Categories
LUKA

LUKA 6

Yesu Mbuye wa tsiku la Sabata

1 Ndipo kunali tsiku laSabata, Iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipoophunziraake analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m’manja mwao, nadya.

2 KomaAfarisiena anati, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika tsiku la Sabata?

3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale chimene anachita Davide, pamene paja anamva njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi;

4 kuti analowa m’nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?

5 Ndipo Iye ananena kwa iwo, kuti,Mwana wa Munthuali Mbuye wa tsiku la Sabata.

Achiritsa munthu wa dzanja lopuwala

6 Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, Iye analowa m’sunagoge, naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja linali lopuwala.

7 Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye.

8 Koma Iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lake lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.

9 Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?

10 Ndipo pamene anaunguzaunguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako. Ndipo iye anatero, ndi dzanja lake linabwerera momwe.

11 Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.

Yesu asankha ophunzira khumi ndi awiri

12 Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m’kupemphera kwa Mulungu.

13 Ndipo kutacha, anaitana ophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawatchanso dzina laoatumwi:

14 Simoni, amene anamutchanso Petro, ndi Andrea mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeo,

15 ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwaZelote,

16 ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Iskariote, amene anali wompereka Iye.

Chiphunzitso cha paphiri

17 Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndiYerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;

18 ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa,

19 ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nkuchiritsa onsewa.

20 Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

21 Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka.

22 Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu.

23 Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo ao anawachitira aneneri zonga zomwezo.

24 Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandira chisangalatso chanu.

25 Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.

26 Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo ao anawatero momwemo aneneri onama.

27 Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu,

28 dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.

29 Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako.

30 Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.

31 Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.

32 Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti ochimwa omwe akonda iwo akukondana nao.

33 Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu ochimwa omwe amachita chomwecho.

34 Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.

35 Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.

36 Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

37 Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.

38 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m’manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

39 Ndipo Iye ananenanso naofanizo, Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m’mbuna?

40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m’mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.

41 Ndipo uyang’aniranji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda wa m’diso la iwe mwini suuzindikira?

42 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m’diso lako, wosayang’anira iwe mwini mtanda uli m’diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m’diso lako, ndipo pomwepo udzayang’anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m’diso la mbale wako.

43 Pakuti palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zovunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino.

44 Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa.

45 Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m’choipa chake: pakuti m’kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.

46 Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena?

47 Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwachita, ndidzakusonyezani amene afanana naye.

48 Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunathe kuigwedeza; chifukwa idamangika bwino.

49 Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/6-95fca2c57f68424ae8ae883c4645b1b8.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 7

Kenturiyo wa ku Kapernao

1 Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m’makutu a anthu, analowa mu Kapernao.

2 Ndipo kapolo wakenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.

3 Ndipo pamene iye anamva za Yesu, anatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa kapolo wake.

4 Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi;

5 pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ifesunagoge.

6 Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi pa nyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa tsindwi langa;

7 chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa.

8 Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita.

9 Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeze, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.

10 Ndipo pakubwera kunyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wachira ndithu.

Aukitsa mnyamata ku Naini

11 Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumzinda, dzina lake Naini; ndipoophunziraake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye.

12 Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye.

13 Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.

14 Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.

15 Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.

16 Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti,Mneneriwamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.

17 Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya yense, ndi ku dziko lonse loyandikira.

Amithenga a Yohane Mbatizi

18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi.

19 Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

20 Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

21 Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.

22 Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhateakonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

23 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

24 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

25 Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Onani, iwo akuvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m’nyumba za mafumu.

26 Koma munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri.

27 Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye,

Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere,

amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.

28 Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng’ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.

29 Ndipo anthu onse ndiamisonkhoomwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

30 KomaAfarisindi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.

31 Ndipo, ndidzafanizira ndi chiyani anthu a mbadwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani?

32 Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavine ai; tinabuma maliro, ndimo simunalire ai.

33 Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda.

34 Mwana wa Munthuwafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!

35 Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse.

Mkazi adzoza mapazi a Yesu

36 Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m’nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya.

37 Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m’mzindamo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m’nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino,

38 naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.

39 Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.

40 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani.

41 Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu.

42 Popeza analibe chobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Chotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?

43 Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa.

44 Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m’mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m’nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.

45 Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine.

46 Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.

47 Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang’ono, iye akonda pang’ono.

48 Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa.

49 Ndipo iwo akuseama naye pachakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo?

50 Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/7-543b8d72ae78bbff60c8e929963b6646.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 8

Akazi otumikira Yesu ndi chuma chao

1 Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,

2 ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,

3 ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao waHerode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.

Fanizo la Wofesa

4 Ndipo pamene khamu lalikulu la anthu linasonkhana, ndi anthu a kumidzi yonse anafika kwa Iye, anati mwafanizo:

5 Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m’kufesa kwake zina zinagwa m’mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m’mlengalenga zinatha kuzidya.

6 Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho.

7 Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nkuzitsamwitsa.

8 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.

9 Ndipoophunziraake anamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili lili lotani?

10 Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.

11 Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu.

12 Ndipo za m’mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m’mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.

13 Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.

14 Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m’kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

15 Ndipo zija za m’nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

Fanizo la nyali

16 Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

17 Pakuti palibe chinthu chobisika, chimene sichidzakhala choonekera; kapena chinsinsi chimene sichidzadziwika ndi kuvumbuluka.

18 Chifukwa chake yang’anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.

Amake ndi abale a Yesu

19 Ndipo anadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sanakhoze kumfika, chifukwa cha khamu la anthu.

20 Ndipo anamuuza Iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu.

21 Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita.

Yesu atontholetsa namondwe

22 Ndipo panali limodzi la masiku aja, Iye analowa m’ngalawa, ndi ophunzira ake; nati kwa iwo, Tiolokere kutsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.

23 Ndipo m’mene iwo anali kupita pamadzi, Iye anagona tulo. Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa.

24 Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata.

25 Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo m’kuchita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?

Munthu wa ku Gerasa wogwidwa ndi ziwanda

26 Ndipo iwo anakocheza kudooko ku dziko la Agerasa, ndilo lopenyana ndi Galileya.

27 Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumzinda, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m’nyumba, koma m’manda.

28 Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau aakulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.

29 Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.

30 Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.

31 Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya.

32 Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m’phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.

33 Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nkulowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanjamo, nilitsamwa.

34 Ndipo akuwetawo m’mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza okhala mumzinda ndi kuminda.

35 Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.

36 Ndipo amene anaona anawauza iwo machiritsidwe ake a wogwidwa chiwandayo.

37 Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Ndipo Iye analowa m’ngalawa, nabwerera.

38 Ndipo munthuyo amene ziwanda zinatuluka mwa iye anampempha Iye akhale ndi Iye; koma anamuuza apite, nanena,

39 Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumzinda wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.

Mwana wamkazi wa Yairo. Mkazi wokhudza chofunda cha Yesu

40 Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye.

41 Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wasunagoge; ndipo anagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze kunyumba kwake;

42 chifukwa anali naye mwana wamkazi mmodzi yekha, wa zaka zake ngati khumi ndi ziwiri, ndipo analinkumwalira iye. Koma pakupita Iye anthu a mipingo anakanikizana naye.

43 Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing’anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,

44 anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chovala chake; ndipo pomwepo nthenda yake inaleka.

45 Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.

46 Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti ndazindikira Ine kuti mphamvu yatuluka mwa Ine.

47 Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisike, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti anachiritsidwa pomwepo.

48 Ndipo Iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

49 M’mene Iye anali chilankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usamvute Mphunzitsi.

50 Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupirira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.

51 Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake.

52 Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.

53 Ndipo anamseka Iye pwepwete podziwa kuti anafa.

54 Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka.

55 Ndipo mzimu wake unabwera, ndipo anauka pomwepo; ndipo Iye anawauza kuti ampatse kanthu ka kudya.

56 Ndipo atate wake ndi amake anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu aliyense chimene chinachitika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/8-aaf6e03713788729cc74446afa83cf79.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 9

Yesu atuma ophunzira ake kukalalikira mau

1 Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.

2 Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala.

3 Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri.

4 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko.

5 Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m’mene mutuluka m’mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.

6 Ndipo iwo anatuluka, napita m’midzi yonse, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuchiritsa ponse.

Herode ndi Yohane Mbatizi

7 NdipoHerodechiwangacho anamva mbiri yake ya zonse zinachitika; ndipo inamthetsa nzeru, chifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa;

8 koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kutimneneriwina wa akale aja anauka.

9 Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona Iye.

Yesu achulukitsa mikate

10 Ndipo atabweraatumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumzinda dzina lake Betsaida.

11 Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.

12 Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumadera, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno.

13 Koma anati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

14 Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwaophunziraake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu.

15 Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo.

16 Ndipo Iye, m’mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang’ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo.

17 Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, madengu khumi ndi awiri.

Petro avomereza Khristu

18 Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?

19 Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.

20 Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati,Khristuwa Mulungu.

21 Ndipo Iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ichi kwa munthu aliyense;

22 nati, Kuyenera kutiMwana wa Munthuamve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.

Za kusenza mtanda

23 Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.

24 Pakuti aliyense amene akafuna kupulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma aliyense amene akataya moyo wake chifukwa cha Ine, iye adzaupulumutsa uwu.

25 Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake?

26 Pakuti aliyense amene adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi waangelooyera.

27 Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.

Mawalitsidwe a Yesu paphiri

28 Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m’phiri kukapemphera.

29 Ndipo m’kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira.

30 Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;

31 amene anaonekera mu ulemerero, nanena za kumuka kwake kumene Iye ati adzatsiriza kuYerusalemu.

32 Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m’mene anayera m’maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.

33 Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.

34 Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo.

35 Ndipo munatuluka mau mumtambo, nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani Iye.

36 Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.

Achiritsa mwana wodwala khunyu

37 Ndipo panali, m’mawa mwake, atatsika m’phiri, khamu lalikulu la anthu linakomana naye.

38 Ndipo onani, anafuula munthu wa m’khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang’anirani mwana wanga; chifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine:

39 ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng’amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.

40 Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe.

41 Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.

42 Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng’ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.

43 Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,

44 Alowe mau amenewa m’makutu anu; pakuti Mwana wa Munthu adzaperekedwa m’manja a anthu.

45 Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.

Wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba

46 Ndipo anayamba kutsutsana kuti wamkulu mwa iwo ndani.

47 Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pake, nati kwa iwo,

48 Amene aliyense akalandire kamwana aka m’dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng’onong’ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.

Osatsutsana nafe athandizana nafe

49 Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.

50 Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.

Asamariya amkaniza Yesu

51 Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,

52 natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m’mudzi waAsamariya, kukamkonzera Iye malo.

53 Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu.

54 Ndipo pamene ophunzira ake Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?

55 Koma Iye anapotoloka nawadzudzula.

56 Ndipo anapita kumudzi kwina.

Matsatidwe a Yesu

57 Ndipo m’mene iwo analikuyenda m’njira, munthu anati kwa Iye, Ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako.

58 Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu.

59 Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndiyambe ndamuka kuika maliro a atate wanga.

60 Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.

61 Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muyambe mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga.

62 Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/9-99296c912029fd5fc8bb7bc77ff750ff.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 10

Yesu atuma ophunzira makumi asanu ndi awiri

1 Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.

2 Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.

3 Mukani; taonani, Ine ndituma inu ngati anaankhosa pakati pa mimbulu.

4 Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira.

5 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowamo muyambe mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi.

6 Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m’menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.

7 Ndipo m’nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m’nyumba.

8 Ndipo m’mudzi uliwonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani;

9 ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowako,

10 ndipo salandira inu, m’mene mwatuluka kumakwalala ake nenani,

11 Lingakhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.

12 Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodomu kudzapiririka kuposa mudzi umenewo.

13 Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika mu Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa.

14 Koma ku Tiro ndi Sidoni kudzapiririka m’chiweruziro, koposa inu.

15 Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku dziko la akufa.

16 Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine.

17 Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.

18 Ndipo anati kwa iwo, NdinaonaSatanaalinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba.

19 Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

20 Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.

Yesu akondwera

21 Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.

22 Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.

23 Ndipo m’mene anapotolokera kwaophunziraake, ali pa okha, anati, Odala masowo akuona zimene muona.

24 Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuona zimene inu muziona, koma sanazione; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimve.

Fanizo la Msamariya wachifundo

25 Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?

26 Ndipo anati kwa iye, M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji?

27 Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.

28 Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.

29 Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?

30 Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera kuYerusalemukunka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.

31 Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina.

32 Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina.

33 KomaMsamariyawina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,

34 nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.

35 Ndipo m’mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.

36 Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?

37 Ndipo anati, Iye wakumchitira chifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita nuchite iwe momwemo.

Marita ndi Maria

38 Ndipo pakupita paulendo pao Iye analowa m’mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita anamlandira Iye kunyumba kwake.

39 Ndipo anali ndi mbale wake wotchedwa Maria, ndiye wakukhala pa mapazi a Ambuye, namva mau ake.

40 Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.

41 Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri;

42 koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/10-267ea5208d698f9d5dec155e7c29b820.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 11

Pemphero la Ambuye

1 Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m’mene analeka, wina waophunziraake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.

2 Ndipo anati kwa iwo, M’mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwa; Ufumu wanu udze;

3 tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.

4 Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.

Fanizo la bwenzi laliuma

5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;

6 popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo ndipo ndilibe chompatsa;

7 ndipo iyeyu wa m’katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindingathe kuuka ndi kukupatsa?

8 Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa.

9 Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.

10 Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

11 Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m’malo mwa nsomba?

12 Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira?

13 Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?

Za Yesu ndi Belezebulu

14 Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

15 Koma ena mwa iwo anati, NdiBelezebulumkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.

16 Koma ena anamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba.

17 Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m’kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m’kati mwake igwa.

18 Ndiponso ngatiSatanaagawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu.

19 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.

20 Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.

21 Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere;

22 koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.

23 Iye wosavomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.

24 Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako;

25 ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka.

26 Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.

27 Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.

28 Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.

Chizindikiro cha Yona

29 Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona.

30 Pakuti monga ngati Yona anali chizindikiro kwa Aninive, chotero adzakhalansoMwana wa Munthukwa mbadwo uno.

31 Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano.

32 Amuna a ku Ninive adzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.

Za nyali ya thupi

33 Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m’chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.

34 Nyali ya thupi ndiyo diso lako; pamene paliponse diso lako lili langwiro thupi lako lonse liunikidwanso monsemo; koma likakhala loipa, thupi lako lomwe lili la mdima wokhawokha.

35 Potero yang’anira kuunika kuli mwa iwe kungakhale mdima.

36 Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe.

Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi

37 Ndipo pakulankhula Iye, anamuitanaMfarisikuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.

38 Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe.

39 Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa.

40 Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m’kati mwake?

41 Koma patsani mphatso yachifundo za m’katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.

42 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.

43 Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m’masunagoge, ndi kupatsidwa moni m’misika.

44 Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.

45 Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

46 Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.

47 Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.

48 Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

49 Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndiatumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

50 kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;

51 kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

52 Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.

53 Ndipo pamene Iye anatuluka m’menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumfunsa zinthu zambiri;

54 namlindira akakole kanthu kotuluka m’kamwa mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/11-2845763e9c31457eda97cf907371e2fd.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 12

Yesu awachenjeza za chinyengo

1 Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwaophunziraake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate chaAfarisi, chimene chili chinyengo.

2 Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

3 Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m’khutu, m’zipinda za m’kati chidzalalikidwa pa matsindwi a nyumba.

Awatchulira amene ayenera kumuopa

4 Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita.

5 Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kuGehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.

6 Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;

7 komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.

8 Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde,Mwana wa Munthuadzamvomereza iye pamaso paangeloa Mulungu;

9 Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.

10 Ndipo aliyense amene adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

11 Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m’sunagogendi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;

12 pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.

Fanizo la mwini chuma wopusa

13 Ndipo munthu wa m’khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye.

14 Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?

15 Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang’anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

16 Ndipo Iye ananena naofanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino.

17 Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga?

18 Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa.

19 Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

20 Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?

21 Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.

Nkhawa za moyo wathu

22 Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.

23 Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.

24 Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

25 Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake?

26 Kotero ngati simungathe ngakhale chaching’onong’ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?

27 Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomoni, mu ulemerero wake wonse sanavale ngati limodzi la awa.

28 Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wakuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang’ono?

29 Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.

30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a padziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.

31 Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuonjezerani.

32 Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34 Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

Fanizo la kapolo wochezera

35 Khalani odzimangira m’chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36 ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37 Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m’chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

38 Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.

39 Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe.

40 Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa Munthu akudza.

41 Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?

42 Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake?

43 Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero.

44 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.

45 Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;

46 mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

47 Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonze, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.

48 Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang’ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.

Yesu aponya moto padziko lapansi

49 Ine ndinadzera kuponya moto padziko lapansi; ndipo ndifunanji ngati unatha kuyatsidwa?

50 Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

51 Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere padziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;

52 pakuti kuyambira tsopano adzakhala m’nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

53 Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.

Zizindikiro za nyengo yake

54 Koma Iye ananenanso kwa makamu a anthu, Pamene paliponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero.

55 Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.

56 Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo ino?

57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

58 Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m’nyumba yandende.

59 Ine ndinena kwa iwe, Sudzatulukamo konse kufikira utalipira kakobiri kukumaliza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/12-23493812a929ede4ee5f12ee3c0fe5f3.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 13

Maphedwe a Agalileya, nsanja ya Siloamu

1 Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao.

2 Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akuchimwa koposa Agalileya onse, chifukwa anamva zowawa izi?

3 Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.

4 Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu?

5 Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.

Fanizo la mkuyu wosabala

6 Ndipo Iye ananenafanizoili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m’munda wake wampesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe.

7 Ndipo anati kwa wosungira munda wampesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake?

8 Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe;

9 ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.

Achiritsa mkazi wopeteka

10 Ndipo analikuphunzitsa m’sunagogemwina, tsiku laSabata.

11 Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.

12 Ndipo Yesu m’mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.

13 Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.

14 Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m’menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.

15 Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng’ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?

16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, ameneSatanaanammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?

17 Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m’khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye.

Fanizo la mpiru ndi la chotupitsa

18 Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani?

19 Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m’munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m’mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake.

20 Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani?

21 Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.

Khomo lopapatiza

22 Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.

23 Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo,

24 Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.

25 Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;

26 pomwepo mudzayamba kunena, Ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m’makwalala a kwathu;

27 ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama.

28 Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.

29 Ndipo anthu adzachokera kum’mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu.

30 Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo.

Amchenjeza Yesu za Herode. Yesu alirira Yerusalemu

31 Nthawi yomweyo anadzapoAfarisiena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwaHerodeafuna kupha Inu.

32 Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.

33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkucha, chifukwa sikuloleka kutimneneriaonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu.

34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m’mapiko ake, ndipo simunafunai!

35 Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m’dzina la Ambuye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/13-9528ed474be52e402ab33dfd17d49421.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 14

Yesu achiritsa munthu wambulu

1 Ndipo panali pamene Iye analowa m’nyumba ya mmodzi wa akulu aAfarisitsiku laSabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.

2 Ndipo onani, panali pamaso pake munthu wambulu.

3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai?

4 Koma iwo anakhala chete. Ndipo anamtenga namchiritsa, namuuza apite.

5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng’ombe yake itagwa m’chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?

6 Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi.

Fanizo la mipando ya ulemu

7 Ndipo Iye ananenafanizokwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,

8 Pamene paliponse waitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,

9 ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.

10 Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe.

11 Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.

12 Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.

13 Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;

14 ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.

Fanizo la phwando lalikulu

15 Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.

16 Koma anati kwa iye, Munthu wina anakonza phwando lalikulu; naitana anthu ambiri;

17 ndipo anatumiza kapolo wake pa nthawi ya phwando kukanena kwa oitanidwawo, Idzani, chifukwa zonse zakonzeka tsopano.

18 Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituluke kukauona; ndikupempha undilole ine ndisafika.

19 Ndipo anati wina, Ine ndagula ng’ombe za magoli asanu, ndipo ndinka kukaziyesa; ndikupempha undilole ine ndisafika.

20 Ndipo anati wina, Ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza.

21 Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mzinda, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.

22 Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo.

23 Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale.

24 Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa.

Womtsata Ambuye adzayesedwa

25 Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo Iye anapotoloka, nati kwa iwo,

26 Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzirawanga.

27 Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sangathe kukhala wophunzira wanga.

28 Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?

29 Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang’ana adzayamba kumseka iye,

30 ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.

Fanizo la mfumu yanzeru

31 Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sayamba wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri?

32 Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.

33 Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.

34 Kotero mchere uli wokoma; koma ngati mchere utasukuluka adzaukoleretsa ndi chiyani?

35 Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/14-dc3e05e0d7d0eea440279880ea6b7e76.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 15

Fanizo la nkhosa yosokera

1 Komaamisonkhoonse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva Iye.

2 NdipoAfarisindi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nao.

3 Koma anati kwa iwofanizoili, nanena,

4 Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?

5 Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ake wokondwera.

6 Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nao, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.

7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

Fanizo la ndalama yotayika

8 Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasilivakhumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza?

9 Ndipo m’mene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo.

10 Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso paangeloa Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.

Fanizo la mwana wolowerera

11 Ndipo Iye anati, Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri;

12 ndipo wamng’onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagawira za moyo wake.

13 Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng’onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.

14 Ndipo pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m’dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.

15 Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfumu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba.

16 Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.

17 Koma m’mene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?

18 Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu;

19 sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu.

20 Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.

21 Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.

22 Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake;

23 ndipo idzani naye mwanawang’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere;

24 chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.

25 Koma mwana wake wamkulu anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuimba ndi kuvina.

26 Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani?

27 Ndipo uyu anati kwa iye, Mng’ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwanawang’ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo.

28 Koma anakwiya, ndipo sanafune kulowamo. Ndipo atate wake anatuluka namdandaulira.

29 Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwire lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatse ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.

30 Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang’ombe wonenepa.

31 Koma iye ananena naye, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse zili zako.

32 Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng’ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/15-cafb9bb996ae86a039e1e01d7119cb3a.mp3?version_id=1068—