Categories
YESAYA

YESAYA 10

1 Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu;

2 kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!

3 Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang’anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?

4 Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.

Aneneratu za kuonongeka kwa Asiriya

5 Iwe Asiriya chibonga cha mkwiyo wanga, ndodo m’dzanja lake muli ukali wanga!

6 Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.

7 Koma iye safuna chotero, ndipo mtima wake suganizira chotero, koma mtima wake ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka.

8 Popeza ati, Akalonga anga kodi sali onse mafumu?

9 Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemisi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi? Kodi Samariya sali ngati Damasiko?

10 Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a kuYerusalemundi ku Samariya;

11 monga ndachitira Samariya ndi mafano ake, momwemo kodi sindidzachitira Yerusalemu ndi mafano ake?

12 Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri laZiyonindi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.

13 Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu;

14 dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa mazira osiyidwa, ine ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye.

15 Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.

16 Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.

17 Ndipo kuwala kwa Israele kudzakhala moto, ndi Woyera wake adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yake ndi lunguzi wake tsiku limodzi.

18 Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m’nkhalango yake, ndi wa m’munda wake wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera.

19 Ndipo mitengo yotsala ya m’nkhalango yake idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera.

20 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israele, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israele, ntheradi.

21 Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.

22 Popeza ngakhale anthu anu Israele akunga mchenga wa kunyanja, otsala ao okhaokha adzabwera; chionongeko chatsimikizidwa chilungamo chake chisefukira.

23 Pakuti Ambuye, Yehova wa makamu adzachita chionongeko chotsimikizidwa pakati padziko lonse lapansi.

24 Chifukwa chake atero Ambuye, Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musaope Asiriya; ngakhale amenya inu ndi chibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yake, monga amachitira Ejipito.

25 Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga.

26 Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira chikoti, monga m’kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo chibonga chake chidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anachitira Ejipito,

27 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta.

28 Wafika ku Ayati, wapitirira kunka ku Migironi; pa Mikimasi asunga akatundu ake;

29 wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibea wa Saulo wathawa.

30 Fuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! Tamva, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka!

31 Madimena ali wothawathawa; okhala mu Gebimu asonkhana kuti athawe.

32 Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lake paphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.

33 Taonani, Ambuye Yehova wa makamu adzasadza nthambi moopsa; ndipo zazitali msinkhu zidzadulidwa, ndipo zazitali zidzagwetsedwa.

34 Ndipo adzadula nkhalango za m’thengo ndi chitsulo, ndipo Lebanoni adzagwa ndi wamphamvu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/10-1c274a3620c5390f1d8a0b5966e6ca5d.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 11

Ufumu wa mtendere wa Mesiya

1 Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m’mizu yake idzabala zipatso;

2 Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;

3 ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:

4 koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.

5 Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m’chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.

6 Mmbulu udzakhala pamodzi ndimwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.

7 Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe.

8 Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri.

9 Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.

10 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu,amitunduadzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.

11 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m’nyanja.

12 Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi.

13 Ndipo nsanje ya Efuremu idzachoka, ndi iwo amene avuta Yuda adzadulidwa; Efuremu sachitira nsanje Yuda, ndi Yuda sachitira nsanje Efuremu.

14 Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum’mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.

15 Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.

16 Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m’dziko la Ejipito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/11-cf74500b4ccc87939f4e1bda5835d52b.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 12

Chiyamiko cha anthu a Mulungu atalangidwa

1 Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.

2 Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

3 Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

4 Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.

5 Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m’dziko lonse.

6 Tafuula, takuwa iwe, wokhala muZiyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m’kati mwako ali wamkulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/12-d28253e143a6794a72cd81207ff577eb.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 13

Aneneratu za kuthyoka kwa ufumu wa Babiloni, ndi kubweza Israele kwao

1 Katundu wa Babiloni, amene anamuona Yesaya mwana wa Amozi.

2 Kwezani mbendera paphiri loti see, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m’zipata za akulu.

3 Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, achite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukulu wanga.

4 Mau a khamu m’mapiri, akunga a mtundu waukulu wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo.

5 Achokera m’dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse.

6 Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova lili pafupi; lidzafika monga chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

7 Chifukwa chake manja onse adzafooka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;

8 ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.

9 Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzaonongamo akuchimwa psiti.

10 Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m’kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.

11 Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.

12 Ndipo ndidzachepsa anthu koposa golide, ngakhale anthu koposa golide weniweni wa ku Ofiri.

13 Chifukwa chake ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kuchokera m’malo ake, m’mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wake waukali.

14 Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ake, nathawira yense kudziko lake.

15 Onse opezedwa adzapyozedwa, ndi onse ogwidwa adzagwa ndi lupanga.

16 Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m’nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa.

17 Taonani, ndidzawautsira Amedi, amene sadzasamalirasiliva, ngakhale golide sadzakondwera naye.

18 Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana.

19 Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.

20 Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; Mwarabu sadzamanga hema wake pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu ao kumeneko.

21 Koma zilombo za m’chipululu zidzagona pamenepo; nyumba zao zidzadzala ndi zakukuwa; ndipo nthiwatiwa zidzakhala pamenepo, ndipo atonde adzajidimuka pamenepo.

22 Ndipo mimbulu idzalira m’maboma ao, ndi ankhandwe m’manyumba ao abwino; ndi nthawi yake iyandikira, ndi masiku ake sadzachuluka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/13-a28fe9a770373adae2dcb1f0e26c0320.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 14

1 Pakuti Yehova adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m’dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.

2 Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala naoamitunduwo m’dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta.

3 Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa chisoni chako, ndi nsautso yako, ndi ntchito yako yovuta, imene anakugwiritsa,

4 pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi!

5 Yehova wathyola mkunkhu wa woipa, ndodo yachifumu ya wolamulira.

6 Wokantha anthu mwaukali kuwakantha chikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa.

7 Dziko lonse lapuma, lili duu; iwo ayamba kuimba nyimbo.

8 Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebanoni, ndi kunena, Chigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife.

9 Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m’mipando yao mafumu onse a amitundu.

10 Onse adzavomera, nadzati kwa iwe, Kodi iwe wakhalanso wopanda mphamvu ngati ife? Kodi iwe wafanana nafe?

11 Chifumu chako chatsitsidwa kunsi kumanda, ndi phokoso la mingoli yako; mphutsi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta.

12 Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbandakucha! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!

13 Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m’malekezero a kumpoto;

14 ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam’mwambamwamba.

15 Koma udzatsitsidwa kunsi kumanda, ku malekezero a dzenje.

16 Iwo amene akuona iwe adzayang’anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;

17 amene anapululutsa dziko, napasula mizinda yake, amene sanamasule ndende zake, zinke kwao?

18 Mafumu onse a amitundu, onsewo agona mu ulemerero yense kunyumba kwake.

19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.

20 Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ochita zoipa sidzatchulidwa konse.

21 Konzani inu popherapo ana ake, chifukwa cha kuipa kwa atate ao; kuti iwo asadzuka ndi kukhala nalo dziko, ndi kudzaza dziko lapansi ndi mizinda.

22 Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova.

23 Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi maiwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsache la chionongeko, ati Yehova wa makamu.

Aneneratu za kuthyoka kwa Asiriya

24 Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala;

25 kuti Ine ndidzathyola Aasiriya m’dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphewa pao.

26 Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.

27 Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?

Aneneratu za tsoka la Afilisti

28 Chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo.

29 Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m’muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.

30 Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.

31 Lira, chipata iwe; fuula, mzinda iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m’mizere yake.

32 Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsaZiyoni, ndipo m’menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/14-339c1b1959865f03f5b19aaaf9823c41.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 15

Aneneratu za kuonongeka kwa Mowabu

1 Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.

2 Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.

3 M’makwalala mwao adzimangira chiguduli m’chuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m’malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.

4 Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m’kati mwake.

5 Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m’njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.

6 Pakuti pamadzi a Nimurimu padzakhala mabwinja; popeza udzu wafota, msipu watha.

7 Chifukwa chake zochuluka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo kumtsinje wa mabango.

8 Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu.

9 Pakuti madzi a Diboni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa Diboni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Mowabu, ndi pa otsala a m’dziko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/15-bed74698019bcf4fe35210360f290f02.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 16

1 Tumizani inu anaankhosa kwa wolamulira wa dziko kuchokera ku Sela kunka kuchipululu, mpaka kuphiri la mwana wamkazi waZiyoni.

2 Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.

3 Chitani uphungu, weruzani chiweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opirikitsidwa, osawulula woyendayenda.

4 Opirikitsidwa a Mowabu akhale ndi iwe, khala iwe chomphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m’dziko.

5 Ndipo mpando wachifumu udzakhazikika m’chifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m’zoona, m’chihema cha Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa chiweruziro, nadzafulumira kuchita chilungamo.

6 Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.

7 Chifukwa chake Mowabu adzakuwa chifukwa cha Mowabu, onse adzakuwa; chifukwa cha maziko a Kiri-Haresefi mudzalira maliro, osautsidwa ndithu.

8 Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibima; ambuye a mitundu athyolathyola mitengo yosankhika yake; iwo anafikira ngakhale ku Yazere, nayendayenda m’chipululu; nthambi zake zinatasa, zinapitirira panyanja.

9 Chifukwa chake ndidzalira ndi kulira kwa Yazere, chifukwa cha mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleyale; chifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mfuu wankhondo wagwera.

10 Ndipo chikondwerero ndi msangalalo zachotsedwa m’munda wopatsa zipatso; ndi m’minda ya mipesa simudzakhala kuimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m’moponderamo; ndaleketsa mfuu wa masika amphesa.

11 Chifukwa chake m’mimba mwanga mulirira Mowabu, ngati mngoli, ndi za m’mtima mwanga zilirira Kiriheresi.

12 Ndipo padzakhala kuti pamene Mowabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika kumalo ake oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.

13 Awa ndi mau amene Yehova adanena za Mowabu nthawi zapitazo.

14 Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Mowabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang’onong’ono ndi achabe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/16-777717aeac420c8ce38d25a6e9d5abca.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 17

Aneneratu za Damasiko ndi Efuremu

1 Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mzinda, ndimo udzangokhala muunda wopasulidwa.

2 Mizinda ya Aroere yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsa.

3 Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu.

4 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lake kudzaonda.

5 Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m’chigwa cha Refaimu.

6 Koma mudzasiyidwa m’menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo waazitona, zipatso ziwiri pena zitatu m’nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m’nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.

7 Tsiku limenelo munthu adzayang’ana kwa Mlengi wake, ndipo maso ake adzalemekeza Woyera wa Israele.

8 Ndipo iye sadzayang’ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.

9 Tsiku limenelo mizinda yake yolimba idzakhala ngati mabwinja a m’nkhalango, ndi a pansonga paphiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israele; ndipo padzakhala bwinja.

10 Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukire thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo;

11 tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m’mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.

Aneneratu za kufafanizika kwa nkhondo ya Asiriya

12 Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwaamitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu!

13 Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.

14 Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanache, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/17-efdb277ec5798408a0aff2d05bef1929.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 18

Aneneratu za Etiopiya

1 Ha, dziko lakukupuza mapiko, lili tsidya lija la nyanja za Etiopiya;

2 limene litumiza mithenga pamtsinje m’ngalawa zamagumbwa zoyenda m’madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa!

3 Inu nonse akukhala m’dziko lapansi, ndi inu akukhazikika padziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.

4 Pakuti Yehova watero kwa ine, Ine ndidzakhala chete, ndipo ndidzayang’ana mokhala chete, ndipo ndidzayang’ana mokhalamo Ine, monga kuwala kotentha kwa dzuwa, monga mtambo wa mame m’kutentha kwa masika.

5 Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kuthyola, iye adzadzombolera tinthambi ndi chikwakwa, ndi nthambi zotasa adzazichotsa ndi kuzisadza.

6 Adzasiyira mbalame zakulusa za m’mapiri ndi zilombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m’dzinja, ndi zilombo zonse za dziko zidzakhalapo m’malimwe.

7 Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu aatali ndi osalala, yochokera kwa mtundu woopsa chikhalire chao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa, kumalo a dzina la Yehova wa makamu, phiri laZiyoni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/18-deba77415e447f8614e3fa6e370df396.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 19

Aneneratu za Ejipito

1 Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.

2 Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mzinda kumenyana ndi mzinda, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.

3 Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.

4 Ndipo ndidzapereka Ejipito m’manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

5 Ndipo madzi adzaphwa m’mtsinje waukulu, ndipo mtsinje woyendamo madzi udzaphwa, nuuma.

6 Ndipo timitsinje tidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota.

7 Madambo oyandikana ndi mtsinje, pafupi ndi gombe la mtsinje, ndi zonse zobzala pamtsinje zidzauma, ndipo zidzachotsedwa, osakhalamo konse.

8 Asodzinso adzalira, ndi onse oponya mbedza mu mtsinje adzaliralira, ndi onse oponya makoka m’madzi, adzalefuka.

9 Komanso iwo amene agwira ntchito yakupala thonje, ndi iwo amene aomba nsalu yoyera, adzakhala ndi manyazi.

10 Ndipo maziko ake adzasweka, onse amene agwira ntchito yolipidwa adzavutidwa mtima.

11 Akalonga a Zowani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru aFaraowasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?

12 Nanga tsopano anzeru ali kuti? Akuuze iwe tsopano; adziwe chimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kuchitira Ejipito.

13 Akalonga a Zowani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asocheretsa Ejipito, amene ali mwala wa pangodya wa mafuko ake.

14 Yehova wasakaniza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m’ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake.

15 Ejipito sadzakhala ndi ntchito, imene mutu pena mchira, pena nthambi ya kanjedza, pena mlulu zidzaigwira.

16 Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake.

17 Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Ejipito, yense wakulitchula adzamtembenukira mwamantha, chifukwa cha uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga padzikolo.

18 Tsiku limenelo padzakhala mizinda isanu m’dziko la Ejipito yolankhula chinenero cha Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzatchedwa, Mzinda wa chionongeko.

19 Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati padziko la Ejipito, ndi choimiritsa cha Yehova m’malire ake.

20 Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m’dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.

21 Ndipo Yehova adzadziwika kwa Ejipito, ndipo Aejipito adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kuchitadi.

22 Ndipo Yehova adzakantha Ejipito kukantha ndi kuchiritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawachiritsa.

23 Tsiku limenelo padzakhala khwalala lochokera mu Ejipito kunka ku Asiriya, ndipo Mwasiriya adzafika ku Ejipito, ndi Mwejipito adzafika ku Asiriya, ndipo Aejipito adzapembedzera pamodzi ndi Aasiriya.

24 Tsiku limenelo Israele ndi Ejipito ndi Asiriya atatuwa, adzakhala mdalitso pakati padziko lapansi;

25 pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Ejipito anthu anga, ndi Asiriya ntchito ya manja anga, ndi Israele cholowa changa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/19-4ff733cbe6a7d9076edd801c9fbd9eba.mp3?version_id=1068—