Categories
YESAYA

YESAYA 30

Tsoka okhulupirira Ejipito

1 Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;

2 amene ayenda kutsikira ku Ejipito, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi mphamvu zaFarao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito!

3 Chifukwa chake mphamvu za Farao zidzakhala kwa inu manyazi, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito kudzakhala chisokonezo chanu.

4 Pakuti akalonga ake ali pa Zowani, ndi mithenga yake yafika ku Hanesi.

5 Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi chitonzo.

6 Katundu wa zilombo za kumwera.

M’dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang’ono zolemera zao pa malinundu angamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.

7 Pakuti thangata la Ejipito lili lachabe, lopanda pake; chifukwa chake ndamutcha Wonyada, wokhala chabe.

8 Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m’buku, kuti akakhalebe kunthawi yam’tsogolo, mboni ya masiku onse.

9 Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva chilamulo cha Yehova;

10 amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;

11 chokani inu munjira, patukani m’bande, tiletsereni Woyera wa Israele pamaso pathu.

12 Chifukwa chake atero Woyera wa Israele, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m’menemo;

13 chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m’khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi.

14 Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m’zigamphu zake phale lopalira moto pachoso, ngakhale lotungira madzi padziwe.

15 Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M’kubwera ndi m’kupuma inu mudzapulumutsidwa; m’kukhala chete ndi m’kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.

16 Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; chifukwa chake inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; chifukwa chake iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.

17 Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba paphiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda.

18 Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

19 Pakuti anthu adzakhala muZiyonipaYerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kufuula kwako; pakumva Iye adzayankha.

20 Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu chakudya cha nsautso, ndi madzi a chipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;

21 ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.

22 Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.

23 Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m’nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng’ombe zako zidzadya m’madambo aakulu.

24 Momwemonso ng’ombe ndi ana a bulu olima nthaka adzadya chakudya chochezera, chimene chapetedwa ndi chokokolera ndi mkupizo.

25 Ndipo pamwamba pa mapiri aakulu onse, ndi pa zitunda zonse zazitalitali padzakhala mitsinje ndi micherenje ya madzi, tsiku lophana lalikulu, pamene nsanja zidzagwa.

26 Komanso kuwala kwake kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ake, nadzapoletsa chilonda chimene anawakantha ena.

27 Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi aakulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita;

28 ndi mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m’khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi chopetera cha chionongeko; ndi chapakamwa chalakwitsa, chidzakhala m’nsagwada za anthu.

29 Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.

30 Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.

31 Pakuti ndi mau a Yehova Aasiriya adzathyokathyoka, ndi ndodo yake adzammenya.

32 Ndipo nthawi zonse Yehova adzawakantha ndi ndodo yosankhikayo, padzamveka mangaka ndi zeze; ndi m’nkhondo zothunyanathunyana, Iye adzamenyana nao.

33 Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wasulufure.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/30-a683f7b1eb402ffc57fc56c00f1a4cbc.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 31

Tsoka otama chithandizo cha Ejipito

1 Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang’ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!

2 Koma Iyenso ndi wanzeru, nadzatengera choipa, ndipo sadzabwezanso mau ake, koma adzaukira banja la ochita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira ntchito yoipa.

3 Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.

4 Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri laZiyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.

5 Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wa makamu adzatchinjirizaYerusalemu; Iye adzatchinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.

6 Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israele inu.

7 Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ake asiliva, ndi mafano ake agolide amene manja anuanu anawapanga akuchimwitseni inu.

8 Pamenepo Asiriya adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammaliza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ake adzalamba.

9 Ndipo mwala wake udzachoka, chifukwa cha mantha, ndi akalonga ake adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni, ndi ng’anjo yake mu Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/31-eced3ee99deab8257740a8f7998265e1.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 32

Ufumu wa mfumu yolungama

1 Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.

2 Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.

3 Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera.

4 Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilime la achibwibwi lidzalankhula zomveka msanga.

5 Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.

6 Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.

7 Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.

8 Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m’zaufulu zomwe.

Chilangizo cha kwa akazi

9 Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phee, mumve mau anga; inu ana aakazi osasamalira, tcherani makutu pa kulankhula kwanga.

10 Pakutha chaka, kudza masiku ena inu mudzavutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.

11 Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhala phee; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m’chuuno mwanu.

12 Iwo adzadzimenya pazifuwa chifukwa cha minda yabwino, chifukwa cha mpesa wobalitsa.

13 Padziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m’mzinda wokondwerera;

14 pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mzinda wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;

15 kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.

16 Pamenepo chiweruzo chidzakhala m’chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m’munda wobalitsa.

17 Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.

18 Ndipo anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.

19 Koma kudzagwa matalala m’kugwa kwake kwa nkhalango; ndipo mzinda udzagwetsedwa ndithu.

20 Odala muli inu, amene mubzala m’mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng’ombe ndi bulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/32-5dd9d762e3acebb5c428e1fdc188fe8c.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 33

Adani a anthu a Mulungu adzapasuka; Yerusalemu adzabwezedwa ulemu

1 Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwe; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.

2 Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m’mawa ndi m’mawa, chipulumutso chathunso m’nthawi ya mavuto.

3 Pa mau a phokoso mitundu ya anthu yathawa; ponyamuka iweamitunduabalalika.

4 Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.

5 Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzazaZiyonindi chiweruzo ndi chilungamo.

6 Ndipo kudzakhala chilimbiko m’nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.

7 Taonani, olimba mtima ao angofuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa.

8 Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asiriya wathyolachipangano, wanyoza mizinda, sasamalira anthu.

9 Dziko lirira maliro ndi kulefuka; Lebanoni ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi chipululu; pa Basani ndi Karimele papukutika.

10 Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.

11 Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumalizani inu.

12 Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.

13 Imvani inu amene muli kutali, chimene ndachita ndi inu; amene muli pafupi, vomerezani mphamvu zanga.

14 Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?

15 Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang’ana choipa;

16 iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.

17 Maso ako adzaona mfumu m’kukongola kwake; iwo adzaona dziko lakutali.

18 Mtima wako udzaganizira zoopsa; mlembi ali kuti? Ali kuti iye amene anayesa msonkho? Ali kuti iye amene anawerenga nsanja?

19 Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilime lachibwibwi, limene iwe sungalimve.

20 Tayang’ana pa Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.

21 Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m’menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo.

22 Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.

23 Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula.

24 Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m’menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/33-3b2e1f19cb8ad1b3adf3c72684cfa257.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 34

Yehova aipidwa ndi amitundu

1 Idzani pafupi,amitunduinu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo.

2 Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa.

3 Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.

4 Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.

5 Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.

6 Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira, ndi ophedwa ambiri m’dziko la Edomu.

7 Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng’ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko laolao lidzanona ndi mafuta.

8 Pakuti lili tsiku la kubwezera la Yehova, chaka chakubwezera chilango, mlandu waZiyoni.

9 Ndipo mitsinjeyo idzasanduka matope akuda, ndi fumbilo lidzasandukasulufure, ndi dziko lakelo lidzasanduka matope oyaka moto.

10 Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wake udzakwera nthawi zonse; m’mibadwomibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthawi za nthawi.

11 Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khwangwala adzakhala m’menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu.

12 Iwo adzaitana mfulu zake zilowe mu ufumu, koma sizidzaonekako; ndi akalonga ake onse adzakhala chabe.

13 Ndipo minga idzamera m’nyumba zake zazikulu, khwisa ndi mitungwi m’malinga mwake; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa.

14 Ndipo zilombo za m’chipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzake; inde manchichi adzatera kumeneko, nadzapeza popumira.

15 Kumeneko kadzidzi adzapanga chisa chake, naikira, naumatira, naswa mumthunzi mwake; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzake.

16 Funani inu m’buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzake; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wake wasonkhanitsa iwo.

17 Ndipo Iye wachita maere, chifukwa cha zilombozi, ndipo dzanja lake lazigawira dzikolo ndi chingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwomibadwo, zidzakhala m’menemo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/34-55cbd2d4a1b6d597e31c867817d41ce5.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 35

Chikondwerero cha Ziyoni m’tsogolomo

1 Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti see lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.

2 Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni, ndi ukulu wa Karimele ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.

3 Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.

4 Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.

5 Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.

6 Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti see.

7 Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m’malo a ankhandwe m’mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.

8 Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m’menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m’njira, ngakhale opusa, sadzasochera m’menemo.

9 Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chilombo cholusa sichidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuomboledwa adzayenda m’menemo;

10 ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika kuZiyonialikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/35-6c7b4e6a935ed6f4bd440bc4d2cc5726.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 36

Nkhondo ya Senakeribu idzera Yerusalemu

1 Koma panali chaka chakhumi ndi chinai cha mfumu Hezekiya, Senakeribu, mfumu ya Asiriya anadza, nathira nkhondo pa mizinda ya malinga yonse ya Yuda, nailanda.

2 Ndipo mfumu ya Asiriya inatumiza kazembe kuchokera pa Lakisi, kunka kuYerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima chifupi ndi mcherenje wa thamanda la kumtunda, m’khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu.

3 Ndipo anamtulukira Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi.

4 Ndipo kazembeyo anati kwa iwo, Nenani inu tsopano kwa Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Kodi chikhulupiriro ichi nchotani, uchikhulupirira iwe?

5 Ine nditi, Uphungu wako, ndi mphamvu zako za kunkhondo, zingokhala mau achabe; tsopano ukhulupirira yani, kuti wandipandukira ine?

6 Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Ejipito; imene munthu akaitsamira, idzalowa m’dzanja mwake, ndi kulipyoza; momwemoFarao, mfumu ya Aejipito, kwa onse amene amkhulupirira iye.

7 Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wachotsa misanje yake ndi maguwa ake a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa guwa la nsembe ili?

8 Chifukwa chake upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asiriya, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.

9 Bwanji tsono iwe ungathe kubweza nkhope ya nduna mmodzi wamng’ono wa atumiki a mbuyanga, ndi kukhulupirira Ejipito, kuti adzakupatsa magaleta ndi apakavalo?

10 Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula.

11 Ndipo Eliyakimu, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m’chinenero cha Aramu; pakuti ife tichimva; ndipo musanene kwa ife mu Chiyuda, m’makutu a anthu amene ali palinga.

12 Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? Kodi iye sananditumize ine kwa amuna okhala palinga, kuti adye ndowe zaozao, ndi kumwa madzi aoao ndi inu?

13 Pamenepo kazembeyo anaima, nafuula ndi mau aakulu mu Chiyuda, nati, Imvani, inu, mau a mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya.

14 Mfumu itere, Musaleke Hezekiya anyenge inu; pakuti iye sadzathai kukupulumutsani:

15 ngakhale musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu; mzinda uwu sudzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asiriya.

16 Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake;

17 Kufikira ine ndidzadza, ndi kunka nanu kudziko lofanana ndi lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la chakudya ndi minda yampesa.

18 Chenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iliyonse yaamitunduinapulumutsa dziko lao m’manja mwa mfumu ya ku Asiriya?

19 Ili kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya m’manja mwanga?

20 Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m’manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m’manja mwanga?

21 Koma iwo anakhala chete, osamuyankha mau, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe.

22 Ndipo anafika Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zovala zao zong’ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/36-88067bd2e293dbcdc165b2ad4a3db89b.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 37

Mwa mantha Hezekiya aitana mneneri Yesaya

1 Ndipo panali pamene mfumu Hezekiya anamva, anang’amba zovala zake, navala chiguduli, nalowa m’nyumba ya Yehova.

2 Ndipo anatumiza Eliyakimu, wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi akulu a nsembe, atafunda chiguduli, kwa Yesaya,mneneri, mwana wa Amozi.

3 Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la vuto, ndi lakudzudzula ndi chitonzo; pakuti nthawi yake yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira.

4 Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asiriya mbuyake inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; chifukwa chake, kweza pemphero lako chifukwa cha otsala osiyidwa.

5 Ndipo atumiki a mfumu Hezekiya anadza kwa Yesaya.

6 Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asiriya andilalatira Ine.

7 Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka kudziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m’dziko la kwao.

Uthenga wa Sanakeribu wa kwa Hezekiya

8 Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asiriya ilikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inachoka ku Lakisi.

9 Ndipo anamva anthu alinkunena za Tirihaka, mfumu ya Kusi, Iye watuluka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti,

10 Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti,Yerusalemusadzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asiriya.

11 Taona, iwe wamva chimene mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa?

12 Kodi milungu yaamitunduyaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefe ndi ana a Edeni amene anali mu Telasara.

13 Ili kuti mfumu ya ku Hamati, ndi mfumu ya ku Aripadi, ndi mfumu yamzinda wa ku Sefaravaimu, ya ku Hena, ndi Iva?

Pemphero la Hezekiya

14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m’manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova, nati,

16 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, amene mukhala paakerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

17 Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Senakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.

18 Zoonadi, Yehova, mafumu a Asiriya anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.

19 Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga.

20 Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m’manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.

Kuyankha kwa Yehova mwa Yesaya

21 Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Popeza wandipemphera za Senakeribu mfumu ya Asiriya,

22 awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi waZiyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.

23 Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele.

24 Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magaleta anga ine ndafika kunsonga za mapiri, kumbali za Lebanoni; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pake penipeni, kunkhalango ya munda wake wobalitsa.

25 Ine ndakumba ndi kumwa madzi, ndidzaumitsa mitsinje yonse ya Ejipito ndi kuphazi kwanga.

26 Kodi iwe sunamve, kuti ndinachita ichi kale, ndi kuchikonza nthawi zakale? Tsopano Ine ndachikwaniritsa, kuti iwe ukapasule mizinda yamalinga, isanduke miunda.

27 Chifukwa chake okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa m’munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamatsindwi, ndi munda wa tirigu asanakule.

28 Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.

29 Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m’makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m’mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m’milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m’njira yomwe unadzerayo.

30 Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe: chaka chino mudzadya zimene zili zomera zokha, ndipo chaka chachiwiri mankhokwe ake; ndipo chaka chachitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yampesa ndi kudya chipatso chake.

31 Ndipo otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala chipatso pamwamba.

32 Pakuti mudzaoneka mu Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m’phiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi.

33 Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzafika mu mzinda muno, ngakhale kuponyapo muvi, ngakhale kufika patsogolo pake ndi chikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.

34 Pa njira yomwe anadzerayo, abwerera yomweyo, ndipo sadzafika mu mzinda uno, ati Yehova.

35 Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno, kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide.

36 Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m’zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.

37 Ndipo Senakeribu, mfumu ya Asiriya, anachoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Ninive.

38 Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m’nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere, ana ake anamupha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake, analamulira m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/37-760756ba4c9a11a4fd1e122154e4f05b.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 38

Kudwala kwa Hezekiya ndi kuchiritsidwa kwake

1 Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesayamneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.

2 Ndipo Hezekiya analoza nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati,

3 Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m’zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.

4 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti,

5 Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.

6 Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mzinda uno m’manja mwa mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzatchinjiriza mzinda uno.

7 Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe chochokera kwa Yehova, kuti Yehova adzachita ichi wanenachi;

8 taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.

9 Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atachira nthenda yake.

10 Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m’zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.

11 Ndinati, Sindidzaona Yehova m’dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;

12 Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

13 Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

14 Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.

15 Kodi ndidzanena chiyani? Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wachita ichi; Ine ndidzayenda chete zaka zanga zonse, chifukwa cha zowawa za moyo wanga.

16 Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo. Ndipo m’menemo monse muli moyo wa mzimu wanga; Chifukwa chake mundichiritse ine, ndi kundikhalitsa ndi moyo.

17 Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m’dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m’mbuyo mwanu machimo anga onse.

18 Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.

19 Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.

20 Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m’nyumba ya Yehova.

21 Ndipo Yesaya adati, Atenge m’bulu wankhuyu, auike pafundo, ndipo iye adzachira.

22 Hezekiya anatinso, Chizindikiro nchiyani, kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/38-77634b85d007fba63ddbfdf6d0dffc03.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 39

Hezekiya aonetsa amithenga a ku Babiloni chuma chake, Yesaya namdzudzula

1 Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya; pakuti anamva kuti iye anadwala, nachira.

2 Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yake ya chuma,siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsera, ndi nyumba yonse ya zida zake, ndi zonse zopezedwa m’zosungira zake; munalibe kanthu m’nyumba mwake, kapena m’dziko lake lonse, kamene Hezekiya sanawaonetse.

3 Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo achokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo achokera ku dziko lakutali, kudza kwa ine, kunena ku Babiloni.

4 Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona chiyani m’nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m’nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa chuma changa, kamene ine sindinawaonetse.

5 Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu.

6 Taona, masiku afika, kuti zonse za m’nyumba mwako, ndi zimene atate wako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babiloni; sipadzatsala kanthu, ati Yehova.

7 Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m’chinyumba chake cha mfumu ya ku Babiloni.

8 Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/39-31cb0f98258c72659d1e7d0362cd7bfe.mp3?version_id=1068—