Categories
NUMERI

NUMERI 30

Za chowinda chochita akazi

1 Ndipo Mose ananena ndi akulu a mafuko a ana a Israele, nati, Chinthu anachilamulira Yehova ndi ichi:

2 Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m’kamwa mwake.

3 Ndipo mkazi akachitira Yehova chowinda, nakadzimanga nacho chodziletsa, pokhala ali m’nyumba ya atate wake, mu unamwali;

4 ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga nacho moyo wake, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika.

5 Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa.

6 Ndipo akakwatibwa naye mwamuna, pokhala ali nazo zowinda zake, kapena zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake;

7 nakazimva mwamuna wake, nakakhala naye chete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zake zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.

8 Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.

9 Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira.

10 Ndipo ngati anawinda m’nyumba ya mwamuna wake, kapena anamanga moyo wake ndi chodziletsa ndi kulumbirapo,

11 ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.

12 Koma ngati mwamuna wake anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zotuluka m’milomo yake kunena za zowinda zake, kapena za chodziletsa cha moyo wake sizidzakhazikika; mwamuna wake anafafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira iye.

13 Chowinda chilichonse, ndi cholumbira chilichonse chodziletsa chakuchepetsa nacho moyo, mwamuna wake achikhazikira, kapena mwamuna wake achifafaniza.

14 Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye.

15 Koma akazifafaniza atatha kuzimva; pamenepo adzasenza mphulupulu yake.

16 Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m’nyumba ya atate wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/30-49281e6182ef3cdfb9dc3e40e89434a5.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 31

Aisraele agonjetsa Amidiyani

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Abwezereni chilango Amidiyani chifukwa cha ana a Israele; utatero udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako.

3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidiyani, kuwabwezera Amidiyani chilango cha Yehova.

4 Muwatume kunkhondo a fuko limodzi, chikwi chimodzi, atere mafuko onse a Israele.

5 Ndipo anapereka mwa zikwi za Israele, a fuko limodzi chikwi chimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.

6 Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m’dzanja lake.

7 Ndipo anawathira nkhondo Amidiyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.

8 Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.

9 Ndipo ana a Israele anagwira akazi a Amidiyani, ndi ana aang’ono, nafunkha ng’ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi chuma chao chonse.

10 Ndipo anatentha ndi moto mizinda yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.

11 Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.

12 Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israele, kuchigono, ku zidikha za Mowabu, zili ku Yordani pafupi pa Yeriko.

Mayeretsedwe a ankhondowo

13 Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anatuluka kukomana nao kunja kwa chigono.

14 Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira.

15 Ndipo Mose ananena nao, Kodi mwasunga ndi moyo akazi onse?

16 Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m’khamu la Yehova.

17 Ndipo tsono iphani amuna onse mwa anawo, iphaninso akazi onse akudziwa mwamuna mogona naye.

18 Koma ana aakazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeni ndi moyo akhale anu.

19 Ndipo mukhale m’misasa kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; aliyense adapha munthu, ndi aliyense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lachitatu ndi lachisanu ndi chiwiri, inu ndi andende anu.

20 Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.

21 Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la chilamulocho Yehova analamulira Mose ndi ili:

22 Golide, ndisiliva, mkuwa, chitsulo, ndolo ndi mtovu zokha,

23 zonse zakulola moto, mupititse m’moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m’madzi.

24 Ndipo mutsuke zovala zanu tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m’chigono.

Magawidwe a zofunkha

25 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

26 Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe, ndi Eleazara wansembe, ndi akulu a nyumba za makolo za khamulo;

27 nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anatuluka kunkhondo, ndi khamu lonse.

28 Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng’ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.

29 Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.

30 Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng’ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.

31 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anachita monga Yehova anamuuza Mose.

32 Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,

33 ndi ng’ombe zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri,

34 ndi abulu zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu chimodzi,

35 ndi anthu, ndiwo akazi osadziwa mwamuna mogona naye, onse pamodzi zikwi makumi atatu ndi ziwiri.

36 Ndipo limodzi la magawo awiri, ndilo gawo la iwo adatuluka kunkhondo, linafikira nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.

37 Ndi msonkho wa Yehova wankhosa ndiwo mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu.

38 Ndipo ng’ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.

39 Ndipo abulu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.

40 Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.

41 Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.

42 Ndipo kunena za gawo la ana a Israele, limene Mose adalichotsa kwa anthu ochita nkhondowo,

43 (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,

44 ndi ng’ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi,

45 ndi abulu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu,

46 ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi,)

47 mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Zopereka zaufulu za akazembe

48 Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose;

49 nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife.

50 Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.

51 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.

52 Ndipo golide yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.

53 Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.

54 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye kuchihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/31-1b000e536eb5cc4f18b92490cfc42ad3.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 32

Arubeni, Agadi, ndi Amanase alandira cholowa chao tsidya lino la Yordani

1 Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.

2 Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati,

3 Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,

4 dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.

5 Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani.

6 Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?

7 Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israele kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?

8 Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza achoke ku Kadesi-Baranea kukaona dziko.

9 Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.

10 Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira Iye, nati,

11 Anthu adakwerawo kutuluka mu Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;

12 koma Kalebe mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.

13 Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m’chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova.

14 Ndipo taonani, mwauka m’malo mwa makolo anu, gulu la anthu ochimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israele.

15 Pakuti mukabwerera m’mbuyo kusamtsata Iye, adzawasiyanso m’chipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.

16 Ndipo anayandikiza, nati Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu mizinda;

17 koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang’ono athu adzakhala mizinda ya malinga chifukwa cha okhala m’dzikomo.

18 Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israele atalandira yense cholowa chake.

19 Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m’tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum’mawa.

20 Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzachita ichi, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,

21 ndi kuoloka Yordani pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapirikitsa adani ake pamaso pake,

22 ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova.

23 Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.

24 Dzimangireni mizinda ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzichite zotuluka m’kamwa mwanu.

25 Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira.

26 Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng’ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m’mizinda ya ku Giliyadi;

27 koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.

28 Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a makolo a mafuko a ana a Israele za iwo.

29 Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;

30 koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m’dziko la Kanani.

31 Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita.

32 Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma cholowa chathuchathu chikhale tsidya lino la Yordani.

33 Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi hafu la fuko la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi mizinda yake m’malire mwao, ndiyo mizinda ya dziko lozungulirako.

34 Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroere;

35 Ataroti-Sofani, Yazere, ndi Yogobeha;

36 ndi Betenimura, ndi Beteharani: mizinda ya m’malinga, ndi makola a zoweta.

37 Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu;

38 ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha mizinda adaimanga ndi maina ena.

39 Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase ananka ku Giliyadi, naulanda, napirikitsa Aamori anali m’mwemo.

40 Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Giliyadi; ndipo anakhala m’menemo.

41 Ndipo Yairi mwana wa Manase ananka nalanda midzi yao, naitcha Havoti-Yairi.

42 Ndipo Noba ananka nalanda Kenati, ndi midzi yake, nautcha Noba, dzina lake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/32-320f00cb89339f4a0fc7056b19f9b7ac.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 33

Za ulendo wa Aisraele pakati pa Ramsesi ndi Sitimu

1 Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m’dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.

2 Ndipo Mose analembera matulukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa matulukidwe ao.

3 Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachitaPaskam’mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse,

4 pamene Aejipito analikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.

5 Ndipo ana a Israele anachokera ku Ramsesi, nayenda namanga ku Sukoti.

6 Nachokera ku Sukoti, nayenda namanga mu Etamu, ndiko ku malekezero a chipululu.

7 Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.

8 Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m’chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m’chipululu cha Etamu, namanga mu Mara.

9 Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko.

10 Ndipo anachokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira.

11 Nachokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m’chipululu cha Sini.

12 Nachokera ku chipululu cha Sini, nayenda namanga mu Dofika.

13 Nachokera ku Dofika, nayenda namanga mu Alusi.

14 Nachokera ku Alusi, nayenda namanga mu Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.

15 Ndipo anachokera ku Refidimu, nayenda namanga m’chipululu cha Sinai.

16 Nachokera ku chipululu cha Sinai, nayenda namanga mu Kibroti-Hatava.

17 Nachokera ku Kibroti-Hatava, nayenda namanga mu Hazeroti.

18 Nachokera ku Hazeroti, nayenda namanga mu Ritima.

19 Nachokera ku Ritima, nayenda namanga mu Rimoni-Perezi.

20 Nachokera ku Rimoni-Perezi, nayenda namanga mu Libina.

21 Nachokera ku Libina, nayenda namanga mu Risa.

22 Nachokera Risa, nayenda namanga mu Kehelata.

23 Nachokera ku Kehelata, nayenda namanga m’phiri la Sefera.

24 Nachokera kuphiri la Sefera, nayenda namanga mu Harada.

25 Nachokera ku Harada, nayenda namanga mu Makeloti.

26 Nachokera ku Makeloti, nayenda namanga mu Tahata.

27 Nachokera ku Tahata, nayenda namanga mu Tera.

28 Nachokera ku Tera, nayenda namanga mu Mitika.

29 Nachokera ku Mitika, nayenda namanga mu Hasimona.

30 Nachokera ku Hasimona, nayenda namanga mu Meseroti.

31 Nachokera ku Meseroti, nayenda namanga mu Bene-Yaakani.

32 Nachokera ku Bene-Yaakani, nayenda namanga mu Hori Hagidigadi.

33 Nachokera ku Hori Hagidigadi, nayenda namanga mu Yotibata.

34 Nachokera ku Yotibata, nayenda namanga mu Aborona.

35 Nachokera ku Aborona, nayenda namanga mu Eziyoni-Gebere.

36 Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m’chipululu cha Zini (ndiko Kadesi).

37 Nachokera ku Kadesi, nayenda namanga m’phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.

38 Ndipo Aroni wansembe anakwera m’phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, atatuluka ana a Israele m’dziko la Ejipito zaka makumi anai, mwezi wachisanu, tsiku loyamba la mwezi.

39 Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m’phiri la Hori.

40 Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwera m’dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israele.

41 Ndipo anachokera kuphiri la Hori, nayenda namanga mu Zalimona.

42 Nachokera ku Zalimona, nayenda namanga mu Punoni.

43 Nachokera ku Punoni, nayenda namanga mu Oboti.

44 Nachokera ku Oboti, nayenda namanga mu Iyeabarimu, m’malire a Mowabu.

45 Nachokera ku Iyimu, nayenda namanga mu Diboni Gadi.

46 Nachokera ku Diboni Gadi, nayenda namanga mu Alimoni-Dibulataimu.

47 Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m’mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo.

48 Nachokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m’zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.

49 Ndipo anamanga pa Yordani, kuyambira ku Beteyesimoti kufikira ku Abele-Sitimu m’zidikha za Mowabu.

Aisraele azipirikitsa eni dziko la Kanani

50 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m’zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko, nati,

51 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutaoloka Yordani kulowa m’dziko la Kanani,

52 mupirikitse onse okhala m’dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;

53 ndipo mulande dziko, ndi kukhala m’mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanulanu.

54 Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.

55 Koma mukapanda kupirikitsa okhala m’dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m’maso mwanu, ndi minga m’mbali zanu, nadzakuvutani m’dziko limene mukhalamo.

56 Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/33-5d44ba383ca6b0af402a9568cc0760ca.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 34

Malire a dziko la Kanani

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Uza ana a Israele, nunene nao, Mutalowa m’dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale cholowa chanu, dziko la Kanani monga mwa malire ake,

3 dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m’mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum’mawa;

4 ndi malire anu adzapinda kuchokera kumwera kunka pokwera Akarabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kutuluka kwake adzachokera kumwera ku Kadesi-Baranea, nadzatuluka kunka ku Hazara-Adara, ndi kupita kunka ku Azimoni;

5 ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja.

6 Kunena za malire a kumadzulo Nyanja Yaikulu ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.

7 Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku Nyanja Yaikulu mulinge kuphiri la Hori:

8 kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi.

9 Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.

10 Ndipo mudzilembere malire a kum’mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu;

11 ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum’mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum’mawa,

12 ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga.

13 Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;

14 popeza fuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi hafu la fuko la Manase lalandira cholowa chao;

15 mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum’mawa, kotulukira dzuwa.

16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

17 Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

18 Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao.

19 Maina a amunawo ndiwo: wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune.

20 Wa fuko la ana a Simeoni, Semuele mwana wa Amihudi.

21 Wa fuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni.

22 Wa fuko la ana a Dani, kalonga Buki mwana wa Yogili.

23 Wa ana a Yosefe; wa fuko la ana a Manase, kalonga Haniyele mwana wa Efodi.

24 Wa fuko la ana a Efuremu, kalonga Kemuwele mwana wa Sifutani.

25 Wa fuko la ana a Zebuloni, kalonga Elizafani mwana wa Paranaki.

26 Wa fuko la ana a Isakara, kalonga Palatiele mwana wa Azani.

27 Wa fuko la ana a Asere, kalonga Ahihudi mwana wa Selomi.

28 Wa fuko la ana a Nafutali, kalonga Pedahele mwana wa Amihudi.

29 Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israele cholowa chao m’dziko la Kanani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/34-99a32c84db1e2a56461b834f6b4fb581.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 35

Mizinda ya Alevi

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m’zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti,

2 Uza ana a Israele, kuti apatseko Alevi cholowa chaochao, mizinda yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira mizinda.

3 Ndipo mizinda ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng’ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.

4 Ndipo mabusa a mizindayo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.

5 Ndipo muyese kunja kwa mzinda, mbali ya kum’mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mzindawo pakati; ndiwo mabusa a kumizinda.

6 Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.

7 Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao.

8 Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang’ono mutengeko pang’ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.

Mizinda yopulumukirako

9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pakuoloka inu Yordani kulowa m’dziko la Kanani,

11 muikire mizinda ikukhalireni mizinda yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.

12 Ndipo mizindayo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.

13 Ndipo mizindayo muipereke ikukhalireni mizinda isanu ndi umodzi yopulumukirako.

14 Mupereke mizinda itatu tsidya lino la Yordani, ndi mizinda itatu mupereke m’dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako.

15 Mizinda isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko.

16 Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

17 Kapena akamkantha m’dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

18 Kapena akamkantha m’dzanja muli chipangizo chamtengo, chakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

19 Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.

20 Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;

21 kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.

22 Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamlalira,

23 kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wake, kapena womfunira choipa;

24 pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzakeyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;

25 ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m’dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumzinda wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.

26 Koma wakupha munthu akatuluka nthawi iliyonse kulumpha malire a mzinda wake wopulumukirako kumene anathawirako;

27 nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mzinda wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi;

28 popeza wakupha munthu akadakhala m’mzinda wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.

29 Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la chiweruzo mwa mibadwo yanu, m’nyumba zanu zonse.

30 Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.

31 Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.

32 Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumzinda wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m’dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe.

33 Ndipo musamaipsa dziko muli m’mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m’mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.

34 Usamadetsa dziko ukhala m’mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/35-85538b1fe9e90870ca58db766cebc728.mp3?version_id=1068—

Categories
NUMERI

NUMERI 36

Za kukwatibwa kwa ana aakazi olandira cholowa

1 Ndipo akulu a makolo a mabanja a ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akulu a makolo a ana a Israele;

2 nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.

3 Ndipo akakwatibwa nao ana aamuna a mafuko ena a ana a Israele, achichotse cholowa chao ku cholowa cha makolo athu, nachionjeze ku cholowa cha fuko limene adzakhalako; chotero achichotse ku maere a cholowa chathu.

4 Ndipo pofika chaka choliza cha ana a Israele adzaphatikiza cholowa chao ku cholowa cha fuko limene akhalako; chotero adzachotsa cholowa chao ku cholowa cha fuko la makolo athu.

5 Ndipo Mose analamulira ana a Israele monga mwa mau a Yehova, nati, Fuko la ana a Yosefe linena zoona.

6 Cholamulira Yehova za ana aakazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha.

7 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake.

8 Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake.

9 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake.

10 Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana aakazi a Zelofehadi anachita;

11 popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wao.

12 Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m’fuko la banja la atate wao.

13 Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israele ndi dzanja la Mose m’zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/36-4fd9031ce28cfe81b68970db60e9adb9.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likutchedwa

Deuteronomo

, ndiye kuti “Kubwereza”, chifukwa likulongosola kachiwiri zina ndi zina zimene zidakambidwa kale m’mabuku ena aja. Bukuli likulongosola za malangizo osiyanasiyana amene Mose adapereka kwa ana a Israele pamene anali m’dziko la Mowabu, ali pafupi kulowa m’dziko lamalonjezano la Kanani.

Phunziro lalikulu lopezeka m’bukuli ndi lakuti Yehova apulumutsa Aisraele ndi kuwadalitsa chifukwa amawakonda kwambiri. Motero iwonso ayenera kumakumbukira zimenezi ndi kumkonda Iyeyo potsata malamulo ake, kuti akhale ndi moyo ndi kulandirabe madalitso ena pa moyo wao ukudzawu. Mau odziwika kwambiri apezeka pa 6.4-6: “ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” Paja Yesu adati, pa malamulo onse, lamulo lalikulu ndi lomweli.

Za mkatimu

Malangizo oyamba a Mose

1.1—4.49

Malangizo achiwiri a Mose

5.1—26.19

a. Za Malamulo Khumi

5.1—10.22

b. Mose aperekanso malamulo ena ndi malangizo

11.1—26.19

Machenjezo asanalowe m’dziko la malonjezano

27.1—28.68

Yehova achita chipangano ndi anthu ake

29.1—30.20

Malangizo otsiriza a Mose

31.1—34.12

a. Mose asankha Yoswa kuti adzalowe m’malo mwake

31.1—33.29

b. Imfa ya Mose

34.1-12

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 1

Mose awafotokozera za ulendo wao m’chipululu

1 Awa ndi mau amene Mose ananena kwa Israele wonse, tsidya la Yordani m’chipululu, m’chidikha cha pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofele, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Dizahabu.

2 Ulendo wake wochokera ku Horebu wofikira ku Kadesi-Baranea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.

3 Ndipo kunali, chaka cha makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israele, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;

4 atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.

5 Tsidya lija la Yordani, m’dziko la Mowabu, Mose anayamba kufotokozera chilamulo ichi, ndi kuti,

6 Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife mu Horebu, ndi kuti Yakwanira nthawi yokhala inu m’phiri muno;

7 bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kuchidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwera, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebanoni, kufikira mtsinje waukulu wa Yufurate.

8 Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.

9 Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;

10 Yehova Mulungu wanu anakuchulukitsani, ndipo taonani, lero muchuluka ngati nyenyezi za kumwamba.

11 Yehova Mulungu wa makolo anu, achulukitsire chiwerengero chanu chalero ndi chikwi chimodzi, nakudalitseni monga Iye ananena nanu!

12 Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu?

13 Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akulu anu.

14 Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwachita.

15 Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu.

16 Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye.

17 Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang’ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.

18 Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzichita.

19 Pamenepo tinayenda ulendo kuchokera ku Horebu, ndi kubzola m’chipululu chachikulu ndi choopsa chija chonse munachionachi, panjira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi-Baranea.

20 Ndipo ndinati kwa inu, Mwafikira mapiri a Aamori, amene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

21 Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamachita mantha, musamatenga nkhawa.

22 Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komwemo, ndi za mizinda yoti tidzafikako.

23 Ndipo chinandikomera chinthu ichi; ndipo ndinatenga amuna khumi ndi awiri a inu, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

24 amenewa anatembenuka nakwera kumapiri nalowa ku chigwa cha Esikolo, nachizonda.

25 Ndipo anatengako zipatso za dzikoli m’manja mwao, natsikira nazo kwa ife, natibwezera mau ndi kuti, Dzikoli Yehova Mulungu wathu atipatsa ndi labwino.

26 Koma simunafune kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu.

27 Ndipo munadandaula m’mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, Iye anatitulutsa m’dziko la Ejipito, kutipereka m’manja mwa Aamori, ationonge.

28 Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m’mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.

29 Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamachita mantha nao.

30 Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu;

31 ndi kuchipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wake wamwamuna, m’njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m’malo muno.

32 Koma m’chinthu ichi simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,

33 amene anakutsogolerani m’njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.

34 Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,

35 Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.

36 Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.

37 Yehova anakwiya ndi inenso chifukwa cha inu, ndi kuti, Iwenso sudzalowamo.

38 Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israele.

39 Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.

40 Koma inu, bwererani, mukani ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

41 Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tachimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira nkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zake za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kunka kumapiri.

42 Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindili pakati panu; angakukantheni adani anu.

43 Pamene ndinanena ndi inu simunamvere; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri.

44 Ndipo Aamori, akukhala m’mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani mu Seiri, kufikira ku Horoma.

45 Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvere mau anu, kapena kukutcherani khutu.

46 Potero munakhala mu Kadesi masiku ambiri, monga mwa masiku munakhalako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/1-cc1ccbb8fbb00bf5a88eed87ee5245ec.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 2

1 Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kunka kuchipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.

2 Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,

3 Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kunka kumpoto.

4 Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzola malire a abale anu, ana a Esau okhala mu Seiri; ndipo adzakuopani; muchenjere ndithu;

5 musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai; pakuti ndapatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake.

6 Mugulane nao chakudya ndi ndalama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe.

7 Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m’chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.

8 Potero tinapitirira abale athu, ana a Esau okhala mu Seiri, njira ya chidikha, ku Elati ndi ku Eziyoni-Gebere. Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya chipululu cha Mowabu.

9 Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.

10 (Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki.

11 Anawayesa iwonso Arefaimu, monga Aanaki; koma Amowabu awatcha Aemimu.

12 Ndipo Ahori anakhala mu Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m’malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).

13 Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi.

14 Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m’chigono, monga Yehova adawalumbirira.

15 Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m’chigono, kufikira adawatha.

16 Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu,

17 Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,

18 Lero lomwe utumphe malire a Mowabu, ndiwo Ari.

19 Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawavuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale laolao.

20 (Ilinso aliyesa dziko la Arefaimu; Arefaimu anakhalamo kale; koma Aamoni awatcha Azamzumimu;

21 ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m’malo mwao;

22 monga Iye anachitira ana a Esau, akukhala mu Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m’malo mwao kufikira lero lomwe.

23 Kunena za Aavimu akukhala m’midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m’malo mwao).

24 Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m’dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.

25 Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.

26 Ndipo ndinatuma amithenga ochokera ku chipululu cha Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,

27 Ndipitire m’dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,

28 Undigulitse chakudya ndi ndalama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndalama, kuti ndimwe; chokhachi ndipitire choyenda pansi;

29 monga anandichitira ana a Esau akukhala mu Seiri, ndi Amowabu akukhala mu Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m’dzanja lanu, monga lero lino.

31 Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lake pamaso pako; yamba kulandira dziko lake likhale lakolako.

32 Pamenepo Sihoni anatuluka kukomana nafe, iye ndi anthu ake onse, kumenyana nafe nkhondo ku Yahazi.

33 Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse.

34 Ndipo muja tinalanda mizinda yake yonse; ndipo tinaononga konse mizinda yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense.

35 Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za mizinda tidailanda.

36 Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.

37 Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikize; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi mizinda ya kumapiri, ndi kwina kulikonse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/2-6f4dc7a4f274178cf7e741faa217c2f5.mp3?version_id=1068—