakusowa chiyani, kuti wamemeza anthu ako?

24 Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kuchoka; chinditsaliranso chiyani? Ndipo muneneranji kwa ine, Chakusowa nchiyani?

25 Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m’nyumba mwako.

26 Nayenda ulendo wao ana a Dani; ndipo Mika pakuona kuti anamposa mphamvu, anatembenuka nabwerera kunyumba kwake.

27 M’mwemo anatenga zimene Mika adachipanga, ndi wansembe anali naye, nafika ku Laisi, kwa anthu odekha ndi okhazikika mtima, nawakantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mzinda wao ndi moto.

28 Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku chigwa chokhala ku Beterehobu. Pamenepo anamanganso mzindawo, nakhala m’mwemo.

29 Ndipo analitcha dzina la mzindawo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israele; koma poyambapo dzina la mzinda linali Laisi.

30 Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake aamuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m’dziko.

31 Motero anadziikira fano losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/18-e3d1443fc12d41753502508abe1853f2.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 19

Choopsa adachichita a ku Gibea

1 Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu mu Israele, panali munthu Mlevi wogonera kuseri kwa mapiri a Efuremu amene anadzitengera mkazi wamng’ono wa ku Betelehemu ku Yuda.

2 Koma mkazi wake wamng’ono anachita chigololo akali naye, namchokera kunka kunyumba ya atate wake ku Betelehemu ku Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.

3 Koma anauka mwamuna wake namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wake, ndi abulu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye kunyumba ya atate wake. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo anakondwera kukomana naye.

4 Ndipo mpongozi wake, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.

5 Ndipo kunali, tsiku lachinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kuchoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wake, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang’ono, ndipo utatero upite.

6 Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Uvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.

7 Ndipo munthuyo ananyamuka kuti amuke; koma mpongozi wakeyo anamkakamiza, nagonanso komweko.

8 Nalawirira mamawa tsiku lachisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri.

9 Pamenepo munthuyo ananyamuka kuchoka, iye ndi mkazi wake wamng’ono ndi mnyamata wake; koma mpongozi wake, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kunka ulendo wanu kwanu.

10 Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nachoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwoYerusalemu); ndi pamodzi naye panali abulu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wake wamng’ono.

11 Pofika iwo pa Yebusi linalimkulowa dzuwa, ndi mnyamata anati kwa mbuye wake, Tiyeni, tipatukire mzinda uwu wa Ayebusi ndi kugona pomwepa.

12 Koma mbuye wake ananena naye, Tisapatukire mzinda wachilendo, wosati wa ana a Israele, koma tipitirire kunka ku Gibea.

13 Nati kwa mnyamata wake, Tiyeni, tiyandikire kwinako: tigone mu Gibea, kapena mu Rama.

14 Napitirira iwo, nayenda, ndi dzuwa linawalowera pafupi pa Gibea, ndiwo wa Benjamini.

15 Napatukirako, kuti alowe nagone ku Gibea; nalowa iye, nakhala pansi m’khwalala la mzindawo, pakuti panalibe wina wowalandira m’nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.

16 Ndipo taonani, munthu nkhalamba anachokera ku ntchito yake kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efuremu, nagonera ku Gibea; koma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini.

17 Pamene anakweza maso ake anaona munthu wa pa ulendoyo m’khwalala la mzinda; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? Ufumira kuti?

18 Ndipo ananena nayo, Tili kuchokera ku Betelehemu ku Yuda, kunka ku mbali za mapiri a Efuremu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu ku Yuda; ndipo tsopano ndili kumuka kunyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba.

19 Ngakhale udzu ndi chakudya cha abulu athu ziliko; ndi mkate ndi vinyo zilikonso kwa ine ndi kwa mdzakazi wako ndi kwa mnyamata wokhala ndi akapolo ako; kosasowa kanthu.

20 Ndipo nkhalambayo inati, Mtendere ukhale ndi iwe, komatu, zosowa zako zonse ndidzakupatsa ndi ine; pokhapo usagone m’khwalala.

21 Pamenepo anamlonga m’nyumba yake, napatsa abulu chakudya; ndipo iwo anasamba mapazi ao, nadya, namwa.

22 Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m’mzindawo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m’nyumba mwako kuti timdziwe.

23 Ndipo munthu mwini nyumba anawatulukira nanena nao, Iai, abale anga, musachite choipa chotere; popeza mwamuna uyu walowa m’nyumba mwanga, musachite chopusa ichi.

24 Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wake wamng’ono siwa; ndiwatulutse iwo, muwachepetse iwo, ndi kuwachitira monga muyesa chokoma; koma mwamuna uyu musamchitire chopusa ichi.

25 Koma amunawo sanafune kumvera; motero munthuyu anagwira mkazi wake wamng’ono, natuluka naye kwa iwo kunja; namdziwa iwo, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m’mawa; namlola achoke mbandakucha.

26 Nadza mkaziyo, kutacha, nagwa pakhomo pa nyumba ya munthu padali mbuye wake, kufikira kutayera.

27 Pamene mbuye wake anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, natuluka kunka ulendo wake, taona, mkazi wake wamng’ono, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ake pachiundo.

28 Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pabulu; nanyamuka mwamunayo, nanka kwao.

29 Ndipo pofika iye kunyumba kwake, anatenga mpeni, nagwira mkazi wake wamng’onoyo namgawa chiwalochiwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku malire onse a Israele.

30 Ndipo kunali kuti onse amene anachiona anati, Sichinachitika, inde sichinaoneke chotere chiyambire tsiku lokwera ana a Israele kutuluka m’dziko la Ejipito mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/19-6e5bd169203a5e74833554531f573c75.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 20

Aisraele abwezera chilango fuko la Benjamini

1 Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.

2 Ndipo akulu a anthu onse a mafuko onse a Israele anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga.

3 Ndipo ana a Benjamini anamva kuti ana a Israele adakwera kunka ku Mizipa. Nati ana a Israele, Nenani, choipa ichi chinachitika bwanji?

4 Ndipo Mlevi, mwamuna wa mkazi anaphedwayo, anayankha nati, Ndinadza ine ku Gibea wa Benjamini, ine ndi mkazi wanga wamng’ono, kugonako.

5 Nandiukira eni ake a Gibea, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namchitira choipa mkazi wanga wamng’ono, nafa iye.

6 Pamenepo ndinagwira mkazi wanga wamng’ono ndi kumgawa ndi kumtumiza m’dziko lonse la cholowa cha Israele, pakuti anachita chochititsa manyazi ndi chopusa mu Israele.

7 Taonani, inu nonse, ndinu ana a Israele, mudzinenere mau ndi kudzipangira nokha kuno.

8 Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwake, kapena kupatukira nyumba yake,

9 koma tsopano ichi ndicho tidzachitira Gibea: tidzaukwerera ndi kulota maere.

10 Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mafuko onse a Israele; ndi zana limodzi pa zikwi chimodzi, ndi chikwi chimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibea wa Benjamini, auchitire monga mwa chopusa chonse unachita mu Israele.

11 Potero amuna onse a Israele anasonkhanira mzindawo, olunzika ngati munthu mmodzi.

12 Ndipo mafuko a Israele anatuma anthu mwa fuko lonse la Benjamini, ndi kuti, Choipa chanji ichi chinachitika mwa inu?

13 Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pake, okhala mu Gibea, kuti tiwaphe, ndi kuchotsera Israele choipachi. Koma Benjamini sanafune kumvera mau a abale ao, ana a Israele.

14 Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kuchokera kumizinda kunka ku Gibea, kuti atuluke kulimbana ndi ana a Israele.

15 Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m’mizinda tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala mu Gibea, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.

16 Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya.

17 Ndipo anawerenga amuna a Israele, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okhaokha.

18 Nauka ana a Israele, nakwera kunka ku Betele, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.

19 Nauka ana a Israele m’mawa, naumangira Gibea misasa.

20 Ndipo amuna a Israele anatuluka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israele anawandandalikira nkhondo ku Gibea.

21 Pamenepo ana a Benjamini anatuluka mu Gibea, naononga a Israele tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi.

22 Koma anthu, ndiwo amuna a Israele, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.

23 Ndipo ana a Israele anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.

24 Potero ana a Israele anayandikira ana a Benjamini m’mawa mwake.

25 Ndipo Benjamini anawatulukira ku Gibea m’mawa mwake, naononganso a ana a Israele amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.

26 Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.

27 Ndipo ana a Israele anafunsira kwa Yehova; pakutilikasa la chipanganola Mulungu linakhala komweko masiku aja,

28 namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m’dzanja lako.

29 Ndipo Israele anaika olalira Gibea pozungulira pake.

30 Ndipo ana a Israele anakwerera ana a Benjamini tsiku lachitatu, nanika pa Gibea monga nthawi zina.

31 Natuluka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mzinda, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu aamuna a Israele, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m’makwalala, limodzi la awo lokwera kunka ku Betele, ndi lina ku Gibea kuthengo.

32 Ndipo ana a Benjamini anati, Tawakantha pamaso pathu monga poyamba paja. Koma ana a Israele anati, Tithawe, tiwakokere kutali ndi mzinda kumakwalala.

33 Nauka amuna onse a Israele m’malo ao nanika ku Baala-Tamara; natuluka Aisraele olalira aja m’malo mwao, kumwera kwa Geba.

34 Ndipo anadza pandunji pa Gibea amuna osankhika mu Israele monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwe kuti choipa chili pafupi kuwakhudza.

35 Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israele; ndi ana a Israele anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.

36 Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israele anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibea.

37 Nafulumira olalirawo nathamangira Gibea, nabalalika olalirawo, nakantha mzinda wonse ndi lupanga lakuthwa.

38 Koma kunali chizindikiro choikika pakati pa amuna a Israele ndi olalirawo, ndicho chakuti afukitse mtambo wa utsi kumzinda.

39 Ndi nkhondo ya Israele inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israele, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo.

40 Koma pamene mtambo unayamba kukwera m’mzinda ngati utsi uli tolo, Abenjamini anacheuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.

41 Natembenuka amuna a Israele; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti chidawagwera choipa.

42 Nabwerera iwo pamaso pa amuna a Israele kunka njira ya chipululu; koma nkhondo inawalondetsa; ndi aja otuluka m’mizinda anawaononga pakati pao.

43 Anawazinga Abenjamini, anawapirikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibea, kotulukira dzuwa.

44 Ndipo adagwa a Benjamini amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu; iwo onse ndiwo ngwazi.

45 Natembenuka iwo, nathawira kuchipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m’makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri.

46 Potero onse amene adagwa a Benjamini tsiku lija, ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu, akusolola lupanga; iwo onse ndiwo ngwazi.

47 Koma amuna mazana asanu ndi limodzi anabwerera nathawira kuchipululu, ku thanthwe la Rimoni, nakhala m’thanthwe la Rimoni miyezi inai.

48 Ndipo amuna a Israele anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m’mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/20-3473e48a1aa3b2a9558011a484fae612.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 21

Fuko la Benjamini limangidwanso

1 Koma amuna a Israele adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wake wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wake.

2 Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.

3 Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israele, chachitika ichi chifukwa ninji mu Israele, kuti lasowa lero fuko limodzi mu Israele?

4 Ndipo kunali m’mawa mwake, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.

5 Nati ana a Israele, Ndani iye mwa mafuko onse a Israele amene sanakwere kudza kumsonkhano kwa Yehova? Pakuti panali lumbiro lalikulu pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.

6 Ndipo ana a Israele anamva chifundo chifukwa cha Benjamini mbale wao, nati, Fuko limodzi lalikhidwa pa Israele leroli.

7 Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu aakazi akhale akazi ao?

8 Nati iwo, Kodi pali lina la mafuko a Israele losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kuchokera ku Yabesi-Giliyadi sanadze mmodzi kumisasa, kumsonkhano.

9 Pakuti pamene anawerenga anthu, taonani, panalibe mmodzi komweko wa okhala mu Yabesi-Giliyadi.

10 Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala mu Yabesi-Giliyadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana aang’ono.

11 Ndipo chimene mukachite ndi ichi: mukaononge konse mwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense wodziwa mwamuna mogona naye.

12 Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m’dziko la Kanani.

13 Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m’thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere.

14 Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-Giliyadi; koma sanawafikire.

15 Ndipo anthu anamva chifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang’amba mafuko a Israele.

16 Pamenepo akulu a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti mu Benjamini?

17 Nati iwo, Pakhale cholowa cha iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe fuko mu Israele.

18 Koma ife sitingathe kuwapatsa ana athu aakazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israele adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi.

19 Nati iwo, Taonani, pali madyerero a Yehova chaka ndi chaka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Betele, kum’mawa kwa mseu wokwera kuchokera ku Betele kunka ku Sekemu, ndi kumwera kwa Lebona.

20 Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m’minda yampesa;

21 nimuyang’ane, ndipo taonani, atatuluka ana aakazi a Silo kuvinavina, pamenepo mutuluke m’minda yampesa ndi kudzigwirira yense mkazi wake mwa ana aakazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini.

22 Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkhe awa; mukadatero mukadapalamula tsopano.

23 Nachita chotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a ovina aja, amene anawatenga mwachifwamba; namuka iwo nabwerera ku cholowa chao, namanga midzi, nakhalamo.

24 Ndipo ana a Israele anachokako nthawi ija yense kunka ku fuko lake, ndi banja lake, natulukako yense kunka ku cholowa chake.

25 Panalibe mfumu mu Israele masiku aja; yense anachita chomkomera pamaso pake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/21-d2e034550e44b4aaab9af4ec430846a9.mp3?version_id=1068—

Categories
RUTE

RUTE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likamba nkhani ya Rute, mkazi wachimowabu amene adakwatiwa ndi mwamuna wa ku Israele. Mwamuna wake atamwalira, iye atsatira mpongozi wake Naomi ku Betelehemu kwao chifukwa chokhulupirira Mulungu wa Aisraele.

Nkhani yabwinoyi yochitika panthawi ija yankhanza ya

Oweruza

, iwonetsa kuti ngakhale amitundu nawonso adzalandira madalitso a Mulungu, akakhulupirira Mulungu wa Israele ndi kusanduka anthu ake.

Za mkatimu

Naomi abwerera ku Betelehemu pamodzi ndi Rute

1.1-22

Rute akumana ndi Bowazi

2.1—3.18

Rute akwatiwa ndi Bowazi Davide

4.1-22