Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 23

Oletsedwa ku msonkhano wa Yehova

1 Munthu wofulika kapena woduka chiwalo chaumuna, asalowe m’msonkhano wa Yehova.

2 Mwana wa m’chigololo asalowe m’msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m’msonkhano wa Yehova.

3 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m’msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m’msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;

4 popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m’njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.

5 Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.

6 Musawafunira mtendere, kapena chowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.

7 Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m’dziko lake.

8 Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m’msonkhano wa Yehova.

9 Nkhondo yanu ikatuluka pa adani anu, mudzisunge kusachita choipa chilichonse.

10 Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera chifukwa chochitika usiku, azituluka kunja kwa chigono, asalowe pakati pa chigono;

11 koma kudzali pofika madzulo, asambe m’madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono.

12 Mukhale nao malo kunja kwa chigono kumene muzimukako kuthengo;

13 nimukhale nacho chokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe nacho, ndi kutembenuka ndi kufotsera chakutulukacho;

14 popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.

Za akapolo opulumuka, za achigololo, za okongoletsa mopindulitsa

15 Musamapereka kwa mbuye wake kapolo wopulumuka kwa mbuye wake kuthawira kwa inu;

16 akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m’mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.

17 Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana aakazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana aamuna a Israele.

18 Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m’nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

19 Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa.

20 Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m’dziko limene mulowamo kulilandira.

21 Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.

22 Koma mukapanda kulonjeza chowinda, mulibe kuchimwa.

23 Chotuluka pa milomo yanu muchisamalire ndi kuchichita; monga munalonjezera Yehova Mulungu wanu, chopereka chaufulu munachilonjeza pakamwa panu.

24 Mukalowa m’munda wampesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni; koma musaika kanthu m’chotengera chanu.

25 Mukalowa m’tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi chisenga tirigu wachilili wa mnansi wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/23-fce006c3bc394350bd23b083770edc37.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 24

Za kalata ya chilekaniro, chikole, kuba munthu, khate

1 Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m’dzanja lake, ndi kumtulutsa m’nyumba mwake.

2 Ndipo atatuluka m’nyumba mwake, amuke nakhale mkazi wa mwamuna wina.

3 Ndipo akamuda mwamuna wachiwiriyo, nakamlemberanso kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m’dzanja lake, nakamtulutsa m’nyumba mwake; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wake;

4 pamenepo mwamuna woyamba anamchotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wake, atadetsedwa iye; pakuti ichi ndi chonyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamachimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.

5 Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke ku nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.

6 Munthu asalandire chikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo chikole moyo wa munthu.

7 Akampeza munthu waba mbale wake wina wa ana a Israele, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzichotsa choipacho pakati panu.

8 Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita.

9 Kumbukirani chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriyamu panjira, potuluka inu m’dziko la Ejipito.

Za kukongoletsa

10 Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iliyonse, musamalowa m’nyumba mwake kudzitengera chikole chake.

11 Muime pabwalo, ndi munthu amene umkongoletsayo azituluka nacho chikolecho kwa inu muli pabwalo.

12 Ndipo akakhala munthu waumphawi musagone muli nacho chikole chake;

13 polowa dzuwa mumbwezeretu chikolecho, kuti agone m’chovala chake, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Zachifundo pa antchito aumphawi, alendo ndi amasiye

14 Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m’dziko mwanu, m’midzi mwanu.

15 Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo.

16 Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.

17 Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye;

18 koma muzikumbukira kuti munali akapolo mu Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi.

19 Mutasenga dzinthu zanu m’munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m’mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m’ntchito zonse za manja anu.

20 Mutagwedeza mtengo wanu waazitonamusayesenso nthambi mutatha nazo; akhale a mlendo, a mwana wamasiye, ndi a mkazi wamasiye.

21 Mutatchera m’munda wanu wampesa, musakunkha pambuyo panu; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye.

22 Ndipo muzikumbukira kuti munali akapolo m’dziko la Ejipito; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/24-132d4a323cbbc85ca8a5a33a5edf2133.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 25

Za makwapulidwe a wolakwa

1 Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.

2 Ndipo kudzali, wochita choipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pake, amwerengere zofikira choipa chake.

3 Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.

4 Musamapunamiza ng’ombe popuntha tirigu.

Za kukwatibwa mkazi ndi mlamu wake

5 Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake.

6 Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lake la mbale wake wakufayo, kuti dzina lake lisafafanizidwe mu Israele.

7 Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina mu Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.

8 Pamenepo akulu a mzinda wake amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga;

9 pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake.

10 Ndipo azimutcha dzina lake mu Israele, Nyumba ya uje anamchotsa nsapato.

11 Akalimbana wina ndi mnzake, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wake m’dzanja la wompandayo, nakatulutsa dzanja lake, ndi kumgwira kudzivalo;

12 pamenepo muzidula dzanja lake; diso lanu lisamchitire chifundo.

13 Musamakhala nayo m’thumba mwanu miyala ya miyeso iwiri, waukulu ndi waung’ono.

14 Musamakhala nayo m’nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukulu ndi waung’ono.

15 Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu achuluke m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

16 Pakuti onse akuchita zinthu izi, onse akuchita chisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

Amaleke afafanizike

17 Kumbukirani chochitira inu Amaleke panjira, potuluka inu mu Ejipito;

18 kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofooka akutsala m’mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaope Mulungu.

19 Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu, kuti muzifafaniza chikumbutso cha Amaleke pansi pa thambo; musamaiwala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/25-ea713d769bfa1dc310612fe6ab3579d2.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 26

Chopereka cha zipatso zoyamba

1 Ndipo kudzali, utakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, ndipo mwachilandira ndi kukhala m’mwemo;

2 kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.

3 Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m’masiku awa, ndi kunena naye, Ndivomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m’dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili.

4 Ndipo wansembe alandire dengu m’manja mwanu, ndi kuuika paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu.

5 Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang’ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;

6 koma Aejipito anatichitira choipa, natizunza, natisenza ntchito yolimba.

7 Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi ntchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;

8 ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukulu, ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa;

9 ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

10 Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu;

11 ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.

Limodzi la magawo khumi chaka chachitatu

12 Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse chaka chachitatu, ndicho chaka chogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m’midzi mwanu, ndi kukhuta.

13 Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndachotsa zopatulika m’nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwire malamulo anu, kapena kuwaiwala.

14 Sindinadyeko m’chisoni changa, kapena kuchotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndachita monga mwa zonse munandilamulira ine.

15 Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m’mwamba, ndipo dalitsani anthu anu Israele, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

16 Lero lino Yehova Mulungu wanu akulamulirani kuchita malemba ndi maweruzo awa; potero muzimvera ndi kuwachita ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

17 Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m’njira zake, ndi kusunga malemba ake, ndi malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi kumvera mau ake.

18 Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu akeake a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ake onse;

19 kuti akukulitseni koposaamitunduonse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/26-55cecf4c552c358fdb670636916d9f18.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 27

Za kuutsa miyala ya chikumbutso ataoloka Yordani

1 Ndipo Mose ndi akulu a Israele anauza anthu, nati, Sungani malamulo onse ndikuuzani lero.

2 Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikulu, ndi kuimata ndi njeresa;

3 ndipo mulemberepo mau onse a chilamulo ichi, mutaoloka; kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu.

4 Ndipo kudzali, mutaoloka Yordani, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m’phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa.

5 Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo pangizo chachitsulo.

6 Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu;

7 ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

8 Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a chilamulo ichi mopenyeka bwino.

9 Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israele wonse, ndi kuti, Khalani chete, imvanitu, Israele; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.

10 Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino.

Mdalitso ndi temberero ku Gerizimu ndi Ebala

11 Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti,

12 Aimirire awa paphiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.

13 Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.

14 Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israele, ndi mau omveka.

15 Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m’malo a m’tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti,Amen.

16 Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

17 Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

18 Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m’njira. Ndi anthu onse anene, Amen.

19 Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.

20 Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

21 Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iliyonse. Ndi anthu onse anene, Amen.

22 Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. Ndi anthu onse anene, Amen.

23 Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

24 Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m’tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.

25 Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.

26 Wotembereredwa iye wosavomereza mau a chilamulo ichi kuwachita. Ndi anthu onse anene, Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/27-b29c8c4ac6a5289845274072baee4c4c.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 28

Madalitso pa kumvera kwao

1 Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a padziko lapansi;

2 ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

3 Mudzakhala odala m’mzinda, ndi odala kubwalo.

4 Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

5 Lidzakhala lodala dengu lanu, ndi choumbiramo mkate wanu.

6 Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu.

7 Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.

8 Yehova adzakulamulirani dalitso m’nkhokwe zanu, ndi m’zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

9 Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m’njira zake.

10 Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.

11 Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m’zipatso za thupi lanu, ndi m’zipatso za zoweta zanu, ndi m’zipatso za nthaka yanu, m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.

12 Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m’nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

13 Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita;

14 osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.

Matemberero pa kusamvera kwao

15 Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.

16 Mudzakhala otembereredwa m’mzinda, ndi otembereredwa pabwalo.

17 Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu.

18 Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

19 Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu.

20 Yehova adzakutumizirani temberero, chisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukatulutsa dzanja lanu kuchita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika msanga, chifukwa cha zochita inu zoipa, zimene wandisiya nazo.

21 Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.

22 Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.

23 Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko lili pansi panu ngati chitsulo.

24 Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale fumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kuchokera kumwamba, kufikira mwaonongeka.

25 Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.

26 Ndipo mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi zilombo zonse za padziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa.

27 Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.

28 Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima;

29 ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.

30 Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m’mwemo; mudzaoka munda wampesa, osalawa zipatso zake.

31 Adzapha ng’ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.

32 Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m’maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m’dzanja lanu.

33 Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;

34 nimudzakhala oyeruka chifukwa chomwe muchiona ndi maso anu.

35 Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.

36 Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.

37 Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.

38 Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang’ono; popeza dzombe lidzazitha.

39 Mudzaoka m’minda yampesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wake, kapena kutchera mphesa zake, popeza mbozi zidzaidya.

40 Mudzakhala nayo mitengo yaazitonam’malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka.

41 Mudzabala ana aamuna ndi aakazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.

42 Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe.

43 Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera.

44 Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mchira.

45 Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake ndi malemba ake amene anakulamulirani;

46 ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa, nthawi zonse.

47 Popeza simunatumikire Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse;

48 chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.

49 Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;

50 mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamchitira chifundo mwana;

51 ndipo adzadya zipatso za ng’ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng’ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.

52 Ndipo adzakuzingani m’midzi mwanu monse, kufikira adzagwa malinga anu aatali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m’dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m’midzi mwanu monse, m’dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

53 Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.

54 Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, diso lake lidzaipira mbale wake, ndi mkazi wa pa mtima wake, ndi ana ake otsalira;

55 osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ake alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu monse.

56 Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi;

57 ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m’tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu.

58 Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m’buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu;

59 Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.

60 Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Ejipito, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.

61 Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m’buku la chilamulo ichi, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.

62 Ndipo mudzatsala anthu pang’ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m’mwamba; popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu.

63 Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.

64 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.

65 Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m’maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.

66 Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzachita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.

67 M’mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! Ndi madzulo mudzati, Mwezi utafika m’mawa! Chifukwa cha mantha a m’mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi chifukwa cha zopenya maso anu zimene mudzazipenya.

68 Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, panjira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/28-0ef2c8a5fb8f498b65cdcefff9a39fc8.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 29

Mulungu abwereza kupangana nao

1 Awa ndi mau achipanganochimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m’dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao mu Horebu.

2 Ndipo Mose anaitana Israele wonse, nati nao, Munapenya inu zonse zimene Yehova anachitiraFarao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse, pamaso panu m’dziko la Ejipito;

3 mayesero aakuluwa maso anu anawapenya, zizindikirozo, ndi zozizwa zazikulu zija;

4 koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.

5 Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m’chipululu; zovala zanu sizinathe pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinathe pa phazi lanu.

6 Simunadye mkate, simunamwe vinyo kapena chakumwa cholimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

7 Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, anatuluka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;

8 ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale cholowa chao cha Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase.

9 Chifukwa chake sungani mau a chipangano ichi ndi kuwachita, kuti muchite mwanzeru m’zonse muzichita.

10 Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mafuko anu, akulu anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israele,

11 makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;

12 kuti mulowe chipangano cha Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lake, limene Yehova Mulungu wanu achita ndi inu lero lino;

13 kuti adzikhazikire inu, mtundu wake wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo.

14 Koma sindichita chipangano ichi ndi lumbiro ili ndi inu nokha;

15 komanso ndi iye wakuimirira pano nafe lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndiponso ndi iye wosakhala pano nafe lero lino.

16 Pakuti mudziwa chikhalidwe chathu m’dziko la Ejipito, ndi kuti tinapyola pakati paamitunduamene munawapyola;

17 ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala,silivandi golide, zokhala pakati pao;

18 kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.

19 Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m’mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;

20 Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m’buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.

21 Ndipo Yehova adzamsiyanitsa ndi mafuko onse a Israele ndi kumchitira choipa, monga mwa matemberero onse a chipangano cholembedwa m’buku ili la chilamulo.

22 Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wochokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi, Yehova awadwalitsa nazo.

23 Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndisulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m’mkwiyo wake ndi ukali wake;

24 inde amitundu onse adzati, Yehova anachitira dziko ili chotero chifukwa ninji? Nchiyani kupsa mtima kwakukulu kumene?

25 Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m’dziko la Ejipito;

26 napita natumikira milungu ina, naigwadira, milungu imene sanaidziwe, imene sanawagawire;

27 chifukwa chake Yehova anapsera mtima dziko ili kulitengera temberero lonse lolembedwa m’buku ili.

28 Ndipo Yehova anawazula m’nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi mu ukali waukulu, nawaponya m’dziko lina, monga lero lino.

29 Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti tichite mau onse a chilamulo ichi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/29-33f39eda6e94389fa32c2383536aac29.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 30

Mulungu alonjeza kuwalanditsa akalapa atachimwa

1 Ndipo kudzakhala, zikakugwerani zonsezi, mdalitso ndi temberero, ndinaikazi pamaso panu, ndipo mukazikumbukira mumtima mwanu mwaamitunduonse, amene Yehova Mulungu wanu anakupirikitsiraniko;

2 nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mau ake, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse;

3 pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.

4 Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko;

5 ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m’dziko lidakhala laolao la makolo anu, nilidzakhala lanulanu; ndipo adzakuchitirani zokoma, ndi kukuchulukitsani koposa makolo anu.

6 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.

7 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani.

8 Pamenepo mutembenuke ndi kumvera mau a Yehova, ndi kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino.

9 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakuchulukitsirani ntchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukuchitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu;

10 ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ake ndi malemba ake olembedwa m’buku la chilamulo ichi; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

11 Pakuti lamulo ili ndikuuzani lero lino, silikukanikani kulizindikira, kapena silikhala kutali.

12 Silikhala m’mwamba, kuti mukati, Adzatikwerera m’mwamba ndani, ndi kubwera nalo kwa ife, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite?

13 Ndipo silikhala tsidya la nyanja, kuti mukati, Adzatiolokera ndani tsidya la nyanja, ndi kutitengera ili, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite?

14 Pakuti mauwa ali pafupifupi ndi inu, m’kamwa mwanu, ndi m’mtima mwanu, kuwachita.

15 Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa;

16 popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m’dziko limene mulowako kulilandira.

17 Koma mukatembenukira mtima wanu, osamvera inu, nimukacheteka, ndi kugwadira milungu ina ndi kuitumikira;

18 ndikulalikirani inu lero, kuti mudzatayika ndithu, masiku anu sadzachuluka m’dziko limene muolokera Yordani kulowamo kulilandira.

19 Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;

20 kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/30-e69e4a14f58e9ffff03c49e146de16af.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 31

Yoswa adzalowa m’malo a Mose

1 Ndipo Mose anamuka nanena mau awa kwa Israele wonse,

2 nati nao, Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lero lino; sindikhozanso kutuluka ndi kulowa; ndipo Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordani uyu.

3 Yehova Mulungu wanu ndiye adzaoloka pamaso panu, Iye ndiye adzaonongaamitunduawo pamaso panu, ndipo mudzawalandira. Yoswa ndiye adzakutsogolerani pooloka, monga ananena Yehova.

4 Ndipo Yehova adzawachitira monga anachitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga.

5 Yehova akadzawapereka pamaso panu, muziwachitira monga mwa lamulo lonse ndakuuzani.

6 Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.

7 Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israele wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m’dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.

8 Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.

Pakutha zaka 7 zilizonse azilalikira chilamulocho

9 Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamulalikasa la chipanganola Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele.

10 Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m’chaka chakulekerera, pachikondwerero cha Misasa;

11 pakufika Israele wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m’malo amene adzasankha, muzilalikira chilamulo ichi pamaso pa Israele wonse, m’makutu mwao.

12 Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono, ndi mlendo wokhala m’midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi;

13 ndi kuti ana ao osadziwa amve, naphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu.

Yoswa asenza udindo wake

14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m’chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m’chihema chokomanako.

15 Ndipo Yehova anaoneka m’chihema, m’mtambo njo; ndipo mtambo njo unaima pa khomo la chihema.

16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.

17 Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?

18 Koma Ine ndidzabisatu nkhope yanga tsiku lija chifukwa cha zoipa zonse adazichita; popeza anadzitembenukira milungu ina.

19 Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israele iyi; muiike m’kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indichitire mboni yotsutsa ana a Israele.

20 Pakuti nditakalowetsa awa m’dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kuthyola chipangano changa.

21 Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m’kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m’dziko limene ndinalumbira.

22 Potero Mose analembera nyimboyi tsiku lomweli, naiphunzitsa ana a Israele.

23 Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m’dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.

24 Ndipo kunali, Mose atatha kulembera mau a chilamulo ichi m’buku, kufikira atalembera onse,

25 Mose anauza Alevi akunyamulalikasa la chipanganola Yehova, ndi kuti,

26 Landirani buku ili la chilamulo, nimuliike pambali pa likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.

27 Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine!

28 Ndisonkhanitsire akulu onse a mafuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m’makutu mwao, ndi kuchititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.

29 Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m’njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.

30 Ndipo Mose ananena mau a nyimbo iyi m’makutu mwa msonkhano wonse wa Israele, kufikira adatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/31-f7f71b085bb57e8260aceabdd5902ca0.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 32

Nyimbo adailemba Mose

1 Kumwamba kutchere khutu,

ndipo ndidzanena;

ndi dziko lapansi limve mau a m’kamwa mwanga.

2 Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula;

maneno anga agwe ngati mame;

ngati mvula yowaza pamsipu,

ndi monga madontho a mvula pazitsamba.

3 Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova.

Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.

4 Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro;

pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo;

Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo;

Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.

5 Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema nchao;

iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.

6 Kodi mubwezera Yehova chotero,

anthu inu opusa ndi opanda nzeru?

Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu;

anakulengani, nakukhazikitsani?

7 Kumbukirani masiku akale,

zindikirani zaka za mibadwo yambiri;

funsani atate wanu, adzakufotokozerani;

akulu anu, adzakuuzani.

8 Pamene Wam’mwambamwamba anagawiraamitunducholowa chao,

pamene anagawa ana a anthu,

anaika malire a mitundu ya anthu,

monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.

9 Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake;

Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.

10 Anampeza m’dziko la mabwinja,

m’chipululu cholira chopanda kanthu;

anamzinga, anamlangiza,

anamsunga ngati kamwana ka m’diso.

11 Monga mphungu ikasula chisa chake,

nikapakapa pa ana ake,

Iye anayala mapiko ake, nawalandira,

nawanyamula pa mapiko ake.

12 Yehova yekha anamtsogolera,

ndipo palibe mulungu wachilendo naye.

13 Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi,

ndipo anadya zipatso za m’minda;

namyamwitsa uchi wa m’thanthwe,

ndi mafuta m’mwala wansangalabwe;

14 mafuta a mkaka wang’ombe, ndi mkaka wankhosa,

ndi mafuta a anaankhosa,

ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde,

ndi impso zonenepa zatirigu;

ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa.

15 Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira;

wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta;

pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga,

napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.

16 Anamchititsa nsanje ndi milungu yachilendo,

anautsa mkwiyo wake ndi zonyansa.

17 Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai;

milungu yosadziwa iwo,

yatsopano yofuma pafupi,

imene makolo anu sanaiope.

18 Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,

mwaiwala Mulungu amene anakulengani.

19 Ndipo Yehova anachiona, nawanyoza,

pakuipidwa nao ana ake aamuna, ndi akazi.

20 Ndipo Iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga,

ndidzaona kutsiriza kwao;

popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira,

ana osakhulupirika iwo.

21 Anautsa nsanje yanga ndi chinthu chosati Mulungu;

anautsa mkwiyo wanga ndi zopanda pake zao.

Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu;

ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.

22 Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga,

utentha kumanda kunsi

ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake,

nuyatsa maziko a mapiri.

23 Ndidzawaunjikira zoipa;

ndidzawathera mivi yanga.

24 Adzaonda nayo njala

adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa;

ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo,

ndi ululu wa zokwawa m’fumbi.

25 Pabwalo lupanga lidzalanda,

ndi m’zipinda mantha;

lidzaononga mnyamata ndi namwali,

woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.

26 Ndinati, Ndikadawauzira ndithu,

ndikadafafaniza chikumbukiro chao mwa anthu.

27 Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani,

angayese molakwa outsana nao,

anganene, Lakwezeka dzanja lathu,

ndipo Yehova sanachite ichi chonse.

28 Popeza iwo ndiwo mtundu wa anthu wosowa uphungu konse,

ndipo alibe chidziwitso.

29 Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ichi,

akadasamalira chitsirizo chao!

30 Mmodzi akadapirikitsa zikwi,

awiri akadathawitsa zikwi khumi,

akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao,

akadapanda kuwapereka Yehova.

31 Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu,

oweruza a pamenepo ndiwo adani athu.

32 Pakuti mpesa wao ndiwo wa ku Sodomu,

ndi wa m’minda ya ku Gomora;

mphesa zao ndizo mphesa zandulu,

matsangwi ao ngowawa.

33 Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka,

ndi ululu waukali wa mphiri.

34 Kodi sichisungika ndi Ine,

cholembedwa chizindikiro mwa chuma changa chenicheni?

35 Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe,

pa nyengo ya kuterereka phazi lao;

pakuti tsiku la tsoka lao layandika,

ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.

36 Popeza Yehova adzaweruza anthu ake,

nadzachitira nsoni anthu ake;

pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha,

wosatsala womangika kapena waufulu.

37 Pamenepo adzati, Ili kuti milungu yao,

thanthwe limene anathawirako?

38 Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera,

nimwa vinyo wa nsembe yao yothira?

Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu.

39 Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye,

ndipo palibe mulungu koma Ine;

ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo,

ndikantha, ndichizanso Ine;

ndipo palibe wakulanditsa m’dzanja langa.

40 Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba,

ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha,

41 ndikanola lupanga langa lonyezimira,

ndi dzanja langa likagwira chiweruzo;

ndidzabwezera chilango ondiukira,

ndi kulanga ondida.

42 Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi,

ndi lupanga langa lidzalusira nyama;

ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa,

ndi mutu wachitsitsi wa mdani.

43 Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake;

adzalipsira mwazi wa atumiki ake,

adzabwezera chilango akumuukira,

nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.

44 Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m’makutu mwa anthu, iye, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

45 Ndipo Mose anatha kunena mau awa onse kwa Israele wonse;

46 nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi.

47 Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m’dziko limene muolokera Yordani, kulilandira.

Mulungu auza Mose akwere m’phiri la Nebo

48 Ndipo Yehova ananena ndi Mose tsiku lomweli, ndi kuti,

49 Kwera m’phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m’dziko la Mowabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israele likhale laolao;

50 nufe m’phiri m’mene ukweramo, nuitanidwe kunka kwa anthu a mtundu wako; monga Aroni mbale wako anafa m’phiri la Hori, naitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake;

51 popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m’chipululu cha Zini, popeza simunandipatule Ine pakati pa ana a Israele.

52 Pakuti udzapenya dzikoli pandunji pako; koma osalowako ku dziko limene ndipatsa ana a Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/32-64b4de788f5560fb41ca5eb1e94c8e38.mp3?version_id=1068—