Categories
YOSWA

YOSWA 20

Mizinda yopulumukirako

1 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

2 Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire mizinda yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose.

3 Kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalire inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.

4 Munthu akathawira umodzi wa mizinda iyi, aziima polowera pa chipata cha mzindawo, nafotokozere mlandu wake m’makutu a akulu a mzindawo; pamenepo azimlandira kumzinda kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.

5 Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m’dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale.

6 Ndipo azikhala m’mzindamo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m’masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumzinda kwake, ndi nyumba yake, kumzinda kumene adathawako.

7 Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.

8 Ndipo tsidya lija la Yordani kum’mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m’chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti mu Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani mu Basani wa fuko la Manase.

9 Iyi ndi mizinda yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/20-edbccbdf8f8049f172b09aad7af7838e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 21

Midzi yokhalamo Alevi

1 Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele;

2 nanena nao ku Silo m’dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse mizinda yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu.

3 Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi, kutapa pa cholowa chao, monga mwa lamulo la Yehova, mizinda iyi ndi mabusa ao.

4 Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, mizinda khumi ndi itatu.

5 Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Efuremu, ndi pa fuko la Dani, ndi pa hafu la fuko la Manase, mizinda khumi.

6 Ndipo ana a Geresoni analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa hafu la fuko la Manase mu Basani, mizinda khumi ndi itatu.

7 Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni mizinda khumi ndi iwiri.

8 Motero ana a Israele anapatsa Alevi mizinda iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.

9 Ndipo anapatsa motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la ana a Simeoni, mizinda iyi yotchulidwa maina ao;

10 kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adatulukira iwowa.

11 Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo.

12 Koma minda ya mizinda ndi midzi yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yake.

13 Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzake, ndi Libina ndi mabusa ake;

14 ndi Yatiri ndi mabusa ake, ndi Esitemowa ndi mabusa ake;

15 ndi Holoni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake;

16 ndi Aini ndi mabusa ake, ndi Yuta ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake; mizinda isanu ndi inai yotapira mafuko awiri aja.

17 Ndipo motapira fuko la Benjamini, Gibiyoni ndi mabusa ake, Geba ndi mabusa ake,

18 Anatoti ndi mabusa ake, ndi Alimoni ndi mabusa ake; mizinda inai.

19 Mizinda yonse ya ana a Aroni, ansembe, ndiyo khumi ndi itatu, ndi mabusa ao.

20 Ndipo mabanja a ana a Kohati, Aleviwo, otsala a ana a Kohati, analandira mizinda ya maere ao motapira pa fuko la Efuremu.

21 Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Gezere ndi mabusa ake;

22 ndi Kibizaimu ndi mabusa ake, Betehoroni ndi mabusa ake; mizinda inai.

23 Ndipo motapira fuko la Dani, Eliteke ndi mabusa ake, ndi Gibetoni ndi mabusa ake;

24 Ayaloni ndi mabusa ake, Gatirimoni ndi mabusa ake; mizinda inai.

25 Ndipo motapira pa hafu la fuko la Manase, Taanaki ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake; mizinda iwiri.

26 Mizinda yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao.

27 Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa hafu la fuko la Manase, Golani mu Basani ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; mizinda iwiri.

28 Ndipo motapira pa fuko la Isakara, Kisiyoni ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake;

29 Yaramuti ndi mabusa ake, Enganimu ndi mabusa ake; mizinda inai.

30 Ndipo motapira pa fuko la Asere, Misala ndi mabusa ake, Abidoni ndi mabusa ake;

31 Helekati ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake; mizinda inai.

32 Ndipo motapira pa fuko la Nafutali, Kedesi mu Galileya ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ake, ndi Karitani ndi mabusa ake, mizinda itatu.

33 Mizinda yonse ya Ageresoni monga mwa mabanja ao ndiyo mizinda khumi ndi itatu ndi mabusa ao.

34 Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa fuko la Zebuloni, Yokoneamu ndi mabusa ake, ndi Karita ndi mabusa ake,

35 Dimina ndi mabusa ake, Nahalala ndi mabusa ake; mizinda inai.

36 Ndipo motapira pa fuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,

37 Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake; mizinda inai.

38 Ndipo motapira m’fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake;

39 Hesiboni ndi mabusa ake, Yazere ndi mabusa ake: yonse pamodzi mizinda inai.

40 Yonseyi ndiyo mizinda ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo mizinda khumi ndi iwiri.

41 Mizinda yonse ya Alevi, pakati pa cholowa cha ana a Israele ndiyo mizinda makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao.

42 Mizinda iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero mizinda iyi yonse.

43 Motero Yehova anawapatsa Israele dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira laolao, nakhala m’mwemo.

44 Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaime munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m’manja mwao.

45 Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israele; zidachitika zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/21-376c630b82c10ed5e9159832ac7d26a2.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 22

A fuko la Rubeni, la Gadi, ndi la Manase logawika pakati amuka kwao

1 Pamenepo Yoswa anaitana Arubeni ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase,

2 nanena nao, Mwasunga inu zonsezo anakulamulirani Mose mtumiki wa Yehova; mwamveranso mau anga m’zonse ndinakulamulirani inu;

3 simunasiye abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga chisungire lamulo la Yehova Mulungu wanu.

4 Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani.

5 Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m’njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

6 Momwemo Yoswa anawadalitsa, nawauza amuke; ndipo anamuka ku mahema ao.

7 Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa mu Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;

8 nanena nao ndi kuti, Bwererani nacho chuma chambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndisiliva, ndi golide, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi malaya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.

9 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m’dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.

Guwa la nsembe la umboni

10 Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m’dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake.

11 Ndipo ana a Israele anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga guwa la nsembe pandunji padziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordani, ku mbali ya ana a Israele.

12 Pamene ana a Israele anamva ichi msonkhano wonse wa ana a Israele anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.

13 Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe,

14 ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mafuko onse a Israele; yense wa iwowa ndiye mkulu wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israele.

15 M’mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,

16 Utero msonkhano wonse wa Yehova, Cholakwa ichi nchiyani mwalakwira nacho Mulungu wa Israele, ndi kumtembenukira Yehova lero lino kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?

17 Kodi mphulupulu ya ku Peori itichipera, imene sitinadziyeretsere mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova,

18 kuti mubwerera lero lino kusatsata Yehova? Ndipo kudzakhala kuti popeza lero mupikisana ndi Yehova, mawa adzakwiyira gulu lonse la Israele.

19 Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m’dziko la cholowa cha Yehova m’mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.

20 Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwe m’choperekedwacho, ndipo mkwiyo unagwera gulu lonse la Israele? Osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yake.

21 Pamenepo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anayankha, nanena ndi akulu a mabanja a Israele,

22 Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,

23 tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, achifunse Yehova mwini wake;

24 ndipo ngati ife sitinachite ichi chifukwa cha kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli chiyani inu kwa Yehova Mulungu wa Israele?

25 Pakuti Yehova anaika Yordani ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope Yehova.

26 Chifukwa chake tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai;

27 koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m’tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m’tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.

28 Chifukwa chake tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m’tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, chitsanzo cha guwa la nsembe la Yehova, chomanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.

29 Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa chihema chake.

30 Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.

31 Ndipo Finehasi, mwana wa Eleazara wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira nacho Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israele m’dzanja la Yehova.

32 Ndipo Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, ndi akalonga anabwerera kuchokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m’dziko la Giliyadi, kudza ku dziko la Kanani kwa ana a Israele, nawabwezera mau.

33 Ndipo mauwo anakomera ana a Israele pamaso pao; ndi ana a Israele analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi.

34 Ndipo ana a Rubeni ndi ana a Gadi analitcha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/22-61e38fd80316fb143be3664fc4f52850.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 23

Yoswa achenjeza anthu asunge Malamulo a Mulungu

1 Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israele kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;

2 Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;

3 ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.

4 Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale cholowa cha mafuko anu, kuyambira ku Yordani, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa.

5 Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapirikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwachotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale cholowa chanu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.

6 Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kuchita zonse zolembedwa m’buku la chilamulo cha Mose, osachipatukira kulamanja kapena kulamanzere;

7 osalowa pakati paamitunduawa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;

8 koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munachita mpaka lero lino.

9 Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.

10 Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.

11 Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.

12 Koma, mukadzabwerera m’mbuyo pang’ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;

13 dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m’nthiti mwanu, ndi minga m’maso mwanu, mpaka mudzatayika m’dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

14 Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi.

15 Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m’dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

16 Mukalakwirachipanganocha Yehova Mulungu wanu chimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m’dziko lokomali anakupatsani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/23-1954612448e1e4778fdcc3e91652b98a.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 24

Yoswa akumbutsa anthu zowachitira Mulungu

1 Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzionetsa pamaso pa Mulungu.

2 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.

3 Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m’dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki.

4 Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.

5 Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani.

6 Ndipo ndinatulutsa atate anu mu Ejipito; ndipo munadza kunyanja; koma Aejipito analondola atate anu ndi magaleta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.

7 Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine mu Ejipito; ndipo munakhala m’chipululu masiku ambiri.

8 Pamenepo ndinakulowetsani inu m’dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordani; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m’dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanulanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.

9 Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, anauka naponyana ndi Israele; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;

10 koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m’dzanja lake.

11 Pamenepo munaoloka Yordani, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ake a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m’dzanja lanu.

12 Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.

13 Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo ntchito, ndi mizinda simunaimange, ndipo mukhala m’mwemo; mukudya za m’minda yampesa, ndi minda yaazitonaimene simunaioke.

Yoswa abwereza kuchita pangano pakati pa Mulungu ndi anthu

14 Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi mu Ejipito; nimutumikire Yehova.

15 Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m’dziko lao; koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

16 Ndipo anthu anayankha, nati, Sikungatheke kuti timsiye Yehova, ndi kutumikira milungu ina;

17 pakuti Yehova Mulungu wathu ndi Iye amene anatikweza kutitulutsa m’dziko la Ejipito kunyumba ya ukapolo, nachita zodabwitsa zazikuluzo pamaso pathu, natisunga m’njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao;

18 ndipo Yehova anaingitsa pamaso pathu anthu awa onse, ngakhale Aamori okhala m’dzikomo; chifukwa chake ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu.

19 Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simungathe inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zochimwa zanu.

20 Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yachilendo, adzatembenuka ndi kukuchitirani choipa, ndi kukuthani, angakhale anakuchitirani chokoma.

21 Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Iaitu, koma tidzatumikira Yehova.

22 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu, Inu mwadzichitira mboni inu nokha kuti mwadzisankhira Yehova kumtumikira Iye. Ndipo anati, Ndife mboni.

23 Ndipo tsopano, chotsani milungu yachilendo ili pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israele.

24 Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ake.

25 Motero Yoswa anachita pangano ndi anthu tsiku lija, nawaikira lemba ndi chiweruzo mu Sekemu.

26 Ndipo Yoswa analembera mau awa m’buku la chilamulo cha Mulungu; natenga mwala waukulu, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pamalo opatulika a Yehova.

27 Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.

28 Pamenepo Yoswa anauza anthu amuke, yense ku cholowa chake.

Amwalira Yoswa ndi Eleazara

29 Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi.

30 Ndipo anamuika m’malire a cholowa chake mu Timnati-Sera, ndiwo ku mapiri a Efuremu kumpoto kwa phiri la Gaasi.

31 Ndipo Israele anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa ntchito yonse ya Yehova anaichitira Israele.

32 Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.

33 Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika paphiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/24-9d1440838b9480f21486e3e17c726193.mp3?version_id=1068—