Categories
YESAYA

YESAYA 60

Ulemerero wa Yerusalemu ubwezedwa

1 Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.

2 Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.

3 Ndipoamitunduadzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.

4 Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.

5 Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.

6 Gulu langamiralidzakukuta, ngamira zazing’ono za Midiyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Sheba adzabwera nazo golide ndilubani; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.

7 Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.

8 Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda kumazenera ao?

9 Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako aamuna kutali, golide wao ndisilivawao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.

10 Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m’kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakuchitira iwe chifundo.

11 Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere nacho kwa iwe chuma cha amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi.

12 Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.

13 Ulemerero wa Lebanoni udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a Kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.

14 Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova,Ziyoniwa Woyera wa Israele.

15 Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.

16 Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziwa kuti Ine Yehova ndine Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu ya Yakobo.

17 M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golide, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.

18 Chiwawa sichidzamvekanso m’dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m’malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando.

19 Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.

20 Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha.

21 Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.

22 Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthawi yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/60-52c99d4d4321af87f890a744a5f8aa82.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 61

Alalikira Uthenga Wabwino wa chipulumutso

1 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende;

2 ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;

3 ndikakonzere iwo amene alira maliro muZiyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m’malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m’malo mwa maliro, chovala cha matamando m’malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

4 Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.

5 Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yampesa.

6 Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma chaamitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.

7 M’malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi chitonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; chifukwa chake iwo adzakhala nacho m’dziko mwao cholowa chowirikiza, adzakhala nacho chikondwerero chosatha.

8 Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m’zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.

9 Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.

10 Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.

11 Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/61-cf801f5b19365d1a7b7556189b7e39ae.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 62

Chikhalidwe chokoma cha Yerusalemu

1 Chifukwa chaZiyonisindidzakhala chete, ndi chifukwa chaYerusalemusindidzapuma, kufikira chilungamo chake chidzatuluka monga kuyera, ndi chipulumutso chake monga nyali yoyaka.

2 Ndipoamitunduadzaona chilungamo chako, ndi mafumu onse ulemerero wako; ndipo udzatchedwa dzina latsopano, limene m’kamwa mwa Yehova mudzatchula.

3 Iwe udzakhalanso korona wokongola m’dzanja la Yehova, korona wachifumu m’dzanja la Mulungu wako.

4 Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.

5 Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.

6 Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,

7 ndipo musamlole akhale chete, kufikira Iye atakhazikitsa naika Yerusalemu akhale tamando m’dziko lapansi.

8 Yehova analumbira padzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito;

9 koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m’mabwalo a Kachisi wanga.

10 Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; chotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu.

11 Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.

12 Ndipo iwo adzawatcha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzatchedwa Wofunidwa, Mzinda wosasiyidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/62-1c1a6cd2327a76af5267742ca6e130cd.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 63

Mulungu adzapulumutsa anthu ake, nadzabwezera chilango owasautsa

1 Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonyika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m’chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m’cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa.

2 Chophimba chako chifiiriranji, ndi zovala zako zifanana bwanji ndi woponda mopondera mphesa?

3 Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m’kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga; ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zovala zanga; ndipo ndadetsa chofunda changa chonse.

4 Pakuti tsiku lakubwezera lili mumtima mwanga, ndi chaka cha kuombola anthu anga chafika.

5 Ndipo ndinayang’ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine.

6 Ndipo ndinapondereza anthu m’kukwiya kwanga, ndi kuwatswanya mu ukali wanga, ndi kutsanulira mwazi wa moyo wao.

Kuyamika, kuwulula zoipa, ndi kupempha kwa anthu a Mulungu

7 Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.

8 Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.

9 M’mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m’kukonda kwake ndi m’chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.

10 Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.

11 Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ake, nati, Ali kuti Iye amene anawatulutsa m’nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lake? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wake woyera pakati pao,

12 amene anayendetsa mkono wake waulemerero padzanja lamanja la Mose? Amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?

13 Amene anawatsogolera kupitira mwa kuya monga kavalo m’chipululu osaphunthwa iwo?

14 Monga ng’ombe zotsikira kuchigwa mzimu wa Yehova unawapumitsa; chomwecho inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero.

15 Tayang’anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.

16 Pakuti Inu ndinu Atate wathu, ngakhale Abrahamu satidziwa ife, ndi Israele satizindikira ife. Inu Yehova ndinu Atate wathu, Mombolo wathu wachikhalire ndi dzina lanu.

17 Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.

18 Anthu anu opatulika anakhala nacho kanthawi kokha; adani athu apondereza Kachisi wanu wopatulika.

19 Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulire konse, ngati iwo amene sanatchedwe dzina lanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/63-23799ce093606424fd221d36e75df2df.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 64

1 Mwenzi mutang’amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu;

2 monga pamene moto uyatsa zitsamba, ndi moto uwiritsa madzi; kudziwitsa kwa amaliwongo anu dzina lanu, kutiamitunduanthunthumire pamaso panu.

3 Pamene Inu munachita zinthu zoopsa, zimene ife sitinayang’anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu.

4 Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.

5 Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nachita chilungamo, iwo amene akumbukira Inu m’njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinachimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa?

6 Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.

7 Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikakamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu.

8 Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.

9 Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang’anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu.

10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu,Ziyoniwasanduka chipululu,Yerusalemuwasanduka bwinja.

11 Nyumba yathu yopatulika ndi yokongola, m’mene makolo athu anakutamandani Inu, yatenthedwa ndi moto; ndi zinthu zathu zonse zokondweretsa zapasuka.

12 Kodi mudzadziletsa pa zinthuzi, Yehova? Kodi Inu mudzakhala chete ndi kutivutitsa ife zolimba?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/64-4fcfcf02b1855f41d807edad8c8cc4db.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 65

Achenjeza osamvera kuti adzalangidwa

1 Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchule dzina langa.

2 Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m’njira mosati mwabwino, kutsata maganizo aoao;

3 anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m’minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;

4 amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m’malo am’tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m’mbale zao;

5 amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m’mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.

6 Taonani, chalembedwa pamaso panga; sindidzakhala chete, koma ndidzabwezera, inde ndidzabwezera pa chifuwa chao,

7 zoipa zanuzanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandichitira mwano pazitunda; chifukwa chake Ine ndidzayesa ntchito yao yakale ilowe pa chifuwa chao.

8 Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m’tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m’menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.

9 Ndipo ndidzatulutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira cholowa chao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.

10 Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi chigwa cha Akori chidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.

11 Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwai gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosakaniza;

12 ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m’maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwere nacho.

13 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;

14 taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.

15 Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;

16 chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m’dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m’dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.

Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano

17 Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.

18 Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilengaYerusalemuwosangalala, ndi anthu ake okondwa.

19 Ndipo ndidzasangalala mu Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula.

20 Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa.

21 Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yampesa, ndi kudya zipatso zake.

22 Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.

23 Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbeu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa ao adzakhala pamodzi ndi iwo.

24 Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.

25 Mmbulu ndimwanawankhosazidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng’ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m’phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/65-317aa8a113c4878d9e93f71a6e1f42fd.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 66

Ochita zoipa adzabwezedwa chilango

1 Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?

2 Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang’anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.

3 Wakupha ng’ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe yamwanawankhosaalingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukizalubaniakunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m’zonyansa zao;

4 Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamve konse; koma anachita choipa m’maso mwanga, ndi kusankha chimene sindinakondwere nacho.

5 Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.

6 Mau a phokoso achokera m’mzinda, mau ochokera mu Kachisi, mau a Yehova amene abwezera adani ake chilango.

7 Mkazi asanamve zowawa, anabala mwana; kupweteka kwake kusanadze, anabala mwana wamwamuna.

8 Ndani anamva kanthu kotereko? Ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? Pakuti pameneZiyonianamva zowawa, pomwepo anabala ana ake.

9 Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? Ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? Ati Mulungu wako.

Yehova adzaweruza omchimwira

10 Sangalalani inu pamodzi ndiYerusalemu, ndipo kondwani chifukwa cha iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro;

11 kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mawere a zitonthozo zake; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wake.

12 Pakuti atero Yehova, Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero waamitundungati mtsinje wosefukira. Inu mudzayamwa, ndi kunyamulidwa pambali, ndi kululuzidwa pa maondo.

13 Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima mu Yerusalemu.

14 Ndipo mudzachiona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ake, ndipo adzakwiyira adani ake.

15 Pakuti taonani, Yehova adzafika m’moto, ndi magaleta ake adzafanana ndi kamvulumvulu; kubwezera mkwiyo wake ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto.

16 Pakuti Yehova adzatsutsana ndi moto, ndi lupanga lake, ndi anthu onse; ndi ophedwa a Yehova adzakhala ambiri.

17 Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatanetsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi chonyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova.

18 Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.

19 Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.

20 Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m’magaleta, ndi m’machila, ndi pa nyuru, ndi pangamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m’chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.

21 Ndipo ena a iwo ndidzawatenga akhale ansembe ndi Alevi, ati Yehova.

22 Pakuti monga m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.

23 Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira paSabatalina kufikira kulinzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.

24 Ndipo iwo adzatuluka ndi kuyang’ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mphutsi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/66-d9b14b86c4b9737f3676d6a6e1c5aae8.mp3?version_id=1068—