Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 3

Chifukwa cha malekano ao

1 Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwaKhristu.

2 Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi;

3 pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

4 Pakuti pamene wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mnzake, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi?

5 Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.

6 Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.

7 Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.

8 Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.

Akhristu ali nyumba ya Mulungu, Yesu ali maziko a nyumbayi

9 Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.

10 Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang’anire umo amangira pamenepo.

11 Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo YesuKhristu.

12 Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide,siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu,

13 ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m’moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.

14 Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho.

15 Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.

16 Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

17 Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

18 Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m’nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.

19 Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m’chenjerero lao;

20 ndiponso Ambuye azindikira zolingirira za anzeru, kuti zili zopanda pake.

21 Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu;

22 ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu;

23 koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/3-d6ab084e105bccde0d74c47193e7fa22.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 4

Atumiki a Khristu ndi ogawira zinsinsi za Mulungu

1 Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki aKhristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.

2 Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang’ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.

4 Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m’menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.

5 Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Kudzikuza kwa Akorinto, kudzichepetsa kwa Atumwi

6 Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.

7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?

8 Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.

9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ifeatumwiotsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwaangelo, ndi kwa anthu.

10 Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.

11 Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;

12 ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

13 ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.

14 Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa.

15 Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwaKhristuYesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.

16 Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

17 Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo muMipingoyonse.

18 Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.

19 Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.

20 Pakuti ufumu wa Mulungu suli m’mau, koma mumphamvu. Mufuna chiyani?

21 Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/4-96c635c252617c83e02222b74e6da626.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 5

Za chigololo mu Mpingo wa ku Korinto. Awadzudzulapo

1 Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwaamitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.

2 Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.

3 Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndilipo,

4 m’dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,

5 kumpereka iye wochita chotere kwaSatana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye Yesu.

6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse?

7 Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. PakutinsoPaskawathu waphedwa, ndiyeKhristu;

8 chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi.

9 Ndinalembera inu m’kalata ija, kuti musayanjane ndi achigololo;

10 si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m’dziko lapansi;

11 koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.

12 Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m’katimo simuwaweruze ndi inu,

13 koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/5-8de96fb35045b32164ccac34373262e7.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 6

Awadzudzula pa milandu ya pakati pa abale

1 Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?

2 Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa?

3 Kodi simudziwa kuti tidzaweruzaangelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?

4 Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe muMpingo?

5 Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,

6 koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira?

7 Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?

8 Koma muipsa, nimunyenga, ndipo mutero nao abale anu.

9 Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,

10 kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

11 Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye YesuKhristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Matupi athu ali ziwalo za Khristu

12 Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.

13 Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;

14 koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake.

15 Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero iai.

16 Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.

17 Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.

18 Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.

19 Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

20 Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/6-b5158dd682c61c8a882f6284dbf8cfc3.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 7

Mau a za ukwati

1 Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.

2 Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

3 Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.

4 Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.

5 Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kutiSatanaangakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.

6 Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira.

7 Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndili ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti.

8 Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.

9 Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

10 Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,

11 komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.

12 Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.

13 Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo.

14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.

15 Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M’milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.

16 Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?

17 Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika muMipingoyonse.

18 Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe.

19 Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.

20 Yense akhale m’maitanidwe m’mene anaitanidwamo.

21 Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko.

22 Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo waKhristu.

23 Munagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu.

24 Yense, m’mene anaitanidwamo, abale, akhale momwemo ndi Mulungu.

25 Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.

26 Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo ino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.

27 Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.

28 Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m’thupi, ndipo ndikulekani.

29 Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;

30 ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;

31 ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.

32 Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye;

33 koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake.

34 Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

35 Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.

36 Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe.

37 Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino.

38 Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita koposa.

39 Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.

40 Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/7-660ef4124678503544bd0fac8fb79874.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 8

Kunena za kudya nyama yoperekedwa nsembe kwa mafano

1 Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.

2 Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.

3 Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.

4 Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.

5 Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m’mwamba, kapena padziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;

6 koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi YesuKhristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.

7 Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbumtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa.

8 Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tilibe kupindulako.

9 Koma yang’anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale chokhumudwitsa ofookawo.

10 Pakuti wina akaona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya mu Kachisi wa fano, kodi chikumbumtima chake, popeza ali wofooka, sichidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?

11 Pakuti mwa chidziwitso chako wofookayo atayika, ndiye mbale amene Khristu anamfera.

12 Koma pakuchimwira abale, ndi kulasa chikumbumtima chao chofooka, muchimwira kotero Khristu.

13 Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/8-438bb66241a7b56ca0560c0f2ca78999.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 9

Ufulu ndi ulamuliro wa mtumwiyo

1 Kodi sindine mfulu? Kodi sindinemtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?

2 Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.

3 Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi:

4 Kodi tilibe ulamuliro wa kudya ndi kumwa?

5 Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?

6 Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito?

7 Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

8 Kapena chilamulo sichinenanso zomwezo?

9 Pakuti m’chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng’ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng’ombe?

10 Kapena achinena ichi konsekonse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nao.

11 Ngati takufeserani inu zauzimu, kodi nchachikulu ngati ife tituta za thupi lanu?

12 Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino waKhristu.

13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

14 Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

Kudzipereka kwa mtumwiyo. Makani a liwiro a Mkhristu

15 Koma ine sindinachite nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga.

16 Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.

17 Pakuti ngati ndichita ichi chivomerere, mphotho ndili nayo; koma ngati si chivomerere, anandikhulupirira mu udindo.

18 Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.

19 Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.

20 Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhale ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;

21 kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.

22 Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.

23 Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

24 Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.

25 Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.

26 Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga;

27 koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/9-5728bf7e7c2e3d49a4a549508372b2d1.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 10

Tisayese dala Mulungu monga Israele

1 Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;

2 nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m’nyanja,

3 nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;

4 namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiyeKhristu.

5 Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwere nao; pakuti anamwazika m’chipululu.

6 Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.

7 Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.

8 Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.

9 Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.

10 Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.

11 Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.

12 Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.

13 Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Za kupembedza mafano, za kuyanjana ndi ziwanda

14 Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

15 Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena.

16 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?

17 Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.

18 Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?

19 Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi?

20 Koma nditi kuti zimeneamitunduapereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

21 Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.

22 Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?

Mkhristu ndiye mfulu koma wosamalira ena

23 Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

24 Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.

25 Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbumtima;

26 pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.

27 Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbumtima.

28 Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbumtima.

29 Ndinena chikumbumtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbumtima cha wina?

30 Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo?

31 Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

32 Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapenaMpingowa Mulungu;

33 monga inenso ndikondweretsa onse m’zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/10-7ee5c8f016dffdb4a67765fd2cac3f0f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 11

1 Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanzaKhristu.

Za akazi mu Mpingo wa Ambuye

2 Ndipo ndikutamandani kuti m’zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.

3 Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.

4 Mwamuna yense woveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake.

5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.

6 Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.

7 Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

8 Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;

9 pakutinso mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi;

10 koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa chaangelo.

11 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.

12 Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu.

13 Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?

14 Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chinyozetsa iye?

15 Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.

16 Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapenaMpingowa Mulungu.

Zosayenera pa madyerero a chikondi. Machitidwe a Mgonero wa Ambuye

17 Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa.

18 Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndivomereza penapo.

19 Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.

20 Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;

21 pakuti pakudyaku yense ayamba watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

22 Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m’menemo? Sindikutamani.

23 Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;

24 ndipo m’mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.

25 Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa.

26 Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.

27 Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho.

29 Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.

30 Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.

31 Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa.

32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

33 Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.

34 Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/11-3a196396f2b1e62185a8dd66e86996d8.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 12

Mphatso za Mzimu zisiyana

1 Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa.

2 Mudziwa kuti pamene munaliamitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.

3 Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.

4 Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.

5 Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo.

6 Ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.

7 Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

8 Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:

9 kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo;

10 ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

11 Koma zonse izi achita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afuna.

Thupi ndi limodzi, zingakhale ziwalo zisiyana

12 Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonsoKhristu.

13 Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m’thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

14 Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi, koma zambiri.

15 Ngati phazi likati, Popeza sindili dzanja, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?

16 Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindili diso, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?

17 Ngati thupi lonse likadakhala diso, kukadakhala kuti kununkhiza?

18 Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m’thupi, monga anafuna.

19 Koma ngati zonse zikadakhala chiwalo chimodzi, likadakhala kuti thupi?

20 Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi.

21 Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.

22 Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofooka m’thupi, zifunika;

23 ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m’thupi, pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa.

24 Koma zokoma zathu zilibe kusowa; koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho;

25 kuti kusakhale chisiyano m’thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake.

26 Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.

27 Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

28 Ndipotu Mulungu anaika ena muMpingo, poyambaatumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.

29 Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ochita zozizwa?

30 Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau?

31 Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/12-19cbda32c38bca83612cbbe29e58f93b.mp3?version_id=1068—