Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Iyeyu adalalika mau ake pa nthawi imene mfumu Yosiya anali pafupi kukhazikitsa malamulo oongolera zinthu mu ufumu wake (621 BC.) Bukuli lili ndi mitu yosiyanasiyana ya mauthenga a uneneri monga: tsiku la chiweruzo ndi chiwonogeko, pamene Yuda adzalangidwe chifukwa chopembedza milungu ina. Yehova adzalanganso mitundu ina. Ngakhale Yerusalemu adzawonongeke, patsogolopo mzindawo udzakonzedwanso, ndipo anthu odzichepetsa ndi olungama adzakhala m’menemo.

Za mkatimu

Za tsiku la Yehova pamene Mulungu adzaimba mlandu

1.1—2.3

Tsoka lodzagwera mitundu ina ya anthu yozungulira Israele

2.4-15

Tsoka lodzagwera Yerusalemu; adzalapa ndipo Yehova adzamuwombola

3.1-20

Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA 1

Mau oopsa akuchenjeza Yerusalemu ndi Yuda

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.

2 Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka, ati Yehova.

3 Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.

4 Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala muYerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala aBaalakuwachotsa m’malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;

5 ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;

6 ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.

7 Khala chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake.

8 Ndipo kudzachitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akuvala chovala chachilendo.

9 Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.

10 Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera ku Chipata cha Nsomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.

11 Chemani okhala m’chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenzasilivaaonongeka.

12 Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m’mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.

13 Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.

14 Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.

15 Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;

16 tsiku la lipenga ndi lakufuulira mizinda yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungodya.

17 Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.

18 Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m’dziko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEP/1-a55a56d6e3bf63af96fb2f17018a8680.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA 2

Mau akuchenjeza amitundu ena

1 Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu;

2 lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.

3 Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.

4 Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa.

5 Tsoka, okhala m’dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m’dziko.

6 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala busa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta.

7 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m’nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.

8 Ndinamva kutonza kwa Mowabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao.

9 Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.

10 Ichi adzakhala nacho m’malo mwa kudzikuza kwao, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.

11 Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m’zisumbu zonse zaamitundu.

12 Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.

13 Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.

14 Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m’mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m’mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza.

15 Uwu ndi mzinda wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m’mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama zakuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEP/2-334bf4cb7c19772e6b8e1886a0f2cce5.mp3?version_id=1068—

Categories
ZEFANIYA

ZEFANIYA 3

Mau akudzudzula Yerusalemu. Malonjezo a kwa okhulupirika otsala

1 Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mzinda wozunza!

2 Sanamvera mau, sanalole kulangizidwa; sanakhulupirire Yehova, sanayandikire kwa Mulungu wake.

3 Akalonga ake m’kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.

4 Aneneri ake ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza chilamulo.

5 Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m’mawa ndi m’mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.

6 Ndaonongaamitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; mizinda yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.

7 Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pake pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, navunditsa machitidwe ao onse.

8 Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.

9 Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.

10 Kuchokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera nacho chopereka changa.

11 Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m’phiri langa lopatulika.

12 Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.

13 Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m’kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.

14 Imba, mwana wamkazi waZiyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi waYerusalemu.

15 Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa.

16 Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.

17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m’chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.

18 Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene katundu wake anawakhalira mtonzo.

19 Taonani, nthawi yomweyo ndidzachita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale chilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m’dziko lonse.

20 Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEP/3-838b68b290a5f5d1b0ef62c8710cedad.mp3?version_id=1068—