Categories
YOHANE

YOHANE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mu buku la

Yohane

akumuonetsa Yesu monga Mau amuyaya a Mulungu, amene “anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife.” (1.14) Monga momwe bukuli likunenera, Uthengawo unalembedwa owerenga akhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m’dzina lake (20.31).

Atatha kunena mau oyamba amene akufanizira Yesu ndi mau osatha a Mulungu, gawo loyamba la Uthengawu likutionetsa zozizwitsa zosiyanasiyana zimene zikutitsimikizira kuti Yesu ndiye Mpulumutsi Wolonjezedwa uja, amene ali Mwana wa Mulungu. Kenaka izi zikutsatidwa ndi maneno osiyanasiyana amene akufotokoza tanthauzo la zozizwitsazo. Pa ndime zimenezi, afotokozanso kuti anthu ena anakhulupirira Yesu namutsata, pamene ena sanafune kumkhulupirira. Mutu 13 mpaka 17 anena mwachimvekere za chiyanjano chozama chimene chinalipo pakati pa Yesu ndi ophunzira ake pa usiku umene iye anagwidwa, komanso mawu achilimbikitso amene Iye anawauza asanakhomedwe pamtanda mawa lake. Mitu yotsirizira inena za kugwidwa, kuzengedwa mlandu ndi kupachikidwa pamtanda komanso kuukanso kwa Yesu, ndiponso pamene Iye anaonekera kwa ophunzira ake ataukitsidwa.

Yohane

akutsindika za mphatso ya moyo wosatha mwa Yesu, ndipo mphatso imeneyi imayamba panopa ndi kuperekedwa kwa anthu amene avomera Yesu monga njira, choonadi ndi moyo (14.6). Chinthu chimene chofunikira kwambiri mu buku la

Yohane

ndicho kufotokozera zinthu zauzimu pogwiritsidwa ntchito zinthu zimene timazidziwa masiku onse monga madzi, chakudya, kuwala, mbusa ndi nkhosa zake, mphesa ndi zipatso zake. Ndipo kuchokera pa zinthu zoonekazo, bukuli limathandiza anthu okhulupirira kuti azindikire ndi kukopeka ndi zabwino zobisika zokhudza Mulungu ndi ufumu wake.

Za mkatimu

Chiyambi 1.1-18

Yohane Mbatizi ndi ophunzira oyamba a Yesu 1.19-51

Utumiki wa Yesu 2.1—12.50

Masiku omaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 13.1—17.26

Yesu agwidwa, nazengedwa mlandu, nafa pamtanda 18.1—19.42

Yesu auka kwa akufa naonekera ophunzira ake 20.1-31

Mau otsiriza: Yesu aonekeranso ophunzira ake ku Galileya 21.1-25

Categories
YOHANE

YOHANE 1

Umulungu wa Yesu Khristu

1 Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.

2 Awa anali pachiyambi kwa Mulungu.

3 Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwe kanthu kalikonse kolengedwa.

4 Mwa Iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.

5 Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikire.

Utumiki wa Yohane Mbatizi

6 Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane.

7 Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.

8 Iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku.

Yesu Khristu kuunika koona kutifikira mwa kubadwa m’thupi

9 Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m’dziko lapansi.

10 Anali m’dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye.

11 Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.

12 Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;

13 amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.

14 Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.

Umboni wa Yohane Mbatizi

15 Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.

16 Chifukwa mwa kudzala kwake tinalandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo.

17 Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa YesuKhristu.

18 Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.

19 Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a kuYerusalemuakamfunse iye, Ndiwe yani?

20 Ndipo anavomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Khristu.

21 Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. NdiweMneneriyo kodi? Nayankha, Iai.

22 Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena chiyani za iwe wekha?

23 Anati, Ndine mau a wofuula m’chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.

24 Ndipo otumidwawo anali a kwaAfarisi.

25 Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?

26 Yohane anawayankha, nati, Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa,

27 ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira chingwe cha nsapato yake.

28 Zinthu izi zinachitika mu Betaniya tsidya lija la Yordani, pomwe analikubatiza Yohane.

29 M’mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, OnaniMwanawankhosawa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!

30 Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.

31 Ndipo sindinamdziwe Iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israele, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi.

32 Ndipo Yohane anachita umboni, nati, Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye.

33 Ndipo sindinamdziwe Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.

34 Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.

Ophunzira oyamba a Yesu

35 M’mawa mwakenso analikuimirira Yohane ndi awiri aophunziraake;

36 ndipo poyang’ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!

37 Ndipo ophunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.

38 Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye,Rabi(ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?

39 Nanena nao, Tiyeni, mukaone. Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi.

40 Andrea mbale wake wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata Iye.

41 Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).

42 Anadza naye kwa Yesu. M’mene anamyang’ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).

43 M’mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.

44 Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mzinda wa Andrea ndi Petro.

45 Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m’chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.

46 Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.

47 Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!

48 Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.

49 Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.

50 Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzaona zoposa izi.

51 Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndiangeloa Mulungu akwera natsikira paMwana wa Munthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/1-9fba1f80c65f2713711e6a98d10a4bcf.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 2

Yesu asandutsa madzi vinyo ku Kana

1 Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati mu Kana wa mu Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko.

2 Ndipo Yesu yemwe ndiophunziraake anaitanidwa kuukwatiwo.

3 Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo.

4 Yesu nanena naye, Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga siinafike.

5 Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.

6 Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.

7 Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, ndendende.

8 Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwa mkulu wa phwando. Ndipo anapita nao.

9 Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwe kumene anachokera (koma atumiki amene adatunga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati,

10 nanena naye, Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.

11 Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.

12 Zitapita izi anatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake, ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka.

Yesu ayeretsa Kachisi poyamba paja

13 NdipoPaskawa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka kuYerusalemu.

14 Ndipo anapeza mu Kachisi iwo akugulitsa ng’ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi.

15 Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anatulutsa onse mu Kachisimo, ndi nkhosa ndi ng’ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome;

16 nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.

17 Ophunzira ake anakumbukira kuti kunalembedwa, Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine.

18 Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?

19 Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.

20 Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi chimodzi analimkumanga Kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu?

21 Koma Iye analikunena za Kachisi wa thupi lake.

22 Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.

23 Koma pamene anali mu Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.

24 Koma Yesu sanakhulupirire iwo kuti akhale nao, chifukwa Iye anadziwa anthu onse,

25 ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/2-401de3e8118c949bd7ea12771518a49f.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 3

Yesu aphunzitsa Nikodemo za kubadwa kwatsopano

1 Koma panali munthu waAfarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda.

2 Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye,Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.

3 Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.

4 Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m’mimba ya amake ndi kubadwa?

5 Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.

6 Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.

7 Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.

8 Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu.

9 Nikodemo anayankha nati kwa Iye, Izi zingatheke bwanji?

10 Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israele, ndipo sudziwa izi?

11 Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira.

12 Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupirira, mudzakhulupirira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?

13 Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiyeMwana wa Munthu, wokhala mu Mwambayo.

14 Ndipo monga Mose anakweza njoka m’chipululu, chotero Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa;

15 kuti yense wakukhulupirira akhale nao moyo wosatha mwa Iye.

16 Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

17 Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.

18 Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.

19 Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa.

20 Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.

21 Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.

Yohane achitanso umboni za Yesu

22 Zitapita izi anadza Yesu ndiophunziraake kudziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.

23 Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.

24 Pakuti Yohane sanaikidwe m’ndende.

25 Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ake a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe.

26 Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.

27 Yohane anayankha nati, Munthu sangathe kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba.

28 Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, SindineKhristu, koma kuti ndili wotumidwa m’tsogolo mwake mwa Iye.

29 Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.

30 Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe.

31 Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse.

32 Chimene anachiona nachimva, achita umboni wa ichi chomwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wake.

33 Iye amene analandira umboni wake anaikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali woona.

34 Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.

35 Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m’dzanja lake.

36 Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/3-b44c91b4881964c95b9439658caa460d.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 4

Mkazi wa ku Samariya

1 Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kutiAfarisiadamva kuti Yesu anayesa anthuophunzira, nawabatiza koposa Yohane

2 (angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake),

3 anachokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya.

4 Ndipo anayenera kupita pakati pa Samariya.

5 Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;

6 ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.

7 Kunali ngati ora lachisanu ndi chimodzi. Kunadza mkazi wotuluka mu Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.

8 Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumzinda kuti akagule chakudya.

9 Pamenepo mkazi wa mu Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkaziMsamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya).

10 Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.

11 Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe chotungira madzi, ndi chitsime chili chakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo?

12 Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake?

13 Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu;

14 koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.

15 Mkaziyo ananena kwa Iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga.

16 Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.

17 Mkazi anayankha nati kwa Iye, Ndilibe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndilibe;

18 pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona.

19 Mkazi ananena ndi Iye, Ambuye, ndizindikira kuti muliMneneri.

20 Makolo athu analambira m’phiri ili; ndipo inu munena, kuti muYerusalemumuli malo oyenera kulambiramo anthu.

21 Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri ili, kapena mu Yerusalemu.

22 Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso chichokera kwa Ayuda.

23 Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.

24 Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’choonadi.

25 Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.

26 Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.

27 Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani?

28 Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wake, namuka mumzinda, nanena ndi anthu,

29 Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu saliKhristunanga?

30 Anatuluka iwo m’mzinda ndipo analinkudza kwa Iye.

Za masika ndi antchito

31 Pa mphindikati iyi ophunzira ake anampempha Iye, ndi kunena,Rabi, idyani.

32 Koma Iye anati kwa iwo, Ine ndili nacho chakudya chimene inu simuchidziwa.

33 Chifukwa chake ophunzira ananena wina ndi mnzake, Kodi pali wina anamtengera Iye kanthu kakudya?

34 Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.

35 Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.

36 Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.

37 Pakuti m’menemo chonenacho chili choona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso.

38 Ine ndinatuma inu kukamweta chimene simunagwirirapo ntchito: ena anagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yao.

Yesu ndi Asamariya

39 Ndipo m’mzinda muja anthuAsamariyaambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.

40 Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.

41 Ndipo ambiri oposa anakhulupirira chifukwa cha mau ake;

42 ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.

Yesu achiritsa mwana wa Mkulu

43 Koma atapita masiku awiriwo anachoka komweko kunka ku Galileya.

44 Pakuti Yesu mwini anachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m’dziko la kwao.

45 Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero.

46 Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa mu Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala mu Kapernao.

47 Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wachokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa Iye, nampempha kuti atsike kukachiritsa mwana wake; pakuti anali pafupi imfa.

48 Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.

49 Mkuluyo ananena kwa Iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga.

50 Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo. Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka.

51 Ndipo m’mene analikutsika, akapolo ake anakomana naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo.

52 Chifukwa chake anawafunsa ora lake anayamba kuchiralo. Pamenepo anati kwa iye, kuti, Dzulo, ora lachisanu ndi chiwiri malungo anamsiya.

53 Chifukwa chake atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupirira iye yekha ndi a pa banja lake onse.

54 Ichi ndi chizindikiro chachiwiri Yesu anachita, atachokera ku Yudeya, ndi kulowa mu Galileya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/4-44d2690419aabbc708da975fc95a26d9.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 5

Yesu achiritsa wopuwala kuthamanda la Betesida

1 Zitapita izi panali chikondwerero cha Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka kuYerusalemu.

2 Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.

3 M’menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.

5 Koma panali munthu wina apo, ali m’kudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.

6 Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikulu pamenepo, ananena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi?

7 Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndilibe wondiviika ine m’thamanda, paliponse madzi avundulidwa; koma m’mene ndilinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.

8 Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende.

9 Ndipo pomwepo munthuyu anachira, nayalula mphasa yake, nayenda. Koma tsiku lomwelo linali laSabata.

10 Chifukwa chake Ayuda ananena kwa wochiritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.

11 Koma iyeyu anayankha iwo, Iye amene anandichiritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende.

12 Anamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende?

13 Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m’malo muja.

14 Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.

15 Munthuyo anachoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa.

Yesu adziwulula kuti ali Mwana wa Mulungu

16 Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata.

17 Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.

18 Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.

19 Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sangathe Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.

20 Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa ntchito zoposa izi, kuti mukazizwe.

21 Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.

22 Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana;

23 kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye.

24 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m’kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m’moyo.

25 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.

26 Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha;

27 ndipo anampatsa Iye mphamvu ya kuchita mlandu, pakuti aliMwana wa Munthu.

28 Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mau ake,

29 nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.

30 Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.

31 Ngati ndichita umboni wa Ine ndekha, umboni wanga suli woona.

32 Wochita umboni wa Ine ndi wina; ndipo ndidziwa kuti umboni umene Iye andichitire Ine uli woona.

33 Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anachitira umboni choonadi.

34 Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu: koma ndinena izi, kuti inu mukapulumutsidwe.

35 Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m’kuunika kwake kanthawi.

36 Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.

37 Ndipo Atate wonditumayo, Iyeyu wandichitira Ine umboni. Simunamva mau ake konse, kapena maonekedwe ake simunaone.

38 Ndipo mulibe mau ake okhala mwa inu; chifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.

39 Musanthula m’malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;

40 ndipo simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo.

41 Ulemu sindiulandira kwa anthu.

42 Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha.

43 Ndadza Ine m’dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m’dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamlandira.

44 Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?

45 Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama.

46 Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; pakuti iyeyu analembera za Ine.

47 Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mau anga?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/5-5c8da6a107cc9a108ec4e928ef8be467.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 6

Yesu achulukitsa mikate

1 Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.

2 Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.

3 Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndiophunziraake.

4 NdipoPaska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira.

5 Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?

6 Koma ananena ichi kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha chimene adzachita.

7 Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang’ono.

8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,

9 Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere?

10 Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.

11 Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.

12 Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.

13 Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza madengu khumi ndi awiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo.

14 Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiyemnenerindithu wakudzayo m’dziko lapansi.

15 Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.

Yesu ayenda panyanja

16 Koma pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira kunyanja;

17 ndipo pamene adalowa m’ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.

18 Ndipo nyanja inalikuuka chifukwa cha mphepo yaikulu yakuombako.

19 Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha.

20 Koma Iye ananena nao, Ndine; musaope.

21 Pamenepo analola kumlandira m’ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako.

Yesu mkate wamoyo wa okhulupirira

22 M’mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m’ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha;

23 koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate m’mene Ambuye Yesu adayamika;

24 chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m’ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.

25 Ndipo pamene anampeza Iye tsidya lina la nyanja, anati kwa Iye,Rabi, munadza kuno liti?

26 Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.

27 Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimeneMwana wa Munthuadzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.

28 Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?

29 Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma.

30 Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?

31 Atate athu anadyamanam’chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m’mwamba anawapatsa iwo kudya.

32 Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.

33 Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.

34 Pamenepo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.

35 Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.

36 Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.

37 Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.

38 Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.

39 Koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi ichi, kuti za ichi chonse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza.

40 Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

41 Chifukwa chake Ayuda anang’ung’udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.

42 Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?

43 Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang’ung’udze wina ndi mnzake.

44 Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

45 Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.

46 Sikuti munthu wina waona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate.

47 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira ali nao moyo wosatha.

48 Ine ndine mkate wamoyo.

49 Makolo anu adadya m’chipululu, ndipo adamwalira.

50 Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira.

51 Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.

52 Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?

53 Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.

54 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

55 Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.

56 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.

57 Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.

58 Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.

59 Izi ananena m’sunagoge, pakuphunzitsa mu Kapernao.

Ophunzira ambiri aleka kutsata Yesu

60 Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?

61 Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung’ung’udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?

62 Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa Munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?

63 Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.

64 Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.

65 Ndipo ananena, Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.

Chivomerezo cha Petro

66 Pa ichi ambiri a ophunzira ake anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayendeyendenso ndi Iye.

67 Chifukwa chake Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka?

68 Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.

69 Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.

70 Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?

71 Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/6-3a0ee6223a373a174fa399efa56fb215.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 7

Abale a Yesu samvomereza

1 Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.

2 Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira.

3 Chifukwa chake abale ake anati kwa Iye, Chokani pano, mumuke ku Yudeya, kutiophunziraanunso akapenye ntchito zanu zimene muchita.

4 Pakuti palibe munthu achita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera. Ngati muchita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi.

5 Pakuti angakhale abale ake sanakhulupirire Iye.

6 Chifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse.

7 Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.

8 Kwerani inu kunka kuphwando; sindikwera Ine kuphwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.

9 Ndipo m’mene adanena nao zimenezi anakhalabe mu Galileya.

Yesu aphunzitsa mu Kachisi. Ayesa kumgwira

10 Koma pamene abale ake adakwera kunka kuchikondwerero, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika.

11 Pomwepo Ayuda analikumfuna Iye pachikondwerero, nanena, Ali kuti uja?

12 Ndipo kunali kung’ung’udza kwambiri za Iye m’makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo.

13 Chinkana anatero panalibe munthu analankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuopa Ayuda.

14 Koma pamene padafika pakati pa chikondwerero, Yesu anakwera nalowa mu Kachisi, naphunzitsa.

15 Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?

16 Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.

17 Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.

18 Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.

19 Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha chifukwa ninji?

20 Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu?

21 Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa monse.

22 Chifukwa cha ichi Mose anakupatsani inumdulidwe(si kuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo); ndipo mudula munthu tsiku laSabata.

23 Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata?

24 Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.

25 Pamenepo ena a iwo a kuYerusalemuananena, Kodi suyu amene afuna kumupha?

26 Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiyeKhristuameneyo?

27 Koma ameneyo tidziwa uko achokera: koma Khristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko achokera.

28 Pamenepo Yesu anafuula mu Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.

29 Ine ndimdziwa Iye; chifukwa ndili wochokera kwa Iye, nandituma Ine Iyeyu.

30 Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.

31 Koma ambiri a m’khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?

32 Afarisianamva khamu la anthu ling’ung’udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye.

33 Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine.

34 Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo.

35 Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki?

36 Mau awa amene ananena ndi chiyani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo?

Yesu aneneratu za Mzimu Woyera

37 Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.

38 Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m’kati mwake.

39 Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.

Anthu atsutsana za Iye

40 Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena,Mneneriyo ndi uyu ndithu.

41 Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?

42 Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?

43 Kudakhala tsono kusiyana m’khamulo chifukwa cha Iye.

44 Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.

45 Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe aakulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenge Iye bwanji?

46 Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero.

47 Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso?

48 Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi?

49 Koma khamu ili losadziwa chilamulo, likhala lotembereredwa.

50 Nikodemo ananena kwa iwo, amene uja adadza kwa Iye kale, ali mmodzi wa iwo,

51 Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?

52 Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuone kuti mu Galileya sanauke mneneri.

53 Ndipo anamuka munthu yense kunyumba yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/7-5b1c141fa61ac62554bd106b19a72f85.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 8

Za mkazi wachigololo

1 Koma Yesu anamuka kuphiri la Azitona.

2 Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m’mene anakhala pansi anawaphunzitsa.

3 Koma alembi ndiAfarisianabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m’chigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati,

4 ananena kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkuchita chigololo.

5 Koma m’chilamulo Mose anatilamula, tiwaponye miyala otere. Chifukwa chake Inu munena chiyani za iye?

6 Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m’mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.

7 Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.

8 Ndipo m’mene adaweramanso analemba ndi chala chake pansi.

9 Koma iwo, m’mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.

10 Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?

11 Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso.

Yesu wotumidwa ndi Atate

12 Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.

13 Chifukwa chake Afarisi anati kwa Iye, Muchita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli woona.

14 Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.

15 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.

16 Ndipo ngati ndiweruza Ine, chiweruziro changa chili choona; pakuti sindili pa ndekha, koma Ine ndi Atate amene anandituma Ine.

17 Inde kudalembedwa m’chilamulo chanu kuti umboni wa anthu awiri uli woona.

18 Ine ndine wakuchita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine achita umboni wa Ine.

19 Chifukwa chake ananena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga.

20 Mau awa analankhula m’nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.

21 Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m’tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.

22 Chifukwa chake Ayuda anenana, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?

23 Ndipo ananena nao, Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi.

24 Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m’machimo kwa inu, kuti mudzafa m’machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m’machimo anu.

25 Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.

26 Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.

27 Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate.

28 Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkwezaMwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.

29 Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiye Iye pa ndekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.

30 Pakulankhula Iye zimenezi ambiri anakhulupirira Iye.

31 Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m’mau anga, muliophunziraanga ndithu;

32 ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.

33 Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhale akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu?

34 Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.

35 Koma kapolo sakhala m’nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.

36 Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

37 Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu.

38 Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu.

39 Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.

40 Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite.

41 Inu muchita ntchito za atate wanu. Anati kwa Iye, Sitinabadwe ife m’chigololo; tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.

42 Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadze kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.

43 Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga.

44 Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m’choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.

45 Koma Ine, chifukwa ndinena choonadi, simukhulupirira Ine.

46 Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji?

47 Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.

48 Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinuMsamariya, ndipo muli ndi chiwanda?

49 Yesu anayankha, Ndilibe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.

50 Koma Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza.

51 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.

52 Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.

53 Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?

54 Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu;

55 ndipo inu simunamdziwe Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mau ake.

56 Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona nasangalala.

57 Ayuda pamenepo anati kwa Iye, Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi?

58 Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.

59 Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/8-98cef08d3bf9da2b376256f706101014.mp3?version_id=1068—

Categories
YOHANE

YOHANE 9

Achiritsidwa munthu wosaona chibadwire

1 Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona chibadwire.

2 Ndipoophunziraake anamfunsa Iye, nanena,Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona?

3 Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.

4 Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.

5 Pakukhala Ine m’dziko lapansi, ndili kuunika kwa dziko lapansi.

6 Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m’maso,

7 nati kwa iye, Muka, kasambe m’thamanda la Siloamu (ndilo losandulika, Wotumidwa). Pamenepo anachoka, nasamba, nabwera alikuona.

8 Chifukwa chake anzake ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?

9 Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, Iai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene.

10 Pamenepo anenana ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji?

11 Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m’maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m’mene ndinasamba ndinapenya.

12 Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine.

13 Anapita naye amene anali wosaona kale kwaAfarisi.

14 Koma tsikulo ndi laSabatalimene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ake.

15 Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera. Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m’maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.

16 Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.

17 Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za Iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, AliMneneri.

18 Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya;

19 nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona?

20 Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wake ndi amake anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona;

21 koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.

22 Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiyeKhristu, akhale woletsedwa m’sunagoge.

23 Chifukwa cha ichi atate wake ndi amake anati, Ali wamsinkhu; mumfunse iye.

24 Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.

25 Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wochimwa, sindidziwa; chinthu chimodzi ndichidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya.

26 Chifukwa chake anati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji?

27 Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamve; mufuna kumvanso bwanji? Kodi inunso mufuna kukhala ophunzira ake?

28 Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife ophunzira a Iyeyu, ife ndife ophunzira a Mose.

29 Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene achokera ameneyo.

30 Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m’menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.

31 Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.

32 Kuyambira pachiyambi sikunamveke kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire.

33 Ngati uyu sanachokere kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.

34 Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m’zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.

35 Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupiriraMwana wa Munthu?

36 Iyeyu anayankha nati, Ndipo ndani Iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire Iye?

37 Yesu anati kwa iye, Wamuona Iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo.

38 Koma iye anati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo anamgwadira Iye.

39 Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.

40 Ndipo Afarisi ena akukhala ndi Iye anamva izi, nati kwa Iye, Kodi ifenso ndife osaona?

41 Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/9-c2efc42050d0cd8b4e5e9ce8b76efca3.mp3?version_id=1068—