Categories
YOWELE

YOWELE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Yowele adalalikira makamaka pa nthawi ya ufumu wa Persiya, koma za moyo wake sitidziwa bwino. Iye akamba za mliri wa dzombe ndi chilala; zimene zaonongeratu mbeu zonse ndi mitengo yomwe. Mneneriyu aona ngati ichi ndi chizindikiro chosonyeza kuti tsiku la Yehova lidzabwera pamene Mulungu adzalanga anthu onse okana malamulo ake. Tsono Yowele akuwapempha anthuwo kuti atembenuke mtima ndi kubwerera kwa Chauta, poyembekeza kuti mwina Mulungu adzawakhulukira ndi kuwadalitsa monga adawalonjezera. Mau ena odziwika ndi akuti lidzafika tsiku pamene Yehova adzatuma mzimu wake pa anthu onse, aamuna ndi aakazi, achikulire ndi achinyamata omwe.

Za mkatimu

Mliri wa dzombe

1.1—2.17

Lonjezo la kukonzedwanso kwa zinthu

2.18-27

Tsiku la Ambuye

2.28—3.21

Categories
YOWELE

YOWELE 1

Tsoka lochokera ku dzombe ndi chilala

1 Mau a Yehova a kwa Yowele mwana wa Petuwele.

2 Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m’dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?

3 Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.

4 Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.

5 Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.

6 Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ake akunga mano a mkango, nukhala nao mano a chibwano a mkango waukulu.

7 Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka.

8 Lirani ngati namwali wodzimangira m’chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake.

9 Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro.

10 M’munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang’onong’ono.

11 Gomani, akulima m’minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m’minda zatayika.

12 Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse yakuthengo yafota; pakuti chimwemwe chathera ana a anthu.

13 Mudzimangire chiguduli m’chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m’chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.

14 Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m’dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.

15 Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

16 Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?

17 Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata.

18 Ha! Nyama ziusa moyo, magulu a ng’ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.

19 Ndifuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m’chipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse yakuthengo.

20 Inde nyama zakuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m’chipululu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOL/1-fd86bdda9874eba3be4da86cc13e9789.mp3?version_id=1068—

Categories
YOWELE

YOWELE 2

Chilango choopsa cha Mulungu

1 Muombe lipenga muZiyoni, nimufuulitse m’phiri langa lopatulika; onse okhala m’dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;

2 tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m’mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.

3 Moto unyambita pamaso pao, ndi m’mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m’mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.

4 Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo.

5 Atumphako ngati mkokomo wa magaleta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.

6 Pamaso pao mitundu ya anthu ikumva zowawa, nkhope yonse zitumbuluka.

7 Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m’mabande ao.

8 Sakankhana, ayenda lililonse m’mopita mwake; akagwa m’zida, siithyoka nkhondo yao.

9 Alumphira mzinda, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu.

10 Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;

11 ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m’chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?

12 Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro;

13 ndipo ng’ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.

14 Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.

15 Ombani lipenga mu Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa,

16 sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m’chipinda mwake, ndi mkwatibwi m’mogona mwake.

17 Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kutiamitunduawalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?

Lonjezo lakuti chidzachuluka chakudya

18 Pamenepo Yehova anachitira dziko lake nsanje, nachitira anthu ake chifundo.

19 Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu;

20 koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum’mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.

21 Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wachita zazikulu.

22 Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m’chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.

23 Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere mu Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba.

24 Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m’zosungiramo zao.

25 Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.

26 Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anachita nanu modabwitsa; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.

27 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndili pakati pa Israele, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.

28 Ndipo kudzachitika m’tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;

29 ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.

30 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo.

31 Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.

32 Ndipo kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m’phiri la Ziyoni ndi muYerusalemumudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOL/2-8172963882fc05844fd17ada36452125.mp3?version_id=1068—

Categories
YOWELE

YOWELE 3

Aneneratu za chilango cha Mulungu pa adani ake; Israele adzakonzekanso

1 Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi aYerusalemu,

2 ndidzasonkhanitsaamitunduonse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa.

3 Ndipo anachitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.

4 Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.

5 Popeza inu munatengasilivawanga ndi golide wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma mu akachisi anu;

6 munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwachotsa kutali kwa malire ao;

7 taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera chilango chanu pamutu panu;

8 ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m’dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena.

9 Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.

10 Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi zikwakwa zanu zikhale nthungo; wofooka anene, Ndine wamphamvu.

11 Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.

12 Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira.

13 Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu.

14 Aunyinji, aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira mlandu.

15 Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao.

16 Ndipo Yehova adzadzuma ali kuZiyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.

17 Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,

18 Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m’mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m’nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.

19 Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m’dziko lao.

20 Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo.

21 Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala mu Ziyoni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOL/3-13f23c99e02b5a637d29036cec975688.mp3?version_id=1068—