Categories
YOHANE

YOHANE 20

Yesu auka kwa akufa

1 Koma tsiku loyamba laSabataanadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.

2 Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzirawina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye.

3 Anatuluka tsono Petro ndi wophunzira winayo, nalinkupita kumanda.

4 Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;

5 ndipo m’mene anawerama chosuzumira anaona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sanalowemo.

6 Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m’manda; ndipo anaona nsalu zabafuta zitakhala,

7 ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.

8 Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira.

9 Pakuti kufikira pomwepo sanadziwe lembo lakuti ayenera Iye kuuka kwa akufa.

10 Chifukwa chake ophunzirawo anachokanso, kunka kwao.

Yesu aonekera kwa Maria wa Magadala

11 Koma Maria analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m’mene alikulira anawerama chisuzumirire kumanda;

12 ndipo anaonaangeloawiri atavala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.

13 Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Chifukwa anachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika Iye.

14 M’mene adanena izi, anacheuka m’mbuyo, naona Yesu ali chilili, ndipo sanadziwe kuti ndiye Yesu.

15 Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi Iye, Mbuye ngati mwamnyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzamchotsa.

16 Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m’mene anacheuka, ananena ndi Iye mu Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi.

17 Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.

18 Maria wa Magadala anapita, nalalikira kwa ophunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.

Yesu aonekera kwa ophunzira, Tomasi palibe

19 Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.

20 Ndipo pamene adanena ichi, anaonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera pakuona Ambuye.

21 Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.

22 Ndipo pamene anati ichi anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera.

23 Zochimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.

24 Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sanakhale nao pamodzi, pamene Yesu anadza.

25 Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m’manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m’chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.

Yesu aonekera kwa ophunzira, Tomasi ali nao

26 Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m’nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.

27 Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.

28 Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.

29 Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaone.

30 Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu anazichita pamaso pa ophunzira ake, zimene sizinalembedwe m’buku ili;

31 koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiyeKhristuMwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m’dzina lake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/20-9bfef2c8846cfbc2a83ac62c24f66d1a.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 21

Yesu awaonekera kunyanja ya Tiberiasi

1 Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwaophunziraake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere.

2 Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake.

3 Simoni Petro ananena nao, Ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anatuluka, nalowa m’ngalawa; ndipo mu usiku muja sanagwire kanthu.

4 Koma pakuyamba kucha, Yesu anaimirira pambali pa nyanja, komatu ophunzirawo sanadziwe kuti ndiye Yesu.

5 Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha Iye, Iai.

6 Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba.

7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m’nyanja.

8 Koma ophunzira ena anadza m’kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo.

9 Ndipo pamene anatulukira pamtunda, anapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate.

10 Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano.

11 Chifukwa chake Simoni Petro anakwera m’ngalawa nakokera khoka kumtunda lodzala ndi nsomba zazikulu, zana limodzi, ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinachuluka kotere, kokha silinang’ambika.

12 Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa ophunzira anatha kumfunsa Iye, Ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye.

13 Yesu anadza natenga mkate napatsa iwo, momwemonso nsomba.

14 Imeneyo ndi nthawi yachitatu yakudzionetsera Yesu kwa ophunzira ake, m’mene atauka kwa akufa.

15 Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa anaankhosa anga.

16 Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.

17 Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.

18 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m’chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.

19 Koma ichi ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m’mene ananena ichi, anati kwa iye, Nditsate Ine.

20 Petro, m’mene anacheuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?

21 Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu?

22 Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe? Unditsate Ine iwe.

23 Chifukwa chake mau awa anatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe?

24 Yemweyu ndiye wophunzira wakuchita umboni za izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi woona.

25 Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phee, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/21-0b31bbef89140ffd52fa16d665994e0e.mp3?version_id=1068—