Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 13

Achenjere nao owanyenga kuwapembedzetsa mafano

1 Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani chizindikiro kapena chozizwa;

2 ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu ina, imene simunaidziwe, ndi kuitumikira;

3 musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

4 Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.

5 Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Ejipito, nakuombolani m’nyumba ya ukapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.

6 Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m’tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;

7 ndiyo milungu ya mitundu ya anthu akuzungulira inu, akukhala pafupi pali inu, kapena akukhala patali pali inu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero ena a dziko lapansi;

8 musamavomerezana naye, kapena kumvera iye; diso lanu lisamchitire chifundo, kapena kumleka, kapena kumbisa;

9 koma muzimupha ndithu; liyambe dzanja lanu kukhala pa iye kumupha, ndi pamenepo dzanja la anthu onse.

10 Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukuchetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Ejipito, m’nyumba ya ukapolo.

11 Kuti Israele yense amve, ndi kuopa, ndi kusaonjeza kuchita choipa chotere chonga ichi pakati pa inu.

12 Ukamva za umodzi wa mizinda yanu, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani kukhalako, ndi kuti,

13 Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m’mzinda mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwe;

14 pamenepo muzifunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa; ndipo taonani, chikakhala choona, chatsimikizika chinthuchi, kuti chonyansa chotere chachitika pakati pa inu;

15 muzikanthatu okhala m’mzinda muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuononga konse, ndi zonse zili m’mwemo, ng’ombe zake zomwe, ndi lupanga lakuthwa.

16 Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mzinda, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.

17 Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;

18 pakumvera inu mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino, kuchita zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/13-6ddffa2d6d727e49c0b84354adcf0191.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 14

Za nyama yodyedwa ndi yosadyedwa

1 Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pamaso chifukwa cha akufa.

2 Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope padziko lapansi.

Za nyama zodyeka ndi zosadyeka ndi zakufa zodetsa munthu

3 Musamadya chonyansa chilichonse.

4 Nyamazi muyenera kumadya ndi izi: ng’ombe, nkhosa, ndi mbuzi,

5 ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.

6 Ndipo nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya.

7 Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda:ngamira, ndi kalulu, ndi mbira, popeza zibzikula, koma zosagawanika chiboda, muziyese zodetsa;

8 ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.

9 Mwa zonse zili m’madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba, zimenezi muyenera kumadya;

10 koma zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa.

11 Mbalame zosadetsa zonse muyenera kumadya.

12 Koma izi ndi zimene simuyenera kumadya: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi,

13 ndi kamtema, ndi mphamba, ndi muimba monga mwa mtundu wake;

14 ndi khwangwala aliyense monga mwa mtundu wake;

15 ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi monga mwa mtundu wake;

16 ndi nkhutukutu, ndi manchichi, ndi tsekwe;

17 ndi vuwo, ndi dembo, ndi nswankhono;

18 ndi indwa, ndi chimeza, monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme.

19 Ndipo zokwawa zonse zakuuluka muziyesa zonyansa; musamazidya.

20 Mbalame zonse zosadetsa muyenera kumadya.

21 Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m’mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.

Za limodzi mwa magawo khumi

22 Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka.

23 Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m’malo m’mene asankhamo Iye, kukhalitsamo dzina lake; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng’ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.

24 Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simungathe kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lake, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;

25 pamenepo mulisinthe ndalama, ndi kumanga ndalama ikhale m’dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;

26 ndipo mugule ndi ndalamazo chilichonse moyo wanu ukhumba, ng’ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena chakumwa cholimba, kapena chilichonse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.

27 Koma Mlevi wokhala m’mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.

28 Pakutha pake pa zaka zitatu muzitulutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za chaka icho, ndi kuwalinditsa m’mudzi mwanu;

29 ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m’mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/14-d5027b84152eeaf612cc5914454236ba.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 15

Za chaka cha chilekerero

1 Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri pakhale chilekerero.

2 Chilekererocho ndichi: okongoletsa onse alekerere chokongoletsa mnansi wake; asachifunse kwa mnansi wake, kapena mbale wake; popeza analalikira chilekerero cha Yehova.

3 Muyenera kuchifunsa kwa mlendo; koma chanu chilichonse chili ndi mbale wanu, dzanja lanu lichilekerere;

4 ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu;

5 chokhachi mumvere chimverere mau a Yehova Mulungu wanu, kuti musamalire kuchita malamulo awa onse amene ndikuuzani lero lino.

6 Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monga ananena nanu; ndipo mudzakongoletsaamitunduambiri, osakongola nokha; nimudzachita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzachita ufumu pa inu.

Za aumphawi ndi akapolo

7 Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wina wa abale anu, mu umodzi wa midzi yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi;

8 koma muzimtansira dzanja lanu ndithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwake, monga umo amasowa.

9 Dzichenjerani, mungakhale mau opanda pake mumtima mwanu, ndi kuti, Chayandika chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka cha chilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale tchimo.

10 Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m’zonse muikapo dzanja lanu.

11 Popeza waumphawi salekana m’dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m’dziko mwanu.

Lamulo la pa kapolo

12 Mukagula mbale wanu, Muhebri wamwamuna kapena Muhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi chimodzi; koma chaka chachisanu ndi chiwiri umlole achoke kwanu waufulu.

13 Ndipo pomlola iwe achoke kwanu waufulu, musamamlola achoke wopanda kanthu;

14 mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za popondera mphesa, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.

15 Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m’dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.

16 Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituluka kuchoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;

17 pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m’khutu mwake, kulikanikiza ndi chitseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzichitanso momwemo ndi adzakazi anu.

18 Musamayesa nchosautsa, pomlola akuchokereni waufulu; popeza anakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi monga wolipidwa wakulandira chowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m’zonse muzichita.

Za nyama zoyamba kubadwa

19 Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng’ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa ntchito yoyamba kubadwa mwa ng’ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.

20 Muzidye chaka ndi chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m’malo amene Yehova adzasankha, inu ndi a m’banja mwanu.

21 Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.

22 Muidye m’mudzi mwanu; odetsa ndi oyera aidye chimodzimodzi, monga mphoyo ndi nswala.

23 Mwazi wake wokha musamadya; muuthire pansi ngati madzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/15-bcd08cdc637bff389094e25da9da2980.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 16

Zikondwerero za Paska, za Masabata, ndi za Misasa

1 Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanuPaska; popeza m’mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m’dziko la Ejipito usiku.

2 Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, ya nkhosa ndi ya ng’ombe, m’malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lake.

3 Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m’dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m’dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.

4 Ndipo m’malire mwanu monse musaoneke chotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m’mawa.

5 Simuyenera kuphera nsembe ya Paska m’midzi yanu iliyonse, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani;

6 koma pamalo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsapo dzina lake, pamenepo muphere nsembe ya Paska, madzulo, polowa dzuwa, nyengo ya kutuluka inu mu Ejipito.

7 Ndipo muiphike ndi kuidya m’malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha; koma m’mawa mwake mubwerere kunka ku mahema anu.

8 Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda chotupitsa; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira ntchito pamenepo.

9 Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kusenga tirigu wachilili.

10 Ndipo muchitire Yehova Mulungu wanu chikondwerero cha Masabata, ndiwo msonkho waufulu wa dzanja lanu, umene mupereke monga Yehova Mulungu wanu akudalitsani.

11 Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m’mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m’malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.

12 Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo mu Ejipito; musamalire kuchita malemba awa.

13 Mudzichitirechikondwerero cha Misasamasiku asanu ndi awiri, mutasunga za padwale ndi za mopondera mphesa;

14 nimukondwere m’madyerero mwanu, inu, ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye okhala m’mudzi mwanu.

15 Masiku asanu ndi awiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m’malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m’zipatso zanu zonse, ndi m’ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.

16 Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m’malo amene Iye adzasankha, katatu m’chaka; pachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;

17 apereke yense monga mwa mphatso ya m’dzanja lake, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

Za oweruza milandu

18 Mudziikire oweruza ndi akapitao m’midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.

19 Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, ndi kuipisa mau a olungama.

20 Chilungamo, chilungamo ndicho muzichitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

21 Musazike kwa inu nokha mzati wa Ashera, wa mtengo uliwonse, pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira.

22 Ndipo musamadziutsira choimiritsa chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu adana nacho.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/16-997a0d359e10e188987c9099fd406a04.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 17

1 Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng’ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu.

2 Akapeza pakati panu, m’mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwirachipanganochake,

3 nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;

4 ndipo akakuuzani, nimudamva, pamenepo muzifunsira, ndipo taonani, chikakhala choonadi, choti nzenizeni, chonyansachi chachitika mu Israele;

5 pamenepo mutulutse mwamunayo kapena mkaziyo, anachita choipacho, kunka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe.

6 Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi.

7 Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse. Potero muzichotsa choipacho pakati panu.

8 Ukakukanikani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo milandu yakutengana m’midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kunka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;

9 nimufike kwa ansembe, Alevi, ndi kwa woweruza wa m’masiku awo; nimufunsire; ndipo adzakufotokozerani maweruzidwe ake.

10 Ndipo muchite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kuchita monga mwa zonse akulangizanizi.

11 Monga momwe anena malamulo akulangizani, ndi monga mwa chiweruzo akufotokozerani muchite; mau akufotokozerani musawapatukire kulamanja kapena kulamanzere.

12 Koma munthu wakuchita modzikuza, osamvera wansembe wokhala chilili kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo muchotse choipacho kwa Israele.

13 Ndipo anthu onse adzamva ndi kuchita mantha, osachitanso modzikuza.

Za kusankha mfumu ndi zomuyenera

14 Mutakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanulanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, mongaamitunduonse akutizinga;

15 mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha; wina pakati pa abale anu mumuike mfumu yanu; simuyenera kudziikira mlendo, wosakhala mbale wanu.

16 Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.

17 Ndipo asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake; kapena asadzichulukitsire kwambirisilivandi golide.

18 Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m’buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi;

19 ndipo azikhala nacho, nawerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mau onse a chilamulo ichi ndi malemba awa, kuwachita;

20 kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, mu ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/17-22c08d236d46ed9c611a617f5e3c0885.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 18

Zoyenera ansembe ndi Alevi

1 Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake.

2 Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao.

3 Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng’ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m’masaya ndi chifu.

4 Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.

5 Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mafuko anu onse, aimirire natumikire m’dzina la Yehova, iwo ndi ana ao aamuna kosalekeza.

6 Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina mu Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;

7 pamenepo azitumikira m’dzina la Yehova Mulungu wake, monga amachita abale ake onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.

8 Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.

Mulungu aipidwa nao anyanga ndi obwebweta ndi onse otere

9 Mutakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa zaamitunduaja.

10 Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.

11 Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.

12 Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.

13 Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.

14 Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero.

Lonjezo lakuti adzabadwa mneneri womveka

15 Yehova Mulungu wanu adzakuukitsiranimneneriwa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;

16 monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu mu Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe.

17 Ndipo Yehova anati kwa ine, Chokoma ananenachi.

18 Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m’kamwa mwake, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.

19 Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m’dzina langa, ndidzamfunsa.

20 Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m’dzina langa, amene sindinamlamulire anene, kapena kunena m’dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.

21 Ndipo mukati m’mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene?

22 Mneneri akanena m’dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/18-acddb736ae7b1b77e4e4487a2c5bafbf.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 19

Za mizinda yopulumukirako

1 Pamene Yehova Mulungu wanu ataonongaamitundu, amene Yehova Mulungu wanu akupatsani dziko lao, ndipo mutalilandira lanulanu, ndi kukhala m’mizinda mwao, ndi m’nyumba zao;

2 pamenepo mudzipatulire mizinda itatu pakati padziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.

3 Mudzikonzere njira, ndi kugawa malire a dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, patatu; kuti wakupha munthu athawireko.

4 Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse;

5 monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzake kutema mitengo, ndi dzanja lake liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguluka m’mpinimo, nikomana ndi mnzake, nafa nayo; athawire ku wina wa mizinda iyi, kuti akhale ndi moyo;

6 kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzake, pokhala mtima wake watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanapalamule imfa, poona sanamude kale lonse.

7 Chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Mudzipatulire mizinda itatu.

8 Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;

9 ukadzasunga lamulo ili lonse kulichita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m’njira zake masiku onse; pamenepo mudzionjezere mizinda itatu ina pamodzi ndi itatu iyi;

10 kuti angakhetse mwazi wosachimwa pakati padziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, pangakhale mwazi pa inu.

11 Koma munthu akamuda mnzake, namlalira, ndi kumuukira ndi kumkantha moyo wake, kuti wafa; nakathawira ku wina wa mizinda iyi;

12 pamenepo akulu a mzinda wake atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m’manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe.

13 Diso lanu lisamchitire chifundo, koma muchotse mwazi wosachimwa mu Israele, kuti chikukomereni.

Za kusendeza malire, ndi za mboni yonama

14 Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m’cholowa chanu mudzalandirachi, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.

15 Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.

16 Mboni yachiwawa ikaukira munthu kumneneza ndi kuti analakwa;

17 pamenepo anthu onse awiri, pakati pao pali makaniwo, aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza okhala m’masiku awa;

18 ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wake;

19 mumchitire monga iye anayesa kumchitira mbale wake; motero muchotse choipacho pakati panu.

20 Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusachitanso monga choipacho pakati panu.

21 Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/19-dc075c082b3f9147b2b7439c3996a220.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 20

Malamulo a kunkhondo

1 Pamene mutuluka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magaleta ndi anthu akuchulukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukutulutsani m’dziko la Ejipito, ali ndi inu.

2 Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu,

3 nati nao, Tamverani, Israele, muyandikiza kunkhondo lero pa adani anu; musafumuka mitima yanu; musachita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;

4 pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.

5 Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.

6 Ndipo ndani munthuyo anaoka munda wampesa osalawa zipatso zake? Amuke nabwerere kunyumba yake, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zake.

7 Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.

8 Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake.

9 Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu.

10 Pamene muyandikiza mzinda kuchita nao nkhondo, muziufuulira ndi mtendere.

11 Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opezeka m’mwemo akhale akapolo anu, nadzakugwirirani ntchito yathangata.

12 Koma ukapanda kuchita zamtendere ndi inu, koma kuchita nkhondo nanu, pamenepo muumangire tsasa.

13 Ndipo pamene Yehova Mulungu wanu aupereka m’dzanja lanu, mukanthe amuna ake onse ndi lupanga lakuthwa.

14 Koma akazi ndi ana ndi ng’ombe ndi zonse zili m’mzindamo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

15 Muzitero nayo mizinda yonse yokhala kutalitali ndi inu, yosakhala mizinda yaamitunduawa.

16 Koma za mizinda ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale cholowa chanu, musasiyepo chamoyo chilichonse chakupuma;

17 koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;

18 kuti angakuphunzitseni kuchita monga mwa zonyansa zao zonse, amazichitira milungu yao; ndipo mungachimwire Yehova Mulungu wanu.

19 Pamene mumangira tsasa mzinda masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yake ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m’munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa?

20 Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mzinda wochita nanu nkhondo muumangire machemba, mpaka mukaugonjetsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/20-61ba721a21afa93af53b4e7dd5a27688.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 21

Za wophedwa mosadziwika

1 Akapeza munthu waphedwa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, nagona pamunda, wosadziwika wakumkantha,

2 pamenepo azituluka akulu anu ndi oweruza anu, nayese kumizinda yomzinga wophedwayo;

3 ndipo kudzali kuti mzinda wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akulu a mzinda uwu atenge ng’ombe yaikazi yosagwira ntchito, yosakoka goli;

4 ndipo akulu a mzinda uwu atsike nayo ng’ombeyo ku chigwa choyendako madzi, chosalima ndi chosabzala, nayidula khosi ng’ombeyo m’chigwamo;

5 ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m’dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.

6 Ndipo akulu onse a mzindawo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa ng’ombeyo yodulidwa khosi m’chigwamo;

7 nayankhe nati, Manja athu sanakhetse mwazi uwu, ndi maso athu sanauone.

8 Landirani, Yehova, chotetezera anthu anu Israele, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israele; ndipo adzawatetezera cha mwaziwo.

9 Chotero mudzichotsere mwazi wosachimwa pakati panu, pakuti wachita choyenera pamaso pa Yehova.

Za akazi otengedwa kunkhondo

10 Pamene mutuluka kunka ku nkhondo ya pa adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu awapereka m’manja mwanu, ndipo muwagwira akhale akapolo anu;

11 mukaona mwa akapolowa mkazi wokongola, mukamkhumba, ndi kufuna mumtenga akhale mkazi wanu;

12 pamenepo mufike naye kwanu kunyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kuwenga makadabo ake;

13 navule zovala za ukapolo wake, nakhale m’nyumba mwanu, nalire atate wake, ndi mai wake mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wake, ndi iye akhale mkazi wanu.

14 Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa chuma, popeza wamchepetsa.

Mphamvu ya oyamba kubadwa

15 Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;

16 pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ake aamuna chuma chake, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.

17 Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.

Za ana opulukira osamvera

18 Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga;

19 azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mzinda wake, ndi ku chipata cha malo ake;

20 ndipo anene kwa akulu a mzinda wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.

21 Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.

Za kuika wophedwa mompachika

22 Munthu akakhala nalo tchimo loyenera imfa, kuti amuphe, ndipo wampachika;

23 mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/21-3d5c8c0c6adbb5762e6062edc3aa4999.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 22

Za zoweta zolowerera

1 Mukapenya ng’ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.

2 Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo.

3 Mutero nayenso bulu wake; mutero nachonso chovala chake, mutero nachonso chotayika chilichonse cha mbale wanu, chakumtayikira mukachipeza ndi inu; musamazilekerera.

4 Mukapenya bulu kapena ng’ombe ya mbale wanu, zitagwa m’njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.

Zosayenerana zisaphatikizike

5 Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.

6 Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana;

7 muloletu make amuke, koma mudzitengere ana; kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke.

8 Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.

9 Musamabzala mbeu zosiyana m’munda wanu wampesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wampesa zomwe.

10 Musamalima ndi bulu ndi ng’ombe zikoke pamodzi.

11 Musamavala nsalu yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje.

12 Mudzipangire mphonje pangodya zinai za chofunda chanu chimene mudzifunda nacho.

Za akazi onenezedwa

13 Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda,

14 namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeze zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu;

15 pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mzinda kuchipata;

16 ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda;

17 ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeze zizindikiro za unamwali wake m’mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mzindawo.

18 Pamenepo akulu a mzindawo azitenga munthuyu ndi kumkwapula;

19 ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi asiliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sangathe kumchotsa masiku ake onse.

20 Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo;

21 pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m’nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.

Zoyanjana zosaloledwa

22 Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele.

23 Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m’mzinda mwamuna, nagona naye;

24 muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mzinda uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m’mzinda; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu.

25 Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye;

26 koma namwaliyo musamamchitira kanthu; namwaliyo alibe tchimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha;

27 pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anafuula, koma panalibe wompulumutsa.

28 Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo,

29 pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sangathe kumchotsa masiku ake onse.

30 Munthu asatenge mkazi wa atate wake, kapena kuvula atate wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/22-7f10dc81e1fe53d6038aa66ae9435545.mp3?version_id=1068—