Categories
MARKO

MARKO 13

Yesu aneneratu za masautso alinkudza

1 Ndipo pamene analikutuluka Iye mu Kachisi, mmodzi waophunziraake ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.

2 Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.

3 Ndipo pamene anakhala Iye paphiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m’tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti,

4 Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse?

5 Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang’anirani kuti munthu asakusocheretseni.

6 Ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri.

7 Ndipo m’mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro.

8 Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake: padzakhala zivomezi m’malo m’malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.

9 Koma inu mudziyang’anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kubwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m’masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.

10 Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.

11 Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m’mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.

12 Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa.

13 Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.

Yesu aneneratu za chisautso chachikulu

14 Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:

15 ndi iye amene ali pamwamba pa tsindwi asatsike, kapena asalowe kukatulutsa kanthu m’nyumba mwake;

16 ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake.

17 Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awo!

18 Ndipo pempherani kuti kusakhale m’nyengo yachisanu.

19 Pakuti masiku aja padzakhala chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso, nthawi zonse.

20 Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.

21 Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, OnaniKhristuali pano; kapena, Onani, uko; musavomereze;

22 pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.

23 Koma yang’anirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike.

Yesu aneneratu kuti adzabwera

24 Koma m’masikuwo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake,

25 ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera m’mwamba ndi mphamvu zili m’mwamba zidzagwedezeka.

26 Ndipo pamenepo adzaonaMwana wa Munthualinkudza m’mitambo ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemerero.

27 Ndipo pamenepo adzatumaangelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.

28 Ndipo phunzirani ndi mkuyufanizolake; pamene pafika kuti nthambi yake ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ake, muzindikira kuti layandikira dzinja;

29 chomwecho inunso, pamene muona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo.

30 Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika.

31 Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.

32 Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo mu Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.

Za kulindirira

33 Yang’anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake.

34 Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire.

35 Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;

36 kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m’tulo.

37 Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/13-6d200414ac6ff9cc911b0268c801a7dc.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 14

Ansembe aakulu achita chiwembu pa Yesu

1 Ndipo popita masiku awiri kuli phwando laPaskandi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:

2 pakuti anati, Pachikondwerero ai, kuti pangakhale phokoso la anthu.

Phwando la ku Betaniya

3 Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate, m’mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino anaridoweniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.

4 Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji?

5 Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphamvu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo.

6 Koma Yesu anati, Mlekeni, mumvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino.

7 Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.

8 Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m’manda.

9 Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.

Yudasi apangana ndi ansembe aakulu

10 Ndipo Yudasi Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka napita kwa ansembe aakulu, kuti akampereke Iye kwa iwo.

11 Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino.

Paska wotsiriza

12 Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska,ophunziraananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?

13 Ndipo anatuma awiri a ophunzira ake, nanena nao, Lowani m’mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye;

14 ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Chilikuti chipinda cha alendo changa, m’menemo ndikadye Paska ndi ophunzira anga?

15 Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m’menemo mutikonzere.

16 Ndipo ophunzira anatuluka, nafika m’mzinda, napeza monga anati kwa iwo; ndipo anakonza Paska.

17 Ndipo pofika madzulo anadza Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

18 Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.

19 Anayamba iwo kukhala ndi chisoni, ndi kunena naye mmodzimmodzi, kuti, Ndine kodi?

20 Ndipo anati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m’mbale.

21 Pakuti Mwana wa Munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa Munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.

Mgonero wa Ambuye

22 Ndipo pamene iwo analikudya, Iye anatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, ananyema, napereka kwa iwo, kuti, Tengani; thupi langa ndi ili.

23 Ndipo anatenga chikho, ndipo pamene adayamika, anapereka kwa iwo; ndipo iwo onse anamweramo.

24 Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wachipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri.

25 Ndithu ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.

26 Ndipo ataimba nyimbo, anatuluka, namuka kuphiri la Azitona.

Yesu achenjeza Petro

27 Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa,

Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.

28 Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.

29 Koma Petro ananena naye, Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iai.

30 Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.

31 Koma iye analimbitsa mau chilimbitsire, kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo anatero.

Getsemani

32 Ndipo iwo anadza kumalo dzina lake Getsemani; ndipo ananena kwa ophunzira ake, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera.

33 Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.

34 Ndipo ananena nao, Moyo wanga uli wa chisoni chambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimundikire.

35 Ndipo Iye anapita m’tsogolo pang’ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire.

36 Ndipo ananena,Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.

37 Ndipo anadza nawapeza iwo ali m’tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?

38 Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m’kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.

39 Ndipo anachokanso, napemphera, nanena mau omwewo.

40 Ndipo anadzanso nawapeza ali m’tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwe chomyankha Iye.

41 Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m’manja a anthu ochimwa.

42 Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi.

Amgwira Yesu

43 Ndipo pomwepo, Iye ali chilankhulire, anadza Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ochokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu.

44 Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire.

45 Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena,Rabi; nampsompsonetsa.

46 Ndipo anamthira manja, namgwira.

47 Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lake, nakantha kapolo wake wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake.

48 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira Ine monga wachifwamba?

49 Masiku onse ndinali nanu mu Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwire Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwaniritsidwe.

50 Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.

51 Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atafundira pathupi nsalu yabafuta yokha; ndipo anamgwira;

52 koma iye anasiya nsaluyo, nathawa wamaliseche.

Yesu aweruzidwa ndi akulu a Ayuda

53 Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe aakulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi.

54 Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m’bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto.

55 Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeze.

56 Pakuti ambiri anamchitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingane.

57 Ndipo ananyamukapo ena, namchitira umboni wakunama, nanena kuti,

58 Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.

59 Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingane.

60 Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira mboni?

61 Koma anakhala chete, osayankha kanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Khristu, Mwana wake wa Wolemekezeka?

62 Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa Munthu alikukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.

63 Ndipo mkulu wa ansembe anang’amba malaya ake, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?

64 Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.

65 Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu.

Petro akana kuti sadziwa Yesu

66 Ndipo pamene Petro anali pansi m’bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;

67 ndipo anaona Petro alikuotha moto, namyang’ana iye, nanena, Iwenso unali naye Mnazarene, Yesu.

68 Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo anatuluka kunka kuchipata; ndipo tambala analira.

69 Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo.

70 Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya.

71 Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena.

72 Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/14-573e5591b496bf8172db623563b120c7.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 15

Yesu aweruzidwa ndi Pilato

1 Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.

2 Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.

3 Ndipo ansembe aakulu anamnenera Iye zinthu zambiri.

4 Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere.

5 Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.

6 Ndipo ankawamasulira pachikondwerero wandende mmodzi, amene iwo anampempha.

7 Ndipo analipo wina dzina lake Barabasi, womangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumpanduko.

8 Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti achite monga anali kuwachitira nthawi zonse.

9 Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?

10 Pakuti anazindikira kuti ansembe aakulu anampereka Iye mwanjiru.

11 Koma ansembe aakulu anasonkhezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Barabasi.

12 Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula mfumu ya Ayuda?

13 Ndipo anafuulanso, Mpachikeni pamtanda.

14 Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsatu, Mpachikeni Iye.

15 Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.

16 Ndipo asilikali anachoka naye nalowa m’bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse.

17 Ndipo anamveka Iye chibakuwa, naluka korona waminga, namveka pa Iye;

18 Ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!

19 Ndipo anampanda Iye pamutu pake ndi bango, namthira malovu, nampindira maondo, namlambira.

20 Ndipo atatha kumnyoza anamvula chibakuwacho namveka Iye zovala zake. Ndipo anatuluka naye kuti akampachike Iye pamtanda.

Ampachika Yesu pamtanda

21 Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake.

22 Ndipo anamtenga kunka naye kumalo Gologota, ndiwo, osandulika, Malo a Bade.

23 Ndipo anampatsa vinyo wosakaniza ndimure; koma Iye sanamlandire.

24 Ndipo anampachika Iye, nagawana zovala zake mwa iwo okha, ndi kuchita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatenga chiyani.

25 Ndipo panali ora lachitatu, ndipo anampachika Iye.

26 Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.

27 Ndipo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri; mmodzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamanzere.

29 Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu,

30 udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda.

31 Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sangathe kudzipulumutsa yekha.

32 Atsike tsopano pamtanda,Khristumfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.

Yesu afa pamtanda

33 Ndipo pofika ora lachisanu ndi chimodzi, panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.

34 Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza,Eloi, Eloi, lama sabakitani?ndiko kusandulika,

Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?

35 Ndipo ena akuimirirapo, pakumva, ananena, Taonani, aitana Eliya.

36 Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa.

37 Ndipo Yesu anatulutsa mau okweza, napereka mzimu wake.

38 Ndipo chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang’ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi.

39 Ndipo pamenekenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.

40 Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang’anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng’ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;

41 amene anamtsata Iye, pamene anali mu Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye kuYerusalemu.

Yesu aikidwa m’manda

42 Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo paSabata,

43 anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu.

44 Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.

45 Ndipo pamene anachidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe mtembowo.

46 Ndipo anagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m’bafutamo, namuika m’manda osemedwa m’thanthwe; nakunkhunizira mwala pakhomo la manda.

47 Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/15-7d67cb9447ef586d9640862f5b6a4c78.mp3?version_id=1068—

Categories
MARKO

MARKO 16

Yesu auka kwa akufa

1 Ndipo litapitaSabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.

2 Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litatuluka dzuwa.

3 Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pakhomo la manda?

4 Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti unali waukulu ndithu.

5 Ndipo pamene analowa m’manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.

6 Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapachikidwa; anauka; sali pano; taonani, mbuto m’mene anaikamo Iye!

7 Koma mukani, uzaniophunziraake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.

8 Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha.

Yesu aonekera kwa ophunzira ake

9 Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.

10 Iyeyu anapita kuwauza iwo amene ankakhala naye, ali ndi chisoni ndi kulira misozi.

11 Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvere.

12 Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m’maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumidzi.

13 Ndipo iwowa anachoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawavomereze.

14 Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.

15 Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.

16 Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.

17 Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m’dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;

18 adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira.

19 Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.

20 Ndipo iwowa anatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anachita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikiro zakutsatapo.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/16-e61ac6f0ef6fafd88a5facb0f37dbc0b.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Luka

likunena za Yesu monga Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Aisraele komanso Mpulumutsi wa anthu onse. Luka akunena kuti Yesu anaitanidwa ndi Mzimu wa Ambuye kuti, “awuze anthu osauka Uthenga Wabwino” (4.18), ndipo uthengawo ukuonetsa kuti Yesu anali wokhudzidwa ndi anthu amene ali ndi zosowa zosiyanasiyana. Nkhani inanso imene ikuonekera kwambiri mu buku la

Luka

ndiyo ya chimwemwe. Makamaka izi zikupezeka mu mitu yoyambirira ya bukuli pamene akunena za kubwera kwa Yesu, komanso kumapeto pamene Yesu akukwera kunka kumwamba. Luka analembanso mbiri ya chiyambi ndi kukula kwa mpingo wa Chikhristu Yesu atakwera mu buku lija la

Machitidwe

.

Bukuli lili ndi magawo awiri (mutu 1—2 ndi 9—19) m’mene muli nkhani zimene zikupezeka mu

Luka

yekha, nkhanizi ndi monga nyimbo ya angelo ndi ulendo wa abusa kukaona Yesu ali kakhanda, mwana Yesu ali mu Kachisi, ndiponso fanizo la Msamariya wachifundo ndi la Mwana wolowerera. Mu buku lonseli, nkhani yaikulu yagona pa pemphero, Mzimu Woyera, udindo wa azimai pa utumiki wa Yesu komanso kuti Mulungu amakhululukira machimo.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-4

Kubadwa ndi ubwana wa Yohane Mbatizi komanso Yesu 1.5—2.52

Utumiki wa Yohane Mbatizi 3.1-20

Ubatizo ndi kuyesedwa kwa Yesu 3.21—4.13

Utumiki wa Yesu ku Galileya 4.14—9.50

Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu 9.51—19.27

Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 19.28—23.56

Kuukanso, kuonekera ndi kukwera kumwamba kwa Ambuye 24.1-53

Categories
LUKA

LUKA 1

1 Popeza ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinachitika pakati pa ife,

2 monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,

3 kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe;

4 kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira.

Aneneratu za kubadwa kwa Yohane

5 Masiku aHerode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti.

6 Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.

7 Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.

8 Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu,

9 monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye mu Kachisi wa Ambuye.

10 Ndipo khamu lonse la anthu linalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.

11 Ndipo anamuonekera iyemngelowa Ambuye, naimirira kudzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.

12 Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.

13 Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.

14 Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake.

15 Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.

16 Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israele ambiri kwa Ambuye Mulungu wao.

17 Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.

18 Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka.

19 Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.

20 Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirire mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake.

21 Ndipo anthu analikulindira Zekariya, nazizwa ndi kuchedwa kwake mu Kachisimo.

22 Koma m’mene iye anatulukamo, sanathe kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya mu Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.

23 Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wake anamalizidwa, anamuka kunyumba kwake.

24 Ndipo atatha masiku awa, Elizabeti mkazi wake anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati,

25 Ambuye wandichitira chotero m’masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.

Aneneratu za kubadwa kwa Yesu

26 Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete,

27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria.

28 Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.

29 Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulonjera uku nkutani.

30 Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Maria; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu.

31 Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.

32 Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake:

33 ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.

34 Koma Maria anati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?

35 Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.

36 Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

37 Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

38 Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.

Maria acheza kwa Elizabeti

39 Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumzinda wa Yuda;

40 nalowa m’nyumba ya Zekariya, nalonjera Elizabeti.

41 Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m’mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;

42 nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako.

43 Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga?

44 Pakuti ona, pamene mau a moni wako analowa m’makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m’mimba mwanga.

45 Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.

Nyimbo ya Maria

46 Ndipo Maria anati,

Moyo wanga ulemekeza Ambuye,

47 ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

48 chifukwa Iye anayang’anira umphawi wa mdzakazi wake;

pakuti taonani, kuyambira tsopano,

anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.

49 Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu;

ndipo dzina lake lili loyera.

50 Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo

pa iwo amene amuopa Iye.

51 Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake;

Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao.

52 Iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yachifumu,

ndipo anakweza aumphawi.

53 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino,

ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu.

54 Anathangatira Israele mnyamata wake,

kuti akakumbukire chifundo,

55 (Monga analankhula kwa makolo athu)

kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse.

56 Ndipo Maria anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwake.

Kubadwa kwa Yohane Mbatizi

57 Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna.

58 Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.

59 Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya.

60 Ndipo amake anayankha, kuti, Iai; koma adzatchedwa Yohane.

61 Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili.

62 Ndipo anakodola atate wake, afuna amutche dzina liti?

63 Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse.

64 Ndipo pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu.

65 Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m’dziko lonse la mapiri a Yudeya.

66 Ndipo onse amene anazimva anazisunga m’mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.

Nyimbo ya Zekariya

67 Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,

68 Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele;

chifukwa Iye anayang’ana, nachitira anthu ake chiombolo.

69 Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso,

mwa fuko la Davide mwana wake.

70 Monga Iye analankhula ndi m’kamwa

mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe,

71 chipulumutso cha adani athu,

ndi padzanja la anthu onse amene atida ife.

72 Kuchitira atate athu chifundo,

ndi kukumbukira pangano lake lopatulika;

73 chilumbiro chimene Iye anachilumbira

kwa Abrahamu atate wathu.

74 Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu,

tidzamtumikira Iye, opanda mantha,

75 m’chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse.

76 Eya, ndipo iwetu kamwanawe,

udzanenedwamneneriwa Wamkulukulu;

pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.

77 Kuwapatsa anthu ake adziwitse chipulumutso,

ndi makhululukidwe a machimo ao,

78 chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu.

M’menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife.

79 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa;

kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.

80 Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m’mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/1-fdb33d2e143fa4e8486eef00956e02c1.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 2

Kubadwa kwa Yesu Khristu

1 Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwaKaisaraAugusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;

2 ndiko kulembera koyamba pokhala Kwirinio kazembe wa Siriya.

3 Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumzinda wake.

4 Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumzinda wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide;

5 kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati.

6 Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira.

7 Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m’nsalu, namgoneka modyera ng’ombe, chifukwa kuti anasowa malo m’nyumba ya alendo.

Abusa a ku Betelehemu

8 Ndipo panali abusa m’dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang’anira zoweta zao usiku.

9 Ndipomngelowa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha aakulu.

10 Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse;

11 pakuti wakubadwirani inu lero, m’mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene aliKhristuAmbuye.

12 Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera.

13 Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,

14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,

ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.

15 Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife.

16 Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.

17 Ndipo iwo, m’mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.

18 Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.

19 Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake.

20 Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.

Kudulidwa ndi kuperekedwa kwa Yesu

21 Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m’mimba.

22 Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka kuYerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye,

23 (monga mwalembedwa m’chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye)

24 ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m’chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.

Za Simeoni ndi za Anna

25 Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.

26 Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye.

27 Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo,

28 pomwepo iye anamlandira Iye m’manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati,

29 Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja,

lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere;

30 chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu,

31 chimene munakonza pamaso pa anthu onse,

32 kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu,

ndi ulemerero wa anthu anu Israele.

33 Ndipo atate ndi amake anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za Iye.

34 Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;

35 eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m’mitima yambiri akaululidwe.

36 Ndipo panali Anna,mneneriwamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,

37 zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndikusala kudyandi kupemphera usiku ndi usana.

38 Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.

39 Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete.

40 Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Mnyamata Yesu pakati pa aphunzitsi

41 Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu kuPaska.

42 Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero;

43 ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m’mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe;

44 koma iwo anayesa kuti Iye ali m’chipiringu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna Iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;

45 ndipo pamene sanampeze, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna Iye.

46 Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.

47 Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.

48 Ndipo m’mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa.

49 Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?

50 Ndipo sanadziwitse mau amene Iye analankhula nao.

51 Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.

52 Ndipo Yesu anakulabe m’nzeru ndi mumsinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/2-013093f3a1226e51e733da965eae0be0.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 3

Kulalikira kwa Yohane Mbatizi

1 Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa TiberioKaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndiHerodechiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;

2 pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m’chipululu.

3 Ndipo iye anadza kudziko lonse la m’mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo;

4 monga mwalembedwa m’buku la Yesayamneneri, kuti,

Mau a wofuula m’chipululu,

konzani khwalala la Ambuye,

lungamitsani njira zake.

5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa,

ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa;

ndipo zokhota zidzakhala zolungama,

ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;

6 ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.

7 Chifukwa chake iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anatulukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?

8 Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.

9 Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.

10 Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani?

11 Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.

12 Ndipoamisonkhoomwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani?

13 Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa chimene anakulamulirani.

14 Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

15 Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m’mitima yao za Yohane, ngati kapena iye aliKhristu;

16 Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

17 amene chouluzira chake chili m’dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m’nkhokwe yake; koma mankhusu adzatentha m’moto wosazima.

18 Choteretu iye anauza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri.

19 KomaHerodemfumu ija, m’mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita,

20 anaonjeza pa zonsezi ichinso, kuti anatsekera Yohane m’nyumba yandende.

Yesu abatizidwa

21 Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,

22 ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m’thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Makolo a Yesu

23 Ndipo Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Eli,

24 mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe,

25 mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai,

26 mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda,

27 mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, mwana wa Neri,

28 mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Eri,

29 mwana wa Yose, mwana wa Eliyezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,

30 mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu,

31 mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide,

32 mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Nasoni,

33 mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,

34 mwana wa Yakobo, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahori,

35 mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi, mwana wa Sela,

36 mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,

37 mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani,

38 mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana waAdamu, mwana wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/3-1e8865de12b328f436ba6493d1c9c9ea.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 4

Kuyesedwa kwa Yesu

1 Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu

2 kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

3 Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.

4 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,

Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.

5 Ndipo m’mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m’kamphindi kakang’ono.

6 Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna.

7 Chifukwa chake ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.

8 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,

Ambuye Mulungu wako uzimgwadira,

ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.

9 Ndipo anamtsogolera Iye kuYerusalemu, namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisiyo, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi;

10 pakuti kwalembedwa kuti,

Adzalamulaangeloake za iwe, kuti akutchinjirize.

11 Ndipo,

Pa manja ao adzakunyamula iwe,

kuti ungagunde konse phazi lako pamwala.

12 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa,

Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

13 Ndipo mdierekezi, m’mene adamaliza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi ina.

Yesu aphunzitsa ku Nazarete nachotsedwako

14 Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

15 Ndipo Iye anaphunzitsa m’masunagogemwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.

16 Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m’sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m’kalata.

17 Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesayamneneri. Ndipo m’mene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,

18 Mzimu wa Ambuye uli pa Ine,

chifukwa chake Iye anandidzoza Ine

ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:

anandituma Ine kulalikira am’nsinga mamasulidwe,

ndi akhungu kuti apenyanso,

kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

19 kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye.

20 Ndipo m’mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m’sunagogemo anamyang’anitsa Iye.

21 Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu.

22 Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m’kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

23 Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing’anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.

24 Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao.

25 Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri mu Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu padziko lonselo;

26 ndipo Eliya sanatumidwe kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoni, kwa mkazi wamasiye.

27 Ndipo munali akhateambiri mu Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya.

28 Ndipo onse a m’sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi;

29 nanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mzindawo, nanka naye pamutu paphiri pamene panamangidwa mzinda wao, kuti akamponye Iye pansi.

30 Koma Iye anapyola pakati pao, nachokapo.

Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi chiwanda

31 Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mzinda wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake;

32 chifukwa mau ake anali ndi ulamuliro.

33 Ndipo m’sunagoge munali munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti,

34 Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu.

35 Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m’mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.

36 Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.

37 Ndipo mbiri yake ya Iye inafalikira kumalo onse a dziko loyandikira.

Yesu achiritsa mpongozi wa Simoni

38 Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m’sunagoge, nalowa m’nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.

39 Ndipo Iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira.

40 Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundumitundu, anadza nao kwa Iye; ndipo Iye anaika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa.

41 Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiyeKhristu.

Yesu alalikira m’masunagoge

42 Ndipo kutacha anatuluka Iye nanka kumalo achipululu; ndi makamu a anthu analikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere.

43 Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.

44 Ndipo Iye analikulalikira m’masunagoge a ku Yudeya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/4-1264bf56b62a6c7b943fffc488829b55.mp3?version_id=1068—

Categories
LUKA

LUKA 5

Asodzi athandizidwa ndi Yesu, namtsata

1 Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete;

2 ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m’mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m’menemo, nalikutsuka makoka ao.

3 Ndipo Iye analowa m’ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang’ono. Ndipo anakhala pansi m’menemo, naphunzitsa m’ngalawa makamuwo a anthu.

4 Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.

5 Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.

6 Ndipo pamene anachita ichi, anazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka ao analinkung’ambika;

7 ndipo anakodola anzao a m’ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.

8 Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.

9 Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;

10 ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

11 Ndipo m’mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye.

Wakhate achiritsidwa

12 Ndipo panali, pamene Iye anali mumzinda wina, taona, munthu wodzala ndikhate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.

13 Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.

14 Ndipo Iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.

15 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao.

16 Koma Iye anazemba, nanka m’mapululu, nakapemphera.

Yesu achiritsa munthu wamanjenje

17 Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapoAfarisindiaphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndiYerusalemu:ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.

18 Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye.

19 Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa tsindwi, namtsitsira iye poboola pa tsindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.

20 Ndipo Iye, pakuona chikhulupiriro chao, anati, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa.

21 Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?

22 Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m’mitima yanu?

23 Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?

24 Koma kuti mudziwe kutiMwana wa Munthuali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.

25 Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu.

26 Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.

Kuitanidwa kwa Levi

27 Ndipo zitatha izi Iye anatuluka, naona munthuwamsonkho, dzina lake Levi, alikukhala polandirira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine.

28 Ndipo iye anasiya zonse, nanyamuka, namtsata Iye.

29 Ndipo Levi anamkonzera Iye phwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo panali khamu lalikulu la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pachakudya pamodzi nao.

30 Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang’ung’udza kwaophunziraake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?

31 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing’anga; koma akudwala ndiwo.

32 Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.

Za kudzikana kudya

33 Ndipo iwo anati kwa Iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.

34 Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?

35 Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.

36 Ndipo Iye ananenansofanizokwa iwo, kuti, Palibe munthu ang’amba chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong’ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo.

37 Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m’matumba akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.

38 Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m’matumba atsopano.

39 Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/5-8c13c28ffeb75c80b5816d67601277f7.mp3?version_id=1068—