Categories
YOSWA

YOSWA 18

Autsa chihema ku Silo

1 Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komwekochihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.

2 Ndipo anatsala mwa ana a Israele mafuko asanu ndi awiri osawagawira cholowa chao.

3 Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Muchedwa mpaka liti kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani?

4 Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati padziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine.

5 Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m’malire ake kumwera, ndi a m’nyumba ya Yosefe adzakhala m’malire mwao kumpoto.

6 Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ake; ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu.

7 Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo cholowa chao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi fuko la Manase logawika pakati adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani kum’mawa, chimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.

8 Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati padziko, ndi kulilemba, nimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova pa Silo.

9 Namuka amunawo, napitapita pakati padziko, nalilemba m’buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo.

10 Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.

Malire a Benjamini

11 Ndipo maere a fuko la ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anatuluka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.

12 Ndipo malire ao a kumpoto anachokera ku Yordani; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi matulukiro ake anali ku chipululu cha Betaveni.

13 Ndipo malire anapitirirapo kunka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Betele, kumwera; ndi malire anatsikira kunka ku Ataroti-Adara, kuphiri lokhala kumwera kwa Betehoroni wa kunsi.

14 Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mzinda wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.

15 Ndipo mbali ya kumwera inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; natuluka malire kunka kumadzulo, natuluka kunka ku chitsime cha madzi a Nefitowa;

16 natsikira malire kunka polekezera phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha mwana wa Hinomu, ndicho cha m’chigwa cha Refaimu kumpoto; natsikira ku chigwa cha Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwera, natsikira ku Enirogele;

17 nalembedwa kunka kumpoto, natuluka ku Enisemesi, natuluka ku Geliloti, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumimu; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;

18 napitirira ku mbali ya pandunji pa Betaraba kumpoto, natsirika kunka ku Araba;

19 napitirira malire kunka ku mbali ya Betehogila kumpoto; ndi matulukiro ake a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mchere; pa kulekezera kwa kumwera kwa Yordani; ndiwo malire a kumwera.

20 Ndipo malire ake mbali ya kum’mawa ndiwo Yordani, ndicho cholowa cha ana a Benjamini, kunena za malire ake pozungulira pake, monga mwa mabanja ao.

21 Koma mizinda ya fuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Betehogila, ndi Emekezizi;

22 ndi Betaraba, ndi Zemaraimu, ndi Betele;

23 ndi Avimu ndi Para, ndi Ofura;

24 ndi Kefaramoni, ndi Ofini, ndi Geba; mizinda khumi ndi iwiri pamodzi ndi midzi yao;

25 Gibiyoni ndi Rama, ndi Beeroti;

26 ndi Mizipa, ndi Kefira, ndi Moza;

27 ndi Rekemu, ndi Iripele ndi Tarala;

28 ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndiYerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/18-c6ad6a4457f16f0b75bc1868bb2d6739.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 19

Malire a Simeoni

1 Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.

2 Ndipo anali nacho cholowa chao Beereseba, kapena Sheba, ndi Molada;

3 ndi Hazara-Suwala, ndi Bala, ndi Ezemu;

4 ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horoma;

5 ndi Zikilagi, ndi Betemara-Kaboti, ndi Hazara-Susa:

6 ndi Betelebaoti, ndi Saruheni; mizinda khumi ndi itatu ndi midzi yao;

7 Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asani; mizinda inai ndi midzi yao;

8 ndi midzi yonse yozungulira mizinda iyi mpaka Baalati-Bere ndiwo Rama kumwera. Ndicho cholowa cha fuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.

9 M’gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao.

Malire a Zebuloni

10 Ndipo maere achitatu anakwerera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a cholowa chao anafikira ku Saridi;

11 nakwera malire ao kunka kumadzulo ndi ku Mareyala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokoneamu;

12 ndi kuchokera ku Saridi anazungulira kunka kum’mawa kumatulukira dzuwa, mpaka malire a Kisiloti-Tabori; natuluka kunka ku Daberati, nakwera ku Yafiya;

13 ndi pochoka pamenepo anapitirira kunka kum’mawa ku Gatihefere, ku Etikazini; natuluka ku Rimoni umene ulembedwa mpaka ku Neya,

14 nauzungulira malire kumpoto, kunka ku Hanatoni; ndi matulukiro ake anali ku chigwa cha Ifutahele;

15 ndi Katati, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: mizinda khumi ndi iwiri ndi midzi yao.

16 Ichi ndi cholowa cha ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, mizinda iyi ndi midzi yao.

Malire a Isakara

17 Maere achinai anamtulukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao.

18 Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu;

19 ndi Hafaraimu, ndi Siyoni, ndi Anaharati;

20 ndi Rabiti ndi Kisiyoni, ndi Ebezi;

21 ndi Remeti ndi Enganimu ndi Enihada, ndi Betepazezi;

22 ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi matulukiro a malire ao anali ku Yordani; mizinda khumi ndi isanu ndi umodzi ndi midzi yao.

23 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Isakara, monga mwa mabanja ao, mizinda ndi midzi yao.

Malire a Asere

24 Ndipo maere achisanu analitulukira fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao.

25 Ndi malire ao ndiwo Helekati, ndi Hali, ndi Beteni ndi Akisafu;

26 ndi Alamumeleki, ndi Amada, ndi Misala; nafikira ku Karimele kumadzulo ndi ku Sihori-Libinati;

27 nazungulira kotulukira dzuwa ku Betedagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifutahele, kumpoto ku Betemeke, ndi Neiyeli; natulukira ku Kabulu kulamanzere,

28 ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu;

29 nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumzinda wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu;

30 Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobu; mizinda makumi awiri mphambu iwiri ndi midzi yao.

31 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao, mizinda iyi ndi midzi yao.

Malire a Nafutali

32 Maere achisanu ndi chimodzi anatulukira ana a Nafutali, ana a Nafutali monga mwa mabanja ao.

33 Ndipo malire ao anayambira ku Helefe ku thundu wa ku Zaananimu, ndi Adami-Nekebu, ndi Yabinele, mpaka ku Lakumu; ndi matulukiro ake anali ku Yordani;

34 nazungulira malire kunka kumadzulo ku Azinoti-Tabori, natulukira komweko kunka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Asere kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordani kum’mawa.

35 Ndipo mizinda yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;

36 ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;

37 ndi Kedesi, ndi Ederei, ndi Enihazori;

38 ndi Yironi, ndi Migidalele, Horemu, ndi Betanati, ndi Betesemesi; mizinda khumi ndi isanu ndi inai, ndi midzi yao.

39 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Nafutali, monga mwa mabanja ao, mizinda ndi midzi yao.

Malire a Dani

40 Maere achisanu ndi chiwiri anatulukira fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.

41 Ndipo malire a cholowa chao anali Zora, ndi Esitaoli, ndi Irisemesi;

42 Saalabini, ndi Ayaloni ndi Itila;

43 ndi Eloni ndi Timna ndi Ekeroni;

44 ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati;

45 ndi Yehudi, ndi Beneberaki, ndi Gatirimoni;

46 ndi Meyarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pa Yopa.

47 Koma malire a ana a Dani anatuluka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m’mwemo, nautcha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.

48 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, mizinda iyi ndi midzi yao.

Cholowa cha Yoswa

49 Ndipo atatha kuligawa dziko likhale cholowa chao monga mwa malire ake, ana a Israele anapatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa pakati pao;

50 monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mzinda umene anawapempha, ndiwo Timnati-Sera, ku mapiri a Efuremu; ndipo anamanga mzindawo nakhala m’mwemo.

51 Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo lachihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/19-882057485df2f1ef6e6ef57fe376555f.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 20

Mizinda yopulumukirako

1 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

2 Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire mizinda yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose.

3 Kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalire inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.

4 Munthu akathawira umodzi wa mizinda iyi, aziima polowera pa chipata cha mzindawo, nafotokozere mlandu wake m’makutu a akulu a mzindawo; pamenepo azimlandira kumzinda kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.

5 Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m’dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale.

6 Ndipo azikhala m’mzindamo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m’masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumzinda kwake, ndi nyumba yake, kumzinda kumene adathawako.

7 Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.

8 Ndipo tsidya lija la Yordani kum’mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m’chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti mu Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani mu Basani wa fuko la Manase.

9 Iyi ndi mizinda yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/20-edbccbdf8f8049f172b09aad7af7838e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 21

Midzi yokhalamo Alevi

1 Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele;

2 nanena nao ku Silo m’dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse mizinda yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu.

3 Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi, kutapa pa cholowa chao, monga mwa lamulo la Yehova, mizinda iyi ndi mabusa ao.

4 Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, mizinda khumi ndi itatu.

5 Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Efuremu, ndi pa fuko la Dani, ndi pa hafu la fuko la Manase, mizinda khumi.

6 Ndipo ana a Geresoni analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa hafu la fuko la Manase mu Basani, mizinda khumi ndi itatu.

7 Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni mizinda khumi ndi iwiri.

8 Motero ana a Israele anapatsa Alevi mizinda iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.

9 Ndipo anapatsa motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la ana a Simeoni, mizinda iyi yotchulidwa maina ao;

10 kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adatulukira iwowa.

11 Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo.

12 Koma minda ya mizinda ndi midzi yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yake.

13 Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzake, ndi Libina ndi mabusa ake;

14 ndi Yatiri ndi mabusa ake, ndi Esitemowa ndi mabusa ake;

15 ndi Holoni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake;

16 ndi Aini ndi mabusa ake, ndi Yuta ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake; mizinda isanu ndi inai yotapira mafuko awiri aja.

17 Ndipo motapira fuko la Benjamini, Gibiyoni ndi mabusa ake, Geba ndi mabusa ake,

18 Anatoti ndi mabusa ake, ndi Alimoni ndi mabusa ake; mizinda inai.

19 Mizinda yonse ya ana a Aroni, ansembe, ndiyo khumi ndi itatu, ndi mabusa ao.

20 Ndipo mabanja a ana a Kohati, Aleviwo, otsala a ana a Kohati, analandira mizinda ya maere ao motapira pa fuko la Efuremu.

21 Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Gezere ndi mabusa ake;

22 ndi Kibizaimu ndi mabusa ake, Betehoroni ndi mabusa ake; mizinda inai.

23 Ndipo motapira fuko la Dani, Eliteke ndi mabusa ake, ndi Gibetoni ndi mabusa ake;

24 Ayaloni ndi mabusa ake, Gatirimoni ndi mabusa ake; mizinda inai.

25 Ndipo motapira pa hafu la fuko la Manase, Taanaki ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake; mizinda iwiri.

26 Mizinda yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao.

27 Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa hafu la fuko la Manase, Golani mu Basani ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; mizinda iwiri.

28 Ndipo motapira pa fuko la Isakara, Kisiyoni ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake;

29 Yaramuti ndi mabusa ake, Enganimu ndi mabusa ake; mizinda inai.

30 Ndipo motapira pa fuko la Asere, Misala ndi mabusa ake, Abidoni ndi mabusa ake;

31 Helekati ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake; mizinda inai.

32 Ndipo motapira pa fuko la Nafutali, Kedesi mu Galileya ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ake, ndi Karitani ndi mabusa ake, mizinda itatu.

33 Mizinda yonse ya Ageresoni monga mwa mabanja ao ndiyo mizinda khumi ndi itatu ndi mabusa ao.

34 Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa fuko la Zebuloni, Yokoneamu ndi mabusa ake, ndi Karita ndi mabusa ake,

35 Dimina ndi mabusa ake, Nahalala ndi mabusa ake; mizinda inai.

36 Ndipo motapira pa fuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,

37 Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake; mizinda inai.

38 Ndipo motapira m’fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake;

39 Hesiboni ndi mabusa ake, Yazere ndi mabusa ake: yonse pamodzi mizinda inai.

40 Yonseyi ndiyo mizinda ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo mizinda khumi ndi iwiri.

41 Mizinda yonse ya Alevi, pakati pa cholowa cha ana a Israele ndiyo mizinda makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao.

42 Mizinda iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero mizinda iyi yonse.

43 Motero Yehova anawapatsa Israele dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira laolao, nakhala m’mwemo.

44 Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaime munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m’manja mwao.

45 Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israele; zidachitika zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/21-376c630b82c10ed5e9159832ac7d26a2.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 22

A fuko la Rubeni, la Gadi, ndi la Manase logawika pakati amuka kwao

1 Pamenepo Yoswa anaitana Arubeni ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase,

2 nanena nao, Mwasunga inu zonsezo anakulamulirani Mose mtumiki wa Yehova; mwamveranso mau anga m’zonse ndinakulamulirani inu;

3 simunasiye abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga chisungire lamulo la Yehova Mulungu wanu.

4 Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani.

5 Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m’njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

6 Momwemo Yoswa anawadalitsa, nawauza amuke; ndipo anamuka ku mahema ao.

7 Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa mu Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;

8 nanena nao ndi kuti, Bwererani nacho chuma chambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndisiliva, ndi golide, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi malaya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.

9 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m’dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.

Guwa la nsembe la umboni

10 Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m’dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake.

11 Ndipo ana a Israele anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga guwa la nsembe pandunji padziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordani, ku mbali ya ana a Israele.

12 Pamene ana a Israele anamva ichi msonkhano wonse wa ana a Israele anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.

13 Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe,

14 ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mafuko onse a Israele; yense wa iwowa ndiye mkulu wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israele.

15 M’mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,

16 Utero msonkhano wonse wa Yehova, Cholakwa ichi nchiyani mwalakwira nacho Mulungu wa Israele, ndi kumtembenukira Yehova lero lino kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?

17 Kodi mphulupulu ya ku Peori itichipera, imene sitinadziyeretsere mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova,

18 kuti mubwerera lero lino kusatsata Yehova? Ndipo kudzakhala kuti popeza lero mupikisana ndi Yehova, mawa adzakwiyira gulu lonse la Israele.

19 Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m’dziko la cholowa cha Yehova m’mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.

20 Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwe m’choperekedwacho, ndipo mkwiyo unagwera gulu lonse la Israele? Osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yake.

21 Pamenepo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anayankha, nanena ndi akulu a mabanja a Israele,

22 Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,

23 tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, achifunse Yehova mwini wake;

24 ndipo ngati ife sitinachite ichi chifukwa cha kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli chiyani inu kwa Yehova Mulungu wa Israele?

25 Pakuti Yehova anaika Yordani ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope Yehova.

26 Chifukwa chake tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai;

27 koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m’tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m’tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.

28 Chifukwa chake tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m’tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, chitsanzo cha guwa la nsembe la Yehova, chomanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.

29 Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa chihema chake.

30 Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.

31 Ndipo Finehasi, mwana wa Eleazara wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira nacho Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israele m’dzanja la Yehova.

32 Ndipo Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, ndi akalonga anabwerera kuchokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m’dziko la Giliyadi, kudza ku dziko la Kanani kwa ana a Israele, nawabwezera mau.

33 Ndipo mauwo anakomera ana a Israele pamaso pao; ndi ana a Israele analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi.

34 Ndipo ana a Rubeni ndi ana a Gadi analitcha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/22-61e38fd80316fb143be3664fc4f52850.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 23

Yoswa achenjeza anthu asunge Malamulo a Mulungu

1 Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israele kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;

2 Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;

3 ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.

4 Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale cholowa cha mafuko anu, kuyambira ku Yordani, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa.

5 Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapirikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwachotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale cholowa chanu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.

6 Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kuchita zonse zolembedwa m’buku la chilamulo cha Mose, osachipatukira kulamanja kapena kulamanzere;

7 osalowa pakati paamitunduawa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;

8 koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munachita mpaka lero lino.

9 Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.

10 Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.

11 Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.

12 Koma, mukadzabwerera m’mbuyo pang’ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;

13 dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m’nthiti mwanu, ndi minga m’maso mwanu, mpaka mudzatayika m’dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

14 Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi.

15 Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m’dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

16 Mukalakwirachipanganocha Yehova Mulungu wanu chimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m’dziko lokomali anakupatsani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/23-1954612448e1e4778fdcc3e91652b98a.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 24

Yoswa akumbutsa anthu zowachitira Mulungu

1 Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzionetsa pamaso pa Mulungu.

2 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.

3 Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m’dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki.

4 Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.

5 Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani.

6 Ndipo ndinatulutsa atate anu mu Ejipito; ndipo munadza kunyanja; koma Aejipito analondola atate anu ndi magaleta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.

7 Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine mu Ejipito; ndipo munakhala m’chipululu masiku ambiri.

8 Pamenepo ndinakulowetsani inu m’dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordani; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m’dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanulanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.

9 Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, anauka naponyana ndi Israele; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;

10 koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m’dzanja lake.

11 Pamenepo munaoloka Yordani, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ake a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m’dzanja lanu.

12 Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.

13 Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo ntchito, ndi mizinda simunaimange, ndipo mukhala m’mwemo; mukudya za m’minda yampesa, ndi minda yaazitonaimene simunaioke.

Yoswa abwereza kuchita pangano pakati pa Mulungu ndi anthu

14 Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi mu Ejipito; nimutumikire Yehova.

15 Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m’dziko lao; koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

16 Ndipo anthu anayankha, nati, Sikungatheke kuti timsiye Yehova, ndi kutumikira milungu ina;

17 pakuti Yehova Mulungu wathu ndi Iye amene anatikweza kutitulutsa m’dziko la Ejipito kunyumba ya ukapolo, nachita zodabwitsa zazikuluzo pamaso pathu, natisunga m’njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao;

18 ndipo Yehova anaingitsa pamaso pathu anthu awa onse, ngakhale Aamori okhala m’dzikomo; chifukwa chake ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu.

19 Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simungathe inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zochimwa zanu.

20 Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yachilendo, adzatembenuka ndi kukuchitirani choipa, ndi kukuthani, angakhale anakuchitirani chokoma.

21 Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Iaitu, koma tidzatumikira Yehova.

22 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu, Inu mwadzichitira mboni inu nokha kuti mwadzisankhira Yehova kumtumikira Iye. Ndipo anati, Ndife mboni.

23 Ndipo tsopano, chotsani milungu yachilendo ili pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israele.

24 Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ake.

25 Motero Yoswa anachita pangano ndi anthu tsiku lija, nawaikira lemba ndi chiweruzo mu Sekemu.

26 Ndipo Yoswa analembera mau awa m’buku la chilamulo cha Mulungu; natenga mwala waukulu, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pamalo opatulika a Yehova.

27 Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.

28 Pamenepo Yoswa anauza anthu amuke, yense ku cholowa chake.

Amwalira Yoswa ndi Eleazara

29 Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi.

30 Ndipo anamuika m’malire a cholowa chake mu Timnati-Sera, ndiwo ku mapiri a Efuremu kumpoto kwa phiri la Gaasi.

31 Ndipo Israele anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa ntchito yonse ya Yehova anaichitira Israele.

32 Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.

33 Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika paphiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/24-9d1440838b9480f21486e3e17c726193.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba zochitika zina ndi zina kuyambira nthawi imene Aisraele analowa m’dziko la Kanani kufikira nthawi yokhazikitsa ufumu. Pa nthawi yonseyo Aisraele anakhala akuzunzika kwambiri chifukwa chokhala pakati pa anthu a mitundu ina, anthu ofunkha ndi ankhanza, kotero kuti panali chisokonezo. Bukuli litchedwa

Oweruza

, kunena anthu angapo amene Yehova awaitana kuti azitsogolera Aisraele anzao pa nkhondo yomenyana ndi adani. Woweruza wina wodziwika kwambiri ndi Samisoni amene zochita zake zikukambidwa pamutu 13 mpaka 16.

Phunziro lopezeka m’bukuli ndilo lakuti, Israele akakhala okhulupirika kwa Yehova, amakhala pa mtendere. Koma akafulatira Mulungu ndi kumamchimwira, amagwa m’mavuto aakulu. Komabe ngakhale iwo apandukira Yehova ndi kugwa m’mavuto, Mulungu ali wokonzeka kuwapulumutsa anthu akewo, ataona kuti atembenuka ndi kubwerera kwa Iyeyo.

Za mkatimu

Zochitika zina kufikira nthawi ya imfa ya Yoswa

1.1—2.10

Za oweruza ena ndi ena

2.11—16.31

Zochitika zinanso

17.1—21.25

Categories
OWERUZA

OWERUZA 1

Aisraele aonjeza kugonjetsa Akanani

1 Ndipo atafa Yoswa, ana a Israele anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?

2 Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m’dzanja lake.

3 Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.

4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m’dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki.

5 Ndipo anapeza Adoni-Bezeki mu Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi.

6 Koma Adoni-Bezeki anathawa; ndipo anampirikitsa, namgwira, namdula zala zazikulu za m’manja ndi za m’mapazi.

7 Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m’manja ndi m’mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye kuYerusalemu, nafa iye komweko.

8 Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mzinda ndi moto.

9 Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwera ndi kuchidikha.

10 Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala mu Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.

11 Pochoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Debiri, koma kale dzina la Debiri ndilo mudzi wa Kiriyati-Sefere.

12 Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha mudzi wa Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake.

13 Ndipo Otiniyele, mwana wa Kenazi mng’ono wa Kalebe anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.

14 Ndipo kunali, m’mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; natsika pabulu wake; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji?

15 Ndipo anati kwa iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.

16 Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m’mzinda wa m’migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m’chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.

17 Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala mu Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mzindawo analitcha Horoma.

18 Yuda analandanso Gaza ndi malire ake, ndi Asikeloni ndi malire ake ndi Ekeroni ndi malire ake.

19 Ndipo Yehova anali ndi Yuda, iye nawaingitsa a kumapiri, osaingitsa nzika za kuchigwa, popeza zinali nao magaleta achitsulo.

20 Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana aamuna atatu a Anaki.

21 Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala mu Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala mu Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.

22 Ndipo anakwera iwo a m’nyumba ya Yosefe, naonso kunka ku Betele; ndipo Yehova anakhala nao.

23 Ndipo iwo a m’nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Betele. Koma kale dzina la mzindawo ndilo Luzi.

24 Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m’mzinda, nanena naye, Utionetsetu polowera m’mzinda, ndipo tidzakuchitira chifundo.

25 Nawaonetsa polowera m’mzinda iye, naukantha mzinda iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lake lonse amuke.

26 Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mzinda, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino.

Aisraele aleka kugonjetsa Akanani ena

27 Koma Manase sanaingitse a ku Beteseani ndi midzi yake kapena a Taanaki ndi midzi yake, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yake, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yake, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yake; koma Akanani anakhumba kukhala m’dziko muja.

28 Ndipo kunali, atakula mphamvu Israele, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.

29 Ndipo Efuremu sanaingitse Akanani okhala mu Gezere; koma Akanani anakhala mu Gezere pakati pao.

30 Zebuloni sanaingitse nzika za ku Kitironi, kapena za ku Nahaloli; koma Akanani anakhala pakati pao, nawasonkhera.

31 Asere sanaingitse nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Alabu, kapena a Akizibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobu;

32 koma Asere anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitse.

33 Nafutali sanaingitse nzika za ku Betesemesi, kapena nzika za ku Betanati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Betesemesi, ndi a ku Betanati zinawasonkhera.

34 Ndipo Aamori anakankha ana a Dani akhale kumapiri pakuti sanawalole atsikire kuchigwa;

35 Aamori anakhumbanso kukhala kuphiri la Heresi, ku Ayaloni, ndi ku Saalibimu; koma dzanja la a m’nyumba ya Yosefe linawagonjetsa, nakhala iwo akupereka msonkho.

36 Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akarabimu, pathanthwe ku Sela, ndi pokwererapo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/1-0ff455f23c670f97faaea4ae62cf22d5.mp3?version_id=1068—

Categories
OWERUZA

OWERUZA 2

Mngelo wa Mulungu adzudzula Aisraele

1 Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m’dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyolachipanganochanga nanu ku nthawi yonse;

2 ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m’dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvere mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?

3 Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m’nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.

4 Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.

5 Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.

Aisraele alowerera atamwalira Yoswa

6 Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israele anamuka, yense ku cholowa chake, dziko likhale laolao.

7 Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele.

8 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zake zana ndi khumi.

9 Ndipo anamuika m’malire a cholowa chake mu Timnati-Heresi, ku mapiri a Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.

10 Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israele.

11 Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala;

12 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m’dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.

13 Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndiAsitaroti.

14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m’manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m’dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.

15 Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.

16 Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m’dzanja la iwo akuwafunkha.

17 Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m’njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.

18 Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m’dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.

19 Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m’mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni.

20 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga;

21 Inenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu ina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu;

22 kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai.

23 Motero Yehova analeka mitundu iyi osaiingitsa msanga, ndipo sadaipereke m’dzanja la Yoswa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/2-2505c2e715f0948e077fe96f11a42d82.mp3?version_id=1068—