Categories
YOSWA

YOSWA 8

Kupasulidwa kwa Ai

1 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m’dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mzinda wake ndi dziko lake;

2 ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng’ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mzinda.

3 Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,

4 nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mzinda; musakhalira kutali ndi mzinda, koma mukhale okonzekeratu nonse;

5 ndipo ine, ndi anthu onse ali nane, tidzayandikira mzinda; ndipo kudzali, pamene atuluka kudzakomana nafe, monga poyamba paja, tidzathawa pamaso pao;

6 ndipo adzatuluka kutitsata mpaka tidawakokera asiyane ndi mzinda; pakuti adzanena, Atithawa pamaso pathu monga poyamba paja; nafenso tidzathawa pamaso pao;

7 pamenepo muziuka m’molalira ndi kulowa m’mzinda; pakuti Yehova Mulungu wanu; adzaupereka m’manja mwanu.

8 Ndipo kudzali, mutagwira mzinda, muzitentha mzindawo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.

9 Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m’molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.

10 Ndipo Yoswa analawira m’mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akulu a Israele, pamaso pa anthu a ku Ai.

11 Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mzinda, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali chigwa.

12 Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m’molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda.

13 Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mzinda, ndi olalira ao kumadzulo kwa mzinda, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa chigwa.

14 Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m’mzinda kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mzinda.

15 Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse anaoneka ngati a ku Ai alikuwathyola, nathawira njira ya kuchipululu.

16 Pamenepo anthu onse okhala m’mzinda, anaitanidwa awapirikitse, nampirikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mzinda.

17 Ndipo sanatsale mwamuna mmodzi yense mu Ai kapena mu Betele osatulukira kwa Israele; nasiya mzinda wapululu, napirikitsa Israele.

18 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m’dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m’dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m’dzanja lake kuloza mzinda.

19 Nauka msanga olalirawo m’mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lake, nalowa m’mzinda, naugwira; nafulumira nayatsa mzindawo.

20 Pamene amuna a ku Ai anacheuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mzinda unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa chakuno kapena chauko; ndi anthu othawira kuchipululu anatembenukira owapirikitsa.

21 Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israele yense kuti olalirawo adagwira mzinda, ndi kuti utsi wa mzinda unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.

22 A kumzindanso anawatulukira; potero anakhala pakati pa Israele, ena mbali ina, ena mbali ina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsale kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.

23 Koma mfumu ya ku Ai anamgwira wamoyo, nadza naye kwa Yoswa.

24 Ndipo kunali, atatha Israele kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kuchipululu kumene anawapirikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisraele onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa.

25 Ndipo onse amene adagwa tsiku lija, amuna ndi akazi, ndiwo zikwi khumi ndi ziwiri, anthu onse a ku Ai.

26 Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.

27 Koma ng’ombe ndi zofunkha za mzinda uwu Israele anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa.

28 Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino.

29 Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mzinda; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino.

Apereka nsembe nawerenga Malamulo a Mose ku Ebala ndi Gerizimu

30 Pomwepo Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Israele guwa la nsembe m’phiri la Ebala,

31 monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israele, monga mulembedwa m’buku la chilamulo cha Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo chitsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika.

32 Ndipo analembapo pa miyalayi chitsanzo cha chilamulo cha Mose, chimene analembera pamaso pa ana a Israele.

33 Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenzalikasa la chipanganola Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji paphiri la Gerizimu, ndi ena pandunji paphiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele.

34 Atatero, anawerenga mau onse a chilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m’buku la chilamulo.

35 Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, ndi akazi ndi ana aang’ono, ndi alendo akuyenda pakati pao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/8-1622db8fca89bda53e311bd9b5bc2076.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 9

Yoswa anyengedwa ndi Agibiyoni napangana nao

1 Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;

2 anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israele, ndi mtima umodzi.

3 Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,

4 zinachita momchenjerera, ndipo zinapita mooneka ngati mithenga, ndipo zinatenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong’ambika ndi omangamanga;

5 ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, ndipo zinavala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

6 Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, ndipo zinati kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe.

7 Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?

8 Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? Ndipo mufuma kuti?

9 Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita mu Ejipito,

10 ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.

11 Ndipo akulu athu ndi nzika zonse za m’dziko mwathu zidanena nafe ndi kuti, Mutenge m’dzanja lanu kamba wa paulendo, kakomane naoni, nimunene nao, Ndife akapolo anu; ndipo tsopano mupangane nafe.

12 Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m’nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku lotuluka ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani uli wouma ndi woyanga nkhungu;

13 ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang’ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu.

14 Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.

15 Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira.

16 Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao.

17 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.

18 Ndipo ana a Israele sanawakanthe, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga.

19 Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israele, m’mwemo sitikhoza kuwachitira kanthu.

20 Tidzawachitira ichi, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo chifukwa cha lumbirolo tidawalumbirira.

21 Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao.

22 Ndipo Yoswa anawaitana, nanena nao, kuti, Mwatinyenga chifukwa ninji, ndi kuti, Tikhala kutalitali ndi inu, pokhala kwanu kuli pakati pa ife?

23 Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.

24 Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m’dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.

25 Ndipo tsopano, taonani, tili m’dzanja lanu; monga muyesa chokoma ndi choyenera kutichitira ife, chitani.

26 Pamenepo anawachitira chotero, nawalanditsa m’dzanja la ana a Israele, angawaphe.

27 Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/9-6ddc3c83cb92b6e3fc44a6c80cb24380.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 10

Chinkhondo ku Gibiyoni

1 Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu yaYerusalemuanamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, n’kukhala pakati pao;

2 anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mzinda waukulu, monga wina wa mizinda yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu.

3 Chifukwa chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piramu mfumu ya Yaramuti, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Debiri mfumu ya Egiloni, ndi kuti,

4 Kwerani kwanga kuno, ndi kundithandiza kuti tikanthe Gibiyoni, pakuti unachitirana mtendere ndi Yoswa ndi ana a Israele.

5 Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.

6 Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.

7 Pamenepo Yoswa anakwera kuchokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi zonse.

8 Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m’dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.

9 Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kuchokera ku Giligala usiku wonse.

10 Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.

11 Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.

Kuimitsidwa kwa dzuwa ndi mwezi

12 Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele,

Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni,

ndi Mwezi iwe, m’chigwa cha Ayaloni.

13 Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima

mpaka anthu adabwezera chilango adani ao.

Kodi ichi sichilembedwa m’buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.

14 Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m’tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israele nkhondo.

15 Pamenepo Yoswa anabwezera, ndi Aisraele onse pamodzi naye, ku chigono cha ku Giligala.

16 Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m’phanga la ku Makeda.

17 Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m’phanga la ku Makeda.

18 Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikulu kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;

19 koma inu musaime, pirikitsani adani anu, ndi kukantha a m’mbuyo mwao; musawalole alowe m’mizinda mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m’dzanja lanu.

20 Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israele atatha kuwakantha, makanthidwe aakulukulu mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m’mizinda ya malinga,

21 anthu onse anabwerera kuchigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anachitira chipongwe mmodzi yense wa ana a Israele.

22 Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditulutsira m’phanga mafumu asanuwo.

23 Ndipo anatero, natulutsira m’phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni.

24 Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana aamuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.

25 Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani anu onse amene mugwirana nao nkhondo.

26 Ndipo atatero, Yoswa anawakantha nawapha, nawapachika pa mitengo isanu; nalikupachikidwa pa mitengo mpaka madzulo.

27 Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m’phanga m’mene adabisala; naika miyala yaikulu pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.

Midzi ya kumwera igonja kwa Yoswa

28 Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake yomwe; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m’mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nachitira mfumu ya ku Makeda monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.

29 Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye anapitirira kuchokera ku Makeda kunka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina;

30 ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yake m’dzanja la Israele; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m’mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namchitira mfumu yake monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.

31 Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anapitirira kuchokera ku Libina kunka ku Lakisi; namanga misasa, nathira nkhondo pa uwo;

32 napereka Yehova Lakisi m’dzanja la Israele, ndipo anaulanda tsiku lachiwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m’mwemo monga mwa zonse anachitira Libina.

33 Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ake mpaka sanamsiyire ndi mmodzi yense.

34 Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anapitirira kuchokera ku Lakisi mpaka ku Egiloni; namanga misasa, nathira nkhondo.

35 Naulanda tsiku lomwelo, naukantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse amoyo onse anali m’mwemo tsiku lomwelo, monga mwa zonse anachitira Lakisi.

36 Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse naye anakwera kuchokera ku Egiloni mpaka ku Hebroni, nauthira nkhondo;

37 naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse, ndi amoyo onse anali m’mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anachitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m’mwemo.

38 Pamenepo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anabwerera kudza ku Debiri, nauthira nkhondo,

39 naulanda, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m’mwemo; sanasiye ndi mmodzi yense; monga anachitira Hebroni momwemo anachitira Debiri ndi mfumu yake, monganso anachitira Libina ndi mfumu yake.

40 Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira.

41 Ndipo Yoswa anawakantha kuyambira Kadesi-Baranea mpaka ku Gaza, ndi dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibiyoni.

42 Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo.

43 Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye, anabwerera kuchigono ku Giligala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/10-ee9d818ba8d107374f352c4e3f0ef10b.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 11

Yoswa agonjetsa mafumu a kumpoto

1 Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazori anachimva, anatuma kwa Yobabu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akisafu,

2 ndi kwa mafumu akukhala kumpoto kumapiri, ndi kuchigwa kumwera kwa Kineroti, ndi kuchidikha, ndi ku mitunda ya Dori kumadzulo;

3 kwa Akanani kum’mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Heremoni, m’dziko la Mizipa.

4 Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m’mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri.

5 Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo.

6 Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; udzawadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.

7 Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera.

8 Ndipo Yehova anawapereka m’dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m’mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense.

9 Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto.

10 Ndipo Yoswa anabwerera m’mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yake ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukulu wa maufumu aja onse.

11 Ndipo anakantha amoyo onse anali m’mwemo, ndi lupanga lakuthwa, ndi kuwaononga konse, osasiyapo ndi mmodzi yense wakupuma mpweya; ndipo anatentha Hazori ndi moto.

12 Ndipo Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.

13 Koma mizinda yonse yomangidwa pa zitunda zao Israele sanaitenthe, koma wa Hazori wokha; umenewu Yoswa anautentha.

14 Ndi zofunkha zonse za mizinda iyi ndi ng’ombe ana a Israele anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.

15 Monga Yehova adalamulira Mose mtumiki wake, momwemo Mose analamulira Yoswa; momwemonso anachita Yoswa; sanachotsepo mau amodzi pa zonse Yehova adalamulira Mose.

16 Motero Yoswa analanda dziko lonselo, la kumapiri, ndi la kumwera, ndi dziko lonse la Goseni, ndi dziko la kuchidikha, ndi la kuchigwa; ndi la kumapiri la Israele, ndi la ku chidikha chake;

17 kuyambira phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri, mpaka Baala-Gadi m’chigwa cha Lebanoni patsinde paphiri la Heremoni; nagwira mafumu ao onse, nawakantha, nawapha.

18 Yoswa anathira nkhondo mafumu awa onse nthawi yaikulu.

19 Palibe mzinda wakupangana mtendere ndi ana a Israele, koma Ahivi okhala mu Gibiyoni; anaigwira yonse ndi nkhondo.

20 Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.

21 Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwachotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israele; Yoswa anawaononga konse, ndi mizinda yao yomwe.

22 Panalibe Aanaki otsala m’dziko la ana a Israele; koma mu Gaza ndi mu Gati ndi mu Asidodi anatsalamo ena.

23 Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale cholowa chao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/11-10458e83590b696d306ce357c28d58a2.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 12

Mafumu amene ana a Israele anawakantha

1 Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum’mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum’mawa;

2 Sihoni mfumu ya Aamori wokhala mu Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;

3 ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum’mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum’mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga.

4 Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basani wotsala wa Arefaimu, wokhala ku Asitaroti ndi ku Ederei,

5 nachita ufumu m’phiri la Heremoni, ndi mu Saleka, ndi mu Basani lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Giliyadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.

6 Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi hafu la fuko la Manase, likhale cholowa chao.

7 Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israele anawakantha tsidya lija la Yordani kumadzulo, kuyambira Baala-Gadi m’chigwa cha Lebanoni mpaka phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mafuko a Israele, likhale laolao, monga mwa magawo ao;

8 kumapiri ndi kuchigwa, ndi kuchidikha, ndi kumatsikiro, ndi kuchipululu, ndi kumwera: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:

9 mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m’mbali mwa Betele, imodzi;

10 mfumu ya kuYerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi;

11 mfumu ya ku Yaramuti, imodzi; mfumu ya ku Lakisi, imodzi;

12 mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi;

13 mfumu ya ku Debiri, imodzi; mfumu ya ku Gederi, imodzi;

14 mfumu ya ku Horoma, imodzi; mfumu ya ku Aradi, imodzi;

15 mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi;

16 mfumu ya ku Makeda, imodzi; mfumu ya ku Betele, imodzi;

17 mfumu ya ku Tapuwa, imodzi; mfumu ya ku Hefere, imodzi;

18 mfumu ya ku Afeki, imodzi; mfumu ya ku Lasaroni, imodzi;

19 mfumu ya ku Madoni, imodzi; mfumu ya ku Hazori, imodzi;

20 mfumu ya ku Simironi-Meroni, imodzi; mfumu ya ku Akisafu, imodzi;

21 mfumu ya ku Taanaki, imodzi; mfumu ya ku Megido, imodzi;

22 mfumu ya ku Kedesi, imodzi; mfumu ya ku Yokoneamu ku Karimele, imodzi;

23 mfumu ya ku Dori, mpaka ponyamuka pa Dori, imodzi; mfumu ya ku Goimu mu Galileya, imodzi;

24 mfumu ya ku Tiriza, imodzi. Mafumu awa onse ndiwo makumi atatu ndi imodzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/12-68e558cb955bb3c503a07d9376f89c64.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 13

Chigawo cha dziko la kum’mawa kwa Yordani

1 Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikulukulu, alilandire cholowa chao.

2 Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse,

3 kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;

4 kumwera dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeki, mpaka ku malire a Aamori;

5 ndi dziko la Agebala, ndi Lebanoni, lonse kum’mawa, kuyambira Baala-Gadi pa tsinde la phiri la Heremoni, mpaka polowera pake pa Hamati;

6 nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.

7 Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi hafu la fuko la Manase, dziko ili likhale cholowa chao.

8 Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum’mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;

9 kuyambira pa Aroere, wokhala m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;

10 ndi mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, wakuchita ufumu mu Hesiboni, mpaka malire a ana a Amoni;

11 ndi Giliyadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Heremoni, ndi Basani lonse mpaka ku Saleka;

12 ufumu wonse wa Ogi mu Basani, wa kuchita ufumu mu Asitaroti, ndi mu Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.

13 Koma ana a Israele sanainge Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israele, mpaka lero lino.

14 Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye.

15 Ndipo Mose anapatsira fuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao.

16 Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba;

17 Hesiboni ndi mizinda yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni;

18 ndi Yahazi ndi Kedemoti, ndi Mefaati;

19 ndi Kiriyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m’phiri la kuchigwa;

20 ndi Betepeori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beteyesimoti;

21 ndi mizinda yonse ya kuchidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wochita ufumu mu Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midiyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m’dziko.

22 Ana a Israele anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.

23 Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordani ndi malire ake. Ndicho cholowa cha ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, mizinda yake ndi midzi yake.

24 Ndipo Mose anapatsira fuko la Gadi, ana a Gadi, monga mwa mabanja ao.

25 Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi mizinda yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba;

26 ndi kuyambira Hesiboni mpaka Ramati-Mizipe, ndi Betonimu; ndi kuyambira Mahanaimu mpaka malire a Debiri;

27 ndipo m’chigwa Beteharamu, ndi Betenimura, ndi Sukoti, ndi Zafoni, chotsala cha ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yordani ndi malire ake, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordani kum’mawa.

28 Ichi ndi cholowa cha ana a Gadi, monga mwa mabanja ao, mizinda yake ndi midzi yake.

29 Mose anaperekanso cholowa kwa hafu la fuko la Manase, ndicho cha hafu la fuko la Manase monga mwa mabanja ao.

30 Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basani lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basani, ndi mizinda yonse ya Yairi, yokhala mu Basani, mizinda makumi asanu ndi limodzi;

31 ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.

32 Izi ndi zolowazi Mose anazigawira m’zidikha za Mowabu, tsidya ilo la Yordani ku Yeriko, kum’mawa.

33 Koma fuko la Levi, Mose analibe kulipatsa cholowa: Yehova Mulungu wa Israele, ndiye cholowa chao, monga ananena nao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/13-18dc620e1811bebd2b1c80fd8da78e82.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 14

Kalebe alandira Hebroni

1 Ndipo awa ndi maiko ana a Israele anawalanda m’dziko la Kanani, amene Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, anawagawira.

2 Cholowa chao chinachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko la hafu.

3 Pakuti Mose adapatsa mafuko awiri, ndi fuko la hafu, cholowa tsidya ilo la Yordani; koma sanapatse Alevi cholowa pakati pao.

4 Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m’dziko, koma mizinda yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao.

5 Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israele anachita, nagawana dziko.

6 Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa chimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu mu Kadesi-Baranea.

7 Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga.

8 Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.

9 Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala cholowa chako, ndi cha ana ako kosalekeza, chifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.

10 Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi makumi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israele m’chipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino.

11 Koma lero lino ndili wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kutuluka ndi kulowa.

12 Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi mizinda yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.

13 Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale cholowa chake.

14 Chifukwa chake Hebroni likhala cholowa chake cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wonse.

15 Koma kale dzina la Hebroni linali mzinda wa Araba, ndiye munthu wamkulu pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/14-ab2738924caf4bcc646b681dc90b0507.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 15

Malire a Yuda

1 Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.

2 Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera;

3 natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;

4 napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera.

5 Ndi malire a kum’mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani;

6 nakwera malire kunka ku Betehogila, napitirira kumpoto kwa Betaraba; nakwera malire kunka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;

7 nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele;

8 nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndikoYerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.

9 Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba paphiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumizinda ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka kuBaala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.

10 Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna;

11 natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.

12 Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.

13 Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.

14 Ndipo Kalebe anaingitsako ana aamuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.

15 Nakwera komweko kunka kwa nzika za Debiri; koma kale dzina la Debiri ndilo Kiriyati-Sefere.

16 Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wake.

17 Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake.

18 Ndipo kunali, m’mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pabulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?

19 Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.

20 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.

21 Ndipo mizinda ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru;

22 ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;

23 ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Itinani;

24 Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;

25 ndi Hazori-Hadata, ndi Keriyoti-Hezironi, ndiwo Hazori;

26 Amama ndi Sema ndi Molada;

27 ndi Hazara-Gada, ndi Hesimoni, ndi Betepeleti;

28 ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya;

29 Baala, ndi Iyimu, ndi Ezemu;

30 ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horoma;

31 ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana;

32 ndi Lebaoti, ndi Silihimu, ndi Aini ndi Rimoni; mizinda yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi midzi yao.

33 Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;

34 ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu;

35 Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;

36 ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yao.

37 Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi;

38 ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele;

39 Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni;

40 ndi Kaboni, ndi Lahamasi, ndi Kitilisi;

41 ndi Gederoti, Betedagoni, ndi Naama, ndi Makeda; mizinda khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.

42 Libina ndi Eteri ndi Asani;

43 ndi Ifuta ndi Asina ndi Nezibu;

44 ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao.

45 Ekeroni pamodzi ndi mizinda yake ndi midzi yao;

46 kuyambira ku Ekeroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodi, pamodzi ndi midzi yao.

47 Asidodi, mizinda yake ndi midzi yake; Gaza, mizinda yake ndi midzi yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.

48 Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko;

49 ndi Dana, ndi Kiriyati-Sana, ndiwo Debiri;

50 ndi Anabu, ndi Esitemowa, ndi Animu;

51 ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; mizinda khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.

52 Arabu, ndi Duma, ndi Esani;

53 ndi Yanimu, ndi Betetapuwa, ndi Afeka;

54 ndi Humata, ndi Kiriyati-Ariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziyori; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao.

55 Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta;

56 ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa;

57 Kaini, Gibea ndi Timna; mizinda khumi pamodzi ndi midzi yao.

58 Halahulu, Betezuri, ndi Gedori,

59 ndi Maarati, ndi Betanoti, ndi Elitekoni; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.

60 Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yao.

61 M’chipululu, Betaraba, Midini, ndi Sekaka;

62 ndi Nibisani, ndi Mzinda wa Mchere, ndi Engedi; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.

63 Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m’mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/15-78dfdf7a9db0a30e2ff94f2ed0cb0d32.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 16

Malire a Efuremu

1 Ndipo gawo la ana a Yosefe linatuluka kuchokera ku Yordani ku Yeriko, ku madzi a Yeriko kum’mawa, kuchipululu, nakwera kuchokera ku Yeriko kunka kumapiri ku Betele;

2 natuluka ku Betele kunka ku Luzi, napitirira kunka ku malire a Aariki, ku Ataroti;

3 natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja.

4 Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu analandira cholowa chao,

5 Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum’mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda;

6 natuluka malire kumadzulo ku Mikametati kumpoto; nazungulira malire kum’mawa kunka ku Taanatisilo, naupitirira kum’mawa kwake kwa Yanowa:

7 natsika kuchokera ku Yanowa, kunka ku Ataroti, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, natuluka ku Yordani.

8 Kuyambira ku Tapuwa malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuremu monga mwa mabanja ao;

9 pamodzi ndi mizinda adaipatulira ana a Efuremu pakati pa cholowa cha ana a Manase, mizinda yonse pamodzi ndi midzi yao.

10 Ndipo sanaingitse Akanani akukhala mu Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/16-c28510d9b513a4592e152d301ab60b4c.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 17

Malire a Manase

1 Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.

2 Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiyezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriele, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao.

3 Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana aamuna koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

4 Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.

5 Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Giliyadi ndi Basani lokhala tsidya lija la Yordani:

6 popeza ana aakazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake aamuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala.

7 Ndipo malire a Manase anayambira ku Asere, kunka ku Mikametati, wokhala chakuno cha Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapuwa.

8 Dziko la Tapuwa linali la Manase; koma Tapuwa mpaka malire a Manase linakhala la ana a Efuremu.

9 Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; mizinda iyi inakhala ya Efuremu pakati pa mizinda ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndi matulukiro ake anali kunyanja;

10 kumwera nkwa Efuremu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ake ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Asere, ndi kum’mawa anakomana ndi Isakara.

11 Ndipo mu Isakara ndi mu Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu.

12 Koma ana a Manase sanathe kuingitsa a m’mizinda aja, popeza Akanani anafuna kukhala m’dziko lija.

13 Ndipo kunali pamene ana a Israele atakula mphamvu anasonkhetsa Akanani osawaingitsa onse.

14 Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?

15 Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m’dziko la Aperizi ndi la Arefaimu; akakucheperani malo kuphiri la Efuremu.

16 Ndipo ana a Yosefe anati, Ku phiriko sikudzatifikira; ndipo Akanani onse akukhala m’dziko la chigwa ali nao magaleta achitsulo, iwo akukhala mu Beteseani, ndi midzi yake ndi iwo omwe akukhala m’chigwa cha Yezireele.

17 Ndipo Yoswa ananena kwa iwo a m’nyumba ya Yosefe, kwa Efuremu ndi Manase, ndi kuti, Inu ndinu anthu aunyinji, muli nayo mphamvu yaikulu; simudzakhala nalo gawo limodzi lokha;

18 koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi matulukiro ake adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magaleta achitsulo, angakhale ali amphamvu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/17-30824d478415cf4fe846c84c28ca4e27.mp3?version_id=1068—