Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 13

Kuposa kwa Chikondi

1 Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi aangelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.

2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.

3 Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.

4 Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,

5 sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;

6 sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;

7 chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.

8 Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.

9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.

10 Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.

11 Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.

12 Pakuti tsopano tipenya m’kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.

13 Ndipo tsopano zitsala zitatu izi: chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/13-59be74f2e331cc2e9e24b4a393cdee84.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 14

Mphatso ya kunenera iposa ya malilime

1 Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere.

2 Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.

3 Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa.

4 Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangiriraMpingo.

5 Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.

6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m’vumbulutso, kapena m’chidziwitso, kapena m’chinenero, kapena m’chiphunzitso?

7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa?

8 Pakuti ngati lipenga lipereka mau osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?

9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.

10 Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau padziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.

11 Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine.

12 Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo.

13 Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.

14 Pakuti ngati ndipemphera m’lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.

15 Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.

16 Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzatiAmenbwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?

17 Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe.

18 Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19 koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m’lilime.

20 Abale, musakhale ana m’chidziwitso, koma m’choipa khalani makanda, koma m’chidziwitso akulu misinkhu.

21 Kwalembedwa m’chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22 Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.

23 Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka?

24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

25 zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.

Chipembedzo chichitike molongosoka

26 Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.

27 Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.

28 Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.

29 Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.

30 Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo.

31 Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;

32 ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;

33 pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.

34 Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.

35 Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.

36 Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha?

37 Ngati wina ayesa kuti alimneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.

38 Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.

39 Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.

40 Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/14-73ce4af24a4d9a4a6d78295b4fe5a292.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 15

Za kuuka kwa akufa

1 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,

2 umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.

3 Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kutiKhristuanafera zoipa zathu, monga mwa malembo;

4 ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;

5 ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;

6 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;

7 pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwaatumwionse;

8 ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.

9 Pakuti ine ndili wamng’ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalondaMpingowa Mulungu.

10 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.

11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupirira.

12 Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa?

13 Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwe;

14 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.

15 Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitse, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa.

16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Khristunso sanaukitsidwe;

17 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake; muli chikhalire m’machimo anu.

18 Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika.

19 Ngati tiyembekezera Khristu m’moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse.

20 Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.

21 Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.

22 Pakuti monga mwaAdamuonse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.

23 Koma yense m’dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.

24 Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.

25 Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.

26 Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.

27 Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.

28 Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.

29 Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?

30 Nanga ifenso tili m’moopsa bwanji nthawi zonse?

31 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwaKhristuYesu, Ambuye wathu.

32 Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.

33 Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.

34 Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.

35 Koma wina adzati, Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?

36 Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa;

37 ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina;

38 koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbeu yonse thupi lakelake.

39 Nyama yonse siili imodzimodzi; koma ina ndi ya anthu, ndi ina ndiyo nyama ya zoweta, ndi ina ndiyo nyama ya mbalame, ndi ina ya nsomba.

40 Palinso matupi am’mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam’mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.

41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi mu ulemerero.

42 Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m’chivundi, liukitsidwa m’chisavundi;

43 lifesedwa m’mnyozo, liukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m’chifooko, liukitsidwa mumphamvu;

44 lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.

45 Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.

46 Koma chauzimu sichili choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu.

47 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.

48 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.

49 Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo.

50 Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.

51 Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,

52 m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.

53 Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa.

54 Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m’chigonjetso.

55 Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?

56 Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo:

57 koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

58 Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/15-2f7b137e8c952e88d37426bd21f54b15.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 16

Zopereka za kwa Akhristu a ku Yerusalemu

1 Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangizaMipingoya ku Galatiya, motero chitani inunso.

2 Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.

3 Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi makalata, apite nayo mphatso yanu kuYerusalemu.

4 Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.

Za maulendo akudza, ndi malonje a Paulo

5 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya;

6 ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.

7 Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.

8 Koma ndidzakhala ku Efeso kufikiraPentekoste.

9 Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.

10 Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;

11 chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.

12 Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.

13 Dikirani, chilimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.

14 Zanu zonse zichitike m’chikondi.

15 Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba chaAkaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),

16 kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito.

17 Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.

18 Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muzindikire otere.

19 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m’nyumba yao.

20 Akupatsani moni abale onse. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kopatulika.

21 Ndikupereka moni ine Paulo ndi dzanja langa.

22 Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.

23 Chisomo cha Ambuye YesuKhristuchikhale ndi inu.

24 Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/16-ace8df393251fd7d667478e3f41aadd2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yachiwiri ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Akorinto

inalembedwa panthawi imene ubale wake ndi mpingo wa ku Korinto sunali bwino konse. Anthu ena a ku mpingo wa ku Korinto ankamunena Paulo, komabe iye anaonetsa kuti amafunitsitsa kuti ayanjane naonso ndipo izi zitachitika, iye anakondwera kwambiri.

Mu gawo loyamba la kalatayi Paulo akukamba za ubale wake ndi mpingo wa ku Korinto, ndipo akulongosola chifukwa chimene iye anawayankha mokwiya potsata chipongwe chimene iwo anamuchitira komanso za mtsutsano umene unalipo mu mpingowo. Iye akulongosola kuti ali ndi chimwemwe kuti kukwiya kwake kunathandizira kuti iwo alape ndi kuyanjana. Kenaka akuwupempha mpingowo kuti upereke moolowa manja pothandiza Akhristu osowa a ku Yudeya. Mu mitu yomalizira, Paulo akuteteza utumiki wake wa utumwi kwa anthu ochepa a ku Korinto amene adadzikhazikitsa wokha ngati atumwi enieni, namanena kuti Paulo ndi mtumwi wonyenga.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-11

Paulo ndi mpingo wa ku Korinto 1.12—7.16

Chopereka cha Akhristu a ku Yudeya 8.1—9.15

Paulo adziteteza pa udindo wake monga mtumwi 10.1—13.10

Mau omaliza 13.11-14

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 1

1 Paulo,mtumwiwaKhristuYesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwaMpingowa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali muAkayamonse:

2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chiyamiko pa matonthozo a Mulungu

3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,

4 wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

5 Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.

6 Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.

7 Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.

8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho mu Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;

9 koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;

10 amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;

11 pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.

Chifukwa cha kuchedwa Paulo kudza ku Korinto

12 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m’chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m’nzeru ya thupi, koma m’chisomo cha Mulungu tinadzisunga m’dziko lapansi, koma koposa kwa inu.

13 Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga, kapenanso muvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti mudzavomereza kufikira chimaliziro;

14 monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m’tsiku la Ambuye wathu Yesu.

15 Ndipo m’kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nacho chisomo chachiwiri;

16 ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.

17 Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?

18 Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhale eya ndi iai.

19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhale eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.

20 Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa IyeAmen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

21 Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;

22 amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

23 Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.

24 Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/1-082e8bba3815b27435b39e619dbbf640.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 2

1 Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni.

2 Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni?

3 Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse.

4 Pakuti m’chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa.

5 Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititse chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse.

6 Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira;

7 kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.

8 Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.

9 Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m’zonse.

10 Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso paKhristu;

11 kuti asatichenjerereSatana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.

12 Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,

13 ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya.

Makhalidwe ndi zipatso za utumiki wa Paulo

14 Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m’chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.

15 Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa;

16 koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

17 Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/2-c4b1668cccf3b2bfa834370cbe557c6a.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 3

1 Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?

2 Inu ndinu kalata yathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;

3 popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata yaKhristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome amiyala, koma m’magome a mitima yathupi.

4 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu:

5 si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;

6 amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.

7 Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m’miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang’anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:

8 koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala mu ulemerero?

9 Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri.

10 Pakutinso chimene chinachitidwa cha ulemerero sichinachitidwe cha ulemerero m’menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo.

11 Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala mu ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili mu ulemerero.

12 Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu,

13 ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang’anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa;

14 koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.

15 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao.

16 Koma pamene akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chichotsedwa.

17 Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

18 Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/3-6a88c6d8f884f0eb8f463b4c541c9820.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 4

Paulo alalikira Yesu yekhayekha

1 Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka;

2 koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.

3 Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika;

4 mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero waKhristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.

5 Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma YesuKhristuAmbuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.

6 Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m’mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.

7 Koma tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;

8 ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi;

9 olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;

10 nthawi zonse tilikusenzasenza m’thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m’thupi mwathu.

11 Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m’thupi lathu lakufa.

12 Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu.

13 Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula;

14 podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.

15 Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.

Chipatso cha kumva zowawa. Zosaoneka zilinganizidwa ndi zooneka

16 Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

17 Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;

18 popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/4-f0cff854b9bf218f95d71864820da0f7.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 5

1 Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.

2 Pakutinso m’menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba;

3 ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche.

4 Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.

5 Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.

6 Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m’thupi, sitili kwa Ambuye.

7 (Pakuti tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe);

8 koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m’thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.

9 Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye.

10 Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza waKhristu, kuti yense alandire zochitika m’thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.

Utumiki wa chiyanjanitso

11 Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m’zikumbu mtima zanu.

12 Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.

13 Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.

14 Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;

15 ndipo adafera onse kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma mwa Iye amene adawafera iwo, nauka.

16 Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.

17 Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

18 Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;

19 ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.

20 Chifukwa chake tili atumiki m’malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m’malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

21 Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/5-62a841973f31974eb932ff57b097646f.mp3?version_id=1068—