Za Mbusa Wabwino
1 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m’khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.
2 Koma iye wakulowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa.
3 Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.
4 Pamene adatulutsa zonse nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mau ake.
5 Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; chifukwa sizidziwa mau a alendo.
6 Fanizoili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikire zimene Yesu analikulankhula nao.
7 Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.
8 Onse amene anadza m’tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamve iwo.
9 Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.
10 Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.
11 Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.
12 Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;
13 chifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.
14 Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine,
15 monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
16 Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.
17 Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso.
18 Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.
19 Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda chifukwa cha mau awa.
20 Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji?
21 Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosaona?
Yesu adziwulula ali Mwana wa Mulungu
22 Koma kunali phwando la kukonzetsanso muYerusalemu; nyengoyo ndi yachisanu.
23 Ndipo Yesu analikuyendayenda mu Kachisi m’khonde la Solomoni.
24 Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinuKhristu, tiuzeni momveka.
25 Yesu anayankha iwo, Ndakuuzani, ndipo simukhulupirira. Ntchitozi ndidzichita Ine m’dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni.
26 Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa nkhosa zanga.
27 Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.
28 Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa.
29 Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m’dzanja la Atate.
30 Ine ndi Atate ndife amodzi.
31 Ayuda anatolanso miyala kuti amponye Iye.
32 Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?
33 Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.
34 Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m’chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu?
35 Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),
36 kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?
37 Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine.
38 Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.
39 Anafunanso kumgwira Iye; ndipo anapulumuka m’dzanja lao.
40 Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.
41 Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona.
42 Ndipo ambiri anakhulupirira Iye komweko.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/10-2d9027098beab02152a4207220b0b591.mp3?version_id=1068—