Categories
YOBU

YOBU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba za Yobu, munthu wolungama amene anakumana ndi mavuto aakulu, nakhala akuzunzika ndi kudandaula, nafunitsitsa kudziwa chifukwa chimene Mulungu walolera zoterezi.

Yobu anagwa m’mavuto aakulu: ana ake onse anafa, chuma chake chonse nkuwonongeka, ndipo mwinawakeyo anagwidwa ndi nthenda yoopsa, thupi lake nkuwola.

Abwenzi ake atatu anabwera kudzampepesa pa mavuto akewo, nayamba kukambirana za gwero lake la mavutowo, aliyense natulutsa maganizo ake. Abwenzi atatu aja, pofuna kufotokoza za gwero la mavuto a Yobu, angotsata maganizo a makolo achiyuda, akuti Mulungu amadalitsa anthu abwino ndipo amalanga anthu ochimwa; ndiye kuti mavuto amene Yobuyu anakumana nawo akusonyeza kuti iye anachimwa. Pamenepo Yobu akuti, Iyayi, nchosatheka; pakuti iyeyo wakhala akuyesetsa kukhala wabwino ndi wolungama masiku onse. Chifukwa chosamvetsa gwero lake la mavuto akewo, ayamba kufunsa Mulungu mafunso, ndipo amupempha kuti achitepo kanthu kosonyeza kuti iye ngwolungamadi, ndipo motero mbiri yake isaipitsidwe pamaso pa anthu.

Yehova poyankha sasamala mafunso a Yobu aja, angomuwonetsa ukulu wake, mphamvu zake ndi nzeru zake zodabwitsa, kulimbitsa chikhulupiriro cha Yobu. Apo Yobuyo adzichepetsa pamaso pa Mulungu ndipo amupepesa chifukwa cha mau okalipa aja omwe iye adalankhula potsutsana ndi Yehova.

Pambuyo pake Mulungu amudalitsa Yobu pomubwezera zabwino zake mowirikiza, ndipo adzudzula abwenzi ake atatu aja, chifukwa iwo adalephera kumvetsa tanthauzo la mavuto a Yobu. Yobu yekhayu adazindikira kuti Mulungu ngwamkulu koposa m’mene makolo achiyuda ankaganizira.

Za mkatimu

Mau oyambirira

1.1—2.13

Yobu ndi abwenzi ake

3.1—31.40

a. Kudandaula kwa Yobu

3.1-26

b. Kukambirana koyamba

4.1—14.22

c. Kukambirana kwachiwiri

15.1—21.34

d. Kukambirana kwachitatu

22.1—27.23

e. Mau oyamikira nzeru

28.1-28

f. Mau otsiriza a Yobu

29.1—31.40

Mau a Elihu

32.1—37.24

Mau a Yehova oyankha Yobu

38.1—42.6

Mau omaliza

42.7-17

Categories
YOBU

YOBU 1

Yobu wosautsidwabe alimbika kutama Mulungu

1 Panali munthu m’dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.

2 Ndipo anabala ana aamuna asanu ndi awiri, ndi ana aakazi atatu.

3 Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndingamirazikwi zitatu, ndi ng’ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum’mawa.

4 Ndipo ana ake aamuna anamuka kukachita madyerero m’nyumba ya yense pa tsiku lake; natumiza mthenga kuitana alongo ao atatu adzadye nadzamwe nao.

5 Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m’mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.

6 Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzansoSatanapakati pao.

7 Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m’dziko ndi kuyendayenda m’mwemo.

8 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.

9 Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe?

10 Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m’dziko.

11 Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.

12 Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m’dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.

13 Tsono panali tsiku loti ana ake aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya mkulu wao;

14 nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng’ombe zinalikulima, ndi abulu aakazi analikudya pambali pao;

15 koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

16 Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

17 Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Ababiloni anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamira, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

18 Akali chilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya mkulu wao;

19 ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

20 Pamenepo Yobu ananyamuka, nang’amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,

21 nati, Ndinatuluka m’mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.

22 Mwa ichi chonse Yobu sanachimwe, kapena kunenera Mulungu cholakwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/1-39622e1b07c595d70d8d6edbd856ff10.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 2

1 Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadzaSatanayemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.

2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m’dziko, ndi kuyendayenda m’mwemo.

3 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa.

4 Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.

5 Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.

6 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m’dzanja lako; moyo wake wokha uuleke.

7 Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.

8 Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m’maphulusa.

9 Pamenepo mkazi wake ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.

10 Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.

Mabwenzi ake atatu adzacheza naye

11 Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

12 Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang’amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao.

13 Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukulu ndithu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/2-7862c23242b46a078b9b4cba4e23b540.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 3

Madandaulo a Yobu

1 Atatero, Yobu anatsegula pakamwa pake, natemberera tsiku lake.

2 Nalankhula Yobu nati,

3 Litayike tsiku lobadwa ine,

ndi usikuwo udati, Waima naye mwana wamwamuna.

4 Tsiku lija likhale mdima;

Mulungu asalifunse kumwamba,

ndi kuunika kusaliwalire.

5 Mdima ndi mthunzi wa imfa ziliyese laolao;

mtambo ulikhalire;

zonse zodetsa usana bii ziliopse.

6 Usiku uja, mdima weniweni uugwere;

usakondwerere mwa masiku a m’chaka;

usalowe m’chiwerengedwe cha miyezi.

7 Ha! Usiku uja ukhale chumba;

kuimbira kokondwera kusalowe m’mwemo.

8 Autemberere iwo akutemberera usana,

Odziwa kuutsaLeviyatani.

9 Nyenyezi za chizirezire zide;

uyembekezere kuunika, koma kuusowe;

usaone kephenyuka kwa mbandakucha;

10 popeza sunatseke pa makomo ake mimba ya mai wanga.

Kapena kundibisira mavuto pamaso panga.

11 Ndinalekeranji kufera m’mimba?

Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine.

12 Anandilandiriranji maondo?

Kapena mawere kuti ndiyamwe?

13 Pakuti ndikadagona pansi pomwepo ndi kukhala chete;

ndikanagona tulo; pamenepo ndikadaona popumula;

14 pamodzi ndi mafumu ndi maphungu a padziko,

akudzimangira m’mabwinja;

15 kapena pamodzi ndi akalonga eni ake a golide,

odzaza nyumba zao ndisiliva;

16 Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zii;

ngati makanda osaona kuunika.

17 Apo oipa aleka kumavuta;

ndi apo ofooka mphamvu akhala m’kupumula.

18 Apo a m’kaidi apumula pamodzi,

osamva mau a wofulumiza wao.

19 Ang’ono ndi akulu ali komwe;

ndi kapolo amasuka kwa mbuyake.

20 Amninkhiranji kuunika wovutika,

ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima,

21 wakuyembekezera imfa, koma kuli zii,

ndi kuikumba koposa chuma chobisika,

22 wakusekerera ndi chimwemwe

ndi kukondwera pakupeza manda?

23 Amuonetseranji kuunika munthu wa njira yobisika,

amene wamtsekera Mulungu?

24 Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga;

ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.

25 Pakuti chimene ndinachiopa chandigwera,

ndi chimene ndachita nacho mantha chandidzera.

26 Wosakhazikika, ndi wosakhala chete, ndi wosapumula ine,

koma mavuto anandidzera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/3-6202c66f3a581cf16dd9267fbbf35907.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 4

Elifazi adzudzula Yobu

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2 Munthu akayesa kunena nawe mau,

kodi udzamva nao chisoni?

Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?

3 Taona iwe walangiza aunyinji,

walimbitsa manja a ofooka.

4 Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa,

walimbitsanso maondo otewa.

5 Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka;

chikukhudza, ndipo uvutika.

6 Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,

ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako?

7 Takumbukira tsopano, watayika ndani wosapalamula konse?

Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?

8 Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu,

nabzala vuto, akololapo zomwezo.

9 Atayika ndi mpweya wa Mulungu,

nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.

10 Kubangula kwa mkango,

ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,

ndi mano a misona ya mkango athyoledwa.

11 Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,

ndi misona ya mkango waukazi imwazika.

12 Anditengera mau m’tseri,

m’khutu mwanga ndinalandira kunong’oneza kwake.

13 M’malingaliro a masomphenya a usiku,

powagwira anthu tulo tatikulu

14 Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,

nanthunthumira nako mafupa anga onse.

15 Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;

tsitsi la thupi langa lidati nyaunyau.

16 Unaima chilili, koma sindinathe kuzindikira maonekedwe ake;

panali mzukwa pamaso panga;

kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti,

17 Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?

Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake?

18 Taona, sakhulupirira atumiki ake;

nawanenera amithenga ake zopusa;

19 kopambana kotani nanga iwo akukhala m’nyumba zadothi,

amene kuzika kwao kuli m’fumbi,

angothudzulidwa ngati njenjete.

20 Kuyambira m’mawa kufikira madzulo athudzuka;

aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.

21 Kukometsetsa kwao sikumachotsedwa nao?

Amafa koma opanda nzeru.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/4-c4008d5cfe7524034f6cf5fb55f3f00e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 5

1 Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi?

Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo?

2 Pakuti mkwiyo umapha wopusa,

ndi nsanje imakantha wopanda pake.

3 Ndinapenya wopusa woyala mizu;

koma pomwepo ndinatemberera pokhala pake.

4 Ana ake akhala otekeseka,

napsinjika kuchipata,

wopanda wina wakuwapulumutsa.

5 Zokolola zao anjala azidya,

azitenga ngakhale kuminga,

ndi aludzu ameza chuma chao.

6 Pakuti nsautso sutuluka m’fumbi,

ndi mavuto saphuka m’nthaka.

7 Koma munthu abadwira mavuto,

monga mbaliwali zikwera ziuluzika.

8 Koma ine ndikadafuna Mulungu,

ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;

9 amene achita zazikulu ndi zosalondoleka,

zinthu zodabwitsa zosawerengeka.

10 Amene avumbitsa mvula panthaka,

natumiza madzi paminda;

11 kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka,

kuti iwo a maliro akwezedwe kosatekeseka.

12 Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera,

kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.

13 Akola eni nzeru m’kuchenjera kwao,

ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pachabe.

14 Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa,

nayambasa dzuwa lili pakati pamutu monga usiku.

15 Apulumutsa aumphawi kulupanga

la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu.

16 Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo,

ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.

17 Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula;

chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.

18 Pakuti apweteka, namanganso mabala;

alasa, ndi manja ake omwe apoletsa.

19 Adzakupulumutsa m’masautso asanu ndi limodzi;

chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.

20 Adzakuombola kuimfa m’njala,

ndi kumphamvu ya lupanga m’nkhondo.

21 Udzabisikira mkwapulo wa lilime,

sudzachiopanso chikadza chipasuko.

22 Chipasuko ndi njala udzaziseka;

ngakhale zilombo za padziko osaziopa.

23 Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala yakuthengo;

ndi nyama zakuthengo zidzakhala nawe mumtendere.

24 Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere;

nudzazonda za m’banja mwako osasowapo kanthu.

25 Udzapezanso kuti mbeu zako zidzachuluka,

ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.

26 Udzafika kumanda utakalamba,

monga abwera nao mtolo wa tirigu m’nyengo yake.

27 Taona, ichi tachifunafuna, chili chotero;

uchimvere, nuchidziwire wekha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/5-35f8439fd0bb1a9554af3b9fdb4ba2a9.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 6

Yobu adzilungamitsa pa kudandaula kwake

1 Koma Yobu anayankha, nati,

2 Mwenzi atayesa bwino chisoni changa,

ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso!

3 Pakuti zikadalemera tsopano koposa mchenga wa kunyanja;

chifukwa chake mau anga ndasonthokera kunena.

4 Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa,

mzimu wanga uwumwa ulembe wake;

zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.

5 Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu?

Ilira kodi ng’ombe pa chakudya chake?

6 Kodi chinthu chosakolera chidyeka chopanda mchere?

Choyera cha dzira chikolera kodi?

7 Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza

zikunga chakudya chosakolera kwa ine.

8 Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha,

Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira!

9 Chimkomere Mulungu kundiphwanya,

alole dzanja lake lindilikhe!

10 Pamenepo ndidzasangalala,

ndidzakondwera nacho chowawa chosandileka;

pakuti sindinawabise mau a Woyerayo.

11 Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze?

Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?

12 Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala?

Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?

13 Mulibe thandizo mwa ine ndekha; chipulumutso chandithawa.

14 Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo;

angaleke kuopa Wamphamvuyonse.

15 Abale anga anachita monyenga ngati kamtsinje,

ngati madzi a timitsinje akupitirira.

16 Amada chifukwa cha madzi oundana.

M’menemo chipale chofewa chibisika;

17 atafikira mafundi, mitsinje iuma;

kukatentha, imwerera m’malo mwao.

18 Aulendo akutsata njira yao apatukapo,

akwerera poti see, natayika.

19 Aulendo a ku Tema anapenyerera,

makamu a ku Sheba anaiyembekezera.

20 Anazimidwa popeza adaikhulupirira;

anafikako, nathedwa nzeru.

21 Pakuti tsopano mukhala momwemo;

muona choopsa, muchitapo mantha.

22 Ngati ndinati, Mundipatse?

Kapena, Muperekeko kwa ine chuma chanu?

23 Kapena, Mundilanditse m’dzanja la mdani?

Kapena, Mundiombole m’dzanja la oopsa?

24 Mundilangize, ndipo ndidzakhala chete ine;

mundizindikiritse umo ndinalakwira.

25 Mau oongoka si ndiwo amphamvu?

Koma kudzudzula kwanu mudzudzula chiyani?

26 Kodi muyesa kudzudzula mau?

Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.

27 Indetu, mugwetsera wamasiye msampha,

mumkumbira bwenzi lanu mbuna.

28 Koma tsopano balindani, mundipenyerere;

ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira.

29 Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu;

inde, bwereraninso mlandu wanga ngwolungama.

30 Kodi pali chosalungama palilime panga?

Ngati sindizindikire zopanda pake m’kamwa mwanga?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/6-622f1e656ca2334371fef00e9a5cd165.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 7

1 Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno?

Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?

2 Monga kapolo woliralira mthunzi,

monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,

3 momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pake.

Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.

4 Ndigona pansi, ndikuti,

Ndidzauka liti? Koma usiku undikulira;

ndipo ndimapalapata mpaka mbandakucha.

5 Mnofu wanga wavala mphutsi ndi nkanambo zadothi;

khungu langa lang’ambika, nilinyansa.

6 Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba,

apitirira opanda chiyembekezo.

7 Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo,

diso langa silidzaonanso chokoma.

8 Diso la amene andiona silidzandionanso,

maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.

9 Mtambo wapita watha,

momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.

10 Sadzabweranso kunyumba yake,

osamdziwanso malo ake.

11 Potero sindidzaletsa pakamwa panga;

ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga;

ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.

12 Ndine nyanja kodi, kapena chinjoka cha m’nyanja,

kuti Inu mundiikira odikira?

13 Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,

pogona panga padzachepsa chondidandaulitsa;

14 pamenepo mundiopsa ndi maloto,

nimundichititsa mantha ndi masomphenya;

15 potero moyo wanga usankha kupotedwa,

ndi imfa, koposa mafupa anga awa.

16 Ndinyansidwa nao moyo wanga;

sindidzakhala ndi moyo chikhalire;

mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.

17 Munthu ndani kuti mumkuze,

ndi kuti muike mtima wanu pa iye,

18 ndi kuti mucheze naye m’mawa ndi m’mawa,

ndi kumuyesa nthawi zonse?

19 Mukana kundichokera kufikira liti,

kapena kundileka mpaka nditameza dovu?

20 Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani,

Inu wodikira anthu?

Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu?

Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?

21 Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga

ndi kundichotsera mphulupulu yanga?

Popeza tsopano ndidzagona kufumbi;

mudzandifunafuna, koma ine palibe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/7-733b988db546a25ec801104bdc4ae2fc.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 8

Poona tsoka lao Bilidadi akuti Yobu ndi ana ake anachimwa, anena mofanizira

1 Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,

2 Udzanena izi kufikira liti?

Ndipo mau a pakamwa pako

adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

3 Ngati Mulungu akhotetsa chiweruzo?

Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?

4 Chinkana ana ako anamchimwira Iye,

ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;

5 koma ukafunitsitsa Mulungu,

ndi kupembedza Wamphamvuyonse;

6 ukakhala woyera ndi woongoka mtima,

zoonadi adzakugalamukira tsopano,

ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.

7 Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching’ono,

chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.

8 Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo,

nusamalire zimene makolo ao adazisanthula.

9 Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu,

popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;

10 amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera,

ndi kutulutsa mau a mumtima mwao?

11 Ngati gumbwa aphuka popanda chinyontho?

Ngati manchedza amera popanda madzi?

12 Akali auwisi, sanawacheke,

auma, asanaume mathengo onse ena.

13 Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu;

ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.

14 Kulimbika mtima kwake kudzathyoka,

chikhulupiriro chake chikunga nyumba ya kangaude.

15 Adzatsamira nyumba yake, koma yosamlimbira;

adzaiumirira koma yosakhalitsa.

16 Akhala wamuwisi pali dzuwa,

ndi nthambi zake zitulukira pamunda pake.

17 Mizu yake iyangayanga pa kasupe wamadzi,

apenyerera pokhalapo miyala.

18 Akamuononga kumchotsa pamalo pake,

padzamkana, ndi kuti, Sindinakuone.

19 Taona, ichi ndicho chomkondweretsa panjira pake,

ndi panthaka padzamera ena.

20 Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro;

kapena kugwiriziza ochita zoipa.

21 Koma adzadzaza m’kamwa mwako ndi kuseka,

ndi milomo yako kufuula.

22 Iwo akudana nawe adzavala manyazi;

ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/8-cc0837d44517aafd54c6f9308f29da7c.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 9

Yobu avomereza ukulu wa Mulungu, koma okoma ndi oipa alangidwa mmodzimmodzi. Masautso ake amfunitsa kufa

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Zoona, ndidziwa kuti chili chotero.

Koma munthu adzakhala wolungama bwanji kwa Mulungu?

3 Akafuna Iye kutsutsana naye,

sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa chikwi.

4 Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu;

ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?

5 Ndiye amene asuntha mapiri, osachidziwa iwo,

amene amagubuduza mu mkwiyo wake.

6 Amene agwedeza dziko lapansi lichoke m’malo mwake,

ndi mizati yake injenjemere.

7 Amene alamulira dzuwa ndipo silituluka,

nakomera nyenyezi chizindikiro chakuzitsekera.

8 Woyala thambo yekha,

naponda pa mafunde a panyanja.

9 Wolenga Mlalang’amba, Akamwiniatsatana,

ndi Nsangwe, ndi Kumpotosimpita.

10 Wochita zazikulu zosasanthulika,

ndi zodabwitsa zosawerengeka.

11 Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya;

napitirira, koma osamzindikira ine.

12 Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani?

Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani?

13 Mulungu sadzabweza mkwiyo wake;

athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.

14 Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji,

ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye?

15 Ameneyo, chinkana ndikadakhala wolungama,

sindikadamyankha;

ndikadangompembedza wondiweruza ine.

16 Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye,

koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.

17 Pakuti andithyola ndi mkuntho,

nachulukitsa mabala anga kopanda chifukwa.

18 Sandilola kuti ndipume,

koma andidzaza ndi zowawa.

19 Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu?

Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani?

20 Chinkana ndikhala wolungama,

pakamwa panga padzanditsutsa;

chinkana ndikhala wangwiro,

padzanditsutsa wamphulupulu.

21 Chinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini,

ndipeputsa moyo wanga.

22 Kuli chimodzimodzi monsemo, m’mwemo ndikuti

Iye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi.

23 Mkwapulo ukapha modzidzimutsa,

adzaseka tsoka la wosachimwa.

24 Dziko lapansi laperekedwa m’dzanja la woipa;

aphimba maso a oweruza ake.

Ngati sindiye, pali yaninso?

25 Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma;

athawa osaona chokoma.

26 Apitirira ngati zombo zaliwiro;

ngati mphungu igudukira chakudya chake.

27 Ndikati, Ndidzaiwala chondidandaulitsa,

ndidzasintha nkhope yanga yachisoni, ndidzasekerera.

28 Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse,

ndidziwa kuti simudzandiyesa wosachimwa.

29 Mlandu udzanditsutsa;

potero ndigwire ntchito chabe chifukwa ninji?

30 Ndikasamba madzi a chipale chofewa

ndi kuyeretsa manja anga ndi sopo.

31 Mudzandiviikanso muli zoola,

ndi zovala zanga zidzanyansidwa nane.

32 Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe.

Kuti tikomane mlandu.

33 Palibe wakutiweruza,

wakutisanjika ife tonse awiri manja ake.

34 Andichotsere ndodo yake,

choopsa chake chisandichititse mantha;

35 kuti ndinene, osamuopa,

pakuti sinditero monga umo ndili.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/9-c084b770067fd667d80b53bd6ef70365.mp3?version_id=1068—