Categories
YESAYA

YESAYA 40

Lonjezo la chipulumutso cha Israele

1 Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu.

2 Munene inu zotonthoza mtima kwaYerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m’dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.

3 Mau a wofuula m’chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m’dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.

4 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zidzachepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;

5 ndipo ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena chomwecho.

6 Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m’thengo;

7 udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.

8 Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.

9 Iwe amene utengera mau abwino kuZiyoni, kwera iwe pamwamba paphiri lalitali; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena kumizinda ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!

10 Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; taonani, mphotho yake ili ndi Iye, ndipo chobwezera chake chili patsogolo pa Iye.

11 Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m’manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mulungu ndi wamphamvuyonse, mafano ndi achabe

12 Ndani wayesa madzi m’dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m’nsengwa, ndi kuyesa mapiri m’mbale zoyesera, ndi zitunda m’mulingo?

13 Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lake, ndi kumphunzitsa Iye?

14 Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m’njira ya chiweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?

15 Taonani,amitunduakunga dontho la m’mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m’muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang’ono.

16 Ndipo Lebanoni sakwanira kutentha, ngakhale nyama zake sizikwanira nsembe yopsereza.

17 Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake.

18 Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani?

19 Fano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golide analikuta ndi golide, naliyengera maunyolo asiliva.

20 Wosowa nsembe yoteroyo asankha mtengo umene sungavunde, iye adzisankhira yekha munthu mmisiri waluso, akonze fano losema, limene silisunthika.

21 Kodi inu simunadziwe? Kodi inu simunamve? Kodi sanakuuzeni inu chiyambire? Kodi inu simunadziwitse chiyambire mayambiro a dziko lapansi?

22 Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;

23 amene asandutsa akalonga kuti akhale achabe, nasandutsa oweruza a dziko lapansi akhale opanda pake.

24 Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.

25 Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo.

26 Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.

27 Bwanji iwe, Yakobo, umati, ndi bwanji umanena iwe, Israele, Njira yanga yabisika kwa Yehova; ndipo chiweruzo cha Mulungu wanga chandipitirira?

28 Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.

29 Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

30 Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu:

31 koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/40-06c7b9729727923956d9c325b3ee5a65.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 41

Yehova yekha ndiye Mulungu, Israele amkhulupirire Iye yekhayekha

1 Khalani chete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni tiyandikire pamodzi kuchiweruziro.

2 Ndani anautsa wina wochokera kum’mawa, amene amuitana m’chilungamo, afike pa phazi lake? Iye aperekaamitundupatsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.

3 Iye awathamangitsa, napitirira mwamtendere; panjira imene asanapitemo ndi mapazi ake.

4 Ndani wachipanga, nachimaliza icho, kutchula mibadwo chiyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pachimaliziro ndine ndemwe.

5 Zisumbu zinaona ndipo zinaopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.

6 Iwo anathangata yense mnansi wake, ndi yense anati kwa mbale wake, Khala wolimba mtima.

7 Chotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golide, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi ntovu, Kuli kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.

8 Koma iwe, Israele, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;

9 iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kuchokera m’ngodya zake, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaye kunja;

10 usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

11 Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati chabe, nadzaonongeka.

12 Iwe udzawafuna osawapeza, ngakhale iwo amene akangana ndi iwe; ochita nkhondo ndi iwe, adzakhala ngati chabe, ndi monga kanthu kopanda pake.

13 Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.

14 Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.

15 Taona, ndidzakuyesa iwe choombera tirigu chatsopano chakuthwa chokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.

16 Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.

17 Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.

18 Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti see, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa chipululu, chikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.

19 Ndidzabzala m’chipululu mkungudza, ndi msangu, ndi kasiya, ndi mtengo waazitona; ndidzaika m’chipululu pamodzi mlombwa, ndi mkuyu, ndi naphini;

20 kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lachita ichi, ndipo Woyera wa Israele wachilenga ichi.

21 Onetsani mlandu wanu, ati Yehova; tulutsani zifukwa zanu zolimba, ati mfumu ya Yakobo.

22 Azitulutse, atitchulire ife, chimene chidzaoneka; tchulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziwa mamaliziro ao; kapena tionetseni ife zinthu zimene zilinkudza.

23 Tchulani zinthu zimene zilinkudza m’tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, chitani zabwino, kapena chitani zoipa, kuti ife tiopsedwe, ndi kuona pamodzi.

24 Taonani, inu muli achabe, ndi ntchito yanu yachabe; wonyansa ali iye amene asankha inu.

25 Ndautsa wina wakuchokera kumpoto; ndipo iye wafika wakuchokera potuluka dzuwa, amene atchula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.

26 Ndani watchula icho chiyambire, kuti ife tichidziwe? Ndi nthawi zakale, kuti ife tinene, Iye ali wolungama? Inde, palibe wina amene atchula, inde, palibe wina amene asonyeza, inde palibe wina amene amvetsa mau anu.

27 Poyamba Ine ndidzati kwaZiyoni, Taona, taona iwo; ndipo ndidzapereka kwaYerusalemuwina, amene adza ndi mau abwino.

28 Ndipo pamene ndayang’ana, palibe munthu; ngakhale mwa iwo, palibe phungu, amene angathe kuyankha mau, pamene ndiwafunsa.

29 Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/41-70ae944896603c7438991f50b02c861b.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 42

Mtumiki wa Yehova

1 Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsiraamitunduchiweruziro.

2 Iye sadzafuula, ngakhale kukuwa, pena kumvetsa mau ake m’khwalala.

3 Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m’zoona.

4 Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m’dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.

5 Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m’menemo, Iye amene amapatsa anthu a m’menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m’menemo;

6 Ine Yehova ndakuitana Iwe m’chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;

7 kuti utsegule maso akhungu, utulutse am’nsinga m’ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m’nyumba ya kaidi.

8 Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.

9 Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani.

10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m’menemo, zisumbu ndi okhala mommo.

11 Chipululu ndi mizinda yake ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala mu Sela aimbe, akuwe kuchokera pamwamba pa mapiri.

12 Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m’zisumbu.

13 Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.

14 Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.

15 Ndidzapasula mapiri ndi zitunda, ndi kuumitsa zitsamba zao zonse; ndi kusandutsa nyanja zisumbu, ndi kuumitsa matamanda.

16 Ndipo ndidzayendetsa akhungu m’khwalala, limene iwo salidziwa, m’njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m’tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.

17 Iwo adzabwezedwa m’mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.

18 Imvani, agonthi inu; yang’anani, akhungu inu, kuti muone.

19 Ndani ali wakhungu, koma mtumiki wanga? Pena wagonthi, monga mthenga wanga, amene ndimtumiza? Ndani ali wakhungu monga bwenzi langa, ndi wakhungu monga mtumiki wa Yehova?

20 Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.

21 Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.

22 Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m’mauna, nabisidwa m’nyumba za akaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.

23 Ndani mwa inu adzatchera khutu lake pamenepo? Amene adzamvera ndi kumva nthawi yakudza?

24 Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israele, kuti awawanyidwe? Kodi si Yehova? Iye amene tamchimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m’njira zake, ngakhale kumvera chiphunzitso chake.

25 Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m’mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/42-f6c035579459ccd80783324ebc7345d8.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 43

Mulungu Yehova yekha apulumutsa Israele

1 Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.

2 Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

3 Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m’malo mwako.

4 Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m’malo mwa moyo wako.

5 Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum’mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo.

6 Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga akazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi;

7 yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.

8 Tulutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu.

9 Amitunduonse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ichi ndi kuonetsa ife zinthu zakale? Atenge mboni zao, kuti avomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.

10 Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.

11 Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.

12 Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.

13 Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m’dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa?

14 Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m’ngalawa za kukondwa kwao.

15 Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu.

16 Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m’madzi amphamvu;

17 amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.

18 Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale.

19 Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m’chipululu, ndi mitsinje m’zidalala.

20 Nyama za m’thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m’chipululu, ndi mitsinje m’mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;

21 anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.

22 Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israele.

23 Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing’ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritse ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndilubani.

24 Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndalama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi machimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.

25 Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.

26 Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe.

27 Atate wako woyamba anachimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine.

28 Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/43-e5e1e8d22744fa337b4ec8e4436bd24a.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 44

Mulungu ndi wamkulukulu, mafano ndi achabe

1 Koma tsopano, imva Yakobo, mtumiki wanga, ndi Israele, amene ndakusankha;

2 atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kuchokera m’mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe.

3 Pakuti ndidzathira madzi padziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;

4 ndipo iwo adzaphuka pakati pa udzu, ngati msondodzi m’mphepete mwa madzi.

5 Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele.

6 Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

7 Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ichi ndi kundilongosolera ichi, chikhazikitsire Ine anthu akale? Milunguyo iwadziwitse zomwe zilinkudza, ndi za m’tsogolo.

8 Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.

9 Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi.

10 Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?

11 Taonani anzake onse adzakhala ndi manyazi, ndi amisiri ake ndi anthu; asonkhane onse pamodzi, aimirire; adzaopa, iwo onse adzakhala ndi manyazi.

12 Wachipala achita zake ndi nsompho, nagwira ntchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira ntchito yake ndi mkono wake wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zake zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.

13 Mmisiri wa mitengo atambalitsa chingwe; nalilemba ndi cholembera, nalikonza ndi ncherero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m’nyumba.

14 Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa.

15 Ndipo udzakhala kuti munthu autenthe; iye natengako, nauotha moto; inde auyatsa, naotcha mkate; inde, apanga mulungu, naulambira, naupanga fano losema, naligwadira.

16 Iye atenthako mbali ina pamoto; ndi mbali yinayo adya nyama; akazinga zokazinga nakhuta, inde, aotha moto, nati, Ha, ndakongonoka, ndauona moto.

17 Ndipo chotsalacho apanga mulungu, ngakhale fano lake losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, chifukwa kuti ndinu mulungu wanga.

18 Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m’mitima mwako kuti sangadziwitse.

19 Palibe wina wokumbukira, kapena kudziwa, kapena kuzindikira, ndi kuti, Ndatentha mbali ina pamoto, inde ndaotchanso mkate pamakala pake, ndakazinga nyama ndi kuidya; kodi ndichipange chotsala chake, chikhale chonyansa? Ndidzagwadira kodi tsinde la mtengo?

20 Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m’dzanja langa lamanja?

Mulungu Mpulumutsi wa Israele

21 Kumbukira zinthu izi, Yakobo; ndi Israele, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, sindidzakuiwala.

22 Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.

23 Imbani m’mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi padziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m’menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.

24 Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m’mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lapansi; ndani ali ndi Ine?

25 Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m’mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:

26 Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena zaYerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.

27 Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako;

28 ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/44-3319f81c3ebff5bfb4e2247101f0514d.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 45

Yehova amuyesa Kirusi chipangizo chake

1 Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m’chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa:

2 Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo;

3 ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m’malo am’tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.

4 Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israele wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwe Ine.

5 Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m’chuuno, ngakhale sunandidziwe;

6 kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.

7 Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.

8 Igwani pansi, inu m’mwamba, kuchokera kumwamba, thambo litsanulire pansi chilungamo; dziko lapansi litseguke, kuti libalitse chipulumutso, nilimeretse chilungamo chimere pamodzi; Ine Yehova ndinachilenga chimenecho.

9 Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wake! Phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga chiyani? Pena ntchito yako, Iye alibe manja?

10 Tsoka kwa iye amene ati kwa atate wake, Kodi iwe ubalanji? Pena kwa mkazi, Ulikusauka ninji iwe?

11 Atero Yehova Woyera wa Israele ndi Mlengi wake, Ndifunse Ine za zinthu zimene zilinkudza; za ana anga aamuna, ndi za ntchito ya manja anga, ndilamulireni Ine.

12 Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m’menemo, ndinazilamulira ndine.

13 Ine ndautsa Kirusi m’chilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zake zonse; iye adzamanga mzinda wanga, nadzaleka andende anga anke mwaufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.

14 Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m’maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.

15 Ndithu Inu ndinu Mulungu, amene mudzibisa nokha, Mulungu wa Israele, Mpulumutsi.

16 Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m’masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.

17 Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.

18 Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.

19 Ine sindinanene m’tseri m’malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwachabe; Ine Yehova ndinena chilungamo, ndinena zimene zili zoona.

20 Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumukaamitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.

21 Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.

22 Yang’anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.

23 Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m’kamwa mwanga m’chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.

24 Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.

25 Mwa Yehova mbeu yonse ya Israele idzalungamitsidwa ndi kudzikuza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/45-7df87c22df3de720e9f77f354cfe3adf.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 46

Aneneratu za kupasuka kwa mafano a ku Babiloni

1 Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng’ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama.

2 Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m’ndende.

3 Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israele, amene ndakunyamulani kuyambira m’mimba, ndi kukusenzani chibadwire;

4 ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.

5 Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?

6 Amene ataya golide, namtulutsa m’thumba, ndi kuyesasilivandi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.

7 Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m’malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m’zovuta zake.

8 Kumbukirani ichi, nimuchilimike, mudzikumbutsenso, olakwa inu.

9 Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina wofanana ndi Ine;

10 ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;

11 ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum’mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera kudziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.

12 Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutali ndi chilungamo;

13 ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m’Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/46-28fb4dd565eb6de3d8fcb10f8bd0b881.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 47

Babiloni adzaonongeka konse

1 Tsika, ukhale m’fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.

2 Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m’mwendo, oloka mitsinje.

3 Maliseche ako adzakhala osafundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzachita kubwezera, osasamalira munthu.

4 Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lake, Woyera wa Israele.

5 Khala iwe chete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Ababiloni; pakuti sudzatchedwanso mkazi wa maufumu.

6 Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m’manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.

7 Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalire izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.

8 Chifukwa chake tsono, imva ichi, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;

9 koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri.

10 Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi chidziwitso chako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.

11 Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi.

12 Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m’menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.

13 Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam’mwamba, oyang’ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.

14 Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.

15 Zinthu zomwe unagwira ntchito yake, zidzatero nawe; iwo amene anachita malonda ndi iwe chiyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwake; sipadzakhala wopulumutsa iwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/47-82ba4ef1b918cb4954434fd2c0c95ead.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 48

Awadandaulira Aisraele, awachenjeza, nalonjezana nao

1 Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m’madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m’zoona, pena m’chilungamo.

2 Pakuti adziyesa okha a mzinda wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu.

3 Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinatuluka m’kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazichita izo, ndipo zinaoneka.

4 Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;

5 chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira.

6 Iwe wachimva; taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzachinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kuchokera nthawi ino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.

7 Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa.

8 Inde, iwe sunamve; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.

9 Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse.

10 Taona ndakuyenga, koma si mongasiliva, ndakuyesa iwe m’ng’anjo ya masautso.

11 Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.

12 Mverani Ine, Yakobo ndi Israele, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womaliza.

13 Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m’mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.

14 Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni.

15 Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yake.

16 Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m’tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.

17 Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.

18 Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;

19 mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m’chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.

20 Tulukani inu mu Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo.

21 Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m’mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m’matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.

22 Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/48-91a7d481441172fbae83c7ff6fc9751e.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 49

Mtumiki wa Yehova, kuunika kwa amitundu

1 Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m’mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;

2 nachititsa pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa, mu mthunzi wa dzanja lake wandibisa Ine; wandipanga Ine; muvi wotuulidwa; m’phodo mwake Iye wandisungitsa Ine, nati kwa Ine,

3 Iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, amene ndidzalemekezedwa nawe.

4 Koma ndinati, Ndagwira ntchito mwachabe, ndatha mphamvu zanga pachabe, ndi mopanda pake; koma ndithu chiweruziro changa chili ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.

5 Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wake, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israele asonkhanidwe kwa Iye; chifukwa Ine ndili wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;

6 inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwaamitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.

7 Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.

8 Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m’zolowa zopasuka m’malo abwinja;

9 ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m’njira, ndi m’zitunda zonse zoti see mudzakhala busa lao.

10 Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.

11 Ndipo ndidzasandutsa mapiri anga onse akhale njira, ndipo makwalala anga adzakwezeka.

12 Taonani, awa adzachokera kutali; ndipo taonani, awa ochokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ochokera kudziko la Asuwani.

13 Imbani inu, m’mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.

14 KomaZiyonianati, Yehova wandisiya ine, ndipo Ambuye wandiiwala ine.

15 Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.

16 Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga.

17 Ana ako afulumira; opasula ako ndi iwo amene anakusakaza adzachoka pa iwe.

18 Tukula maso ako kuunguzaunguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadziveka wekha ndi iwo onse, monga ndi chokometsera, ndi kudzimangira nao m’chuuno ngati mkwatibwi.

19 Pakuti, kunena za malo ako osiyidwa ndi abwinja ndi dziko lako limene lapasulidwa tsopano, ndithu iwe udzakhala wochepera okhalamo, ndi iwo amene anakumeza iwe adzakhala kutali.

20 Ana ako amasiye adzanena m’makutu ako, Malo andichepera ine, ndipatse malo, kuti ndikhalemo.

21 Pamenepo udzati m’mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anachotsedwa kwa ine, ndipo ndili wouma, ndi wochotsedwa m’dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? Ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?

22 Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako aamuna pa chifuwa chao, ndi ana ako aakazi adzatengedwa pa mapewa ao.

23 Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang’ana pansi, nadzaseteka fumbi la m’mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.

24 Kodi chofunkha chingalandidwe kwa wamphamvu, pena am’nsinga a woopsa angapulumutsidwe?

25 Koma atero Yehova, Ngakhale am’nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi chofunkha cha woopsa chidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.

26 Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yaoyao; ndi mwazi waowao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndili Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/49-7604832c96af49fb1837a58e8eecca6e.mp3?version_id=1068—