Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 3

1 Pamenepo tinatembenuka, ndi kubwera kunka njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya Basani anatuluka kukomana nafe, kumenyana nafe nkhondo, iye ndi anthu ake onse, ku Ederei.

2 Ndipo Yehova anati kwa ine, Usamuopa; popeza ndampereka iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake, m’dzanja lako; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anakhala mu Hesiboni.

3 Potero Yehova Mulungu wathu anaperekanso m’manja mwathu Ogi mfumu ya Basani, ndi anthu ake onse, ndipo tinamkantha kufikira sanamtsalire ndi mmodzi yense.

4 Ndipo muja tinalanda mizinda yake yonse; kunalibe mzinda sitinaulande m’manja mwao, mizinda makumi asanu ndi limodzi, dera lonse la Arigobu, dziko la Ogi mu Basani.

5 Yonseyi ndiyo mizinda yozinga ndi malinga aatali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga.

6 Ndipo tinaiononga konse, monga umo tinachitira Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi kuononga konse mizinda yonse, amuna, akazi ndi ana.

7 Koma zoweta zonse ndi zofunkha za m’mizinda, tinadzifunkhira tokha.

8 Ndipo muja tinalanda dziko m’manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni;

9 (Asidoni alitcha Heremoni Sirioni, koma Aamori alitcha Seniri);

10 mizinda yonse ya kuchidikha, ndi Giliyadi lonse, ndi Basani lonse kufikira ku Saleka ndi Ederei, mizinda ya dziko la Ogi mu Basani.

11 (Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).

12 Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroere, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Giliyadi, ndi mizinda yake, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi.

13 Ndi chotsalira cha Giliyadi, ndi Basani lonse, dziko la Ogi, ndinapatsa hafu la fuko la Manase; dziko lonse la Arigobu, pamodzi ndi Basani. (Ndilo lotchedwa dziko la Arefaimu.

14 Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).

15 Ndipo ndinampatsa Makiri Giliyadi.

16 Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Giliyadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa chigwa ndi malire ake, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;

17 ndi chidikha, ndi Yordani ndi malire ake, kuyambira ku Kinereti kufikira ku Nyanja ya Araba, ndiyo Nyanja ya Mchere, patsinde pa Pisiga, kum’mawa.

18 Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.

19 Koma akazi anu, ndi ana anu, ndi zoweta zanu, (ndidziwa muli nazo zoweta zambiri), zikhale m’mizinda yanu imene ndinakupatsani;

20 kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.

21 Ndipo ndinauza Yoswa muja, ndi kuti, Maso ako anapenya zonse Yehova Mulungu wanu anawachitira mafumu awa awiri; momwemo Yehova adzachitira maufumu onse kumene muolokerako.

22 Musawaopa popeza Yehova Mulungu wanu, ndiye agwirira inu nkhondo.

23 Ndipo ndinapempha chifundo kwa Yehova nthawi yomwe ija, ndi kuti,

24 Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m’mwamba kapena padziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?

25 Ndioloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordani, mapiri okoma aja, ndi Lebanoni.

26 Koma Yehova anakwiya ndi ine, chifukwa cha inu, sanandimvere ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Chikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za chinthuchi.

27 Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, ndi kum’mawa, nuyang’ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordani uyo.

28 Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.

29 Potero tinakhala m’chigwamo pandunji pa Betepeori.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/3-dc539c885085cb44533767f127b19b5d.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 4

Mose awadandaulira amvere Malamulo a Mulungu

1 Ndipo tsopano, Israele, tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwachite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.

2 Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kuchotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani.

3 Maso anu anapenya chochita Yehova chifukwa cha Baala-Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala-Peori, Yehova Mulungu wanu anawaononga pakati panu.

4 Koma inu amene munamamatira Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo nonsenu lero lomwe.

5 Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.

6 Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziwitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo athu anzeru ndi akuzindikira.

7 Pakuti mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pao monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene paliponse timaitanira Iye?

8 Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?

9 Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.

10 Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu mu Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo padziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.

11 Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde paphiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.

12 Pamenepo Yehova ananena ndi inu ali pakati pa moto; munamva kunena kwa mau, osaona maonekedwe, koma kunenako.

13 Pamenepo anakufotokozeranichipanganochake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.

14 Ndipo Yehova anandilamulira muja ndikuphunzitseni malemba ndi maweruzo, kuti mukawachite m’dziko limene muolokerako kulilandira likhale lanulanu.

15 Potero dzichenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenye mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu mu Horebu, ali pakati pa moto;

16 kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga chifaniziro chilichonse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi;

17 mafanidwe a nyama iliyonse ili padziko lapansi, mafanidwe a mbalame iliyonse yamapiko yakuuluka m’mlengalenga,

18 mafanidwe a chinthu chilichonse chokwawa pansi, mafanidwe a nsomba iliyonse yokhala m’madzi pansi padziko;

19 ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.

20 Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m’ng’anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.

21 Yehova anakwiyanso nane chifukwa cha mau anu, nalumbira kuti sindidzaoloka Yordani ine, ndi kuti sindidzalowa m’dziko lokomali Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu;

22 pakuti ndidzafa m’dziko muno, osaoloka Yordani; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanulanu.

23 Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.

24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.

25 Mutakabala ana, ndi zidzukulu, ndipo mutakakhala nthawi yaikulu m’dzikomo, ndi kudziipsa, ndi kupanga fano losema, m’chifaniziro cha kanthu kalikonse, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kuutsa mkwiyo wake:

26 ndiitana kumwamba ndi dziko lapansi zichite mboni pa inu lero lino, kuti mudzaonongeka msangatu kuchotsedwa ku dziko limene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu; masiku anu sadzachuluka pamenepo, koma mudzaonongeka konse.

27 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang’ono mwaamitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.

28 Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, ntchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.

29 Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

30 Mukakhala nao msauko, zikakugwerani zonsezi, masiku otsiriza mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvera mau ake;

31 popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.

32 Pakuti, funsiranitu, masiku adapitawo, musanakhale inu, kuyambira tsikuli Mulungu analenga munthu padziko lapansi, ndi kuyambira malekezero ena a thambo kufikira malekezero anzake a thambo, ngati chinthu chachikulu chonga ichi chinamveka, kapena kuchitika?

33 Kodi pali mtundu wa anthu udamva mau a mulungu wina akunena pakati pa moto, monga mudamva inu, ndi kukhala ndi moyo?

34 Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?

35 Inu munachiona ichi, kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu; palibe wina wopanda Iye.

36 Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo padziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto.

37 Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito;

38 kupirikitsa amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale cholowa chanu, monga lero lino.

39 Potero dziwani lero lino nimukumbukire m’mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m’thambo la kumwamba ndi padziko lapansi; palibe wina.

40 Muzisunga malemba ake, ndi malamulo ake, amene ndikuuzani lero lino, kuti chikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu achuluke padziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.

Mizinda itatu yopulumukirako kum’mawa kwa Yordani

41 Pamenepo Mose anapatula mizinda itatu tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa;

42 kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wake dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa mizinda iyi, akhale ndi moyo:

43 ndiyo Bezeri, m’chipululu, m’dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti mu Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, mu Basani, ndiwo wa Amanase.

44 Ndipo ichi ndi chilamulo Mose anachiika pamaso pa ana a Israele;

45 izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israele, potuluka iwo mu Ejipito;

46 tsidya lija la Yordani, m’chigwa cha pandunji pa Betepeori, m’dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo mu Ejipito;

47 ndipo analanda dziko lake, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa;

48 kuyambira ku Aroere, ndiwo m’mphepete mwa mtsinje wa Arinoni, kufikira phiri la Sirioni (ndilo Heremoni),

49 ndi chidikha chonse tsidya lija la Yordani kum’mawa, kufikira ku Nyanja ya Araba, pa tsinde lake la Pisiga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/4-1ffa6ea78092b5e469811c196309d9f2.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 5

Mose abwereza kuwatchulira Malamulo a Mulungu

1 Ndipo Mose anaitana Aisraele onse, nanena nao, Tamverani, Israele, malemba ndi maweruzo ndinenawa m’makutu mwanu lero, kuti muwaphunzire, ndi kusamalira kuwachita.

2 Yehova Mulungu wathu anapangana nafechipanganomu Horebu.

3 Yehova sanachite chipangano ichi ndi makolo athu, koma ndi ife, ife amene tili ndi moyo tonsefe pano lero.

4 Yehova ananena ndi inu popenyana maso m’phirimo, ali pakati pa moto,

5 (ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m’phirimo) ndi kuti:

6 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m’dziko la Ejipito, m’nyumba ya ukapolo.

7 Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.

8 Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi padziko;

9 usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate wao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;

10 ndi kuchitira chifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.

11 Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa amene atchula pachabe dzina lakelo.

12 Samalira tsiku laSabatalikhale lopatulika, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira.

13 Masiku asanu ndi limodzi uzigwiritsa ntchito, ndi kuchita ntchito zako zonse;

14 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng’ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m’mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.

15 Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.

16 Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

17 Usaphe.

18 Usachite chigololo.

19 Usabe.

20 Usamnamizire mnzako.

21 Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.

22 Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m’phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.

23 Ndipo kunali, pamene munamva liu lotuluka pakati pa mdima, potentha phiri ndi moto, munayandikiza kwa ine, ndiwo mafumu onse a mafuko anu ndi akulu anu;

24 ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wake, ndi ukulu wake, ndipo tidamva liu lake ali pakati pa moto; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.

25 Ndipo tsopano tiferenji? Popeza moto waukulu uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa.

26 Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo?

27 Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita.

28 Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; chokoma chokhachokha adanenachi.

29 Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!

30 Muka, nuti nao, Bwererani ku mahema anu.

31 Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m’dziko limene ndiwapatsa likhale laolao.

32 Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.

33 Muziyenda m’njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m’dziko limene mudzakhala nalo lanulanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/5-98abd942bd59a754061406610597f0a5.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 6

Awapempha asunge Malamulo a Mulungu kuti adale

1 Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwachita m’dziko limene muolokerako kulilandira;

2 kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke.

3 Potero imvani, Israele, musamalire kuwachita, kuti chikukomereni ndi kuti muchuluke chichulukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

4 Imvani, Israele; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;

5 ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.

6 Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu;

7 ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.

8 Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pamaso anu.

9 Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.

10 Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m’dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; mizinda yaikulu ndi yokoma, imene simunaimange;

11 ndi nyumba zodzala nazo zokoma zilizonse, zimene simunazidzaze, ndi zitsime zosema, zimene simunaziseme, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioke, ndipo mutakadya ndi kukhuta;

12 pamenepo mudzichenjera mungaiwale Yehova, amene anakutulutsani m’dziko la Ejipito, m’nyumba ya ukapolo.

13 Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake.

14 Musamatsate milungu ina, milungu ina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;

15 pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukuchotsani pankhope padziko lapansi.

16 Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa mu Masa.

17 Muzisunga mwachangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zake, ndi malemba ake, amene anakulamulirani.

18 Ndipo muzichita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti chikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu,

19 kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena.

20 Akakufunsani ana anu m’tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani?

21 Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo aFaraomu Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.

22 Ndipo Yehova anapatsa zizindikiro ndi zozizwa zazikulu ndi zowawa mu Ejipito, pa Farao, ndi pa nyumba yake yonse, pamaso pathu;

23 ndipo anatitulutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu.

24 Ndipo Yehova anatilamulira tizichita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino.

25 Ndipo kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/6-d790dfb15b79abb09bf31e16b28f9f46.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 7

Awapangira za Akanani ndi zipembedzo zao

1 Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m’dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakatayaamitunduambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;

2 nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.

3 Ndipo musakwatitsane nao; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.

4 Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.

5 Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.

6 Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.

7 Yehova sanakondwere nanu, ndi kukusankhani chifukwa cha kuchuluka kwanu koposa mitundu ina yonse ya anthu, kapena kuchepera kwanu;

8 koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m’nyumba ya ukapolo, m’dzanja laFaraomfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.

9 Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusungachipanganondi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.

10 Ndipo awabwezera onse akudana ndi Iye, pamaso pao, kuwaononga; sachedwa naye wakudana ndi Iye, ambwezera pamaso pake.

11 Potero muzisunga malamulo, ndi malemba, ndi maweruzo amene ndikuuzani lero kuwachita.

12 Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;

13 ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m’dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.

14 Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.

15 Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.

16 Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.

17 Mukadzanena m’mtima mwanu, Amitundu awa andichulukira; ndikhoza bwanji kuwapirikitsa?

18 Musamawaopa; mukumbukire bwino chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao, ndi Ejipito wonse;

19 mayesero aakulu maso anu anawapenya, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakutulutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.

20 Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu.

21 Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.

22 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang’onopang’ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakuchulukireni zilombo.

23 Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapirikitsa ndi kupirikitsa kwakukulu, kufikira ataonongeka.

24 Adzaperekanso mafumu ao m’dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga.

25 Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirirasilivandi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.

26 Musamalowa nacho chonyansachi m’nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/7-1a62e5a353fb959c52196993a45b2adb.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 8

Akumbuke zokoma zazikulu Mulungu anawachitira

1 Muzisamalira kuchita malamulo onse amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale ndi moyo, ndi kuchuluka, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.

2 Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.

3 Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndimana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.

4 Zovala zanu sizinathe pathupi panu, phazi lanu silinatupe zaka izi makumi anai.

5 Ndipo muzindikire m’mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.

6 Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake, ndi kumuopa.

7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m’dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe ndi la maiwe akutuluka m’zigwa, ndi m’mapiri;

8 dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uchi;

9 dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yake nja chitsulo, ndi m’mapiri ake mukumbe mkuwa.

10 Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko lokomali anakupatsani.

11 Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino;

12 kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;

13 ndipo zitachuluka ng’ombe zanu, ndi nkhosa zanu, atachulukansosilivawanu ndi golide wanu, zitachulukanso zonse muli nazo;

14 mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Ejipito, m’nyumba ya ukapolo;

15 amene anakutsogolerani m’chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m’thanthwe lansangalabwi;

16 amene anakudyetsani m’chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;

17 ndipo munganene m’mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi.

18 Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitsechipanganochake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.

19 Ndipo kudzakhala kuti mukaiwalatu Yehova Mulungu wanu, ndi kutsata milungu ina ndi kuitumikira, ndikuchitirani mboni lero lino kuti mudzaonongeka ndithu.

20 Mongaamitunduamene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; chifukwa cha kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/8-54122929546aa90c150717b099aaf210.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 9

1 Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandiraamitunduakulu ndi amphamvu akuposa inu, mizinda yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,

2 anthu aakulu ndi ataliatali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?

3 Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; Iye adzawaononga, Iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapirikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.

4 Musamanena mumtima mwanu, atawapirikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Chifukwa cha chilungamo changa Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa.

5 Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.

6 Potero mudziwe, kuti Yehova Mulungu wanu sakupatsani dziko ili lokoma mulilandire, chifukwa cha chilungamo chanu; pakuti inu ndinu mtundu wa anthu opulukira.

7 Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m’chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m’dziko la Ejipito, kufikira munalowa m’malo muno munapikisana ndi Yehova.

8 Mu Horebu momwe munautsa mkwiyo wa Yehova; ndipo Yehova anakwiya nanu kukuonongani.

9 Muja ndinakwera m’phiri kukalandira magome amiyala, ndiwo magome achipanganochimene Yehova anapangana ndi inu, ndinakhala m’phiri masiku makumi anai usana ndi usiku; osadya mkate osamwa madzi.

10 Ndipo Yehova anapereka kwa ine magome awiri amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu; ndipo panalembedwa pamenepo monga mwa mau onse amene Yehova adanena ndi inu m’phirimo, ali pakati pa moto, tsiku lakusonkhana.

11 Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a chipangano.

12 Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawatulutsa mu Ejipitowa anadziipsa; anapatuka msanga m’njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.

13 Yehova ananenanso ndi ine, ndi kuti, Ndapenya anthu awa, taona, awa ndi anthu opulukira;

14 undileke, ndiwaononge, ndi kufafaniza dzina lao pansi pa thambo; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi waukulu woposa iwo.

15 Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m’phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a chipangano anali m’manja mwanga.

16 Ndipo ndinapenya, taonani, mudachimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwanawang’ombe woyenga; mudapatuka msanga m’njira imene Yehova adalamulira inu.

17 Pamenepo ndinagwira magome awiriwo, ndi kuwataya achoke m’manja anga awiri, ndi kuwaswa pamaso panu.

18 Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, chifukwa cha machimo anu onse mudachimwa, ndi kuchita choipacho pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.

19 Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani. Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso.

20 Ndipo Yehova anakwiya kwambiri ndi Aroni kumuononga; koma ndinampempherera Aroni nthawi yomweyo.

21 Ndipo ndinatenga tchimo lanu, mwanawang’ombe mudampangayo, ndi mumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati fumbi; ndipo ndinataya fumbi lake m’mtsinje wotsika m’phirimo.

22 Ku Tabera, ndi ku Masa, ndi ku Kibroti-Hatava, munautsanso mkwiyo wa Yehova.

23 Ndipo pamene Yehova anakutumizani kuchokera ku Kadesi-Baranea, ndi kuti Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ake.

24 Munakhala opikisana ndi Yehova kuyambira tsikuli ndinakudziwani.

25 Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova masiku makumi anai usana ndi usiku ndinagwa pansiwa; popeza Yehova adati kuti adzakuonongani.

26 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawatulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.

27 Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo; musapenyerera kupulukira kwa anthu awa, kapena choipa chao, kapena tchimo lao;

28 kuti linganene dziko limene mudatitulutsako, Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa m’dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawatulutsa kuti awaphe m’chipululu.

29 Koma iwo ndiwo anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawatulutsa ndi mphamvu yanu yaikulu ndi dzanja lanu lotambasuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/9-b65d91be500dab45c0b8d5c3a6b0d6a0.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 10

Za magome achiwiri a Malamulo

1 Masiku aja Yehova anati kwa ine, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja, nukwere kuno kwa Ine m’phiri umu, nudzipangire likasa lamtengo.

2 Ndipo ndidzalembera pa magomewo mauwo anali pa magome oyamba aja amene unawaswa, ndipo uwaike m’likasamo.

3 Potero ndinapanga likasa la mtengo wakasiya, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m’phirimo, magome awiri ali m’manja mwanga.

4 Ndipo analembera pamagome, monga mwa malembedwe oyamba, mau khumiwo, amene Yehova adanena ndi inu m’phirimo, ali pakati pa moto, tsiku la kusonkhanako; ndipo Yehova anandipatsa awa.

5 Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m’phiri, ndi kuika magome m’likasa ndinalipanga, ali m’menemo monga Yehova anandilamulira ine.

6 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wao kuchokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wake anachita ntchito ya nsembe m’malo mwake.

7 Kuchokerako ananka ulendo ku Gudigoda, ndi kuchokera ku Gudigoda kunka ku Yotibata, dziko la mitsinje yamadzi.

8 Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamulelikasa la chipanganola Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m’dzina lake kufikira lero lino.

9 Chifukwa chake Levi alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi abale ake; Yehova mwini wake ndiye cholowa chake, monga Yehova Mulungu wake ananena naye.

10 Ndipo ndinakhala m’phiri monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku; ndipo Yehova anandimvera ine pameneponso; Yehova sanafune kukuonongani.

11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, tenga ulendo pamaso pa anthu; kuti alowe ndi kulandira dzikoli ndinalumbirira makolo ao kuti ndidzawapatsa.

Abwereza kuwadandaulira akonde namvere Mulungu

12 Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,

13 kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?

14 Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m’mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.

15 Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.

16 Potero dulani khungu la mitima yanu, ndipo musamapulukiranso.

17 Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.

18 Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.

19 M’mwemo mukondane naye mlendo; popeza munali alendo m’dziko la Ejipito.

20 Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake.

21 Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m’maso mwanu.

22 Makolo anu anatsikira ku Ejipito ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri; ndipo Yehova Mulungu wanu anakusandulizani tsopano muchuluke ngati nyenyezi za kumwamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/10-03341179e6ea49ff4f9d57f3f0dda54d.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 11

1 Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse.

2 Ndipo dziwani lero lino; pakuti sindinena ndi ana anu osadziwa, ndi osapenya kulanga kwa Yehova Mulungu wanu, ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, ndi mkono wake wotambasuka,

3 ndi zizindikiro zake, ndi ntchito zake, adazichitiraFaraomfumu ya Aejipito, ndi dziko lake lonse pakati pa Ejipito;

4 ndi chochitira Iye nkhondo ya Ejipito, akavalo ao, ndi agaleta ao; kuti anawamiza m’madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m’mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;

5 ndi chimene anakuchitirani m’chipululu, kufikira munadza kumalo kuno;

6 ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse.

7 Koma maso anu anapenya ntchito yonse yaikulu ya Yehova anaichita.

8 Potero muzisunga malamulo onsewa ndikuuzani lero lino, kuti mukhale amphamvu, ndi kulowa ndi kulandira dziko, limene munkako kulilandira;

9 ndi kuti masiku anu achuluke m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, kuti adzawapatsa iwo ndi mbeu zao, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

10 Pakuti dziko limene munkako kulilandira ndi losanga dziko la Ejipito lija mudatulukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;

11 koma dziko limene munkako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba;

12 ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo chikhalire, kuyambira chaka mpaka kutsiriza chaka.

Za madalitso otsatira kumvera kwao

13 Ndipo kudzakhala mukasamalira chisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kumtumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,

14 ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m’nyengo yake, ya chizimalupsa ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.

15 Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.

16 Dzichenjerani nokha, angachete mitima yanu, nimungapatuke, ndi kutumikira milungu ina, ndi kuipembedza;

17 ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zake; ndi kuti mungaonongeke msanga m’dziko lokomali Yehova akupatsani.

18 Chifukwa chake muzisunga mau anga awa mumtima mwanu ndi m’moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati chizindikiro pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pamaso anu.

19 Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m’nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.

20 Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu;

21 kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke m’dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo lili pamwamba padziko.

22 Pakuti mukasunga chisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwachita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake zonse, ndi kummamatira;

23 Yehova adzapirikitsaamitunduawa onse pamaso panu, ndipo mudzalanda amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu.

24 Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pamtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m’tsogolo, ndiwo malire anu.

25 Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.

Mdalitso ndi temberero

26 Taonani, ndilikuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero;

27 dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino;

28 koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m’njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu ina imene simunaidziwa.

29 Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m’dziko limene munkako kulilandira, munene mdalitso paphiri la Gerizimu, ndi temberero paphiri la Ebala.

30 Sakhala kodi tsidya lija la Yordani, m’tseri mwake mwa njira yake yolowa dzuwa, m’dziko la Akanani, akukhala m’chidikha, pandunji pake pa Giligala, pafupi pa mathundu a More?

31 Pakuti mulinkuoloka Yordani kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndipo mudzachilandira cholowa chanu, ndi kukhalamo.

32 Potero samalirani kuchita malemba ndi maweruzo onse ndiwaika pamaso panu lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/11-bddff0ff35d7252b84613849635eea54.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 12

Malo Oyera akhale amodzi

1 Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwachita m’dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanulanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu padziko lapansi.

2 Muononge konse malo onse,amitunduamene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;

3 nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m’malomo.

4 Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.

5 Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;

6 ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng’ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;

7 ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m’mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.

8 Musamadzichita monga mwa zonse tizichita kuno lero, yense kuchita chilichonse chiyenera m’maso mwake;

9 pakuti mpaka lero simunafikire mpumulo ndi cholowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.

10 Koma mudzaoloka Yordani, ndi kukhala m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.

11 Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.

12 Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m’midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.

13 Dzichenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona:

14 koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mafuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzichita zonse ndikuuzani.

15 Koma monga mwa chikhumbo chonse cha moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m’midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.

16 Mwazi wao wokha musamadya; muziuthira panthaka ngati madzi.

17 Simungathe kudya m’mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyamba kubadwa a ng’ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu zilizonse muzilonjeza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m’dzanja lanu;

18 koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m’malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m’mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m’zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.

19 Dzichenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m’dziko mwanu.

Za kudya nyama

20 Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.

21 Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lake akakutanimphirani, muziphako ng’ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m’mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.

22 Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko chimodzimodzi.

23 Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yake.

24 Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi.

25 Musamadya uwu; kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m’mbuyo mwanu, pakuchita inu zoyenera pamaso pa Yehova.

26 Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasankha;

27 ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yake muidye.

28 Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m’mbuyo mwanu nthawi zonse, pochita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29 Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m’dziko lao,

30 dzichenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? Ndichite momwemo inenso.

31 Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m’moto, nsembe ya milungu yao.

32 Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/12-7319adb3f78255ed6e7102d703727548.mp3?version_id=1068—