Categories
YESAYA

YESAYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likutchedwa

Yesaya

, kunena mneneri wotchuka amene ankakhala ku Yerusalemu kuyambira zaka ngati 750 mpaka 700 BC. Bukuli lili ndi zigawo zitatu, ndiye kuti mau ake adalalikidwa pa nthawi zosiyana:

Mutu 1 mpaka 39:

Awa ndi mau ochenjeza Ayuda pa nthawi imene mfumu ya Aasiriya inkawaopseza. Mneneri awauza kuti chenicheni chimene chingaononge moyo wao si mphamvu za Aasiriya aja, koma kusamvera kwao ndi machimo ao, posakhulupirira Yehova. Yesaya awapempha anthuwo ndi atsogoleri ao kuti atembenuke mtima, achite zolungama ndi zokhulupirika; akapanda kutero, dziko lao lidzaonongeka ndithu. Mau ena alonjeza kuti kutsogoloko padzakhala mtendere ponseponse ndipo mmodzi wa zidzukulu za Davide adzakhala mfumu yangwiro yokhazikitsa chilungamo m’dziko lonse.

Mutu 40 mpaka 55

: Awa ndi mau owalimbitsa mtima Ayuda pa nthawi imene anzao ambiri otengedwa ukapolo ankazunzika ku Babiloni. Ndiwo mau olonjeza zabwino ndi outsa chikhulupiriro. Yehova abwera posachedwa kudzawapulumutsa ndi kuwabwezeretsa kwao ku Yerusalemu. Phunziro lalikulu ndi lakuti Yehova ndiye aongolera zinthu zonse pa moyo wa anthu, ndipo wapatsa anthu ake ntchito younikira mitundu ina ya anthu, mwakuti nawonso adzalandira madalitso kudzera mwa Aisraelewo. Mau odziwika kwambiri ndi omwe anena za Mtumiki wa Yehova.

Mutu 56 mpaka 66:

Awa ndi malangizo ndi mau ena owalimbitsa mtima Ayuda aja amene adabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babiloni. Mneneri awatsimikizira kuti Mulungu adzachitadi zonse zija analonjeza. Koma iwo kumbali yao ayenera kuchita zolungama ndi zokhulupirika, ndi kumaika mtima pa zoyeretsa tsiku la Sabata ndi kupereka nsembe. Mau ena odziwika ndi omwe Yesu adawagwiritsa ntchito pamene adayamba kulalikira (60.1-2).

Za mkatimu

Uneneri asanatengedwe kupita ku ukapolo ku Babiloni

1.1—39.8

a. Mau ena ochenjeza anthu ndipo mau ena olonjeza zabwino

1.1—12.6

b. Chauta adzalanga mitundu ya anthu

13.1—23.18

c. Chauta aimba mlandu dziko lapansi

24.1—27.13

d. Mau ena ochenjeza anthu ndipo mau ena olonjeza zabwino

28.1—35.10

e. Aasiriya aopseza Hezekiya mfumu ya Ayuda

36.1—39.8

Uneneri wachilimbikitso ali ku ukapolo

40.1—55.13

Uneneri atabwerako ku ukapolo

56.1—66.24

Categories
YESAYA

YESAYA 1

Machimo ndi masauko a ana a Israele

1 Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndiYerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.

2 Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.

3 Ng’ombe idziwa mwini wake, ndi bulu adziwa pomtsekereza: koma Israele sadziwa, anthu anga sazindikira.

4 Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m’mbuyo.

5 Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.

6 Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m’menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.

7 Dziko lanu lili bwinja; mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.

8 Ndipo mwana wamkazi waZiyoniwasiyidwa ngati chitando cha m’munda wampesa, chilindo cha m’munda waminkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.

9 Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang’onong’ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.

Machenjezo ndi maopso a Mulungu

10 Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, tcherani makutu ku chilamulo cha Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.

11 Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng’ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.

12 Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna chimenechi m’dzanja lanu, kupondaponda m’mabwalo mwanga?

13 Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndiSabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano.

14 Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.

15 Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.

16 Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa;

17 phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.

18 Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.

19 Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,

20 koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m’kamwa mwa Yehova mwatero.

21 Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.

22 Silivawako wasanduka mphala, vinyo wako wasakanizidwa ndi madzi.

23 Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.

24 Chifukwa chake Ambuye ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;

25 ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzachotsa seta wako wonse:

26 ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi; pambuyo pake udzatchedwa Mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.

27 Ziyoni adzaomboledwa ndi chiweruzo, ndi otembenuka mtima ake ndi chilungamo.

28 Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ochimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.

29 Chifukwa adzakhala ndi manyazi, chifukwa cha mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, chifukwa cha minda imene mwaisankha.

30 Chifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lake linyala, ngatinso munda wopanda madzi.

31 Ndimo wamphamvu adzakhala ngati chingwe chathonje, ndi ntchito yake ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/1-c6a339399952a3633da8dfa6c8fabc5e.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 2

Ulemerero wa Israele m’tsogolomo, maweruzo a Mulungu pakatipo

1 Mau amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, onena za Yuda ndiYerusalemu.

2 Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.

3 Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake; chifukwa muZiyonimudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.

4 Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.

5 Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m’kuwala kwa Yehova.

6 Chifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, chifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum’mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m’manja ndi ana a achilendo.

7 Dziko lao ladzalasilivandi golide, ngakhale chuma chao nchosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magaleta ao ngosawerengeka.

8 Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza ntchito ya manja aoao, imene zala zaozao zinaipanga.

9 Munthu wachabe agwada pansi, ndi munthu wamkulu adzichepetsa, koma musawakhululukire.

10 Lowa m’phanga, bisala m’fumbi, kuchokera pa kuopsa kwa Yehova, ndi pa ulemerero wachifumu wake.

11 Maso a munthu akuyang’anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

12 Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;

13 ndi pa mitengo yonse yamkungudza ya Lebanoni, yaitali ndi yotukulidwa, ndi pa mitengo yonse yathundu ya Basani;

14 ndi pa mapiri onse aatali, ndi pa zitunda zonse zotukulidwa;

15 ndi pa nsanja zazitali zonse, ndi pa machemba onse;

16 ndi pa ngalawa zonse za Tarisisi, ndi pa zithunzithunzi zonse zokondweretsa.

17 Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

18 Ndimo mafano adzapita psiti.

19 Anthu adzalowa m’mapanga a m’matanthwe, ndi m’maenje apansi, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.

20 Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;

21 kuti akalowe m’mapanga a m’matanthwe, ndi m’mindala a m’miyala, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.

22 Siyani munthu, amene mpweya wake uli m’mphuno mwake; chifukwa m’mene awerengedwamo ndi muti?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/2-2584f1fca3e4a88a7624287f709bc971.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 3

1 Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa kuYerusalemundi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo;

2 munthu wamphamvu, ndi munthu wankhondo; woweruza ndimneneri, ndi waula, ndi nkhalamba;

3 kapitao wa makumi asanu, ndi munthu wolemekezeka, ndi phungu, ndi mmisiri waluso, ndi wodziwa matsenga.

4 Ndipo ndidzapereka ana, kuti akhale akulu ao, mwachibwana adzawalamulira.

5 Ndi anthu adzavutidwa, yense ndi wina, yense ndi mnansi wake; mwana adzadzinyaditsa yekha pa akulu, ndi onyozeka pa olemekezedwa.

6 Pamene mwamuna adzamgwira mbale wake m’nyumba ya atate wake, nadzati, Iwe uli ndi chovala, khala wolamulira wathu, ndi kupasula kumeneku kukhale m’dzanja lako;

7 tsiku limenelo adzakweza mau ake, kuti, Sindine wochiritsa, chifukwa kuti m’nyumba mwanga mulibe chakudya kapena chovala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu.

8 Chifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; chifukwa kuti lilime lao ndi machitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m’maso a ulemerero wake.

9 Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.

10 Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; chifukwa oterowo adzadya zipatso za machitidwe ao.

11 Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye.

12 Anthu anga awavuta ndi ana, awalamulira ndi akazi. Anthu anga inu, iwo amene akutsogolerani, ndiwo akuchimwitsani, naononga njira zanu zoyendamo.

13 Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu.

14 Yehova adzalowa m’bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wampesa, zofunkha za waumphawi zili m’nyumba zanu;

15 muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye, Yehova wa makamu.

16 Komanso Yehova ati, Chifukwa kuti ana aakazi aZiyoniangodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang’ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao;

17 chifukwa chake Ambuye adzachita nkanambo pa liwombo la ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzavundukula m’chuuno mwao.

18 Tsiku limenelo Ambuye adzachotsa zigwinjiri zao zokoma, ndi zitunga, ndi mphande;

19 mbera, ndi makoza, ndi nsalu za pankhope;

20 ndi zisada, ndi maunyolo a kumwendo, ndi mipango, ndi nsupa zonunkhira, ndi mphinjiri;

21 mphete, ndi zipini;

22 malaya a paphwando, ndi zofunda, ndi zimbwi, ndi timatumba;

23 akalirole, ndi nsalu zabafuta, ndi nduwira, ndi zophimba.

24 Ndipo padzakhala m’malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m’malo mwa lamba chingwe; ndipo m’malo mwa tsitsi labwino dazi; m’malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m’malo mwa ukoma.

25 Amuna ako adzagwa ndi lupanga, ndi wamphamvu wako m’nkhondo.

26 Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/3-0f0fea617de1baa0146875a316f43ade.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 4

Tsiku la Mulungu, kuyeretsedwa kwa Yerusalemu

1 Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.

2 Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.

3 Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa muZiyoni, ndi iye amene atsala muYerusalemuadzatchedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo mu Yerusalemu;

4 pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.

5 Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung’azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.

6 Ndipo padzakhala chihema cha mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/4-5a266abaab2ef364b095e3a844987b45.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 5

Fanizo la munda wampesa ndi kumasulira kwake

1 Ndiimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wake wampesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wampesa m’chitunda cha zipatso zambiri;

2 ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.

3 Ndipo tsopano, inu okhala muYerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzanitu mlandu wa ine ndi munda wanga wampesa.

4 Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wampesa, chimene sindinachite m’menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?

5 Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;

6 ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula.

7 Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.

8 Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati padziko!

9 M’makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikulu ndi zokoma zopanda wokhalamo.

10 Chifukwa kuti munda wampesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi.

11 Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa!

12 Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m’maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang’ana pa machitidwe a manja ake.

13 Chifukwa chake anthu anga amuka m’nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.

14 Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.

15 Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wotchuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa;

16 koma Yehova wa makamu wakwezedwa m’chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m’chilungamo.

17 Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m’busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo.

18 Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zachabe, ndi tchimo ngati ndi chingwe cha galeta;

19 amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe!

20 Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima; amene aika zowawa m’malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m’malo mwa zowawa!

21 Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ochenjera!

22 Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusakaniza zakumwa zaukali;

23 amene alungamitsa woipa pa chokometsera mlandu, nachotsera wolungama chilungamo chake!

24 Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m’malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m’mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.

25 Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.

26 Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutali mbendera, nadzawaimbira mluzu, achokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msangamsanga;

27 palibe amene adzalema, kapena adzaphunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m’chuuno mwao silidzamasuka, kapena chomangira cha nsapato zao sichidzaduka;

28 amene mivi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kamvulumvulu;

29 kubangula kwao kudzafanana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naichotsa bwino opanda wakupulumutsa.

30 Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang’ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m’mitambo yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/5-a1784c53eab47cdfd7fb139e6e377276.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 6

Masomphenya a Yesaya

1 Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala mu Kachisi.

2 Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao.

3 Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.

4 Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anafuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi.

5 Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.

Yesaya akonzedwa akhale mneneri

6 Pompo anaulukira kwa ine mmodzi wa aserafi, ali nalo khala lamoto m’dzanja mwake, limene analichotsa ndi mbaniro paguwa la nsembe;

7 nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zaomboledwa.

8 Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.

9 Ndipo Iye anati, Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang’anani inu ndithu, koma osadziwitsa.

10 Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.

11 Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka mizinda ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu,

12 ndipo Yehova wasunthira anthu kutali, ndi mabwinja adzachuluka pakati padziko.

13 Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m’menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/6-b492e6e88ad14ff2d3e138b46f065721.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 7

Rezini ndi Peka akwerera Yerusalemu

1 Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka kuYerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana.

2 Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m’nkhalango igwedezeka ndi mphepo.

3 Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Tuluka tsopano kukachingamira Ahazi, iwe ndi Seari-Yasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamaliziro a mcherenje wa thamanda la pamtunda, kukhwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu;

4 nukati kwa iye, Chenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, chifukwa cha zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.

5 Chifukwa Aramu ndi Efuremu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukuchitira zoipa, nati,

6 Tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pake, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeele;

7 atero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzachitidwa.

8 Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efuremu adzathyokathyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;

9 ndipo mutu wa Efuremu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.

Lonjezo lakunena za Imanuele

10 Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati,

11 Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham’mwakuya, kapena cham’mwamba.

12 Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova.

13 Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang’ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga?

14 Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.

15 Iye adzadya mafuta ndi uchi, pamene adziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino.

16 Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa.

17 Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya.

18 Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzaimbira mluzu ntchentche ili m’mbali ya kumtunda kwa mitsinje ya Ejipito, ndi njuchi ili m’dziko la Asiriya.

19 Ndipo zidzafika ndi kutera zonse m’zigwa zabwinja, ndi m’maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.

20 Tsiku limenelo Ambuye adzameta mutu, ndi ubweya wa m’mapazi, ndi lumo lobwereka lili tsidya lija la nyanja, kunena mfumu ya Asiriya; ndilo lidzamalizanso ndevu.

21 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti munthu adzaweta ng’ombe yaikazi yaing’ono, ndi nkhosa ziwiri;

22 ndipo padzakhala, chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uchi adzadya yense wosiyidwa pakati padziko.

23 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti paliponse panali mipesa chikwi chimodzi ya mtengo wake wa sekeli chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.

24 Munthu adzafikako ndi mivi ndi uta; pakuti dziko lonse lidzakhala la lunguzi ndi minga.

25 Ndipo zitunda zonse zinalimidwa ndi khasu, iwe sudzafikako chifukwa cha kuopa lunguzi ndi minga, koma pomwepo padzakhala potumizira ng’ombe ndi popondaponda nkhosa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/7-ce9c9da34e1a122fc4b8bb90dd030977.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 8

Choneneratu chakuti Aasiriya adzagonjetsa Israele

1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Tenga iwe polembapo papakulu, nulembe pamenepo ndi malembedwe odziwika, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.

2 Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.

3 Ndipo ndinanka kwamneneriwamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Utche dzina lake, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.

4 Chifukwa kuti mwana asanakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.

5 Ndipo Yehova ananena kwa ine kachiwirinso, nati,

6 Popeza anthu awa akana madzi a Siloamu, amene ayenda pang’onopang’ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya;

7 chifukwa chake, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a mtsinje wa Yufurate, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asiriya ndi ulemerero wake wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zake zonse, nadzasefukira pamtunda ponse.

8 Ndipo iye adzapitapita kulowa mu Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m’khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ake, kudzakwanira dziko lanu m’chitando mwake, inu Imanuele.

9 Chitani phokoso, anthu inu, koma mudzathyokathyoka; tcherani khutu, inu nonse a maiko akutali; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka.

10 Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.

11 Pakuti Yehova watero kwa ine ndi dzanja lolimba, nandilangiza ine kuti ndisayende m’njira ya anthu awa, nati,

12 Musachinene, Chiwembu; chilichonse chimene anthu awa adzachinena, Chiwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musachite mantha.

13 Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akuchititseni mantha Iye.

14 Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala muYerusalemu.

15 Ndipo ambiri adzaphunthwapo, nagwa, nathyoka, nakodwa, natengedwa.

16 Manga umboni, mata chizindikiro pachilamulo mwa ophunzira anga.

17 Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.

18 Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m’phiri laZiyoni.

19 Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang’ung’udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?

20 Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.

21 Ndipo iwo adzapitirira ovutidwa ndi anjala, ndipo padzakhala kuti pokhala ndi njala iwo adzadziputa okha, ndi kutemberera mfumu yao, ndi Mulungu wao; ndi kugadamira nkhope zao kumwamba;

22 nadzayang’ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/8-232c931e0f2a5d8e4d3ac083aa063b2e.mp3?version_id=1068—

Categories
YESAYA

YESAYA 9

Choneneratu cha ufumu wa Mesiya

1 Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutali, koma potsiriza pake Iye analichitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordani, Galileya waamitundu.

2 Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.

3 Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m’masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.

4 Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.

5 Pakuti zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m’phokosomo, ndi zovala zomvimvinika m’mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.

6 Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

7 Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.

Aisraele achenjezedwa kuti adzalangidwa

8 Ambuye anatumiza mau kwa Yakobo, ndipo anatsikira pa Israele.

9 Ndipo anthu onse adzadziwa, ngakhale Efuremu ndi okhala mu Samariya, amene anena m’kunyada ndi m’kukula kwa mtima,

10 Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza.

11 Chifukwa chake Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ake;

12 Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.

13 Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.

14 Chifukwa chake Yehova adzadula mutu wa Israele ndi mchira wake; nthambi ya kanjedza ndi mlulu, tsiku limodzi.

15 Nkhalamba ndi wolemekezeka ndiye mutu, ndimneneriwophunzitsa zonama ndiye mchira.

16 Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka.

17 Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m’kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.

18 Pakuti kuchimwa kwayaka ngati moto kumaliza lunguzi ndi minga, inde kuyaka m’nkhalango ya m’thengo, ndipo zifuka chapamwamba, m’mitambo yautsi yochindikira.

19 M’kukwiya kwa Yehova wa makamu, dziko latenthedwa ndithu, anthunso ali ngati nkhuni; palibe munthu wochitira mbale wake chisoni.

20 Ndipo wina adzakwatula ndi dzanja lamanja, nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lamanzere, osakhutai; iwo adzadya munthu yense nyama ya mkono wake wa iye mwini.

21 Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/9-c655ede279e4a3de05d0f661eb30f09e.mp3?version_id=1068—