Categories
YOBU

YOBU 40

1 Ndipo Yehova anabwereza kwa Yobu, nati,

2 Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse?

Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.

3 Pamenepo Yobu anayankha Yehova nati,

4 Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani?

Ndigwira pakamwa.

5 Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha;

inde kawiri, koma sindionjezanso.

6 Ndipo Yehova anamyankha Yobu m’kamvulumvulu, nati,

7 Dzimangire m’chuuno tsono ngati mwamuna;

ndidzakufunsa, undidziwitse.

8 Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi?

Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi,

kuti ukhale wolungama ndiwe?

9 Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?

Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?

10 Udzikometsere tsono ndi ukulu ndi kukuzika,

nuvale ulemu ndi ulemerero.

11 Tsanulira mkwiyo wako wosefuka,

nupenyerere aliyense wodzikuza ndi kumchepetsa.

12 Upenyerere aliyense wodzikuza, numtsitse,

nupondereze oipa pomwe akhala.

13 Uwakwirire pamodzi m’fumbi,

uzimange nkhope zao pobisika.

14 Pamenepo inenso ndidzakuvomereza,

kuti dzanja lakolako lamanja likupulumutsa.

15 Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe,

ikudya udzu ngati ng’ombe.

16 Tapenya tsono, mphamvu yake ili m’chuuno mwake,

ndi kulimbalimba kwake kuli m’mitsempha ya m’mimba yake.

17 Igwedeza mchira wake ngati mkungudza;

mitsempha ya ntchafu zake ipotana.

18 Mafupa ake akunga misiwe yamkuwa;

ziwalo zake zikunga zitsulo zamphumphu.

19 Iyo ndiyo chiyambi cha machitidwe a Mulungu;

wakuilenga anaininkha lupanga lake.

20 Pakuti mapiri aiphukitsira chakudya,

kumene zisewera nyama zonse zakuthengo.

21 Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi,

pobisala pabango ndi pathawale.

22 Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao,

misondodzi ya kumtsinje iizinga.

23 Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera;

ilimbika mtima, ngakhale Yordani atupa mpaka pakamwa pake.

24 Ikakhala maso, munthu adzaigwira kodi?

Kapena kuboola m’mphuno mwake ili m’khwekhwe?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/40-1e6529ccf0fa7095a692e8a602fb6a4d.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 41

1 Kodi ukhoza kukokaLeviyatanindi mbedza?

Kapena kukanikiza kalandira wake ndi chingwe?

2 Kodi ukhoza kumanga m’mphuno ndi mlulu?

Kapena kuboola nsagwada wake ndi mbedza?

3 Kodi idzachulukitsa mau akukupembedza?

Kapena idzanena nawe mau ofatsa?

4 Kodi idzapangana ndi iwe,

kuti uitenge ikhale kapolo wako wachikhalire?

5 Kodi udzasewera nayo ngati mbalame?

Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete?

6 Kodi opangana malonda adzaitsatsa?

Adzaigawana eni malonda?

7 Kodi udzadzaza khungu lake ndi ntchetho,

kapena mutu wake ndi miomba?

8 Isanjike dzanja lako;

ukakumbukira nkhondoyi, sudzateronso.

9 Taona, chiyembekezo chako cha pa iyo chipita pachabe.

Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?

10 Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa.

Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?

11 Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze?

Zilizonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.

12 Sindikhala chete osatchula ziwalo za ng’onayo,

ndi mbiri ya mphamvu yake, ndi makonzedwe ake okoma.

13 Ndani adzasenda chovala chake chakunja?

Adzalowa ndani kumizere iwiri ya mano ake?

14 Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pake?

Mano ake aopsa pozungulira pao.

15 Mamba ake olimba ndiwo kudzitama kwake;

amangika pamodzi ngati okomeredwatu.

16 Alumikizana lina ndi linzake,

mphepo yosalowa pakati pao.

17 Amamatirana lina ndi linzake,

agwirana osagawanikana.

18 Pakuyetsemula ing’anipitsa kuunika,

ndi maso ake akunga zikope za m’mawa.

19 M’kamwa mwake mutuluka miuni,

mbaliwali za moto zibukamo.

20 M’mphuno mwake mutuluka utsi,

ngati nkhali yobwadamuka ndi moto wa zinyatsi

21 mpweya wake uyatsa makala,

ndi m’kamwa mwake mutuluka lawi la moto.

22 Kukhosi kwake kukhala mphamvu,

ndi mantha avumbuluka patsogolo pake.

23 Nyama yake yopsapsala igwirana

ikwima pathupi pake yosagwedezeka.

24 Mtima wake ulimba ngati mwala,

inde ulimba ngati mwala wa mphero.

25 Ikanyamuka, amphamvu achita mantha;

chifukwa cha kuopsedwa azimidwa nzeru.

26 Munthu akaiyamba ndi lupanga, ligoma;

ngakhale nthungo, kapena muvi, kapena mkondo.

27 Chitsulo ichiyesa phesi,

ndi mkuwa ngati mtengo woola.

28 Muvi suithawitsa,

miyala ya pachoponyera iisandutsa chiputu.

29 Zibonga ziyesedwa chiputu,

iseka kuthikuza kwake kwa nthungo.

30 Kumimba kwake ikunga mapale akuthwa,

itasalala kuthope ngati chopunthira.

31 Ichititsa nthubwinthubwi pozama ngati nkhali,

isanduliza nyanja ikunge mafuta.

32 Ichititsa mifunde yonyezimira pambuyo pake;

munthu akadati pozama pali ndi imvi.

33 Padziko lapansi palibe china cholingana nayo,

cholengedwa chopanda mantha.

34 Ipenya chilichonse chodzikuza,

ndiyo mfumu ya zodzitama zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/41-f9fb380fe6f436d6af11a46c49efd6ed.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 42

Yobu adzichepetsa pamaso pa Mulungu, mabwenziwo adzudzulidwa ndi Mulungu, Yobu apulumutsidwa nadalitsidwanso

1 Pamenepo Yobu anayankha Yehova, nati,

2 Ndidziwa kuti mukhoza kuchita zonse,

ndi kuti palibe choletsa cholingirira chanu chilichonse.

3 Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu?

Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikire,

zondidabwitsa, zosazidziwa ine.

4 Tamveranitu, ndidzanena ine,

ndidzakufunsani, mundidziwitse.

5 Kumva ndidamva mbiri yanu,

koma tsopano ndikupenyani maso;

6 chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa

m’fumbi ndi mapulusa.

7 Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.

8 Ndipo tsono, mudzitengere ng’ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.

9 Namuka Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, nachita monga Yehova adawauza; ndipo Yehova anavomereza Yobu.

10 Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.

11 Pamenepo anamdzera abale ake onse, ndi alongo ake onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m’nyumba yake, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndalama ndi mphete yagolide.

12 Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake, ndipo anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinai, ndingamirazikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng’ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu aakazi chikwi chimodzi.

13 Anali naonso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu.

14 Ndipo anamutcha dzina la woyamba Yemima, ndi dzina la wachiwiri Keziya, ndi dzina la wachitatu Kerenihapuki.

15 Ndipo m’dziko monse simunapezeke akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, nawapatsa cholowa atate wao pamodzi ndi alongo ao.

16 Ndipo zitatha izi, Yobu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi mphambu makumi anai, naona ana ake ndi zidzukulu zake mibadwo inai.

17 Namwalira Yobu, wokalamba ndi wa masiku ochuluka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/42-b498856fe6ef03dc6b1b05409a179fba.mp3?version_id=1068—