Categories
YOSWA

YOSWA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba za m’mene Aisraele adalowera m’dziko la Kanani nkulilanda, Yoswa akuwatsogolera. Kenaka adagawana dzikolo.

Nkhani zodziwika bwino m’bukuli ndizo kuoloka Yordani, kugwa kwa Yeriko, kugonjetsedwa kwa Ai, ndi kukonzanso kwa chipangano pakati pa Mulungu ndi anthu ake.

Mau odziwika bwino ndi awa: “mudzisankhire lero amene mudzamtumikira…koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova” (24.15).

Za mkatimu

Aisraele atenga dziko la Kanani

1.1—12.24

a. Aoloka mtsinje wa Yordani

1.1—5.15

b. Agonjetsa mzinda la Yeriko

6.1—7.26

c. Agonjetsa mzinda wa Ai ndi mizinda ina

8.1—12.24

Aisraele agawana dziko

13.1—22.34

a. Dziko la kum’mawa kwa Yordani

13.1-33

b. Dziko la kuzambwe kwa Yordani

14.1—19.51

c. Mizinda yopulumukirako

20.1-9

d. Mafuko awiri akum’mawa abwerera ku dziko lao

22.1-34

Mau a Yoswa otsanzikana nawo

23.1-16

Abwereza kuchita chipangano ku Sekemu

24.1-33

Categories
YOSWA

YOSWA 1

1 Ndipo atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose,

2 Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordani uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m’dzikomo ndilikuwapatsa, ndiwo ana a Israele.

3 Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose.

4 Kuyambira chipululu, ndi Lebanoni uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Yufurate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.

5 Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.

6 Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.

7 Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako.

8 Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.

9 Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.

10 Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,

11 Pitani pakati pa chigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordani uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanulanu.

12 Ndipo Yoswa anati kwa Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, ndi kuti,

13 Kumbukirani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino.

14 Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m’dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;

15 mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanulanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordani la kum’mawa,

16 Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka.

17 Monga momwe tinamvera mau onse a Mose momwemo tidzamvera inu; komatu akhale ndi inu Yehova Mulungu wanu monga anakhala ndi Mose.

18 Aliyense wakupikisana ndi inu, osamvera mau anu mulimonse mukamlamulira, aphedwe; komatu khalani wamphamvu, nimulimbike mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/1-6b362df3be4ed66824cb37a3e37c2a5a.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 2

Yoswa atuma anthu awiri azonde Yeriko

1 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m’nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo.

2 Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israele, kulizonda dziko.

3 Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m’nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.

4 Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwe uko afuma;

5 ndipo m’mene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.

6 Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi.

7 Ndipo amunawo anawalondola panjira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata.

8 Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye,

9 nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m’dziko onse asungunuka pamaso panu.

10 Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a mu Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka mu Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse.

11 Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m’mwamba umo, ndi padziko lapansi.

12 Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m’nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona,

13 kuti mudzawasunga ndi moyo atate wanga ndi mai wanga, ndi alongo anga ndi abale anga, ndi zonse ali nazo, ndi kupulumutsa miyoyo yathu kuimfa.

14 Ndipo amunawo anati kwa iye, Moyo wathu ndiwo moyo wanu, mukapanda kuwulula chodzera ife; ndipo kudzakhala kuti, pakutipatsa ife dziko ili Yehova, tidzakuchitira chifundo ndi choonadi.

15 Pamenepo anawatsitsa pazenera ndi chingwe; popeza nyumba yake inali pa linga la mzinda, nakhala iye palingapo.

16 Ndipo anati kwa iwo, Mukani kuphiri, olondola angakupezeni; mubisale kumeneko masiku atatu, mpaka atabwerera olondolawo, pamenepo muyende ulendo wanu.

17 Ndipo amunawo anati kwa iye, Sitidzachimwira lumbiro lako ili watilumbiritsali.

18 Taona, tikadzalowa m’dzikomo ife, uzimanga chingwe ichi chofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m’nyumbamo atate wako ndi mai wako ndi abale ako ndi a m’nyumba onse a atate wako.

19 Ndipo kudzakhala kuti aliyense akadzatuluka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yake, tilibe kupalamula ife; koma aliyense adzakhala ndi iwe m’nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu.

20 Koma ukawulula chodzera ifecho tidzamasukira lumbiro lako watilumbiritsali.

21 Nati iye, Momwemo, monga mwa mau anu. Ndipo anawauza amuke, iwo namuka; namanga iye chingwe chofiiracho pazenera.

22 Ndipo anayenda iwo, nafika kuphiri, nakhalako masiku atatu mpaka atabwerera olondolawo; popeza olondolawo anawafunafuna panjira ponse, osawapeza.

23 Pamenepo amuna awiriwo anabwerera, natsika m’phirimo naoloka, nafika kwa Yoswa mwana wa Nuni, namfotokozera zonse zidawagwera.

24 Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m’manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/2-62ccc8efc30ba17f9b712f989a17f777.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 3

Aisraele aoloka Yordani

1 Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke.

2 Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa chigono;

3 nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaonalikasa la chipanganola Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata.

4 Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapite njirayi kufikira lero.

5 Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu.

6 Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu.

7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.

8 Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima mu Yordani.

9 Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Idzani kuno, mumve mau a Yehova Mulungu wanu.

10 Nati Yoswa, Ndi ichi mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapirikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.

11 Taonani, likasa la chipangano la Ambuye wa dziko lonse lapansi lioloka Yordani pamaso panu.

12 Ndipo tsono, mudzitengere amuna khumi ndi awiri mwa mafuko a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi.

13 Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m’madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.

14 Ndipo kunali pochoka anthu ku mahema ao kukaoloka Yordani, ansembe anasenza likasa la chipangano pamaso pa anthu.

15 Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordani, nathibika m’mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordani asefuka m’magombe ake onse, nyengo yonse ya masika,

16 pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.

17 Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/3-b0ba56b90b66acda86edc1e38b2604eb.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 4

Aimiritsa miyala 12 ikhale chikumbutso ku Giligala

1 Ndipo kunali, utatha kuoloka Yordani mtundu wonse, Yehova ananena ndi Yoswa, nati,

2 Mudzitengere mwa anthu, amuna khumi ndi awiri, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

3 ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kuiika m’mogona m’mene mugonamo usiku uno.

4 Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

5 nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele;

6 kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m’tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?

7 Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo palikasa la chipanganocha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.

8 Ndipo ana a Israele anachita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele; ndipo anaoloka nayo kunka kogona, naiika komweko.

9 Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.

10 Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.

11 Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

12 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;

13 ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.

14 Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisraele onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse a moyo wake.

15 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

16 Lamulira ansembe akusenza likasa la umboni, kuti akwere kutuluka mu Yordani.

17 Pamenepo Yoswa analamulira ansembe, ndi kuti, Kwerani kutuluka mu Yordani.

18 Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la chipangano la Yehova, kutuluka pakati pa Yordani, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a mu Yordani anabwera m’njira mwake, nasefuka m’magombe ake onse monga kale.

19 Ndipo anthu anakwera kutuluka mu Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m’mawa kwa Yeriko.

20 Ndipo Yoswa anaimika ku Giligala miyala ija khumi ndi iwiri adaitenga mu Yordani.

21 Ndipo anati kwa ana a Israele, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani?

22 Pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israele anaoloka Yordani uyu pouma.

23 Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordani pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anachitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka;

24 kuti mitundu yonse ya padziko lapansi idziwe dzanja la Yehova, kuti ndilo lamphamvu; kuti iope Yehova Mulungu wanu masiku onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/4-f438774cf7afbf99465fb9017ed25607.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 5

Anthu adulidwa nachita Paska

1 Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.

2 Nthawi imeneyo Yehova anati kwa Yoswa, Udzisemere mipeni yamiyala nudulenso ana a Israele kachiwiri.

3 Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israele pa Gibea-Naraloti.

4 Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka mu Ejipito, anthu aamuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m’chipululu panjira, atatuluka mu Ejipito.

5 Pakuti anthu onse anatulukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m’chipululu panjira potuluka mu Ejipito sanadulidwe.

6 Pakuti ana a Israele anayenda m’chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.

7 Koma ana ao aamuna amene anawautsa m’malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadule panjira.

8 Ndipo kunali, atatha kudula mtundu wonse, anakhala m’malo mwao m’chigono mpaka adachira.

9 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndakukunkhunizirani mtonzo wa Ejipito. Chifukwa chake dzina la malowo analitcha Giligala kufikira lero lino.

10 Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachitaPaskatsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m’zidikha za Yeriko.

11 Ndipo m’mawa mwake atatha Paska, anadya tirigu wakhwimbi wa m’dziko, mikate yopanda chotupitsa ndi tirigu wokazinga tsiku lomwe lija.

12 Koma m’mawa mwakemanaanaleka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m’dziko; ndipo ana a Israele analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani chaka chomwe chija.

Masomphenya a Yoswa

13 Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m’dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?

14 Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake?

15 Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Vula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nachita Yoswa chomwecho.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/5-b2f11255df9488808d2cc8a8666a0aea.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 6

Kupasulidwa kwa Yeriko

1 Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.

2 Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m’dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake.

3 Ndipo muzizungulira mzinda inu nonse ankhondo, kuuzungulira mzinda kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.

4 Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mzindawo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo.

5 Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mzindawo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwake.

6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzanilikasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.

7 Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mzinda, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova.

8 Ndipo atanena kwa anthu Yoswa, ansembe asanu ndi awiri akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo pamaso pa Yehova, anapita naliza mphalasazo; ndipo likasa la chipangano cha Yehova linawatsata.

9 Ndipo okonzeka kunkhondo anatsogolera ansembe akuliza mphalasa, koma akudza m’mbuyo anatsata likasa, ansembe ali chiombere poyenda iwo.

10 Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamafuula, kapena kumveketsa mau anu, asatuluke konse mau m’kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Fuulani; pamenepo muzifuula.

11 Ndipo anazungulitsa likasa la Yehova mzinda, kuzungulira kamodzi; pamenepo analowa kuchigono, nagona m’mwemo.

12 Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova.

13 Ndipo ansembe asanu ndi awiri, akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo ndi kutsogolera nazo likasa la Yehova, anayenda chiyendere naliza mphalasazo; ndi okonzeka kunkhondowo anawatsogolera, ndi akudza m’mbuyo anatsata likasa la Yehova, ansembe ali chiombere poyenda iwo.

14 Ndipo tsiku lachiwiri anazungulira mzinda kamodzi, nabwera kuchigono; anatero masiku asanu ndi limodzi.

15 Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri analawira mamawa, mbandakucha, nazungulira mzinda mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mzinda kasanu ndi kawiri.

16 Ndipo kunali, pa nthawi yachisanu ndi chiwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Fuulani; pakuti Yehova wakupatsani mzindawo.

17 Koma mzindawo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m’mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m’nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.

18 Ndipo inu, musakhudze choperekedwacho, mungadziononge konse, potapa choperekedwacho; ndi kuononga konse chigono cha Israele ndi kuchisautsa.

19 Komasilivayense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m’mosungira chuma cha Yehova.

20 Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m’mzinda, yense kumaso kwake; nalanda mzindawo.

Apulumutsidwa Rahabi

21 Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m’mzinda, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng’ombe, ndi nkhosa, ndi abulu, ndi lupanga lakuthwa.

22 Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m’nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.

23 Pamenepo anyamata ozondawo analowa, natulutsa Rahabi, ndi atate wake ndi mai wake ndi abale ake, ndi onse anali nao; anatulutsanso achibale ake onse; nawaika kunja kwa chigono cha Israele.

24 Ndipo anatentha mzinda ndi moto, ndi zonse zinali m’mwemo; koma siliva ndi golide ndi zotengera zamkuwa ndi zachitsulo anaziika m’mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.

25 Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wake, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israele mpaka lero lino; chifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.

26 Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mzinda uwu wa Yeriko; adzamanga maziko ake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.

27 Potero Yehova anakhala ndi Yoswa; ndi mbiri yake inabuka m’dziko lonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/6-377a297cb3168c6f4e263aaf50c6f9da.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 7

Kuchimwa kwa Akani

1 Koma ana a Israele analakwa ndi choperekedwacho; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatapa choperekedwacho; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israele.

2 Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum’mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.

3 Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kunkako, pakuti a komweko ndi owerengeka.

4 Potero mwa anthu anakwerako amuna monga zikwi zitatu; koma anathawa pamaso pa amuna a ku Ai.

5 Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.

6 Ndipo Yoswa anang’amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.

7 Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordani, kutipereka ife m’dzanja la Aamori, kutiononga ife? Mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordani!

8 Ndidzanenanji, Ambuye, Israele atabwerera m’mbuyo pamaso pa adani ao?

9 Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m’dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?

10 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere?

11 Israele wachimwa, nalakwiransochipanganochanga, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao.

12 Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu.

13 Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sungathe kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu.

14 Koma m’mawa adzakuyandikitsani, fuko ndi fuko; ndipo kudzali kuti fukoli Yehova aliwulula lidzayandikira mwa zibale zake; ndi chibale Yehova achiwulula chidzayandikira monga mwa a nyumba ake; ndi a m’nyumbawo Yehova awawulula adzayandikira mmodzimmodzi.

15 Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali nacho choperekedwacho adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo chifukwa analakwira chipangano cha Yehova, ndi chifukwa anachita chopusa mu Israele.

16 Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israele, fuko ndi fuko; ndi fuko la Yuda linagwidwa;

17 nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira chibale cha Azera; nayandikizitsa chibale cha Azera, mmodzimmodzi, nagwidwa Zabidi;

18 nayandikizitsa a m’nyumba yake mmodzimmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimi, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anagwidwa.

19 Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.

20 Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndachimwira Yehova Mulungu wa Israele, ndachita zakutizakuti;

21 pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri asiliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m’nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo.

22 Pamenepo Yoswa anatuma mithenga, iwo nathamangira kuhema; ndipo taonani, zidabisika m’hema mwake ndi siliva pansi pake.

23 Ndipo anazichotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israele, nazitula pamaso pa Yehova.

24 Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi malayawo, ndi chikute chagolide, ndi ana ake aamuna ndi aakazi, ndi ng’ombe zake, ndi abulu ake, ndi nkhosa zake, ndi hema wake ndi zake zonse; nakwera nazo ku chigwa cha Akori.

25 Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.

26 Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/7-ef0e3588cccc4dbc6d15db8a8ddfb710.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 8

Kupasulidwa kwa Ai

1 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m’dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mzinda wake ndi dziko lake;

2 ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng’ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mzinda.

3 Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,

4 nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mzinda; musakhalira kutali ndi mzinda, koma mukhale okonzekeratu nonse;

5 ndipo ine, ndi anthu onse ali nane, tidzayandikira mzinda; ndipo kudzali, pamene atuluka kudzakomana nafe, monga poyamba paja, tidzathawa pamaso pao;

6 ndipo adzatuluka kutitsata mpaka tidawakokera asiyane ndi mzinda; pakuti adzanena, Atithawa pamaso pathu monga poyamba paja; nafenso tidzathawa pamaso pao;

7 pamenepo muziuka m’molalira ndi kulowa m’mzinda; pakuti Yehova Mulungu wanu; adzaupereka m’manja mwanu.

8 Ndipo kudzali, mutagwira mzinda, muzitentha mzindawo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.

9 Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m’molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.

10 Ndipo Yoswa analawira m’mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akulu a Israele, pamaso pa anthu a ku Ai.

11 Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mzinda, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali chigwa.

12 Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m’molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda.

13 Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mzinda, ndi olalira ao kumadzulo kwa mzinda, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa chigwa.

14 Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m’mzinda kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mzinda.

15 Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse anaoneka ngati a ku Ai alikuwathyola, nathawira njira ya kuchipululu.

16 Pamenepo anthu onse okhala m’mzinda, anaitanidwa awapirikitse, nampirikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mzinda.

17 Ndipo sanatsale mwamuna mmodzi yense mu Ai kapena mu Betele osatulukira kwa Israele; nasiya mzinda wapululu, napirikitsa Israele.

18 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m’dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m’dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m’dzanja lake kuloza mzinda.

19 Nauka msanga olalirawo m’mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lake, nalowa m’mzinda, naugwira; nafulumira nayatsa mzindawo.

20 Pamene amuna a ku Ai anacheuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mzinda unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa chakuno kapena chauko; ndi anthu othawira kuchipululu anatembenukira owapirikitsa.

21 Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israele yense kuti olalirawo adagwira mzinda, ndi kuti utsi wa mzinda unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.

22 A kumzindanso anawatulukira; potero anakhala pakati pa Israele, ena mbali ina, ena mbali ina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsale kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.

23 Koma mfumu ya ku Ai anamgwira wamoyo, nadza naye kwa Yoswa.

24 Ndipo kunali, atatha Israele kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kuchipululu kumene anawapirikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisraele onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa.

25 Ndipo onse amene adagwa tsiku lija, amuna ndi akazi, ndiwo zikwi khumi ndi ziwiri, anthu onse a ku Ai.

26 Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.

27 Koma ng’ombe ndi zofunkha za mzinda uwu Israele anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa.

28 Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino.

29 Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mzinda; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino.

Apereka nsembe nawerenga Malamulo a Mose ku Ebala ndi Gerizimu

30 Pomwepo Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Israele guwa la nsembe m’phiri la Ebala,

31 monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israele, monga mulembedwa m’buku la chilamulo cha Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo chitsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika.

32 Ndipo analembapo pa miyalayi chitsanzo cha chilamulo cha Mose, chimene analembera pamaso pa ana a Israele.

33 Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenzalikasa la chipanganola Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji paphiri la Gerizimu, ndi ena pandunji paphiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele.

34 Atatero, anawerenga mau onse a chilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m’buku la chilamulo.

35 Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, ndi akazi ndi ana aang’ono, ndi alendo akuyenda pakati pao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/8-1622db8fca89bda53e311bd9b5bc2076.mp3?version_id=1068—

Categories
YOSWA

YOSWA 9

Yoswa anyengedwa ndi Agibiyoni napangana nao

1 Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;

2 anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israele, ndi mtima umodzi.

3 Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,

4 zinachita momchenjerera, ndipo zinapita mooneka ngati mithenga, ndipo zinatenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong’ambika ndi omangamanga;

5 ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, ndipo zinavala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

6 Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, ndipo zinati kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe.

7 Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?

8 Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? Ndipo mufuma kuti?

9 Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita mu Ejipito,

10 ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.

11 Ndipo akulu athu ndi nzika zonse za m’dziko mwathu zidanena nafe ndi kuti, Mutenge m’dzanja lanu kamba wa paulendo, kakomane naoni, nimunene nao, Ndife akapolo anu; ndipo tsopano mupangane nafe.

12 Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m’nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku lotuluka ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani uli wouma ndi woyanga nkhungu;

13 ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang’ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu.

14 Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.

15 Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira.

16 Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao.

17 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.

18 Ndipo ana a Israele sanawakanthe, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga.

19 Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israele, m’mwemo sitikhoza kuwachitira kanthu.

20 Tidzawachitira ichi, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo chifukwa cha lumbirolo tidawalumbirira.

21 Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao.

22 Ndipo Yoswa anawaitana, nanena nao, kuti, Mwatinyenga chifukwa ninji, ndi kuti, Tikhala kutalitali ndi inu, pokhala kwanu kuli pakati pa ife?

23 Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.

24 Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m’dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.

25 Ndipo tsopano, taonani, tili m’dzanja lanu; monga muyesa chokoma ndi choyenera kutichitira ife, chitani.

26 Pamenepo anawachitira chotero, nawalanditsa m’dzanja la ana a Israele, angawaphe.

27 Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/9-6ddc3c83cb92b6e3fc44a6c80cb24380.mp3?version_id=1068—